20 – Pemphero

Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Pemphero.

Mavesi atatu ofunika kwambiri

Pakuti Ambuye amayangʼanira bwino anthu olungama ndipo amatchera khutu ku mapemphero awo. Koma Ambuye sawayangʼana bwino amene amachita zoyipa.”

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe zoyimbira za zitoliro. Salimo la Davide. Tcherani khutu ku mawu anga, Inu Yehova, ganizirani za kusisima kwanga Mverani kulira kwanga kofuna thandizo, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, pakuti kwa Inu, ine ndikupemphera. Mmawa, Yehova mumamva mawu anga; Mmawa ndimayala zopempha zanga pamaso panu ndi kudikira mwachiyembekezo.

“Chifukwa chake pempherani motere: “ ‘Atate athu akumwamba, dzina lanu lilemekezedwe, Ufumu wanu ubwere, chifuniro chanu chichitike pansi pano monga kumwamba. Mutipatse chakudya chathu chalero. Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso tawakhululukira amangawa athu. Ndipo musatitengere kokatiyesa; koma mutipulumutse kwa woyipayo.’

Mavesi onse motsatira dongosolo lolondola – 293 ndime

Ndipo Abrahamu anayankhulanso nati, “Tsono poti ndalimba mtima kuyankhula ndi Ambuye, ngakhale kuti ndine fumbi ndi phulusa chabe,

Ndipo wantchito uja anapemphera nati, “Haa, Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, mulole kuti zinthu zindiyendere ine lero, ndipo muonetseni mbuye wanga Abrahamu kukoma mtima kwanu kosasinthika. Taonani ndayima pambali pa chitsimechi, ndipo atsikana a mu mzindawu akubwera kudzatunga madzi. Ine ndipempha mtsikana wina kuti, ‘Chonde tula mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono iye akayankha kuti ‘Imwani,’ ndipo ndidzapatsanso ngamira zanu madziwo, ameneyo akhale mkazi amene mwasankhira mtumiki wanu Isake.” Zimenezi zikachitika, ndidzadziwa kuti mwaonetsadi kukoma mtima kwanu kosasinthika kwa mbuye wanga. Asanatsirize kupemphera, anangoona Rebeka watulukira atasenza mtsuko wake pa phewa. Iyeyu anali mwana wa Betueli mwana wa Milika, mkazi wa Nahori mʼbale wake wa Abrahamu.

Isake anapempherera mkazi wake kwa Yehova popeza iye anali wosabereka. Yehova anayankha pemphero lake ndipo mkazi wake Rebeka anatenga pathupi.

Tsono Yakobo anatsala yekha. Tsono munthu wina anadzalimbana naye mpaka mʼmbandakucha. Pamene munthuyo anaona kuti sangathe kumugonjetsa, anakhudza nyungʼunyu ya pa ntchafu ya Yakobo ndipo inaguluka polimbanapo. Kenaka munthuyo anati, “Ndisiye ndizipita, popeza kunja kukucha.” Koma Yakobo anayankha, “Sindikulolani kupita pokhapokha mutandidalitsa.” Munthu uja anamufunsa Yakobo kuti, “Kodi dzina lako ndiwe yani?” Iye anayankha, “Ndine Yakobo.” Pamenepo munthuyo anati, “Dzina lako silidzakhalanso Yakobo koma Israeli, chifukwa walimbana ndi Mulungu ndi anthu ndipo wapambana.” Yakobo anati, “Chonde, uzeni dzina lanu.” Koma munthuyo anati, “Chifukwa chiyani ukundifunsa dzina?” Kenaka anamudalitsa pomwepo. Choncho Yakobo anawatcha malowo Penueli, popeza anati, “Ndinaonana ndi Mulungu maso ndi maso koma sindinafe.”

Mose anakhala kumeneko pamodzi ndi Yehova masiku 40, usana ndi usiku, wosadya kanthu kapena kumwa madzi. Ndipo iye analemba pa miyala ija mawu a pangano, malamulo khumi.

Koma Mose ndi Aaroni anadzigwetsa chafufumimba ndipo analira mokweza, “Chonde Mulungu, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, kodi mudzakwiyira gulu lonse pamene munthu mmodzi yekha ndiye amene wachimwa?”

Mukanali komweko, ngati mudzamufunafuna Yehova Mulungu wanu mudzamupeza koma ngati mutamufunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Mukadzakhala pa chipsinjo ndipo zonsezi zikadzakuchitikirani, ndi pamene pambuyo pake mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumumvera Iye. Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wachifundo, Iye sadzakutayani kapena kukuwonongani kapena kuyiwala pangano lake ndi makolo anu, limene analitsimikiza mwa lumbiro.

Nditakwera ku phiri kuti ndikalandire miyala iwiri ya malamulo, ya pangano limene Yehova anachita ndi inu, ndinakhala ku phiriko kwa masiku makumi anayi usiku ndi usana, sindinadye buledi kapena kumwa madzi.

Tsono nthawi yomweyo ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usiku ndi usana. Sindinadye buledi kapena kumwa madzi chifukwa cha machimo onse amene munawachita, kuchita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kumukwiyitsa kwambiri.

Ine ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku chifukwa Yehova ananena kuti akuwonongani.

Tsopano ndinakhala ku phiri kuja kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku monga ndinachitira poyamba, ndipo Yehova anandimveranso nthawi iyi. Sichinali chifuniro chake kuti akuwonongeni.

Tsono Yoswa anangʼamba zovala zake nagwada nʼkuweramitsa mutu wake pansi patsogolo pa Bokosi la Yehova. Akuluakulu a Israeli nawonso anadzigwetsa pansi ndipo anakhala pomwepo mpaka madzulo atadziwaza fumbi kumutu kwawo.

Tsono Aisraeli onse, gulu lonse la ankhondo, anapita ku Beteli kukalira pamaso pa Yehova. Anakhala pansi nasala zakudya tsiku lonse mpaka madzulo. Anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova.

Yehova anabwera ndi kuyima pomwepo, ndi kuyitana monga nthawi zina zija, “Samueli! Samueli!” Ndipo Samueli anayankha, “Yankhulani, pakuti mtumiki wanu akumvetsera.”

Ndiponso kunena za ine, zisachitike kuti ndichimwire Yehova pakulephera kukupemphererani. Ndipo ine ndidzakuphunzitsani njira yabwino ndi yolungama kuti muziyendamo.

Pamenepo Solomoni anayimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova pamaso pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake kumwamba, nati: “Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, palibe Mulungu wofanana nanu kumwamba kapena pansi pa dziko, inu amene mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse.

Solomoni atamaliza mapemphero ndi mapembedzero onsewa kwa Yehova, anayimirira pa guwa lansembe la Yehova, nagwada atakweza manja ake kumwamba.

Pa nthawi yopereka nsembe, mneneri Eliya anasendera pafupi ndi guwa lansembe, napemphera kuti, “Inu Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, lero zidziwike kuti ndinu Mulungu mu Israeli ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, kuti ine ndachita zonsezi chifukwa mwalamula ndinu. Ndiyankheni, Inu Yehova, ndiyankheni, kuti anthu awa adziwe Inu Yehova, kuti ndinu Mulungu, ndipo kuti mutembenuziranso mitima yawo kwa Inu.” Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nunyeketsa nsembe yopserezayo, nkhuni, miyala ndi dothi lomwe. Unawumitsanso madzi amene anali mʼngalande. Anthu onse ataona zimenezi, anaweramitsa nkhope zawo pansi, nafuwula kuti, “Yehova ndiye Mulungu! Yehova ndiye Mulungu!”

Inu Yehova, tcherani khutu lanu ndipo mumve Yehova tsekulani maso anu ndipo muone, imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza kunyoza Inu Mulungu wamoyo.

Ndipo tsopano Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni ndithu mʼdzanja lake, kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndinu Mulungu.”

Hezekiya anatembenuka nayangʼana ku khoma ndipo anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, kumbukirani ndithu mmene ndayendera mokhulupirika ndi mtima wonse ndipo ndachita zolungama pamaso panu.” Hezekiya analira kwambiri.

Yabesi analira kwa Mulungu wa Israeli kuti, “Mundidalitse ndipo mukulitse dziko langa! Dzanja lanu likhale pa ine ndipo mundisunge kuti choyipa chisandigwere ndi kundisautsa.” Ndipo Mulungu anamupatsa chopempha chakecho.

Yamikani Yehova, itanani dzina lake; lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.

Dalirani Yehova ndi mphamvu zake; funafunani nkhope yake nthawi zonse.

Yamikani Yehova, pakuti Iye ndi wabwino; chikondi chake chikhala mpaka muyaya.

Iwo amayimiriranso mmawa uliwonse kuthokoza ndi kutamanda Yehova. Amachitanso chomwecho madzulo,

Pamenepo Solomoni anayimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova patsogolo pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake. Iyeyo anali atapanga nsanja yamkuwa, kutalika kwake kunali mamita awiri, mulifupi mwake munali mamita awiri, msinkhu wake unali mita imodzi ndi theka ndipo nsanjayo anayimika pakati pa bwalo lakunja. Iye anayimirira pa nsanjapo nagwada pamaso pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake kumwamba. Iye anati, “Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, palibe Mulungu wofanana nanu kumwamba kapena pa dziko. Inu amene mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse.

Koma Inu Yehova, Mulungu wanga, imvani pemphero ndi pembedzero la mtumiki wanu. Imvani kulira ndi pemphero la mtumiki wanu limene ndikupempha pamaso panu. Maso anu azikhala otsekuka kuyangʼana Nyumba ino usana ndi usiku, malo ano amene Inu munati mudzayikamo Dzina lanu, imvani pemphero la mtumiki wanu limene akupemphera pa malo ano. Imvani mapembedzero a mtumiki wanu ndi a anthu anu Aisraeli pamene akupemphera akuyangʼana malo ano. Imvani kumwambako, malo anu amene mumakhala; ndipo mukamva muzitikhululukira.

ndipo wina aliyense mwa Aisraeli akapemphera kapena kukudandaulirani, aliyense wa iwo akadziwa masautso ake ndi ululu wake, ndi kukweza manja awo kuloza Nyumba ino, pamenepo imvani kumwambako, malo anu wokhalamo. Khululukani ndipo muchitire aliyense molingana ndi zonse zimene anachita popeza Inu mumadziwa mtima wake, (pakuti ndinu nokha amene mumadziwa mitima ya anthu), motero iwo adzakuopani ndipo adzayenda mʼnjira zanu masiku onse amene adzakhale mʼdziko limene munalipereka kwa makolo athu.

“Tsono Inu Mulungu wanga, tsekulani maso anu ndi makutu anu kuti mumve mapemphero ochitikira pa malo ano.

ngati anthu anga, amene amatchedwa ndi dzina langa adzichepetsa ndi kupemphera ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zawo zoyipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwamba ndipo ndidzakhululuka tchimo lawo ndi kuchiritsa dziko lawo. Ndipo maso anga adzatsekuka ndi makutu anga adzakhala tcheru kumva mapemphero a pamalo pano.

Rehobowamu anachita zoyipa chifuwa mtima wake sunafunefune Yehova.

Kenaka Asa anafuwulira Yehova Mulungu wake ndipo anati “Yehova palibe wina wofanana nanu kuti angathandize anthu opanda mphamvu pakati pa amphamvu. Tithandizeni Inu Yehova Mulungu wathu pakuti ife timadalira Inu ndipo mʼdzina lanu ife tabwera kudzalimbana ndi gulu la ankhondo lalikulu kwambiri ngati ili. Inu Yehova ndinu Mulungu wathu, musalole kuti munthu akupambaneni.”

Iwo anachita pangano loti azifunafuna Yehova, Mulungu wa makolo awo, ndi mtima ndi moyo wawo wonse.

Ansembe ndi Alevi anayimirira kudalitsa anthu, ndipo Mulungu anawamvera pakuti pemphero lawo linafika kumwamba, malo ake oyera.

Mfumu Hezekiya ndi mneneri Yesaya mwana wa Amozi anafuwulira kumwamba mʼpemphero chifukwa cha zimenezi.

Ku mtsinje wa Ahava, ndinalengeza kuti anthu onse asale zakudya, adzichepetse pamaso pa Mulungu wathu ndi kupempha kuti atiyendetse bwino ife ndi ana athu, ndi kuteteza katundu wathu yense. Ine ndinali ndi manyazi kupempha mfumu kuti atipatse asilikali oyenda pansi ndi ena okwera pa akavalo kuti atiteteze kwa adani athu pa ulendo wathuwu popeza tinali titawuza kale mfumu kuti “Yehova amateteza aliyense amene amamudalira, koma amakwiyira onse amene amamukana.” Choncho tinasala zakudya ndi kupemphera kwa Mulungu wathu kuti atiteteze ndipo Iye anamva pemphero lathu.

Ndipo pa nthawi ya nsembe ya madzulo, ndinadzidzimuka mu mtima wanga wokhumudwa nʼkuyimirira, zovala zanga ndi mwinjiro wanga zikanali zongʼambika ndipo ndinagwada ndi kukweza manja anga kwa Yehova Mulungu wanga ndipo ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu wanga, ndine wamanyazi ndi wachisoni moti sindingathe kukweza nkhope yanga kwa Inu Mulungu wanga, chifukwa machimo athu akwera kupambana mitu yathu, ndipo kulakwa kwathu kwafika ku thambo.

Ezara anachoka ku Nyumba ya Mulungu napita ku chipinda cha Yehohanani, mwana wa Eliyasibu. Anatandala kumeneko usiku wonse ndipo sanadye chakudya kapena kumwa madzi popeza ankalira chifukwa cha kusankhulupirika kwa anthu obwera ku ukapolo.

Nditamva zimenezi, ndinakhala pansi ndi kuyamba kulira. Ndinalira kwa masiku angapo. Ndinkasala zakudya ndi kumapemphera pamaso pa Mulungu Wakumwamba. Ndinkati: “Inu Yehova, Mulungu wakumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa. Mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa onse amene amakukondani ndi kumvera malamulo anu. Tcherani khutu lanu ndi kutsekula maso anu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune limene ndikupemphera usana ndi usiku pamaso panu kupempherera Aisraeli, atumiki anu. Ndikuvomereza machimo a Aisraeli amene tinakuchimwirani. Ndithu, ine ndi banja la makolo anga tinakuchimwirani.

Ezara anatamanda Yehova, Mulungu wamkulu, ndipo anthu onse anakweza manja awo ndi kuyankha kuti, “Ameni, ameni.” Pambuyo pake onse anaweramitsa pansi mitu yawo napembedza Yehova akanali chizolikire choncho.

Pa tsiku la 24 la mwezi womwewo, Aisraeli anasonkhana pamodzi ndi kusala chakudya, kuvala ziguduli ndi kudzithira dothi pa mutu. Aisraeliwa anadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina ndipo anayimirira nayamba kuwulula machimo awo ndi zolakwa za makolo awo.

Chigawo chilichonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinafika, kunali maliro akulu pakati pa Ayuda. Iwo ankasala zakudya, kulira mofuwula ndi kumadandaula. Ambiri anavala ziguduli ndi kudzola phulusa.

“Pitani, mukasonkhanitse pamodzi Ayuda onse amene ali mu Susa ndipo mundisalire chakudya. Musadye kapena kumwa kwa masiku atatu, usiku ndi usana. Ine ndi anamwali anga onditumikira tidzasala chakudya monga inu. Izi zikachitika, ine ndidzapita kwa mfumu, ngakhale kutero ndikutsutsana ndi lamulo. Ndipo ngati nʼkufa ndife ndithu.”

Atamva zimenezi, Yobu anayimirira nangʼamba mkanjo wake, ndi kumeta tsitsi lake. Kenaka anadzigwetsa pansi napembedza Mulungu,

“Koma ndikanakhala ine, ndikanamudandawulira Mulungu; ndikanapereka mlandu wanga kwa Iye. Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka, zodabwitsa zimene sizingatheke kuwerengedwa.

Koma utayangʼana kwa Mulungu, ndi kudandaulira Wamphamvuzonse,

“Koma ngati upereka mtima wako kwa Iye ndi kutambasulira manja ako kwa Iyeyo,

Tsono muyitane ndipo ndidzayankha, kapena mulole kuti ine ndiyankhule ndipo Inu muyankhe.

Udzamupempha ndipo adzakumvera, ndipo udzapereka zimene unalonjeza.

Iye sayankha pamene anthu akufuwulira kwa Iye chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oyipa. Ndithu, Mulungu samva kupempha kwawo kopanda pake; Wamphamvuzonse sasamalira zimenezi.

Yobu atawapempherera abwenzi ake aja, Yehova anamubwezera chuma chake ndipo anamupatsa mowirikiza kuposa zomwe anali nazo kale.

Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwula ndipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera. Sela

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide. Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu, Inu Mulungu wa chilungamo changa. Pumulitseni ku zowawa zanga; chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe zoyimbira za zitoliro. Salimo la Davide. Tcherani khutu ku mawu anga, Inu Yehova, ganizirani za kusisima kwanga Mverani kulira kwanga kofuna thandizo, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, pakuti kwa Inu, ine ndikupemphera. Mmawa, Yehova mumamva mawu anga; Mmawa ndimayala zopempha zanga pamaso panu ndi kudikira mwachiyembekezo.

Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu, pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.

Mwa kunyada kwake woyipa safunafuna Mulungu; mʼmaganizo ake wonse mulibe malo a Mulungu.

Pemphero la Davide. Imvani Inu Yehova pempho langa lachilungamo; mverani kulira kwanga. Tcherani khutu kuti mumve pemphero langa popeza silikuchokera pakamwa pachinyengo.

Ine ndikuyitana Inu, Mulungu wanga, pakuti mudzandiyankha; tcherani khutu lanu kwa ine ndipo mumve pemphero langa.

Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize. Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.

tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa, pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga, ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.

Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova, ichi ndi chimene ndidzachifunafuna: kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova, ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.

Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu Yehova mundichitire chifundo ndipo mundiyankhe. Mtima wanga ukuti kwa Inu, “Funafuna nkhope yake!” Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna.

Dikirani pa Yehova; khalani anyonga ndipo limbani mtima nimudikire Yehova.

Salimo la Davide. Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa; musakhale osamva kwa ine. Pakuti mukapitirira kukhala chete, ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje. Imvani kupempha chifundo kwanga pomwe ndikuyitana kwa Inu kuti mundithandize, pomwe ndikukweza manja anga kuloza ku malo anu oyeretsetsa.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mwa Inu Yehova, ine ndimathawiramo; musalole nʼkomwe kuti ndichititsidwe manyazi; mundipulumutse chifukwa cha chilungamo chanu. Tcherani khutu lanu kwa ine, bwerani msanga kudzandilanditsa; mukhale thanthwe langa lothawirapo, linga lolimba kundipulumutsa ine.

Ine ndinafunafuna Yehova ndipo Iye anandiyankha; anandilanditsa ku mantha anga onse. Iwo amene amayangʼana kwa Iye, nkhope zawo zimanyezimira; nkhope zawo sizikhala zophimbidwa ndi manyazi. Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva; Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse. Mngelo wa Yehova amatchinjiriza amene amakonda Iye ndi kuwalanditsa. Lawani ndipo onani kuti Yehova ndi wabwino; wodala munthu amene amathawira kwa Iye.

Maso a Yehova ali pa olungama ndipo makutu ake ali tcheru kumva kulira kwawo; nkhope ya Yehova ikutsutsana ndi amene amachita zoyipa, kuwachotsa kuti asawakumbukirenso pa dziko lapansi. Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva; Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse. Yehova ali pafupi kwa osweka mtima ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.

Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu; pakati pa gulu lalikulu la anthu ndidzakutamandani.

Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa; usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo, pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.

“Imvani pemphero langa Inu Yehova, mverani kulira kwanga kopempha thandizo; musakhale chete pamene ndikulirira kwa Inu, popeza ndine mlendo wanu wosakhalitsa; monga anachitira makolo anga onse.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mofatsa ndinadikira Yehova Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.

Zambiri, Yehova Mulungu wanga, ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita. Zinthu zimene munazikonzera ife palibe amene angathe kukuwerengerani. Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera, zidzakhala zambiri kuzifotokoza.

Koma iwo amene amafunafuna Inu akondwere ndi kusangalala mwa Inu; iwo amene amakonda chipulumutso chanu nthawi zonse anene kuti, “Yehova akwezeke!” Komabe Ine ndine wosauka ndi wosowa; Ambuye andiganizire. Inu ndinu thandizo langa ndi wondiwombola wanga; Inu Mulungu wanga, musachedwe.

Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake, nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane; pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.

Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu; ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu; ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.” Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

“Pereka nsembe zachiyamiko kwa Mulungu, kwaniritsa malonjezo ako kwa Wammwambamwamba. Ndipo undiyitane pa tsiku lako la masautso; Ine ndidzakulanditsa, ndipo udzandilemekeza.”

Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga; mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya Davide. Pa zoyimbira za zingwe. Mvetserani pemphero langa, Inu Mulungu, musakufulatire kupempha kwanga,

Koma ine ndinafuwulira kwa Mulungu, ndipo Yehova anandipulumutsa. Madzulo, mmawa ndi masana ndimalira mowawidwa mtima, ndipo Iye amamva mawu anga.

Tulani nkhawa zanu kwa Yehova ndipo Iye adzakulimbitsani; Iye sadzalola kuti wolungama agwe.

Inu mphamvu yanga, ine ndiyangʼana kwa inu; Inu Mulungu, ndinu linga langa. Mulungu wanga wachikondi. Mulungu adzapita patsogolo panga ndipo adzandilola kunyada pa iwo amene amandinyoza.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Loyimbidwa ndi zipangizo za zingwe. Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu; mvetserani pemphero langa. Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka; tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kutsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Davide. Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha; chipulumutso changa chimachokera kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka.

Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga; chiyembekezo changa chichokera mwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka. Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu: Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga. Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu; khuthulani mitima yanu kwa Iye, pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu. Sela

Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda. Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, moona mtima ine ndimakufunafunani; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka inu, mʼdziko lowuma ndi lotopetsa kumene kulibe madzi.

Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga, matamando ake anali pa lilime panga. Ndikanasekerera tchimo mu mtima mwanga Ambuye sakanamvera; koma ndithu Mulungu wamvetsera ndipo watchera khutu ku mawu a kupempha kwanga. Matamando akhale kwa Mulungu amene sanakane pemphero langa kapena kuletsa chikondi chake pa ine!

Ndafowoka ndikupempha chithandizo; kummero kwanga kwawuma gwaa, mʼmaso mwanga mwada kuyembekezera Mulungu wanga.

Wosauka adzaona ndipo adzasangalala, Inu amene mumafunafuna Mulungu, mitima yanu ikhale ndi moyo!

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Salimo la Asafu. Nyimbo. Tikuthokoza Inu Mulungu, tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe, anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Asafu. Ndinafuwulira Mulungu kupempha thandizo; ndinafuwula mokweza kwa Mulungu kuti anditcherere khutu. Pamene ndinali pa masautso ndinafunafuna Ambuye; usiku ndinatambasula manja mosalekeza ndipo moyo wanga unakana kutonthozedwa.

Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena; Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake, koma musawalole kuti abwerere ku zopusa.

Yehova imvani pemphero langa; mvetserani kulira kwanga kofuna chifundo. Pa tsiku la mavuto anga ndidzayitana Inu, pakuti Inu mudzandiyankha.

Salimo la ana a Kora. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a nyimbo yoti: “Pa Matenda ndi pa Mazunzo.” Ndakatulo ya Hemani, wa banja la Ezara. Inu Yehova, Mulungu amene mumandipulumutsa, usana ndi usiku ndimalira pamaso panu. Pemphero langa lifike pamaso panu; tcherani khutu lanu kuti mumve kulira kwanga.

Inu Yehova, Ine ndimalirira thandizo; mmawa mapemphero anga amafika pamaso panu.

Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola, kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.

Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha; ndidzakhala naye pa mavuto, ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza.

Salimo. Nyimbo ya pa tsiku la Sabata. Nʼkwabwino kutamanda Yehova ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba, Kulengeza chikondi chanu mmawa, ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku,

Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira, tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu; pakuti Iye ndiye Mulungu wathu ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za mʼdzanja lake. Lero ngati inu mumva mawu ake, musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba, monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu.

Pemphero la munthu wosautsidwa, pamene walefuka, nakhuthulira pamaso pa Yehova kulira kwakeko. Yehova imvani pemphero langa; kulira kwanga kopempha thandizo kufike kwa Inu. Musandibisire nkhope yanu pamene ndili pa msautso. Munditcherere khutu; pamene ndiyitana ndiyankheni msanga.

Iye adzayankha pemphero la anthu otayika; sadzanyoza kupempha kwawo.

Munyadire dzina lake loyera; mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere. Dalirani Yehova ndi mphamvu zake; funafunani nkhope yake nthawi yonse.

Mawondo anga afowoka chifukwa cha kusala zakudya, thupi langa lawonda ndi mutu wanga womwe.

Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga; Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo. Pakuti ananditchera khutu, ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga. Zingwe za imfa zinandizinga, zoopsa za ku dziko la anthu akufa zinandigwera; ndinapeza mavuto ndi chisoni. Pamenepo ndinayitana dzina la Yehova: “Inu Yehova, pulumutseni!”

Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.

Ndili mʼmasautso anga ndinalirira Yehova, ndipo Iye anayankha pondichotsa mʼmasautsowo.

Ndidzakuyamikani chifukwa Inu munandiyankha; mwakhala chipulumutso changa.

Odala ndi amene amasunga malamulo ake, amene amafunafuna Iyeyo ndi mtima wawo wonse.

Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse; musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.

Ndimayitana ndi mtima wanga wonse; ndiyankheni Inu Yehova, ndipo ndidzamvera zophunzitsa zanu. Ndikuyitana kwa Inu; pulumutseni ndipo ndidzasunga umboni wanu. Ndimadzuka tambala asanalire kuti ndipemphe thandizo; chiyembekezo changa chili mʼmawu anu. Maso anga amakhala chipenyere nthawi yonse ya usiku, kuti ndithe kulingalira malonjezo anu. Imvani mawu anga molingana ndi chikondi chanu chosasinthika; Yehova sungani moyo wanga, molingana ndi malamulo anu.

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama; Ambuye imvani mawu anga. Makutu anu akhale tcheru kumva kupempha chifundo kwanga.

Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera, ndipo ndimakhulupirira mawu ake. Moyo wanga umayembekezera Ambuye, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa, inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,

Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino. Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

Yamikani Mulungu wa milungu. Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

Yamikani Ambuye wa ambuye, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

Salimo la Davide. Inu Yehova ndikukuyitanani; bwerani msanga kwa ine. Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu. Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani; kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo.

Ndakatulo ya Davide, pamene iyeyo anali mʼphanga. Pemphero. Ndikulirira Yehova mofuwula; ndikukweza mawu anga kwa Yehova kupempha chifundo. Ndikukhuthula madandawulo anga pamaso pake; ndikufotokoza za masautso anga pamaso pake.

Salimo la Davide. Yehova imvani pemphero langa, mvetserani kulira kwanga kopempha chifundo; mwa kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu bwerani kudzandithandiza.

Maso a onse amayangʼana kwa Inu, ndipo Inu mumawapatsa chakudya chawo pa nthawi yoyenera. Mumatsekula dzanja lanu ndi kukwaniritsa zokhumba za chamoyo chilichonse. Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse, ndi wokonda zonse zimene anazipanga. Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana, onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi. Iye amakwaniritsa zokhumba za iwo amene amamuopa; amamva kulira kwawo ndi kuwapulumutsa.

“Tsono mudzandiyitana koma sindidzayankha; mudzandifunafuna, koma simudzandipeza. Popeza iwo anadana ndi chidziwitso ndipo sanasankhe kuopa Yehova, popeza iwo sanasamale malangizo anga ndipo ananyoza chidzudzulo changa.

Ndimakonda amene amandikonda, ndipo amene amandifunafuna amandipeza.

Wokana kumvera malamulo ngakhale pemphero lake lomwe limamunyansa Yehova.

Usamafulumire kuyankhula, usafulumire mu mtima mwako kunena chilichonse pamaso pa Mulungu. Mulungu ali kumwamba ndipo iwe uli pa dziko lapansi, choncho mawu ako akhale ochepa.

Zikondwerero zanu za Mwezi Watsopano ndi masiku anu opatulika ndimadana nazo. Zasanduka katundu wondilemera; ndatopa kuzinyamula. Mukamatambasula manja anu popemphera, Ine sindidzakuyangʼanani; ngakhale muchulukitse mapemphero anu, sindidzakumverani. Manja anu ndi odzaza ndi magazi; sambani, dziyeretseni. Chotsani pamaso panu ntchito zanu zoyipa! Lekani kuchita zoyipa,

Ndidzayembekezera Yehova, amene akubisira nkhope yake nyumba ya Yakobo. Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.

Moyo wanga umalakalaka Inu usiku wonse; nthawi yammawa ndimafunafuna Inu. Pamene muweruza dziko lapansi anthu amaphunzira kuchita chilungamo.

Inu anthu a ku Ziyoni, amene mukhala mu Yerusalemu simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu kopempha thandizo! Ndipo akadzamva, adzakuyankhani.

koma iwo amene amakhulupirira Yehova adzalandira mphamvu zatsopano. Adzawuluka ngati chiwombankhanga; adzathamanga koma sadzalefuka, adzayenda koma sadzatopa konse.

Funafunani Yehova pamene Iye akupezeka. Mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.

amenewa Ine ndidzawafikitsa ku phiri langa lopatulika, ndidzawapatsa chimwemwe mʼnyumba yanga ya mapemphero. Zopereka zawo zopsereza ndi nsembe zawo ndidzazilandira pa guwa langa la nsembe. Paja nyumba yanga idzatchedwa nyumba ya mapemphero ya anthu a mitundu yonse.”

Kodi kusala kudya kumene ndimakufuna Ine nʼkumeneku, kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi? Kodi ndi tsiku loti munthu angowerama pansi ngati bango ndi kumayala ziguduli nʼkuthirapo phulusa nʼkugonapo? Kodi ndiye mumati kusala kudya kumeneko, tsiku lokondweretsa Yehova? “Kodi si uku kusala kudya kumene Ine ndimakufuna: Kumasula maunyolo ozunzizira anthu ndi kumasula zingwe za goli, kupereka ufulu kwa oponderezedwa ndi kuphwanya goli lililonse?

Koma zoyipa zanu zakulekanitsani ndi Mulungu wanu; ndipo wakufulatirani chifukwa cha machimo anu, kotero Iye sadzamva.

“Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a amene sankandipempha kanthu; ndipo ndinalola kuti anthu amene ankandifunafuna kuti andipeze. Kwa mtundu wa anthu umene sunkapempha chithandizo kwa Ine, ndinati, ‘Ine ndili pano, Ine ndili pano.’

Ndidzawayankha ngakhale asanathe nʼkupempha komwe. Pamene akuyankhula kumene Ine ndidzakhala nditamva kale.

Choncho Yehova akuti, ‘Ndidzawagwetsera mavuto amene sadzatha kuwalewa. Ngakhale adzandilirire, sindidzawamvera. Anthu a mʼmizinda ya Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu adzapita ndi kukalirira milungu imene ankayifukizira lubani, koma milunguyo sidzawathandiza ndi pangʼono pomwe mavuto akadzafika.

Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani,” akutero Yehova, “ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo. Nthawi imeneyo mudzandiyitana, ndi kunditama mopemba ndipo ndidzakumverani. Mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza. Mukadzandifuna ndi mtima wanu wonse mudzandipezadi,” akutero Yehova, “ndipo ndidzakubwezerani zabwino zanu. Ndidzakusonkhanitsani kuchokera ku mayiko onse ndi kumalo konse kumene munali,” akutero Yehova, “ndipo ndidzakubweretsani kumalo kumene munali ndisanakuchotseni kukupititsani ku ukapolo.”

‘Unditame mopemba ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuwuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziwa.’

Tsono iwe upite ku Nyumba ya Yehova pa tsiku losala kudya ndipo ukawerenge mawu a Yehova ochokera mʼbukumu amene ndinakulembetsa anthu onse akumva. Ukawawerengere anthu onse a ku Yuda amene amabwera ku Nyumba ya Mulungu kuchokera ku mizinda yawo. Mwina mwake adzapempha kwa Yehova ndipo aliyense adzatembenuka ndi kusiya makhalidwe ake oyipa pakuti mkwiyo ndi ukali wa Yehova pa anthu awa ndi woopsa kwambiri.”

“Masiku amenewo, nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “anthu a ku Israeli ndi anthu a ku Yuda onse pamodzi adzabwera akulira. Adzafunitsitsa kuchita zimene Yehova Mulungu wawo akufuna. Adzafunsa njira ya ku Ziyoni ndi kuyamba ulendo wopita kumeneko. Iwo adzadzipereka kwa Yehova pochita naye pangano lamuyaya limene silidzayiwalika.

Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye, kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo; nʼkwabwino kudikira chipulumutso cha Yehova modekha.

Tiyeni tikweze mitima yathu ndi manja athu kwa Mulungu kumwamba ndipo tinene kuti:

Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi? Iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri kuposa izi.” Kenaka Iye anapita nane mʼkati mwa bwalo la Nyumba ya Yehova. Kumeneko ku khomo lolowera ku Nyumba ya Yehova pakati pa khonde ndi guwa lansembe, panali amuna 25. Anafulatira Nyumba ya Mulungu wa Yehova ndipo nkhope zawo zinaloza kummawa, ndipo ankapembedza dzuwa choyangʼana kummawa. Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waziona zimenezi? Kodi nʼchinthu chopepuka kuti anthu a ku Yuda azichita zonyansa zimene akuchitazi pano? Kodi afike mpaka pomafalitsa za ndewu mʼdziko lonse? Iwotu akuwutsa ukali wanga. Akundipsetsa mtima ndi zochita zawo! Choncho Ine ndidzawalanga ndili wokwiya. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka. Ngakhale atandifuwulira mʼmakutu mwanga sindidzawamvera.”

Amasintha nthawi ndi nyengo; amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso. Amapatsa nzeru kwa anzeru ndi chidziwitso kwa ozindikira zinthu. Amavumbulutsa zinthu zozama ndi zobisika; amadziwa zimene zili mu mdima, ndipo kuwunika kumakhala ndi Iye. Ndikuyamika ndi kutamanda Inu Mulungu wa makolo anga: mwandipatsa nzeru ndi mphamvu, mwandiwululira zomwe tinakupemphani, mwatiwululira maloto a mfumu.”

Nduna zoyendetsa ufumu wanu, aphungu, akalonga ndi abwanamkubwa tonse tagwirizana kuti inu mfumu mukhazikitse lamulo ndi kulisindikiza kuti aliyense amene apemphera kwa mulungu wina kapena kwa munthu kupatula kwa inu mfumu, pa masiku makumi atatu otsatirawa, adzaponyedwa mʼdzenje la mikango. Tsopano inu mfumu khazikitsani lamulo limeneli ndipo musindikizepo dzina lanu kuti lisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperezi, amene sasinthidwa.” Choncho mfumu Dariyo anasindikizapo dzina lake pa lamuloli.

Danieli atamva kuti lamulo lasindikizidwa, anapita ku nyumba kwake nalowa mʼchipinda chapamwamba chimene mazenera ake anali otsekula kuloza ku Yerusalemu. Katatu pa tsiku iye ankagwada pansi pa mawondo ndipo amapemphera, kuyamika Mulungu wake, monga momwe ankachitira kale. Ndipo anthu awa anapita pamodzi ndi kukapeza Danieli akupemphera ndi kupempha Mulungu wake kuti amuthandize. Kotero iwo anapita kwa mfumu ndipo anayankhula naye za lamulo lake kuti, “Kodi simunasindikize lamulo lakuti pa masiku makumi atatu otsatirawa aliyense amene apemphera kwa mulungu wina aliyense kapena kwa munthu kupatula kwa inu mfumu, adzaponyedwa mʼdzenje la mikango?” Mfumu inayankha kuti, “Lamulo lilipobe monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperezi, amene sangathe kusinthika.” Kenaka iwo anati kwa mfumu, “Danieli, amene ndi mmodzi mwa akapolo ochokera ku Yuda, sakulabadira inu mfumu, kapena lamulo limene munasindikizapo dzina lanu lija. Iye akupempherabe katatu pa tsiku.”

Choncho ndinatembenukira kwa Ambuye Mulungu ndipo ndinamudandaulira ndi kupempha posala kudya, ndi kuvala chiguduli ndi kudzola phulusa. Ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza kuti tinachimwa: Ndinati, “Inu Ambuye, Mulungu wamkulu ndi woopsa, amene mumasunga pangano lanu la chikondi kwa onse amene amakukondani ndi kumvera malamulo anu, tachimwa ndipo tachita zolakwa ndi zoyipa. Takuwukirani posiya malangizo ndi malamulo anu.

“Tsopano Mulungu wathu, imvani mapemphero ndi zopempha za mtumiki wanu. Kuti anthu onse akudziweni kuti ndinu Ambuye, komerani mtima malo anu opatulika amene asanduka bwinja. Tcherani khutu, Inu Mulungu, ndipo imvani; tsekulani maso anu ndipo onani mabwinja athu ndi mzinda umene umadziwika ndi dzina lanu. Sitikupempha chifukwa chakuti ndife olungama, koma chifukwa cha kukula kwa chifundo chanu. Inu Ambuye imvani mawu athu! Ambuye khululukani! Ambuye timvereni, ndipo muchitepo kanthu! Kuti anthu adziwe kuti Inu ndinu Mulungu wanga musachedwe chifukwa mzinda wanu ndi anthu anu amadziwika ndi dzina lanu.”

Ndikuyankhula ndi kupemphera, kuvomereza machimo anga ndi machimo a anthu anga Aisraeli ndi kupempherera phiri lake loyera kwa Yehova Mulungu wanga, Gabrieli, munthu uja amene ndinamuona mʼmasomphenya poyambirira, anabwera kwa ine mowuluka. Iyi inali nthawi ya nsembe ya madzulo. Anandilangiza kuti, “Danieli ndabwera tsopano kuti ndikupatse nzeru kuti uzitha kumvetsa zinthu. Utangoyamba kupemphera, Mulungu anayankha. Tsono ine ndabwera kudzakuwuza yankholo, popeza ndiwe wokondedwa kwambiri. Choncho mvetsetsa pamene ndikufotokoza za zinthu zimene unaziona mʼmasomphenya.

Pa nthawi imeneyi, ine Danieli ndinalira kwa masabata atatu. Sindinadye chakudya chokoma; nyama ndi vinyo sizinakhudze milomo yanga ndi pangʼono pomwe; ndipo sindinadzole mafuta aliwonse mpaka patatha masabata atatu.

Dzanja linandikhudza ndi kundinyamula ndipo ndinachita ngati kuwerama pa mawondo manja atagwira pansi. Iye anati, “Danieli, iwe wokondedwa kwambiri, imirira ndipo uganizire mosamala mawu ndiyankhule kwa iwe, popeza tsopano ndatumidwa kwa iwe.” Atanena izi kwa ine ndinayimirira monjenjemera. Ndipo iye anapitiriza nati, “Usachite mantha Danieli. Kuyambira tsiku loyamba pamene unatsimikiza mtima kuti umvetse zinthuzi ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, pempho lako linamveka ndipo ndabwera kudzayankha mapemphero akowo. Koma mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya ananditchingira pa masiku 21, kenaka Mikayeli, mmodzi mwa angelo akuluakulu anadza kudzandithandiza chifukwa ndinakhala komweko ndi mafumu a ku Peresiya. Tsopano ndafika kuti ndidzakufotokozere zimene zidzachitika kwa anthu a mtundu wako kutsogolo. Ndipo pali masomphenya enanso okhudza nthawi imene ikudza.” Pa nthawi yomwe ankanena izi kwa ine, ndinazolika nkhope yanga pansi kusowa chonena.

Ndipo ndidzabwerera ku malo anga mpaka anthu anga atavomereza kulakwa kwawo. Ndipo iwo adzafunafuna nkhope yanga; mʼmasautso awo adzandifunitsitsa Ine.”

Lengezani tsiku lopatulika losala zakudya, itanani msonkhano wopatulika. Sonkhanitsani akuluakulu ndi anthu onse okhala mʼdziko ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu ndipo alirire Yehova.

“Ngakhale tsopano, bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse posala zakudya ndi kukhetsa misozi,” akutero Yehova. Ngʼambani mtima wanu osati zovala zanu. Bwererani kwa Yehova Mulungu wanu, pakuti Iye ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka, ndipo amaleka kubweretsa mavuto.

Yona ali mʼmimba mwa chinsomba chija anapemphera kwa Yehova Mulungu wake. Iye anati: “Pamene ndinali mʼmavuto anga ndinayitana Yehova, ndipo Iye anandiyankha. Ndili ku dziko la anthu akufa ndinapempha thandizo, ndipo Inu munamva kulira kwanga.

“Pamene moyo wanga umachoka mwa ine, ine ndinakumbukira Inu Yehova, ndipo pemphero langa linafika kwa inu, ku Nyumba yanu yopatulika.

Anthu a ku Ninive anakhulupirira Mulungu. Analengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamngʼono yemwe asale zakudya ndipo avale chiguduli. Mfumu ya ku Ninive itamva nkhaniyi, inatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake waufumu ndipo inavala chiguduli ndi kukhala pansi pa fumbi. Tsono mfumuyo inalengeza mu Ninive kuti, “Mwa lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake: “Munthu aliyense kapenanso nyama, ngʼombe kapena nkhosa, zisadye kanthu kalikonse; musazilole kuti zidye kapena kumwa. Koma anthu avale ziguduli, ndipo nyamanso aziveke ziguduli. Munthu aliyense azifuwula kwa Mulungu ndi mphamvu zake zonse. Anthuwo asiye makhalidwe awo oyipa ndi machitidwe achiwawa. Angadziwe ndani? Mwina Mulungu nʼkutikhululukira ndipo mwa chifundo chake nʼkuleka kutikwiyira, ifeyo osawonongedwa.” Mulungu ataona zimene anthuwo anachita, ndi mmene anasiyira makhalidwe awo oyipa, anawachitira chifundo ndipo sanabweretse chiwonongeko chimene anawaopseza nacho.

Pamenepo adzalira kwa Yehova, koma Iye sadzawayankha. Nthawi imeneyo Iye adzawabisira nkhope yake chifukwa cha zoyipa zimene anazichita.

Koma ine ndikudikira Yehova mwachiyembekezo, ndikudikira Mulungu Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga adzamvetsera.

Funafunani Yehova, inu nonse odzichepetsa a mʼdziko, inu amene mumachita zimene amakulamulani. Funafunani chilungamo, funafunani kudzichepetsa; mwina mudzatetezedwa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.

“Funsa anthu onse a mʼdziko ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala zakudya pa mwezi wachisanu ndi wachisanu ndi chiwiri pa zaka 70 zapitazi, kodi munkasala chifukwa cha Ine?

ndipo nzika za mzinda wina zidzapita ku mzinda wina, kukanena kuti, ‘Tiyeni mwamsanga tikapemphe madalitso kwa Yehova ndi kukapembedza Yehova Wamphamvuzonse. Inenso ndikupita kumeneko.’ Anthu ambiri ndiponso a ku mayiko amphamvu adzabwera ku Yerusalemu kudzapembedza Yehova Wamphamvuzonse ndi kudzapempha madalitso.”

Chigawo chachitatuchi ndidzachiyika pa moto; ndidzawayeretsa monga momwe amayeretsera siliva ndi kuwayesa monga momwe amayesera golide. Adzayitana pa dzina langa ndipo Ine ndidzawayankha; Ine ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’ ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndiye Mulungu wathu.’ ”

Ndipo atasala kudya masiku makumi anayi usana ndi usiku, anamva njala.

Koma Ine ndikuwuzani kuti, ‘Kondani adani anu ndi kuwapempherera okuzunzani

“Pamene mupemphera, musakhale ngati achiphamaso, chifukwa iwo amakonda kupemphera choyimirira mʼmasunagoge ndi pa mphambano za mʼmisewu kuti anthu awaone. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse. Koma pamene mupemphera, lowani mʼchipinda chanu chamʼkati, ndi kutseka chitseko ndipo mupemphere kwa Atate anu amene saoneka. Ndipo Atate anu, amene amaona zochitika mseri, adzakupatsani mphotho. Ndipo pamene mukupemphera, musamabwerezabwereza monga akunja, pakuti iwo amaganiza kuti adzamveka chifukwa chochulutsa mawu. Musakhale ngati iwo chifukwa Atate anu amadziwa zimene musowa musanapemphe.

“Chifukwa chake pempherani motere: “ ‘Atate athu akumwamba, dzina lanu lilemekezedwe, Ufumu wanu ubwere, chifuniro chanu chichitike pansi pano monga kumwamba. Mutipatse chakudya chathu chalero. Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso tawakhululukira amangawa athu. Ndipo musatitengere kokatiyesa; koma mutipulumutse kwa woyipayo.’

“Pamene mukusala kudya, musaonetse nkhope yachisoni monga achita achiphamaso, pakuti iwo amasintha nkhope zawo kuonetsa anthu kuti akusala kudya. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwo alandiriratu mphotho yawo yonse. Koma pamene ukusala kudya, samba mʼmaso nudzole mafuta kumutu, kuti usaonekere kwa anthu kuti ukusala kudya koma kwa Atate ako ali mseri; ndipo Atate ako amene amaona za mseri adzakupatsa mphotho.

Chifukwa chake musadere nkhawa ndi kuti, ‘Tidzadya chiyani?’ kapena ‘Tidzamwa chiyani?’ kapena ‘Tidzavala chiyani?’ Pakuti anthu akunja amazifuna zinthu zonsezi ndipo Atate anu akumwamba adziwa kuti musowa zimenezi. Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu.

“Pemphani ndipo mudzapatsidwa; funafunani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsekulirani. Pakuti wopempha aliyense amalandira; ndi wofuna amapeza; ndipo iye amene agogoda, adzamutsekulira. “Ndani mwa inu, mwana wake akamupempha buledi amamupatsa mwala? Kapena ngati mwana apempha nsomba, kodi amamupatsa njoka? Tsono ngati inu woyipitsitsa mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanga Atate anu akumwamba sadzapereka mphatso zabwino kwa iwo amene amupempha?

Ndipo ophunzira a Yohane anabwera namufunsa Iye kuti, “Bwanji ife ndi Afarisi timasala kudya koma ophunzira anu sasala kudya?” Yesu anayankha kuti, “Kodi oyitanidwa ku ukwati angamalire bwanji pamene mkwati ali naye pamodzi? Nthawi idzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa ndi pamene adzasala kudya.”

Pa nthawi imeneyo Yesu anati, “Ine ndikukuyamikani Inu Atate Ambuye akumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa Inu mwawabisira zinthu izi anzeru ndi ophunzira ndi kuziwulula kwa ana angʼonoangʼono.

Atatha kuwawuza kuti azipita kwawo, Iye anakwera ku phiri yekha kukapemphera. Pamene kumada anali kumeneko yekha.

“Komanso ndikukuwuzani inu kuti ngati awiri a inu pa dziko lapansi avomerezana kanthu kalikonse kamene mukapempha, Atate anga akumwamba adzakuchitirani. Pakuti pamene awiri kapena atatu asonkhana pamodzi mʼdzina langa, Ine ndili nawo pomwepo.”

Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi. Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero.”

Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo nati, “Imwani nonsenu.

Kenaka Yesu anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo anawawuza kuti, “Khalani pano pamene Ine ndikukapemphera apo.” Anatenga Petro ndi ana awiri a Zebedayo, ndipo anayamba kumva chisoni ndi kuvutika mu mtima. Pamenepo anawawuza kuti, “Moyo wanga uli ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo dikirani pamodzi ndi Ine.” Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi chafufumimba napemphera kuti, “Atate anga, ngati ndikotheka, chikho ichi chichotsedwe kwa Ine. Koma osati monga mmene ndifunira, koma monga mufunira Inu.” Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nawapeza ali mtulo. Iye anafunsa Petro kuti, “Kodi anthu inu, simukanakhala maso pamodzi ndi Ine kwa ora limodzi lokha? Khalani maso ndi kupemphera kuti musagwe mʼmayesero. Mzimu ukufuna koma thupi ndi lofowoka.” Anachokanso nakapemphera kachiwiri kuti, “Atate anga, ngati chikhochi sichingandichoke, mpaka nditamwa, kufuna kwanu kuchitike.”

Pa nthawi imeneyo chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. Dziko linagwedezeka ndipo miyala inangʼambika.

Mmamawa, kukanali kamdima, Yesu anadzuka, nachoka pa nyumbapo kupita kumalo kwa yekha, kumene anakapemphera.

Ndipo ophunzira a Yohane ndi a Afarisi amasala kudya. Anthu ena anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Zitheka bwanji kuti ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma anu satero?” Yesu anayankha nati, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya bwanji pamene iye ali nawo pamodzi? Iwo sangatero, pamene iye ali nawo pamodzi. Koma nthawi idzafika pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo, ndipo pa tsiku limenelo adzasala kudya.

Atawasiya, Iye anakwera ku phiri kukapemphera.

Yesu anati, “ ‘Ngati mungathe!’ Zinthu zonse ndi zotheka kwa iye amene akhulupirira.” Nthawi yomweyo abambo a mwanayo anafuwula kuti, “Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga!”

Iye anayankha kuti, “Mtundu uwu umatuluka pokhapokha mwapemphera ndi kusala kudya.”

Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo. Nʼchifukwa chake ndikukuwuzani kuti chilichonse chimene mupempha mʼpemphero, khulupirirani kuti mwalandira, ndipo chidzakhala chanu.

Pamene muyimirira kupemphera, ngati muli ndi chifukwa ndi wina, mukhululukireni, kuti Atate anu akumwamba akukhululukireni machimo anu.” (Koma ngati simukhululukirana, ngakhale Atate anu akumwamba sadzakhululukira machimo anu).

Ndipo anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Khalani pano pamene Ine ndi kupemphera.” Iye anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane, ndipo anayamba kumva chisoni kwambiri ndi kuvutika mu mtima. Iye anawawuza kuti, “Moyo wanga wagwidwa ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo musagone.” Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi ndi kupemphera kuti ngati ndi kotheka oralo limupitirire. Iye anati, “Abba, Atate, zinthu zonse ndi zotheka ndi Inu. Chotsereni chikhochi. Komabe chitani zimene Inu mukufuna, osati zimene Ine ndikufuna.” Kenaka anabwerera kwa ophunzira ake ndipo anawapeza akugona, Iye anati kwa Petro, “Simoni, kodi uli mtulo? Kodi simukanatha kukhala maso kwa ora limodzi? Khalani tcheru ndi kupemphera kuti musalowe mʼmayesero. Mzimu ukufuna, koma thupi ndi lofowoka.”

Chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi.

Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.”

ndipo kenaka anakhala wamasiye mpaka pamene anali ndi zaka 84. Iye sanachoke mʼNyumba ya Mulungu koma ankapembedza usiku ndi usana, kusala kudya ndi kupemphera. Pa nthawiyo pamene ankapita kwa iwo, iye anayamika Mulungu ndi kuyankhula za Mwanayo kwa onse amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.

Pamene anthu onse ankabatizidwa, Yesu anabatizidwanso. Ndipo akupemphera, kumwamba kunatsekuka.

kumene anayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anayi. Sanadye kena kalikonse pa masiku amenewo, ndipo pa mapeto pake anamva njala.

Koma Yesu nthawi zambiri ankachoka kupita ku malo a yekha kukapemphera.

Iwo anati kwa Iye, “Ophunzira a Yohane amasala kudya ndi kupemphera kawirikawiri, monganso ophunzira a Afarisi, koma anu amangodya ndi kumwa.” Yesu anawayankha kuti, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya pamene mkwati ali pakati pawo? Koma nthawi ikubwera pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo. Masiku amenewo adzasala kudya.”

Tsiku lina, masiku amenewo, Yesu anapita ku phiri kukapemphera ndipo anakhala usiku wonse akupemphera kwa Mulungu.

“Koma Ine ndikuwuza inu amene mukundimva: Kondani adani anu, chitirani zabwino amene amakudani. Dalitsani amene amakutembererani, apempherereni amene amakusautsani.

Patatha pafupifupi masiku asanu ndi atatu Yesu atanena izi, Iye anatenga Petro, Yohane ndi Yakobo ndi kukwera ku phiri kukapemphera. Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake, ndi zovala zake zinawala monyezimira kwambiri.

Tsiku lina Yesu amapemphera pamalo ena. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Ambuye tiphunzitseni kupemphera, monga momwe Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.” Yesu anawawuza kuti, “Pamene mukupemphera muzinena kuti: “ ‘Atate, dzina lanu lilemekezedwe, ufumu wanu ubwere. Mutipatse chakudya chathu chalero, mutikhululukire machimo athu, monga ifenso timakhululukira aliyense amene watilakwira. Ndipo musalole kuti tigwe mʼmayesero.’ ”

Kenaka anawawuza kuti, “Tiyerekeze: Mmodzi mwa inu atakhala ndi bwenzi lake, ndipo iye nʼkupita ku nyumba yake pakati pa usiku, nakanena kuti, ‘Mnzanga, bwereke malofu atatu abuledi, chifukwa ndalandira bwenzi langa amene ali pa ulendo ndipo ine ndilibe choti ndimupatse.’ “Ndipo yerekezani kuti amene ali mʼnyumbamo ndi kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine, ndatseka kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona. Ine sindingadzukenso kuti ndidzakupatse.’ Ine ndikukuwuzani kuti adzadzuka ndi kumupatsa bulediyo, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma la munthu wopemphayo, ndipo kudzamupatsa zonse zimene akuzifuna.

“Choncho Ine ndikunena kwa inu kuti: Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani ndipo adzakutsekulirani. Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira. “Ndani mwa inu abambo, kodi mwana wanu atapempha nsomba, mʼmalo mwake mungamupatse njoka? Kapena atapempha dzira, kodi mungamupatse chinkhanira? Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!”

ngati anthu oyembekezera kubwera kwa mbuye wawo kuchokera kuphwando la ukwati, kuti pamene afika ndi kugogoda akhoza nthawi yomweyo kumutsekulira chitseko. Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo pobwera adzawapeze akudikira. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti adzakonzekera kuwatumikira, adzakhala nawo pa tebulo ndipo adzabwera ndi kuwatumikira.

Kenaka Yesu anawuza ophunzira ake fanizo kuwaonetsa kuti iwo ayenera kumapemphera nthawi zonse ndikuti asafowoke. Iye anati, “Mʼmudzi wina munali woweruza wosaopa Mulungu ngakhalenso kulabadira za anthu. Ndipo panali mkazi wamasiye mʼmudzimo amene ankabwerabwera kwa iye ndi dandawulo lake kuti, ‘Mundiweruze mlandu mwachilungamo pakati pa ine ndi otsutsana nane.’ “Kwa nthawi yayitali woweruzayo ankakana. Koma pa mapeto analingalira nati, ‘Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kulabadira za anthu, koma chifukwa chakuti mkazi wamasiyeyu akundivutitsa, ine ndimuweruzira mlandu wake mwachilungamo kuti asanditopetse ndi kubwerabwera kwakeko!’ ” Ndipo Ambuye anati, “Tamvani zimene woweruza wopanda chilungamoyu wanena. Tsono chingamuletse nʼchiyani Mulungu kubweretsa chilungamo kwa osankhika ake, amene amalira kwa Iye usana ndi usiku? Kodi adzapitirirabe osawalabadira? Ine ndikukuwuzani inu, adzaonetsetsa kuti alandire chilungamo, ndiponso mofulumira. Komabe, pamene Mwana wa Munthu akubwera, kodi adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi?”

“Anthu awiri anapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera, wina Mfarisi ndi winayo wolandira msonkho. Mfarisiyo anayimirira ndipo anapemphera za iye mwini kuti, ‘Mulungu, ine ndikuyamika kuti sindili ngati anthu ena onse, achifwamba, ochita zoyipa, achigololo, sindilinso ngati wolandira msonkhoyu. Ine ndimasala kudya kawiri pa Sabata ndipo ndimapereka chakhumi pa zonse ndimapeza.’ “Koma wolandira msonkhoyo ali chiyimire potero, sanathe nʼkomwe kuyangʼana kumwamba; koma anadziguguda pachifuwa ndipo anati, ‘Mulungu, chitireni chifundo, ine wochimwa.’ “Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”

Khalani tcheru nthawi zonse ndi kupemphera kuti inu mudzathe kuthawa zonse zimene zili pafupi kuchitika, ndi kuti mudzathe kuyima pamaso pa Mwana wa Munthu.”

Koma Ine ndakupempherera Simoni, kuti chikhulupiriro chako chisafowoke ndipo pamene udzabwerera kwa Ine, udzalimbikitse abale ako.”

Atafika pamalopo, Iye anawawuza kuti, “Pempherani kuti musagwe mʼmayesero.” Iye anapita patsogolo pangʼono patali ngati kuponya mwala, anagwada napephera kuti, “Atate ngati mukufuna chotsereni chikho ichi. Komatu muchite zimene mukufuna osati zimene ndikufuna ine.” Mngelo wochokera kumwamba anafika namulimbikitsa. Ndipo mopsinjika mtima, anapemphera moona mtima, ndipo thukuta lake linali ngati madontho a magazi akugwera pansi. Iye atamaliza kupemphera, ndi kubwerera kwa ophunzira ake, anawapeza atagona atafowoka ndi chisoni. Iye anafunsa kuti, Nʼchifukwa chiyani mukugona? “Dzukani ndipo pempherani kuti inu musagwe mʼmayesero.”

Yesu anati, “Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita.” Ndipo anagawana malaya ake mochita maere.

pakuti dzuwa linaleka kuwala. Ndipo chinsalu cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati.

Kenaka Yesu anatenga bulediyo, atayamika anagawira iwo amene anakhala pansi, chimodzimodzinso nsombazo monga momwe iwo anafunira.

Munthu wochokera kwa Mulungu amamva zimene Mulungu amanena. Chifukwa chimene simumvera nʼchakuti, inuyo sindinu ochokera kwa Mulungu.”

Ife tikudziwa kuti Mulungu samvera wochimwa. Iye amamvera munthu woopa Mulungu amene amachita chifuniro chake.

Mlonda amamutsekulira khomo, ndipo nkhosa zimamvera mawu ake. Iye amaziyitana mayina nkhosa zakezo, nazitulutsa. Akazitulutsa nkhosa zake zonse, iye amazitsogolera, ndipo nkhosa zakezo zimamutsata chifukwa zimadziwa mawu ake.

Ine ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za gulu ili. Ine ndiyenera kuzibweretsanso. Izonso zidzamvera mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi mʼbusa mmodzi.

Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine.

Choncho iwo anachotsa mwalawo. Kenaka Yesu anayangʼana kumwamba ndikuti, “Atate, Ine ndikukuthokozani chifukwa mumandimvera. Ine ndimadziwa kuti Inu mumandimvera nthawi zonse, koma Ine ndanena izi chifukwa cha anthu amene ayima pano, kuti iwo akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.” Yesu atanena izi, Iye anayitana ndi mawu ofuwula kuti, “Lazaro, tuluka!”

Ndipo Ine ndidzachita chilichonse chimene inu mudzapempha mʼdzina langa kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu kalikonse mʼdzina langa, Ine ndidzachita. “Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga. Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse. Nkhosweyo ndiye Mzimu wachoonadi. Dziko lapansi silingalandire Nkhosweyi chifukwa samuona kapena kumudziwa. Koma inu mumamudziwa pakuti amakhala nanu ndipo adzakhala mwa inu.

Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani.

Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa.

Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa.

Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera.

Tsiku limenelo inu simudzandipemphanso kalikonse. Ine ndikukuwuzani zoona kuti Atate anga adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. Mpaka tsopano simunapemphe kalikonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.

Yesu atatha kunena izi, anayangʼana kumwamba ndipo anapemphera: “Atate, nthawi yafika. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanuyo akulemekezeni Inu. Pakuti Inu munamupatsa Iye ulamuliro pa anthu onse kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mwamupatsa. Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma. Ine ndabweretsa ulemerero wanu pa dziko pamene ndamaliza ntchito imene munandipatsa kuti ndi igwire. Ndipo tsopano, Atate, ndilemekezeni Ine pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu dziko lapansi lisanayambe. “Ine ndawadziwitsa za Inu anthu amene munandipatsa mʼdziko lapansi. Iwo anali anu. Inu munawapereka kwa Ine ndipo amvera mawu anu. Tsopano akudziwa kuti zonse zimene munandipatsa nʼzochokera kwa Inu. Pakuti Ine ndiwapatsa mawu amene Inu munandipatsa ndipo awalandira. Iwo akudziwa ndithu kuti Ine ndinachokera kwa Inu, ndipo akukhulupirira kuti Inu ndiye amene munandituma Ine. Ine ndikuwapempherera. Ine sindikupempherera dziko lapansi, koma anthu amene Inu mwandipatsa, pakuti ndi anu. Zonse zimene Ine ndili nazo ndi zanu, ndipo zonse zimene Inu muli nazo ndi zanga. Choncho Ine ndalemekezedwa mwa iwowo. Ine sindikukhalanso mʼdziko lapansi nthawi yayitali, koma iwo akanali mʼdziko lapansi. Ine ndikubwera kwa Inu. Atate Woyera, atetezeni ndi mphamvu za dzina lanu. Dzina limene munandipatsa Ine, kuti iwo akhale amodzi monga Ife tili amodzi. Pamene ndinali nawo, ndinawateteza ndi kuwasunga mosamala mʼdzina limene munandipatsa. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatayika kupatula yekhayo amene anayenera kuwonongeka kuti malemba akwaniritsidwe. “Tsopano ndikubwera kwa Inu. Ndikunena izi ndikanali mʼdziko lapansi, kuti iwo akhale ndi muyeso wodzaza wachimwemwe changa mʼkati mwawo. Ine ndawapatsa mawu anu ndipo dziko lapansi likudana nawo, pakuti sali a dziko lapansi monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko lapansi koma kuti muwateteze kwa woyipayo. Iwo si a dziko lapansi, monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi. Monga Inu munandituma Ine mʼdziko lapansi, Inenso ndikuwatuma mʼdziko lapansi. Chifukwa cha iwowa Ine ndikudziyeretsa, kuti iwo ayeretsedwenso kwenikweni. “Ine sindikupempherera iwo okhawa, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha uthenga wawo. Ndikuwapempherera kuti onsewa akhale amodzi. Monga Inu Atate muli mwa Ine ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife kuti dziko lapansi likhulupirire kuti Inu munandituma Ine. Ine ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa Ine, kuti akhale amodzi monga Ife tili amodzi. Ine ndikhale mwa iwo ndipo Inu mwa Ine kuti umodzi wawo ukhale wangwiro. Choncho dziko lapansi lidzadziwa kuti Inu munandituma Ine ndipo Inu mwawakonda iwowa monga momwe Inu munandikondera Ine. “Atate, Ine ndikufuna kuti anthu amene mwandipatsa Ine adzakhale ndi Ine kumene kuli Ine, ndi kuona ulemerero wanga, ulemerero umene munandipatsa chifukwa Inu munandikonda dziko lapansi lisanalengedwe. “Atate wolungama, ngakhale kuti dziko lapansi silikudziwani Inu, Ine ndimakudziwani, ndipo iwo amadziwa kuti Inu munandituma Ine. Ine ndawadziwitsa dzina lanu, ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzina lanulo, kuti chikondi chomwe munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”

Onsewa ndi mtima umodzi anapitiriza kupemphera pamodzi ndi amayi, ndi Mariya amayi ake a Yesu, ndiponso abale ake a Yesu.

Litafika tsiku la chikondwerero cha Pentekosite, onse anali pamodzi. Mwadzidzidzi kunamveka mkokomo kuchokera kumwamba ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo inadzaza nyumba yonse imene amakhala. Iwo anaona zinthu zokhala ngati malilime amoto ogawikana ndipo anakhala pa aliyense wa iwo. Ndipo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kuyankhula mu ziyankhulo zina, monga Mzimu Woyerayo anawayankhulitsa.

Anthu atamva zimenezi anafuwula ndi mtima umodzi napemphera kwa Mulungu. Iwo anati, “Ambuye wolamulira zonse, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndiponso zonse zili mʼmenemo.

Iwo atatha kupemphera, malo amene anasonkhanapo anagwedezeka. Ndipo iwo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo anayankhula Mawu a Mulungu molimba mtima.

Atafika anawapempherera kuti alandire Mzimu Woyera,

Komeliyo anayankha kuti, “Masiku anayi apitawo, nthawi yonga yomwe ino, 3 koloko masana ndimapemphera mʼnyumba mwanga. Mwadzidzidzi patsogolo panga panayimirira munthu wovala zovala zonyezimira. Ndipo anati, ‘Korneliyo, Mulungu wamva mapemphero ako ndipo wakumbukira mphatso zako kwa osauka.

Kotero Petro anasungidwa mʼndende, koma mpingo unamupempherera kolimba kwa Mulungu. Usiku woti mmawa mwake Herode amuzenga mlandu, Petro amagona pakati pa asilikali awiri, atamangidwa maunyolo awiri, ndiponso alonda atayima pa khomo. Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye anaonekera ndipo kuwala kunawunika mʼchipindamo. Mngeloyo anamugwedeza Petro mʼnthiti ndi kumudzutsa. Iye anati, “Fulumira, imirira!” Ndipo maunyolo anagwa kuchoka mʼmanja a Petro.

Ndipo atasala kudya ndi kupemphera anasanjika manja awo pa iwo nawatumiza.

Paulo ndi Barnaba anasankha akulu ampingo pa mpingo uliwonse, ndipo atapemphera ndi kusala kudya anawapereka kwa Ambuye amene anamukhulupirira.

Koma pakati pa usiku Paulo ndi Sila ankapemphera ndi kuyimba nyimbo zolemekeza Mulungu, ndipo akayidi ena ankamvetsera. Mwadzidzidzi kunachitika chivomerezi champhamvu kotero kuti maziko a ndende anagwedezeka. Nthawi yomweyo zitseko zonse za ndende zinatsekuka, ndipo maunyolo a aliyense anamasuka.

Pamene Paulo anawasanjika manja, Mzimu Woyera anadza pa iwo ndipo anayankhula mʼmalilime ndipo ananenera.

Atanena zimenezi, anagwada pansi pamodzi ndi ena onse, napemphera.

Ndipo tsopano ukudikira chiyani? Dzuka ndi kutama dzina la Ambuye mopemba, ubatizidwe ndi kuchotsa machimo ako.’

Paulo atanena zimenezi, anatenga buledi nayamika Mulungu pamaso pa onse. Ndipo ananyema bulediyo nayamba kudya.

Momwemonso, Mzimu amatithandiza ife mʼkufowoka kwathu. Ife sitidziwa momwe tiyenera kupempherera koma Mzimu mwini amatipempherera mobuwula ndi mawu osafotokozedwa. Koma Iye amene amasanthula mitima yathu amadziwa maganizo a Mzimu, chifukwa Mzimu amapempherera oyera mtima molingana ndi chifuniro cha Mulungu.

Abale, chokhumba cha mtima wanga ndi pemphero langa kwa Mulungu ndi chakuti Aisraeli apulumutsidwe.

Kondwerani mʼchiyembekezo, pirirani mʼmasautso ndiponso khulupirikani mʼpemphero.

Iye amene amaganiza kuti tsiku limodzi ndi lopambana, amatero kwa Ambuye. Iye amene amadya nyama, amadya mwa Ambuye pakuti amayamika Mulungu. Ndipo iye amene sadya, amatero kwa Ambuye ndi kuyamika Mulungu.

Abale, ine ndikukupemphani, mwa Ambuye athu Yesu Khristu ndi mwachikondi cha Mzimu, kuti mukhale nane pa kulimbika kwanga pondipempherera kwa Mulungu.

Pakuti aliyense amene amayankhula malilime sayankhula kwa anthu, koma kwa Mulungu. Zoonadi, palibe amene amamva zimene akunena chifukwa Mzimu ndiye amamuyankhulitsa zachinsinsi.

Iye amene amayankhula malilime amadzilimbikitsa yekha, koma amene amanenera amalimbikitsa mpingo.

Pa chifukwa ichi munthu amene amayankhula malilime apemphere kuti azitha kutanthauzira zimene akunena. Popeza ngati ndipemphera mʼmalilime, ndi mzimu wanga umene ukupemphera, koma nzeru zanga sizikupindula kanthu. Tsono pamenepa nʼkutani? Ndidzapemphera ndi mzimu wanga, komanso ndidzapemphera ndi nzeru zanga. Ndidzayimba ndi mzimu wanga, komanso ndidzayimba ndi nzeru zanga. Ngati mutamanda Mulungu mu mzimu, kodi munthu amene wapezeka pakati pa amene akuyankhula zomwe sakumva, adzavomereza bwanji kuti “Ameni” pa pemphero lanu loyamikalo popeza sakumva chimene mukunena? Mukhoza kumathokoza mokwanira, koma munthu winayo sanathandizikepo. Ndikuyamika Mulungu chifukwa ndimayankhula malilime kuposa nonsenu. Koma mu mpingo ndi kwabwino kuti ndiyankhule mawu asanu okha omveka bwino kuti ndilangize bwino ena kusiyana ndikuyankhula mawu ambirimbiri mʼmalilime.

Kotero, malilime ndi chizindikiro, osati cha kwa okhulupirira koma kwa osakhulupirira. Koma kunenera ndi chizindikiro kwa okhulupirira osati kwa osakhulupirira. Kotero kuti ngati mpingo wonse utasonkhana pamodzi ndipo aliyense namayankhula malilime, ndipo wina amene sangazindikire kapena ena osakhulupirira nabwerapo, kodi sadzanena kuti mwachita misala? Koma ngati wosakhulupirira kapena wina amene sakuzindikira abwera pamene aliyense akunenera, adzatsutsika mu mtima ndi zonse zimene akumva ndipo adzaweruzidwa ndi onse ndipo zinsinsi za mu mtima mwake zidzawululika. Kotero kuti adzadzigwetsa pansi ndi kupembedza Mulungu akufuwula kuti, “Mulungu ali pakati panudi!”

Ngati wina ayankhula malilime, awiri kapena akachulukapo atatu ndiye ayankhule mmodzimmodzi, ndipo wina ayenera kutanthauzira zimene ayankhulazo. Ngati palibe wotanthauzira, woyankhulayo akhale chete mu mpingo ndipo adziyankhulire iye mwini ndi Mulungu.

Nʼchifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse anthu kuyankhula malilime.

ine sindilekeza kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani mʼmapemphero anga. Ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate a ulemerero akupatseni mzimu wa nzeru ndi wa vumbulutso, kuti mumudziwe kwenikweni.

Pakuti mwa Iye, ife tonse titha kufika kwa Atate mwa Mzimu mmodzi.

Tsopano kwa Iye amene angathe kuchita zochuluka kuposa zimene tingapemphe, kapena kuganiza molingana ndi mphamvu zake zimene zikugwira ntchito mwa ife, Iyeyo akhale ndi ulemu mu mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibado yonse mpaka muyaya. Ameni.

Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu. Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu.

Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse.

Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira inu. Mʼmapemphero anga onse opempherera inu, nthawi zonse ndimapemphera ndi chimwemwe

Ndipo pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chipitirire kukulirakulira pa chidziwitso ndi kuzama mʼmaganizo, kuti mukhoza kuzindikira chabwino koposa zonse ndi chiti kuti muthe kukhala wopanda chodetsa ndi wopanda chilema kufikira tsiku la Khristu. Ndipo moyo wanu udzakhala odzazidwa ndi chipatso cha chilungamo chimene chimachokera mwa Yesu Khristu. Pakuti zimenezi zidzapereka ulemerero ndi matamando kwa Mulungu.

Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu. Komatu munachita bwino kundithandiza mʼmavuto anga.

Ndipo Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu monga mwa chuma chake chaulemerero mwa Khristu Yesu.

Timayamika Mulungu Atate wa Ambuye athu Yesu Khristu, nthawi zonse pamene tikukupemphererani.

Chifukwa cha ichi, kuyambira tsiku limene tinamva za inu, sitinasiye kukupemphererani ndi kumupempha Mulungu kuti akudzazeni ndi chidziwitso cha chifuniro chake kudzera mu nzeru yonse yauzimu ndi kumvetsetsa.

Pempherani modzipereka, mukhale atcheru ndiponso oyamika. Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende.

Epafra ndi mmodzi mwa inu ndiponso mtumiki wa Khristu Yesu, akupereka moni. Iyeyu nthawi zonse amakupemphererani mwamphamvu, kuti mukhazikike pa chifuniro chonse cha Mulungu, mukhale okhwima ndi otsimikiza kwathunthu.

Ife timayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu. Timakutchulani mʼmapemphero athu.

Kondwerani nthawi zonse. Pempherani kosalekeza. Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.

Abale, mutipempherere.

Potsiriza, abale, mutipempherere kuti uthenga wa Ambuye ufalikire msanga ndi kulemekezedwa monga momwe munachitira inu.

Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika. Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima.

Choncho ndikufuna kuti paliponse popemphera, amuna azikweza manja awo kwa Mulungu mopanda mkwiyo kapena kukangana.

Pakuti chilichonse chimene Mulungu analenga ndi chabwino, ndipo chilichonse chisasalidwe, akamachilandira moyamika, pakuti chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndi pemphero.

Mkazi wamasiye amene ali yekha ndi wopanda womuthandiza, ameneyo wayika chiyembekezo chake pa Mulungu, ndipo amapemphera kosalekeza usana ndi usiku kuti Mulungu azimuthandiza.

Ndikuyamika Mulungu amene ndimamutumikira ndi chikumbumtima chosatsutsika, monga momwe ankachitira makolo anga. Usiku ndi usana ndimakukumbukira mosalekeza mʼmapemphero anga.

Ine ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakukumbukira iwe mʼmapemphero anga.

Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano, Mulungu wayankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Mwanayu anamusankha kuti akhale mwini wa zinthu zonse, ndiponso Mulungu analenga dziko lonse kudzera mwa Iye.

Monga kunanenedwa kuti, “Lero ngati mumva mawu ake, musawumitse mitima yanu ngati momwe munachitira pamene munawukira.”

Nʼchifukwa chake Mulungu anayikanso tsiku lina limene analitcha “Lero.” Patapita nthawi yayitali Iye anayankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide, monga ndinanena kale kuti, “Lero mukamva mawu ake, musawumitse mitima yanu.”

Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.

Yesu, pa nthawi imene anali munthu pa dziko lapansi pano, anapereka mapemphero ake ndi zopempha mofuwula ndi misozi kwa Iye amene akanamupulumutsa ku imfa, ndipo anamumvera chifukwa anagonjera modzipereka. Ngakhale Iye anali Mwana wa Mulungu anaphunzira kumvera pomva zowawa.

Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu.

Ndipo popanda chikhulupiriro nʼkosatheka kukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene amabwera kwa Iye ayenera kukhulupirira kuti Mulungu alipodi ndi kuti Iye amapereka mphotho kwa amene akumufunitsitsa.

Tsono, tiyeni kudzera mwa Yesu tipereke nsembe zachiyamiko kwa Mulungu osalekeza, chipatso cha milomo imene imavomereza dzina lake.

Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa. Koma pamene mupempha, muyenera kukhulupirira osakayika, chifukwa amene amakayika ali ngati mafunde pa nyanja amene amawinduka nakankhika ndi mphepo.

Koma ngakhale mumapempha simulandira, chifukwa mumapempha ndi zolinga zoyipa. Mumapempha kuti muzigwiritse ntchito pa zokusangalatsani nokha.

Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira. Chitani chisoni chifukwa cha zimene mwachita, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni. Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.

Kodi alipo wina mwa inu amene ali pa mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Ayimbe nyimbo zolemekeza. Kodi alipo wina mwa inu akudwala? Ayitane akulu ampingo kuti adzamupempherere ndi kumudzoza mafuta mʼdzina la Ambuye. Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa. Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito. Eliya anali munthu ngati ife. Iye anapemphera mwamphamvu kuti mvula isagwe ndipo sinagwedi kwa zaka zitatu ndi theka. Kenaka anapempheranso, ndipo kumwamba kunagwetsa mvula, ndipo dziko lapansi linatulutsa zomera zake.

Pakuti Ambuye amayangʼanira bwino anthu olungama ndipo amatchera khutu ku mapemphero awo. Koma Ambuye sawayangʼana bwino amene amachita zoyipa.”

Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera.

Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.

Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.

Ndipo timalandira chilichonse chimene tichipempha kwa Iye, chifukwa timamvera malamulo ake ndi kuchita zimene zimamukondweretsa.

Ife timalimba mtima tikamafika pamaso pa Mulungu, popeza kuti ngati tipempha kanthu kalikonse monga mwa chifuniro chake, amatimvera. Ndipo ngati tikudziwa kuti amatimvera, chilichonse chimene timapempha, tikudziwanso kuti tili nacho chimene tamupempha Iye.

Wokondedwa, ndimakupempherera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndikuti ukhale bwino mʼthupi mwako, monga momwe ulili moyo wako wauzimu.

Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.

Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”

Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.’ ”

Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”

Chichewa - Chichewa - NY

NYCCL - Mawu A Mulungu Mu Chichewa Chalero - 2016

This Bible text is from Biblica Open God's Word In Contemporary Chichewa
https://open.bible/bibles/chichewa-biblica-text-bible/
provided by: Biblica Inc, available by Creative Commons CC-BY-SA-4.0,
and this new compilation is shared as www.creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0.
Languages are made available to you by www.ipedge.net