02 – Mulungu

Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Mulungu.

Mavesi atatu ofunika kwambiri

“Ine ndine Alefa ndi Omega,” akutero Ambuye Mulungu Wamphamvuzonseyo “amene muli, amene munalipo, ndi amene mudzakhalapo.”

“Mulungu amene analenga dziko lapansi ndiponso zonse zili mʼmenemo ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndipo sakhala mʼnyumba zachipembedzo zomangidwa ndi manja.

Palibe kanthu kobisika pamaso pa Mulungu. Zinthu zonse zili poyera ndi zovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.

Mavesi onse motsatira dongosolo lolondola – 187 ndime

Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Pamene Abramu anali ndi zaka 99, Yehova anamuonekera nati, “Ine ndine Mulungu Wamphamvuzonse. Ukhale munthu wochita zolungama nthawi zonse.

Mose anati kwa Mulungu, “Ngati ndipita kwa Aisraeli ndi kukawawuza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ ndipo iwo nʼkukandifunsa kuti ‘Dzina lake ndi ndani?’ Tsono ine ndikawawuze chiyani?” Mulungu anati kwa Mose, “NDINE AMENE NDILI. Izi ndi zimene ukanene kwa Aisraeli: ‘NDINE wandituma kwa inu.’ ” Mulungu anatinso kwa Mose, “Ukanene kwa Aisraeli kuti ‘Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo, wandituma kwa inu.’ Ili ndilo dzina langa mpaka muyaya, ndipo mibado ya mʼtsogolomo izidzanditchula ndi dzina limeneli.

Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamutamanda, Mulungu wa makolo anga, ine ndidzamukweza. Yehova ndi wankhondo; Yehova ndilo dzina lake.

Yehova, dzanja lanu lamanja ndi laulemerero chifukwa cha mphamvu zake. Ndithu Yehova, dzanja lanu lamanja linaphwanya mdani.

Ndipo Iye anadutsa kutsogolo kwa Mose akulengeza kuti, “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosapsa mtima msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, waonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu miyandamiyanda, wokhululukira zoyipa, kuwukira, ndiponso tchimo, komatu salekerera ochimwa kuti asalangidwe. Iye amalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha machimo a makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi.”

Musapembedze mulungu wina, pakuti Yehova amene dzina lake ndi Nsanje, ndi Mulungu wa nsanje.

Komabe, ndikunenetsa kuti pali Ine, ndiponso pamene dziko lapansi ladzaza ndi ulemerero wa Yehova,

Mulungu si munthu kuti aname, kapena mwana wa munthu kuti asinthe maganizo ake. Kodi amayankhula koma osachita? Kodi amalonjeza koma osakwaniritsa?

Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi moto wonyeketsa ndipo ndi Mulungu wansanje.

Iye anakuonetsani zonsezi kuti inu muzindikire kuti Yehova ndiye Mulungu, palibenso wina wofanana naye. Kuchokera kumwamba, Iye anafuna kuti inu mumve mawu ake ndi kuti mukhale osunga mwambo. Pa dziko lapansi anakuonetsani moto waukulu, ndipo inu munamva mawu ake kuchokera mʼmotomo.

Tamvani inu Aisraeli, Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi.

Choncho dziwani kuti Yehova Mulungu wanu, ndi Mulungu. Iye ndi Mulungu wokhulupirika, wosunga pangano lake la chikondi chosasinthika ku mibadomibado, kwa iwo amene amamukonda nasunga malamulo ake. Koma iwo amene amamuda adzawabwezera powawononga pamaso pawo; sadzachedwa kuwabwezera iwo amene amadana naye.

Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu, Ambuye wa ambuye, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, amene sakondera ndipo salandira ziphuphu.

Iye ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro, njira zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupirika amene salakwitsa, Iye ndiye wolungama ndi wosalakwa.

Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu, ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu, adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’

“Palibe wina woyera ngati Yehova, palibe wina koma inu nokha, palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu.

“Kodi Mulungu angakhaledi pa dziko lapansi? Mlengalenga ngakhale kumwamba kwenikweni, sikungakukwaneni. Nanga kuli bwanji ndi Nyumba iyi imene ndamanga!

Koma Yehova anawachitira chifundo Aisraeliwo ndi kukhudzika ndi zomwe zinkawachitikira chifukwa cha pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Mpaka lero lino Iye sanafune kuwawononga kapena kuwachotsa pamaso pake.

Yamikani Yehova, pakuti Iye ndi wabwino; chikondi chake chikhala mpaka muyaya.

“Ndipo iwe mwana wanga Solomoni, umvere Mulungu wa abambo ako, umutumikire ndi mtima wodzipereka kwathunthu ndi mtima wako wonse, pakuti Yehova amasanthula mtima wa aliyense, ndipo amadziwa maganizo aliwonse a munthu. Ngati ufunafuna Yehova, Iye adzapezeka; koma ngati umutaya, Iye adzakukana kwamuyaya.

Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu, ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola. Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu. Wanu, Inu Yehova ndi ufumu; Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse. Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu; Inu ndinu wolamulira zinthu zonse. Mʼdzanja lanu muli nyonga ndi mphamvu, kukweza ndi kupereka nyonga kwa onse.

ndipo anati: “Inu Yehova, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu amene muli kumwamba? Inu mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu. Mphamvu ndi nyonga zili mʼmanja mwanu, ndipo palibe amene angalimbane nanu.

Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, ndinu wachifundo, pakuti ndife otsala amene tapulumuka monga mmene zilili lero lino. Ife tayima pamaso panu ngakhale tikudziwa kuchimwa kwathu pakuti palibe munthu amene angathe kuyima pamaso panu chifukwa cha machimo ake.”

Inu nokha ndiye Yehova. Munalenga kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, zolengedwa zonse zimene zili mʼmenemo. Munalenga dziko ndi zonse zokhalamo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo. Zonse mumazisunga ndi moyo ndipo zonse za kumwamba zimakupembedzani.

“Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu? Kodi ungafufuze malire a nzeru za Wamphamvuzonse?

“Ndikudziwa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse; chimene mufuna kuchita wina sangaletse konse.

Wokhala mmwamba akuseka; Ambuye akuwanyoza iwowo.

Mulungu amaweruza molungama, Mulungu amene amaonetsa ukali wake tsiku ndi tsiku.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Chitsiru chimati mu mtima mwake, “Kulibe Mulungu.” Oterewa ndi oyipa ndipo ntchito zawo ndi zonyansa; palibe amene amachita zabwino. Yehova kumwamba wayangʼana pansi, kuyangʼana anthu onse kuti aone ngati alipo wina wanzeru, amene amafunafuna Mulungu. Onse atembenukira kumbali, onse pamodzi asanduka oyipa; palibe amene amachita zabwino, palibiretu ndi mmodzi yemwe.

Onetsani kudabwitsa kwa chikondi chanu chachikulu, Inu amene mumapulumutsa ndi dzanja lanu lamanja iwo amene amathawira kwa inu kuchoka kwa adani awo.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu; thambo limalalikira ntchito za manja ake.

Salimo la Davide. Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

Liwu la Yehova ndi lamphamvu; liwu la Yehova ndi laulemerero.

Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi ndi kuona anthu onse; kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira onse amene amakhala pa dziko lapansi.

Oyipa amakonza chiwembu kutsutsana ndi olungama ndipo amawakukutira mano; koma Ambuye amaseka oyipa pakuti Iye amadziwa kuti tsiku lawo likubwera.

Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi; imbirani Iye salimo la matamando. Mulungu akulamulira mitundu ya anthu; Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.

Musandichotse pamaso panu kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.

Ndiyankheni Inu Yehova mwa ubwino wanu wa chikondi chanu; mwa chifundo chanu chachikulu tembenukirani kwa ine.

Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake. Ameni ndi Ameni.

Inu Ambuye, ndinu wokhululuka ndi wabwino, wodzaza ndi chikondi kwa onse amene amayitana Inu.

Pakati pa milungu palibe wina wofanana nanu Ambuye; palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu. Mitundu yonse ya anthu imene munayipanga idzabwera ndi kudzalambira pamaso panu Ambuye; iwo adzabweretsa ulemerero pa dzina lanu. Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa; Inu nokha ndiye Mulungu.

Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.

Chilungamo ndi chiweruzo cholungama ndiye maziko a mpando wanu waufumu; chikondi ndi kukhulupirika zimayenda patsogolo panu.

Mapiri asanabadwe, musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse, kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.

Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi; ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.

Yehova akulamulira, mitundu ya anthu injenjemere; Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi, dziko lapansi ligwedezeke.

Kwezani Yehova Mulungu wathu ndipo mumulambire pa phiri lake loyera, pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.

Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya; kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.

Pachiyambi Inu munakhazikitsa maziko a dziko lapansi ndipo mayiko akumwamba ndi ntchito ya manja anu. Izi zidzatha, koma Inu mudzakhalapo; zidzatha ngati chovala. Mudzazisintha ngati chovala ndipo zidzatayidwa. Koma Inu simusintha, ndipo zaka zanu sizidzatha.

Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka.

Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa; monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo, koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.

Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa, ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo; iwo amene amasunga pangano lake ndi kukumbukira kumvera malangizo ake. Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba ndipo ufumu wake umalamulira onse.

Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri; mwavala ulemerero ndi ufumu. Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala; watambasula miyamba ngati tenti

Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake ndi chosatha.

Yehova wakwezeka pa anthu a mitundu yonse, ulemerero wake ndi woposa mayiko akumwamba.

Mulungu wathu ali kumwamba; Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.

Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera, kumwamba ndi dziko lapansi, ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.

Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino. Pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

Yamikani Ambuye wa ambuye, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

Amene mwachidziwitso chake anapanga mayiko akumwamba, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

Yamikani Mulungu wakumwamba, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

Kodi ndingapite kuti kufuna kuzemba Mzimu wanu? Kodi ndingathawire kuti kuchoka pamaso panu? Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko; ndikakagona ku malo a anthu akufa, Inu muli komweko.

Yehova ndi wamkulu ndi woyenera matamando onse; ukulu wake palibe angawumvetsetse.

Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu, ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.

Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika.

Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse, ndi wokonda zonse zimene anazipanga. Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana, onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi.

Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo; Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya. Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala. Yehova amamasula amʼndende,

Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi, ndipo iliyonse amayitchula dzina. Yehova ndi wamkulu ndi wamphamvu kwambiri; nzeru zake zilibe malire.

Ndimakonda amene amandikonda, ndipo amene amandifunafuna amandipeza.

Maso a Yehova ali ponseponse, amayangʼana pa oyipa ndi abwino omwe.

Kodi ndani anakwera kumwamba ndi kutsikako? Ndani anafumbatapo mphepo mʼmanja mwake? Ndani anamanga madzi mʼchovala chake? Ndani anakhazikitsa mathero onse a dziko lapansi? Dzina lake ndani? Ndiwuze ngati ukudziwa! Ndipo mwana wake dzina lake ndani?

Lowani mʼmatanthwe, bisalani mʼmaenje, kuthawa kuopsa kwa Yehova ndi ulemerero wa ufumu wake!

Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti “Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse. Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”

Yehova Wamphamvuzonse ndiye amene uyenera kumuona kuti ndi woyera, ndiye amene uyenera kumuopa, ndiye amene uyenera kuchita naye mantha,

Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife, ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake. Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.

Mzimu wa Yehova udzakhala pa iye Mzimu wanzeru ndi wa kumvetsa zinthu, Mzimu wauphungu ndi wamphamvu, Mzimu wachidziwitso ndi wakuopa Yehova.

Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima, iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo. Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!

Pakuti Yehova ndi woweruza wathu, Yehova ndiye wotilamulira, Yehova ndiye mfumu yathu; ndipo ndiye amene adzatipulumutse.

Pamaso pa Yehova mitundu yonse ya anthu ili ngati chinthu chopandapake; Iye amayiwerengera ngati chinthu chopanda phindu ndi cha chabechabe. Kodi tsono Mulungu mungamuyerekeze ndi yani? Kodi mungamufanizire ndi chiyani?

Yehova amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba ndiye analenga dziko lapansi, Iye amaona anthu a dziko lapansi ngati ziwala. Ndipo anafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchinga, nayikunga ngati tenti yokhalamo.

Kodi simukudziwa? Kodi simunamve? Yehova ndiye Mulungu wamuyaya, ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi. Iye sadzatopa kapena kufowoka ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.

“Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo! Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense kapena matamando anga kwa mafano.

Yehova akunena kuti, “Inu Aisraeli ndinu mboni zanga, ndi mtumiki wanga amene ndinakusankha, kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira, ndipo mudzamvetsa kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipanapangidwepo mulungu wina, ngakhale pambuyo panga sipadzakhalaponso wina.” Akutero Yehova, “Ine, Inetu ndine Yehova, ndipo palibe Mpulumutsi wina koma Ine ndekha.

“Yehova Mfumu ndi Mpulumutsi wa Israeli, Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndine woyamba ndi wotsiriza; palibenso Mulungu wina koma Ine ndekha.

Yehova Mpulumutsi wanu, amene anakuwumbani mʼmimba ya amayi anu akuti: “Ine ndine Yehova, amene anapanga zinthu zonse, ndinatambasula ndekha zinthu zakuthambo, ndinayala ndekha dziko lapansi.

kotero kuti kuchokera kummawa mpaka kumadzulo anthu adzadziwa kuti palibe wina koma Ine ndekha. Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina. Ndimalenga kuwala ndi mdima, ndimabweretsa madalitso ndi tsoka; ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.

Yehova analenga zinthu zakumwamba, Iye ndiye Mulungu; amene akulenga dziko lapansi, ndi kulikhazikitsa, sanalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma analipanga kuti anthu akhalemo. Iyeyu akunena kuti: Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.

Fotokozani mlandu wanu, mupatsane nzeru nonse pamodzi. Kodi ndani ananeneratu zimenezi kalekale? Ndani anazifotokozeratu zimenezi nthawi yamakedzana? Kodi si Ineyo Yehova? Ndipo palibenso Mulungu wina kupatula Ine, Mulungu wolungama ndi Wopulumutsa, palibenso wina kupatula Ine. “Tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke, inu anthu onse a pa dziko lapansi, pakuti Ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.

Kumbukirani zinthu zakale zinthu zamakedzana; chifukwa Ine ndine Mulungu ndipo palibe wina ofanana nane. Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe. Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike. Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi. Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.

Pakuti Mlengi wako ali ngati mwamuna wako, dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse. Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wanu; dzina lake ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi.

“Pakuti maganizo anga siwofanana ndi maganizo anu, ngakhale njira zanu si njira zanga,” akutero Yehova. “Monga momwe mlengalenga muli kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nʼzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.

Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo, akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika, koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.

Yehova akuti, “Kumwamba ndi mpando wanga waufumu ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga. Tsono nyumba ili kuti yomwe mundimangire, ndipo malo ali kuti amene inu mungandikonzere kuti ndizipumuliramo?

Koma Yehova ndiye Mulungu woona; Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo, Mfumu yamuyaya. Akakwiya, dziko limagwedezeka; anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo.

Koma Mulungu analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake; Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake ndipo anayala thambo mwaluso lake.

“Choncho Ine ndidzawaphunzitsa, kokha kano kuti adziwe za mphamvu yanga ndi za nyonga zanga. Pamenepo adzadziwa kuti dzina langa ndi Yehova.

Kodi wina angathe kubisala Ine osamuona?” “Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?” Akutero Yehova.

Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati, “Ine ndakukondani ndi chikondi chopanda malire. Nʼchifukwa chake ndipitiriza kukukondani.

Sipadzafunikanso kuti wina aphunzitse mnzake, kapena munthu wina kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, ‘Mudziwe Yehova,’ chifukwa onse adzandidziwa Ine, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,” akutero Yehova. “Ndidzawakhululukira zoyipa zawo ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”

“Aa, inu Ambuye Yehova, munalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Munazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo palibe chokulakani. Mumaonetsa chikondi chanu kwa anthu osawerengeka koma mumalanga ana chifukwa cha machimo a makolo awo. Inu ndinu Mulungu Wamkulu ndi Wamphamvu. Dzina lanu ndinu Yehova Wamphamvuzonse.

“Taonani, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse. Kodi chilipo chinthu choti Ine nʼkundikanika?

ndipo anati: “Litamandike dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi; nzeru ndi mphamvu zonse ndi zake. Amasintha nthawi ndi nyengo; amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso. Amapatsa nzeru kwa anzeru ndi chidziwitso kwa ozindikira zinthu. Amavumbulutsa zinthu zozama ndi zobisika; amadziwa zimene zili mu mdima, ndipo kuwunika kumakhala ndi Iye.

Ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya; ndidzakutomera mwachilungamo, mwaungwiro, mwachikondi ndi mwachifundo.

Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Yehova ndiye dzina lake lotchuka!

Iye amene amawumba mapiri, amalenga mphepo, ndipo amawululira munthu za mʼmaganizo ake, Iye amene amasandutsa usana kuti ukhale mdima, ndipo amayenda pa zitunda za dziko lapansi, dzina lake ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.

Yehova ndi Mulungu wansanje ndiponso wobwezera; Yehova amabwezera ndipo ndi waukali. Yehova amabwezera adani ake ndipo ukali wake umakhala nthawi zonse pa adani akewo. Yehova sakwiya msanga koma ndi wa mphamvu yayikulu; ndipo sadzalola kuti munthu wolakwa asalangidwe. Iye amayenda mʼkamvuluvulu ndi mʼnamondwe, ndipo mitambo ndi fumbi la ku mapazi ake.

Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova, monga momwe madzi amadzazira nyanja.

Yehova Mulungu wako ali pakati pako, ali ndi mphamvu yopulumutsa. Adzakondwera kwambiri mwa iwe, adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake, adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe.”

Koma ndikuwuzani kuti musalumbire ndi pangʼono pomwe kutchula kumwamba chifukwa kuli mpando waufumu wa Mulungu. Kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa ndi chopondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa ndi mzinda wa mfumu yayikulu.

Nʼchifukwa chake, inu khalani angwiro monga Atate anu akumwamba ali wangwiro.”

“Chifukwa chake pempherani motere: “ ‘Atate athu akumwamba, dzina lanu lilemekezedwe,

Ndipo musatitengere kokatiyesa; koma mutipulumutse kwa woyipayo.’

Pa nthawi imeneyo Yesu anati, “Ine ndikukuyamikani Inu Atate Ambuye akumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa Inu mwawabisira zinthu izi anzeru ndi ophunzira ndi kuziwulula kwa ana angʼonoangʼono.

Yesu anawayangʼana iwo nati, “Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka.”

‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo?’ Iyeyo si Mulungu wa akufa koma wa amoyo.”

“Pamene Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wake, pamodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pa mpando waufumu mu ulemerero wakumwamba. Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa pamaso pake, ndipo adzawalekanitsa iwo wina ndi mnzake monga mʼbusa amalekanitsa nkhosa ndi mbuzi.

Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine. Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera,

Yesu anawayangʼana ndipo anati, “Kwa munthu zimenezi nʼzosatheka, koma osati ndi Mulungu; zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu.”

Yesu anayankha kuti, “Lamulo loposa onse ndi ili: ‘Tamvani inu Aisraeli! Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi!

Yesu anati, “Ndine, ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera mʼmitambo ya kumwamba.”

Yesu, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anachoka ku mtsinje wa Yorodani ndipo anatsogozedwa ndi Mzimu Woyerayo kupita ku chipululu,

Khalani achifundo, monga momwe Atate anu ali achifundo.”

Nthawi imeneyo Mzimu Woyera anadzaza Yesu ndi chimwemwe ndipo anati, “Ine ndikulemekeza Inu, Atate Ambuye a kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwawabisira anthu anzeru ndi ophunzira zinthu izi ndipo mwaziwulula kwa ana aangʼono. Inde, Atate, pakuti munachita zimenezi mwachifuniro chanu.

Yesu anawawuza kuti, “Pamene mukupemphera muzinena kuti: “ ‘Atate, dzina lanu lilemekezedwe, ufumu wanu ubwere.

Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu. Mawuwa anali ndi Mulungu pachiyambi. Zinthu zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo popanda Iye sikukanakhala kanthu kalikonse kolengedwa.

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha.

Atate amakonda Mwana ndipo apereka zonse mʼmanja mwake.

Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi.”

Kenaka Yesu ananenetsa kuti, “Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu.

Ine ndine chakudya chamoyo.

Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo.”

Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”

Ine ndikudzichitira ndekha umboni; ndipo mboni inanso ndi Atate amene anandituma.”

Koma Iye anapitiriza kuti, “Inu ndi ochokera pansi pano. Ine ndine wochokera kumwamba. Inu ndinu anthu a dziko la pansi. Ine sindine wa dziko lapansi lino.

Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuzani choonadi, Abrahamu asanabadwe, Ine Ndine!”

“Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.

Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo.

Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine. Mukanandidziwadi Ine, mukanadziwanso Atate anga. Kuyambira tsopano, mukuwadziwa ndipo mwawaona.”

Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani.

Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.

Pamene Yesu anati, “Ndine,” iwo anabwerera mʼmbuyo ndi kugwa pansi.

Kenaka iwo anapemphera nati, “Ambuye mukudziwa mtima wa aliyense. Tionetseni amene mwamusankha mwa awiri awa

“Komatu, Wammwambamwambayo sakhala mʼnyumba zomangidwa ndi anthu. Monga mneneri akunena kuti, “ ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu, ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Kodi mudzandimangira nyumba yotani? Akutero Ambuye. Kapena malo opumuliramo Ine ali kuti?

“Mulungu amene analenga dziko lapansi ndiponso zonse zili mʼmenemo ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndipo sakhala mʼnyumba zachipembedzo zomangidwa ndi manja.

Mkwiyo wa Mulungu ukuonekera kuchokera kumwamba. Ukutsutsana ndi kusapembedza konse ndi kuyipa kwa anthu amene amapondereza choonadi mwa chikhalidwe chawo choyipa. Za Mulungu zimene zingathe kudziwika, ndi zomveka bwino kwa iwo pakuti Mulungu anazionetsera kwa iwo. Pakuti kuyambira pamene dziko lapansi linalengedwa, zinthu zosaoneka za Mulungu, mphamvu zake zosatha ndi chikhalidwe cha umulungu, zakhala zikuoneka bwinobwino. Akhala akuzindikira poona zimene Mulungu analenga, kotero kuti anthu sangathe kuwiringula.

Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera.

Pakuti ine ndatsimikiza ndi mtima wonse kuti ngakhale imfa, kapena moyo, ngakhale angelo, kapena ziwanda, ngakhale zinthu zilipo, kapena zili mʼtsogolo, kapena mphamvu zina, ngakhale kutalika, kapena kuya, kapena chilichonse mʼchilengedwe chonse, sizingathe kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Aa! Nzeru za Mulungu ndi chidziwitso chake ndi zozama kwambiri! Ndani angazindikire maweruzidwe ake, ndipo njira zake angazitulukire ndani? “Kodi wadziwa ndani maganizo a Ambuye? Kapena ndani anakhalapo mlangizi wake?” “Kodi ndani anapereka mphatso kwa Mulungu, kuti Mulunguyo amubwezere iye?” Pakuti zinthu zonse nʼzochokera kwa Iye, nʼzolengedwa ndi Iye ndipo zimabweretsa ulemerero kwa Iye. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya! Ameni.

kuti chikhulupiriro chanu chisatsamire pa nzeru ya anthu koma pa mphamvu za Mulungu.

Pakuti ufumu wa Mulungu si mawu chabe koma mphamvu.

koma kwa ife pali Mulungu mmodzi yekha, Atate, zinthu zonse zinachokera mwa Iye ndipo ndife ake. Komanso pali Ambuye mmodzi Yesu Khristu kumene zinthu zonse zinachokera ndipo mwa Iye ife tili ndi moyo.

imene inagwira ntchito pamene Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa, namukhazika Iye ku dzanja lake lamanja mʼdziko la kumwamba. Anamukhazika pamwamba pa ulamuliro onse ndi mafumu, mphamvu ndi ufumu, ndiponso pamwamba pa dzina lililonse limene angalitchule, osati nthawi ino yokha komanso imene ikubwerayo. Ndipo Mulungu anayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake ndi kumusankha Iyeyo kukhala mutu pa chilichonse chifukwa cha mpingo, umene ndi thupi lake, chidzalo cha Iye amene adzaza chilichonse mu njira iliyonse.

Koma chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ndi olemera mʼchifundo,

Pakuti mwa Iye, ife tonse titha kufika kwa Atate mwa Mzimu mmodzi.

Mulungu mmodzi ndi Atate a onse, ndipo ali mwa onse.

Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa.

Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri, ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire, kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko, ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye kuchitira ulemu Mulungu Atate.

Mwanayu ndiye chithunzi cha Mulungu wosaonekayo. Iye ndiye Mwana wake woyamba kubadwa ndi wolamulira zolengedwa zonse. Pakuti zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye. Zinthu zakumwamba ndi za pa dziko lapansi, zooneka ndi zosaoneka, maufumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu. Zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye ndipo anazilengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse zisanalengedwe ndipo zinthu zonse zimamangika pamodzi mwa Iye. Iye ndiyenso mutu wa thupi, limene ndi mpingo. Iye ndiye chiyambi chake, woyamba kuuka kwa akufa, kuti Iyeyo akhale wopambana zonse. Pakuti kunamukomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristu.

Pakuti mʼthupi la Khristu mumakhala umulungu wonse wathunthu. Ndipo inunso ndinu athunthu mwa Khristu. Iye ndiye mtsogoleri wa pamwamba pa maufumu onse ndi maulamuliro wonse.

Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni.

Ndiye yekha wosafa ndipo amakhala mʼkuwala koopsa. Mulungu amene munthu aliyense sanamuone. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Ameni.

Kale lija Mulungu ankayankhula ndi makolo athu pa nthawi zosiyanasiyana ndiponso mwa njira zosiyanasiyana kudzera mwa aneneri. Koma masiku otsiriza ano, Mulungu wayankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Mwanayu anamusankha kuti akhale mwini wa zinthu zonse, ndiponso Mulungu analenga dziko lonse kudzera mwa Iye. Mwanayo ndiye kuwala kwa ulemerero wa Mulungu, chithunzithunzi chenicheni cha khalidwe lake. Iyeyu amachirikiza zinthu zonse ndi mphamvu ya mawu ake. Iye atayeretsa anthu kuchoka ku machimo awo, anakhala pansi kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu waulemerero.

Koma za Mwana wake akuti, “Inu Mulungu, mpando wanu waufumu udzakhala mpaka muyaya, ndipo mudzaweruza molungama mu ufumu wanu.

Palibe kanthu kobisika pamaso pa Mulungu. Zinthu zonse zili poyera ndi zovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.

Pakuti Mulungu wathu ndi moto wonyeketsa.

Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse.

Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda.

Mumakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi yekha. Mumachita bwino. Komatu ngakhale ziwanda zimakhulupirira zimenezi ndipo zimanjenjemera ndi mantha.

amene anapita kumwamba ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu komwe angelo ndi maulamuliro ndi amphamvu amamvera Iye.

Pakuti Iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate atamufikira mawu ochokera ku ulemerero wa ukulu akuti, “Uyu ndi mwana wanga amene Ine ndimukonda, amene ndimakondwera naye kwambiri.”

Uthenga umene tinamva kwa Iye ndipo tikuwulalikira kwa inu ndi uwu: Mulungu ndiye kuwunika ndipo mwa Iye mulibe mdima konse.

Aliyense amene alibe chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.

Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye.

Pakuti pali atatu amene amachitira umboni. Mzimu Woyera, madzi ndi magazi; ndipo atatu amavomerezana.

Tikudziwa kuti Mwana wa Mulungu anafika ndipo anatipatsa nzeru, kuti timudziwe Iye amene ali woona. Ndipo ife tili mwa Iye amene ndi woona, Mwana wake, Yesu Khristu. Iye ndi Mulungu woona ndi moyo wosatha.

kwa Mulungu yekhayo, Mpulumutsi wathu, kwa Iye kukhale ulemerero, ukulu, mphamvu ndi ulamuliro, mwa Yesu Khristu Ambuye athu, kuyambira isanayambe nthawi, tsopano mpaka muyaya. Ameni.

“Ine ndine Alefa ndi Omega,” akutero Ambuye Mulungu Wamphamvuzonseyo “amene muli, amene munalipo, ndi amene mudzakhalapo.”

“Lembera mngelo wampingo wa ku Sarde kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene amasunga mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri. Iye akuti: Ndimadziwa ntchito zako; umadziwika kuti ndiwe wamoyo koma ndiwe wakufa.

Nthawi yomweyo ndinatengedwa ndi Mzimu Woyera, ndipo patsogolo panga ndinaona mpando waufumu wina atakhalapo. Ndipo amene anakhalapoyo anali wa maonekedwe ngati miyala ya jasipa ndi sardiyo. Utawaleza wooneka ngati simaragido unazinga mpando waufumuwo. Kuzungulira mpando waufumuwu panalinso mipando ina yaufumu yokwana 24 ndipo panakhala akuluakulu 24 atavala zoyera ndipo anavala zipewa zaufumu zagolide pamutu. Kumpando waufumuwo kunkatuluka mphenzi, phokoso ndi mabingu. Patsogolo pake pa mpando waufumuwo panali nyale zisanu ndi ziwiri zoyaka. Iyi ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu. Patsogolo pa mpando waufumu pomwepo panalinso ngati nyanja yagalasi yonyezimira ngati mwala wa krustalo. Pakatinʼpakati, kuzungulira mpando waufumuwo panali zamoyo zinayi zokhala ndi maso ponseponse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe. Chamoyo choyamba chinali ngati mkango, chachiwiri chinali ngati mwana wangʼombe, chachitatu chinali ndi nkhope ngati munthu, chachinayi chinali ngati chiwombankhanga chowuluka. Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo chinali ndi maso ponseponse ndi mʼkati mwa mapiko momwe. Usana ndi usiku zimanena mosalekeza kuti, “Woyera, woyera, woyera ndi Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, amene munali, amene muli ndi amene mukubwera.” Nthawi zonse zamoyozo zimapereka ulemerero, ulemu ndi mayamiko kwa uja wokhala pa mpando waufumu, amene ali ndi moyo wamuyaya. Izi zikamachitika akuluakulu 24 aja amadzigwetsa pansi pamaso pa wokhala pa mpando waufumuyo, namupembedza wokhala ndi moyo wamuyayayo. Iwo amaponya pansi zipewa zawo zaufumu patsogolo pa mpando waufumu nati: “Ndinu woyeneradi kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu, Ambuye ndi Mulungu wathu, pakuti munalenga zinthu zonse, ndipo mwakufuna kwanu zinalengedwa monga zilili.”

Kenaka ndinaona Mwana Wankhosa akuoneka ngati wophedwa atayimirira pakatikati pa mpando waufumu uja ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Mwana Wankhosayo anali ndi nyanga zisanu ndi ziwiri ndi maso asanu ndi awiri omwe ndi Mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu yomwe anayitumiza ku dziko lonse lapansi.

Kenaka ndinamva mawu a cholengedwa chilichonse kumwamba, pa dziko lapansi, kunsi kwa dziko lapansi, pa nyanja ndi zonse zili mʼmenemo zikuyimba kuti, “Kwa wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa, kukhale mayamiko, ulemu, ulemerero ndi mphamvu mpaka muyaya!”

Mngeloyo anayankhula mokweza mawu kuti, “Wopani Mulungu ndi kumutamanda, chifukwa nthawi yoweruza anthu yafika. Mumupembedze Iye amene analenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi akasupe amadzi.”

Kenaka ndinamva chimene chinamveka ngati gulu lalikulu, ngati mkokomo wamadzi othamanga ndipo ngati kugunda kwakukulu kwa bingu, ndipo anati, “Haleluya! Pakuti Ambuye Mulungu wathu Wamphamvuzonse akulamulira.

Pa chovala ndi pa ntchafu pake panalembedwa dzina ili: MFUMU YA MAFUMU NDI MBUYE WA AMBUYE.

Ine sindinaone Nyumba ya Mulungu iliyonse mu mzindawo chifukwa Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse ndi Mwana Wankhosa ndiwo Nyumba yake. Palibe chifukwa choti dzuwa kapena mwezi ziwale popeza mu mzindawo ulemerero wa Mulungu ndiwo umawalamo ndipo nyale yake ndi Mwana Wankhosa uja.

Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chimaliziro ndine.

Chichewa - Chichewa - NY

NYCCL - Mawu A Mulungu Mu Chichewa Chalero - 2016

This Bible text is from Biblica Open God's Word In Contemporary Chichewa
https://open.bible/bibles/chichewa-biblica-text-bible/
provided by: Biblica Inc, available by Creative Commons CC-BY-SA-4.0,
and this new compilation is shared as www.creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0.
Languages are made available to you by www.ipedge.net