17 – Zipembedzo zabodza
Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Zipembedzo zabodza.
Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Zipembedzo zabodza.
Koma mafano awo ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo koma sayankhula, maso ali nawo koma sapenya; makutu ali nawo koma samva, mphuno ali nazo koma sanunkhiza; manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu; mapazi ali nawo koma sayenda; kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu. Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo, chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.
”“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.” “Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane.
”“ ‘Mwamuna kapena mkazi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena wanyanga pakati panu ayenera kuphedwa. Muwagende ndi miyala, ndipo magazi awo adzakhala pa mitu pawo.’ ”
”Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ”
”Kenaka anati, “Tiyeni tidzimangire mzinda wokhala ndi nsanja yoti ikafike kumwamba kuti titchuke. Kupanda kutero tibalalikana pa dziko lonse lapansi.” Koma Yehova anatsika kudzaona mzindawo ndi nsanja imene anthu aja ankayimanga. Yehova anati, “Anthuwa ndi amodzi, ndipo ali ndi chiyankhulo chimodzi. Izi akuchitazi nʼchiyambi chabe cha zomwe akufuna kukwaniritsa kuchita. Tiyeni titsikireko tikasokoneze chiyankhulo chawo kuti asamamvetsetsane.” Choncho Yehova anabalalitsa anthu aja pa dziko lonse lapansi ndipo analeka kumanga mzindawo. Nʼchifukwa chake mzindawo unatchedwa Babeli, popeza Yehova anasokoneza chiyankhulo cha anthu onse. Powachotsa kumeneko, Yehova anawabalalitsira pa dziko lonse lapansi.
”Mngelo wa Yehova uja anamuwuzanso kuti, “Ndiwe woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna. Udzamutcha dzina lake Ismaeli, pakuti Yehova wamva kulira chifukwa cha kuzunzika kwako. Iye adzakhala munthu wa khalidwe ngati mʼmbulu wamisala; adzadana ndi aliyense ndipo anthu onse adzadana naye, adzakhala mwaudani pakati pa abale ake onse.”
”Ndipo Abrahamu anati kwa Mulungu, “Bwanji mumudalitse Ismaeli.” Koma Mulungu anati, “Ayi, koma mkazi wako Sara adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha Isake. Ndidzasunga pangano langa losatha ndi iyeyu komanso ndi zidzukulu zobwera pambuyo pake. Koma za Ismaeli, ndamva. Ndidzamudalitsadi, ndipo adzakhala ndi zidzukulu zambiri. Iye adzakhala kholo la mafumu khumi ndi awiri ndipo mwa iye mudzatuluka mtundu waukulu wa anthu. Koma ndidzasunga pangano langali ndi Isake amene Sara adzakubalira pofika nthawi ngati ino chaka chamawa.”
”Tsono Abrahamu anachita mdulidwe mwana wake Ismaeli ndi onse amene anali mʼbanja lake, mbadwa ngakhale kapolo ochita kugula ndi ndalama, monga mmene Mulungu analamulira.
”Kotero Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kuchita monga momwe Yehova anawalamulira. Aaroni anaponya ndodo yake pansi patsogolo pa Farao ndi nduna zake ndipo inasanduka njoka. Naye Farao anayitanitsa anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo nawonso amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. Aliyense wa iwo anaponya ndodo yake pansi ndipo inasanduka njoka. Koma ndodo ya Aaroni inameza ndodo zawo. Koma mtima wa Farao unawuma ndipo sanawamvere monga momwe Yehova ananenera.
”Koma amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. Choncho Farao anawumabe mtima, ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananeneratu.
”Kotero Aaroni analoza dzanja lake pa madzi a ku Igupto, ndipo achule anatuluka nadzaza dziko lonse la Igupto. Koma amatsenga anachita zinthu zomwezo mʼmatsenga awo. Iwonso anatulutsa achule mʼdziko lonse la Igupto.
”Iwo anachita momwemo, ndipo pamene Aaroni anakweza ndodo yake ndi kumenya fumbi, nsabwe zinafika pa munthu aliyense ndi pa ziweto. Fumbi lonse la mʼdziko la Igupto linasanduka nsabwe. Koma amatsenga atayesa kupanga nsabwe mwa matsenga awo, analephera. Ndipo nsabwezo zinali pa munthu aliyense ndi pa ziweto zawo. Amatsenga anati kwa Farao, “Izi wachita ndi Mulungu.” Koma mtima wa Farao unali wowumabe ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananenera.
”Amatsenga sanathe kumuyandikira Mose chifukwa nawonso anali ndi zithupsa monga mmene analili Aigupto ena onse.
”“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.” “Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane.
”Choncho musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide kuti muziyipembedza pamodzi ndi Ine.’ ”
”“Musayilole mfiti yayikazi kuti ikhale ndi moyo.
”“Aliyense wopereka nsembe kwa mulungu wina osati Yehova awonongedwe.
”“Samalani pochita zonse zimene ine ndanena. Musamapemphere kwa milungu ina ndipo mayina awo musamawatchule.
”Anthu ataona kuti Mose akuchedwa kutsika mʼphiri, anasonkhana kwa Aaroni ndipo anati, “Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.” Aaroni anawayankha kuti, “Vulani ndolo zagolide zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi aakazi ndipo muzibweretse kwa ine.” Kotero anthu onse anavula ndolo zagolide ndi kubwera nazo kwa Aaroni. Choncho Aaroni analandira golideyo ndipo anamuwumba ndi chikombole ndi kupanga fano la mwana wangʼombe. Kenaka anthu aja anati, “Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.”
”Iwo apatuka mwamsanga kuleka kutsatira zimene ndinawalamula. Ndiye adzipangira fano la mwana wangʼombe. Aligwadira ndi kuliperekera nsembe nʼkumati, ‘Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ” Yehova anati kwa Mose, “Ine ndikuwadziwa anthu amenewa. Iwowa ndi ankhutukumve. Chifukwa chake undileke kuti mkwiyo wanga uyake pa iwo ndi kuwawononga. Ndipo Ine ndidzakusandutsa kuti ukhale mtundu waukulu.”
”Kotero Mose anabwereranso kwa Yehova ndipo anati, “Aa! Anthu awa achita tchimo lalikulu! Iwo adzipangira milungu yagolide.
”Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, ndipo mukadule mitengo yawo ya Asera. Musapembedze mulungu wina, pakuti Yehova amene dzina lake ndi Nsanje, ndi Mulungu wa nsanje. “Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa iwo akamakachita zadama ndi milungu yawo ndi kupereka nsembe, adzakuyitanani ndipo inu mudzadya nsembe zawo. Ndipo inu mukasankha ena mwa ana awo aakazi kukhala akazi a ana anu, akaziwo akakachita zadama ndi milungu yawo, akatsogolera ana anu aamuna kuchita chimodzimodzi. “Musadzipangire milungu yosungunula.
”Motero asadzapherenso nsembe fano la mbuzi limene amachita nalo zadama. Limeneli ndi lamulo la muyaya kwa iwo ndi mibado ya mʼtsogolo.’ ”
”“ ‘Musatembenukire ku mafano kapena kudzipangira nokha milungu ya zitsulo zosungunula. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
”“ ‘Musadye nyama ya magazi. “ ‘Musamawombeze kapena kuchita zamatsenga.
”“ ‘Musadzichekecheke pathupi panu chifukwa cha munthu wakufa kapena kudzitema mphini pa thupi lanu. Ine ndine Yehova.
”“ ‘Musamapite kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena kwa owombeza. Musamawafunefune kuti angakuyipitseni. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
”“Uza Aisraeli kuti, ‘Mwisraeli aliyense kapena mlendo aliyense wokhala mu Israeli wopereka mwana wake kwa Moleki ayenera kuphedwa. Anthu a mʼdera lakelo amuphe ndi miyala. Munthu ameneyo ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anzake.’ Popereka mwana wake kwa Moleki, wadetsa malo anga wopatulika ndi kuyipitsa dzina langa loyera.
”“ ‘Ngati munthu adzapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena kwa owombeza, nadziyipitsa powatsatira iwowo, Ine ndidzamufulatira ndi kumuchotsa pakati pa anthu anzake.
”“ ‘Mwamuna kapena mkazi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa kapena wanyanga pakati panu ayenera kuphedwa. Muwagende ndi miyala, ndipo magazi awo adzakhala pa mitu pawo.’ ”
”“ ‘Musadzipangire mafano ndipo musayimike chifanizo chosema kapena mwala woti mudzipembedza. Musayike mwala wosema mʼdziko mwanu kuti muziwugwadira. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
”Ine ndidzawononga malo anu opembedzera mafano a ku mapiri. Ndidzagwetsa maguwa anu ofukizira lubani, ndipo ndidzawunjika pamodzi mitembo ya mafano anu wopanda moyowo, ndipo ndidzanyansidwa nanu.
”mukathamangitse nzika zonse za mʼdzikomo pamaso panu. Mukawononge mafano awo onse a miyala ndi osula ndi malo awo achipembedzo.
”Tsiku limene Yehova anayankhula nanu ku Horebu mʼmoto uja, simunaone thupi lake. Choncho mudziyangʼanire nokha mosamalitsa, kuti musasokonezeke ndi kudzipangira nokha fano kapena chifanizo cha mtundu uliwonse, kaya chokhala ngati mwamuna kapena ngati mkazi, kaya chokhala ngati nyama iliyonse ya pa dziko lapansi kapena mbalame iliyonse yowuluka mlengalenga. Kapena cholengedwa chilichonse choyenda pa nthaka kapena nsomba ya mʼmadzi akuya. Ndipo pamene muyangʼana kumwamba muona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, zonse zakumwambazo musakopeke kuti muzigwadire ndi kumapembedza zinthu zimene Yehova wapereka kwa anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi.
”Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi moto wonyeketsa ndipo ndi Mulungu wansanje.
”“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha. “Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane,
”Musamatsatire milungu ina, milungu ya anthu ena okuzungulirani, pakuti Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu, ndi Mulungu wansanje ndipo adzakukwiyirani kwambiri ndi kukuwonongani, kukufafanizani mʼdziko.
”Musadzakwatirane nawo. Musadzapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna kapena kutenga ana anu aamuna ndi kuwapereka kwa ana awo aakazi. Mukadzatero, iwo adzasocheretsa ana anu aamuna kuti asanditsatire ndi kutumikira milungu ina. Motero Yehova adzakukwiyirani ndi kukuwonongani mwachangu. Koma mukachite izi: Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, mukadule mitengo yawo ya Asera, ndi kutentha mafano awo pa moto.
”Muwonongeretu kwathunthu malo onse a pamwamba pa mapiri ataliatali ndi pa mapiri angʼonoangʼono ndi pansi pa mtengo uliwonse wotambalala pamene mitundu imene muyilande dzikolo ankapembedzerapo milungu yawo. Mugumule maguwa awo ansembe, ndi kuphwanya miyala yawo yachipembedzo ndipo mutenthe pa moto mafano awo a Asera: mugwetse mafano a milungu yawo ndi kufafaniza mayina awo mʼmalo amenewo. Musapembedze Yehova Mulungu wanu monga mmene amachitira iwowa.
”ndipo pamene iwo awonongeka pamaso panu, samalirani kuti musakodwe mu msampha pa kufufuza za milungu yawo, nʼkumati, “Kodi anthu a mitunduwa amatumikira bwanji milungu yawo? Ifenso tichita momwemo.” Musapembedze Yehova Mulungu wanu momwe amachitira iwowo, chifukwa popembedza milungu yawoyo amachita zonyansa zamitundumitundu zimene Yehova amadana nazo. Amatentha ngakhale ana awo aamuna ndi aakazi pa moto ngati nsembe za kwa milungu yawo.
”Ngati mneneri kapena wina aliyense amene amanena zamʼtsogolo mwa maloto atuluka pakati panu, nalengeza za chizindikiro chozizwitsa kapena chodabwitsa, chinthu nʼkuchitikadi, tsono iyeyo nʼkunena kuti, “Tiyeni titsatire milungu ina, tiyeni tiyipembedze,” (kunena milungu imene simunayidziwe), musamumvere mneneriyo kapena wolotayo. Yehova Mulungu wanu afuna akuyeseni kuti aone ngati mumamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
”Ngati mʼbale wanu weniweni kapena mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi, kapena mkazi wanu wokondedwa, kapena mnzanu wapamtima akukakamizani mwachinsinsi, nʼkumati, “Tiyeni tipite tikapembedze milungu ina” (milungu imene inuyo kapena makolo anu sanayidziwe, milungu ya anthu okuzungulirani, kaya ndi apafupi kapena akutali, kuchokera kumapeto mpaka kumapeto kwina kwa dziko lapansi), musamugonjere kapena kumumvera. Musamumvere chisoni. Musamuleke kapena kumutchinjiriza.
”ndipo ngati motsutsana ndi lamulo langa wapembedza milungu ina, kuyigwadira milunguyo, kaya ndi dzuwa kapena mwezi kapena nyenyezi zakumwamba, ndipo inu nʼkuwuzidwa zimenezi, mufufuze bwinobwino. Ngati ndi zoona, ndipo ngati zatsimikizika kuti chonyansa choterechi chachitikadi mu Israeli, mumutengere mwamuna kapena mkazi amene wachita chonyansa choterechi ku chipata cha mzinda wanu ndi kumupha pomugenda miyala.
”Pasapezeke pakati panu munthu wootcha pa moto mwana wake wamwamuna kapena wamkazi ngati nsembe. Asapezekenso pakati panu munthu wowombeza kapena wochita mawula, wolosera, wochita za ufiti, wolodza, kapena woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ndi kumafunsira nzeru kwa anthu akufawo. Aliyense wochita zinthu zotere ndi wonyansa pamaso pa Yehova, ndipo chifukwa cha zonyansa zimenezi Yehova adzakupirikitsirani mitundu ya anthu imeneyi.
”Koma mneneri wonena zinthu mʼdzina langa ndisanamulamulire kutero, kapena mneneri wonenera mʼdzina la milungu ina, ayenera kuphedwa.”
”“Ndi wotembereredwa munthu amene asema chifanizo kapena kupanga fano, ndi kuchiyika mobisa, pakuti chimenechi ndi chinthu chodetsedwa pamaso pa Yehova, ntchito za manja a anthu.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
”Anamuchititsa nsanje ndi milungu yawo yachilendo ndiponso anamukwiyitsa ndi mafano awo onyansa. Anapereka nsembe kwa ziwanda zimene si Mulungu, milungu imene sankayidziwa nʼkale lomwe, milungu yongobwera kumene, milungu imene makolo anu sankayiopa.
”Anandichititsa kukhala wansanje pamene ankapembedza chimene si mulungu ndi kundikwiyitsa chifukwa cha mafano awo achabechabe. Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake; ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.
”Komabe iwo sanawamvere atsogoleri awowo popeza ankapembedza milungu ina ndi kumayigwadira. Iwo anapatuka msangamsanga mu njira imene ankayendamo makolo awo. Iwo aja ankamvera malamulo a Yehova, koma mʼbado uwu ayi.
”Koma nthawi zonse mtsogoleri akamwalira, Aisraeli ankabwerera mʼmbuyo. Iwo amadzisandutsa oyipa kupambana makolo awo popeza ankatsata milungu ina, kuyitumikira ndi kumayigwadira. Anakana kusiya makhalidwe awo oyipa ndi njira zawo zamakani.
”Aisraeli anachitanso zoyipira Yehova. Iwo anatumikira Abaala ndi Asitoreti, milungu ya ku Aramu, Sidoni, Mowabu, Aamoni ndi Afilisti. Choncho analeka osatumikiranso Yehova. Tsono Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa Afilisti ndi Aamoni.
”Kenaka Aisraeli analira kwa Yehova kuti, “Ife takuchimwirani popeza tasiya Inu Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala.”
”Komabe inu mwandikana ndipo mukutumikira milungu ina. Choncho sindidzakupulumutsaninso. Pitani kalireni kwa milungu imene mwayisankha. Iyoyo ikupulumutseni ku mavuto anuwo.” Koma Aisraeli anayankha Yehova kuti, “Ife tachimwa. Tichitireni chimene mukuona kuti ndi chabwino, koma chonde tipulumutseni lero lokha.” Ndipo anachotsa milungu ya chilendo pakati pawo ndi kuyamba kutumikira Yehova. Ndipo Yehova anamva chisoni poona mmene Aisraeli ankazunzikira.
”Kenaka anatenga Bokosi la Chipanganolo nabwera nalo ku nyumba ya Dagoni ndi kuliyika pambali pa Dagoni. Anthu a ku Asidodi atadzuka mmawa mwake, anangoona Dagoni atagwa pansi chafufumimba pamaso pa Bokosi la Yehova! Iwo anatenga Dagoni ndi kumuyimika pamalo pake. Koma mmawa mwakenso atadzuka, anaona Dagoni atagwa chafufumimba pamaso pa Bokosi la Yehova. Mutu wake ndi manja ake zinali zitaduka ndi kugwera pa khonde polowera, thunthu lake lokha ndilo linatsala. Nʼchifukwa chake mpaka lero ansembe a Dagoni kapena wina aliyense amene amalowa mʼkachisi wa Dagoni ku Asidodi saponda pa khonde. Yehova analanga koopsa anthu a ku Asidodi. Yehova anawawononga ndi kuwazunza ndi zithupsa Asidoniwa pamodzi ndi anthu a madera ozungulira. Anthu a ku Asidodi ataona zimene zimachitika anati, “Bokosi la Mulungu wa Israeli lisakhale kuno chifukwa akutizunza ife pamodzi ndi mulungu wathu Dagoni.”
”Pakuti kuwukira kuli ngati tchimo lowombeza, ndipo kukhala nkhutukumve kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Chifukwa mwakana mawu a Yehova. Iyenso wakukana kuti iweyo ukhale mfumu.”
”Nthawi imeneyi nʼkuti Samueli atamwalira, ndipo Aisraeli onse anamulira namuyika mʼmanda ku mzinda wake wa Rama. Sauli anali atachotsa mʼdzikomo anthu owombeza mawula ndi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa.
”Kenaka Sauli anawuza nduna zake kuti, “Mundipezere mkazi amene amawombeza mawula kuti ndipite ndikafunse kwa iye.” Nduna zakezo zinamuyankha kuti, “Alipo mkazi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ku Endori.” Kotero Sauli anadzizimbayitsa navala zovala zachilendo. Tsono iye pamodzi ndi anthu awiri anapita nakafika kwa mkazi uja usiku, ndipo anamupempha kuti, “Chonde ndifunsireni nzeru kwa mizimu ya anthu akufa. Koma makamaka munditulutsire mzimu wa amene ndimutchule.” Koma mkaziyo anayankha kuti, “Ndithu inu mukudziwa chimene Sauli anachita. Paja iye anachotsa mʼdziko muno anthu onse owombeza ndi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Chifukwa chiyani mukutchera moyo wanga msampha kuti ndiphedwe?”
”Solomoni atakalamba, akazi akewo anakopa mtima wake kuti atsatire milungu ina, ndipo sanatsatire Yehova Mulungu wake ndi mtima wodzipereka, monga unalili mtima wa Davide abambo ake. Pakuti iye ankapembedza Asitoreti, mulungu wamkazi wa Asidoni, ndiponso Moleki mulungu wonyansa wa Aamoni. Kotero Solomoni anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Sanatsatire Yehova kwathunthu monga anachitira Davide abambo ake. Pa phiri la kummawa kwa Yerusalemu, anamanga malo opembedzerapo Kemosi, mulungu wonyansa wa Mowabu, ndiponso malo a Moleki, mulungu wonyansa wa Aamoni. Iye anamangiranso malo oterewa akazi ake onse achilendo, amene amafukiza lubani ndi kumapereka nsembe kwa milungu yawo.
”Ndidzachita zimenezi chifukwa wandisiya Ine ndi kupembedza Asitoreti mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi mulungu wa Amowabu ndiponso Moleki mulungu wa Aamoni, ndipo sanayende mʼnjira yanga, kapena kusunga mawu anga ndi malamulo anga monga anachitira Davide abambo ake.
”Itapempha nzeru, mfumuyo inapanga mafano awiri a ana angʼombe. Mfumuyo inati kwa anthuwo, “Mwakhala mukupita ku Yerusalemu nthawi yayitali. Iwe Israeli, nayi milungu yako imene inakutulutsa mʼdziko la Igupto.”
”Iwonso anadzipangira malo opembedzerapo mafano pa chitunda chilichonse ndi kuyimika miyala ya chipembedzo ndi mitengo ya Asera pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri. Mʼdzikomo munalinso amuna ochita zachiwerewere mwa chipembedzo. Anthu ankachita zonyansa zonse za anthu a mitundu ina imene Yehova anayipirikitsa asanafike Aisraeli.
”Eliya anapita patsogolo pa anthuwo ndipo anati, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iwiri mpaka liti? Ngati Yehova ndi Mulungu, mutsateni; koma ngati Baala ndi Mulungu, mutsateni.” Koma anthu aja sanayankhe. Pamenepo Eliya ananena kwa iwo kuti, “Ine ndilipo ndekha mneneri wa Yehova, koma Baala ali ndi aneneri 450. Tibweretsereni ngʼombe zazimuna ziwiri. Iwo asankhepo okha ngʼombe imodzi, ndipo ayidule nthulinthuli ndi kuziyika pa nkhuni nthulizo, koma osakolezapo moto. Ndipo ine ndidzadula nthulinthuli ngʼombe inayo ndi kuyika pa nkhuni koma sindikolezapo moto. Kenaka inu muyitane dzina la mulungu wanu, ndipo ine ndidzayitana dzina la Yehova. Mulungu amene ati ayankhe potumiza moto, iyeyo ndiye Mulungu.” Pamenepo anthu onse anati, “Izi mwanena zamveka bwino.”
”Eliya anawuza aneneri a Baala kuti, “Yambani ndinu. Sankhani ngʼombe yayimuna imodzi, muyikonze, popeza mulipo ambiri. Muyitane dzina la mulungu wanu, koma musakoleze moto.” Choncho iwo anatenga ngʼombe yayimunayo imene anawapatsa, nayikonza. Kenaka anayitana dzina la Baala kuyambira mmawa mpaka masana. Iwo anafuwula kuti, “Inu Baala, tiyankheni ife.” Koma panalibe yankho; palibe amene anayankha. Ndipo anavinavina mozungulira guwa lansembe limene anapanga. Nthawi yamasana Eliya anayamba kuwanyogodola ndipo anati, “Fuwulani kwambiri. Ndithudi, iye ndi mulungu! Mwinatu akulingalira kwambiri, kapena watanganidwa, kapena ali paulendo. Mwina wagona ndipo nʼkofunika kuti adzutsidwe.” Choncho iwo anafuwula kwambiri ndi kudzichekacheka ndi malupanga ndi mikondo, potsata miyambo yawo, mpaka kutuluka magazi. Nthawi yamasana inadutsa, ndipo anapitiriza kunenera mwakhama mpaka nthawi yopereka nsembe ya madzulo. Koma panalibe yankho. Palibe amene anayankha, kapena kulabadira zimenezo.
”Pamenepo Eliya anati kwa anthu onse, “Senderani pafupi ndi ine.” Ndipo anthu onsewo anasendera pafupi ndi iye, ndipo iye anakonza guwa lansembe la Yehova limene linali litawonongeka. Eliya anatenga miyala 12, mwala uliwonse kuyimira fuko lililonse la Yakobo, amene Yehova anamuwuza kuti, “Dzina lako lidzakhala Israeli.” Ndi miyala imeneyo anamanga guwa mʼdzina la Yehova, ndipo anakumba ngalande yayikulu yolowa malita 15 a madzi kuzungulira guwalo. Anayika nkhuni zija mʼmalo mwake nadula nthulinthuli ngʼombe yayimuna ija ndi kuyika nthulizo pa nkhunipo. Pamenepo Eliya anati, “Dzazani mitsuko inayi ndi madzi ndipo muwathire pa nyama ya nsembeyo ndi nkhunizo.” Eliya anati, “Thiraninso kachiwiri.” Anthu aja anathiranso madziwo kachiwiri. Iye analamula kuti, “Thiraninso kachitatu.” Ndipo iwo anathiranso kachitatu. Madziwo anayenderera pansi kuzungulira guwa lansembe, nadzaza ngalande yonse.
”Pa nthawi yopereka nsembe, mneneri Eliya anasendera pafupi ndi guwa lansembe, napemphera kuti, “Inu Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, lero zidziwike kuti ndinu Mulungu mu Israeli ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, kuti ine ndachita zonsezi chifukwa mwalamula ndinu. Ndiyankheni, Inu Yehova, ndiyankheni, kuti anthu awa adziwe Inu Yehova, kuti ndinu Mulungu, ndipo kuti mutembenuziranso mitima yawo kwa Inu.” Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nunyeketsa nsembe yopserezayo, nkhuni, miyala ndi dothi lomwe. Unawumitsanso madzi amene anali mʼngalande. Anthu onse ataona zimenezi, anaweramitsa nkhope zawo pansi, nafuwula kuti, “Yehova ndiye Mulungu! Yehova ndiye Mulungu!” Pamenepo Eliya analamula anthuwo kuti, “Gwirani aneneri a Baala. Musalole kuti wina aliyense athawe!” Anagwira onsewo ndipo Eliya anabwera nawo ku Chigwa cha Kisoni, nawapha kumeneko.
”Iye anachita zonyansa kwambiri popembedza mafano, monga mmene ankachitira Aamori amene Yehova anawachotsa pamene Aisraeli ankafika).
”Yoramu ataona Yehu anafunsa kuti, “Yehu, kodi wabwera mwamtendere?” Yehu anayankha kuti, “Pangakhale bwanji mtendere pamene zopembedza mafano zonse zilipo ndiponso ufiti wa amayi ako Yezebeli uli ponseponse?”
”Iwo anakatulutsa mwala wopatulika umene unali mʼnyumba ya Baala ndipo anawutentha. Anawononga mwala wopatulika wa Baala ndi kugwetsa nyumba ya Baala, ndipo anthu anayisandutsa chimbudzi mpaka lero lino.
”Pa malo aliwonse opembedzera mafano, anthuwa ankafukiza lubani monga momwe ankachitira anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika. Iwo anachita zinthu zoyipa zomwe zinaputa mkwiyo wa Yehova. Ndipo iwowo ankapembedza mafano ngakhale Yehova ananena kuti, “Musadzachite zimenezi.”
”Koma anthuwa sanamvere ndipo anawumitsa khosi ngati momwe analili makolo awo, amene sanadalire Yehova Mulungu wawo. Anakana malangizo ake ndi pangano anachita ndi makolo awo ndipo ananyoza zochenjeza za Yehova. Iwo anatsatira mafano achabechabe nasanduka achabechabe. Anthuwa anatsanzira mitundu ya anthu owazungulira ngakhale kuti Yehova anawalamula kuti, “Musamachite zomwe iwo amachita,” koma iwo anachita zomwe Yehova anawaletsa. Iwowo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wawo, nadzipangira mafano awiri osungunula a ana angʼombe ndiponso fano la Asera, napembedza zonse zamlengalenga ndi kutumikira Baala. Ndipo anadutsitsa mʼmoto ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo ankawombeza mawula, namachitanso zanyanga ndipo anadzipereka kuchita zoyipa pamaso pa Yehova namukwiyitsa. Choncho Yehova anakwiya nawo kwambiri Aisraeli ndipo anawachotsa pamaso pake. Palibe amene anatsala kupatula fuko la Yuda lokha.
”Koma mtundu uliwonse wa anthu unkapangabe mafano a milungu yawoyawo mʼmizinda yambiri imene anthuwo ankakhala, ndipo anayika milunguyo mʼnyumba za milungu zimene anthu a ku Samariya anamanga ku malo opembedzera mafano.
”Iwowo ankapembedza Yehova, komanso ankatumikira milungu yawo molingana ndi miyambo ya mitundu ya kumene ankachokera. Mpaka lero lino iwo akupitirizabe kuchita zimene ankachita poyamba. Sapembedza Yehova kapenanso kutsata malangizo ake ndi malamulo ake, chiphunzitso chake monga mwa malamulo amene Yehova anawapereka kwa zidzukulu za Yakobo, amene anamutcha Israeli. Pamene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli, Iye anawalamula kuti, “Musapembedze milungu ina kapena kuyigwadira iyo, kuyitumikira kapena kupereka nsembe kwa iyoyo.
”Anachotsa malo opembedzerako mafano, anaphwanya miyala yachipembedzo ndiponso anadula mafano a Asera. Iye anaphwanya njoka yamkuwa imene Mose anapanga, pakuti mpaka kufikira nthawi imeneyi Aisraeli amafukiza lubani kwa njoka imeneyi. (Imatchedwa Nehusitani).
”“Inu Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu iyi ndi mayiko awo. Iwo anaponya milungu yawo pa moto ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mitengo ndi miyala chabe, yopangidwa ndi anthu.
”Iye anapsereza mwana wake pa moto ngati nsembe, ankachita za matsenga, ankawombeza mawula, ankapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ndiponso ankapembedza mizimu. Iyeyo anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova ndipo anakwiyitsa Yehovayo.
”“Manase mfumu ya Yuda wachita machimo onyansawa ndipo wachita zoyipa kupambana Aamori amene analipo kale iye asanabadwe ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda ndi mafano ake. Choncho Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taonani, ndikubweretsa pa Yerusalemu ndi Yuda mavuto akuti aliyense amene adzawamve adzathedwa nzeru.
”Anatsatira makhalidwe onse a abambo ake. Ankapembedza mafano amene abambo akewo ankawapembedza ndipo ankawagwadira.
”Iye anachotsa ansembe a mafano amene anayikidwa ndi mafumu a Yuda kuti azifukiza lubani ku malo opembedzera mafano a ku mizinda ya ku Yuda ndi kumalo ozungulira Yerusalemu, amene ankafukiza lubani kwa Baala, dzuwa, mwezi, nyenyezi ndi zinthu zonse zamlengalenga. Anachotsa fano la Asera mʼNyumba ya Yehova napita nalo kunja kwa Yerusalemu, ku Chigwa cha Kidroni, nalitentha kumeneko. Anapera fanolo ndi kukataya phulusa lake pa manda a anthu wamba. Iye anagwetsanso tinyumba ta ochita zachiwerewere, timene tinali mʼNyumba ya Yehova, kumene akazi ankalukirako mikanjo yovala popembedza Asera. Yosiya anabweretsanso ansembe onse kuchokera mʼmizinda ya Yuda, nawononga malo opembedzera mafano, kuyambira ku Geba mpaka ku Beeriseba, kumene ansembe ankafukizako lubani. Anagwetsa nyumba za milungu zimene zinali pa chipata cha Yoswa, bwanamkubwa wa mzindawo, kumanzere kwa chipata cha mzinda.
”Kuwonjezera apa, Yosiya anachotsa anthu a mawula, woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, milungu ya mʼnyumba, mafano ndiponso zinthu zonse zonyansa zopezeka mu Yuda ndi Yerusalemu. Iye anachita izi pokwaniritsa lamulo lolembedwa mʼbuku limene Hilikiya analipeza mʼNyumba ya Yehova.
”Sauli anafa chifukwa anali wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Iye sanasunge mawu a Yehova, pakuti anakafunsira nzeru kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa,
”Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano wopanda pake, koma Yehova analenga kumwamba.
”Ndipo iye anasankha ansembe akeake a pa malo opatulika ndi a mafano a mbuzi ndi mwana wangʼombe amene anapanga.
”Iye anachotsa maguwa achilendo ndi malo opembedzerapo mafano, anaphwanya zipilala za miyala yachipembedzo ndi kugwetsa mafano a Asera.
”Iwo anasiya Nyumba ya Yehova, Mulungu wa makolo awo ndipo anapembedza Asera ndi mafano. Chifukwa cha kulakwa kwawo, mkwiyo wa Yehova unabwera pa Yuda ndi Yerusalemu.
”Ahazi ankapereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko, imene inamugonjetsa. Iye ankaganiza kuti, “Popeza milungu ya mafumu a Aaramu yawathandiza, ine ndidzapereka nsembe kwa iyo kuti indithandize.” Koma iyoyo inakhala kugwa kwake ndi kugwa kwa Aisraeli onse. Ahazi anasonkhanitsa pamodzi zinthu zonse kuchokera mʼNyumba ya Mulungu ndipo anazitenga. Iye anatseka zitseko za Nyumba ya Yehova ndipo anayimika maguwa ansembe pa ngodya iliyonse ya msewu mu Yerusalemu. Mu mzinda uliwonse wa Yuda anamangamo malo achipembedzo, operekerapo nsembe zopsereza kwa milungu ina ndipo anaputa mkwiyo wa Yehova, Mulungu wa makolo ake.
”Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, potsatira machitidwe a mitundu imene Yehova anayithamangitsa pamaso pa Aisraeli. Iyeyo anamanganso malo opembedzerapo mafano amene Hezekiya abambo ake anawaphwasula; anamanganso maguwa ansembe a Baala ndi kupanga mafano a Asera. Iye amagwadira zolengedwa zonse zamlengalenga ndi kumazipembedza.
”Iye ankakapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza ku chigwa cha Hinomu, ankachita zamatsenga, kuwombeza ndi ufiti, ankakafunsira kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Iye anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova, kumukwiyitsa Iyeyo. Manase anatenga fano losema limene anapanga ndi kuliyika mʼNyumba ya Mulungu, zimene Mulungu ananena kwa Davide ndi kwa mwana wake Solomoni kuti, “Mʼnyumba ya Mulungu muno, mu Yerusalemu muno, malo amene ndawasankha pakati pa mafuko onse a Israeli, ndidzakhalamo mpaka muyaya.
”Anthu amene amathamangira kwa milungu ina mavuto awo adzachulukadi. Ine sindidzathira nawo nsembe zawo zamagazi kapena kutchula mayina awo ndi pakamwa panga.
”Anakwiyitsa Iyeyo ndi malo awo opembedzera mafano; anawutsa nsanje yake ndi mafano awo. Pamene Mulungu anamva zimenezi, anakwiya kwambiri; Iye anakana Israeli kwathunthu.
”Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano, koma Yehova analenga mayiko akumwamba.
”Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi, iwo amene amanyadira mafano; mulambireni, inu milungu yonse!
”Ndipo anapembedza mafano awo, amene anakhala msampha kwa iwowo. Anapereka nsembe ana awo aamuna ndi ana awo aakazi kwa ziwanda. Anakhetsa magazi a anthu osalakwa, magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi, amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanaani, ndipo dziko linayipitsidwa ndi magazi awo.
”Koma mafano awo ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo koma sayankhula, maso ali nawo koma sapenya; makutu ali nawo koma samva, mphuno ali nazo koma sanunkhiza; manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu; mapazi ali nawo koma sayenda; kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu. Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo, chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.
”Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo koma sayankhula maso ali nawo, koma sapenya; makutu ali nawo, koma sakumva ndipo mʼkamwa mwawo mulibe mpweya uliwonse. Iwo amene amapanga mafanowo adzakhala ngati mafanowo, chimodzimodzinso iwo amene amadalira mafanowo.
”Inu Yehova mwawakana anthu anu, nyumba ya Yakobo. Iwo adzaza ndi zamatsenga zochokera Kummawa; amawombeza mawula ngati Afilisti, ndipo amayanjana ndi anthu osapembedza Mulungu.
”Dziko lawo ndi lodzaza ndi mafano; iwo amapembedza ntchito ya manja awo, amagwadira zomwe anapanga ndi zala zawo.
”Tsiku limenelo anthu adzatayira mfuko ndi mileme mafano awo asiliva ndi mafano awo agolide, amene anawapanga kuti aziwapembedza.
”Anthu akakuwuza kuti kafunsire kwa oyankhula ndi mizimu, amene amayankhula monongʼona ndi mongʼungʼudza, kodi anthu sayenera kukafunsira kwa Mulungu wawo? Chifukwa chiyani amafunsira kwa anthu akufa mʼmalo mwa kwa anthu amoyo, kuti akalandireko mawu enieni ndi malangizo? Ngati anthuwo sayankhula monga mwa mawu awa, mwa iwo mulibe kuwala.
”Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mʼbandakucha! Wagwetsedwa pansi pa dziko lapansi, Iwe amene unagonjetsapo mitundu ya anthu! Mu mtima mwako unkanena kuti, “Ndidzakwera mpaka kumwamba; ndidzakhazika mpando wanga waufumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pa mpando waufumu pa phiri losonkhanirako, pamwamba penipeni pa phiri la kumpoto. Ndidzakwera pamwamba pa mitambo; ndidzafanana ndi Wammwambamwamba.” Koma watsitsidwa mʼmanda pansi penipeni pa dzenje.
”Aigupto adzataya mtima popeza ndidzalepheretsa zolinga zawo; adzapempha nzeru kwa mafano awo ndiponso kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kwa amawula ndi kwa oyankhula ndi mizimu.
”Pamenepo mudzawononga mafano anu okutidwa ndi siliva ndiponso zifanizo zanu zokutidwa ndi golide; mudzawataya ngati zinthu zonyansa ndipo mudzati, “Zichoke zonsezi!”
”Pakuti tsiku limenelo nonsenu mudzataya mafano anu a siliva ndi golide amene mumapanga ndi manja anu auchimo.
”“Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo! Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense kapena matamando anga kwa mafano.
”Koma onse amene amadalira mafano amene amanena kwa mafanowo kuti, ‘ndinu milungu yathu,’ ndidzawachititsa manyazi kotheratu.
”Yehova akunena kuti, “Inu Aisraeli ndinu mboni zanga, ndi mtumiki wanga amene ndinakusankha, kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira, ndipo mudzamvetsa kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipanapangidwepo mulungu wina, ngakhale pambuyo panga sipadzakhalaponso wina.”
”“Yehova Mfumu ndi Mpulumutsi wa Israeli, Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndine woyamba ndi wotsiriza; palibenso Mulungu wina koma Ine ndekha.
”Onse amene amapanga mafano ngachabe, ndipo milungu imene amayilemekeza ndi yopanda phindu. Iwo amene amapembedza mafano ndi wosaona; ndipo sazindikira kanthu. Choncho adzawachititsa manyazi. Ndani amasema mulungu ndi kuwumba fano, limene silingamupindulire? Iye pamodzi ndi anzake onse adzawachititsa manyazi; amisiri a mafano ndi anthu chabe. Aloleni onse asonkhane ndi kuyima pabwalo la milandu; onse adzaopsedwa ndipo adzachita manyazi. Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulo ndipo amachiyika pa makala amoto; ndi dzanja lake lamphamvu amachisula pochimenya ndi nyundo. Pambuyo pake mʼmisiri uja amamva njala natha mphamvu; iye samwa madzi, ndipo amalefuka. Mmisiri wa matabwa nayenso amayeza mtengo ndi chingwe ndipo amajambula chithunzi ndi cholembera; amasema bwinobwino ndi chipangizo chake ndipo amachiwongola bwino ndi chida chake. Amachipanga ngati munthu, munthu wake wokongola kuti aliyike mʼnyumba yake yachipembedzo. Amagwetsa mitengo ya mkungudza, mwinanso amatenga mtengo wa payini kapena wa thundu nʼkudzisankhira mtengo wabwino pakati pa mitengo ya mʼnkhalango, ndipo amadzala mtengo wa payini ndi kuwuleka kuti ukule ndi mvula. Mitengoyo munthu amachitako nkhuni; nthambi zina amasonkhera moto wowotha, amakolezera moto wophikira buledi ndi mbali ina ya mtengowo amapangira mulungu ndipo amapembedza; iye amapanga fano ndi kumaligwadira.
”Chigawo chotsala amapanga kamulungu, fano lake limenelo; amaligwadira ndi kulipembedza. Amapemphera kwa fanolo ndipo amanena kuti, “Iwe ndiwe mulungu wanga, ndipulumutse.” Anthu otere sadziwa kanthu, samvetsa kanthu kalikonse; maso awo ndi omatirira ndipo sangathe kuona, ndipo mitu yawo ndi yogontha kotero sangathe kumvetsa.
”Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina; kupatula Ine palibenso Mulungu wina. Ndidzakupatsa mphamvu, ngakhale sukundidziwa Ine,
”Yehova akuti, “Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere; yandikirani, inu amene munapulumuka pothawa nkhondo kwa anthu a mitundu ina. Ndinu opanda nzeru amene mumanyamula mafano a mitengo, amene mumapemphera kwa milungu imene singathe kupulumutsa.
”Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo ndipo amayeza siliva pa masikelo; amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu, kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko. Amanyamula nʼkumayenda nayo milunguyo pa mapewa awo; amayikhazika pa malo pake ndipo imakhala pomwepo. Singathe kusuntha pamalo pakepo. Ngakhale wina apemphere kwa milunguyo singathe kuyankha; kapena kumupulumutsa ku mavuto ake.
”“Pitiriza tsono kukhala ndi matsenga ako, pamodzi ndi nyanga zako zochulukazo, wakhala ukuzigwiritsa ntchito kuyambira ubwana wako. Mwina udzatha kupambana kapena kuopsezera nazo adani ako. Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi! Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni. Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi zimene ziti zidzakuchitikire. Ndithudi, anthuwo ali ngati phesi; adzapsa ndi moto. Sangathe kudzipulumutsa okha ku mphamvu ya malawi a moto. Awa si makala a moto woti wina nʼkuwotha; kapena moto woti wina nʼkuwukhalira pafupi. Umu ndi mmene adzachitire amatsenga, anthu amene wakhala ukugwira nawo ntchito ndi kuchita nawo malonda chiyambire cha ubwana wako. Onse adzamwazika ndi mantha, sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”
”“Kodi inu muziba ndi kupha, kuchita chigololo ndi kulumbira monama, kufukiza lubani kwa Baala ndi kutsatira milungu ina imene simunayidziwe, ndipo kenaka nʼkubwera kudzayima pamaso panga mʼNyumba ino, Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langa, inu nʼkumati, ‘Tapulumuka.’ Mwapulumuka kuti muzichitabe zonyansazi? Kodi Nyumba ino imene imadziwika ndi Dzina langa, yasanduka phanga la anthu olanda zinthu anzawo mwachifwamba inu mukuona? Komatu ndakhala ndi kuziona zonsezi! akutero Yehova.”
”Ana akutorera nkhuni, abambo akusonkha moto, ndipo amayi akukanda ufa kuti aphike makeke oti akapereke nsembe kwa mfumukazi yazakumwamba. Iwo amathira nsembe ya zakumwa kwa milungu ina kuti andipsetse mtima.
”Adzawamwaza pa nthaka kuyangʼana dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zonse zamlengalenga, zimene ankazikonda, kuzitumikira ndi kuzitsatira, kupemphako nzeru ndiponso kuzilambira. Mafupawo sadzawasonkhanitsa kapena kuwakwirira, koma adzakhala ngati ndowe pamwamba pa nthaka.
”Pakuti miyambo ya mitundu inayo ndiyachabechabe. Iwo amakadula mtengo ku nkhalango ndipo mmisiri amawusema ndi sompho. Amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide; kenaka amachikhomerera ndi misomali kuti chisagwedezeke. Mafano awo ali ngati mtengo wakanjedza woopsezera mbalame mʼmunda wa minkhaka. Mafanowo sangathe nʼkuyankhula komwe ndipo ayenera kunyamulidwa popeza sangathe nʼkuyenda komwe. Musachite nawo mantha popeza sangathe kukuchitani choyipa ndiponso alibe mphamvu yochitira chabwino chilichonse.”
”“Awuze anthu awa kuti, ‘Milungu iyi, imene sinalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzawonongeka pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.’ ”
”Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru; mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake. Mafano akewo ndi abodza; alibe moyo mʼkati mwawo. Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo. Pamene anthuwo azidzaweruzidwa, mafanowo adzawonongedwa.
”Anthuwa ndi oyipa. Iwo akana kumvera mawu anga. Mʼmalo mwake amawumirira kutsata milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Anthu amenewa adzakhala ngati lamba wopanda ntchitoyu.
”Kodi anthu nʼkudzipangira milungu? Atati atero ndiye kuti imeneyo ikhala milungu yachabechabe.”
”Pakuti anthu andikana Ine ndipo ayipitsa malo ano. Afukiza lubani pa malo ano kwa milungu imene iwo ngakhale makolo awo ngakhalenso mafumu a ku Yuda sanayidziwe. Iwo adzaza malowa ndi magazi a anthu osalakwa. Amanga nsanja zopembedzerapo Baala, kuperekapo ana awo kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala, chinthu chimene Ine sindinalamule kapena kuchiyankhula, ngakhalenso kuchiganizira. Nʼchifukwa chake taonani, masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzatchulanso malo ano kuti Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma Chophera anthu.
”Nyumba za mu Yerusalemu ndi za mafumu a ku Yuda ndidzazisandutsa ngati za ku Tofeti chifukwa ndi nyumba zimene pa madenga ake ankafukiza lubani kwa zolengedwa zamlengalenga ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’ ”
”Musatsatire milungu ina nʼkuyitumikira ndi kuyipembedza. Musapute mkwiyo wanga ndi mafano amene mwapanga ndi manja anu. Mukatero Ine sindidzakuwonongani.
”Choncho musamvere aneneri anu, owombeza anu, otanthauza maloto anu, amawula anu kapena amatsenga anu akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni.’ Iwo akukuloserani zabodza kotero kuti adani adzakuchotsani mʼdziko lanu nʼkupita nanu ku dziko lakutali. Ndidzakupirikitsani ndi kukuwonongani kotheratu.
”Iwo anayika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi dzina langa ndipo anayipitsa. Anamanga malo opembedzerapo Baala mʼChigwa cha Hinomu kuti aziperekapo ana awo aamuna ndi aakazi ngati nsembe kwa Moleki. Ine sindinawalamulire kutero, ndipo sindinaganizepo nʼkomwe kuti iwo angachite chinthu chonyansa chotero, ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda.
”“Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru; mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake. Mafano akewo ndi abodza; alibe moyo mʼkati mwawo. Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo. Pamene anthuwo azidzaweruzidwa mafanowo adzawonongedwa.
”Uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Tsoka kwa akazi amene amasoka zithumwa zapamkono, amenenso amasoka nsalu za kumutu za anthu. Kodi mufuna kukola mitima ya anthu anga, inuyo nʼkupulumutsa moyo wanu?
”“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikudana ndi zithumwa zanu zimene mumakokera nazo mitima ya anthu ngati mbalame. Ndidzazingʼamba kudzichotsa pa mikono yanu. Choncho ndidzapulumutsa miyoyo ya anthu amene munawakola ngati mbalame.
”“Iwe mwana wa munthu, anthu awa ayika mtima pa mafano awo. Ayikanso maso awo pa zinthu zina zoyipa zopunthwitsa. Kodi ayembekezera kuti ndiwayankhe chimene atandifunse? Tsono yankhula nawo ndi kuwawuza kuti zimene akunena Ambuye Yehova: ‘Ngati Mwisraeli aliyense ayika mtima wake pa mafano ndi kuyika maso ake pa zinthu zoyipa zopunthwitsa, kenaka nʼkupita kwa mneneri, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha molingana ndi kuchuluka kwa mafano ake. Ine ndidzachita zimenezi kuti mwina nʼkukopa mitima ya anthu a Israeli, amene andisiya chifukwa cha mafano awo.’
”“Nʼchifukwa chake uwawuze Aisraeli kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Lapani! Siyani mafano anu ndi ntchito zanu zonse zonyansa! “ ‘Ngati Mwisraeli wina aliyense kapena mlendo wina aliyense wokhala pakati pa Israeli adzichotsa yekha kwa Ine ndi kuyika mtima pa mafano ake ndi kuyikanso maso ake pa zinthu zopunthwitsa ndipo kenaka nʼkupita kwa mneneri kukafunsa nzeru, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha.
”Pakuti mfumu ya ku Babuloni yayima pa msewu, pa mphambano ya misewu iwiriyo. Ikuwombeza ndi mivi yake kuti idziwe njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake ndipo ikuyangʼana chiwindi cha nyama yoperekedwa ku nsembe.
”Danieli anayankha kuti, “Palibe munthu wanzeru, wowombeza, wamatsenga kapena wamawula amene akhoza kufotokozera mfumu chinsinsi chimene mwafuna kudziwa, koma kuli Mulungu kumwamba amene amawulula zinsinsi. Iye waonetsera mfumu Nebukadinezara zimene zidzachitika mʼmasiku akutsogolo. Maloto ndi masomphenya anu amene munawaona mukugona pa bedi lanu ndi awa:
”Pamene amatsenga, owombeza, alawuli ndi amawula anabwera, ndinawafotokozera maloto, koma sanathe kunditanthauzira.
”Koma mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya ananditchingira pa masiku 21, kenaka Mikayeli, mmodzi mwa angelo akuluakulu anadza kudzandithandiza chifukwa ndinakhala komweko ndi mafumu a ku Peresiya.
”“Iwo amene amagwiritsitsa mafano achabechabe amataya chisomo chawo.
”Ndidzawononga ufiti wanu ndipo sikudzakhalanso anthu owombeza mawula. Ndidzawononga mafano anu osema pamodzi ndi miyala yanu yopatulika imene ili pakati panu; simudzagwadiranso zinthu zopanga ndi manja anu. Ndidzazula mitengo ya mafano a Asera imene ili pakati panu, ndipo ndidzawononga mizinda yanu.
”“Kodi fano lili ndi phindu lanji, poti analisema ndi munthu, kapena chifanizo chimene chimaphunzitsa mabodza? Pakuti munthu amene walipanga amakhulupirira ntchito ya manja ake; amapanga mafano amene samatha kuyankhula. Tsoka kwa amene amawuza mtengo kuti, ‘Khala wamoyo!’ Kapena mwala wopanda moyo kuti, ‘Dzuka!’ Kodi zimenezi zingathe kulangiza? Ndi zokutidwa ndi golide ndi siliva; mʼkati mwake mulibe mpweya.
”Ndidzatambasula dzanja langa pa Yuda ndi onse okhala mu Yerusalemu. Ndidzawononga pamalo pano otsalira opembedza Baala, mayina a anthu osapembedza pamodzi ndi ansembe a mafano: amene amagwada pa madenga a nyumba zawo kupembedza zolengedwa zamumlengalenga, amene amagwada ndi kulumbira mʼdzina la Yehova, komanso mʼdzina la Moleki,
”Mafano amayankhula zachinyengo, owombeza mawula amaona masomphenya abodza; amafotokoza maloto onama, amapereka chitonthozo chopandapake. Choncho anthu amangoyendayenda ngati nkhosa zozunzika chifukwa chosowa mʼbusa.
”Yuda waleka kukhulupirika. Chinthu chonyansa chachitika mu Israeli ndi mu Yerusalemu: Yuda wayipitsa malo opatulika amene Yehova amawakonda, pokwatira mkazi wopembedza mulungu wachilendo. Ndipo wina aliyense wochita zimenezi, kaya munthuyo ndi wotani, Yehova amuchotse ku banja la Yakobo, ngakhale atabweretsa zopereka kwa Yehova Wamphamvuzonse.
”Ndipo musamatchule wina aliyense pansi pano kuti ‘Atate,’ pakuti muli ndi Atate mmodzi, ndipo ali kumwamba.
”Poyankha Yesu ananena kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu.” Nekodimo anati, “Kodi munthu angabadwenso bwanji atakalamba? Kodi angalowe kachiwiri mʼmimba ya amayi ake kuti abadwenso?” Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu. Thupi limabereka thupi, koma Mzimu amabereka mzimu. Iwe usadabwe chifukwa ndakuwuza kuti, ‘Uyenera kubadwanso.’ Mphepo imawomba kulikonse kumene ikufuna. Ungathe kumva kuwomba kwake, koma sungathe kudziwa kumene ikuchokera kapena kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi amene abadwa ndi Mzimu Woyera.”
”“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi. Aliyense wokhulupirira Iye saweruzidwa, koma aliyense wosakhulupirira waweruzidwa kale chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.
”“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani inu Afarisi, kuti munthu amene salowera pa khomo mʼkhola la nkhosa, koma amalowera pena pake ndi wakuba ndi wachifwamba.
”Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.
”Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera.
”Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”
”Koma mu mzindawo munali munthu dzina lake Simoni, amene amachita za matsenga ndi kudabwitsa anthu a mu Samariya. Iye amadzitamandira kuti ndi wopambana, ndipo anthu onse, aakulu ndi aangʼono anamumvera ndi kunena kuti, “Munthu uyu ndi mphamvu ya Mulungu yotchedwa Mphamvu yayikulu.” Anthu amamutsata chifukwa kwa nthawi yayitali amawadabwitsa ndi matsenga akewo. Koma atakhulupirira Filipo akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ndiponso dzina la Yesu Khristu, anthuwo anabatizidwa amuna ndi amayi. Nayenso Simoni anakhulupirira ndipo anabatizidwa, natsatira Filipo kulikonse, ndipo anadabwa kwambiri pamene anaona zizindikiro zazikulu ndi zozizwitsa.
”Iwo anayenda pa chilumba chonse mpaka anafika ku Pafo, kumeneko anapezanako ndi Myuda, wamatsenga amene analinso mneneri wonama dzina lake Barayesu. Iyeyu, amathandiza mkulu wa boma, Sergio Paulo. Mkulu wa bomayu, munthu wanzeru, anayitana Barnaba ndi Saulo chifukwa anafuna kumva Mawu a Mulungu. Koma Elima wamatsengayo, (Elima tanthauzo lake ndi wamatsenga), anatsutsana nawo ndipo anafuna kumuletsa mkulu wa bomayo kuti asakhulupirire. Koma Saulo, amenenso amatchedwa Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera anamuyangʼanitsitsa Elima ndipo anati, “Iwe ndiwe mwana wa mdierekezi ndiponso mdani wa chilungamo! Ndiwe wodzaza ndi chinyengo cha mtundu uliwonse ndi kuchenjera konse. Kodi sudzaleka kupotoza njira zolungama za Ambuye? Tsopano dzanja la Ambuye likukutsutsa iwe. Udzakhala wosaona ndipo kwa kanthawi sudzatha kuona kuwala kwa dzuwa.” Nthawi yomweyo khungu ndi mdima zinamugwera ndipo anafunafuna munthu woti amugwire dzanja kuti amutsogolere. Pamene mkulu wa bomayo anaona zimene zinachitika anakhulupirira pakuti anadabwa ndi chiphunzitso cha Ambuye.
”Barnaba anamutcha Zeusi ndipo Paulo anamutcha Herimesi chifukwa ndiye amatsogolera kuyankhula. Wansembe wa Zeusi amene nyumba yopembedzera Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo, anabweretsa ngʼombe yayimuna yovekedwa nkhata za maluwa pa chipata cha mzindawo chifukwa iyeyo pamodzi ndi anthu ena onse aja amafuna kudzipereka nsembe kwa Paulo ndi Barnaba. Koma Barnaba ndi Paulo atamva zimenezi, anangʼamba zovala zawo, nathamangira pakati pa gulu la anthuwo, akufuwula kuti, “Anthu inu, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Ife takubweretserani Uthenga Wabwino, kuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo.
”Tsiku lina pamene timapita kumalo wopempherera, tinakumana ndi mtsikana wina amene anali ndi mzimu woyipa umene umanena zamʼtsogolo. Iye amapezera ndalama zambiri ambuye ake pa ulosi wake. Mtsikanayu anatsatira Paulo ndi ife, akufuwula kuti, “Anthu awa ndi atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, amene akukuwuzani inu njira yachipulumutso.” Iye anachita izi masiku ambiri. Kenaka Paulo anavutika mu mtima, natembenuka ndipo anati kwa mzimuwo, “Ndikukulamula iwe mʼdzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa iye!” Nthawi yomweyo mzimuwo unatuluka.
”Paulo anayimirira mʼbwalo la Areopagi nati: “Inu anthu a ku Atene! Ine ndikuona kuti mʼnjira zonse ndinu opembedza kwambiri. Pakuti pamene ndimayenda ndi kuona zinthu zimene mumazipembedza, ndapezanso guwa lansembe lolembedwapo kuti, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Tsopano chimene mumachipembedza osachidziwa ndi chimene ndikuchilalikira. “Mulungu amene analenga dziko lapansi ndiponso zonse zili mʼmenemo ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndipo sakhala mʼnyumba zachipembedzo zomangidwa ndi manja. Ndipo satumikiridwa ndi manja a anthu ngati kuti Iye amasowa kanthu, chifukwa Iye ndiye amapereka moyo ndi mpweya kwa anthu onse ndi zina zonse. Kuchoka kwa munthu mmodzi Iye analenga mtundu uliwonse wa anthu, kuti akakhale pa dziko lonse lapansi; ndipo Iye anakonzeratu nthawi yawo ndiponso malo enieni kumene adzakhale. Mulungu anachita izi kuti anthu amufunefune, ndikuti pomufunafunapo amupeze ngakhale kuti Iye sali kutali ndi aliyense wa ife. ‘Pakuti timakhala mwa Iye, kuyenda mwa Iye ndi kukhala moyo mwa Iye.’ Monga olemba ndakatulo anu ena akuti, ‘Ife ndi zidzukulu zake.’ “Tsono popeza ndife ana a Mulungu, tisaganize kuti umulungu wake ndi wofanana ndi ndalama zagolide, zasiliva, mwala, kapenanso fanizo lopangidwa mwaluso la nzeru za anthu. Nthawi imene anthu sankadziwa, Mulungu anawalekerera koma tsopano akulamulira kuti anthu onse, kulikonse atembenuke mtima.
”Ambiri amene amachita za matsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi nawatentha pamaso pa anthu onse. Atawonkhetsa mtengo wa mabukuwo, unakwanira ndalama zasiliva 50,000.
”Ngakhale ankadzitama kuti ndi anzeru, anasanduka opusa. Iwo anasinthanitsa ulemerero wa Mulungu wosafa ndi mafano opangidwa ndi manja wooneka ngati munthu amene amafa, kapena ngati mbalame, ndi nyama kapena zokwawa.
”Iwo anasinthanitsa choonadi cha Mulungu ndi bodza ndipo anapembedza ndi kutumikira zinthu zolengedwa mʼmalo mwa Mlengi amene ali woyenera kutamandidwa mpaka muyaya. Ameni.
”Choncho kunena za chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano; ife tikudziwa kuti mafano si kanthu nʼpangʼonongʼono pomwe pa dziko lapansi, ndiponso kuti palibe Mulungu wina koma mmodzi yekha. Popeza kuti ngakhale pali yotchedwa milungu, kaya ndi kumwamba kapena pa dziko lapansi (poti ilipodi milungu yambirimbiri ndi ambuye ambirimbiri),
”Choncho abwenzi anga okondedwa, lekani kupembedza mafano.
”Kodi ndikutanthauza kuti nsembe zoperekedwa kwa mafano ndi kanthu konse, kapena kuti mafano ndi kanthu konse? Ayi. Nsembe za osakhulupirira zimaperekedwa kwa ziwanda, osati kwa Mulungu, ndipo sindikufuna kuti muziyanjana ndi ziwandazo. Simungamwe chikho cha Ambuye, ndi kukamweranso chikho cha ziwanda. Simungadyere pa tebulo la Ambuye ndiponso la ziwanda. Kodi tikufuna kuwutsa mkwiyo wa Ambuye? Kodi ndife amphamvu kuposa Iye?
”Inu mukudziwa kuti pamene munali akunja, ankakusocheretsani mʼnjira zosiyanasiyana ndi kukukokerani ku mafano osayankhula. Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti palibe munthu amene ali ndi Mzimu wa Mulungu angayankhule kuti, “Yesu atembereredwe,” ndiponso palibe munthu anganene kuti “Yesu ndi Ambuye,” popanda kutsogozedwa ndi Mzimu Woyera.
”Pali mgwirizano wanji pakati pa Khristu ndi Beliyali? Kapena munthu wokhulupirira angayanjane bwanji ndi munthu wosakhulupirira? Pali mgwirizano wanji pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ya mafano? Popezatu ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo. Monga Mulungu wanena kuti, “Ndidzakhala mwa iwo ndipo ndidzayendayenda pakati pawo, ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo adzakhala anthu anga.”
”Pakuti anthu oterewa ndi atumwi onama, antchito achinyengo, odzizimbayitsa ngati atumwi a Khristu. Sizododometsa zimenezi, pakuti Satana mwini amadzizimbayitsa kuoneka ngati mngelo wowunikira anthu.
”Ine ndikudabwa kuti mukusiya mwamsangamsanga chotere Mulungu amene anakuyitanani mwachisomo cha Khristu ndipo mwatembenuka ndi kutsatira uthenga wina wosiyana, umene si Uthenga Wabwino konse. Pali anthu ena amene akukusokonezani komanso akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wa Khristu. Ngakhale ife kapena mngelo wochokera kumwamba, akalalikira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene tinakulalikirani uja, iyeyo akhale wotembereredwa! Monga tanena kale, tsopano ndikubwereza kunenanso kuti, “Ngati wina aliyense akulalikirani Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene munawulandira, iyeyo akhale wotembereredwa.”
”Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu.
”Mzimu akunena momveka bwino kuti mʼmasiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chawo ndi kutsatira mizimu yonyenga ndi zinthu zophunzitsidwa ndi ziwanda.
”Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa,
”Mumakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi yekha. Mumachita bwino. Komatu ngakhale ziwanda zimakhulupirira zimenezi ndipo zimanjenjemera ndi mantha.
”Wabodzayo ndani? Ndi munthu aliyense amene amanena kuti Yesu si Mpulumutsi. Munthu woteroyo ndi wokana Khristu, ndiponso amakana Atate, ndi Mwana. Aliyense wokana Mwana alibenso Atate. Wovomereza Mwana alinso ndi Atate.
”Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi. Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: Mzimu uliwonse umene umavomereza kuti Yesu Khristu anabwera mʼthupi, ndi wochokera kwa Mulungu, koma mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu, siwochokera kwa Mulungu. Uwu ndi mzimu wa wokana Khristu umene munawumva kuti ukubwera ndipo ngakhale tsopano wabwera kale mʼdziko lapansi.
”Ife ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo aliyense amene amadziwa Mulungu amamvera zimene timayankhula. Koma aliyense amene sachokera kwa Mulungu samvera zimene timayankhula. Mmenemu ndiye mmene timasiyanitsira pakati pa mzimu wachoonadi ndi Mzimu wachinyengo.
”Ana okondedwa, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.
”Aliyense amene sasunga chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu. Koma amene amasunga chiphunzitsochi, ameneyo alinso ndi Atate ndi Mwana. Ngati wina aliyense abwera kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamulandire mʼnyumba mwanu kapena kumupatsa moni. Aliyense wolandira munthu wotere ndiye kuti akuvomerezana nazo ntchito zake zoyipa.
”Anthu ena onse amene sanaphedwe ndi miliri imeneyi sanalapebe kuti asiye ntchito zawo zoyipa. Iwo sanasiye kupembedza ziwanda ndi mafano agolide, asiliva, amkuwa, amwala ndi amtengo, mafano amene sangathe kuona, kumva kapena kuyankhula. Sanalapenso kuleka zakupha, zamatsenga awo, zachigololo zawo kapena umbava wawo.
”Chinjoka chachikulu chija chinagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakalekale ija yotchedwa Mdierekezi kapena Satana, amene amasocheretsa anthu a pa dziko lonse lapansi. Chinaponyedwa pa dziko la pansi pamodzi ndi angelo ake.
”Anthu anapembedza chinjoka chija chifukwa chinapereka ulamuliro wake kwa chirombocho. Nachonso chirombo chija anachipembedza nʼkumafunsa kuti, “Ndani angafanane ndi chirombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?”
”Chirombo cha chiwirichi chinapatsidwa mphamvu zakupereka mpweya kwa fano la chirombo choyamba chija kuti liyankhule ndi kuphetsa aliyense wokana kupembedza fanolo. Chinakakamiza aliyense, wamngʼono, wamkulu, wolemera, wosauka, mfulu ndi kapolo kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi. Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, chimene ndi dzina la chirombocho kapena nambala yotanthauza dzina lake. Pano pafunika nzeru. Munthu amene ali ndi nzeru atanthauze nambala ya chirombocho, pakuti nambalayo ikutanthauza munthu. Nambala yake ndi 666.
”Mngelo wachitatu anatsatana nawo ndi mawu ofuwula anati, “Ngati wina apembedza chirombo chija ndi fano lake ndi kulembedwa chizindikiro pa mphumi kapena pa dzanja, nayenso adzamwa vinyo waukali wa Mulungu, umene wathiridwa popanda kuchepetsa mphamvu zake mʼchikho cha ukali wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto wamiyala yasulufure pamaso pa angelo oyera ndi pa Mwana Wankhosa. Ndipo utsi wa moto wowazunzawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya. Sikudzakhala kupumula usana ndi usiku kwa amene anapembedza chirombo chija ndi fano lake kapena kwa aliyense amene analembedwa chizindikiro cha dzina lake lija.”
”Mkaziyo anavala zovala za pepo ndi zofiira nadzikongoletsa ndi golide, miyala yapamwamba ndi ngale. Ananyamula chikho chagolide mʼdzanja lake, chodzaza ndi zinthu zonyansa ndi fungo loyipa la zigololo zake. Pa mphumi pake panalembedwa dzina lodabwitsa: BABULONI WAMKULU MAYI WA AKAZI ADAMA NDI WAZOYIPITSA ZA DZIKO LAPANSI. Ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera mtima, magazi a amene anachitira umboni Yesu. Nditamuona mkaziyo ndinadabwa kwambiri.
”Kuwala kwa nyale sikudzawunikanso mwa inu. Mawu a mkwati ndi mkwatibwi sadzamvekanso mwa iwe. Amalonda anu anali akuluakulu a dziko lapansi. Mitundu yonse inasokonezedwa ndi zamatsenga zako.
”Koma amantha, osakhulupirira, okonda zonyansa, opha anthu, achiwerewere, amatsenga, opembedza mafano ndi abodza, malo awo adzakhala nyanja yamoto ya sulufule wotentha. Iyi ndi imfa yachiwiri.”
”