14 – Kuchotsa Mimba

Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Kuchotsa Mimba.

Mavesi atatu ofunika kwambiri

Anapereka nsembe ana awo aamuna ndi ana awo aakazi kwa ziwanda. Anakhetsa magazi a anthu osalakwa, magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi, amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanaani, ndipo dziko linayipitsidwa ndi magazi awo.

“ ‘Ndipo unatenga ana ako aamuna ndi ana aakazi amene unandibalira ine, ndipo unakawapereka ngati nsembe kwa mafanowo. Kodi zigololo zakozo sizinakukwanire kuti uziphanso ana anga ndi kuwapereka ngati nsembe kwa mafano akowo? Chifukwa cha zadama zako zonyansazi unayiwala masiku a ubwana wako pamene unali wamaliseche, wausiwa ndiponso womangovivinizika mʼmagazi.

Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga; munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga. Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa; ntchito zanu ndi zodabwitsa, zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.

Mavesi onse motsatira dongosolo lolondola – 96 ndime

Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.

“Aliyense wopha munthu, adzaphedwanso ndi munthu; pakuti Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake.

“Ana onse aamuna oyamba kubadwa uwapatule, ndi anga. Aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisraeli ndi wanga, kaya ndi wa munthu kapena wa chiweto.”

“Usaphe.

“Munthu aliyense amene amenya mnzake namupha, iyenso ayenera kuphedwa.

“Ngati anthu akumenyana ndi kupweteka mayi woyembekezera, mayiyo napita padera, koma osavulala, wolakwayo ayenera kulipira chilichonse chimene mwamuna wake wa mkaziyo adzalamula ndipo bwalo lamilandu lavomereza. Koma ngati wavulazidwa kwambiri, ndiye malipiro ake adzakhala motere: moyo kulipa moyo,

“Usakhotetse milandu ya anthu osauka. Upewe zabodza ndipo usaphetse munthu wosalakwa ndi wolungama, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.

Pakuti moyo wa cholengedwa chilichonse uli mʼmagazi, ndipo ndawupereka kwa inu kuti muzichitira mwambo wopepesera machimo a moyo wanu pa guwa. Pajatu magazi ndiwo amachotsa machimo chifukwa moyo uli mʼmenemo.

“ ‘Usapereke mwana wako aliyense kuti akhale nsembe yamoto kwa Moleki ndi kuyipitsa dzina la Yehova. Ine ndine Yehova.

Yehova anawuza Mose kuti, “Uza Aisraeli kuti, ‘Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala mu Israeli wopereka mwana wake kwa Moleki ayenera kuphedwa. Anthu a mʼdera lakelo amuphe ndi miyala. Munthu ameneyo ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anzake.’ Popereka mwana wake kwa Moleki, wadetsa malo anga wopatulika ndi kuyipitsa dzina langa loyera. Ngati anthu a mʼderalo achita ngati sakumuona munthuyo pamene akupereka mwana wake kwa Moleki ndi kusamupha, Ineyo ndidzamufulatira pamodzi ndi banja lake. Ndidzawachotsa pakati pa anthu anzawo onse amene anamutsatira, nadziyipitsa okha popembedza Moleki.”

“ ‘Ngati munthu wina aliyense achotsa moyo wa munthu mnzake, munthuyo ayenera kuphedwa.

“ ‘Aliyense wopha munthu ayeneranso kuphedwa ngati pali umboni okwanira. Koma wina asaphedwe ngati pali mboni imodzi yokha. “ ‘Osalola kulandira dipo lowombolera munthu wakupha yemwe ayenera kuphedwa. Wakupha ayenera kuphedwa.

“ ‘Musayipitse dziko limene mukukhalamolo. Magazi amayipitsa dziko ndipo nʼkosatheka kulipirira dziko chifukwa cha magazi amene akhetsedwa mʼmenemo, kupatula pokhetsa magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo.

“Usaphe.

Musapembedze Yehova Mulungu wanu momwe amachitira iwowo, chifukwa popembedza milungu yawoyo amachita zonyansa zamitundumitundu zimene Yehova amadana nazo. Amatentha ngakhale ana awo aamuna ndi aakazi pa moto ngati nsembe za kwa milungu yawo.

Pasapezeke pakati panu munthu wootcha pa moto mwana wake wamwamuna kapena wamkazi ngati nsembe. Asapezekenso pakati panu munthu wowombeza kapena wochita mawula, wolosera, wochita za ufiti,

“Ndi wotembereredwa munthu amene alandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!” “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita kapena sasunga mawu a malamulo awa.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

Lero kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni zodzakutsutsani pakuti ndayika pamaso panu moyo ndi imfa, madalitso ndi matemberero. Tsopano sankhani moyo kuti inu ndi ana anu mukhale ndi moyo.

Iye anayenda mʼnjira ya mafumu a Israeli mpaka kupereka mwana wake wamwamuna pa moto ngati nsembe yopsereza, potsatira zonyansa za anthu a mitundu imene Yehova anayipirikitsa mʼdzikomo Aisraeli asanafike.

Ndipo anadutsitsa mʼmoto ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo ankawombeza mawula, namachitanso zanyanga ndipo anadzipereka kuchita zoyipa pamaso pa Yehova namukwiyitsa.

Aava anapanga Nibihazi ndi Taritaki, ndipo Asefaravaimu ankawotcha ana awo pa moto ngati nsembe kwa Adirameleki ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu.

Iye anapsereza mwana wake pa moto ngati nsembe, ankachita za matsenga, ankawombeza mawula, ankapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ndiponso ankapembedza mizimu. Iyeyo anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova ndipo anakwiyitsa Yehovayo.

Iye amapsereza nsembe ku chigwa cha Hinomu, ndipo anaperekanso ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza kutsatira njira zonyansa za mitundu imene Yehova anayithamangitsa pamaso pa Aisraeli.

Iye ankakapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza ku chigwa cha Hinomu, ankachita zamatsenga, kuwombeza ndi ufiti, ankakafunsira kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Iye anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova, kumukwiyitsa Iyeyo.

“Munandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu. Kodi tsopano Inu mudzatembenuka ndi kundiwononga? Kumbukirani kuti munandipanga ndi dothi, kodi tsopano mundibwezeranso ku fumbi? Suja munapatsa abambo anga mphamvu zoti andibale, suja munandikuza bwino mʼmimba mwa amayi anga? Munandikuta ndi khungu ndi mnofu ndi kundilumikiza pamodzi ndi mafupa ndi mitsempha?

chifukwa ndinkapulumutsa mʼmphawi wofuna chithandizo, ndiponso mwana wamasiye amene analibe aliyense womuthandiza.

Kodi amene anapanga ine mʼmimba mwa amayi anga si yemwe anapanganso iwo? Kodi si mmodzi yemweyo amene anatipanga tonsefe mʼmimba mwa amayi athu?

Mumamva Inu Yehova, zokhumba za osautsidwa; mumawalimbikitsa ndipo mumamva kulira kwawo. Kuteteza ana amasiye ndi oponderezedwa, ndi cholinga chakuti munthu amene ali wa dziko lapansi asaopsenso.

Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga. Munachititsa kuti ndizikudalirani ngakhale pa nthawi imene ndinkayamwa. Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu; kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga.

Landitseni kwa anthu ochita zoyipa ndipo mundipulumutse kwa anthu okhetsa magazi. Onani momwe iwo akundibisalira! Anthu owopsa agwirizana zolimbana nane; osati chifukwa cha mlandu kapena tchimo langa, Inu Yehova. Ine sindinachite cholakwa, koma iwo ndi okonzeka kundithira nkhondo. Dzukani kuti mundithandize; penyani mavuto anga!

Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye, ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.

Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu; Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga, ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse.

Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye; mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika. Landitsani anthu ofowoka ndi osowa; apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa. “Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse. Amayendayenda mu mdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.

Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko; amapha ana amasiye. Iwo amati, “Yehova sakuona; Mulungu wa Yakobo salabadirako.” Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu; zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru?

Kodi mpando waufumu woyipa ungathe kugwirizana nanu umene umabweretsa masautso chifukwa cha malamulo ake? Iwo amasonkhana pamodzi kulimbana ndi wolungama ndi kugamula kuti wosalakwa aphedwe. Koma Yehova wakhala linga langa, ndipo Mulungu ndiye thanthwe limene ndimathawirako. Iye adzawabwezera chifukwa cha machimo awo ndi kuwawononga chifukwa cha kuyipa kwawo; Yehova Mulungu wathu adzawawononga.

Anapereka nsembe ana awo aamuna ndi ana awo aakazi kwa ziwanda. Anakhetsa magazi a anthu osalakwa, magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi, amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanaani, ndipo dziko linayipitsidwa ndi magazi awo. Iwo anadzidetsa okha ndi zimene anachita; ndi machitidwe awo amakhala ngati munthu wachigololo. Tsono Yehova anakwiya ndi anthu ake ndipo ananyansidwa ndi cholowa chake.

Manja anu anandilenga ndi kundiwumba; patseni nzeru zomvetsa zinthu kuti ndiphunzire malamulo anu. Iwo amene amakuopani akondwere akandiona, chifukwa chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.

Ana ndiye cholowa chochokera kwa Yehova, ana ndi mphotho yochokera kwa Iye.

Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga; munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga. Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa; ntchito zanu ndi zodabwitsa, zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe. Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi, pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga. Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe. Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.

pakuti Iye amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako ndi kudalitsa anthu ako mwa iwe.

Akadzati, “Tiye kuno; tikabisale kuti tiphe anthu, tikabisalire anthu osalakwa; tiwameze amoyo ngati manda, ndi athunthu ngati anthu otsikira mʼdzenje.

Nʼchifukwa chake tsoka lidzamugwera modzidzimutsa; adzawonongeka msangamsanga popanda chomupulumutsa. Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo, zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa: maso onyada, pakamwa pabodza, manja akupha munthu wosalakwa,

Uwapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe; uwalanditse amene akuyenda movutika kupita kokaphedwa. Ukanena kuti, “Koma ife sitinadziwe kanthu za izi,” kodi Iye amene amasanthula mtima sazindikira zimenezi? Kodi Iye amene amateteza moyo wako sazidziwa zimenezi? Kodi Iye sadzalipira munthu malingana ndi ntchito zake?

Munthu amene wapalamula mlandu wopha munthu adzakhala wothawathawa mpaka imfa yake; wina aliyense asamuthandize.

Momwe sudziwira mayendedwe a mphepo, kapena momwe mzimu umalowera mʼthupi la mwana mʼmimba mwa amayi, momwemonso sungathe kudziwa ntchito za Mulungu, Mlengi wa zinthu zonse.

Mukamatambasula manja anu popemphera, Ine sindidzakuyangʼanani; ngakhale muchulukitse mapemphero anu, sindidzakumverani. Manja anu ndi odzaza ndi magazi; sambani, dziyeretseni. Chotsani pamaso panu ntchito zanu zoyipa! Lekani kuchita zoyipa, phunzirani kuchita zabwino! Funafunani chilungamo, thandizani oponderezedwa. Tetezani ana amasiye, muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.” Yehova akuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu. Ngakhale machimo anu ali ofiira, adzayera ngati thonje. Ngakhale ali ofiira ngati kapezi, adzayera ngati ubweya wankhosa.

Tsoka kwa amene zoyipa amaziyesa zabwino ndipo zabwino amaziyesa zoyipa, amene mdima amawuyesa kuwala ndipo kuwala amakuyesa mdima, amene zowawasa amaziyesa zotsekemera ndipo zotsekemera amaziyesa zowawasa.

Taonani, Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala; akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo awo. Dziko lapansi lidzawulula magazi amene anakhetsedwa pa dzikolo; dziko lapansi silidzabisanso mitembo ya anthu ophedwa.

Yehova amene anakupanga iwe, anakuwumba iwe mʼmimba ya amayi ako, ndi amene adzakuthandiza iwe. Iye akuti, Usachite mantha, iwe Yakobo, mtumiki wanga, Yesuruni, amene ndinakusankha.

Yehova Mpulumutsi wanu, amene anakuwumbani mʼmimba ya amayi anu akuti: “Ine ndine Yehova, amene anapanga zinthu zonse, ndinatambasula ndekha zinthu zakuthambo, ndinayala ndekha dziko lapansi.

Mverani Ine, Inu nyumba ya Yakobo, inu nonse otsala a mʼnyumba ya Israeli, Ine ndakhala ndi kukusamalirani kuyambira mʼmimba ya amayi anu, ndakhala ndikukunyamulani chibadwire chanu.

Mverani Ine, inu anthu a pa zilumba tcherani khutu, inu anthu a mayiko akutali: Yehova anandiyitana ine ndisanabadwe, ananditchula dzina ndili mʼmimba ya amayi anga.

Yehova anandiwumba ine mʼmimba mwa amayi anga kuti ndikhale mtumiki wake kuti ndibweze fuko la Yakobo kwa Iye ndi kusonkhanitsa Israeli kwa Iye, choncho ndimalemekezeka mʼmaso mwa Yehova, ndipo ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.

“Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni? Ngakhale iye angathe kuyiwala, Ine sindidzakuyiwala iwe! Taona, ndakulemba iwe mʼzikhantho zanga; makoma ako ndimawaona nthawi zonse.

Kodi Ine ndingangofikitsa amayi apakati mpaka nthawi yake yochira, koma osalola kuti abaledi mwana?” akutero Yehova. “Kodi ndingatseke mimba pa nthawi yoti abeleke?” akutero Mulungu wako.

Yehova anayankhula nane kuti, “Ndisanakuwumbe mʼmimba mwa amayi ako ndinali nditakudziwa kale, iwe usanabadwe ndinali nditakupatula kale; ndinakuyika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”

Ngakhale pa zovala zako anthu amapezapo magazi a anthu osauka osalakwa. Anthuwo simunawapeze akuthyola nyumba. Komabe ngakhale zinthu zili chomwechi, inu mukunena kuti, ‘Ndife osalakwa, sadzatikwiyira.’ Ndidzakuyimbani mlandu chifukwa mukunena kuti, ‘Ife sitinachimwe.’

Amanga nsanja yopembedzera Tofeti mʼChigwa cha Hinomu kuti apserezereko ana awo aamuna ndi aakazi. Zimenezi Ine sindinawalamulire ngakhale kuziganizira nʼkomwe.

Pakuti anthu andikana Ine ndipo ayipitsa malo ano. Afukiza lubani pa malo ano kwa milungu imene iwo ngakhale makolo awo ngakhalenso mafumu a ku Yuda sanayidziwe. Iwo adzaza malowa ndi magazi a anthu osalakwa. Amanga nsanja zopembedzerapo Baala, kuperekapo ana awo kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala, chinthu chimene Ine sindinalamule kapena kuchiyankhula, ngakhalenso kuchiganizira. Nʼchifukwa chake taonani, masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzatchulanso malo ano kuti Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma Chophera anthu. “ ‘Pamalo pano ndidzasokoneza maganizo a anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Ndidzachititsa kuti adani awo awaphe ku nkhondo. Ndidzawakanthitsa kwa anthu amene akuwazonda. Mitembo yawo ndidzayipereka kwa mbalame za mlengalenga ndi zirombo za kutchire kuti ikhale chakudya chawo.

Chifukwa sanandiphere mʼmimba, kuti amayi anga asanduke manda anga, mimba yawo ikhale yayikulu mpaka kalekale.

“Koma maso ako ndi mtima sizili penanso, koma zili pa phindu lachinyengo, pa zopha anthu osalakwa ndi pa kuzunza ndi pakulamulira mwankhanza.”

Yehova akuti, “Kulira kukumveka ku Rama, kulira kwakukulu, Rakele akulirira ana ake. Sakutonthozeka chifukwa ana akewo palibe.”

Anamanga malo opembedzerapo Baala mʼChigwa cha Hinomu kuti aziperekapo ana awo aamuna ndi aakazi ngati nsembe kwa Moleki. Ine sindinawalamulire kutero, ndipo sindinaganizepo nʼkomwe kuti iwo angachite chinthu chonyansa chotero, ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda.

“ ‘Ndipo unatenga ana ako aamuna ndi ana aakazi amene unandibalira ine, ndipo unakawapereka ngati nsembe kwa mafanowo. Kodi zigololo zakozo sizinakukwanire kuti uziphanso ana anga ndi kuwapereka ngati nsembe kwa mafano akowo? Chifukwa cha zadama zako zonyansazi unayiwala masiku a ubwana wako pamene unali wamaliseche, wausiwa ndiponso womangovivinizika mʼmagazi. “ ‘Tsoka! Tsoka kwa iwe, akutero Ambuye Yehova chifukwa powonjezera pa zoyipa zako zonse,

Ambuye Yehova akuti, popeza unavula ndi kuonetsa umaliseche wako mopanda manyazi, unachita chigololo ndi zibwenzi zako pamodzi ndi mafano ako onyansa, komanso popeza unapereka ana ako kuti aphedwe ngati nsembe zoperekedwa kwa mafano, nʼchifukwa chake Ine ndidzasonkhanitsa zibwenzi zako zonse, zimene unkasangalala nazo, amene unkawakonda ndi amene unkawada. Ndidzawasonkhanitsa motsutsana nawe kuchokera ku madera onse okuzungulira ndipo Ine ndidzakuvula pamaso pawo, ndipo iwo adzaona umaliseche wako wonse. Ine ndidzakulanga monga mmene amalangira akazi amene amachita chigololo ndiponso opha anthu. Chifukwa cha ukali wanga ndi nsanje yanga, ndidzakhetsa magazi ako mokwiya kwambiri.

Pakuti moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa abambo ndi wanga, wamwananso ndi wanga. Munthu wochimwa ndi amene adzafe.

Pamene mubwera kudzapereka mphatso zanu ndi kudzapereka ana kuti akhale ngati nsembe zopsereza mumadziyipitsa ndi mafano anu mpaka lero. Kodi Aisraeli, ndingathe kukulolani bwanji kuti mulandire malangizo kwa Ine? Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, sindidzalola kuti mupemphe nzeru kwa Ine.

Iwo achita chigololo ndipo anapha anthu. Anachita chigololo popembedza mafano awo. Ngakhale ana amene anandiberekera Ine anawapereka kwa mafanowo ngati chakudya chawo. Anachitanso izi: Iwo anayipitsa malo anga opatulika ndi kudetsa masabata anga. Atapereka ana awo kwa mafano, tsiku lomwelo anakalowanso mʼNyumba yanga yopatulika ndi kuyipitsamo. Izi ndi zimene anachita mʼNyumba mwanga.

Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Amoni akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anatumbula akazi oyembekezera a ku Giliyadi nʼcholinga choti akuze malire awo,

Herode atazindikira kuti Anzeruwo anamupusitsa, anakwiya kwambiri. Ndipo anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna a mʼBetelehemu ndi midzi yozungulira amene anali a zaka ziwiri kapena zocheperapo, molingana ndi nthawi imene Anzeruwo anamuwuza.

“Munamva kuti kunanenedwa kwa anthu kale kuti, ‘Usaphe ndipo kuti aliyense amene apha munthu adzaweruzidwa.’

Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena.

Ndipo aliyense amene alandira kamwana kakangʼono ngati aka mu dzina langa, alandira Ine.

Ngati dzanja lako kapena phazi lako likuchimwitsa, lidule ndi kulitaya. Ndi bwino kwa iwe kulowa mʼmoyo wosatha wolumala kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri kapena mapazi awiri ndi kukaponyedwa ku moto wosatha. Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Ndi bwino kwa iwe kuti ukalowe ku moyo wosatha ndi diso limodzi kuposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kukaponyedwa ku moto wa gehena.” “Onetsetsani kuti musanyoze mmodzi wa anawa. Pakuti ndikuwuzani kuti angelo awo kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga akumwamba nthawi zonse.” (Mwana wa Munthu anabwera kudzapulumutsa chimene chinatayika).

Chimodzimodzinso Atate anu akumwamba safuna kuti mmodzi wa anawa atayike.

Yesu anati, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa.”

Pakuti kuchokera mʼkati mwa mitima ya anthu, mumatuluka maganizo oyipa, chiwerewere, kuba, kupha, chigololo,

Iwe umadziwa malamulo: ‘Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni wonama, usachite chinyengo, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”

chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Iye sadzamwa vinyo kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo adzazadzidwa ndi Mzimu Woyera kuyambira pa kubadwa.

Elizabeti atamva moni wa Mariya, mwana anatakataka mʼmimba mwake, ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi Mzimu Woyera. Anafuwula ndi mawu akulu kuti, “Ndiwe wodala pakati pa akazi, ndipo ndi wodala mwana amene udzabereke! Koma nʼchifukwa chiyani andikomera mtima kuti amayi a Ambuye anga abwere kwa ine? Nthawi yomwe ndinamva mawu akulonjera kwanu, mwana anatakataka mʼmimba mwanga chifukwa cha chimwemwe.

(Monga mmene zinalembedwera mu lamulo la Ambuye kuti, “Muzikapereka kwa Ambuye mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa”),

Iwe umadziwa malamulo: ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usapereke umboni wonama, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”

Nʼchifukwa chiyani simukumvetsetsa mawu anga? Chifukwa chake nʼchakuti simungathe kumva zoyankhula zanga. Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza. Koma chifukwa ndikuwuzani choonadi, inu simukundikhulupirira Ine!

Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa mʼdziko lapansi.

Ndipo popeza anaona kuti nʼchopanda nzeru kumvera Mulungu, Iye anawasiya kuti atsatire maganizo achitayiko kuti achite zosayenera kuchitazo. Iwo ndi odzazidwa ndi mtundu uliwonse wa makhalidwe oyipa, zonyansa, umbombo ndi dumbo. Iwo ndi odzazidwa ndi kaduka, kupha, mikangano, chinyengo ndi udani. Iwowo ndi amiseche, osinjirira, odana ndi Mulungu, achipongwe, odzitama ndi odzitukumula. Iwo amapeza njira zochitira zoyipa. Samvera makolo awo, alibe nzeru, chikhulupiriro, sakhudzidwa mu mtima ndipo ndi ankhanza. Ngakhale kuti amadziwa chiweruzo cholungama cha Mulungu chakuti amene amachita zinthu zotere amayenera imfa, iwo sangopitiriza chabe zimenezi, koma amavomerezanso amene amazichita zimenezi.

Musakhale ndi ngongole ndi wina aliyense kupatula ngongole ya kukondana wina ndi mnzake. Pakuti amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa lamulo. Malamulo awa: “Usachite chigololo,” “Usaphe,” “Usabe,” “Usasirire,” ndi malamulo ena onse amene alipo, akhazikika pa lamulo limodzi ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.” Chikondi sichichitira mnzake zoyipa. Chifukwa chake chikondi ndicho chokwaniritsa lamulo.

Kodi simukudziwa kuti thupi lanu ndi Nyumba ya Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene mwalandira kuchokera kwa Mulungu? Inu simuli panokha ayi.

Koma Mulungu, amene anandipatula ine ndisanabadwe, ndi kundiyitana mwachisomo chake, atakondweretsedwa kuvumbulutsa Mwana wake mwa ine, kuti ndikalalikire Khristuyo pakati pa anthu a mitundu ina, ine sindinapemphe nzeru kwa munthu aliyense.

Ngati atumwi a Khristu tikanatha kukhala cholemetsa kwa inu, mʼmalo mwake tinali ngati ana aangʼono pakati panu. Monga mmene amayi amasamalira ana awo angʼono,

Tsono atha kulangiza amayi achichepere kukonda amuna awo ndi ana awo.

Monga thupi lopanda mzimu ndi lakufa, chomwechonso chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.

Musakhale ngati Kaini, amene anali wa woyipayo ndipo anapha mʼbale wake. Nanga anamupha chifukwa chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoyipa ndipo zochita za mʼbale wake zinali zolungama.

Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha.

Iwo anafuwula kuti, “Mudzawaleka mpaka liti, Inu Ambuye wamkulu, woyera ndi woona, osawaweruza anthu okhala mʼdziko lapansi ndi kulipsira magazi athu?”

Koma amantha, osakhulupirira, okonda zonyansa, opha anthu, achiwerewere, amatsenga, opembedza mafano ndi abodza, malo awo adzakhala nyanja yamoto ya sulufule wotentha. Iyi ndi imfa yachiwiri.”

Chichewa - Chichewa - NY

NYCCL - Mawu A Mulungu Mu Chichewa Chalero - 2016

This Bible text is from Biblica Open God's Word In Contemporary Chichewa
https://open.bible/bibles/chichewa-biblica-text-bible/
provided by: Biblica Inc, available by Creative Commons CC-BY-SA-4.0,
and this new compilation is shared as www.creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0.
Languages are made available to you by www.ipedge.net