05 – Kumwamba

Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Kumwamba.

Mavesi atatu ofunika kwambiri

Komabe monga zalembedwa kuti, “Palibe diso linaona, palibe khutu linamva, palibe amene anaganizira, zimene Mulungu anakonzera amene amukonda”

Sipadzakhalanso temberero lililonse. Mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa udzakhala mu mzindawo, ndipo atumiki ake adzamutumikira. Iwo adzaona nkhope yake ndipo dzina lake lidzalembedwa pa mphumi zawo. Sipadzakhalanso usiku. Sadzafuna kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuwala kwawo. Ndipo adzalamulira kwamuyaya.

Ambiri mwa amene akugona mʼnthaka adzadzuka: ena adzapita ku moyo wosatha, ena ku malo amanyazi ndi chilango chosatha. Amene ali anzeru mʼnjira ya chilungamo adzawala ngati kuwala kwa mlengalenga, ndipo amene alondolera ambiri ku njira yolungama, adzawala ngati nyenyezi ku nthawi zosatha.

Mavesi onse motsatira dongosolo lolondola – 183 ndime

Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Ndipo Yehova Mulungu anameretsa mʼmundamo mitengo ya mitundu yonse. Inali mitengo yokongola ndi ya zipatso zokoma. Pakati pa munda uja panali mtengo wopatsa moyo ndi mtengo wopatsa nzeru zodziwitsa chabwino ndi choyipa.

Mʼmaloto, anaona makwerero oyimikidwa pansi ndipo anakafika kumwamba. Angelo a Mulungu amakwera ndi kutsika pa makwereropo.

Tsono anachita mantha ndipo anati, “Malo ano ndi woopsa ndithu. Zoonadi pano ndi pa nyumba ya Mulungu ndi khomo la kumwamba.”

Yehova Mulungu wanu ndiye mwini wake kumwamba ngakhale mmwambamwamba, dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo.

Yangʼanani pa dziko kuchokera kumwamba, ku malo anu wopatulika, ndi kudalitsa anthu anu Aisraeli ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi limene mwatipatsa ife monga momwe munalonjezera pa malumbiro anu kwa makolo athu.”

“Kodi Mulungu angakhaledi pa dziko lapansi? Mlengalenga ngakhale kumwamba kwenikweni, sikungakukwaneni. Nanga kuli bwanji ndi Nyumba iyi imene ndamanga!

Imvani pembedzero la mtumiki wanu ndi la anthu anu Aisraeli pamene akupemphera akuyangʼana malo ano. Imvani kumwambako, malo anu amene mumakhala; ndipo mukamva muzitikhululukira.

Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu, ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola. Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu. Wanu, Inu Yehova ndi ufumu; Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse.

Inu nokha ndiye Yehova. Munalenga kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, zolengedwa zonse zimene zili mʼmenemo. Munalenga dziko ndi zonse zokhalamo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo. Zonse mumazisunga ndi moyo ndipo zonse za kumwamba zimakupembedzani.

Yehova ali mʼNyumba yake yoyera; Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba. Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu; maso ake amawayesa.

Inu mwandidziwitsa njira ya moyo; mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu, ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja.

Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake; Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.

Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsa masiku ochuluka kwamuyaya.

kuti iye akhale ndi moyo mpaka muyaya ndi kusapita ku manda.

Magaleta a Mulungu ndi osawerengeka, ndi miyandamiyanda; Ambuye wabwera kuchokera ku Sinai, walowa mʼmalo ake opatulika.

Ine ndidzakhazikitsa zidzukulu zake mpaka muyaya, mpando wake waufumu ngati masiku a miyamba.

Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa;

Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba ndipo ufumu wake umalamulira onse.

Zili ngati mame a ku Heremoni otsikira pa Phiri la Ziyoni. Pakuti pamenepo Yehova amaperekapo dalitso, ndiwo moyo wamuyaya.

Mʼnjira yachilungamo muli moyo; koma njira ya munthu woyipa imafikitsa ku imfa.

Iye anapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthawi yake. Anayika nzeru zamuyaya mʼmitima ya anthu; komabe anthuwo sangathe kuzindikira zomwe Mulungu wachita kuyambira pa chiyambi mpaka chimaliziro.

Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova. Pamwamba pawo panayimirira Aserafi, aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: awiri anaphimba nkhope zawo, awiri anaphimba mapazi awo, ndipo awiri ankawulukira. Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti “Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse. Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”

Ulamuliro ndi mtendere wake zidzakhala zopanda malire. Iye adzalamulira ufumu wake ali pa mpando waufumu wa Davide, ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikiza mwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamo kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya. Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza kuchita zimenezi.

Mʼmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa, kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwana wambuzi, mwana wangʼombe ndi mwana wa mkango adzadyera limodzi ndipo mwana wamngʼono adzaziweta.

Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya, Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmaso mwa munthu aliyense; adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi, Yehova wayankhula.

Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.

Sipadzakhala dzuwa kuti likuwunikire, kapena mwezi kuti uwunikire usiku, pakuti Yehova ndiye adzakhale kuwunika kwako kwa muyaya, ndipo Mulungu wako adzakhala ulemerero wako. Dzuwa lako silidzalowanso, ndipo mwezi wako sudzazimiriranso; Yehova adzakhala kuwunika kwako kwamuyaya, ndipo masiku a mavuto ako adzatha. Ndipo anthu ako onse adzakhala olungama ndipo dzikolo lidzakhala lawo mpaka muyaya. Iwo ndi mphukira imene Ine ndayidzala, ntchito ya manja anga, kuti aonetse ulemerero wanga.

“Taonani, ndikulenga mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukika, zidzayiwalika kotheratu.

Yehova akuti, “Kumwamba ndi mpando wanga waufumu ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga. Tsono nyumba ili kuti yomwe mundimangire, ndipo malo ali kuti amene inu mungandikonzere kuti ndizipumuliramo?

“Monga momwe mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ndidzapanga zidzakhala mpaka muyaya pamaso panga, ndi chonchonso dzina lanu ndi zidzukulu zanu zidzakhalire.” Akutero Yehova.

Yehova akuti, “Ndidzataya fuko la Israeli chifukwa cha machimo awo. Ngati patapezeka munthu amene angathe kupima zakuthambo nʼkufufuza maziko a dziko lapansi.”

Pamwamba pa thambo la pa mitu yake panali chinthu chimene chimaoneka ngati mpando waufumu wopangidwa ndi mwala wa safiro, ndipo pamwamba pa mpando waufumuwo panali chinthu chooneka ngati munthu. Ndinaona kuti mmwamba mwa chiwuno chake munali ngati chitsulo chowala konsekonse ngati moto. Mʼmunsi mwa chiwuno chake munalinso ngati moto wokhawokha. Kuwala kwa mphamvu kunamuzungulira munthuyo. Kuwalako kunali ndi maonekedwe a utawaleza mʼmitambo tsiku limene kwagwa mvula. Umu ndi mmene ulemerero wa Yehova umaonekera. Pamene ndinawuona ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akundiyankhula.

Mʼmbali zonse za mtsinje mudzamera mitengo ya zipatso zakudya za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota kapena kulephera kubereka zipatso. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake adzakhala ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya ndipo masamba ake azidzachitira mankhwala.”

“Pa nthawi ya mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa, kapenanso kuperekedwa kwa anthu ena. Udzawononga maufumu onse aja ndi kuwatheratu, koma iwo wokha udzakhalapobe mpaka muyaya.

“Ndikuyangʼanabe zinthu mʼmasomphenya usiku, ndinaona wina ngati mwana wa munthu, akubwera ndi mitambo ya kumwamba. Anayandikira Mkulu Wachikhalire uja. Ena anamuperekeza kwa Iye. Anapatsidwa ulamuliro, ulemerero ndi mphamvu za ufumu kuti anthu a mitundu ina yonse, mayiko ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana apembedze iye. Mphamvu zake ndi mphamvu zamuyaya zimene sizidzatha, ndipo ufumu wake sudzawonongeka konse.

Koma oyera mtima a Wammwambamwamba adzalandira ufumu ndipo udzakhala nawo mpaka muyaya, inde ku nthawi zonse.’

Kenaka ulamuliro, mphamvu ndi ukulu wa maufumu pa dziko lonse lapansi zidzaperekedwa kwa oyera mtima, a Wammwambamwamba. Ufumu wawo udzakhala ufumu wosatha, ndipo olamulira onse adzawalamulira ndi kuwamvera.’ ”

Ambiri mwa amene akugona mʼnthaka adzadzuka: ena adzapita ku moyo wosatha, ena ku malo amanyazi ndi chilango chosatha. Amene ali anzeru mʼnjira ya chilungamo adzawala ngati kuwala kwa mlengalenga, ndipo amene alondolera ambiri ku njira yolungama, adzawala ngati nyenyezi ku nthawi zosatha.

kuti, “Tembenukani mtima chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.”

Mʼdzanja lake muli chopetera ndipo adzayeretsa popunthirapo pake nadzathira tirigu wake mʼnkhokwe ndi kutentha zotsalira zonse ndi moto wosazima.”

Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, “Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira.”

“Odala ndi amene ali osauka mu mzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.

Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.” “Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine. Sangalalani, kondwerani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba, chifukwa moterenso ndi mmene anazunzira aneneri inu musanabadwe.

Chifukwa chake aliyense amene aphwanya limodzi la malamulowa ngakhale lalingʼonongʼono ndi kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, adzakhala wotsirizira mu ufumu wakumwamba, koma aliyense amene achita ndi kuphunzitsa malamulo awa adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba. Chifukwa chake ndikuwuzani kuti ngati chilungamo chanu sichiposa cha Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, zoonadi, simudzalowa mu ufumu wakumwamba.

“Chifukwa chake pempherani motere: “ ‘Atate athu akumwamba, dzina lanu lilemekezedwe, Ufumu wanu ubwere, chifuniro chanu chichitike pansi pano monga kumwamba.

Ndipo musatitengere kokatiyesa; koma mutipulumutse kwa woyipayo.’

“Musadziwunjikire chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga ndi pamene mbala zimathyola ndi kuba. Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba. Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko.

“Lowani pa chipata chopapatiza. Pakuti chipata cholowera kuchiwonongeko nʼchachikulu ndipo msewu wake ndi waukulunso. Ndipo anthu ambiri amalowera pamenepo. Koma chipata ndi chopapatiza ndi msewu ndi waungʼono umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene ayipeza njirayo.

“Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba.

Pamene mukupita, muzikalalikira uthenga uwu: ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’

Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pakati pa obadwa ndi mkazi sipanaoneke wina aliyense wamkulu woposa Yohane Mʼbatizi; komatu amene ndi wamngʼono kwambiri mu ufumu wakumwamba ndi wamkulu koposa iye.

Ophunzira anabwera kwa Iye ndikumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani Inu mukuyankhula kwa anthu mʼmafanizo?” Iye anayankha kuti, “Nzeru zakudziwa zinsinsi za ufumu wakumwamba zapatsidwa kwa inu koma osati kwa iwo.

Iye anawawuza fanizo lina kuti, “Ufumu wakumwamba uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. Ngakhale mbewuyi ndi yayingʼono mwa mbewu zanu zonse za mʼmunda, imakula ndi kukhala mtengo kotero kuti mbalame zamlengalenga zimabwera ndi kupumula mʼnthambi zake.”

Pamenepo olungama adzawala ngati dzuwa mu ufumu wa Atate awo. Amene ali ndi makutu amve.”

“Ufumu wakumwamba ufanana ndi chuma chobisika mʼmunda. Munthu atachipeza anachibisanso ndipo ndi chimwemwe anapita nakagulitsa zonse anali nazo, nakagula mundawo.

“Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi wogulitsa malonda amene amafuna ngale zabwino. Atapeza imodzi ya mtengowapatali, iye anapita nakagulitsa chilichonse anali nacho ndi kukayigula.”

“Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi khoka limene linaponyedwa mʼnyanja ndipo linakola mitundu yonse ya nsomba. Litadzaza, asodzi analikokera ku mtunda. Pomwepo anakhala pansi nasonkhanitsa nsomba zabwino mʼmadengu koma zoyipa anazitaya. Umu ndi mmene kudzakhalira pakutha kwa dziko. Angelo adzabwera ndi kulekanitsa oyipa ndi olungama.

Iye anawawuza kuti, “Chifukwa chake mphunzitsi aliyense wa malamulo amene walangizidwa za ufumu wakumwamba ali ngati mwini nyumba amene amatulutsa chuma chatsopano komanso chakale.”

Ndipo anamupempha alole kuti akhudze mphonje ya mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachiritsidwa.

Ine ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, ndipo chilichonse chimene iwe udzachimanga pansi pano chidzamangidwanso kumwamba.”

Ndipo Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba.

“Onetsetsani kuti musanyoze mmodzi wa anawa. Pakuti ndikuwuzani kuti angelo awo kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga akumwamba nthawi zonse.”

“Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti chilichonse chimene muchimanga pa dziko lapansi, chidzamangidwanso kumwamba, ndipo chilichonse chimene muchimasula pa dziko chidzamasulidwanso kumwamba.

Yesu anati, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa.”

Taonani mnyamata wina anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, ndi chinthu chiti chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndipeze moyo wosatha?” Yesu anayankha kuti, “Ukundifunsiranji Ine za chinthu chimene ndi chabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino. Ngati ukufuna kulowa mʼmoyo wosatha mvera malamulo.” Mnyamatayo anamufunsa kuti, “Ndi ati?” Yesu anayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni onama, lemekeza abambo ako ndi amayi ako ndipo konda mnansi wako monga iwe mwini.” Mnyamatayo anati, “Zonsezi ndimazisunga, nanga chatsala ndi chiyani?” Yesu anayankha kuti, “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndi kupereka kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ukakachita zimenezi, ukabwere udzanditsate Ine.” Mnyamatayo atamva zimenezi, anachoka mokhumudwa, chifukwa anali ndi chuma chambiri.

Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti nʼkovuta kuti olemera akalowe mu ufumu wakumwamba. Komanso ndikuwuzani kuti, nʼkwapafupi kuti ngamira idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi kuti wolemera akalowe mu ufumu wa Mulungu.”

Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti pa nthawi yokonzanso zinthu zonse, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake waufumu mu ulemerero wake kumwamba, inu amene mwanditsata Ine mudzakhalanso pa mipando khumi ndi iwiri yaufumu, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli. Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena bambo kapena mayi kapena mkazi, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine adzalandira madalitso ochuluka ndi kulandiranso moyo wosatha.

“Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonzera phwando mwana wake wamwamuna. Anatumiza antchito ake kwa amene anayitanidwa kuphwando koma anakana kubwera.

Anthu akadzaukitsidwa, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. Koma za kuukitsidwa kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo?’ Iyeyo si Mulungu wa akufa koma wa amoyo.”

“Pa nthawi imeneyo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka mlengalenga, ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalira. Idzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu.

Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”

“Nthawi imeneyo ufumu wakumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi amene anatenga nyale zawo napita kukakumana ndi mkwati. Asanu anali opusa ndipo asanu ena anali ochenjera. Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta; koma ochenjerawo anatenga mafuta awo mʼmabotolo pamodzi ndi nyale zawo.

“Ambuye ake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika iwe! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika iwe kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’

“Pamenepo mfumu idzati kwa a ku dzanja lamanja, ‘Bwerani inu odalitsika ndi Atate anga; landirani ufumu umene unakonzedwa chifukwa cha inu kuyambira pachiyambi cha dziko.

“Amenewa adzapita ku chilango chosatha pamene olungama ku moyo wosatha.”

Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine.

Pamene Yesu anaona zimenezi anayipidwa. Anati kwa iwo, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse, pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa onga awa. Ndikukuwuzani choonadi, aliyense amene sadzalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana sadzalowamo.”

Yesu atanyamuka, munthu wina anamuthamangira nagwa mogwada pamaso pake. Iye anafunsa kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?” Yesu anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula wabwino? Palibe wabwino koma Mulungu yekha. Iwe umadziwa malamulo: ‘Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni wonama, usachite chinyengo, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ” Iye anati, “Aphunzitsi zonsezi ndinazisunga kuyambira ndili mnyamata.” Yesu anamuyangʼana ndi kumukonda nati, “Ukusowa chinthu chimodzi. Pita, kagulitse zonse zimene uli nazo ndipo kapereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ndipo ukabwere ndi kunditsata Ine.” Pa chifukwa ichi nkhope yake inagwa. Anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi chuma chambiri.

Pamene akufa auka, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. Tsopano kunena zakuti akufa amauka, kodi simunawerenge mʼbuku la Mose, pa nkhani yachitsamba choyaka moto, mmene Mulungu anati kwa iye, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?’

Akuyangʼana ophunzira ake, Iye anati, “Odala ndinu amene ndi osauka, chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu. Inu amene mukumva njala tsopano, ndinu odala chifukwa mudzakhutitsidwa. Inu amene mukulira tsopano, ndinu odala chifukwa mudzasekerera. Ndinu odala, anthu akamakudani, kukusalani ndi kukunyozani ndi kumayipitsa dzina lanu chifukwa cha Mwana wa Munthu. “Nthawi imeneyo sangalalani ndipo lumphani ndi chimwemwe chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba. Pakuti ndi zomwezonso zimene makolo awo anachitira aneneri.

Iye anati, “Kudziwa zinsinsi za ufumu wa Mulungu kwapatsidwa kwa inu, koma kwa ena ndimawayankhula mʼmafanizo kuti, “ngakhale akuona, asapenye; ngakhale akumva, asazindikire.”

Komabe musakondwere chifukwa mizimu yoyipa inakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina anu analembedwa kumwamba.”

Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, “Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?” Yesu anayankha kuti, “Mwalembedwa chiyani mʼMalamulo, ndipo iwe umawerenga zotani?” Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.” Yesu anayankha kuti, “Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo.”

Koma funafunani ufumu wake, ndipo mudzapatsidwa zonsezi. “Musachite mantha, inu kagulu kankhosa, pakuti zinakondweretsa Atate anu kuti akupatseni ufumu. Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupereke kwa osauka. Dzipezereni zikwama zandalama zimene sizidzatha, ndi kudzikundikira chuma chomwe sichidzatha kumwamba, kumene mbala sizingafikeko, ndipo dzimbiri silingawononge. Popeza kumene kuli chuma chanu, mtima wanunso udzakhala komweko.”

Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale.”

“Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo. Ndipo kuwonjezera pa zonsezi, pakati pa inu ndi ife pali chiphompho chachikulu chimene chinayikidwa, kotero kuti amene akufuna kubwera kumeneko sangathe, kapena palibe amene angawoloke kuchokera kumeneko kudzafika kuno.’

Koma Yesu anayitana anawo kuti abwere kwa Iye nati, “Lolani ana abwere kwa Ine ndipo musawatsekereze, pakuti ufumu wa Mulungu uli wa anthu otere. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene salandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamngʼono, sadzalowamo.”

Oweruza wina wake anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?” Yesu anamuyankha kuti, “Chifukwa chiyani ukunditcha wabwino, palibe wabwino kupatula Mulungu yekha. Iwe umadziwa malamulo: ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usapereke umboni wonama, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ” Iye anati, “Zonsezi ndinasunga kuyambira ndili mnyamata.” Yesu atamva izi, anati kwa iye, “Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine.” Atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri chifukwa anali munthu wachuma chambiri. Yesu anamuyangʼana nati, “Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu! Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.” Amene anamva izi anafunsa kuti, “Nanga ndani amene angapulumuke?” Yesu anayankha kuti, “Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”

Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.”

Kenaka anati, “Yesu, mundikumbukire ine pamene mulowa mu ufumu wanu.” Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti lero lino udzakhala ndi Ine mʼparadaiso.”

Ndipo Iye anapitirira kuti, “Zoonadi, Ine ndikuwuza kuti iwe udzaona kumwamba, kutatsekuka ndi angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pa Mwana wa Munthu.”

Poyankha Yesu ananena kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu.” Nekodimo anati, “Kodi munthu angabadwenso bwanji atakalamba? Kodi angalowe kachiwiri mʼmimba ya amayi ake kuti abadwenso?” Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu. Thupi limabereka thupi, koma Mzimu amabereka mzimu.

Ine ndikuyankhula kwa iwe zinthu za dziko lapansi ndipo sukukhulupirira. Nanga kodi udzakhulupirira bwanji ngati nditayankhula zinthu zakumwamba? Palibe wina aliyense anapita kumwamba, koma yekhayo amene watsika kuchokera kumwamba, Mwana wa Munthu. Tsono monga Mose anapachika njoka mʼchipululu, moteronso Mwana wa Munthu ayenera kupachikidwa, kuti aliyense amene akhulupirira Iye akhale ndi moyo wosatha. “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.

Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.”

koma aliyense amene adzamwa madzi amene Ine ndidzamupatsa sadzamvanso ludzu. Ndithudi, madzi amene ndidzamupatsa adzakhala kasupe wamadzi wotumphukira ku moyo wosatha.”

“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo.

“Musadabwe ndi zimenezi. Pakuti nthawi ikubwera pamene onse amene ali mʼmanda adzamva mawu ake ndi kutuluka. Iwo amene anachita zabwino adzauka ndi kupita ku moyo wosatha ndipo amene anachita zoyipa adzauka ndi kupita ku chilango chamuyaya.

Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni.

Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.”

Pakuti chifuniro cha Atate anga ndi chakuti aliyense amene aona Mwanayo namukhulupirira akhale ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.”

Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Iye amene akhulupirira ali nawo moyo wosatha.

Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo.”

Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga ali ndi moyo wosatha ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.

Simoni Petro anamuyankha Iye kuti, “Ambuye, ife tidzapita kwa yani? Inu muli ndi mawu amoyo wosatha.

Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa.

Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo. Aliyense amene ali ndi moyo ndi kukhulupirira Ine sadzamwalira. Kodi iwe ukukhulupirira izi?” Marita anamuwuza Iye kuti, “Inde Ambuye, ine ndikukhulupirira kuti ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene abwera mʼdziko lapansi.”

Munthu amene amakonda moyo wake adzawutaya, pamene munthu amene amadana ndi moyo wake mʼdziko lino lapansi adzawusungira ku moyo wosatha.

Mʼnyumba mwa Atate anga muli zipinda zambiri. Kukanakhala kuti mulibemo ndikanakuwuzani. Ine ndikupita kumeneko kukakukonzerani malo. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti kumene kuli Ineko, inunso mukakhale komweko.

Yesu atatha kunena izi, anayangʼana kumwamba ndipo anapemphera: “Atate, nthawi yafika. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanuyo akulemekezeni Inu. Pakuti Inu munamupatsa Iye ulamuliro pa anthu onse kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mwamupatsa. Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma.

Yesu anati, “Ufumu wanga si wa dziko lapansi lino. Ukanakhala wa pansi pano, antchito anga akanachita nkhondo kulepheretsa Ayuda kundigwira. Koma tsopano ufumu wanga ndi wochokera kumalo ena.”

“ ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu, ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Kodi mudzandimangira nyumba yotani? Akutero Ambuye. Kapena malo opumuliramo Ine ali kuti?

Anthu a mitundu ina atamva izi, anakondwa ndipo analemekeza Mawu Ambuye; ndipo onse amene anawasankha kuti alandire moyo osatha anakhulupirira.

Kumeneko analimbikitsa mitima ya ophunzira ndi kuwapatsa mphamvu kuti akhalebe woona mʼchikhulupiriro. Iwo anati, “Ife tiyenera kudutsa mʼmasautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.”

Molimba mtima ndi popanda womuletsa, Paulo analalikira za ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu.

Iye adzapereka moyo wosatha kwa amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pochita ntchito zabwino mopirira.

Choncho monga momwe tchimo linkalamulira anthu ndi kubweretsa imfa pa iwo, chomwecho kunali koyenera kuti chisomo chilamulire pobweretsa chilungamo kwa anthu, ndi kuwafikitsa ku moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha. Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”

Komabe monga zalembedwa kuti, “Palibe diso linaona, palibe khutu linamva, palibe amene anaganizira, zimene Mulungu anakonzera amene amukonda”

Zidzaterenso pamene akufa adzauka. Thupi loyikidwa mʼnthaka ngati mbewu limavunda, koma likadzauka lidzakhala losavunda. Limayikidwa mʼmanda mopanda ulemu, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi ulemerero. Limayikidwa mʼmanda lili lofowoka, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi mphamvu. Limayikidwa mʼmanda thupi la mnofu chabe, koma likadzaukitsidwa lidzakhala lauzimu. Ngati pali thupi la mnofu, palinso thupi lauzimu. Kwalembedwa kuti, “Munthu woyamba Adamu anakhala wamoyo,” Adamu wotsiriza anakhala wopatsa moyo. Zauzimu sizinabwere koyambirira, koma zachilengedwe, pambuyo pake zauzimu. Munthu woyamba anali wa dziko lapansi, wochokera mʼnthaka koma munthu wachiwiri anali wochokera kumwamba. Monga analili munthu wa dziko lapansi, momwemonso anthu onse amene ndi a dziko lapansi. Ndipo monga alili munthu wakumwamba, momwemonso anthu onse amene ndi akumwamba. Ndipo monga momwe tinabadwa ofanana ndi munthu wa dziko lapansi uja, momwemonso tidzakhala ofanana ndi munthu wakumwamba.

Ndikunenetsa, abale, kuti thupi ndi magazi sizingathe kulowa mu ufumu wa Mulungu, ndipo zimene zimavunda sizingathe kulowa kumene zinthu sizivunda. Tamverani, ndikuwuzeni chinsinsi. Tonse sitidzagona tulo, koma tonse tidzasandulika. Zidzachitika mwadzidzidzi, mʼkamphindi kochepa, monga ngati kuphethira kwa diso, pa lipenga lotsiriza. Pakuti lipenga lidzalira, akufa adzaukitsidwa opanda chovunda, ndipo ife tidzasandulika. Pakuti chovunda chiyenera kuvala chosavunda, ndi thupi ili lakufa liyenera kuvala losafa. Pamene thupi lovundali likadzasanduka losavunda, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzakwaniritsidwa zimene zinalembedwa zakuti, “Imfa yogonjetsedwa kwathunthu.” “Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?” Ululu wa imfa ndi tchimo, ndipo mphamvu ya tchimo ndi lamulo.

Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri. Motero sitiyangʼana zinthu zimene ndi zooneka ndi maso, koma zinthu zimene ndi zosaoneka. Pakuti zimene zimaoneka ndi zosakhalitsa, koma zimene sizioneka ndi zamuyaya.

Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu. Pakali pano tibuwula, ndi kulakalaka kuvala nyumba yathu ya kumwambayo,

Inde, ife tikulimba mtima, ndipo tikanakonda kulekana nalo thupi lathu ndi kukhala ndi Ambuye.

Ndikudziwa munthu mwa Khristu amene zaka khumi ndi zinayi zapitazo anatengedwa kupita kumwamba kwachitatu. Sindikudziwa ngati zinachitika ali mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu. Ndipo ndikumudziwa munthu ameneyu. Sindikudziwa ngati zinachitika mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu. Munthuyu anatengedwa kupita ku paradizo. Ndipo anamva zinthu zosatheka kuneneka, zinthu zimene munthu saloledwa kunena.

Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa. Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha.

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, amene anatipatsa madalitso onse a uzimu kumwamba mwa Khristu.

Kotero kuti, inu sindinunso alendo ndi adani, koma nzika pamodzi ndi anthu a Mulungu ndiponso a mʼbanja la Mulungu.

Pakuti kwa ine kukhala moyo ndi Khristu ndipo kufa ndi phindu. Ngati nditi ndipitirire kukhala ndi moyo mʼthupi ndiye kuti kwa ine ndi kugwira ntchito yopindulitsa. Kodi ndisankhe chiyani? Sindikudziwa. Ndathinidwa ndi zinthu ziwirizi: Ndikulakalaka kunyamuka kuti ndikakhale ndi Khristu, chimene ndi chinthu chabwino kwambiri.

Koma ife ndife nzika za kumwamba ndipo tikudikirira mwachidwi Mpulumutsi wochokera kumeneko, Ambuye Yesu Khristu. Iyeyo, ndi mphamvu imene imamuthandiza kukhazikitsa zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, adzasintha matupi athu achabewa kuti akhale ofanana ndi thupi lake la ulemerero.

Pakuti Iye anatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima ndi kutibweretsa mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa.

Muzifunafuna zinthu za kumwamba, osati zinthu za pa dziko lapansi.

kulimbikitsa, kutonthoza ndi kukupemphani kuti mukhale moyo oyenera Mulungu amene anakuyitanani kuti mulowe mu ufumu wake ndi ulemerero.

ndikukupatsani mpumulo amene mukusautsidwa, pamodzi ndi ifenso. Izi zidzachitika Ambuye Yesu akadzaoneka mʼmalawi amoto kuchokera kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu.

Ndipo pa chifukwa chimenechi, Mulungu anandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwitsitsa, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse kuti ndikhale chitsanzo cha omwe angathe kumukhulupirira ndi kulandira moyo wosatha. Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni.

Pakuti kulimbitsa thupi kumapindulitsapo pangʼono, koma moyo woopa Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo umene ukubwerawo.

Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi.

Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuyitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa mboni zambiri.

Uwalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, owolowamanja ndi okonda kugawana zinthu zawo ndi anzawo. Potero adzadziwunjikira chuma chokhalitsa ngati maziko okhazikika a nthawi zakutsogolo, kuti akalandire moyo, umene ndi moyo weniweni.

Koma tsopano Mulungu watiwululira kudzera mʼkuoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu, amene anathetsa mphamvu za imfa ndipo mwa Uthenga Wabwino anaonetsa poyera moyo umene sungafe.

Ambuye adzandilanditsa ku chilichonse chofuna kundichita choyipa ndipo adzandisamalira bwino mpaka kundilowetsa chonse mu ufumu wake wakumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya.

ndi kuwapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu amene sanama, analonjeza nthawi isanayambe.

kuti titalungamitsidwa mwachisomo chake, tikhale olowamʼmalo okhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.

Koma za Mwana wake akuti, “Inu Mulungu, mpando wanu waufumu udzakhala mpaka muyaya, ndipo mudzaweruza molungama mu ufumu wanu.

Kotero tsono kwatsala mpumulo wa Sabata kwa anthu a Mulungu;

Atasanduka wangwiro kotheratu, anakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye.

Tsono panafunika kuti zinthu zingofanizira zenizeni za kumwamba, ziyeretsedwe ndi nsembe zimenezi, koma zinthu za kumwamba zenizenizo kuti ziyeretsedwe panafunika nsembe zina zoposa zimenezo. Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.

Mʼmalo mwake, iwo amafunitsitsa dziko labwino, ndilo lakumwamba. Nʼchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wawo, pakuti Iye anawalonjeza mudzi.

Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ku mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba. Mwafika mu msonkhano wa angelo osangalala osawerengeka. Mwafika mu mpingo wa ana oyamba kubadwa, amene mayina awo analembedwa kumwamba. Inu mwafika kwa Mulungu, woweruza anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama ndi osandutsidwa kukhala angwiro.

Pakuti ife tilibe mzinda wokhazikika koma tikudikira mzinda umene ukubwera.

kuti tidzalandire chuma chomwe sichingawonongeke, kuyipitsidwa kapena kufota. Chuma chimenechi akukusungirani kumwamba.

amene anapita kumwamba ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu komwe angelo ndi maulamuliro ndi amphamvu amamvera Iye.

Nʼchifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi, simudzagwa konse. Mudzalandiridwa bwino kwambiri mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.

Koma ife tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene Mulungu analonjeza, mʼmene chilungamo chidzakhalamo.

Tikukulalikirani za Mawu a moyo amene analipo kuyambira pachiyambi, amene tinawamva, amene tinawaona ndi maso athu, amene tinawapenyetsetsa, ndipo tinawakhudza ndi manja athu. Moyowo unaoneka, tinawuona ndipo tikuchitira umboni. Tikukulalikirani za moyo wosatha umene unali ndi Atate ndipo unaonekera kwa ife.

Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya.

Ndipo chimene anatilonjeza nʼchimenechi: moyo wosatha.

Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili.

Ndipo umboniwo ndi uwu: Mulungu anatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowu uli mwa Mwana wake. Iye amene ali ndi Mwana ali ndi moyo, amene alibe Mwana wa Mulungu alibe moyo. Ine ndikulemba zimenezi kwa inu, amene mwakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha.

Tikudziwa kuti Mwana wa Mulungu anafika ndipo anatipatsa nzeru, kuti timudziwe Iye amene ali woona. Ndipo ife tili mwa Iye amene ndi woona, Mwana wake, Yesu Khristu. Iye ndi Mulungu woona ndi moyo wosatha.

Khalani mʼchikondi cha Mulungu pamene mukudikira chifundo cha Ambuye athu Yesu Khristu kuti akubweretsereni moyo wosatha.

Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wakudya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku paradizo wa Mulungu.

Amene adzapambane adzavala zoyera ngati ena aja. Sindidzafafaniza dzina lake mʼbuku lamoyo, koma ndidzamuchitira umboni pamaso pa Atate anga ndi angelo ake.

Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambana ndi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu.

Kenaka, nditayangʼana patsogolo panga ndinaona khomo lotsekuka la kumwamba. Ndipo liwu lija ndinalimva poyamba lokhala ngati lipenga linati, “Bwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene zichitike zikatha izi.” Nthawi yomweyo ndinatengedwa ndi Mzimu Woyera, ndipo patsogolo panga ndinaona mpando waufumu wina atakhalapo. Ndipo amene anakhalapoyo anali wa maonekedwe ngati miyala ya jasipa ndi sardiyo. Utawaleza wooneka ngati simaragido unazinga mpando waufumuwo. Kuzungulira mpando waufumuwu panalinso mipando ina yaufumu yokwana 24 ndipo panakhala akuluakulu 24 atavala zoyera ndipo anavala zipewa zaufumu zagolide pamutu.

Kumpando waufumuwo kunkatuluka mphenzi, phokoso ndi mabingu. Patsogolo pake pa mpando waufumuwo panali nyale zisanu ndi ziwiri zoyaka. Iyi ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu. Patsogolo pa mpando waufumu pomwepo panalinso ngati nyanja yagalasi yonyezimira ngati mwala wa krustalo. Pakatinʼpakati, kuzungulira mpando waufumuwo panali zamoyo zinayi zokhala ndi maso ponseponse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe. Chamoyo choyamba chinali ngati mkango, chachiwiri chinali ngati mwana wangʼombe, chachitatu chinali ndi nkhope ngati munthu, chachinayi chinali ngati chiwombankhanga chowuluka. Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo chinali ndi maso ponseponse ndi mʼkati mwa mapiko momwe. Usana ndi usiku zimanena mosalekeza kuti, “Woyera, woyera, woyera ndi Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, amene munali, amene muli ndi amene mukubwera.”

Nthawi zonse zamoyozo zimapereka ulemerero, ulemu ndi mayamiko kwa uja wokhala pa mpando waufumu, amene ali ndi moyo wamuyaya. Izi zikamachitika akuluakulu 24 aja amadzigwetsa pansi pamaso pa wokhala pa mpando waufumuyo, namupembedza wokhala ndi moyo wamuyayayo. Iwo amaponya pansi zipewa zawo zaufumu patsogolo pa mpando waufumu nati: “Ndinu woyeneradi kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu, Ambuye ndi Mulungu wathu, pakuti munalenga zinthu zonse, ndipo mwakufuna kwanu zinalengedwa monga zilili.”

Inu munawasandutsa kukhala mtundu waufumu ndi ansembe otumikira Mulungu, ndipo adzalamulira dziko lapansi.” Kenaka nditayangʼananso ndinamva mawu a angelo ambiri, miyandamiyanda kuchulukitsa ndi miyandamiyanda. Anazungulira mpando waufumu pamodzi ndi zamoyo zija ndi akuluakulu aja.

Zitatha izi ndinayangʼana patsogolo panga ndipo ndinaona gulu lalikulu la anthu loti munthu sangathe kuliwerenga lochokera dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu wa anthu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse, atayima patsogolo pa mpando waufumu, pamaso pa Mwana Wankhosa. Iwo anali atavala mikanjo yoyera ndi kunyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo. Ndipo ankafuwula mokweza kuti: “Chipulumutso chimachokera kwa Mulungu wathu, wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa.” “Angelo onse anayimirira kuzungulira mpando waufumu uja, kuzunguliranso akuluakulu aja ndi zamoyo zinayi zija. Angelo aja anadzigwetsa pansi chafufumimba patsogolo pa mpando waufumu napembedza Mulungu. Iwo anati, “Ameni! Matamando ndi ulemerero, nzeru, mayamiko, ulemu, ulamuliro ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kunthawi zanthawi, Ameni!”

Nʼchifukwa chake, “iwowa ali patsogolo pa mpando waufumu wa Mulungu ndipo akutumikira usana ndi usiku mʼNyumba ya Mulungu; ndipo Iye wokhala pa mpando waufumu adzawaphimba ndi tenti yake. ‘Iwowa sadzamvanso njala, sadzamvanso ludzu, dzuwa kapena kutentha kulikonse sikudzawawotcha.’ Pakuti Mwana Wankhosa amene ali pakati pa mpando waufumu adzakhala mʼbusa wawo. ‘Iye adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.’ ‘Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.’ ”

Pamenepo anatsekula Nyumba ya Mulungu kumwamba ndipo mʼkati mwake munaoneka Bokosi la Chipangano. Kenaka kunachita mphenzi, phokoso, mabingu, chivomerezi ndipo kunachita mkuntho wamatalala akuluakulu.

Zitatero, kumwamba kunayambika nkhondo. Mikayeli ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho ndi angelo ake anabwezeranso. Koma analibe mphamvu ndipo anagonjetsedwa nathamangitsidwa kumwambako.

Kenaka mngelo anandiwuza kuti, “Lemba kuti, Odala amene ayitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwana Wankhosa.” Ndipo anatinso, “Awa ndiwo mawu woona a Mulungu.”

Kenaka ndinaona Mpando Waufumu waukulu woyera ndi Iye amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake ndipo panalibenso malo awo.

Kenaka ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano pakuti kumwamba koyamba ndi dziko lapansi loyamba zinapita ndipo kunalibenso nyanja ina iliyonse. Ndinaona mzinda wopatulika, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wovala zokongola kukonzekera mwamuna wake. Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, “Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo. ‘Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ ”

Amene anakhala pa mpando waufumuyo anati, “Ndikulenga zinthu zonse zikhale zatsopano!” Ndipo anati, “Lemba izi, pakuti mawu awa ndi okhulupirika ndi woona.” Iye anandiwuza kuti, “Kwatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa onse akumva ludzu, ndidzawapatsa zakumwa zaulere zochokera ku kasupe wamadzi amoyo. Iye amene adzapambane adzalandira zonsezi, ndipo ndidzakhala Mulungu wake ndi Iye adzakhala mwana wanga. Koma amantha, osakhulupirira, okonda zonyansa, opha anthu, achiwerewere, amatsenga, opembedza mafano ndi abodza, malo awo adzakhala nyanja yamoto ya sulufule wotentha. Iyi ndi imfa yachiwiri.” Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja, anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri zodzaza ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri anandiwuza kuti, “Bwera, ine ndidzakuonetsa mkwatibwi wa Mwana Wankhosa.”

Ndipo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku phiri lalikulu ndi lalitali nandionetsa mzinda wopatulika, Yerusalemu ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu. Unawala ndi ulemerero wa Mulungu, ndipo kuthwanima kwake kunali ngati mwala wamtengowapatali, ngati jasipa; woyera ngati krustalo. Mzindawo unali ndi mpanda waukulu ndi wautali, unali ndi zipata khumi ndi ziwiri, ndipo panali angelo khumi ndi awiri. Pa chipata chilichonse panayima mngelo. Pa chipata chilichonse panalembedwa dzina la fuko la Israeli. Kummawa kunali zipata zitatu, kumpoto zitatu, kummwera zitatu ndi kumadzulo zitatu. Mpanda wa mzindawu unali ndi maziko khumi ndi awiri ndipo pa mazikopo panali mayina khumi ndi awiri a atumwi a Mwana Wankhosa.

Mngelo amene ankayankhula nane uja anali ndi ndodo yagolide yoyezera mzindawo, zipata zake ndi mpanda wake. Mzindawo unamangidwa mofanana kutalika kwake, mulitali ndi mulifupi munali mofanana. Anayeza mzindawo ndi ndodo ija ndipo anapeza kuti mulitali, mulifupi ndi msinkhu wake kutalika kwake kunali makilomita 2,200. Anayesa mpanda uja ndipo kuchindikala kwake kunali kopitirirapo mamita 65 monga mwa muyeso wa anthu umene mngelo anagwiritsa ntchito. Mpandawo unapangidwa ndi yasipa, ndipo mzindawo unali wagolide oyengeka owala ngati galasi. Maziko a mpanda wa mzindawo anali okongoletsedwa ndi miyala yamtengowapatali ya mtundu uliwonse. Maziko oyamba anali yasipa, achiwiri anali safiro, achitatu ndi kalikedo, achinayi ndi simaragido, achisanu ndi sardiyo, achisanu ndi chiwiri ndi krusolito, achisanu ndi chitatu ndi berulo, achisanu ndi chinayi ndi topaziyo, a khumi ndi krusoprazo, a khumi ndi chimodzi ndi huakito, a khumi ndi chiwiri ndi emetusto. Zipata khumi ndi ziwiri zija zinapangidwa ndi ngale, chipata chilichonse chinapangidwa ndi ngale imodzi. Misewu ya mzindawo inali yopangidwa ndi golide oyengeka, owala ngati galasi.

Ine sindinaone Nyumba ya Mulungu iliyonse mu mzindawo chifukwa Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse ndi Mwana Wankhosa ndiwo Nyumba yake. Palibe chifukwa choti dzuwa kapena mwezi ziwale popeza mu mzindawo ulemerero wa Mulungu ndiwo umawalamo ndipo nyale yake ndi Mwana Wankhosa uja. Mitundu ya anthu idzayenda mʼkuwala kwake ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mu mzindamo. Zipata zake sizidzatsekedwa ngakhale tsiku limodzi lomwe pakuti sikudzakhala usiku kumeneko. Ulemerero ndi ulemu wa mitundu ya anthu adzapita nazo kumeneko. Kanthu kosayeretsedwa sikadzalowamo, kuphatikizanso aliyense wochita zinthu zochititsa manyazi ndi zachinyengo, koma okhawo amene mayina awo alembedwa mʼbuku lamoyo la Mwana Wankhosa.

Ndipo mngeloyo anandionetsa mtsinje wamadzi amoyo, oyera ngati mwala wa krustalo ukutuluka ku mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa, Ukuyenda pakati pa msewu waukulu wa mu mzindawo. Mbali iliyonse ya mtsinjewo kunali mtengo wamoyo, utabala zipatso khumi ndi ziwiri. Kubereka zipatso mwezi uliwonse. Ndipo masamba a mtengowo ndi mankhwala wochiritsa anthu a mitundu ina. Sipadzakhalanso temberero lililonse. Mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa udzakhala mu mzindawo, ndipo atumiki ake adzamutumikira. Iwo adzaona nkhope yake ndipo dzina lake lidzalembedwa pa mphumi zawo. Sipadzakhalanso usiku. Sadzafuna kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuwala kwawo. Ndipo adzalamulira kwamuyaya.

“Odala amene achapa mikanjo yawo, kuti akhale ndi ufulu wopita ku mtengo wamoyo ndi kuti akalowe mʼzipata za mu mzindawo.

Mzimu Woyera ndi mkwatibwi akuti, “Bwerani!” Ndipo amene akumva anena kuti Bwerani! Iye amene ali ndi ludzu abwere, ndipo aliyense amene afuna alandire mphatso yaulere ya madzi amoyo.

Chichewa - Chichewa - NY

NYCCL - Mawu A Mulungu Mu Chichewa Chalero - 2016

This Bible text is from Biblica Open God's Word In Contemporary Chichewa
https://open.bible/bibles/chichewa-biblica-text-bible/
provided by: Biblica Inc, available by Creative Commons CC-BY-SA-4.0,
and this new compilation is shared as www.creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0.
Languages are made available to you by www.ipedge.net