07 – Tsiku la chiweruzo

Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Tsiku la chiweruzo.

Mavesi atatu ofunika kwambiri

Kenaka ndinaona Mpando Waufumu waukulu woyera ndi Iye amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake ndipo panalibenso malo awo. Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aangʼono omwe atayimirira patsogolo pa Mpando Waufumu ndipo mabuku anatsekulidwa. Buku lina linatsekulidwa limene linali Buku Lamoyo. Akufa anaweruzidwa monga mwa zimene anachita monga mmene zinalembedwera mʼmabuku.

Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa,

Iye amene akana Ine ndipo salandira mawu anga ali ndi womuweruza. Tsiku lomaliza mawu amene ndiyankhulawa adzamutsutsa.

Mavesi onse motsatira dongosolo lolondola – 177 ndime

Pamene Abramu anali ndi zaka 99, Yehova anamuonekera nati, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse. Ukhale munthu wochita zolungama nthawi zonse.

Ndithu simungachite zimenezi, kupha anthu olungama pamodzi ndi oyipa. Nʼzosatheka kuti inu nʼkufananitsa olungama ndi oyipa. Kodi woweruza wa dziko lapansi nʼkulephera kuchita chilungamo?”

Muzikhala angwiro pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.

Ndipo mitengo ya mʼnkhalango idzayimba, idzayimba chifukwa cha chimwemwe pamaso pa Yehova, pakuti akubwera kudzaweruza dziko lapansi.

“Ndipo iwe mwana wanga Solomoni, umvere Mulungu wa abambo ako, umutumikire ndi mtima wodzipereka kwathunthu ndi mtima wako wonse, pakuti Yehova amasanthula mtima wa aliyense, ndipo amadziwa maganizo aliwonse a munthu. Ngati ufunafuna Yehova, Iye adzapezeka; koma ngati umutaya, Iye adzakukana kwamuyaya.

Koma ndikudziwa kuti mpulumutsi wanga ali ndi moyo, ndipo pa nthawi yomaliza adzabwera kudzanditeteza. Ndipo khungu langa litatha nʼkuwonongeka, mʼthupi langa lomweli ndidzamuona Mulungu. Ine ndemwe ndidzamuona Iye ndi maso angawa, ineyo, osati wina ayi. Ndithu mtima wanga ukufunitsitsadi! “Koma inu mukuti, ‘Haa! Tingamuzunze bwanji, popeza kuti zonsezi zaoneka chifukwa cha iye yemweyo?’ Inu muyenera kuopa lupanga; pakuti mkwiyo wake umalangadi ndi lupanga; zikadzatero muzadziwa kuti chiweruzo chilipo ndithu.”

Zakuti munthu woyipa amasungidwa chifukwa cha tsiku la tsoka, kuti amapulumutsidwa chifukwa cha tsiku la ukali wa Mulungu?

Mulungu andiyeze ndi muyeso wake wolungama ndipo Iye adzadziwa kuti ine ndine wosalakwa,

Sizitero ndi anthu oyipa! Iwo ali ngati mungu umene umawuluzidwa ndi mphepo. Kotero anthu oyipa sadzatha kuyima pa chiweruzo, kapena anthu ochimwa mu msonkhano wa anthu olungama. Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama, koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka.

Yehova akulamulira kwamuyaya; wakhazikitsa mpando wake waufumu woweruzira. Iye adzaweruza dziko mwachilungamo; adzalamulira mitundu ya anthu mosakondera.

Oyipa amabwerera ku manda, mitundu yonse imene imayiwala Mulungu.

Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.

Oyipa amakonza chiwembu kutsutsana ndi olungama ndipo amawakukutira mano; koma Ambuye amaseka oyipa pakuti Iye amadziwa kuti tsiku lawo likubwera.

Koma Mulungu adzawombola moyo wanga kuchoka ku manda; ndithu Iye adzanditengera kwa Iye mwini.

Musalole konse kuti athawe; mu mkwiyo wanu Mulungu mugwetse mitundu ya anthu. Mulembe za kulira kwanga, mulembe chiwerengero cha misozi yanga mʼbuku lanu. Kodi zimenezi sizinalembedwe mʼbuku lanulo?

Iwo afufutidwe mʼbuku la amoyo ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.

Udzapenya ndi maso ako ndipo udzaona mmene anthu oyipa amalangidwira.

idzayimba pamaso pa Yehova, pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lonse mwachilungamo ndi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.

izo ziyimbe pamaso pa Yehova, pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo, ndi mitundu ya anthu mosakondera.

Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe. Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.

Yehova amayangʼana onse amene amamukonda koma adzawononga anthu onse oyipa.

Chuma sichithandiza pa tsiku lawukali wa Mulungu, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.

Ndinalingalira mu mtima mwanga kuti; “Mulungu adzaweruza olungama pamodzi ndi oyipa omwe, pakuti anayika nthawi yochitikira chinthu chilichonse, nthawi ya ntchito iliyonse.”

Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino, ndipo tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa.

Basi zonse zamveka; mathero a nkhaniyi ndi awa: uziopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wa anthu onse. Pakuti Mulungu adzaweruza zochita zonse, kuphatikizanso zinthu zonse zobisika, kaya zabwino kapena zoyipa.

Ndipo akadzayangʼana pa dziko lapansi adzangoona mavuto okhaokha ndi mdima woopsa ndi wodetsa nkhawa, ndipo adzaponyedwa mu mdima wandiweyani.

Ndidzalanga dziko lonse chifukwa cha zolakwa zake, anthu oyipa ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo. Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza, ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.

Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya, Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmaso mwa munthu aliyense; adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi, Yehova wayankhula.

Koma anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo; matupi awo adzadzuka. Iwo amene ali ku fumbi tsopano adzadzuka ndi kuyimba mosangalala. Monga mame amafewetsa pansi kutsitsimutsa zomera, momwenso Yehova adzaukitsa anthu amene anafa kale.

Maliseche ako adzakhala poyera ndipo udzachita manyazi. Ndidzabwezera chilango ndipo palibe amene adzandiletse.” Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wathu, dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.

Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake; za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake. Wandituma kuti ndikatonthoze olira.

“Taonani, ndikulenga mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. Zinthu zakale sizidzakumbukika, zidzayiwalika kotheratu.

“Monga momwe mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ndidzapanga zidzakhala mpaka muyaya pamaso panga, ndi chonchonso dzina lanu ndi zidzukulu zanu zidzakhalire.” Akutero Yehova. “Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzandipembedza ku Yerusalemu, pa chikondwerero chilichonse cha pokhala pa mwezi watsopano ndi tsiku la Sabata lililonse,” akutero Yehova. “Akamachoka adzaona mitembo ya anthu amene anandiwukira Ine. Mphutsi zawo sizidzafa, kapena moto wawo sudzazimitsidwa. Anthu a mitundu ina yonse powaona adzanyansidwa nawo.”

Pakuti moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa abambo ndi wanga, wamwananso ndi wanga. Munthu wochimwa ndi amene adzafe.

“Ine ndikuyangʼanabe ndinaona “mipando yaufumu ikukhazikitsidwa, ndipo Mkulu Wachikhalire anakhala pa mpando wake. Zovala zake zinali zoyera ngati chisanu chowundana; tsitsi la kumutu kwake linali loyera ngati thonje. Mpando wake waufumu unali wonga malawi a moto, ndipo mikombero yake yonse inkayaka moto. Mtsinje wa moto unkayenda, kuchokera patsogolo pake. Anthu miyandamiyanda ankamutumikira; ndipo anthu osawerengeka anayima pamaso pake. Abwalo anakhala malo awo, ndipo mabuku anatsekulidwa.

Koma oyera mtima a Wammwambamwamba adzalandira ufumu ndipo udzakhala nawo mpaka muyaya, inde ku nthawi zonse.’

Ndikuyangʼanitsitsa, nyanga imeneyi inathira nkhondo anthu oyera mtima ndi kuwagonjetsa, mpaka pamene Mkulu Wachikhalire uja anafika ndi kuweruza mokomera oyera mtima a Wammwambamwamba. Tsono nthawi inafika imene anthu oyera mtimawo analandira ufumu.

Idzayankhula motsutsana ndi Wammwambamwamba ndipo adzazunza oyera mtima ndi kusintha masiku azikondwerero ndi malamulo. Oyera mtimawo adzalamulidwa ndi mfumuyi kwa zaka zitatu ndi theka. “ ‘Koma bwalo lidzapereka chiweruzo, ndipo mphamvu zake zidzalandidwa ndi kuwonongedwa kotheratu mpaka muyaya. Kenaka ulamuliro, mphamvu ndi ukulu wa maufumu pa dziko lonse lapansi zidzaperekedwa kwa oyera mtima, a Wammwambamwamba. Ufumu wawo udzakhala ufumu wosatha, ndipo olamulira onse adzawalamulira ndi kuwamvera.’ ”

“Pa nthawi imeneyo Mikayeli, mngelo wamkulu amene amateteza anthu a mtundu wako, adzabwera. Imeneyi idzakhala nthawi ya mavuto aakulu omwe sanaonekepo kuyambira pachiyambi cha mitundu ya anthu mpaka nthawi ikudzayo. Komatu pa nthawiyi anthu a mtundu wako, aliyense amene dzina lake lidzapezeke lolembedwa mʼbuku adzapulumutsidwa. Ambiri mwa amene akugona mʼnthaka adzadzuka: ena adzapita ku moyo wosatha, ena ku malo amanyazi ndi chilango chosatha. Amene ali anzeru mʼnjira ya chilungamo adzawala ngati kuwala kwa mlengalenga, ndipo amene alondolera ambiri ku njira yolungama, adzawala ngati nyenyezi ku nthawi zosatha. Koma iweyo, Danieli, sungitsa mawuwa, umate bukuli kufikira nthawi ya chimaliziro. Anthu ambiri adzapita uku ndi uko ndipo nzeru zidzanka zikukulirakulira.”

“Koma iweyo Danieli, pitiriza ndipo ulimbikire mpaka matsiriziro. Kenaka udzamwalira. Koma mʼmasiku otsiriza udzauka kuti ulandire gawo lako.”

“Tsiku la Yehova layandikira limene adzaweruza mitundu yonse ya anthu. Adzakuchitira zomwe unawachitira ena; zochita zako zidzakubwerera wekha.

Koma iye ataona Afarisi ndi Asaduki ambiri akubwera kumene ankabatiza, anawawuza kuti, “Ana a njoka inu! Ndani anakuchenjezani kuthawa mkwiyo umene ukubwera?

Tikukamba pano nkhwangwa yayikidwa kale pa mizu ya mitengo, ndipo mtengo umene subala chipatso chabwino udulidwa ndi kuponyedwa pa moto.

Mʼdzanja lake muli chopetera ndipo adzayeretsa popunthirapo pake nadzathira tirigu wake mʼnkhokwe ndi kutentha zotsalira zonse ndi moto wosazima.”

Ngati diso lako lakumanja likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena.

Pakuti momwe inu muweruzira ena, inunso mudzaweruzidwa chimodzimodzi, muyeso umene muyesera ena inunso mudzayesedwa ndi womwewo.

“Lowani pa chipata chopapatiza. Pakuti chipata cholowera kuchiwonongeko nʼchachikulu ndipo msewu wake ndi waukulunso. Ndipo anthu ambiri amalowera pamenepo. Koma chipata ndi chopapatiza ndi msewu ndi waungʼono umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene ayipeza njirayo.

Mudzawazindikira iwo ndi zipatso zawo. Kodi anthu amathyola mpesa pa mtengo wa minga, kapena nkhuyu pa nthula? Chimodzimodzinso mtengo wabwino umabala chipatso chabwino, koma mtengo woyipa umabala chipatso choyipa. Mtengo wabwino sungabale chipatso choyipa, ndi mtengo woyipa sungabale chipatso chabwino. Mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino umadulidwa ndi kuponyedwa pa moto. Momwemonso, ndi zipatso zawo iwo mudzawazindikira.

“Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine pa tsikulo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinkanenera mʼdzina lanu ndi mʼdzina lanunso tinkatulutsa ziwanda ndi kuchita zodabwitsa zambiri?’ Pamenepo ndidzawawuza momveka bwino kuti, ‘Sindinakudziweni inu. Chokani kwa Ine, inu ochita zoyipa!’

Ngati wina aliyense sakakulandirani kapena sakamvera mawu anu, musase fumbi la kumapazi anu pamene mutuluka mʼnyumbayo kapena mu mzindawo. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku lachiweruziro, mlandu wa Sodomu ndi Gomora udzachepa kusiyana ndi wa mzindawo.

Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena.

Koma ndikuwuzani inu kuti pa tsiku lachiweruzo mlandu wa Turo ndi Sidoni udzachepako kusiyana ndi wanu. Ndipo iwe Kaperenawo, kodi udzakwezedwa kufika kumwamba? Ayi, udzatsitsidwa mpaka pansi kufika ku Hade. Ngati zodabwitsa zimene zinachitika mwa iwe, zikanachitika mu Sodomu, bwenzi iye alipo kufikira lero. Koma Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro mlandu wa Sodomu udzachepako kusiyana ndi wanu.”

Ine ndikukuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro munthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mawu aliwonse wopanda pake amene anayankhula. Pakuti ndi mawu anu mudzapezeka osalakwa ndiponso ndi mawu anu mudzapezeka olakwa.”

Munda ndi dziko lapansi ndipo mbewu yabwino ndi ana a ufumu. Namsongole ndi ana a woyipayo. Ndipo amene anafesa namsongole ndi Satana. Kukolola ndiko kutha kwa dzikoli ndipo otuta ndi angelo. “Monga momwe namsongole azulidwa ndi kutenthedwa ndi moto, momwemonso kudzakhala pakutha kwa dziko. Mwana wa Munthu adzatumiza angelo ake ndipo iwo adzachotsa mu ufumu wake chilichonse chochimwitsa ndi onse amene amachita zoyipa. Adzawaponya mʼngʼanjo yamoto kumene kudzakhala kulira ndi kukuta mano. Pamenepo olungama adzawala ngati dzuwa mu ufumu wa Atate awo. Amene ali ndi makutu amve.”

“Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi khoka limene linaponyedwa mʼnyanja ndipo linakola mitundu yonse ya nsomba. Litadzaza, asodzi analikokera ku mtunda. Pomwepo anakhala pansi nasonkhanitsa nsomba zabwino mʼmadengu koma zoyipa anazitaya. Umu ndi mmene kudzakhalira pakutha kwa dziko. Angelo adzabwera ndi kulekanitsa oyipa ndi olungama. Ndipo oyipa adzawaponya mʼngʼanjo ya moto kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”

Pakuti mu mtima mumatuluka maganizo oyipa, zakupha, zachigololo, zadama, zakuba, zaumboni wonama ndi zachipongwe.

Kodi munthu adzapindula chiyani ngati atapeza zonse za dziko lapansi nataya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthana ndi moyo wake? Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate ake ndi angelo ake ndipo pamenepo Iye adzapereka mphotho kwa munthu mofanana ndi zimene anachita.

Ndipo Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba.

“Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonzera phwando mwana wake wamwamuna. Anatumiza antchito ake kwa amene anayitanidwa kuphwando koma anakana kubwera.

“Koma pamene mfumu inabwera kudzaona oyitanidwawo, inaona munthu amene sanavale zovala zaukwati. Inamufunsa kuti, ‘Bwenzi walowa bwanji muno wopanda zovala zaukwati?’ Munthuyo anakhala chete. “Pamenepo mfumuyo inawuza otumikira kuti, ‘Mʼmangeni manja ndi miyendo, ndipo muponyeni kunja, ku mdima kumene kudzakhale kulira ndi kukuta mano.’

“Njoka inu! Ana amamba! Mudzachithawa bwanji chilango cha gehena?

koma wopirira kufikira chimaliziro adzapulumuka.

“Nthawi imeneyo ufumu wakumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi amene anatenga nyale zawo napita kukakumana ndi mkwati. Asanu anali opusa ndipo asanu ena anali ochenjera. Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta; koma ochenjerawo anatenga mafuta awo mʼmabotolo pamodzi ndi nyale zawo. Mkwati anachedwa ndipo onse anayamba kusinza nagona. “Pakati pa usiku kunamveka kufuwula kuti, ‘Onani Mkwati! Tulukani kuti mukakumane naye!’ “Pamenepo anamwali onse anadzuka nayatsa nyale zawo. Opusawo anati kwa ochenjerawo, ‘Tipatseniko mafuta anu; nyale zathu zikuzima.’ “Ochenjerawo anayankha, nati, ‘Ayi sangakwanire inu ndi ife. Pitani kwa ogulitsa mafuta ndi kukadzigulira nokha.’ “Koma pamene ankapita kukagula mafutawo, mkwati anafika. Anamwali amene anali okonzeka aja analowa naye pamodzi mʼnyumba ya phwando la ukwati. Ndipo khomo linatsekedwa. “Pambuyo pake enawo anabwera nati, ‘Ambuye! Ambuye! Titsekulireni!’ “Koma iye anayankha kuti, ‘Zoonadi, ine ndikuwuzani kuti sindikukudziwani.’

“Ambuye ake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika iwe! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika iwe kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’

“Pamene Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wake, pamodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pa mpando waufumu mu ulemerero wakumwamba. Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa pamaso pake, ndipo adzawalekanitsa iwo wina ndi mnzake monga mʼbusa amalekanitsa nkhosa ndi mbuzi. Adzayika nkhosa ku dzanja lake lamanja ndi mbuzi ku lamanzere. “Pamenepo mfumu idzati kwa a ku dzanja lamanja, ‘Bwerani inu odalitsika ndi Atate anga; landirani ufumu umene unakonzedwa chifukwa cha inu kuyambira pachiyambi cha dziko. Pakuti ndinali ndi njala ndipo munandipatsa chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo munandipatsa madzi akumwa, ndinali mlendo ndipo munandilandira, ndinali wausiwa ndipo munandiveka, ndinali wodwala ndipo munandisamalira, ndinali ku ndende ndipo inu munandiyendera.’ “Ndipo olungamawo adzamuyankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala ndipo tinakudyetsani, kapena ludzu ndipo tinakupatsani madzi akumwa? Ndi liti tinakuonani muli mlendo ndipo tinakulandirani, kapena wa usiwa ndipo tinakuvekani? Ndi liti tinakuonani mutadwala kapena ku ndende ndipo tinakuyenderani?’ “Mfumu idzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene munachitira mmodzi wa abale anga onyozekawa munandichitira Ine.’ “Pamenepo adzanena kwa akumanzere kwake kuti, ‘Chokani kwa Ine, inu otembereredwa, pitani ku moto wosatha wokonzedwera mdierekezi ndi angelo ake. Pakuti ndinali ndi njala ndipo simunandipatse chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo simunandipatse madzi akumwa, ndinali mlendo koma inu simunandilandire, ndinali wa usiwa koma simunandiveke, ndinali wodwala komanso ku ndende simunandisamalire.’ “Iwo adzayankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala kapena ludzu kapena mlendo kapena wausiwa kapena wodwala kapena mʼndende, ndipo kuti sitinakuthandizeni?’ “Iye adzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene simunachitire mmodzi wa abale anga onyozekawa simunandichitire Ine.’ “Amenewa adzapita ku chilango chosatha pamene olungama ku moyo wosatha.”

koma aliyense amene achitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa pakuti wachita tchimo losatha.”

Ndipo ngati pa malo ena sakakulandirani kapena kukumverani, sasani fumbi la kumapazi anu pamene mukuchoka, kuti ukhale umboni wowatsutsa.”

Pakuti kuchokera mʼkati mwa mitima ya anthu, mumatuluka maganizo oyipa, chiwerewere, kuba, kupha, chigololo, dyera, nkhwidzi, chinyengo, machitidwe onyansa, kaduka, chipongwe, kudzikuza ndi kupusa.

“Ndipo ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana angʼono awa amene akhulupirira Ine, kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala waukulu mʼkhosi mwake. Ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo ndi dzanja limodzi kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri ndi kupita ku gehena, kumene moto wake suzima. (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima). Ndipo ngati phazi lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo olumala kusiyana ndi kukhala ndi mapazi awiri ndi kuponyedwa mu gehena. (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima). Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu gehena, kumene “ ‘mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima.’

Aliyense amene akakhulupirire nabatizidwa adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira adzalangidwa.

Mʼdzanja lake muli chopetera kuti ayeretse powomberapo tirigu ndi kusonkhanitsa tirigu ndipo adzatentha zotsalira zonse ndi moto wosazimitsika.”

Palibe chinthu chophimbika chimene sichidzawululika, kapena chobisika chimene sichidzadziwika. Chimene mwanena mu mdima chidzamveka dzuwa likuwala, ndipo zimene mwanongʼona mʼkhutu mʼchipinda chamʼkati, zidzayankhulidwa pa denga la nyumba. “Ine ndikuwuzani, abwenzi anga, musachite mantha ndi amene amapha thupi chifukwa akatero sangachitenso kanthu. Koma Ine ndidzakuonetsani amene muyenera kumuopa: Wopani Iye, amene pambuyo pakupha thupi, ali ndi mphamvu yakukuponyani ku gehena. Inde, Ine ndikuwuzani, muopeni Iye.

Ine ndikuti, ayi! Koma ngati inu simutembenuka mtima, inunso mudzawonongeka nonse.

Wina anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndi anthu ochepa okha amene adzapulumutsidwe?” Iye anawawuza kuti, “Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza, chifukwa ndikukuwuzani kuti ambiri adzafuna kulowa koma sadzatha kutero. Nthawi yomwe mwini nyumba adzayimirira ndi kutseka chitseko, inu mudzayima kunja kugogoda ndi kudandaula kuti, ‘Bwana, tatitsekulirani khomo.’ “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera.’ “Ndipo inu mudzati, tinkadya ndi kumwa ndi inu ndipo munkaphunzitsa mʼmisewu yathu. “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera. Chokereni inu nonse ochita zoyipa!’ “Mudzalira ndi kukuta mano mukadzaona Abrahamu, Isake ndi Yakobo ndi aneneri onse ali mu ufumu wa Mulungu koma inuyo mutaponyedwa kunja.

Koma ukakonza phwando, itana anthu osauka, ofa ziwalo, olumala ndi osaona. Pamenepo udzakhala wodala, chifukwa iwo sangakubwezere kanthu, koma Mulungu ndiye adzakubwezera pa chiukitso cha olungama.”

Mmodzi wa achifwambawo, amene anapachikidwa, anamunenera Iye zamwano nati, “Kodi sindiwe Khristu? Dzipulumutse wekha ndi ifenso!” Koma wachifwamba winayo anamudzudzula iye nati, “Suopa Mulungu, iwenso ukulandira chilango chomwechi? Ife tikulangidwa mwachilungamo, pakuti ife tikulandira monga mwa ntchito zathu. Koma munthu uyu sanachimwe kanthu.” Kenaka anati, “Yesu, mundikumbukire ine pamene mulowa mu ufumu wanu.” Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti lero lino udzakhala ndi Ine mʼparadaiso.”

Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu.

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi. Aliyense wokhulupirira Iye saweruzidwa, koma aliyense wosakhulupirira waweruzidwa kale chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. Ndipo chiweruzo ndi ichi: kuwunika kunabwera mʼdziko lapansi, koma anthu anakonda mdima mʼmalo mwa kuwunikako, chifukwa ntchito zawo zinali zoyipa. Aliyense wochita zoyipa amadana ndi kuwunika, ndipo sabwera poyera chifukwa cha mantha kuti ntchito zake zingaonekere. Koma aliyense wokhala mu choonadi amabwera ku kuwunika, kuti zionekere poyera zimene iye wachita zachitika kudzera mwa Mulungu.”

Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.”

“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo. Pakuti monga Atate ali gwero la moyo, momwemonso anapereka mphamvu zopereka moyo mwa Mwana. Ndipo wamupatsa Iye ulamuliro woweruza chifukwa ndi Mwana wa Munthu. “Musadabwe ndi zimenezi. Pakuti nthawi ikubwera pamene onse amene ali mʼmanda adzamva mawu ake ndi kutuluka. Iwo amene anachita zabwino adzauka ndi kupita ku moyo wosatha ndipo amene anachita zoyipa adzauka ndi kupita ku chilango chamuyaya.

Pakuti chifuniro cha Atate anga ndi chakuti aliyense amene aona Mwanayo namukhulupirira akhale ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.”

Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene anandituma Ine samubweretsa. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.

Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Iye amene akhulupirira ali nawo moyo wosatha.

Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga ali ndi moyo wosatha ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.

Kenakanso Yesu anawawuza kuti, “Ine ndikupita, ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa muli mʼmachimo anu. Kumene ndikupita, inu simungabwereko.”

Marita anayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti adzauka pa kuukanso pa tsiku lomaliza.” Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo.

Ino tsopano ndi nthawi yachiweruzo pa dziko lapansi; tsopano olamulira wa dziko lapansi adzathamangitsidwa.

Iye amene akana Ine ndipo salandira mawu anga ali ndi womuweruza. Tsiku lomaliza mawu amene ndiyankhulawa adzamutsutsa.

Ngati wina aliyense sakhala mwa Ine, iyeyo ali ngati nthambi imene yatayidwa ndi kufota. Nthambi zotero zimatoledwa, kuponyedwa pa moto ndi kupsa.

Iye anatilamulira ife kuti tilalikire kwa anthu ndi kuchitira umboni kuti Iye ndiye amene Mulungu anamusankha kukhala woweruza wa amoyo ndi akufa.

Nthawi imene anthu sankadziwa, Mulungu anawalekerera koma tsopano akulamulira kuti anthu onse, kulikonse atembenuke mtima. Pakuti Iye wayika tsiku limene adzaweruze dziko lapansi mwa chilungamo kudzera mwa Munthu amene anamusankha. Iye watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.” Atamva za kuuka kwa akufa, ena a iwo anaseka, koma enanso anati, “Ife tikufuna tidzamvenso zimenezi tsiku lina.”

Ine ndili nacho chiyembekezo chomwecho chimene iwo ali nacho mwa Mulungu, kuti kudzakhala kuuka kwa akufa kwa olungama ndiponso kwa ochimwa. Kotero ine ndimayesetsa kuti ndikhale ndi chikumbumtima chosanditsutsa pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.

Ndipo popeza anaona kuti nʼchopanda nzeru kumvera Mulungu, Iye anawasiya kuti atsatire maganizo achitayiko kuti achite zosayenera kuchitazo. Iwo ndi odzazidwa ndi mtundu uliwonse wa makhalidwe oyipa, zonyansa, umbombo ndi dumbo. Iwo ndi odzazidwa ndi kaduka, kupha, mikangano, chinyengo ndi udani. Iwowo ndi amiseche, osinjirira, odana ndi Mulungu, achipongwe, odzitama ndi odzitukumula. Iwo amapeza njira zochitira zoyipa. Samvera makolo awo, alibe nzeru, chikhulupiriro, sakhudzidwa mu mtima ndipo ndi ankhanza. Ngakhale kuti amadziwa chiweruzo cholungama cha Mulungu chakuti amene amachita zinthu zotere amayenera imfa, iwo sangopitiriza chabe zimenezi, koma amavomerezanso amene amazichita zimenezi.

Choncho, iwe amene umaweruza munthu wina, ulibe pokanira pakuti nthawi iliyonse pamene uweruza wina ukudzitsutsa wekha chifukwa iwe amene umaweruzawe umachitanso zinthu zomwezo. Tsopano ife tikudziwa kuti chiweruzo cha Mulungu, chotsutsa amene amachita zinthu zotere, nʼchokhazikika pa choonadi. Kodi ukuganiza kuti udzathawa chiweruzo cha Mulungu iwe munthu wamba, pamene uweruza ena, iwe ndi kumachitanso zomwezo? Kodi kapena ukupeputsa kukoma mtima kwa Mulungu, kuleza mtima kwake ndi kupirira kwake? Kodi sukuzindikira kuti kukoma mtima kwakeko, nʼkofuna kuti iweyo ulape machimo ako? Koma pakuti ndiwe wosamvera ndi wa mtima wosafuna kulapa, ukudzisungira chilango pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu, pamene chiweruzo cholungama cha Mulungu chidzaonetsedwa. Mulungu adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake. Iye adzapereka moyo wosatha kwa amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pochita ntchito zabwino mopirira. Koma Mulungu adzakhuthulira mkwiyo ndi ukali wake pa amene amachita zofuna zawo ndi kukana choonadi nʼkumatsatira zoyipa. Masautso ndi zowawa zidzagwera munthu aliyense amene amachita zonyansa, kuyambira Myuda kenaka anthu a mitundu ina. Koma ulemerero, ulemu ndi mtendere zidzakhala kwa aliyense amene amachita zabwino, kuyambira Myuda kenaka anthu a mitundu ina. Pajatu Mulungu alibe tsankho.

Onse amene amachimwa osadziwa Malamulo, adzawonongeka ngakhale kuti sadziwa Malamulowo. Ndipo onse amene amachimwa akudziwa Malamulo adzaweruzidwa potsata Malamulowo. Pakuti si amene amangomva Malamulo amene amakhala wolungama pamaso pa Mulungu, koma ndi okhawo amene amachita zili mʼMalamulomo amene adzatchedwa olungama. Ndithu, pamene a mitundu ina, amene alibe Malamulo, koma mwachikhalidwe chawo amachita zimene zili mʼMalamulo, iwowo ndi Malamulo pa iwo okha, ngakhale kuti alibe Malamulowo. Ntchito zawo zimaonetsa kuti Malamulowo alembedwa mʼmitima mwawo. Chikumbumtima chawonso chimawachitira umboni pakuti maganizo awo amawatsutsa kapena kuwavomereza. Izi zidzachitika pa tsiku limene Mulungu adzaweruza zinsinsi za anthu kudzera mwa Yesu Khristu, monga momwe Uthenga wanga Wabwino unenera.

Tsopano tikudziwa kuti chilichonse Malamulo amanena, amanena kwa amene amalamulidwa ndi Malamulowo, ndi cholinga chakuti aliyense asowe chonena, ndipo dziko lonse lidzayimbidwa mlandu ndi Mulungu.

komanso chifukwa ife amene Mulungu adzatiyesa olungama, ife amene tikhulupirira mwa Iye amene anamuukitsa kwa akufa, Yesu Ambuye athu. Iye anaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha machimo athu ndipo anaukitsidwa ndi kukhala ndi moyo kuti tilungamitsidwe.

Chifukwa chake ife tinayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo. Tinalowa mu imfa ndi cholinga choti monga momwe Khristu anaukitsidwa kwa akufa ndi ulemerero wa Atate, ifenso tikakhale mʼmoyo watsopano. Pakuti ngati ife tinakhala amodzi ndi Iye mu imfa yake, tidzakhalanso ndithu amodzi ndi Iye mu kuuka kwake.

Koma tsopano pakuti inu mwamasulidwa ku tchimo ndipo mwasanduka akapolo a Mulungu, phindu lomwe mulipeza ndi kuyera mtima ndipo chotsatira chake ndi moyo wosatha. Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa chifukwa mwa Khristu Yesu, lamulo la Mzimu Woyera amene amapereka moyo, lawamasula ku lamulo la tchimo ndi la imfa.

Okondedwa anga, musabwezere choyipa, koma lekerani Mulungu. Pakuti kwalembedwa, “Kubwezera chilango nʼkwanga. Ndidzawalanga ndine,” akutero Ambuye.

Tsono nʼchifukwa chiyani iwe ukuweruza mʼbale wako? Kapena nʼchifukwa chiyani ukumunyoza mʼbale wako? Pakuti ife tonse tidzayima pa mpando wakuweruza wa Mulungu. Kwalembedwa, akutero Ambuye, “Pamene Ine ndili ndi moyo, aliyense adzandigwadira ndipo lilime lililonse lidzavomereza Mulungu.” Choncho tsopano, aliyense wa ife adzafotokoza yekha kwa Mulungu.

Adzakulimbikitsani mpaka kumapeto kuti mudzakhale wopanda mlandu pa tsiku lobwera Ambuye athu Yesu Khristu.

Pakuti wina sangayikenso maziko ena oposera amene anakhazikitsidwa kale, amene ndi Yesu Khristu. Ngati munthu aliyense amanga pa maziko awa pogwiritsa ntchito golide, siliva, miyala yamtengowapatali, milimo yamitengo, tsekera kapena udzu, ntchito yake idzaonekera pamene Tsiku la chiweruzo lidzazionetsa poyera. Tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito ya munthu aliyense. Ngati zimene zamangidwazo sizidzagwa, adzalandira mphotho yake. Ndipo ngati zidzanyeke ndi moto, sadzalandira mphotho koma iye mwini adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wapulumuka mʼmoto.

Chomwecho musaweruze nthawi yoweruza isanakwane. Dikirani mpaka Ambuye atabwera. Iye adzaonetsa poyera zimene zabisika mu mdima ndipo adzaonetsa maganizo a mʼmitima ya anthu. Pa nthawi imeneyo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko.

Kodi simukudziwa kuti munthu woyipa sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musanyengedwe: achigololo, kapena opembedza mafano, kapena achiwerewere, kapena amuna adama, kapena ogonana ndi amuna okhaokha; kapena akuba, kapena aumbombo, kapena oledzera, kapena achipongwe, kapena opeza ndalama mwachinyengo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu. Ndipo umu ndi mmene ena mwa inu munalili. Koma munatsukidwa, munayeretsedwa, munalungamitsidwa mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu ndi Mzimu wa Mulungu wathu.

Koma tikanadziyesa tokha sitikaweruzidwanso.

Koma nʼzoonadi kuti Khristu anaukitsidwa kwa kufa, chipatso choyamba cha onse ogona tulo. Pakuti monga imfa inadza kudzera mwa munthu, kuuka kwa akufa kwabweranso kudzera mwa munthu. Pakuti monga mwa Adamu onse amafa, chomwechonso mwa Khristu onse adzakhala ndi amoyo. Koma aliyense adzauka pa nthawi yake. Khristu ndiye woyambirira, pambuyo pake, pamene Khristu adzabwera, iwo amene ali ake adzauka. Pamenepo chimaliziro chidzafika, pamene Iye adzapereka ufumu kwa Mulungu Atate, atathetsa ufumu wonse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse. Pakuti Iye ayenera kulamulira mpaka Mulungu atayika pansi pa mapazi ake adani ake onse. Mdani wotsiriza kuwonongedwa ndi imfa. Pakuti Mulungu “wayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.” Ponena kuti wayika “zinthu zonse pansi pa mapazi ake,” nʼchodziwikiratu kuti sakuphatikizapo ndi Mulungu yemwe, amene anayika zinthu zonse pansi pa Khristu. Pamene adzatsiriza kuchita zimenezi, Mwana weniweniyo adzakhala pansi pa ulamuliro wa Iye amene anayika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.

Zidzaterenso pamene akufa adzauka. Thupi loyikidwa mʼnthaka ngati mbewu limavunda, koma likadzauka lidzakhala losavunda. Limayikidwa mʼmanda mopanda ulemu, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi ulemerero. Limayikidwa mʼmanda lili lofowoka, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi mphamvu. Limayikidwa mʼmanda thupi la mnofu chabe, koma likadzaukitsidwa lidzakhala lauzimu. Ngati pali thupi la mnofu, palinso thupi lauzimu. Kwalembedwa kuti, “Munthu woyamba Adamu anakhala wamoyo,” Adamu wotsiriza anakhala wopatsa moyo. Zauzimu sizinabwere koyambirira, koma zachilengedwe, pambuyo pake zauzimu. Munthu woyamba anali wa dziko lapansi, wochokera mʼnthaka koma munthu wachiwiri anali wochokera kumwamba. Monga analili munthu wa dziko lapansi, momwemonso anthu onse amene ndi a dziko lapansi. Ndipo monga alili munthu wakumwamba, momwemonso anthu onse amene ndi akumwamba. Ndipo monga momwe tinabadwa ofanana ndi munthu wa dziko lapansi uja, momwemonso tidzakhala ofanana ndi munthu wakumwamba.

Ndikunenetsa, abale, kuti thupi ndi magazi sizingathe kulowa mu ufumu wa Mulungu, ndipo zimene zimavunda sizingathe kulowa kumene zinthu sizivunda. Tamverani, ndikuwuzeni chinsinsi. Tonse sitidzagona tulo, koma tonse tidzasandulika. Zidzachitika mwadzidzidzi, mʼkamphindi kochepa, monga ngati kuphethira kwa diso, pa lipenga lotsiriza. Pakuti lipenga lidzalira, akufa adzaukitsidwa opanda chovunda, ndipo ife tidzasandulika. Pakuti chovunda chiyenera kuvala chosavunda, ndi thupi ili lakufa liyenera kuvala losafa. Pamene thupi lovundali likadzasanduka losavunda, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzakwaniritsidwa zimene zinalembedwa zakuti, “Imfa yogonjetsedwa kwathunthu.”

Pakuti tonsefe tiyenera kukaonekera pa mpando woweruza wa Khristu, kuti aliyense wa ife akalandire zomuyenera molingana ndi zimene anachita ali mʼthupi; zabwino kapena zoyipa. Tsono popeza tikudziwa tanthauzo la kuopa Ambuye, ife timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziwa bwino lomwe, ndipo tikukhulupirira kuti inunso mumatidziwa bwino mʼmitima mwanu.

Pakuti ndikuona kuti pamene ndibwera sindidzakupezani monga mmene ndikufunira kuti muzikhalira, ndipo simungadzandione monga mmene mukufunira kundionera. Ndikuopa kuti pangadzakhale mkangano, nsanje, kupserana mitima, kugawikana, ugogodi, miseche, kudzitukumula ndi chisokonezo. Ndikuopa kuti pamene ndidzabwerenso, Mulungu adzandichepetsa pamaso panu, ndipo ndidzamva chisoni ndi ambiri amene anachimwa kale ndipo sanalape zonyansa, zachigololo ndi zilakolako zoyipa zimene anachita.

Ntchito za thupi lanu la uchimo zimaonekera poyera ndi izi: dama, zodetsa ndi kuchita zonyansa; kupembedza mafano ndi ufiti; kudana, kukangana, kupsa mtima, kudzikonda, kugawikana, mipatuko ndi nsanje, kuledzera, mchezo ndi zina zotere. Ine ndikukuchenjezani monga ndinachita poyamba paja kuti amene amachita zimenezi sadzalandira ufumu wa Mulungu.

Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa. Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha.

Mwa Yesu Khristu, chifukwa cha magazi ake, ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo athu molingana ndi kuchuluka kwa chisomo cha Mulungu

Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu. Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika. Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu. Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera.

Ine ndikufuna kudziwa Khristu, ndithu, kudziwa mphamvu zake za kuuka kwa akufa. Ndikufuna kuyanjana naye mʼmasautso ake, kufanana naye pa imfa yake kuti nanenso ndidzaukitsidwe kwa akufa.

Koma ife ndife nzika za kumwamba ndipo tikudikirira mwachidwi Mpulumutsi wochokera kumeneko, Ambuye Yesu Khristu. Iyeyo, ndi mphamvu imene imamuthandiza kukhazikitsa zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, adzasintha matupi athu achabewa kuti akhale ofanana ndi thupi lake la ulemerero.

Pakuti Iye anatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima ndi kutibweretsa mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo.

Koma tsopano Iye anakuyanjanitsani mʼthupi la Khristu kudzera mu imfa kuti akuperekeni pamaso pake oyera, opanda banga ndi opanda chotsutsidwa nacho ngati mupitirirabe kukhala mʼchikhulupiriro chanu, okhazikika ndi olimba, osasunthidwa kuchoka pa chiyembekezo chimene munachigwira mu Uthenga Wabwino. Uwu ndi Uthenga Wabwino umene munawumva, umene wakhala ukulalikidwa kwa olengedwa onse a pansi pa thambo, ndi umenenso, ine Paulo ndinakhala mtumiki wake.

Choncho, iphani zilakolako za dziko lapansi mwa inu, monga: dama, zodetsa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoyipa ndi umbombo, pakuti umbombo ndiko kupembedza mafano. Chifukwa cha zimenezi, mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa ana osamvera. Inunso kale munkachita zomwezi, mʼmoyo wanu wakale uja. Koma tsopano mukuyenera kuzichotsa zinthu zonsezi monga: mkwiyo, ukali, dumbo, chipongwe ndi mawu onyansa. Musanamizane wina ndi mnzake, popeza munavula munthu wakale pamodzi ndi zochita zake

Aliyense amene amachita zolakwa adzalandira malipiro molingana ndi kulakwa kwake, ndipo palibe tsankho.

Iye alimbikitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera mtima pamaso pa Mulungu ndi Atate athu pamene Ambuye athu Yesu akubwera ndi oyera ake onse.

Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Zonsezi zikutsimikiza kuti Mulungu amaweruza molungama. Zotsatira zake ndi zakuti mudzatengedwa kukhala oyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu umene mukuwuvutikira. Mulungu ndi wolungama ndipo adzalanga amene amakusautsaniwo ndikukupatsani mpumulo amene mukusautsidwa, pamodzi ndi ifenso. Izi zidzachitika Ambuye Yesu akadzaoneka mʼmalawi amoto kuchokera kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu. Iye adzalanga amene sadziwa Mulungu ndi amene samvera Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu. Adzalangidwa ndi chiwonongeko chamuyaya ndipo sadzaonanso nkhope ya Ambuye ndi ulemerero wamphamvu zake pa tsiku limene iye adzabwera kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ndi kuyamikidwa ndi onse amene anakhulupirira. Inu mudzakhala nawo mʼgulumo chifukwa munakhulupirira umboni wathu.

Tikudziwa kuti Malamulo ndi abwino ngati munthu awagwiritsa ntchito bwino. Tikudziwanso kuti Malamulo sakhazikitsidwa chifukwa cha anthu olungama, koma ophwanya lamulo ndi owukira, osaopa Mulungu ndi ochimwa, wopanda chiyero ndi osapembedza; amene amapha abambo awo ndi amayi awo, kapena anthu ena. Malamulo amayikidwa chifukwa cha anthu achigololo ndi ochita zadama ndi amuna anzawo, anthu ogulitsa akapolo, abodza ndi olumbira zabodza, ndi ochita chilichonse chotsutsana ndi chiphunzitso choona. Chiphunzitso chimene chimagwirizana ndi Uthenga Wabwino wonena za ulemerero wa Mulungu wodala, umene Iye mwini anandisungitsa.

Pereka malangizo amenewa kwa anthu kuti akhale opanda zolakwa.

Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi.

Usunge lamuloli mopanda banga ndi cholakwa kufikira Ambuye athu Yesu Khristu ataonekera.

Mawu oyenera kuwadalira ndi awa: Ngati ife tinafa naye pamodzi, tidzakhalanso moyo pamodzi naye. Ngati tinapirira, tidzalamuliranso naye pamodzi. Ngati ife timukana, Iye adzatikananso.

Pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa omwe pamene adzaonekera ndi ufumu wake, ndikukulamula kuti:

Pakuti moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthawi yakwana yoti ndinyamuke ulendo wanga. Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liwiro ndipo ndasunga chikhulupiriro. Tsopano mphotho yanga ikundidikira imene ndi chipewa cha chilungamo, imene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa pa tsiku lijalo, osati ine ndekha komanso onse amene akufunitsitsa kubwera kwake.

Nʼchifukwa chake, ife tiyenera kusamalira kwambiri zimene tinamva, kuopa kuti pangʼono ndi pangʼono tingazitaye. Popeza uthenga umene unayankhulidwa kudzera mwa angelo unali okhazikika ndithu, choncho aliyense amene ananyozera ndi kusamvera analandira chilango choyenera. Nanga ife tidzapulumuka bwanji tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotere? Ambuye ndiye anayamba kuyankhula za chipulumutsochi, kenaka amenenso anamvawo anatitsimikizira.

Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa,

Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine, Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa mʼMalemba.’ ”

Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira. Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu

Pakuti timadziwa amene anati, “Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.” Iye anatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.” Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo.

Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ku mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba. Mwafika mu msonkhano wa angelo osangalala osawerengeka. Mwafika mu mpingo wa ana oyamba kubadwa, amene mayina awo analembedwa kumwamba. Inu mwafika kwa Mulungu, woweruza anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama ndi osandutsidwa kukhala angwiro.

Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo mwamuna ndi mkazi azikhala wokhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzawalanga.

Pakuti mwataya kale nthawi yambiri mʼmbuyomu pochita zimene anthu osapembedza amachita, moyo wokhumba zonyansa, zilakolako zoyipa kuledzera, zochitika zoyipa za pa phwando, mapokoso ndi kupembedza mafano onyansa.

Koma adzafotokoza okha mlandu wawo kwa Mulungu amene wakonzeka kuweruza amoyo ndi akufa. Pa chifukwa chimenechi, Uthenga Wabwino unalalikidwa ngakhale kwa iwo amene tsopano ndi akufa, kuti adzaweruzidwe monga anthu ku thupi, koma adzakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mu mzimu. Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera.

Pakuti nthawi yafika kuti chiweruzo chiyambe mʼnyumba ya Mulungu, ndipo ngati chiyamba ndi ife nanga podzafika kwa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, chidzakhala chotani?

Pakuti Mulungu sanalekerere angelo atachimwa paja, koma anawaponya mʼndende, nawayika mʼmaenje amdima, kuwasunga kuti adzaweruzidwe.

Tsono mutha kuona kuti Ambuye amadziwa kuwapulumutsa kwake pa mayesero anthu opembedza. Amadziwanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo. Makamaka amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi nanyoza ulamuliro. Anthu amenewa ndi odzikuza, ndipo otsata chifuniro cha iwo eni, sasamala za munthu, saopa kuchitira chipongwe zolengedwa za mmwamba. Komatu ngakhale angelo, amene ali akulu ndi amphamvu kuwaposa, sayankhula za chipongwe pobweretsa chiweruzo pa iwo kuchokera kwa Ambuye. Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ali ngati zirombo zopanda nzeru. Zirombo zolengedwa kuti zigwidwe ndi kuwonongedwa, ndipo ngati zirombozo adzawonongedwa. Iwo adzalangidwa chifukwa cha zoyipa zimene anachita. Koma chimene chimawakomera ndi kumangochita zokondweretsa thupi masanasana. Iwo ali ngati mawanga ndi zilema. Podya nanu pamodzi amakondwera kuchita za chinyengo. Ndi maso awo odzaza ndi chigololo, salekeza kuchimwa. Amanyengerera anthu osakhazikika. Iwo ndi akatswiri pa dyera ndi chuma, ndipo ndi ana otembereredwa! Iwo anasiya njira yolungama ndipo anapatuka kutsata njira ya Baalamu mwana wa Beori, amene anakonda malipiro a chosalungama. Koma anadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwakeko. Bulu, nyama imene siyankhula, inayankhula ngati munthu kuletsa misala ya mneneriyo. Anthu amenewa ali ngati akasupe wopanda madzi, ndiponso ngati nkhungu yowuluzidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu wawasungira mdima wandiweyani.

Dziko la kumwamba ndi lapansi la masiku ano akulisunga ndi mawu omwewo kuti adzalitentha ndi moto. Akuzisunga mpaka tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osapembedza Mulungu. Koma abale okondedwa, musayiwale chinthu chimodzi ichi: Kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi! Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape.

Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikuli zinthu zakumwamba zidzachoka ndi phokoso lalikulu. Zinthu zonse zidzawonongedwa ndi moto, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo zidzapsa. Popeza kuti zinthu zonse zidzawonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wachiyero ndi opembedza Mulungu pamene mukuyembekezera tsiku la Mulungu ndi kufulumiza kufika kwake. Pa tsiku limeneli zinthu zakumwamba zidzawonongedwa ndi moto, ndipo zidzasungunuka ndi kutentha. Koma ife tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene Mulungu analonjeza, mʼmene chilungamo chidzakhalamo.

Chomwecho okondedwa, popeza inu mukudikira zimenezi, chitani changu kuti mukhale wopanda chilema kuti mukhale pa mtendere ndi Iye.

Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye. Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili.

Ife tikudziwa kuti tinatuluka mu imfa ndi kulowa mʼmoyo, chifukwa timakonda abale athu. Aliyense amene sakonda mʼbale wake akanali mu imfa. Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha.

Chikondi chafika pachimake penipeni pakati pathu, kotero kuti pa tsiku lachiweruzo tidzakhala olimba mtima chifukwa mʼdziko lapansi moyo wathu uli ngati wa Khristu.

Ndipo umboniwo ndi uwu: Mulungu anatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowu uli mwa Mwana wake. Iye amene ali ndi Mwana ali ndi moyo, amene alibe Mwana wa Mulungu alibe moyo.

Ndipo mukumbukire angelo amene sanakhutire ndi maudindo awo, koma anasiya malo awo. Angelo amenewa Mulungu anawamanga ndi maunyolo osatha, ndipo akuwasunga mʼmalo a mdima mpaka tsiku lalikulu lachiweruzo. Musayiwale mizinda ya Sodomu ndi Gomora ija, ndi mizinda yoyandikana nayo. Anthu mʼmenemo anadziperekanso kuchita zadama ndi kuchita zonyansa zachilendo. Mizinda imeneyi yakhala ngati chitsanzo cha amene adzalangidwa ndi moto wosatha.

Iwowa ali ngati mafunde awukali apanyanja, amene amatulutsa thovu la zonyansa zawo. Amenewa ali ngati nyenyezi zosochera, ndipo Mulungu akuwasungira mdima wandiweyani mpaka muyaya.

kuti adzaweruze aliyense, ndi kudzagamula kuti onse osapembedza ndi olakwa, chifukwa cha ntchito zawo zosalungama zimene anachita mʼmoyo wawo osaopa Mulungu. Adzawatsutsa chifukwa cha mawu onse achipongwe amene osapembedzawa ananyoza nawo Ambuye.”

Muwachitire chifundo amene akukayika. Ena muwapulumutse powalanditsa ku moto. Enanso muwachitire chifundo, koma mwa mantha, ndipo muzidana ngakhale ndi mwinjiro yomwe yayipitsidwa ndi machimo. Kwa Iye amene angathe kukusungani kuti mungagwe mʼmachimo, ndiponso amene angathenso kukufikitsani pamaso pake pa ulemerero wopanda cholakwa muli okondwa,

Nditamuona ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa. Kenaka Iye anasanjika dzanja lake lamanja pa ine nati, “Usachite mantha. Ndine Woyamba ndi Wotsiriza. Ine ndine Wamoyo; ndinali wakufa ndipo taona ndine wamoyo mpaka muyaya! Ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi Hade.

Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wakudya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku paradizo wa Mulungu.

Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana sadzapwetekedwa ndi pangʼono pomwe ndi imfa yachiwiri.

Amene adzapambane adzavala zoyera ngati ena aja. Sindidzafafaniza dzina lake mʼbuku lamoyo, koma ndidzamuchitira umboni pamaso pa Atate anga ndi angelo ake.

Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambana ndi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu.

Iwo anafuwula kuti, “Mudzawaleka mpaka liti, Inu Ambuye wamkulu, woyera ndi woona, osawaweruza anthu okhala mʼdziko lapansi ndi kulipsira magazi athu?”

Mngelo wachisanu ndi chiwiri anawomba lipenga lake, ndipo kumwamba kunamveka mawu ofuwula amene anati, “Ufumu wa dziko lapansi uli mʼmanja mwa Ambuye athu ndi Khristu wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”

A mitundu ina anapsa mtima; koma yafika nthawi yoonetsa mkwiyo. Nthawi yakwana yoweruza anthu akufa, yopereka mphotho kwa atumiki anu, aneneri, anthu oyera mtima anu ndi amene amaopa dzina lanu, wamngʼono pamodzi ndi wamkulu yemwe. Yafika nthawi yowononga amene awononga dziko lapansi.” Pamenepo anatsekula Nyumba ya Mulungu kumwamba ndipo mʼkati mwake munaoneka Bokosi la Chipangano. Kenaka kunachita mphenzi, phokoso, mabingu, chivomerezi ndipo kunachita mkuntho wamatalala akuluakulu.

Iwo sananenepo bodza ndipo alibe cholakwa.

Mngeloyo anayankhula mokweza mawu kuti, “Wopani Mulungu ndi kumutamanda, chifukwa nthawi yoweruza anthu yafika. Mumupembedze Iye amene analenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi akasupe amadzi.”

nayenso adzamwa vinyo waukali wa Mulungu, umene wathiridwa popanda kuchepetsa mphamvu zake mʼchikho cha ukali wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto wamiyala yasulufure pamaso pa angelo oyera ndi pa Mwana Wankhosa. Ndipo utsi wa moto wowazunzawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya. Sikudzakhala kupumula usana ndi usiku kwa amene anapembedza chirombo chija ndi fano lake kapena kwa aliyense amene analembedwa chizindikiro cha dzina lake lija.”

Kenaka ndinamva mngelo wolamulira madzi uja akuti, “Inu mwachita chilungamo, Inu Woyerayo, amene mulipo ndipo munalipo; pakuti iwo anakhetsa magazi a oyera anu ndi aneneri anu, nʼchifukwa chake mwawapatsa magazi kuti amwe, zomwe zikuwayenera.” Kenaka ndinamva mawu ochokera ku guwa lansembe akuti, “Inde, Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, chiweruzo chanu ndi choona ndi cholungama.”

Zitatha izi, ndinamva chimene chinamveka ngati phokoso la gulu lalikulu mmwamba likufuwula kuti, “Haleluya! Chipulumutso ndi ulemerero ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu, pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake. Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake.” Ndipo anafuwulanso kuti, “Haleluya! Utsi wochokera kwa mkazi wadamayo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.”

Kenaka mngelo anandiwuza kuti, “Lemba kuti, Odala amene ayitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwana Wankhosa.” Ndipo anatinso, “Awa ndiwo mawu woona a Mulungu.”

Ndinaona kumwamba kutatsekuka ndipo patsogolo panga panali kavalo woyera, amene anakwerapo dzina lake linali Wokhulupirika ndiponso Woona. Poweruza ndi kuchita nkhondo, amachita molungama.

Ndinaona mipando yaufumu pamene anakhalapo anthu amene anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndipo ndinaona mizimu ya amene anadulidwa makosi chifukwa cha umboni wa Yesu ndi chifukwa cha Mawu a Mulungu. Iwo sanapembedze nawo chirombo kapena fano lake ndipo sanalembedwe chizindikiro chake pa mphumi zawo kapena pa manja awo. Iwo anakhalanso ndi moyo nalamulira pamodzi ndi Khristu zaka 1,000. (Akufa ena onse sanaukenso mpaka zitatha zaka 1,000). Uku ndiko kuuka kwa akufa koyamba.

Kenaka ndinaona Mpando Waufumu waukulu woyera ndi Iye amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake ndipo panalibenso malo awo. Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aangʼono omwe atayimirira patsogolo pa Mpando Waufumu ndipo mabuku anatsekulidwa. Buku lina linatsekulidwa limene linali Buku Lamoyo. Akufa anaweruzidwa monga mwa zimene anachita monga mmene zinalembedwera mʼmabuku. Nyanja inapereka amene anaferamo ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufa ake ndipo munthu aliyense anaweruzidwa monga mwa ntchito zake. Kenaka imfa ndi Hade zinaponyedwa mʼnyanja ya moto. Nyanja yamoto ndiyo imfa yachiwiri. Ngati dzina la wina aliyense silinapezeke mʼBuku Lamoyo, anaponyedwa mʼnyanja yamoto.

Kenaka ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano pakuti kumwamba koyamba ndi dziko lapansi loyamba zinapita ndipo kunalibenso nyanja ina iliyonse. Ndinaona mzinda wopatulika, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wovala zokongola kukonzekera mwamuna wake. Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, “Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo. ‘Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ ”

Amene anakhala pa mpando waufumuyo anati, “Ndikulenga zinthu zonse zikhale zatsopano!” Ndipo anati, “Lemba izi, pakuti mawu awa ndi okhulupirika ndi woona.” Iye anandiwuza kuti, “Kwatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa onse akumva ludzu, ndidzawapatsa zakumwa zaulere zochokera ku kasupe wamadzi amoyo. Iye amene adzapambane adzalandira zonsezi, ndipo ndidzakhala Mulungu wake ndi Iye adzakhala mwana wanga. Koma amantha, osakhulupirira, okonda zonyansa, opha anthu, achiwerewere, amatsenga, opembedza mafano ndi abodza, malo awo adzakhala nyanja yamoto ya sulufule wotentha. Iyi ndi imfa yachiwiri.”

Kanthu kosayeretsedwa sikadzalowamo, kuphatikizanso aliyense wochita zinthu zochititsa manyazi ndi zachinyengo, koma okhawo amene mayina awo alembedwa mʼbuku lamoyo la Mwana Wankhosa.

Wochita zoyipa apitirire kuchita zoyipazo; wochita zonyansa apitirire kuchita zonyansazo; wochita zabwino apitirire kuchita zabwinozo; ndipo woyera mtima apitirire kukhala woyera mtima.” “Taonani, ndikubwera posachedwa! Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense malinga ndi zimene anachita.

Chichewa - Chichewa - NY

NYCCL - Mawu A Mulungu Mu Chichewa Chalero - 2016

This Bible text is from Biblica Open God's Word In Contemporary Chichewa
https://open.bible/bibles/chichewa-biblica-text-bible/
provided by: Biblica Inc, available by Creative Commons CC-BY-SA-4.0,
and this new compilation is shared as www.creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0.
Languages are made available to you by www.ipedge.net