06 – Gehena

Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Gehena.

Mavesi atatu ofunika kwambiri

Nyanja inapereka amene anaferamo ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufa ake ndipo munthu aliyense anaweruzidwa monga mwa ntchito zake. Kenaka imfa ndi Hade zinaponyedwa mʼnyanja ya moto. Nyanja yamoto ndiyo imfa yachiwiri. Ngati dzina la wina aliyense silinapezeke mʼBuku Lamoyo, anaponyedwa mʼnyanja yamoto.

Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu

Umu ndi mmene kudzakhalira pakutha kwa dziko. Angelo adzabwera ndi kulekanitsa oyipa ndi olungama. Ndipo oyipa adzawaponya mʼngʼanjo ya moto kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”

Mavesi onse motsatira dongosolo lolondola – 123 ndime

Yehova anamuyankha Mose kuti, “Ndidzafuta mʼbuku aliyense amene wandichimwira. Tsopano pita ukawatsogolere anthu kumalo kumene ine ndinanena, ndipo mngelo wanga adzakutsogolerani. Komabe, nthawi yanga ikadzafika kuti ndiwalange, ndidzawalanga chifukwa cha tchimo lawo.”

Yehova sadzamukhululukira. Mkwiyo ndi nsanje ya Yehova zidzamuyakira munthuyo. Matemberero onse wolembedwa mʼbukuli adzamugwera iye ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pa dziko lapansi.

Pakuti mkwiyo wanga wayaka ngati moto, umene umayaka mpaka ku dziko la anthu akufa. Motowo udzanyeketsa dziko lapansi ndi zokolola zake ndipo udzapsereza maziko a mapiri.

Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka, momwemonso munthu amene walowa mʼmanda sabwerera.

Zakuti munthu woyipa amasungidwa chifukwa cha tsiku la tsoka, kuti amapulumutsidwa chifukwa cha tsiku la ukali wa Mulungu?

Oyipa amabwerera ku manda, mitundu yonse imene imayiwala Mulungu.

chifukwa Inu simudzandisiya ku manda, simudzalola kuti woyera wanu avunde.

Anandimanga ndi zingwe za ku manda; misampha ya imfa inalimbana nane.

Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse; dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu. Pa nthawi ya kuonekera kwanu mudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha. Mu ukali wake Yehova adzawameza, ndipo moto wake udzawatha.

Mulole imfa itenge adani anga mwadzidzidzi; alowe mʼmanda ali amoyo pakuti choyipa chili pakati pawo.

Iwo afufutidwe mʼbuku la amoyo ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.

Iwo amene amadana ndi Yehova akanakhwinyata pamaso pake, ndipo chilango chawo chinakakhala mpaka kalekale.

Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu kwa ine; mwandipulumutsa ku malo ozama a manda.

Munthu wopanda nzeru sadziwa, zitsiru sizizindikira, kuti ngakhale anthu oyipa aphuka ngati udzu ndipo anthu onse ochita zoyipa apindula, adzawonongedwa kwamuyaya.

Ena anakhala mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu, amʼndende ovutika mʼmaunyolo achitsulo, pakuti iwowo anawukira mawu a Mulungu ndi kunyoza uphungu wa Wammwambamwamba.

Yehova amayangʼana onse amene amamukonda koma adzawononga anthu onse oyipa.

Koma amunawo sadziwa kuti akufa ali kale komweko, ndi kuti alendo ake alowa kale mʼmanda akuya.

Manda ndi chiwonongeko ndi zosabisika pamaso pa Yehova, nanji mitima ya anthu!

Munthu wanzeru amatsata njira yopita ku moyo kuti apewe malo okhala anthu akufa.

Usaleke kumulangiza mwana; ngati umulanga ndi chikwapu sadzafa. Ukamukwapula ndi tsatsa udzapulumutsa moyo wake.

Manda sakhuta, nawonso maso a munthu sakhuta.

Basi zonse zamveka; mathero a nkhaniyi ndi awa: uziopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wa anthu onse. Pakuti Mulungu adzaweruza zochita zonse, kuphatikizanso zinthu zonse zobisika, kaya zabwino kapena zoyipa.

Mulungu, Kuwala kwa Israeli, adzakhala ngati moto, Woyera uja wa Israeli adzakhala ngati malawi a moto. Motowo udzawatentha ndi kuwapsereza ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi. Ankhondo ake adzawonongedwa ngati nkhalango yayikulu ndi ngati nthaka yachonde.

Ndipo kuopa Yehova ndiye chidzakhale chinthu chomukondweretsa. Iye sadzaweruza potsata zooneka pamaso, kapena kugamula mlandu potsata zakumva; koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo, adzaweruza mwachilungamo mlandu wa anthu osauka a dziko lapansi. Iye adzakantha dziko lapansi ndi mawu ake; atalamula Iyeyu anthu oyipa adzaphedwa.

Lirani mofuwula, pakuti tsiku la Yehova layandikira; lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse. Zimenezi zinafowoketsa manja onse, mtima wa munthu aliyense udzachokamo. Anthu adzagwidwa ndi mantha aakulu, zowawa ndi masautso zidzawagwera; adzamva zowawa zonga amamva mayi pobereka. Adzayangʼanana mwamantha, nkhope zawo zikufiira ngati malawi amoto. Taonani, tsiku la Yehova likubwera, tsiku lopanda chisoni, lawukali ndi lamkwiyo; kudzasandutsa dziko kuti likhale chipululu ndi kuwononga anthu ochimwa a mʼmenemo. Nyenyezi zakumwamba ndiponso zonse zamlengalenga sizidzaonetsa kuwala kwawo. Dzuwa lidzada potuluka, ndipo mwezi sudzawala konse. Ndidzalanga dziko lonse chifukwa cha zolakwa zake, anthu oyipa ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo. Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza, ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.

Tsono ndidzagwedeza miyamba ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake. Izi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Wamphamvuzonse pa tsiku la mkwiyo wake woopsa.

Ku manda kwatekeseka kuti akulandire ukamabwera; mizimu ya anthu akufa, aja amene anali atsogoleri a dziko lapansi, yadzutsidwa. Onse amene anali mafumu a mitundu ya anthu ayimiritsidwa pa mipando yawo. Onse adzayankha; adzanena kwa iwe kuti, “Iwenso watheratu mphamvu ngati ife; Iwe wafanana ndi ife.” Ulemerero wako wonse walowa mʼmanda, pamodzi ndi nyimbo za azeze ako; mphutsi zayalana pogona pako ndipo chofunda chako ndi nyongolotsi.

Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mʼbandakucha! Wagwetsedwa pansi pa dziko lapansi, Iwe amene unagonjetsapo mitundu ya anthu! Mu mtima mwako unkanena kuti, “Ndidzakwera mpaka kumwamba; ndidzakhazika mpando wanga waufumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pa mpando waufumu pa phiri losonkhanirako, pamwamba penipeni pa phiri la kumpoto. Ndidzakwera pamwamba pa mitambo; ndidzafanana ndi Wammwambamwamba.” Koma watsitsidwa mʼmanda pansi penipeni pa dzenje.

Iwo tsopano sadzadzukanso; mizimu yawo sidzabwera kudzativutitsa pakuti mwawalanga ndipo mwawawononga; palibenso amene amawakumbukira.

Taonani, Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala; akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo awo. Dziko lapansi lidzawulula magazi amene anakhetsedwa pa dzikolo; dziko lapansi silidzabisanso mitembo ya anthu ophedwa.

Motowo sudzazimitsidwa usiku ndi usana; utsi wake udzafuka kosalekeza. Dzikolo lidzakhala chipululu pa mibado ndi mibado; palibe ndi mmodzi yemwe amene adzadutsemo.

Pakuti akumanda sangathe kukutamandani, akufa sangayimbe nyimbo yokutamandani. Iwo amene akutsikira ku dzenje sangakukhulupirireni.

Taonani, Yehova akubwera ngati moto, ndipo magaleta ake ali ngati kamvuluvulu; Iye adzaonetsa mkwiyo wake nadzalanga adani ake ndi malawi amoto. Pakuti Yehova adzalanga anthu onse ndi moto ndi lupanga, Yehova adzapha anthu ambiri.

“Akamachoka adzaona mitembo ya anthu amene anandiwukira Ine. Mphutsi zawo sizidzafa, kapena moto wawo sudzazimitsidwa. Anthu a mitundu ina yonse powaona adzanyansidwa nawo.”

Pakuti moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa abambo ndi wanga, wamwananso ndi wanga. Munthu wochimwa ndi amene adzafe.

“Ndinapitiriza kuyangʼanitsitsa chifukwa cha mawu odzitamandira amene nyanga ija inkayankhula. Ndili chiyangʼanire choncho chirombo chachinayi chija chinaphedwa ndipo thupi lake linawonongedwa ndi kuponyedwa mʼngʼanjo ya moto.

Idzayankhula motsutsana ndi Wammwambamwamba ndipo adzazunza oyera mtima ndi kusintha masiku azikondwerero ndi malamulo. Oyera mtimawo adzalamulidwa ndi mfumuyi kwa zaka zitatu ndi theka. “ ‘Koma bwalo lidzapereka chiweruzo, ndipo mphamvu zake zidzalandidwa ndi kuwonongedwa kotheratu mpaka muyaya.

Ambiri mwa amene akugona mʼnthaka adzadzuka: ena adzapita ku moyo wosatha, ena ku malo amanyazi ndi chilango chosatha.

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndithu tsiku likubwera; lidzayaka ngati ngʼanjo. Anthu onse odzikuza, ndi aliyense ochita zoyipa adzapsa ngati chiputu, ndipo pa tsiku limene likubweralo adzapserera ndi moto. Sipadzatsalira muzu kapena nthambi.

Koma iye ataona Afarisi ndi Asaduki ambiri akubwera kumene ankabatiza, anawawuza kuti, “Ana a njoka inu! Ndani anakuchenjezani kuthawa mkwiyo umene ukubwera?

Tikukamba pano nkhwangwa yayikidwa kale pa mizu ya mitengo, ndipo mtengo umene subala chipatso chabwino udulidwa ndi kuponyedwa pa moto.

Mʼdzanja lake muli chopetera ndipo adzayeretsa popunthirapo pake nadzathira tirigu wake mʼnkhokwe ndi kutentha zotsalira zonse ndi moto wosazima.”

“Munamva kuti kunanenedwa kwa anthu kale kuti, ‘Usaphe ndipo kuti aliyense amene apha munthu adzaweruzidwa.’ Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wokwiyira mʼbale wake adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene wonena mʼbale wake kuti, ‘Ndiwe wopanda phindu,’ adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu lalikulu. Ndipo aliyense amene anganene mnzake ‘wopandapake’ adzatengeredwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene angamunene mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe,’ adzaponyedwa ku gehena.

Ngati diso lako lakumanja likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena.

“Lowani pa chipata chopapatiza. Pakuti chipata cholowera kuchiwonongeko nʼchachikulu ndipo msewu wake ndi waukulunso. Ndipo anthu ambiri amalowera pamenepo. Koma chipata ndi chopapatiza ndi msewu ndi waungʼono umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene ayipeza njirayo.

Mtengo uliwonse umene subala chipatso chabwino umadulidwa ndi kuponyedwa pa moto. Momwemonso, ndi zipatso zawo iwo mudzawazindikira.

“Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine pa tsikulo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinkanenera mʼdzina lanu ndi mʼdzina lanunso tinkatulutsa ziwanda ndi kuchita zodabwitsa zambiri?’ Pamenepo ndidzawawuza momveka bwino kuti, ‘Sindinakudziweni inu. Chokani kwa Ine, inu ochita zoyipa!’

Koma eni ake ufumuwo adzaponyedwa ku mdima wakunja kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”

Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena.

Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zomwe zili mumtima mwake ndipo munthu woyipa amatulutsanso zinthu zoyipa zomwe zili mwa iye. Ine ndikukuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro munthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mawu aliwonse wopanda pake amene anayankhula. Pakuti ndi mawu anu mudzapezeka osalakwa ndiponso ndi mawu anu mudzapezeka olakwa.”

Munda ndi dziko lapansi ndipo mbewu yabwino ndi ana a ufumu. Namsongole ndi ana a woyipayo. Ndipo amene anafesa namsongole ndi Satana. Kukolola ndiko kutha kwa dzikoli ndipo otuta ndi angelo. “Monga momwe namsongole azulidwa ndi kutenthedwa ndi moto, momwemonso kudzakhala pakutha kwa dziko. Mwana wa Munthu adzatumiza angelo ake ndipo iwo adzachotsa mu ufumu wake chilichonse chochimwitsa ndi onse amene amachita zoyipa. Adzawaponya mʼngʼanjo yamoto kumene kudzakhala kulira ndi kukuta mano.

Umu ndi mmene kudzakhalira pakutha kwa dziko. Angelo adzabwera ndi kulekanitsa oyipa ndi olungama. Ndipo oyipa adzawaponya mʼngʼanjo ya moto kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”

Ndipo Ine ndikuwuza iwe kuti ndiwe Petro ndipo pa thanthwe ili Ine ndidzamangapo mpingo wanga ndipo makomo a ku gehena sadzawugonjetsa.

Kodi munthu adzapindula chiyani ngati atapeza zonse za dziko lapansi nataya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthana ndi moyo wake? Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate ake ndi angelo ake ndipo pamenepo Iye adzapereka mphotho kwa munthu mofanana ndi zimene anachita.

Ndipo Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba.

“Koma ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana awa, amene akhulupirira Ine, kuti achimwe, kukanakhala bwino kuti iye amangiriridwe chimwala chachikulu mʼkhosi mwake ndi kumizidwa pansi pa nyanja.

Ngati dzanja lako kapena phazi lako likuchimwitsa, lidule ndi kulitaya. Ndi bwino kwa iwe kulowa mʼmoyo wosatha wolumala kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri kapena mapazi awiri ndi kukaponyedwa ku moto wosatha. Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Ndi bwino kwa iwe kuti ukalowe ku moyo wosatha ndi diso limodzi kuposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kukaponyedwa ku moto wa gehena.”

“Koma pamene mfumu inabwera kudzaona oyitanidwawo, inaona munthu amene sanavale zovala zaukwati. Inamufunsa kuti, ‘Bwenzi walowa bwanji muno wopanda zovala zaukwati?’ Munthuyo anakhala chete. “Pamenepo mfumuyo inawuza otumikira kuti, ‘Mʼmangeni manja ndi miyendo, ndipo muponyeni kunja, ku mdima kumene kudzakhale kulira ndi kukuta mano.’

“Njoka inu! Ana amamba! Mudzachithawa bwanji chilango cha gehena?

Adzamulanga koopsa ndipo adzamuyika kokhala anthu achiphamaso, kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”

“Koma pamene ankapita kukagula mafutawo, mkwati anafika. Anamwali amene anali okonzeka aja analowa naye pamodzi mʼnyumba ya phwando la ukwati. Ndipo khomo linatsekedwa. “Pambuyo pake enawo anabwera nati, ‘Ambuye! Ambuye! Titsekulireni!’ “Koma iye anayankha kuti, ‘Zoonadi, ine ndikuwuzani kuti sindikukudziwani.’

Ndipo muponyeni wantchito wopanda phinduyu kunja, ku mdima kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.’ ”

“Pamene Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wake, pamodzi ndi angelo ake onse, adzakhala pa mpando waufumu mu ulemerero wakumwamba. Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa pamaso pake, ndipo adzawalekanitsa iwo wina ndi mnzake monga mʼbusa amalekanitsa nkhosa ndi mbuzi. Adzayika nkhosa ku dzanja lake lamanja ndi mbuzi ku lamanzere.

“Pamenepo adzanena kwa akumanzere kwake kuti, ‘Chokani kwa Ine, inu otembereredwa, pitani ku moto wosatha wokonzedwera mdierekezi ndi angelo ake. Pakuti ndinali ndi njala ndipo simunandipatse chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo simunandipatse madzi akumwa, ndinali mlendo koma inu simunandilandire, ndinali wa usiwa koma simunandiveke, ndinali wodwala komanso ku ndende simunandisamalire.’ “Iwo adzayankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala kapena ludzu kapena mlendo kapena wausiwa kapena wodwala kapena mʼndende, ndipo kuti sitinakuthandizeni?’ “Iye adzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene simunachitire mmodzi wa abale anga onyozekawa simunandichitire Ine.’ “Amenewa adzapita ku chilango chosatha pamene olungama ku moyo wosatha.”

koma aliyense amene achitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa pakuti wachita tchimo losatha.”

Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake?

“Ndipo ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana angʼono awa amene akhulupirira Ine, kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala waukulu mʼkhosi mwake. Ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo ndi dzanja limodzi kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri ndi kupita ku gehena, kumene moto wake suzima. (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima). Ndipo ngati phazi lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo olumala kusiyana ndi kukhala ndi mapazi awiri ndi kuponyedwa mu gehena. (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima). Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu gehena, kumene “ ‘mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima.’

Aliyense amene akakhulupirire nabatizidwa adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira adzalangidwa.

Mʼdzanja lake muli chopetera kuti ayeretse powomberapo tirigu ndi kusonkhanitsa tirigu ndipo adzatentha zotsalira zonse ndi moto wosazimitsika.”

Yesu anamufunsa kuti, “Dzina lako ndani?” Iye anayankha kuti, “Legiyo,” chifukwa ziwanda zambiri zinalowa mwa iye. Ndipo ziwandazo zimamupempha mobwerezabwereza kuti asazitumize ku dzenje la mdima.

Kodi chabwino ndi chiti kwa munthu, kupata zonse zapansi pano, koma ndi kutaya moyo wake kapena kudziwononga iye mwini?

Kodi iwe Kaperenawo, adzakukweza mpaka kumwamba? Ayi, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa. “Womvera inu, akumvera Ine; wokana inu, akukana Ine. Ndipo wokana Ine; akukana Iye amene anandituma Ine.”

Koma Ine ndidzakuonetsani amene muyenera kumuopa: Wopani Iye, amene pambuyo pakupha thupi, ali ndi mphamvu yakukuponyani ku gehena. Inde, Ine ndikuwuzani, muopeni Iye.

Ine ndikuti, ayi! Koma ngati inu simutembenuka mtima, inunso mudzawonongeka nonse.

Wina anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndi anthu ochepa okha amene adzapulumutsidwe?” Iye anawawuza kuti, “Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza, chifukwa ndikukuwuzani kuti ambiri adzafuna kulowa koma sadzatha kutero. Nthawi yomwe mwini nyumba adzayimirira ndi kutseka chitseko, inu mudzayima kunja kugogoda ndi kudandaula kuti, ‘Bwana, tatitsekulirani khomo.’ “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera.’ “Ndipo inu mudzati, tinkadya ndi kumwa ndi inu ndipo munkaphunzitsa mʼmisewu yathu. “Koma Iye adzayankha kuti, ‘Ine sindikukudziwani ndipo sindikudziwanso kumene mwachokera. Chokereni inu nonse ochita zoyipa!’ “Mudzalira ndi kukuta mano mukadzaona Abrahamu, Isake ndi Yakobo ndi aneneri onse ali mu ufumu wa Mulungu koma inuyo mutaponyedwa kunja.

“Panali munthu wachuma amene ankavala zovala zofiirira za mtengowapatali ndipo ankakhala moyo wachisangalalo tsiku lililonse. Pa khomo la mpanda wake ankagonekapo munthu wopempha wotchedwa Lazaro, wazilonda thupi lonse ndipo ankafunitsitsa atadya zomwe zinkagwa pansi kuchokera pamene munthu wolemerayo amadyerapo. Agalu ankabweranso ndi kumanyambita zilonda zake. “Nthawi inafika imene wopemphayo anamwalira ndipo angelo anamunyamula nakamuyika mʼmanja mwa Abrahamu. Munthu wolemerayo anamwaliranso ndipo anayikidwa mʼmanda. Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake. Ndipo anafuwula kwa iye kuti, ‘Abambo Abrahamu, mundimvere chisoni ine ndipo mutumeni Lazaroyo kuti aviyike msonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikumva ululu mʼmoto muno.’ “Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo. Ndipo kuwonjezera pa zonsezi, pakati pa inu ndi ife pali chiphompho chachikulu chimene chinayikidwa, kotero kuti amene akufuna kubwera kumeneko sangathe, kapena palibe amene angawoloke kuchokera kumeneko kudzafika kuno.’ “Iye anayankha kuti, ‘Ndipo ndikupemphani inu, abambo, mutumeni Lazaro ku nyumba ya abambo anga, pakuti ine ndili ndi abale asanu. Lolani iye akawachenjeze kotero kuti asadzabwere kumalo ano amazunzo.’ “Abrahamu anayankha kuti, ‘Ali ndi Mose ndi Aneneri; aleke amvere iwo.’ “Iye anati, ‘Ayi, bambo Abrahamu, koma ngati wina ochokera kwa akufa adzapita kwa iwo, adzatembenuka mtima.’ “Anati kwa iye, ‘Ngati iwo samvera Mose ndi Aneneri, sadzakhulupirira ngakhale wina atauka kwa akufa.’ ”

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi. Aliyense wokhulupirira Iye saweruzidwa, koma aliyense wosakhulupirira waweruzidwa kale chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. Ndipo chiweruzo ndi ichi: kuwunika kunabwera mʼdziko lapansi, koma anthu anakonda mdima mʼmalo mwa kuwunikako, chifukwa ntchito zawo zinali zoyipa. Aliyense wochita zoyipa amadana ndi kuwunika, ndipo sabwera poyera chifukwa cha mantha kuti ntchito zake zingaonekere.

Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.”

“Musadabwe ndi zimenezi. Pakuti nthawi ikubwera pamene onse amene ali mʼmanda adzamva mawu ake ndi kutuluka. Iwo amene anachita zabwino adzauka ndi kupita ku moyo wosatha ndipo amene anachita zoyipa adzauka ndi kupita ku chilango chamuyaya.

Ngati wina aliyense sakhala mwa Ine, iyeyo ali ngati nthambi imene yatayidwa ndi kufota. Nthambi zotero zimatoledwa, kuponyedwa pa moto ndi kupsa.

Chifukwa simudzasiya moyo wanga kumalo a anthu akufa, ku manda, kapena kulekerera Woyerayo kuti awole.

Davide ataoneratu zimene zinali mʼtsogolo anayankhula za kuuka kwa Khristu, kuti Iye sanasiyidwe mʼmanda, ndipo thupi lake silinawole.

Mkwiyo wa Mulungu ukuonekera kuchokera kumwamba. Ukutsutsana ndi kusapembedza konse ndi kuyipa kwa anthu amene amapondereza choonadi mwa chikhalidwe chawo choyipa. Za Mulungu zimene zingathe kudziwika, ndi zomveka bwino kwa iwo pakuti Mulungu anazionetsera kwa iwo. Pakuti kuyambira pamene dziko lapansi linalengedwa, zinthu zosaoneka za Mulungu, mphamvu zake zosatha ndi chikhalidwe cha umulungu, zakhala zikuoneka bwinobwino. Akhala akuzindikira poona zimene Mulungu analenga, kotero kuti anthu sangathe kuwiringula. Ngakhale iwo anadziwa Mulungu, sanamulemekeze ngati Mulungu kapena kumuthokoza, koma maganizo awo anasanduka wopanda pake ndipo mʼmitima yawo yopusa munadzaza mdima. Ngakhale ankadzitama kuti ndi anzeru, anasanduka opusa.

Koma pakuti ndiwe wosamvera ndi wa mtima wosafuna kulapa, ukudzisungira chilango pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu, pamene chiweruzo cholungama cha Mulungu chidzaonetsedwa. Mulungu adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake. Iye adzapereka moyo wosatha kwa amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pochita ntchito zabwino mopirira. Koma Mulungu adzakhuthulira mkwiyo ndi ukali wake pa amene amachita zofuna zawo ndi kukana choonadi nʼkumatsatira zoyipa.

Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa chifukwa mwa Khristu Yesu, lamulo la Mzimu Woyera amene amapereka moyo, lawamasula ku lamulo la tchimo ndi la imfa.

Okondedwa anga, musabwezere choyipa, koma lekerani Mulungu. Pakuti kwalembedwa, “Kubwezera chilango nʼkwanga. Ndidzawalanga ndine,” akutero Ambuye.

Kwalembedwa, akutero Ambuye, “Pamene Ine ndili ndi moyo, aliyense adzandigwadira ndipo lilime lililonse lidzavomereza Mulungu.” Choncho tsopano, aliyense wa ife adzafotokoza yekha kwa Mulungu.

Pakuti tonsefe tiyenera kukaonekera pa mpando woweruza wa Khristu, kuti aliyense wa ife akalandire zomuyenera molingana ndi zimene anachita ali mʼthupi; zabwino kapena zoyipa. Tsono popeza tikudziwa tanthauzo la kuopa Ambuye, ife timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziwa bwino lomwe, ndipo tikukhulupirira kuti inunso mumatidziwa bwino mʼmitima mwanu.

Aliyense amene amachita zolakwa adzalandira malipiro molingana ndi kulakwa kwake, ndipo palibe tsankho.

Iye adzalanga amene sadziwa Mulungu ndi amene samvera Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu. Adzalangidwa ndi chiwonongeko chamuyaya ndipo sadzaonanso nkhope ya Ambuye ndi ulemerero wamphamvu zake

Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa,

Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu

Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo? Pakuti timadziwa amene anati, “Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.” Iye anatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.” Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo.

Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu. Ndipo ali ngati mzimu chomwecho anapita ndi kukalalikira mizimu imene inali mʼndende,

Koma panalinso aneneri onama pakati pa Aisraeli, monga padzakhalanso aphunzitsi onyenga pakati panu. Iwo adzalowetsa mwamseri ziphunzitso zonama ndi zowononga, nadzakana Ambuye amene anawawombola, ndipo motero adzadziyitanira okha chiwonongeko mwadzidzidzi. Ambiri adzatsata njira zawo zochititsa manyazi ndipo chifukwa cha iwowa, anthu adzanyoza njira ya choonadi. Pofuna kupeza chuma, aphunzitsiwa adzakudyerani chuma chanu pokuwuzani nkhani zopeka. Chiweruzo chawo chinakonzedwa kale, ndipo chikuwadikira.

Pakuti Mulungu sanalekerere angelo atachimwa paja, koma anawaponya mʼndende, nawayika mʼmaenje amdima, kuwasunga kuti adzaweruzidwe. Iye sanalekerere dziko lapansi kalelo, koma anapulumutsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, ndi anthu ena asanu ndi awiri atadzetsa chigumula pa dziko lapansi kwa anthu akhalidwe losapembedza Mulunguyo. Mulungu anaweruza mizinda ya Sodomu ndi Gomora nayiwononga ndi moto, kuti ikhale chitsanzo cha zimene zidzachitikira anthu osapembedza Mulungu. Koma Iye anapulumutsa Loti, munthu wolungama, amene ankavutika ndi khalidwe lonyansa la anthu oyipa. (Pakuti munthu wolungamayo, pokhala pakati pawo tsiku ndi tsiku ankavutika mu mtima ndi makhalidwe awo oyipa amene ankawaona ndi kuwamva). Tsono mutha kuona kuti Ambuye amadziwa kuwapulumutsa kwake pa mayesero anthu opembedza. Amadziwanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo. Makamaka amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi nanyoza ulamuliro. Anthu amenewa ndi odzikuza, ndipo otsata chifuniro cha iwo eni, sasamala za munthu, saopa kuchitira chipongwe zolengedwa za mmwamba. Komatu ngakhale angelo, amene ali akulu ndi amphamvu kuwaposa, sayankhula za chipongwe pobweretsa chiweruzo pa iwo kuchokera kwa Ambuye.

Anthu amenewa ali ngati akasupe wopanda madzi, ndiponso ngati nkhungu yowuluzidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu wawasungira mdima wandiweyani.

Dziko la kumwamba ndi lapansi la masiku ano akulisunga ndi mawu omwewo kuti adzalitentha ndi moto. Akuzisunga mpaka tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osapembedza Mulungu.

Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape.

Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha.

Ndipo umboniwo ndi uwu: Mulungu anatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowu uli mwa Mwana wake. Iye amene ali ndi Mwana ali ndi moyo, amene alibe Mwana wa Mulungu alibe moyo.

Pakuti anthu ena amene za chilango chawo zinalembedwa kale, alowa mobisika pakati panu. Amenewa ndi anthu osapembedza Mulungu, amene amapotoza chisomo cha Mulungu wathu kuchisandutsa ufulu ochitira zonyansa ndiponso amakana Yesu Khristu amene Iye ndiye Mbuye ndi Mfumu yathu.

Ndipo mukumbukire angelo amene sanakhutire ndi maudindo awo, koma anasiya malo awo. Angelo amenewa Mulungu anawamanga ndi maunyolo osatha, ndipo akuwasunga mʼmalo a mdima mpaka tsiku lalikulu lachiweruzo. Musayiwale mizinda ya Sodomu ndi Gomora ija, ndi mizinda yoyandikana nayo. Anthu mʼmenemo anadziperekanso kuchita zadama ndi kuchita zonyansa zachilendo. Mizinda imeneyi yakhala ngati chitsanzo cha amene adzalangidwa ndi moto wosatha.

Anthu amenewa ndiwo amayipitsa maphwando anu achikondi. Amadya nanu mopanda manyazi ndipo ali ngati abusa amene amangodzidyetsa okha. Anthuwa ali ngati mitambo yowuluzika ndi mphepo, yopanda mvula. Ali ngati mitengo ya nthawi ya masika, yopanda zipatso, yozuka mizu, mitengo yoferatu. Iwowa ali ngati mafunde awukali apanyanja, amene amatulutsa thovu la zonyansa zawo. Amenewa ali ngati nyenyezi zosochera, ndipo Mulungu akuwasungira mdima wandiweyani mpaka muyaya.

Ena muwapulumutse powalanditsa ku moto. Enanso muwachitire chifundo, koma mwa mantha, ndipo muzidana ngakhale ndi mwinjiro yomwe yayipitsidwa ndi machimo.

Ine ndine Wamoyo; ndinali wakufa ndipo taona ndine wamoyo mpaka muyaya! Ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi Hade.

Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana sadzapwetekedwa ndi pangʼono pomwe ndi imfa yachiwiri.

Mngelo wachisanu anayimba lipenga lake, ndipo ndinaona nyenyezi ikugwa pa dziko lapansi kuchokera ku thambo. Nyenyeziyo inapatsidwa kiyi ya ku chidzenje chakuya. Nyenyeziyo itatsekula pa chidzenje chakuyacho panatuluka utsi ngati wochokera mʼngʼanjo yayikulu. Dzuwa ndi thambo zinada chifukwa cha utsi ochokera mʼdzenjemo.

Mngelo wachitatu anatsatana nawo ndi mawu ofuwula anati, “Ngati wina apembedza chirombo chija ndi fano lake ndi kulembedwa chizindikiro pa mphumi kapena pa dzanja, nayenso adzamwa vinyo waukali wa Mulungu, umene wathiridwa popanda kuchepetsa mphamvu zake mʼchikho cha ukali wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto wamiyala yasulufure pamaso pa angelo oyera ndi pa Mwana Wankhosa. Ndipo utsi wa moto wowazunzawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya. Sikudzakhala kupumula usana ndi usiku kwa amene anapembedza chirombo chija ndi fano lake kapena kwa aliyense amene analembedwa chizindikiro cha dzina lake lija.”

Chirombo chomwe chinalipo kale ndipo tsopano kulibe ndiyo mfumu yachisanu ndi chitatu. Iyo ndi ya mʼgulu la asanu ndi awiriwo ndipo ikupita kukawonongedwa.

Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti: “ ‘Wagwa! Wagwa Babuloni Wamkulu!’ Wasandulika mokhalamo ziwanda ndi kofikako mizimu yonse yoyipa ndi mbalame zonse zonyansa ndi zodetsedwa. Pakuti mayiko onse amwa vinyo ozunguza mutu wazigololo zake. Mafumu a dziko lapansi achita naye chigololo, ndipo amalonda a dziko lapansi analemera kuchokera pa zolakalaka zake zosefukira.”

Kuwala kwa nyale sikudzawunikanso mwa inu. Mawu a mkwati ndi mkwatibwi sadzamvekanso mwa iwe. Amalonda anu anali akuluakulu a dziko lapansi. Mitundu yonse inasokonezedwa ndi zamatsenga zako. Mwa iye munapezeka magazi a aneneri ndi a oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa pa dziko lapansi.”

pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake. Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake.” Ndipo anafuwulanso kuti, “Haleluya! Utsi wochokera kwa mkazi wadamayo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.”

Iye anavala mkanjo woviyika mʼmagazi, ndipo dzina lake ndi Mawu a Mulungu. Magulu ankhondo akumwamba ankamutsatira atakwera pa akavalo oyera, ndipo iwowo atavala nsalu zoyera kwambiri ndi zosada. Mʼkamwa mwake munatuluka lupanga lakuthwa limene anati akaphe nalo mitundu ya anthu. Iye adzalamulira ndi ndodo yachitsulo. Iye anaponda choponderamo mphesa cha ukali wa Mulungu Wamphamvuzonse.

Ndipo ndinaona mngelo atayimirira pa dzuwa amene anafuwula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zowuluka mlengalenga kuti, “Bwerani, sonkhanani pamodzi ku phwando lalikulu la Mulungu. Kuti mudye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, ndi wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi okwerapo awo, ndi wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, angʼono ndi aakulu.”

Koma chirombocho chinagwidwa pamodzi ndi mneneri wonyenga uja amene anachita zizindikiro zodabwitsa pamaso pake. Ndi zizindikirozi anasocheretsa amene analembedwa chizindikiro cha chirombocho napembedza fano lake. Onse awiri anaponyedwa amoyo mʼnyanja yamoto yasulufule wotentha. Ena onse anaphedwa ndi lupanga lija linatuluka mʼkamwa mwa wokwera pa kavalo uja, ndipo mbalame zonse zinadya mokwanira mnofu wa anthu akufawo.

Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi ya ku chidzenje chakuya chija atanyamula mʼdzanja lake unyolo waukulu. Iye anachigwira chinjokacho, chinjoka chakalekale chija, amene ndi Mdierekezi kapena kuti Satana, ndipo anamumanga zaka 1,000. Anamuponya ku chidzenje chakuya chija namutsekera ndi kiyi ndi kumatirira pa khomopo kuti asatulukenso kukanyenga mitundu ya anthu mpaka patapita zaka 1,000. Zikadzatha zakazo, adzamumasula kwa kanthawi pangʼono chabe.

Zaka 1,000 zikadzatha, Satana adzamasulidwa ku ndende yake ndipo adzapita kukanyenga mitundu ya anthu kumbali zonse zinayi za dziko lapansi, Gogi ndi Magogi, kuwasonkhanitsa kuti akachite nkhondo. Kuchuluka kwawo kudzakhala ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Iwo anayenda ponseponse pa dziko lapansi nazinga msasa wa anthu a Mulungu, mzinda umene Iye amawukonda. Koma moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kuwanyeketsa. Ndipo Mdierekezi amene anawanyenga, anaponyedwa mʼnyanja ya sulufule wotentha, kumene kunaponyedwa chirombo chija ndi mneneri wonama uja. Iwo adzazunzika usiku ndi usana kwamuyaya.

Kenaka ndinaona Mpando Waufumu waukulu woyera ndi Iye amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake ndipo panalibenso malo awo. Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aangʼono omwe atayimirira patsogolo pa Mpando Waufumu ndipo mabuku anatsekulidwa. Buku lina linatsekulidwa limene linali Buku Lamoyo. Akufa anaweruzidwa monga mwa zimene anachita monga mmene zinalembedwera mʼmabuku. Nyanja inapereka amene anaferamo ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufa ake ndipo munthu aliyense anaweruzidwa monga mwa ntchito zake. Kenaka imfa ndi Hade zinaponyedwa mʼnyanja ya moto. Nyanja yamoto ndiyo imfa yachiwiri. Ngati dzina la wina aliyense silinapezeke mʼBuku Lamoyo, anaponyedwa mʼnyanja yamoto.

Koma amantha, osakhulupirira, okonda zonyansa, opha anthu, achiwerewere, amatsenga, opembedza mafano ndi abodza, malo awo adzakhala nyanja yamoto ya sulufule wotentha. Iyi ndi imfa yachiwiri.”

Wochita zoyipa apitirire kuchita zoyipazo; wochita zonyansa apitirire kuchita zonyansazo; wochita zabwino apitirire kuchita zabwinozo; ndipo woyera mtima apitirire kukhala woyera mtima.”

Ndikuchenjeza aliyense amene akumva mawu onena zamʼtsogolo a mʼbukuli kuti, “Ngati wina awonjezerapo kalikonse, Mulungu adzamuwonjezera miliri imene yalembedwa mʼbuku ili. Ndipo wina akachotsapo mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili, Mulungu adzachotsa gawo lake pa mtengo wamoyo ndi la mu mzinda woyera zimene zanenedwa mʼbuku ili.”

Chichewa - Chichewa - NY

NYCCL - Mawu A Mulungu Mu Chichewa Chalero - 2016

This Bible text is from Biblica Open God's Word In Contemporary Chichewa
https://open.bible/bibles/chichewa-biblica-text-bible/
provided by: Biblica Inc, available by Creative Commons CC-BY-SA-4.0,
and this new compilation is shared as www.creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0.
Languages are made available to you by www.ipedge.net