16 – Zakudya zoperekedwa nsembe kwa mafano

Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Zakudya zoperekedwa nsembe kwa mafano.

Mavesi atatu ofunika kwambiri

Ayi. Nsembe za osakhulupirira zimaperekedwa kwa ziwanda, osati kwa Mulungu, ndipo sindikufuna kuti muziyanjana ndi ziwandazo. Simungamwe chikho cha Ambuye, ndi kukamweranso chikho cha ziwanda. Simungadyere pa tebulo la Ambuye ndiponso la ziwanda. Kodi tikufuna kuwutsa mkwiyo wa Ambuye? Kodi ndife amphamvu kuposa Iye?

Pakuti ngati aliyense wachikumbumtima chofowoka akakuonani achidziwitsonu mukudya mʼnyumba yopembedzera mafano, kodi iyeyo sichidzamulimbitsa mtima kuti azidya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano? Kotero kuti chifukwa cha chidziwitso chanu mʼbale wofowokayu amene chifukwa cha iye, Khristu anafa, wawonongeka chifukwa cha chidziwitso chanu. Mukamachimwira abale anu motere ndikuwawonongera chikumbumtima chawo chofowokacho, mukuchimwira Khristu. Nʼchifukwa chake ngati zimene ine ndimadya zichititsa mʼbale wanga kugwa mu tchimo, sindidzadyanso chakudyacho kuti mʼbaleyo ndisamuchimwitse.

Komabe ndili ndi chinthu chokudzudzula nacho. Umamulekerera mkazi uja Yezebeli amene amadzitcha yekha kuti ndi mneneri. Iye amaphunzitsa atumiki anga kuti azichita zadama ndi kumadya zansembe zoperekedwa ku mafano.

Mavesi onse motsatira dongosolo lolondola – 67 ndime

Choncho Yakobo anawuza a pa banja pake ndi onse amene anali naye kuti, “Chotsani milungu yachilendo imene muli nayo, ndipo mudziyeretse nokha ndi kusintha zovala zanu.

“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.” “Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane.

“Samalani pochita zonse zimene ine ndanena. Musamapemphere kwa milungu ina ndipo mayina awo musamawatchule.

Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, ndipo mukadule mitengo yawo ya Asera. Musapembedze mulungu wina, pakuti Yehova amene dzina lake ndi Nsanje, ndi Mulungu wa nsanje. “Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa iwo akamakachita zadama ndi milungu yawo ndi kupereka nsembe, adzakuyitanani ndipo inu mudzadya nsembe zawo. Ndipo inu mukasankha ena mwa ana awo aakazi kukhala akazi a ana anu, akaziwo akakachita zadama ndi milungu yawo, akatsogolera ana anu aamuna kuchita chimodzimodzi.

“ ‘Musatembenukire ku mafano kapena kudzipangira nokha milungu ya zitsulo zosungunula. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha. “Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane,

Yehova Mulungu wanu akadzawapereka mʼmanja mwanu, ndipo inu mukadzawagonjetsa, mudzawawononge kwathunthu. Musadzachite mgwirizano ndi anthuwo ndiponso musadzawachitire chifundo. Musadzakwatirane nawo. Musadzapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna kapena kutenga ana anu aamuna ndi kuwapereka kwa ana awo aakazi. Mukadzatero, iwo adzasocheretsa ana anu aamuna kuti asanditsatire ndi kutumikira milungu ina. Motero Yehova adzakukwiyirani ndi kukuwonongani mwachangu. Koma mukachite izi: Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, mukadule mitengo yawo ya Asera, ndi kutentha mafano awo pa moto.

Muwawotche pa moto mafano a milungu yawo. Musasirire siliva ndi golide amene ali pa mafanoyo. Musamutenge kuti akhale wanu chifukwa mukatero mudzakodwa naye ngati msampha, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa nazo. Musabweretse chinthu chonyansa mʼnyumba mwanu kuopa kuwonongedwa ngati chonyasacho. Muziyipidwa ndi kunyansidwa nacho kwambiri pakuti chidzawonongedwanso.

Ine ndine mboni yokutsutsani lero lino, kuti mukayiwala Yehova Mulungu wanu ndi kutsata milungu ina nʼkumayigwadira, mudzawonongeka ndithu. Monga mitundu ina ya anthu imene Yehova anayiwononga pamaso panu, inunso mudzawonongedwa chifukwa chosamvera Yehova Mulungu wanu.

Onetsetsani kuti mukuchita zimene ndikukulamulirani. Musawonjezerepo kapena kuchotserapo.

Anamuchititsa nsanje ndi milungu yawo yachilendo ndiponso anamukwiyitsa ndi mafano awo onyansa. Anapereka nsembe kwa ziwanda zimene si Mulungu, milungu imene sankayidziwa nʼkale lomwe, milungu yongobwera kumene, milungu imene makolo anu sankayiopa.

Koma Samueli anayankha kuti, “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina kapena kumvera mawu a ake? Taona, kumvera ndi kwabwino kuposa nsembe, ndipo kutchera khutu ndi kwabwino kuposa kupereka mafuta a nkhosa. Pakuti kuwukira kuli ngati tchimo lowombeza, ndipo kukhala nkhutukumve kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Chifukwa mwakana mawu a Yehova. Iyenso wakukana kuti iweyo ukhale mfumu.”

Iwo anakatulutsa mwala wopatulika umene unali mʼnyumba ya Baala ndipo anawutentha. Anawononga mwala wopatulika wa Baala ndi kugwetsa nyumba ya Baala, ndipo anthu anayisandutsa chimbudzi mpaka lero lino.

Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kwambiri kumutamanda; Iyeyo ayenera kuopedwa kuposa milungu yonse. Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano wopanda pake, koma Yehova analenga kumwamba.

Ahazi ankapereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko, imene inamugonjetsa. Iye ankaganiza kuti, “Popeza milungu ya mafumu a Aaramu yawathandiza, ine ndidzapereka nsembe kwa iyo kuti indithandize.” Koma iyoyo inakhala kugwa kwake ndi kugwa kwa Aisraeli onse.

Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda; ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse. Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano, koma Yehova analenga mayiko akumwamba.

Koma mafano awo ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo koma sayankhula, maso ali nawo koma sapenya; makutu ali nawo koma samva, mphuno ali nazo koma sanunkhiza; manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu; mapazi ali nawo koma sayenda; kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu. Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo, chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.

Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo koma sayankhula maso ali nawo, koma sapenya; makutu ali nawo, koma sakumva ndipo mʼkamwa mwawo mulibe mpweya uliwonse. Iwo amene amapanga mafanowo adzakhala ngati mafanowo, chimodzimodzinso iwo amene amadalira mafanowo.

Pakuti tsiku limenelo nonsenu mudzataya mafano anu a siliva ndi golide amene mumapanga ndi manja anu auchimo.

Iwo anaponyera pa moto milungu yawo ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mafano a mitengo ndi miyala, yopangidwa ndi manja a anthu.

“Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo! Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense kapena matamando anga kwa mafano.

Koma onse amene amadalira mafano amene amanena kwa mafanowo kuti, ‘ndinu milungu yathu,’ ndidzawachititsa manyazi kotheratu.

Ndidzatulutsa mlandu wanga ndi iwo chifukwa cha zoyipa zimene anachita pondisiya Ine. Iwo anakafukiza lubani kwa milungu ina, ndi kupembedza zimene anapanga ndi manja awo.

Ana akutorera nkhuni, abambo akusonkha moto, ndipo amayi akukanda ufa kuti aphike makeke oti akapereke nsembe kwa mfumukazi yazakumwamba. Iwo amathira nsembe ya zakumwa kwa milungu ina kuti andipsetse mtima. Koma kodi akuvutitsa Ine? Kodi sakungodzivuta okha, ndi kudzichititsa manyazi? akutero Yehova.” “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Ndidzatsanulira mkwiyo wanga pa Nyumba yangayi, anthu, nyama, mitengo ndi zipatso zomwe. Mkwiyowo udzakhala ngati moto wosazimitsika.

Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru; mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake. Mafano akewo ndi abodza; alibe moyo mʼkati mwawo. Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo. Pamene anthuwo azidzaweruzidwa, mafanowo adzawonongedwa.

Ukanene kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu a ku Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti: Tamverani! Ine ndibweretsa mavuto pa malo pano mwakuti aliyense amene adzamve adzadzidzimuka. Pakuti anthu andikana Ine ndipo ayipitsa malo ano. Afukiza lubani pa malo ano kwa milungu imene iwo ngakhale makolo awo ngakhalenso mafumu a ku Yuda sanayidziwe. Iwo adzaza malowa ndi magazi a anthu osalakwa.

Nyumba za mu Yerusalemu ndi za mafumu a ku Yuda ndidzazisandutsa ngati za ku Tofeti chifukwa ndi nyumba zimene pa madenga ake ankafukiza lubani kwa zolengedwa zamlengalenga ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’ ”

Tsono amuna onse amene anadziwa kuti akazi awo ankafukiza lubani kwa milungu ina, ndiponso akazi onse amene anali pamenepo, gulu lalikulu la anthu, pamodzi ndi anthu onse amene amakhala ku Patirosi mʼdziko la Igupto, anati kwa Yeremiya, “Ife sitimvera uthenga umene watiwuza mʼdzina la Yehova! Koma tidzachitadi chilichonse chimene tinanena kuti tidzachita: Tidzafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndipo tidzayipatsa nsembe yachakumwa ngati mmene tinkachitira ifeyo ndi makolo athu, mafumu athu ndi akuluakulu mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu. Nthawi imeneyo ife tinali ndi chakudya chochuluka ndipo tinali pabwino, sitimapeza mavuto. Koma kuchokera nthawi imene tinasiya kufukiza lubani ndi kupereka chopereka cha chakumwa kwa mfumukazi yakumwamba, ifeyo takhala tikusowa zinthu ndipo takhala tikuphedwa ndi lupanga ndi kufa ndi njala.” Akazi anawonjezera kunena kuti, “Pamene tinkafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa, kodi suja amuna athu ankavomereza mmene timayipangira mfumukazi yakumwambayo makeke abwino olembapo chinthunzi chake ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa?”

Ndiye Yehova sakanathanso kupirira ndi machitidwe anu ndi zonyansa zimene munkachita. Nʼchifukwa chake dziko lanu linasanduka chipululu, chinthu choopsa ndi chotembereredwa. Dziko lopandamo anthu monga zilili lero lino. Mavuto awa akugwerani chifukwa munkafukiza lubani ndipo munkachimwira Yehova pokana kumvera mawu ake ndi kutsatira malamulo ndi malangizo ake.”

“Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru; mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake. Mafano akewo ndi abodza; alibe moyo mʼkati mwawo. Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo. Pamene anthuwo azidzaweruzidwa mafanowo adzawonongedwa.

Mʼmalo mwake, mwadzikweza nokha kutsutsana ndi Ambuye wakumwamba. Inu mwatenga ziwiya za mʼNyumba mwake, ndipo inu ndi akalonga anu, akazi anu ndi azikazi anu mwamwera vinyo mu zimenezi. Inu munatamanda milungu yasiliva ndi golide, yamkuwa, chitsulo, mtengo ndi mwala, imene singaone kapena kumva kapena kuzindikira. Koma simunamupatse ulemu Mulungu amene asunga mʼmanja mwake moyo wanu ndi njira zanu zonse.

Amalonga mafumu mosatsata kufuna kwanga. Amasankha akalonga popanda chilolezo changa. Amadzipangira mafano asiliva ndi agolide koma adzawonongeka nawo.

Koma ndimati ndikamapitiriza kuyitana iwo amandithawa kupita kutali. Ankapereka nsembe kwa Abaala ndipo ankafukiza lubani kwa mafano.

“Kodi fano lili ndi phindu lanji, poti analisema ndi munthu, kapena chifanizo chimene chimaphunzitsa mabodza? Pakuti munthu amene walipanga amakhulupirira ntchito ya manja ake; amapanga mafano amene samatha kuyankhula.

“Musaganize kuti ndinadza kudzathetsa malamulo kapena zonena za aneneri; sindinabwere kudzathetsa koma kukwaniritsa. Ine ndikukuwuzani zoonadi kuti, kufikira kutha kwa thambo ndi dziko lapansi, chilichonse chimene chinalembedwa mʼmalamulo, ngakhale kalemba kakangʼonongʼono, chidzakwaniritsidwa. Chifukwa chake aliyense amene aphwanya limodzi la malamulowa ngakhale lalingʼonongʼono ndi kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, adzakhala wotsirizira mu ufumu wakumwamba, koma aliyense amene achita ndi kuphunzitsa malamulo awa adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba.

Iye anawafunsa kuti, “Kodi nanunso simumvetsetsa? Kodi simukuona kuti palibe kanthu kamene kakalowa mwa munthu kochokera kunja kakhoza kumudetsa? Pakuti sikalowa mu mtima wake koma mʼmimba mwake, ndipo kenaka kamatuluka kunja.” (Ndi mawu amenewa, Yesu anayeretsa zakudya zonse).

“Amene akhulupirika pa zinthu zochepa akhoza kukhulupirikanso pa zinthu zambiri, ndipo amene sakhulupirika pa zinthu zochepa adzakhala wosakhulupirika pa zinthu zambiri.

“Palibe wantchito amene angatumikire mabwana awiri. Mwina iye adzadana ndi wina ndi kukonda winayo, kapena adzakhala wodzipereka kwa wina ndi kumunyoza winayo. Inu simungathe kutumikira Mulungu komanso ndalama nthawi imodzi.”

Wansembe wa Zeusi amene nyumba yopembedzera Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo, anabweretsa ngʼombe yayimuna yovekedwa nkhata za maluwa pa chipata cha mzindawo chifukwa iyeyo pamodzi ndi anthu ena onse aja amafuna kudzipereka nsembe kwa Paulo ndi Barnaba. Koma Barnaba ndi Paulo atamva zimenezi, anangʼamba zovala zawo, nathamangira pakati pa gulu la anthuwo, akufuwula kuti, “Anthu inu, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Ife takubweretserani Uthenga Wabwino, kuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo.

Koma tiwalembere iwo, kuwawuza kuti asadye chakudya choperekedwa kwa mafano, apewenso dama, asadyenso nyama zochita kupotola kapena kudya magazi.

Pakuti zinakomera Mzimu Woyera ndiponso ife kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zoyenera zokhazi: Mupewe kudya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano, musadye magazi, kapena nyama yopha mopotola ndiponso musachite dama. Mudzachita bwino mukapewa zimenezi. Tsalani bwino.

Paulo akudikira Timoteyo ndi Sila ku Atene, anavutika mu mtima kwambiri poona kuti mzindawo unali odzaza ndi mafano.

“Tsono popeza ndife ana a Mulungu, tisaganize kuti umulungu wake ndi wofanana ndi ndalama zagolide, zasiliva, mwala, kapenanso fanizo lopangidwa mwaluso la nzeru za anthu. Nthawi imene anthu sankadziwa, Mulungu anawalekerera koma tsopano akulamulira kuti anthu onse, kulikonse atembenuke mtima. Pakuti Iye wayika tsiku limene adzaweruze dziko lapansi mwa chilungamo kudzera mwa Munthu amene anamusankha. Iye watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.”

Koma kunena za anthu a mitundu ina amene asandulika okhulupirira, ife tinawalembera zimene tinavomerezana zakuti asadye chakudya choperekedwa ku mafano, asadye magazi, asadye nyama yopotola ndiponso asachite zadama.” Mmawa mwake Paulo anatenga amuna aja ndipo anachita mwambo wodziyeretsa. Kenaka anapita ku Nyumba ya Mulungu nakadziwitsa ansembe za tsiku limene adzatsiriza nthawi ya kudziyeretsa ndi kuperekera nsembe aliyense wa iwo.

Ngakhale ankadzitama kuti ndi anzeru, anasanduka opusa. Iwo anasinthanitsa ulemerero wa Mulungu wosafa ndi mafano opangidwa ndi manja wooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame, ndi nyama kapena zokwawa.

Mulandire amene ndi ofowoka mʼchikhulupiriro, osatsutsana naye pa maganizo ake. Chikhulupiriro cha munthu wina chimamulola kudya china chilichonse koma munthu wina, amene chikhulupiriro chake ndi chofowoka, amangodya zamasamba zokha.

Kodi simukudziwa kuti thupi lanu ndi Nyumba ya Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene mwalandira kuchokera kwa Mulungu? Inu simuli panokha ayi. Ndinu ochita kugulidwa. Nʼchifukwa chake lemekezani Mulungu mʼthupi lanu.

Tsopano za chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano: Ife tidziwa kuti tonse tili ndi chidziwitso. Komatu chidziwitso chokha chimadzitukumula, koma chikondi ndicho chimapindulitsa. Munthu amene amaganiza kuti amadziwa kanthu, ndiye kuti sakudziwa monga mmene amayenera kudziwira. Koma munthu amene amakonda Mulungu amadziwika ndi Mulunguyo.

Choncho kunena za chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano; ife tikudziwa kuti mafano si kanthu nʼpangʼonongʼono pomwe pa dziko lapansi, ndiponso kuti palibe Mulungu wina koma mmodzi yekha. Popeza kuti ngakhale pali yotchedwa milungu, kaya ndi kumwamba kapena pa dziko lapansi (poti ilipodi milungu yambirimbiri ndi ambuye ambirimbiri), koma kwa ife pali Mulungu mmodzi yekha, Atate, zinthu zonse zinachokera mwa Iye ndipo ndife ake. Komanso pali Ambuye mmodzi Yesu Khristu kumene zinthu zonse zinachokera ndipo mwa Iye ife tili ndi moyo.

Koma saliyense amadziwa zimenezi. Alipo ena ozolowera mafano kwambiri mwakuti akadya chakudya chotere amaganiza kuti chakudyacho chinaperekedwa nsembe kwa mafano. Ndiye poti chikumbumtima chawo nʼchofowoka chimadetsedwadi. Koma chakudya sichitisendeza kufupi ndi Mulungu. Tikapanda kudya si vuto, tikadya sitisinthikanso. Komabe samalani kuti ufulu wanu ochita zinthu usafike pokhumudwitsa ofowoka. Pakuti ngati aliyense wachikumbumtima chofowoka akakuonani achidziwitsonu mukudya mʼnyumba yopembedzera mafano, kodi iyeyo sichidzamulimbitsa mtima kuti azidya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano? Kotero kuti chifukwa cha chidziwitso chanu mʼbale wofowokayu amene chifukwa cha iye, Khristu anafa, wawonongeka chifukwa cha chidziwitso chanu. Mukamachimwira abale anu motere ndikuwawonongera chikumbumtima chawo chofowokacho, mukuchimwira Khristu. Nʼchifukwa chake ngati zimene ine ndimadya zichititsa mʼbale wanga kugwa mu tchimo, sindidzadyanso chakudyacho kuti mʼbaleyo ndisamuchimwitse.

Choncho abwenzi anga okondedwa, lekani kupembedza mafano. Ndikuyankhula kwa a anthu anzeru zawo, nokha muweruze pa zimene ndikunenazi.

Taganizirani zimene amachita Aisraeli. Kodi onse amene amadya zoperekedwa nsembe, samachita nawo miyambo ya pa guwapo? Kodi ndikutanthauza kuti nsembe zoperekedwa kwa mafano ndi kanthu konse, kapena kuti mafano ndi kanthu konse? Ayi. Nsembe za osakhulupirira zimaperekedwa kwa ziwanda, osati kwa Mulungu, ndipo sindikufuna kuti muziyanjana ndi ziwandazo. Simungamwe chikho cha Ambuye, ndi kukamweranso chikho cha ziwanda. Simungadyere pa tebulo la Ambuye ndiponso la ziwanda. Kodi tikufuna kuwutsa mkwiyo wa Ambuye? Kodi ndife amphamvu kuposa Iye?

Mutha kunena kuti, “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zili za phindu. “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zimathandiza. Munthu aliyense asafunefune zokomera iye yekha, koma zokomeranso ena. Idyani nyama iliyonse imene amagulitsa pa msika, osafunsa mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. Popeza kuti, “Dziko lapansi ndi la Ambuye ndi zonse za mʼmenemo ndi zake.” Ngati wosakhulupirira akuyitanani kuti mukadye naye, inuyo ndi kuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni ndipo musakafunse mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. Koma ngati wina akuwuzani kuti, “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo, pofuna kuthandiza amene wakuwuzaniyo komanso chifukwa cha chikumbumtima. Ndikunena za chikumbumtima cha winayo osati chanu. Tsono mungafunse kuti, nʼchifukwa chiyani ufulu wanga ukuphwanyidwa chifukwa cha chikumbumtima cha munthu wina? Ngati ndikuyamika Mulungu chifukwa cha chakudya, nanga munthu angandinyoze bwanji pa zinthu zomwe ndayamikira nazo Mulungu?

Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. Musakhumudwitse aliyense, kaya ndi Myuda, Mgriki, kapena mpingo wa Mulungu. Mu zonse ndikuyesetsa kukondweretsa aliyense mʼnjira iliyonse. Popeza sindikufunafuna zokondweretsa ine ndekha koma zokomera ambiri kuti apulumutsidwe.

Musamasenze goli pamodzi ndi osakhulupirira. Kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kulungama ndi kusalungama? Kapena kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kuwala ndi mdima? Pali mgwirizano wanji pakati pa Khristu ndi Beliyali? Kapena munthu wokhulupirira angayanjane bwanji ndi munthu wosakhulupirira? Pali mgwirizano wanji pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ya mafano? Popezatu ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo. Monga Mulungu wanena kuti, “Ndidzakhala mwa iwo ndipo ndidzayendayenda pakati pawo, ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo adzakhala anthu anga.” Nʼchifukwa chake “Tulukani pakati pawo ndi kudzipatula, akutero Ambuye. Musakhudze chodetsedwa chilichonse, ndipo ndidzakulandirani.”

Nʼchifukwa chake musalole wina aliyense kukuzengani mlandu chifukwa cha zimene mumadya kapena kumwa, kapena za masiku achikondwerero cha chipembedzo, za chikondwerero cha mwezi watsopano, kapena za tsiku la Sabata. Zimenezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zimene zikubwera, koma choonadi chenicheni chikupezeka mwa Khristu.

Popeza munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nayo miyambo ya dziko lapansi lino, nʼchifukwa chiyani mukukhalanso ngati a dziko lapansi lino? Bwanji mukumvera malamulo monga awa: “Usagwire chakuti,” “Usalawe chakuti,” “Usakhudze chakuti?” Malamulo amenewa amakhudza zinthu zimene zimatha zikamagwiritsidwa ntchito, ndipo malamulo ndi zophunzitsa za anthu chabe. Ndithu malamulo oterewa amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamulira anthu ambiri pa zachipembedzo ndi pa zakudzichepetsa kwa chiphamaso, ndi pa zakuzunza thupi lawo, koma alibe mphamvu zoletsa kuchita zofuna za thupilo.

pakuti iwo amafotokoza za momwe munatilandirira. Iwo amatiwuza za momwe munatembenukira kwa Mulungu kusiya mafano ndi kutumikira Mulungu wamoyo ndi woona.

Mzimu akunena momveka bwino kuti mʼmasiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chawo ndi kutsatira mizimu yonyenga ndi zinthu zophunzitsidwa ndi ziwanda. Ziphunzitso zimenezi zimachokera ku chinyengo cha anthu onama, amene chikumbumtima chawo chinamatidwa ndi chitsulo cha moto. Iwo amaletsa anthu ukwati ndi kuwalamula kuti asamadye zakudya zina, zimene Mulungu analenga kuti amene anakhulupirira ndi kudziwa choonadi, azidye moyamika. Pakuti chilichonse chimene Mulungu analenga ndi chabwino, ndipo chilichonse chisasalidwe, akamachilandira moyamika, pakuti chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndi pemphero.

Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena. Munthu aliyense amene amangomva mawu koma osachita zimene mawuwo amanena, ali ngati munthu amene amayangʼana nkhope yake pa galasi. Akadziyangʼana amachoka, nthawi yomweyo nʼkuyiwala mmene akuonekera.

Aliyense amene amachimwa amaphwanya lamulo; pakuti tchimo ndi kuphwanya lamulo.

Ana okondedwa, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.

Aliyense amene sasunga chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu. Koma amene amasunga chiphunzitsochi, ameneyo alinso ndi Atate ndi Mwana. Ngati wina aliyense abwera kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamulandire mʼnyumba mwanu kapena kumupatsa moni. Aliyense wolandira munthu wotere ndiye kuti akuvomerezana nazo ntchito zake zoyipa.

Komabe, ndili ndi zinthu zingapo zotsutsana nanu. Kumeneko muli ndi anthu ena amene amatsata ziphunzitso za Balaamu, uja amene anaphunzitsa Baraki kukopa Aisraeli kuti azidya nsembe zoperekedwa ku mafano ndi kumachita chigololo.

Komabe ndili ndi chinthu chokudzudzula nacho. Umamulekerera mkazi uja Yezebeli amene amadzitcha yekha kuti ndi mneneri. Iye amaphunzitsa atumiki anga kuti azichita zadama ndi kumadya zansembe zoperekedwa ku mafano. Ndamupatsa nthawi kuti aleke zachigololo zake koma sakufuna. Tsono ndidzamugwetsa mʼmasautso ndipo amene amachita naye zadama zakezo ndidzawasautsa kwambiri akapanda kulapa ndi kuleka njira za mkaziyo. Ana ake ndidzawakantha ndi kuwapheratu. Kotero mipingo yonse idzadziwa kuti Ine ndine uja amene ndimafufuza mʼmitima mwa anthu ndi mʼmaganizo mwawo. Aliyense wa inu ndidzachita naye monga mwa ntchito zake.

Anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi sanalapebe kuti asiye ntchito zawo zoyipa. Iwo sanasiye kupembedza ziwanda ndi mafano agolide, asiliva, amkuwa, amwala ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva kapena kuyankhula.

Koma amantha, osakhulupirira, okonda zonyansa, opha anthu, achiwerewere, amatsenga, opembedza mafano ndi abodza, malo awo adzakhala nyanja yamoto ya sulufule wotentha. Iyi ndi imfa yachiwiri.”

Chichewa - Chichewa - NY

NYCCL - Mawu A Mulungu Mu Chichewa Chalero - 2016

This Bible text is from Biblica Open God's Word In Contemporary Chichewa
https://open.bible/bibles/chichewa-biblica-text-bible/
provided by: Biblica Inc, available by Creative Commons CC-BY-SA-4.0,
and this new compilation is shared as www.creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0.
Languages are made available to you by www.ipedge.net