28 – Angelo
Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Angelo.
Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Angelo.
Mngelo wa Yehova amatchinjiriza amene amakonda Iye ndi kuwalanditsa.
”Kodi ndi kwa Mngelo uti kumene Mulungu ananenapo kuti, “Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditapanga adani ako kukhale chopondapo mapazi ako.” Kodi angelo onse si mizimu yotumikira odzalandira chipulumutso?
”Momwemonso, Ine ndikukuwuzani kuti angelo a Mulungu amakondwera kwambiri chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima.”
”Atamuthamangitsa munthu uja, Yehova anayika Akerubi mbali ya kummawa kwa Munda wa Edeni ndi lupanga lamoto limene limayendayenda ponsepo, kuteteza njira ya ku mtengo wopatsa moyo.
”Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri zoti munthu sangaziwerenge.” Mngelo wa Yehova uja anamuwuzanso kuti, “Ndiwe woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna. Udzamutcha dzina lake Ismaeli, pakuti Yehova wamva kulira chifukwa cha kuzunzika kwako. Iye adzakhala munthu wa khalidwe ngati mʼmbulu wamisala; adzadana ndi aliyense ndipo anthu onse adzadana naye, adzakhala mwaudani pakati pa abale ake onse.”
”Yehova anadza kwa Abrahamu pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya thundu ya ku Mamre. Abrahamu nʼkuti atakhala pansi pa khoma la tenti yake masana, dzuwa likutentha. Tsono Abrahamu atakweza maso ake patali anangoona anthu atatu atayima cha potero. Atawaona, ananyamuka mofulumira kuti awachingamire. Atafika anaweramitsa mutu pansi mwa ulemu nati,
”Kenaka anawachititsa khungu anthu amene anali panja pa nyumba aja, aangʼono ndi aakulu omwe, kuti asaone pa khomo. Anthu awiri aja anati kwa Loti, “Kodi uli ndi wina aliyense pano, kaya ndi akamwini ako, kaya ndi ana ako aamuna kapena aakazi, kapena aliyense mu mzindamu amene ndi anzako? Atulutse onse muno, chifukwa tiwononga malo ano. Yehova waona kuti kuyipa kwa anthu a mu mzindawu kwakulitsa. Choncho watituma kuti tiwuwononge.” Choncho Loti anatuluka nayankhula ndi akamwini ake amene anali kuyembekezera kukwatira ana ake akazi nati, “Fulumirani, tiyeni tichoke pa malo ano chifukwa Yehova watsala pangʼono kuwononga mzindawu.” Koma akamwini akewo ankayesa kuti akungoselewula. Mmene kumacha, angelo aja anamufulumizitsa Loti nati, “Nyamuka, tenga mkazi wako ndi ana ako aakazi awiriwo, ndipo mutuluke mu mzindawo kuopa kuti mungaphedwe pamodzi nawo.”
”Koma mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba nati, “Abrahamu! Abrahamu!” Iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.” Mngeloyo anati, “Usatambasulire mwanayo dzanja lako kuti umuphe, pakuti tsopano ndadziwa kuti iwe umaopa Mulungu. Iwe sunandimane mwana wako mmodzi yekhayo.”
”Mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba kachiwiri ndipo anati, “Ndikulumbira mwa Ine ndekha kuti popeza wachita zimenezi, wosandikaniza mwana wako mmodzi yekhayu, ndidzakudalitsa ndithu ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zamlengalenga komanso ngati mchenga wa mʼmphepete mwa nyanja. Zidzukulu zako zidzalanda mizinda ya adani awo, ndipo kudzera mwa chidzukulu chako, mitundu yonse ya anthu pa dziko lapansi idzadalitsika, chifukwa iwe wandimvera.”
”Mʼmaloto, anaona makwerero oyimikidwa pansi ndipo anakafika kumwamba. Angelo a Mulungu amakwera ndi kutsika pa makwereropo.
”Kutulo komweko, mngelo wa Mulungu anati, ‘Yakobo.’ Ine ndinayankha, ‘Ee, Ambuye.’
”Nayenso Yakobo analowera njira yake, ndipo angelo a Mulungu anakumana naye. Pamene Yakobo anawaona anati, “Ili ndi gulu la Mulungu.” Choncho anawatcha malowo Mahanaimu.
”Kumeneko mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye mʼmalawi amoto mʼchitsamba. Mose anaona kuti ngakhale chitsambacho chimayaka koma sichimanyeka. Tsono Mose anati mu mtima mwake, “Ine ndipita komweko ndikaone zodabwitsazi, chitsamba sichikunyeka chifukwa chiyani?”
”Ndipo mngelo wa Mulungu amene amayenda patsogolo pa gulu lankhondo la Israeli anachoka ndi kupita kumbuyo kwawo. Chipilala cha mtambo chinasunthanso kuchoka kutsogolo ndi kupita kumbuyo kwawo. Choncho mtambowo unakhala pakati pa asilikali ankhondo a dziko la Igupto ndi a dziko la Israeli. Choncho panali mdima motero kuti magulu awiri ankhondowa sanathe kuyandikizana usiku wonse.
”“Taona Ine ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu kuti akutetezeni mʼnjiramo ndi kukakufikitsani ku malo amene ndakonza.
”Mngelo wanga adzakhala patsogolo panu ndipo adzakufikitsani mʼdziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanaani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzawapheratu onsewo.
”Ndipo upange Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo, uwayike mbali ziwiri za chivundikirocho, kerubi mmodzi mbali ina ndi wina mbali inayo. Akerubiwa uwapangire limodzi ndi chivundikirocho mʼmapeto mwa mbali ziwirizo. Mapiko a Akerubiwo adzatambasukire pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo adzakhale choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho. Uyike chivundikirocho pamwamba pa bokosi ndipo mʼbokosilo uyikemo miyala ya malamulo, imene ndidzakupatse. Ndizidzakumana nawe pamenepo, pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo, pakati pa Akerubi awiriwo, ndikumadzakupatsa malamulo onse okhudzana ndi Aisraeli.
”Tsopano pita ukawatsogolere anthu kumalo kumene ine ndinanena, ndipo mngelo wanga adzakutsogolerani. Komabe, nthawi yanga ikadzafika kuti ndiwalange, ndidzawalanga chifukwa cha tchimo lawo.”
”Ndipo ndidzatumiza mngelo patsogolo panu kuthamangitsa Akanaani, Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.
”Mose atalowa mu tenti ya msonkhano kukayankhula ndi Yehova, anamva mawu kuchokera pakati pa Akerubi awiri amene anali pamwamba pa chivundikiro cha bokosi la umboni. Ndipo anayankhula naye.
”koma titalirira Yehova, Iyeyo anamva kulira kwathuko ndipo anatitumizira mngelo amene anatitulutsa ku Igupto.” “Taonani, tsopano tili pano pa Kadesi, mzinda wa mʼmalire a dziko lanu.
”Koma Mulungu anakwiya kwambiri pamene ankapita ndipo mngelo wa Yehova anayima pa njira kutsutsana naye. Balaamu anakwera bulu wake wamkazi ndipo antchito ake awiri anali naye. Pamene buluyo anaona mngelo wa Yehova atayima pa njira ndi lupanga mʼmanja mwake, anapatukira kumbali kwa msewu napita kutchire. Balaamu anamumenya kuti abwerere mu msewu. Kenaka mngelo wa Yehova anayima mʼkanjira kakangʼono pakati pa minda iwiri ya mpesa yokhala ndi makoma mbali zonse Bulu uja ataona mngelo wa Yehova anadzipanikiza ku khoma, kukhukhuza phazi la Balaamu kukhomako. Ndipo pomwepo Balaamu anamenya buluyo kachiwiri. Kenaka mngelo wa Yehova anapita patsogolo ndi kuyima pamalo opanikizika pomwe panalibe poti nʼkutembenukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere. Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova uja, anagona pansi Balaamu ali pa msana, ndipo iye anakwiya ndi kumumenya ndi ndodo yake. Pamenepo Yehova anayankhulitsa bulu uja, ndipo buluyo anati kwa Balaamu, “Ndakuchitirani chiyani kuti mundimenye katatuka?” Balaamu anati kwa buluyo, “Wandipusitsa, ndikanakhala ndi lupanga mʼmanja mwanga, ndikanakupha pomwe pano.” Buluyo anati kwa Balaamu, “Kodi sindine bulu wanu, amene mumakwera nthawi zonse kufikira lero? Kodi ndinakuchitiranipo zoterezi?” Iye anati “Ayi.”
”Pomwepo Yehova anatsekula maso Balaamu ndipo anaona mngelo wa Yehovayo ali chiyimire pa njira ndi lupanga losolola. Tsono iye anawerama nalambira pamaso pake. Mngelo wa Yehova anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wamenya bulu wako katatu? Taona, Ine ndabwera kudzakutsutsa chifukwa ulendo wakowu ndi woyipa pamaso panga. Buluyu anandiona ndi kupatuka katatu aka. Akanakhala kuti sanapatuke, ndikanakupha tsopano, koma buluyu nʼkanamusiya ndi moyo.” Balaamu anati kwa mngelo wa Yehova uja, “Ndachimwa. Sindinadziwe kuti munayima pa njira kunditsutsa. Tsopano ngati Inu simunakondwe, ineyo ndibwerera.” Mngelo wa Yehova anati kwa Balaamu, “Pita ndi anthuwa koma ukayankhule zokhazo zimene ndikakuwuze.” Choncho Balaamu anapita ndi akuluakulu a Balaki.
”Tsiku lina pamene Yoswa anali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo mwadzidzidzi anaona munthu atayima patsogolo pake ndi lupanga losolola mʼdzanja lake. Yoswa anapita pamene panali munthuyo ndipo anamufunsa kuti, “Kodi uli mbali yathu kapena ya adani athu?” Iye anayankha kuti “Sindili mbali iliyonse. Ndabwera monga mkulu wa asilikali a Yehova.” Pomwepo Yoswa anadzigwetsa chafufumimba kupereka ulemu, ndipo anamufunsa, “Kodi mbuye wanga muli ndi uthenga wotani kwa mtumiki wanu?” Mkulu wa asilikali a Yehova uja anayankha kuti, “Vula nsapato zako, pakuti wayima pa malo wopatulika.” Ndipo Yoswa anachitadi zimene anawuzidwazo.
”Mngelo wa Mulungu atayankhula izi kwa Aisraeli, onse analira mokweza,
”Ngakhalenso nyenyezi zakumwamba zinachita nkhondo, zinathira nkhondo Sisera, zikuyenda mʼnjira zake.
”Tsono mngelo wa Yehova uja anamuonekera Gideoni nati kwa iye, “Yehova ali nawe, iwe munthu wamphamvu ndi wolimba mtima.”
”Mngelo wa Yehova anatenga msonga ya ndodo imene inali mʼmanja mwake nakhudza nayo nyama ndi makeke aja. Nthawi yomweyo moto unabuka pa thanthwepo ndi kupsereza nyama yonse ndi makeke aja. Ndipo mngelo wa Yehova sanaonekenso. Apo Gideoni anazindikira kuti analidi mngelo wa Ambuye, ndipo anati, “Kalanga ine Yehova Wamphamvuzonse! Ine ndaona mngelo wa Yehova ndi maso!”
”Kenaka mayiyo anapita kukawuza mwamuna wake kuti, “Munthu wa Mulungu anabwera kwa ine, ndipo maonekedwe ake anali ngati mngelo wa Mulungu, maonekedwe woopsa kwambiri. Ine sindinamufunse kumene amachokera, ndipo iyeyo sanandiwuzenso dzina lake.
”Iye anayankha kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufunsa dzina langa? Dzina laketu ndi lodabwitsa.” Ndipo Manowa anatenga mwana wambuzi pamodzi ndi chopereka cha chakudya nakapereka nsembe pa thanthwe kwa Yehova ndipo Yehova anachita zodabwitsa kwa Manowa ndi mkazi wake akuona. Pamene malawi a moto amakwera kumwamba kuchoka pa guwa, mngelo wa Yehova uja anakwera kumwamba mʼmalawi a motowo Manowa ndi mkazi wake akuona. Tsono anadzigwetsa pansi naweramitsa mitu yawo pansi.
”Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, kuyambira mmawa mpaka pa nthawi imene anafuna mwini wake, ndipo unapha anthu 70,000 kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba. Pamene mngelo anatambasula dzanja lake kuti awononge Yerusalemu, Yehova anamva chisoni chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi. Davide ataona mngelo amene ankakantha anthu uja, anati kwa Yehova, “Ine ndi amene ndachimwa. Ine mʼbusa ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Langani ineyo pamodzi ndi banja langa.”
”Ndipo Eliya anagona tulo tofa nato pa tsinde pa kamtengoko. Ndipo taonani, mngelo anamukhudza, namuwuza kuti, “Dzuka udye.” Eliya anayangʼana, ndipo taonani kumutu kwake kunali buledi wootcha pa makala ndi botolo la madzi. Iye anadya ndi kumwa, nʼkugonanso. Mngelo wa Yehova anabweranso kachiwiri, anamukhudza, namuwuza kuti, “Dzuka udye, popeza ulendowu ndi wautali.” Tsono Eliya anadzuka nadya ndi kumwa. Atapeza mphamvu chifukwa cha chakudyacho, anayenda masiku 40, usana ndi usiku mpaka anafika ku Horebu, phiri la Mulungu.
”Mikaya anapitiriza kuyankhula nati, “Tsono imvani mawu a Yehova: Ine ndinaona Yehova atakhala pa mpando wake waufumu, gulu lonse la kumwamba litayima ku dzanja lake lamanja ndi ku dzanja lake lamanzere.
”Mngelo wa Yehova anati kwa Eliya, “Pita naye, usamuope.” Choncho Eliya ananyamuka natsika naye limodzi kupita kwa mfumu.
”Akuyenda ndi kumakambirana, mwadzidzidzi galeta lamoto ndi akavalo amoto anaonekera ndi kuwasiyanitsa awiriwo, ndipo Eliya anapita kumwamba mʼkamvuluvulu. Elisa anaona zimenezi ndipo anafuwula kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi anthu ake okwera pa akavalo!” Ndipo Elisa sanamuonenso Eliyayo. Pamenepo Elisa anagwira zovala zake nazingʼamba pakati.
”Ndipo Elisa anapemphera kuti, “Inu Yehova tsekulani maso ake kuti aone.” Pamenepo Yehova anatsekula maso a mtumikiyo, ndipo anayangʼana naona kuti phiri lonse linali lodzaza ndi akavalo ndi magaleta a moto atazungulira Elisa.
”Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, Inu amene mumakhala pa Akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
”Usiku umenewo mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya ku Asiriya ndi kupha ankhondo 185,000. Ndipo pamene anthu anadzuka mmawa, taonani, mitembo inali ngundangunda!
”Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, ndipo unapha Aisraeli 70,000. Ndipo Mulungu anatumiza mngelo kuti awononge Yerusalemu. Koma pamene mngeloyo amachita zimenezi, Yehova anaona ndipo anavutika mu mtima chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi. Davide anakweza maso ake ndipo anaona mngelo wa Yehova atayima pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba, mʼdzanja lake muli lupanga lotambalitsa kuloza ku Yerusalemu. Ndipo Davide ndi akuluakulu, atavala ziguduli, anadzigwetsa pansi chafufumimba.
”Tenti ya Yehova imene Mose anapanga mʼchipululu, ndi guwa lansembe zopsereza pa nthawi imeneyi zinali pa phiri ku Gibiyoni. Koma Davide sanathe kupita kumeneko kuti akapemphere pamaso pa Yehova, chifukwa amaopa lupanga la mngelo wa Yehova.
”Ku Malo Opatulika Kwambiri iye anapangako Akerubi awiri achitsulo ndipo anawakuta ndi golide. Kutalika kwa mapiko onse a Akerubi kunali mamita asanu ndi anayi. Phiko la Kerubi woyamba linali loposerapo mamita awiri ndipo limakhudza khoma la Nyumba ya Mulungu, pamene phiko linalo, lotalikanso koposerapo mamita awiri, limakhudza phiko la Kerubi winayo.
”Akerubiwo anatambalitsa mapiko awo pamwamba pa Bokosi la Chipangano ndipo anaphimba bokosilo pamodzi ndi mitengo yonyamulira.
”Mfumu Hezekiya ndi mneneri Yesaya mwana wa Amozi anafuwulira kumwamba mʼpemphero chifukwa cha zimenezi. Ndipo Yehova anatumiza mngelo amene anadzapha anthu onse odziwa nkhondo ndi atsogoleri ndiponso oyangʼanira misasa ya mfumu ya ku Asiriya. Choncho Senakeribu anabwerera kwawo wamanyazi. Ndipo atalowa mʼnyumba ya mulungu wake, ena mwa ana ake anamupha ndi lupanga.
”Inu nokha ndiye Yehova. Munalenga kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, zolengedwa zonse zimene zili mʼmenemo. Munalenga dziko ndi zonse zokhalamo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo. Zonse mumazisunga ndi moyo ndipo zonse za kumwamba zimakupembedzani.
”Ana a Mulungu atabwera kudzadzionetsa pamaso pa Yehova, nayenso Satana anafika nawo limodzi.
”Tsiku linanso pamene ana a Mulungu anabwera kudzadzionetsa pamaso pa Yehova, nayenso Satana anabwera nawo limodzi kudzadzionetsa pamaso pa Yehova.
”pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?
”munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira, ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye? Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.
”Mngelo wa Yehova amatchinjiriza amene amakonda Iye ndi kuwalanditsa.
”Akhale ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pamene mngelo wa Yehova akuwapirikitsa. Njira yawo ikhale ya mdima ndi yoterera pamene mngelo wa Yehova akuwathamangitsa. Popeza ananditchera ukonde popanda chifukwa ndipo popanda chifukwa andikumbira dzenje,
”Magaleta a Mulungu ndi osawerengeka, ndi miyandamiyanda; Ambuye wabwera kuchokera ku Sinai, walowa mʼmalo ake opatulika.
”anagwetsa mana kuti anthu adye, anawapatsa tirigu wakumwamba. Anthu anadya buledi wa angelo, Iye anawatumizira chakudya chonse chimene akanatha kudya.
”Anakhuthula moto wa ukali wake pa iwo, anawapsera mtima nawakwiyira nʼkuwabweretsera masautso. Zimenezi zinali ngati gulu la angelo osakaza.
”Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, kuti akutchinjirize mosamala pa njira zako zonse; ndipo adzakunyamula ndi manja awo, kuti phazi lako lisagunde pa mwala.
”Yehova akulamulira, mitundu ya anthu injenjemere; Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi, dziko lapansi ligwedezeke.
”Tamandani Yehova, inu angelo ake, amphamvu inu amene mumachita zimene amalamula, amene mumamvera mawu ake. Tamandani Yehova, zolengedwa zonse zakumwamba, inu atumiki ake amene mumachita chifuniro chake.
”Amapanga mphepo kukhala amithenga ake, malawi amoto kukhala atumiki ake.
”Mutamandeni, inu angelo ake onse, mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.
”Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova. Pamwamba pawo panayimirira Aserafi, aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: awiri anaphimba nkhope zawo, awiri anaphimba mapazi awo, ndipo awiri ankawulukira. Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti “Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse. Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.” Chifukwa cha kufuwulako maziko a zitseko ndi ziwundo anagwedezeka ndipo mʼNyumba ya Yehova munadzaza utsi. Tsono ine ndinafuwula kuti, “Tsoka langa ine! Ndatayika! Pakuti ndine munthu wapakamwa poyipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poyipa, ndipo ndi maso anga ndaona mfumu Yehova Wamphamvuzonse.” Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja anawulukira kwa ine ali ndi khala lamoto mʼdzanja lake, khala limene analichotsa ndi mbaniro pa guwa lansembe. Ndipo anandikhudza pakamwa panga ndi khala lamotolo nati, “Taona ndakhudza pa milomo yako ndi khalali; kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.”
”“Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pakati pa akerubi, Inu nokha ndiye Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
”“Ine ndidzawuteteza ndi kuwupulumutsa mzindawu, chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha pangano ndi mtumiki wanga Davide!” Tsopano mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya nkhondo ya ku Asiriya ndikukapha asilikali 185,000. Podzuka mmawa mwake anthu anangoona mitembo ponseponse!
”Ndinayangʼana ndipo ndinangoona mphepo yamkuntho ikubwera kuchokera kumpoto. Panali mtambo waukulu wozunguliridwa ndi kuwala ndipo moto unali lawilawi kuchokera mu mtambowo. Pakati pa motowo pankaoneka ngati mkuwa wonyezimira. Mʼkatikati mwa motowo munali zinthu zinayi zamaonekedwe a nyama. Thupi lawo limaoneka ngati la munthu koma chilichonse chinali ndi nkhope zinayi ndiponso mapiko anayi. Miyendo yake inali yowongoka; mapazi ake anali a ziboda ngati phazi la mwana wangʼombe. Ndipo zibodazo zinkawala ngati mkuwa wonyezimira. Mʼmunsi mwa mapiko awo kumbali zonse zinayi, nyamazo zinali ndi manja a munthu. Zonse zinayi zinali ndi nkhope ndi mapiko, ndipo mapiko awowo anakhudzana. Chilichonse chimapita molunjika kutsogolo; sizimatembenuka pamene zimayenda. Nkhope zawo zimaoneka motere: Chilichonse chinali ndi nkhope ya munthu, ndipo mbali ya kumanja chilichonse chinali ndi nkhope zinayi zosiyana motere: nkhope ya munthu, nkhope ya mkango ku dzanja lamanja, nkhope ya ngʼombe ku dzanja lamanzere, ndipo kumbuyo kwake nkhope ya chiwombankhanga. Ndi mʼmene zinalili nkhope zawo. Mapiko awo anali otambasukira mmwamba. Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko awiri okhudzana ndi mapiko a chinzake. Chinalinso ndi mapiko ena awiri ophimbira thupi lake. Zamoyozo zinkayenda molunjika kutsogolo. Kulikonse kumene mzimu umazitsogolera kupita, nazonso zimapita kumeneko, osatembenuka pamene zikupita. Pakati pa zamayozo panali chinthu chooneka ngati makala oyaka kapena miyuni yoyaka. Moto umayendayenda pakati pa zamayozo; wowala kwambiri, ndipo mphenzi zimatuluka pakati pawo. Zamoyozo zinkathamanga uku ndi uko ngati kungʼanima kwa mphenzi.
”Pamene ndinali kuyangʼana zamoyozo, ndinangoona mikombero ndipo pansi pambali pa chamoyo chilichonse panali mkombero umodzi. Maonekedwe a mikomberoyo anali ngati mwala wonyezimira. Mikombero yonse inali yofanana ndipo mapangidwe awo anali ngati wongolowanalowana. Mikombero ija poyenda inkatha kupita mbali iliyonse yomwe zamoyozo zinayangʼana popanda kutembenuka. Marimu a mikomberoyo anali aatali ndi ochititsa mantha ndipo marimu onse anayi anali ndi maso ponseponse. Zamoyozo zinkati zikamayenda, mikomberoyo imayendanso mʼmbali mwake; ndipo zamoyozo zinkati zikamakwera mmwamba, mikomberoyo imakweranso. Kulikonse kumene mzimu wake unkazitsogolera, zamoyozo zinkapita komweko. Ndipo mikombero ija inkapita nawo pamodzi popeza kuti mzimu wa zamoyozo ndiwo umayendetsa mikombero ija. Zamoyo zija zinkati zikamayenda mikombero imayendanso. Zamoyozo zimati zikayima, nayonso mikombero inkayima. Zamoyozo zinkati zikawuluka, mikomberonso imawuluka nazo pamodzi chifukwa mzimu wa zamoyo zija ndiwo umayendetsa mikombero ija.
”Pamwamba pa mitu ya zamoyozo panali chinthu chonga thambo, lowala ndipo kunyezimira kwake ngati galasi loyangʼanitsa ku dzuwa, loyalidwa pamwamba pa mitu yake. Zamoyozo zinatambalitsa mapiko ake mʼmunsi mwa thambo lija, mapiko ake ena kumakhudzana, mapiko awiri kumaphimba thupi lake. Pamene zamoyo zimayenda ndimamva phokoso la mapiko ake, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati liwu la Wamphamvuzonse, ngati phokoso la gulu lankhondo. Zimati zikayima zinkagwetsa mapiko ake. Ndipo panamveka mawu kuchokera pamwamba pa thambo la pa mitu ya zamoyo zija. Nthawi iyi nʼkuti zamoyozo zitayima ndi kugwetsa pansi mapiko ake.
”Phokoso ndinkalimvalo linali la kugundana kwa mapiko a zamoyo ndiponso phokoso la mikombero ya pambali pake ija, limene linkamveka ngati chivomerezi chachikulu.
”Ine nditayangʼana ku thambo limene lili pamwamba pa mitu ya akerubi ndinangoona chinthu chooneka ngati mpando waufumu wa mwala wa safiro. Tsono Yehova anawuza munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pita pakati pa mikombero kunsi kwa akerubi. Udzaze manja ako ndi makala oyaka amene ali pakati pa akerubiwo ndipo uwawaze mu mzinda.” Iye anachita zimenezi ine ndikuona. Apa akerubiwo anali atayima mbali ya kummwera kwa Nyumba ya Mulungu pamene munthuyo ankalowa. Tsono mtambo unadzaza bwalo lamʼkati. Ndipo ulemerero wa Yehova unachoka pamwamba pa akerubi ndipo unafika ku chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Mtambo unadzaza Nyumba ya Mulungu, ndipo kuwala kwa ulemerero wa Yehova kunadzaza bwalolo. Phokoso la mapiko a akerubi limamveka mpaka ku bwalo lakunja, monga momwe linamvekera liwu la Mulungu Wamphamvuzonse akamayankhula. Kenaka Yehova analamula munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pala moto pakati pa mikombero, pakati pa akerubi.” Munthu uja anapitadi nakayima pa mbali pa mkombero umodzi. Ndipo mmodzi wa akerubi anatambalitsa dzanja lake mpaka pa moto umene unali pakati pawo. Iye anapalako motowo ndipo anapatsa munthu wovala chovala chabafuta uja. Tsono iye anawulandira natuluka. Ndiye kuti kunsi kwa mapiko akerubi kumaoneka zinthu zooneka ngati manja a munthu.
”Ine nditayangʼanitsitsa ndinaona mikombero inayi pambali pa akerubi. Pambali pa kerubi aliyense panali mkombero umodzi; mikomberoyo inkanyezimira ngati miyala yokongola ya krizoliti. Maonekedwe a mikombero inayi ija anali ofanana. Mkombero uliwonse umaoneka ngati mkombero wolowana ndi unzake. Poyenda akerubiwo, amapita mbali iliyonse ya mbali zinayizo kumene akerubiwo amayangʼana. Mikomberoyo simatembenuka pamene akerubiwo ankayenda. Kulikonse kumene mutu walunjika nʼkumene ankapita popanda kutembenuka. Matupi awo onse, misana yawo, manja awo ndi mapiko awo zinali ndi maso okhaokha, monganso mʼmene inalili mikombero yawo inayi ija. Ine ndinamva mikombero ikutchedwa kuti, “mikombero yakamvuluvulu.” Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi. Nkhope yoyamba inali ya Kerubi, nkhope yachiwiri inali ya munthu, nkhope yachitatu inali ya mkango ndipo nkhope yachinayi inali ya chiwombankhanga. Tsono akerubi aja anawuluka. Izi zinali zamoyo zija zimene ndinaziona ku mtsinje wa Kebara. Pamene akerubi ankayenda, nayonso mikombero ya mʼmbali mwawo inkayenda. Akerubiwo ankati akatambasula mapiko awo kuti auluke mikombero sinkachoka mʼmbali mwawo. Akerubiwo ankati akayima, mikombero inkayimanso. Ngati akerubiwo auluka, mikomberoyo inkapita nawo chifukwa mzimu wa zamoyozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo.
”Pamenepo ulemerero wa Yehova unachoka pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu ndi kukakhala pamwamba pa akerubi. Ine ndikuona akerubi, anatambasula mapiko awo ndi kuwuluka. Pamene ankapita, mikombero inapita nawo pamodzi. Akerubi anakayima pa khomo la chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Tsono ulemerero wowala wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo. Izi ndizo zamoyo ndinaziona pansi pa Mulungu wa Israeli ku mtsinje wa Kebara, ndipo ndinazindikira kuti anali akerubi. Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi ndi mapiko anayi, ndipo kunsi kwa mapiko awo kunali chinthu chimene chimaoneka ngati manja a munthu. Nkhope zawo zinali zofanana ndi zomwe ndinaziona ku mtsinje wa Kebara. Kerubi aliyense amayenda molunjika.
”Tsono akerubi aja anatambasula mapiko awo kuyamba kuwuluka, mikombero ili mʼmbali mwawo. Ulemerero wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo.
”ndipo anyamata atatuwa, ali chimangidwire, anagwera mʼngʼanjo ya moto. Kenaka mfumu Nebukadinezara anadabwa ndipo anafunsa nduna zake kuti, “Kodi sanali amuna atatu amene anamangidwa ndi kuponyedwa mʼmoto?” Iwo anayankha kuti, “Ndi zoonadi, mfumu.” Iye anati, “Taonani! Ndikuona amuna anayi akuyendayenda mʼmoto, osamangidwa ndi osapwetekedwa ndipo wachinayi akuoneka ngati mwana wa milungu.” Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo langʼanjo ya moto ndi kufuwula kuti, “Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, tulukani! Bwerani kuno!” Ndipo Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anatuluka mʼmoto, ndipo akalonga, akazembe, abwanamkubwa ndi nduna zamfumu anasonkhana mowazungulira. Anaona kuti moto sunatenthe matupi awo ngakhale tsitsi kumutu kwawo silinapse; zovala zawo sizinapse, ndipo sankamveka fungo la moto. Kenaka Nebukadinezara anati, “Atamandike Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, amene anatumiza mngelo wake ndi kupulumutsa atumiki ake! Iwo anakhulupirira Iye ndi kunyozera lamulo la mfumu ndipo anali okonzeka kutaya moyo wawo koposa kutumikira kapena kupembedza mulungu wina aliyense wosakhala Mulungu wawo.
”“Ndikanali chigonere ndinaona mʼmasomphenya mngelo atayima pamaso panga, woyera, atatsika kuchokera kumwamba.
”“ ‘Angelo oyera ndiwo akutsimikiza chilangochi. Tsono anthu adziwe kuti Mulungu Wammwambamwamba ali ndi mphamvu yolamulira maufumu onse, ndipo amawapereka kwa aliyense akumufuna, ngakhale munthu wamba kuti alamulire.’
”Mulungu wanga anatumiza mngelo wake, ndipo anatseka pakamwa pa mikango. Iyo sinandivulaze chifukwa Mulungu anaona kuti ndine wosalakwa ndi kutinso sindinakulakwireni inu mfumu.”
”Mtsinje wa moto unkayenda, kuchokera patsogolo pake. Anthu miyandamiyanda ankamutumikira; ndipo anthu osawerengeka anayima pamaso pake. Abwalo anakhala malo awo, ndipo mabuku anatsekulidwa.
”Ndipo ndinamva mawu a munthu kuchokera mʼmbali mwa mtsinje wa Ulai akuyitana kuti, “Gabrieli, muwuze munthuyu tanthauzo la masomphenyawo.” Atayandikira kumene ndinayima, ndinachita mantha ndi kugwa chafufumimba. Iye anati, “Mwana wa munthu, zindikira kuti masomphenyawa akunena za nthawi yachimaliziro.”
”Gabrieli, munthu uja amene ndinamuona mʼmasomphenya poyambirira, anabwera kwa ine mowuluka. Iyi inali nthawi ya nsembe ya madzulo. Anandilangiza kuti, “Danieli ndabwera tsopano kuti ndikupatse nzeru kuti uzitha kumvetsa zinthu.
”Dzanja linandikhudza ndi kundinyamula ndipo ndinachita ngati kuwerama pa mawondo manja atagwira pansi. Iye anati, “Danieli, iwe wokondedwa kwambiri, imirira ndipo uganizire mosamala mawu ndiyankhule kwa iwe, popeza tsopano ndatumidwa kwa iwe.” Atanena izi kwa ine ndinayimirira monjenjemera. Ndipo iye anapitiriza nati, “Usachite mantha Danieli. Kuyambira tsiku loyamba pamene unatsimikiza mtima kuti umvetse zinthuzi ndi kudzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, pempho lako linamveka ndipo ndabwera kudzayankha mapemphero akowo. Koma mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya ananditchingira pa masiku 21, kenaka Mikayeli, mmodzi mwa angelo akuluakulu anadza kudzandithandiza chifukwa ndinakhala komweko ndi mafumu a ku Peresiya. Tsopano ndafika kuti ndidzakufotokozere zimene zidzachitika kwa anthu a mtundu wako kutsogolo. Ndipo pali masomphenya enanso okhudza nthawi imene ikudza.”
”Pa nthawi yomwe ankanena izi kwa ine, ndinazolika nkhope yanga pansi kusowa chonena. Kenaka wina wa maonekedwe ngati munthu anakhudza milomo yanga, ndipo ndinatsekula pakamwa panga ndi kuyamba kuyankhula. Ndinati kwa amene anayima patsogolo panga, “Ine ndasweka mtima chifukwa cha masomphenyawa mbuye wanga, ndipo ndalefuka. Kodi ine mtumiki wamba wa mbuye wanga ndingathe bwanji kuyankhula ndi inu mbuye wanga? Mphamvu zanga zatha, ndipo ndikulephera kupuma.” Kenaka wooneka ngati munthu uja anandikhudzanso ndipo anandipatsa mphamvu. Iye anati, “Usachite mantha, munthu wokondedwa kwambiriwe. Mtendere ukhale ndi Iwe ndipo ukhale wolimba.” Atayankhula nane, ndinalimbikitsidwa ndipo ndinati, “Yankhulani Mbuye wanga, popeza mwandipatsa mphamvu.” Ndipo iye anati, “Kodi ukudziwa chifukwa chimene ndabwerera kwa iwe? Ndiyamba ndabwerera kukamenyana ndi mtsogoleri wa ufumu wa Peresiya, ndipo ndikakanthana naye, kenaka mtsogoleri wa ufumu wa Grisi adzabwera. Koma ndikuwuza zimene zalembedwa mʼbuku la zoona koma palibe wondithandiza kulimbana nawo kupatula Mikayeli, kalonga wako.”
”“Pa nthawi imeneyo Mikayeli, mngelo wamkulu amene amateteza anthu a mtundu wako, adzabwera. Imeneyi idzakhala nthawi ya mavuto aakulu omwe sanaonekepo kuyambira pachiyambi cha mitundu ya anthu mpaka nthawi ikudzayo. Komatu pa nthawiyi anthu a mtundu wako, aliyense amene dzina lake lidzapezeke lolembedwa mʼbuku adzapulumutsidwa.
”Lizani lipenga mu Ziyoni. Chenjezani pa phiri langa loyera. Onse okhala mʼdziko anjenjemere, pakuti tsiku la Yehova likubwera, layandikira; tsiku la mdima ndi chisoni, tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani. Ngati mʼbandakucha umene wakuta mapiri, gulu lalikulu ndi la ankhondo amphamvu likubwera, gulu limene nʼkale lomwe silinaonekepo ngakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso. Patsogolo pawo moto ukupsereza, kumbuyo kwawo malawi amoto akutentha zinthu. Patsogolo pawo dziko lili ngati munda wa Edeni, kumbuyo kwawo kuli ngati chipululu, kulibe kanthu kotsalapo. Maonekedwe awo ali ngati akavalo; akuthamanga ngati akavalo ankhondo. Akulumpha pamwamba pa mapiri ndi phokoso ngati la magaleta, ngati moto wothetheka wonyeketsa ziputu, ngati gulu lalikulu la ankhondo lokonzekera nkhondo. Akangowaona, anthu a mitundu ina amazunzika mu mtima; nkhope iliyonse imagwa. Amathamanga ngati ankhondo; amakwera makoma ngati asilikali. Onse amayenda pa mizere, osaphonya njira yawo. Iwo sakankhanakankhana, aliyense amayenda molunjika. Amadutsa malo otchingidwa popanda kumwazikana. Amakhamukira mu mzinda, amathamanga mʼmbali mwa khoma. Amakwera nyumba ndi kulowamo; amalowera pa zenera ngati mbala. Patsogolo pawo dziko limagwedezeka, thambo limanjenjemera, dzuwa ndi mwezi zimachita mdima, ndipo nyenyezi zimaleka kuwala. Yehova amabangula patsogolo pawo, gulu lake lankhondo ndi losawerengeka, ndipo amphamvu ndi amene amamvera kulamula kwake. Tsiku la Yehova ndi lalikulu; ndi loopsa. Ndani adzapirira pa tsikulo?
”Nthawi ya usiku ndinaona masomphenya. Ndinaona munthu atakwera pa kavalo wofiira. Iye anayima pakati pa mitengo ya mchisu mʼchigwa. Kumbuyo kwake kunali akavalo ofiira, akhofi ndi oyera. Ine ndinafunsa kuti, “Mbuye wanga, kodi zimenezi ndi chiyani?” Mngelo amene amayankhula nane anayankha kuti, “Ndidzakuonetsa kuti zimenezi ndi chiyani.” Pamenepo munthu amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu anafotokoza kuti, “Amenewa ndiwo amene Yehova wawatuma kuti ayendere dziko lonse lapansi.” Ndipo okwera pa akavalo enawo anafotokoza kwa mngelo wa Yehova, amene anayima pakati pa mitengo ya mchisu kuti, “Ife tayendera dziko lonse lapansi ndipo tapeza kuti dziko lonselo lili pa bata ndi mtendere.” Tsono mngelo wa Yehova anati, “Yehova Wamphamvuzonse, kodi mpaka liti mudzakhala osaonetsa chifundo chanu kwa Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda, amene mwawakwiyira kwa zaka izi 70?” Choncho Yehova anayankhula mawu abwino ndi achitonthozo kwa mngelo amene ankayankhula nane. Pamenepo mngelo amene ankayankhula nane anati, “Lengeza mawu awa: Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndikuchitira nsanje Yerusalemu ndi Ziyoni,
”Kenaka ndinayangʼananso, ndipo ndinaona munthu atanyamula chingwe choyezera mʼmanja mwake. Ndipo ndinafunsa kuti, “Kodi ukupita kuti?” Anandiyankha kuti, “Akukayeza Yerusalemu kuti ndidziwe mulifupi mwake ndi mulitali mwake.” Taonani, mngelo amene amayankhula nane uja akuchoka, mngelo wina anabwera kudzakumana naye ndipo anamuwuza kuti, “Thamanga, kamuwuze mnyamatayo kuti, ‘Yerusalemu udzakhala mzinda wopanda malinga chifukwa mudzakhala anthu ambiri ndiponso ziweto zochuluka. Ndipo Ine mwini ndidzakhala linga lamoto kuteteza mzindawo,’ akutero Yehova, ‘ndipo ndidzakhala ulemerero mʼkati mwake.’
”Pamenepo anandionetsa Yoswa, mkulu wa ansembe, atayima pamaso pa mngelo wa Yehova, ndipo Satana anayima ku dzanja lake lamanja kuti atsutsane naye. Yehova anawuza Satana kuti, “Yehova akukudzudzula iwe Satana! Yehova amene wasankha Yerusalemu akukudzudzula! Kodi munthu uyu sali ngati chikuni choyaka chofumula pa moto?” Tsono Yoswa anali atavala zovala zalitsiro pa nthawi imene anayima pamaso pa mngelo. Mngelo uja anawuza anzake amene anali naye kuti, “Muvuleni zovala zake zalitsirizo.” Kenaka anawuza Yoswa kuti, “Taona, ndachotsa tchimo lako, ndipo ndikuveka zovala zokongola.” Ndipo ine ndinati, “Muvekeni nduwira yopatulika pamutu pake.” Choncho anamuveka nduwira yopatulika pamutu pake, namuvekanso zovala zatsopano. Nthawiyi nʼkuti mngelo wa Yehova atayima pambali. Mngelo wa Yehova analimbikitsa Yoswa kuti, “Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ngati uyenda mʼnjira zanga ndi kusunga malamulo anga, pamenepo udzalamulira nyumba yanga ndi kuyangʼanira mabwalo anga, ndipo ndidzakulolani kuti mudzakhale pamodzi ndi amene ali panowa.
”Ndinafunsa mngelo amene amayankhula nane uja kuti, “Kodi mbuye wanga chimenechi nʼchiyani?” Mngeloyo anandiyankha kuti, “Imeneyi ndi mizimu inayi yakumwamba, imene ikuchokera pamaso pa Ambuye wa dziko lonse.
”Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, “Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera. Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.” Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti, “Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli,” kutanthauza kuti, “Mulungu ali nafe.” Yosefe atadzuka, anachita zomwe mngelo wa Ambuye uja anamulamulira. Iye anamutenga Mariya kukhala mkazi wake.
”Atachoka, taonani mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto nati, “Tadzuka, tenga mwanayo pamodzi ndi amayi ake ndipo muthawire ku Igupto. Mukakhale kumeneko mpaka nditakuwuza pakuti Herode adzafunafuna mwanayo kuti amuphe.”
”Atamwalira Herode, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto ku Igupto nanena kuti, “Nyamuka, tenga mwanayo ndi amayi ake ndipo mupite ku dziko la Israeli, popeza amene anafuna moyo wa mwanayo anamwalira.”
”Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, dziponyeni nokha pansi. Pakuti kwalembedwa: “ ‘Adzalamulira angelo ake za iwe, ndipo adzakunyamula ndi manja awo kuti phazi lako lisagunde pa mwala.’ ”
”Pamenepo mdierekezi anamusiya ndipo angelo anamutumikira Iye.
”Ndipo amene anafesa namsongole ndi Satana. Kukolola ndiko kutha kwa dzikoli ndipo otuta ndi angelo. “Monga momwe namsongole azulidwa ndi kutenthedwa ndi moto, momwemonso kudzakhala pakutha kwa dziko. Mwana wa Munthu adzatumiza angelo ake ndipo iwo adzachotsa mu ufumu wake chilichonse chochimwitsa ndi onse amene amachita zoyipa. Adzawaponya mʼngʼanjo yamoto kumene kudzakhala kulira ndi kukuta mano.
”Umu ndi mmene kudzakhalira pakutha kwa dziko. Angelo adzabwera ndi kulekanitsa oyipa ndi olungama. Ndipo oyipa adzawaponya mʼngʼanjo ya moto kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”
”Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate ake ndi angelo ake ndipo pamenepo Iye adzapereka mphotho kwa munthu mofanana ndi zimene anachita.
”“Onetsetsani kuti musanyoze mmodzi wa anawa. Pakuti ndikuwuzani kuti angelo awo kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga akumwamba nthawi zonse.”
”Anthu akadzaukitsidwa, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba.
”Ndipo adzatuma angelo ake, ndi kulira kwa lipenga kwakukulu, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera ku mphepo zinayi, ndi kuchokera kumathero a thambo kufika mbali ina.
”“Palibe amene adziwa za tsikulo kapena nthawi, angakhale angelo akumwamba, angakhale Mwana, koma Atate okha.
”“Pamene Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wake, pamodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pa mpando waufumu mu ulemerero wakumwamba.
”Kodi mukuganiza kuti sindingathe kupempha Atate anga ndipo nthawi yomweyo nʼkundipatsa magulu a angelo oposa khumi ndi awiri?
”Kunachitika chivomerezi chachikulu, pakuti mngelo wa Ambuye anabwera kuchokera kumwamba ndipo anapita ku manda, nakagubuduza mwala nawukhalira. Maonekedwe ake anali ngati mphenzi ndipo zovala zake zinali mbuu ngati matalala. Alondawo anachita naye mantha kwambiri kotero kuti ananjenjemera ndi kuwuma ngati akufa. Mngelo anati kwa amayiwo, “Musachite mantha popeza ndikudziwa kuti mukufuna Yesu amene anapachikidwa. Iye muno mulibe, wauka monga mmene ananenera. Bwerani, dzaoneni malo amene anagona. Ndipo pitani msanga kawuzeni ophunzira ake kuti, ‘Wauka kwa akufa ndipo watsogola kupita ku Galileya. Mukamuona Iye kumeneko.’ Taonani ndakuwuzani.”
”ndipo anali mʼchipululumo masiku makumi anayi, akuyesedwa ndi Satana. Anali pakati pa nyama zakuthengo; ndipo angelo anamutumikira.
”Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”
”Pamene akufa auka, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba.
”Ndipo adzatuma angelo ake kukasonkhanitsa osankhidwiratu ake ku mphepo zinayi, kuyambira kumalekezero a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.
”“Palibe amene akudziwa za tsikulo kapena nthawi, ngakhale angelo akumwamba, kapena Mwana, koma Atate wokha.
”Atalowa mʼmanda, anaona mnyamata atavala mwinjiro woyera atakhala ku mbali ya kumanja, ndipo iwo anachita mantha. Iye anati, “Musaope. Kodi mukufuna Yesu wa ku Nazareti, amene anapachikidwa? Wauka! Sali muno. Onani malo amene anamugonekapo. Koma pitani, kawuzeni ophunzira ake ndi Petro kuti, ‘Iye watsogola kupita ku Galileya. Kumeneko mukamuona Iye monga momwe anakuwuzirani.’ ”
”Kenaka mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye, atayimirira ku dzanja lamanja la guwa lofukizira. Zakariya ataona mngeloyo, anadzidzimuka ndipo anagwidwa ndi mantha. Koma mngeloyo anati kwa iye: “Usachite mantha, Zakariya; pemphero lako lamveka. Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera iwe mwana wamwamuna ndipo udzamutche dzina loti Yohane. Ndipo adzakhala chimwemwe ndi chisangalalo kwa iwe, ndipo ambiri adzasangalala chifukwa cha kubadwa kwake, chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Ambuye. Iye sadzamwa vinyo kapena chakumwa choledzeretsa, ndipo adzazadzidwa ndi Mzimu Woyera kuyambira pa kubadwa. Iye adzabweretsanso Aisraeli ambiri kwa Ambuye Mulungu wawo. Ndipo iye adzabwera Ambuye asanabwere mu mzimu ndi mphamvu ya Eliya. Adzatembenuzira mitima ya abambo kwa ana awo ndi osamvera ku nzeru ya olungama, kuthandiza anthu kuti akonzekere kubwera kwa Ambuye.” Zakariya anamufunsa mngeloyo kuti, “Kodi ndingatsimikize bwanji zimenezi? Ine ndine wokalamba ndipo mkazi wanga ali ndi zaka zambiri.” Mngeloyo anayankha kuti, “Ine ndine Gabrieli. Ndimayima pamaso pa Mulungu, ndipo ndatumidwa kwa iwe kudzakuwuza uthenga wabwinowu. Ndipo kuyambira tsopano sudzatha kuyankhula kufikira izi zitachitika chifukwa sunakhulupirire mawu awa, amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake yoyenera.”
”Mwezi wachisanu ndi chimodzi, Mulungu anatuma mngelo Gabrieli ku Nazareti, mudzi wa ku Galileya, kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, wa fuko la Davide. Dzina la namwaliyo linali Mariya. Mngeloyo anafika kwa iye nati, “Moni, inu amene Ambuye wakukomerani mtima kwambiri! Ambuye ali ndi inu.” Mariya anavutika kwambiri ndi mawu awa ndipo anadabwa ndi kulonjera kotere. Koma mngeloyo anati kwa iye, “Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu. Udzakhala woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu. Iye adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wammwambamwamba. Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando waufumu wa abambo ake Davide, ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha.” Mariya anafunsa mngeloyo kuti, “Izi zingatheke bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna?” Mngelo anayankha kuti, “Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu. Ngakhale Elizabeti mʼbale wako adzakhala ndi mwana mu ukalamba wake ndipo iye amene amati ndi wosabereka, uno mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.” Mariya anayankha kuti, “Ine ndine mtumiki wa Ambuye. Zikhale kwa ine monga mwanenera.”
”Ndipo kunali abusa amene amakhala ku dera lomwelo, kuyangʼanira ziweto zawo usiku. Mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iwo ndipo ulemerero wa Ambuye unawala mowazungulira. Iwo anachita mantha. Koma mngeloyo anawawuza kuti, “Musachite mantha. Ine ndakubweretserani Uthenga Wabwino wachimwemwe chachikulu umene udzakhala wa anthu onse. Lero mʼmudzi wa Davide wakubwadwirani Mpulumutsi; Iye ndi Khristu Ambuye. Ichi chidzakhala chizindikiro kwa inu: mukapeza mwana wakhanda wokutidwa ndi nsalu atagona modyera ngʼombe.” Mwadzidzidzi gulu lalikulu la angelo linaonekera pamodzi ndi mngeloyo, kuyamika Mulungu ndi kumati, “Ulemerero kwa Mulungu mmwambamwamba, ndi mtendere kwa anthu pa dziko lapansi amene Iye akondwera nawo.” Angelowo atabwerera kumwamba, abusawo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni ku Betelehemu tikaone zinthu zomwe zachitika, zimene Ambuye atiwuza ife.”
”Pakuti kwalembedwa, “Adzalamulira angelo ake za iwe kuti akutchinjirize mosamala; ndipo adzakunyamula ndi manja awo, kuti phazi lako lisagunde pa mwala.”
”Ngati wina aliyense achita nane manyazi ndi ndiponso mawu anga, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wake ndi mu ulemerero wa Atate ndi angelo oyera.
”“Ine ndikukuwuza kuti, aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Mwana wa Munthu adzamuvomerezanso pamaso pa angelo a Mulungu. Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu adzakanidwanso pamaso pa angelo a Mulungu.
”Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale.”
”Momwemonso, Ine ndikukuwuzani kuti angelo a Mulungu amakondwera kwambiri chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima.”
”“Nthawi inafika imene wopemphayo anamwalira ndipo angelo anamunyamula nakamuyika mʼmanja mwa Abrahamu. Munthu wolemerayo anamwaliranso ndipo anayikidwa mʼmanda.
”Ndipo sadzafanso, pakuti adzakhala ngati angelo. Iwo ndi ana a Mulungu, chifukwa adzakhala ataukitsidwa kwa akufa.
”Mngelo wochokera kumwamba anafika namulimbikitsa.
”Pamene iwo ankadabwa za zimenezi, mwadzidzidzi, amuna awiri ovala zovala zonyezimira kwambiri anayimirira pambali pawo. Ndi mantha, amayiwo anaweramitsa nkhope zawo pansi, koma amunawo anawawuza kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufuna wamoyo pakati pa akufa? Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya: ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa, napachikidwa ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwanso.’ ”
”koma sanakapeze mtembo wake. Iwo anabwera ndi kudzatiwuza ife kuti anaona masomphenya a angelo amene anati Yesu ali moyo.
”Ndipo Iye anapitirira kuti, “Zoonadi, Ine ndikuwuza kuti iwe udzaona kumwamba, kutatsekuka ndi angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pa Mwana wa Munthu.”
”Ndipo ku Yerusalemuko pafupi ndi chipata cha Nkhosa kuli dziwe limene mʼChihebri limatchedwa Betisaida ndipo ndi lozunguliridwa ndi makumbi asanu. Mʼmenemo munkagonamo gulu lalikulu la anthu odwala, osaona, olumala ndi ofa ziwalo. Pakuti nthawi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira mʼdziwemo nʼkuvundula madziwo. Woyamba kulowamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji.
”koma Mariya anayima kunja kwa manda akulira. Pamene akulira, anawerama ndi kusuzumira mʼmanda ndipo anaona angelo awiri atavala zoyera, atakhala pamene panali mtembo wa Yesu, mmodzi kumutu ndi wina kumapazi. Iwo anamufunsa iye kuti, “Amayi, nʼchifukwa chiyani mukulira?” Iye anati, “Amuchotsa Mbuye wanga, ndipo ine sindikudziwa kumene iwo amuyika.”
”Atatha kuyankhula zimenezi, Yesu anatengedwa kupita kumwamba ophunzira ake akuona, ndipo anabisika mʼmitambo. Yesu akukwera kumwamba, ophunzira ake anayangʼanitsitsa ndi chidwi mʼmitambo. Mwadzidzidzi anaona anthu awiri ovala zoyera atayimirira pambali pawo. Iwo anati, “Inu, anthu a ku Galileya, chifukwa chiyani mukuyima ndi kumayangʼana mʼmitambo? Yesu amene wachotsedwa pakati panu ndi kupita kumwamba, adzabweranso mʼnjira yomweyi mwamuona akupita kumwamba.”
”Iwo anagwira atumwi ndi kuwatsekera mʼndende ya anthu wamba. Koma usiku mngelo wa Ambuye anatsekula zitseko za ndende ndi kuwatulutsa Mngeloyo anati, “Pitani, ku mabwalo a Nyumba ya Mulungu ndipo mukawuze anthu uthenga onse wamoyo watsopanowu.”
”Inu amene munalandira Malamulo amene anaperekedwa ndi angelo ndipo simunawamvere.”
”Mngelo wa Ambuye anati kwa Filipo, “Nyamuka pita chakummwera, ku msewu wa ku chipululu wopita ku Gaza kuchokera ku Yerusalemu.”
”Tsiku lina, nthawi ili ngati 3 koloko masana, anaona masomphenya. Anaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu, amene anabwera kwa iye ndi kuti, “Korneliyo.” Korneliyo anamuyangʼanitsitsa mngeloyo mwa mantha. Iye anafunsa kuti, “Nʼchiyani kodi Ambuye?” Mngelo anayankha kuti, “Mapemphero ako ndi zachifundo zako zafika pamaso pa Mulungu ngati chikumbutso.
”Kotero Petro anasungidwa mʼndende, koma mpingo unamupempherera kolimba kwa Mulungu. Usiku woti mmawa mwake Herode amuzenga mlandu, Petro amagona pakati pa asilikali awiri, atamangidwa maunyolo awiri, ndiponso alonda atayima pa khomo. Mwadzidzidzi mngelo wa Ambuye anaonekera ndipo kuwala kunawunika mʼchipindamo. Mngeloyo anamugwedeza Petro mʼnthiti ndi kumudzutsa. Iye anati, “Fulumira, imirira!” Ndipo maunyolo anagwa kuchoka mʼmanja a Petro. Kenaka mngelo anati kwa iye, “Vala zovala ndi nsapato.” Ndipo Petro atachita izi mngeloyo anamuwuzanso kuti, “Funda chovala chako ndipo unditsate.” Petro anatsatira natuluka mʼndende, koma sanazindikire kuti zimene mngeloyo amachita zimachitikadi; iye amaganiza kuti amaona masomphenya. Iwo anadutsa gulu loyamba ndi lachiwiri la asilikali ndipo anafika pa chitseko chachitsulo cholowera mu mzinda. Chitsekocho chinatsekuka chokha ndipo anadutsa. Pamene anayenda kutalika kwa msewu umodzi, mwadzidzidzi mngelo uja anachoka.
”Pamenepo Petro anazindikira nati, “Tsopano ndikudziwa mosakayika kuti Ambuye anatuma mngelo wake kudzandipulumutsa mʼmanja mwa Herode, ndi ku zoyipa zonse zimene Ayuda amafuna kundichitira.” Atazindikira zimenezi anapita ku nyumba ya Mariya amayi ake a Yohane, wotchedwanso Marko, kumene kunasonkhana anthu ambiri ndipo amapemphera. Petro anagogoda pa chitseko cha panja, ndipo mtsikana wantchito dzina lake Roda anabwera kuti adzatsekule chitseko. Atazindikira mawu a Petro anakondwa kwambiri ndipo anabwerera osatsekula ndipo anafuwula kuti, “Petro ali pa khomopa!” Anthuwo anati kwa iye, “Wopenga iwe!” Atalimbikira kunena kuti zinali zoona, iwo anati, “Ameneyo ndi mngelo wake.” Koma Petro anapitiriza kugogoda ndipo atatsekula chitseko ndi kumuona, anthuwo anadabwa kwambiri.
”Pa tsiku limene anasankha Herode, atavala zovala zake zaufumu, anakhala pa mpando wake ndipo anayankhula kwa anthuwo. Anthuwo anafuwula nati, “Amenewa ndi mawu a mulungu osati a munthu ayi.” Nthawi yomweyo mngelo wa Mulungu anamukantha chifukwa sanapereke ulemu kwa Mulungu ndipo anadyedwa ndi mphutsi nafa.
”Asaduki amati kulibe kuuka kwa akufa, kulibenso ngakhale angelo kapena mizimu, koma Afarisi amakhulupirira zonsezi.
”Usiku wathawu mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake ndipo ndimamutumikira, anayima pafupi ndi ine, ndipo iyeyu anati, ‘Usachite mantha, Paulo. Ukuyenera kukayima pamaso pa Kaisara; ndipo Mulungu mwa kukoma mtima kwake wakupatsa miyoyo ya anthu onse amene ukuyenda nawo.’
”Kodi simukudziwa kuti mudzaweruza angelo? Nanga bwanji zinthu za mʼmoyo uno!
”Pa chifukwa ichi, ndiponso pa chifukwa cha angelo, mkazi akuyenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro wake.
”Ngakhale nditamayankhula mʼmalilime a anthu ndi a angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chinganga chaphokoso kapena ngati chitsulo chosokosera.
”Ngakhale ife kapena mngelo wochokera kumwamba, akalalikira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene tinakulalikirani uja, iyeyo akhale wotembereredwa!
”Musalole kuti wina aliyense amene amakonda kudzichepetsa mwachiphamaso ndi kumapembedza angelo akulepheretseni kukalandira mphotho. Munthu woteroyu amayankhulanso mwatsatanetsatane zinthu zimene akuti anaziona mʼmasomphenya. Anthuwa ndi odzitukumula ndi fundo zopanda pake zochokera mʼmaganizo mwawo amene si auzimu.
”Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba.
”Kodi ndi kwa mngelo uti, kumene Mulungu anati, “Iwe ndiwe mwana wanga; Ine lero ndakhala Atate ako.” Kapena kunenanso kuti, “Ine ndidzakhala abambo ake; iye adzakhala mwana wanga.”
”Pamene Mulungu amatuma Mwana wake woyamba kubadwa ku dziko lapansi anati, “Angelo onse a Mulungu amupembedze Iye.”
”Iye ponena za angelo akuti, “Mulungu amasandutsa angelo ake mphepo, amasandutsa atumiki ake malawi amoto.”
”Kodi ndi kwa Mngelo uti kumene Mulungu ananenapo kuti, “Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditapanga adani ako kukhale chopondapo mapazi ako.” Kodi angelo onse si mizimu yotumikira odzalandira chipulumutso?
”Mulungu sanapereke kwa angelo ulamuliro wa dziko limene likubwerali, limene ife tikulinena. Koma palipo pena pamene wina anachitira umboni kuti, “Kodi munthu ndani kuti muzimukumbukira, kapena mwana wa munthu kuti muzimusamalira? Munamuchepetsa pangʼono kusiyana ndi angelo; munamupatsa ulemerero ndi ulemu.
”Pakuti tikudziwanso kuti sathandiza angelo, koma zidzukulu za Abrahamu.
”Pamwamba pa bokosilo panali zifanizo za angelo otchedwa akerubi aulemerero, ataphimba chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nʼzosatheka tsopano kufotokoza zinthu mwatsatanetsatane.
”Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ku mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba. Mwafika mu msonkhano wa angelo osangalala osawerengeka. Mwafika mu mpingo wa ana oyamba kubadwa, amene mayina awo analembedwa kumwamba. Inu mwafika kwa Mulungu, woweruza anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama ndi osandutsidwa kukhala angwiro.
”Musayiwale kusamalira alendo, pakuti pochita zimenezi anthu ena anasamalira angelo amene samawadziwa.
”Mulungu anawawululira kuti ntchito yawoyo sankayigwira chifukwa cha iwo eni, koma chifukwa inu, pamene iwo ankayankhula zinthu zimene mwamva tsopano kuchokera kwa amene amalalikira Uthenga Wabwino mwamphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera kumwamba. Ngakhale angelo amalakalaka kuona nawo zinthuzi.
”amene anapita kumwamba ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu komwe angelo ndi maulamuliro ndi amphamvu amamvera Iye.
”Komatu ngakhale angelo, amene ali akulu ndi amphamvu kuwaposa, sayankhula za chipongwe pobweretsa chiweruzo pa iwo kuchokera kwa Ambuye.
”Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi. Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: Mzimu uliwonse umene umavomereza kuti Yesu Khristu anabwera mʼthupi, ndi wochokera kwa Mulungu,
”Koma ngakhale mkulu wa angelo Mikayeli, pamene ankalimbana ndi Mdierekezi za mtembo wa Mose, sanamunene kuti wachipongwe, koma anati, “Ambuye akudzudzule iwe!”
”Tanthauzo la nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene waziona mʼdzanja langa lamanja ndi la zoyikapo nyale zagolide zisanu ndi ziwiri ndi ili: Nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndi angelo a mipingo isanu ndi iwiri ija, ndipo zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zija ndi mipingo isanu ndi iwiri ija.”
”Amene adzapambane adzavala zoyera ngati ena aja. Sindidzafafaniza dzina lake mʼbuku lamoyo, koma ndidzamuchitira umboni pamaso pa Atate anga ndi angelo ake.
”Kuzungulira mpando waufumuwu panalinso mipando ina yaufumu yokwana 24 ndipo panakhala akuluakulu 24 atavala zoyera ndipo anavala zipewa zaufumu zagolide pamutu. Kumpando waufumuwo kunkatuluka mphenzi, phokoso ndi mabingu. Patsogolo pake pa mpando waufumuwo panali nyale zisanu ndi ziwiri zoyaka. Iyi ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu.
”Patsogolo pa mpando waufumu pomwepo panalinso ngati nyanja yagalasi yonyezimira ngati mwala wa krustalo. Pakatinʼpakati, kuzungulira mpando waufumuwo panali zamoyo zinayi zokhala ndi maso ponseponse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe. Chamoyo choyamba chinali ngati mkango, chachiwiri chinali ngati mwana wangʼombe, chachitatu chinali ndi nkhope ngati munthu, chachinayi chinali ngati chiwombankhanga chowuluka. Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo chinali ndi maso ponseponse ndi mʼkati mwa mapiko momwe. Usana ndi usiku zimanena mosalekeza kuti, “Woyera, woyera, woyera ndi Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, amene munali, amene muli ndi amene mukubwera.” Nthawi zonse zamoyozo zimapereka ulemerero, ulemu ndi mayamiko kwa uja wokhala pa mpando waufumu, amene ali ndi moyo wamuyaya. Izi zikamachitika akuluakulu 24 aja amadzigwetsa pansi pamaso pa wokhala pa mpando waufumuyo, namupembedza wokhala ndi moyo wamuyayayo. Iwo amaponya pansi zipewa zawo zaufumu patsogolo pa mpando waufumu nati: “Ndinu woyeneradi kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu, Ambuye ndi Mulungu wathu, pakuti munalenga zinthu zonse, ndipo mwakufuna kwanu zinalengedwa monga zilili.”
”Ndipo ndinaona mngelo wamphamvu akulengeza ndi mawu okweza kuti, “Ndani ali woyenera kumatula zomatira ndi kufutukula bukuli?”
”Kenaka ndinaona Mwana Wankhosa akuoneka ngati wophedwa atayimirira pakatikati pa mpando waufumu uja ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Mwana Wankhosayo anali ndi nyanga zisanu ndi ziwiri ndi maso asanu ndi awiri omwe ndi Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu yomwe anayitumiza ku dziko lonse lapansi. Iye anabwera natenga buku lija limene linali mʼdzanja lamanja la wokhala pa mpando waufumuyo. Ndipo atalitenga, zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu 24 aja anadzigwetsa pansi pamaso pa Mwana Wankhosa. Aliyense wa akuluakuluwo anali ndi zeze ndiponso mbale zagolide zodzaza ndi lubani. Lubaniyo ndi mapemphero a oyera mtima.
”Kenaka nditayangʼananso ndinamva mawu a angelo ambiri, miyandamiyanda kuchulukitsa ndi miyandamiyanda. Anazungulira mpando waufumu pamodzi ndi zamoyo zija ndi akuluakulu aja. Ndipo angelowo anayimba ndi mawu ofuwula akuti, “Mwana Wankhosa amene anaphedwayu ndi woyenera kulandira ulamuliro, chuma, nzeru, mphamvu, ulemu, ulemerero ndi mayamiko.” Kenaka ndinamva mawu a cholengedwa chilichonse kumwamba, pa dziko lapansi, kunsi kwa dziko lapansi, pa nyanja ndi zonse zili mʼmenemo zikuyimba kuti, “Kwa wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa, kukhale mayamiko, ulemu, ulemerero ndi mphamvu mpaka muyaya!” Zamoyo zinayi zija zinati: “Ameni,” ndipo akuluakulu aja anadzigwetsa pansi napembedza.
”Zitatha izi ndinaona angelo anayi atayima pa mbali zinayi za dziko lapansi, atagwira mphepo zinayi za dziko lapansi kuletsa kuti mphepo iliyonse isawombe pa dziko kapena pa nyanja kapena pa mtengo uliwonse. Kenaka ndinaona mngelo wina akuchokera kummawa, ali ndi chidindo cha Mulungu wamoyo. Iye anafuwulira angelo anayi aja amene anapatsidwa mphamvu yowononga dziko ndi nyanja kuti, “Musawononge dziko, nyanja ndi mitengo kufikira titalemba chizindikiro pa mphumi za atumiki a Mulungu wathu.”
”“Angelo onse anayimirira kuzungulira mpando waufumu uja, kuzunguliranso akuluakulu aja ndi zamoyo zinayi zija. Angelo aja anadzigwetsa pansi chafufumimba patsogolo pa mpando waufumu napembedza Mulungu. Iwo anati, “Ameni! Matamando ndi ulemerero, nzeru, mayamiko, ulemu, ulamuliro ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kunthawi zanthawi, Ameni!”
”Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri aja amene amayimirira pamaso pa Mulungu, akupatsidwa malipenga asanu ndi awiri. Mngelo wina amene anali ndi chofukizira chagolide anabwera nayimirira pa guwa lansembe. Anapatsidwa lubani wambiri kuti amupereke pamodzi ndi mapemphero a anthu onse oyera mtima pa guwa lansembe lagolide patsogolo pa mpando waufumu. Fungo la lubani pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima zinakwera kumwamba kwa Mulungu kuchokera mʼdzanja la mngeloyo. Kenaka mngeloyo anatenga chofukizira nachidzaza ndi moto wochokera pa guwa lansembe ndi kuponya pa dziko lapansi ndipo nthawi yomweyo panachitika mabingu, phokoso, mphenzi ndi chivomerezi. Angelo asanu ndi awiri anakonzekera kuyimba malipenga asanu ndi awiri.
”Mngelo woyamba anayimba lipenga lake ndipo kunabwera matalala ndi moto wosakanizana ndi magazi ndipo unaponyedwa pa dziko lapansi. Gawo limodzi la magawo atatu a dziko lapansi linapsa, gawo limodzi la magawo atatu a mitengo linapsa ndi gawo limodzi la magawo atatu a udzu wauwisi linapsanso. Mngelo wachiwiri anayimba lipenga lake, ndipo chinthu china chooneka ngati phiri lalikulu loyaka moto, chinaponyedwa mʼnyanja. Gawo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka magazi. Gawo limodzi mwa magawo atatu a zolengedwa zonse zamoyo za mʼnyanja, linafa, ndipo gawo limodzi la sitima za pamadzi linawonongedwa. Mngelo wachitatu anayimba lipenga lake, ndipo nyenyezi yayikulu, yoyaka ngati muni inachoka kumwamba nigwera pa gawo limodzi la magawo atatu a mitsinje ndi pa akasupe amadzi. Dzina la nyenyeziyo ndi Chowawa. Gawo limodzi la magawo atatu a madzi anasanduka owawa ndipo anthu ambiri anafa chifukwa cha madzi owawawo. Mngelo wachinayi anayimba lipenga lake, ndipo chimodzi cha zigawo zitatu za dzuwa, za mwezi ndi za nyenyezi zinamenyedwa kotero chimodzi mwa zitatu za zonsezi zinada. Panalibenso kuwala pa chimodzi mwa zigawo zitatu za usana, ndi chimodzimodzinso usiku. Ndinayangʼananso ndipo ndinaona ndi kumva chiwombankhanga chimene chinkawuluka mlengalenga kwambiri chikuyankhula mofuwula kuti, “Tsoka, Tsoka! Tsoka lalikulu kwa anthu okhala mʼdziko lapansi, angelo otsala aja akangoyimba malipenga awo!”
”Mngelo wachisanu anayimba lipenga lake, ndipo ndinaona nyenyezi ikugwa pa dziko lapansi kuchokera ku thambo. Nyenyeziyo inapatsidwa kiyi ya ku chidzenje chakuya.
”Mngelo wachisanu ndi chimodzi anayimba lipenga lake, ndipo ndinamva liwu lochokera ku ngodya zinayi za guwa lansembe lagolide lija lokhala pamaso pa Mulungu. Liwulo linati kwa mngelo wachisanu ndi chimodzi amene anali ndi lipenga uja, “Masula angelo anayi amene anamangidwa pa mtsinje waukulu wa Yufurate.” Ndipo anamasulidwadi angelo anayi aja amene anasungidwa kukonzekera ora ili, tsiku ili, mwezi uwu ndi chaka ichi kuti aphe limodzi la magawo atatu a anthu. Ndinamva chiwerengero cha ankhondo a pa akavalo aja, kuti chinali 200 miliyoni.
”Kenaka ndinaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera kumwamba. Anavala mtambo ndipo anali ndi utawaleza pamutu pake. Nkhope yake inali ngati dzuwa, ndipo miyendo yake inali ngati mizati yamoto. Mʼdzanja lake munali kabuku kakangʼono kotsekulidwa. Phazi lake lamanja linaponda mʼnyanja ndipo phazi lake lamanzere linaponda pa mtunda. Mngeloyo anafuwula kwambiri ngati kubangula kwa mkango. Atangofuwula, kunamveka kugunda kwa mabingu asanu ndi awiri. Mabingu asanu ndi awiriwo atangogunda, ine ndinkati ndizilemba; koma ndinamva mawu kuchokera kumwamba kuti, “Zisunge mu mtima zimene mabingu asanu ndi awiriwo anena ndipo usazilembe.” Kenaka mngelo amene ndinamuona ataponda mʼnyanja ndi ku mtunda uja, anakweza dzanja lake lamanja kumwamba. Mngeloyo analumbira mʼdzina la Iye wokhala ndi moyo mpaka muyaya, amene analenga kumwamba ndi zonse zili kumeneko, dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo, nati, “Pasakhalenso zochedwa tsopano! Koma patsala pangʼono kuti mngelo wachisanu ndi chiwiri uja awombe lipenga lake, chinsinsi cha Mulungu chidzachitika monga momwe analengezera kwa atumiki ake, aneneri.”
”Pamenepo mawu amene ndinamva kuchokera kumwamba aja, anandiyankhulanso, anati, “Pita katenge buku lotsekulidwalo mʼdzanja la mngelo amene waponda pa nyanja ndi pa mtundayo.” Choncho ndinapita kwa mngeloyo ndipo ndinamupempha kuti andipatse kabukuko. Iye anati, “Tenga, idya. Mʼmimba mwako kaziwawa koma mʼkamwa mwako kazizuna ngati uchi.” Ndinatenga kabukuko mʼdzanja la mngeloyo ndipo ndinadyadi. Mʼkamwa mwanga kankazuna ngati uchi, koma nditakameza, mʼmimbamu munkawawa. Ndipo anandiwuza kuti, “Iwe uyenera kulalikiranso za mitundu yambiri ya anthu, za mayiko, ziyankhulo ndi za mafumu.”
”Mngelo wachisanu ndi chiwiri anawomba lipenga lake, ndipo kumwamba kunamveka mawu ofuwula amene anati, “Ufumu wa dziko lapansi uli mʼmanja mwa Ambuye athu ndi Khristu wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.” Ndipo akuluakulu 24 aja okhala pa mipando yawo yaufumu pamaso pa Mulungu, anadzigwetsa chafufumimba napembedza Mulungu Iwo anati, “Ife tikuyamika Inu Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, amene mulipo ndipo munalipo, chifukwa mwaonetsa mphamvu yanu yayikulu, ndipo mwayamba kulamulira.
”Zitatero, kumwamba kunayambika nkhondo. Mikayeli ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho ndi angelo ake anabwezeranso. Koma analibe mphamvu ndipo anagonjetsedwa nathamangitsidwa kumwambako.
”Anthuwo ankayimba nyimbo yatsopano patsogolo pa mpando waufumu ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kuphunzira nyimboyo kupatula anthu 144,000 aja amene anawomboledwa pa dziko lapansi.
”Kenaka ndinaona mngelo wina akuwuluka mu mlengalenga ndipo anali ndi Uthenga Wabwino wamuyaya woti akalalikire kwa anthu okhala pa dziko lapansi, kwa a mtundu uliwonse, a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse ndi kwa anthu onse. Mngeloyo anayankhula mokweza mawu kuti, “Wopani Mulungu ndi kumutamanda, chifukwa nthawi yoweruza anthu yafika. Mumupembedze Iye amene analenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi akasupe amadzi.” Mngelo wachiwiri anatsatana naye ndipo anati, “Wagwa! Wagwa Babuloni womveka uja, amene anachititsa anthu a mitundu yonse kumwa vinyo wa zilakolako zake zachigololo.” Mngelo wachitatu anatsatana nawo ndi mawu ofuwula anati, “Ngati wina apembedza chirombo chija ndi fano lake ndi kulembedwa chizindikiro pa mphumi kapena pa dzanja, nayenso adzamwa vinyo waukali wa Mulungu, umene wathiridwa popanda kuchepetsa mphamvu zake mʼchikho cha ukali wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto wamiyala yasulufure pamaso pa angelo oyera ndi pa Mwana Wankhosa.
”Tsono mngelo wina anatuluka mʼNyumba ya Mulungu nafuwula mwamphamvu kwa uja wokhala pa mtamboyu. Mngeloyo anati, “Tenga chikwakwa chako ndipo kolola, pakuti nthawi yokolola ya dziko la pansi yakwana” Choncho wokhala pa mtambo uja anayamba kukolola dzinthu pa dziko lapansi ndi chikwakwa chakecho.
”Mngelo wina anatuluka mʼNyumba ya Mulungu kumwamba ndipo nayenso anali ndi chikwakwa chakunthwa. Kenaka mngelo winanso amene amalamulira moto, anatuluka kuchokera ku guwa lansembe nayitana mwamphamvu mngelo uja amene anali ndi chikwakwa chakunthwa chija, nati, “Tenga chikwakwa chako chakunthwacho yamba kudula mphesa za mʼmunda wamphesa wa pa dziko lapansi, pakuti mphesa zapsa kale.” Pamenepo mngeloyo anayambadi kugwiritsa ntchito chikwakwa chake nadula mphesa za dziko lapansi, naziponya mʼchopondera mphesa chachikulu cha ukali woopsa wa Mulungu. Mphesazo zinapondedwa mʼchopondera mphesa kunja kwa mzinda. Mʼchopondera mphesamo munatuluka magazi amene anayenderera ngati mtsinje, kuzama kwake mita ndi theka ndipo kutalika kwake makilomita 300.
”Kumwamba ndinaona chizindikiro china chachikulu ndi chodabwitsa: angelo asanu ndi awiri ali ndi miliri isanu ndi iwiri yomaliza chifukwa Mulungu anakwiya kotheratu.
”Mʼnyumbamo munatuluka angelo asanu ndi awiri ndi miliri isanu ndi iwiri. Angelowo anavala nsalu zoyera bwino zonyezimira ndi malamba agolide pa zifuwa zawo. Ndipo kenaka chimodzi cha zamoyo zinayi zija chinapereka kwa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zodzaza ndi ukali wa Mulungu amene ali ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo Nyumba ya Mulungu inadzaza ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu zake, ndipo panalibe yemwe akanalowa mʼNyumbayo mpaka miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri aja itatha.
”Kenaka ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Nyumba ya Mulungu ija kuwuza angelo asanu ndi awiri kuti, “Pitani, katsanulireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu umene uli mʼmbale zisanu ndi ziwirizi!” Mngelo woyamba anapita natsanula mbale yake pa dziko lapansi ndipo zilonda zoyipa ndi zowawa zinabuka pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chirombo chija, napembedza fano lake. Mngelo wachiwiri anapita natsanula mbale yake pa nyanja ndipo madzi ake anasanduka magazi, magazi ake ngati a munthu wakufa. Chamoyo chilichonse cha mʼnyanjamo chinafa. Mngelo wachitatu anapita natsanula mbale yake pa mitsinje ndi akasupe amadzi ndipo zinasanduka magazi. Kenaka ndinamva mngelo wolamulira madzi uja akuti, “Inu mwachita chilungamo, Inu Woyerayo, amene mulipo ndipo munalipo; pakuti iwo anakhetsa magazi a oyera anu ndi aneneri anu, nʼchifukwa chake mwawapatsa magazi kuti amwe, zomwe zikuwayenera.” Kenaka ndinamva mawu ochokera ku guwa lansembe akuti, “Inde, Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, chiweruzo chanu ndi choona ndi cholungama.” Mngelo wachinayi anapita natsanula mbale yake pa dzuwa ndipo dzuwa linapatsidwa mphamvu yopsereza anthu ndi moto. Anapserera nako kutentha kwakukuluko ndipo anatukwana Mulungu, amene anali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi, koma anakana kulapa ndi kumulemekeza. Mngelo wachisanu anapita natsanula mbale yake pa mpando waufumu wa chirombo chija ndipo mdima unagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu analuma malilime awo chifukwa cha ululu. Ndipo anatukwana Mulungu wakumwamba chifukwa cha maululu awo ndi zilonda zawo koma anakana kulapa pa zimene anachita. Mngelo wachisanu ndi chimodzi anapita natsanula mbale yake pa mtsinje waukulu wa Yufurate, ndipo madzi ake anaphwa kuti pakhale njira yodzera mafumu ochokera kummawa.
”Mngelo wachisanu ndi chiwiri anatsanulira mbale yake mu mlengalenga ndipo ku Nyumba ya Mulungu kunamveka mawu ofuwula kuchokera ku mpando waufumu kuti, “Kwatha!”
”Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri anadza nati kwa ine, “Bwera ndikuonetse chilango cha mkazi wadama wotchuka uja amene akukhala pambali pa madzi ambiri. Mafumu a dziko lapansi amachita naye chigololo ndipo okhala pa dziko lapansi analedzera ndi vinyo wa zigololo zake.” Kenaka mngeloyo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndinaona mkazi atakhala pa chirombo chofiira chokutidwa ndi mayina a chipongwe ndipo chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.
”Zitatha izi ndinaona mngelo wina akutsika kuchokera kumwamba. Iye anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero.
”Kenaka mngelo wamphamvu ananyamula mwala waukulu ngati mphero yayikulu nawuponya mʼnyanja nanena kuti, “Mwa mphamvu chonchi mzinda waukulu wa Babuloni udzaponyedwa pansi, sudzapezekanso.
”Akuluakulu 24 aja ndi zamoyo zinayi zija anadzigwetsa pansi kupembedza Mulungu amene anakhala pa mpando waufumu. Ndipo anafuwula kuti, “Ameni, Haleluya!”
”Ndipo ndinaona mngelo atayimirira pa dzuwa amene anafuwula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zowuluka mlengalenga kuti, “Bwerani, sonkhanani pamodzi ku phwando lalikulu la Mulungu.
”Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi ya ku chidzenje chakuya chija atanyamula mʼdzanja lake unyolo waukulu. Iye anachigwira chinjokacho, chinjoka chakalekale chija, amene ndi Mdierekezi kapena kuti Satana, ndipo anamumanga zaka 1,000.
”Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja, anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri zodzaza ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri anandiwuza kuti, “Bwera, ine ndidzakuonetsa mkwatibwi wa Mwana Wankhosa.” Ndipo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku phiri lalikulu ndi lalitali nandionetsa mzinda wopatulika, Yerusalemu ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu.
”Anayesa mpanda uja ndipo kuchindikala kwake kunali kopitirirapo mamita 65 monga mwa muyeso wa anthu umene mngelo anagwiritsa ntchito.
”Ine Yohane, ndine amene ndinamva ndi kuona zinthu izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kuona izi ndinagwa pansi kuti ndipembedze mngelo amene amandionetsa zimenezi. Koma mngeloyo anandiwuza kuti, “Usatero ayi! Ine ndine wotumikira monga iwe pamodzi ndi abale ako aneneri ndi onse amene amasunga mawu a mʼbuku pembedzani Mulungu.”
”“Ine Yesu, ndatuma mngelo wanga kuti achitire umboni uwu ku mipingo. Ine ndine Muzu ndi Chipatso cha Davide ndipo ndine Nthanda Yonyezimira.”
”