31 – Kulalikira Uthenga Wabwino

Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Kulalikira Uthenga Wabwino.

Mavesi atatu ofunika kwambiri

Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo? Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, “Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!”

Pakuti kwa Mulungu ndife fungo labwino la Khristu pakati pa iwo amene akupulumutsidwa ndi amene akuwonongeka. Kwa amene akuwonongeka ndife fungo la imfa, limawapha. Ndipo kwa amene akupulumuka ndife fungo lamoyo, limawapatsa moyo. Ndani angayithe ntchito yotereyi?

Ngati wina aliyense sakakulandirani kapena sakamvera mawu anu, musase fumbi la kumapazi anu pamene mutuluka mʼnyumbayo kapena mu mzindawo. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku lachiweruziro, mlandu wa Sodomu ndi Gomora udzachepa kusiyana ndi wa mzindawo.

Mavesi onse motsatira dongosolo lolondola – 307 ndime

“Nthawi zonse mmene dziko lapansi lidzakhalire, nthawi yodzala ndi nthawi yokolola yozizira ndi yotentha, dzinja ndi chilimwe, usana ndi usiku, sizidzatha.”

Mose anayankha, “Aisraeliwo sakandikhulupirira ndipo sakandimvera. Iwowo adzati, ‘Yehova sanakuonekere iwe.’ ”

Mose anati kwa Yehova, “Chonde Ambuye, chikhalire ine ndakhala munthu wosatha kuyankhula bwino. Ngakhale tsopano pamene mukundiyankhula, lilime langa ndi lolemera. Ndine wachibwibwi.” Yehova anati kwa iye, “Kodi anapatsa munthu pakamwa ndani? Ndani amasandutsa munthu kuti akhale wosayankhula kapena wosamva? Ndani amapanga munthu kukhala wopenya kapena wosaona? Kodi si Ine Yehova? Tsopano pita, Ine ndidzakuthandiza kuyankhula ndipo ndidzakulangiza zoti ukanene.”

Koma Mose anati, “Chonde Ambuye, pepani, tumani wina kuti akachite zimenezi.” Kenaka Yehova anamupsera mtima Mose ndipo anati, “Kodi suli ndi mʼbale wako Aaroni wa fuko la Levi? Ine ndikudziwa kuti iye amayankhula bwino. Iye wanyamuka kale kudzakumana nawe ndipo adzasangalala akadzakuona. Iwe udzayankhula naye ndi kumuwuza mawu oti akanene. Ine ndidzakuthandizani kuyankhula nonse awirinu ndi kukulangizani zoti mukachite. Iye akayankhula kwa anthu mʼmalo mwako. Iye adzakhala wokuyankhulira ndipo iweyo udzakhala ngati Mulungu kwa iye.

Paliponse pamene phazi lanu liponde, ndikupatsani monga momwe ndinalonjezera Mose.

Imbirani Yehova, dziko lonse lapansi; lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Lengezani za ulemerero wake kwa mitundu yonse, ntchito zake zonse zodabwitsa kwa anthu onse.

Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu; sinditseka milomo yanga monga mukudziwa Inu Yehova. Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga; ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu. Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu pa msonkhano waukulu.

Pakamwa panga padzafotokoza za chilungamo chanu, za chipulumutso chanu tsiku lonse, ngakhale sindikudziwa muyeso wake. Ndidzabwera ndi kulengeza za machitidwe amphamvu zanu Inu Ambuye Wamphamvuzonse. Ndidzalengeza chilungamo chanu, chanu chokha. Kuyambira ubwana wanga, Inu Mulungu mwakhala mukundiphunzitsa, ndipo mpaka lero ine ndikulengeza za ntchito zanu zodabwitsa Ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbuu musanditaye Inu Mulungu, mpaka nditalengeza mphamvu zanu kwa mibado yonse yakutsogolo.

Imbirani Yehova, tamandani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko, ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.

Ndidzayankhula za umboni wanu pamaso pa mfumu ndipo sindidzachititsidwa manyazi,

Iwo amene amafesa akulira, adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe. Iye amene amayendayenda nalira, atanyamula mbewu yokafesa, adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe, atanyamula mitolo yake.

Yehova ikani mlonda pakamwa panga; londerani khomo la pa milomo yanga.

Mʼbado wina udzayamikira ntchito yanu kwa mʼbado wina; Iwo adzafotokoza za machitidwe anu amphamvu.

Munthu woyipa amalandira malipiro wopanda phindu, koma wochita chilungamo amakolola mphotho yeniyeni.

Chipatso cha ntchito zabwino ndi moyo, ndipo kusatsata malamulo kumawonongetsa moyo.

Kuwala kwa maso kumasangalatsa mtima ndipo uthenga wabwino umalimbitsa munthu. Womvera mawu a chidzudzulo amene apatsa moyo adzakhala pakati pa anthu anzeru. Amene amanyoza mwambo amadzinyoza yekha, koma womvera mawu a chidzudzulo amapeza nzeru zomvetsa zinthu. Kuopa Yehova kumaphunzitsa munthu nzeru, ndipo kudzichepetsa ndi ulemu chili patsogolo ndi kudzichepetsa.

Mawu okometsera ali ngati chisa cha njuchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.

Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziwa zinthu, ndipo wodekha mtima ndiye womvetsa bwino zinthu. Ngakhale chitsiru chimakhala ngati chanzeru chikakhala chete; ndipo chikatseka pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.

Chitsiru chilibe chidwi chomvetsa zinthu, koma chimakondwera ndi kuyankhula maganizo ake okha.

Mawu a chitsiru amautsa mkangano; pakamwa pake pamayitana mkwapulo. Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake, ndipo milomo yake ili ngati msampha wa moyo wake.

Ukayankha usanamvetse bwino nkhani, umenewo ndi uchitsiru ndipo umachita manyazi.

Mawu ako angathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo. Wokonda kuyankhulayankhula adzadya zipatso zake.

Mthenga wabwino wochokera ku dziko lakutali ali ngati madzi ozizira kwa munthu waludzu.

Nthawi yongʼamba ndi nthawi yosoka, nthawi yokhala chete ndi nthawi yoyankhula.

Amene amayangʼana mphepo sadzadzala; amene amayangʼana mitambo sadzakolola.

Dzala mbewu zako mmawa ndipo madzulo usamangoti manja lobodo, pakuti sudziwa chimene chidzapindula, mwina ichi kapena icho, kapena mwina zonse ziwiri zidzachita bwino.

Mlaliki sanali wozindikira zinthu kokha ayi, komanso ankaphunzitsa anthu. Iye ankasinkhasinkha ndi kufufuzafufuza ndi kulemba mwadongosolo miyambi yambiri. Mlaliki anafufuzafufuza kuti apeze mawu oyenera, ndipo zimene analemba zinali zolondola ndiponso zoona.

Kenaka ndinamva mawu a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani? Ndipo ndani adzapite mʼmalo mwathu?” Ndipo ine ndinati, “Ndilipo. Tumeni!”

Yehova anati, “Pita ndipo ukawawuze anthu awa: “ ‘Kumva muzimva, koma osamvetsetsa; kupenya muzipenya koma osaona kanthu.’ Tsono anthu amenewa uwaphe mtima; uwagonthetse makutu, ndipo uwatseke mʼmaso. Mwina angaone ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi mitima yawo, kenaka ndi kutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.” Pamenepo ine ndinati, “Zimenezo ndi mpaka liti Inu Ambuye?” Ndipo Iyeyo anandiyankha kuti, “Mpaka mizinda itasanduka mabwinja nʼkusowa wokhalamo, mpaka nyumba zitasowa anthu okhalamo, mpaka dziko litasanduka chipululu ndithu,

kuti akalandireko mawu enieni ndi malangizo? Ngati anthuwo sayankhula monga mwa mawu awa, mwa iwo mulibe kuwala.

Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena chowononga pa phiri lopatulika la Yehova, pakuti anthu a dziko lapansi adzadzaza ndi nzeru yotha kudziwa Yehova monga momwe nyanja imadzazira ndi madzi.

Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Ziyoni, kwera pa phiri lalitali. Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Yerusalemu, fuwula kwambiri, kweza mawu, usachite mantha; uza mizinda ya ku Yuda kuti, “Mulungu wanu akubwera!”

Ngokongoladi mapazi a amithenga obweretsa nkhani yabwino amene akuyenda pa mapiri. Iwo akukubweretserani nkhani zabwino za mtendere, chisangalalo ndi chipulumutso. Iwo akubwera kudzawuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wako ndi mfumu!”

Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine, chifukwa Yehova wandidzoza kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka. Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima, ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende. Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake; za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake. Wandituma kuti ndikatonthoze olira. Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni, nkhata ya maluwa yokongola mʼmalo mwa phulusa, ndiwapatse mafuta achikondwerero mʼmalo mwa kulira. Ndiwapatse chovala cha matamando mʼmalo mwa mtima wopsinjika. Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo, yoyidzala Yehova kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.

Ine ndinati, “Haa! Ambuye Yehova, ine sinditha kuyankhula; popeza ndikanali wamngʼono.” Koma Yehova anandiwuza kuti, “Usanene kuti, ‘Ndikanali wamngʼono’ popeza udzapita kwa munthu aliyense kumene ndidzakutuma ndi kunena chilichonse chimene ndidzakulamulira. Usawaope, pakuti Ine ndili nawe, ndipo ndidzakupulumutsa,” akutero Yehova. Pamenepo Yehova anatambalitsa dzanja lake nakhudza pakamwa panga, nandiwuza kuti, “Taona, tsopano ndayika mawu anga mʼkamwa mwako.

Yehova akuti, “Koma tsopano ndidzayitana adani okhala ngati asodzi ambiri, ndipo adzawagwira ngati nsomba. Izi zitatha adani enanso okhala ngati alenje ambiri, adzawasaka pa phiri lililonse, pa chitunda chilichonse ndiponso mʼmapanga onse a mʼmatanthwe.

Tsono Mulungu anandiwuza kuti, “Mwana wa munthu, idya chimene ndikukupatsachi. Idya kenaka upite ukayankhule ndi Aisraeli.” Choncho ndinayasama ndipo anandipatsa mpukutuwo kuti ndidye. Kenaka Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu umene ndikukupatsa kuti ukhute.” Choncho ndinadya, ndipo unkatsekemera ngati uchi mʼkamwa mwanga. Pamenepo Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, pita tsopano kwa Aisraeli ndipo ukawawuze mawu anga.

Amene ali anzeru mʼnjira ya chilungamo adzawala ngati kuwala kwa mlengalenga, ndipo amene alondolera ambiri ku njira yolungama, adzawala ngati nyenyezi ku nthawi zosatha.

Ndipo Yehova anayankhula ndi Yona kachiwiri kuti, “Nyamuka, pita ku mzinda waukulu wa Ninive ndipo ukalalikire uthenga umene ndikupatsa.”

Yona analowa mu mzindawo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye ankalalikira kuti, “Atsala masiku makumi anayi kuti Ninive awonongedwe.” Anthu a ku Ninive anakhulupirira Mulungu. Analengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamngʼono yemwe asale zakudya ndipo avale chiguduli. Mfumu ya ku Ninive itamva nkhaniyi, inatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake waufumu ndipo inavala chiguduli ndi kukhala pansi pa fumbi. Tsono mfumuyo inalengeza mu Ninive kuti, “Mwa lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake: “Munthu aliyense kapenanso nyama, ngʼombe kapena nkhosa, zisadye kanthu kalikonse; musazilole kuti zidye kapena kumwa. Koma anthu avale ziguduli, ndipo nyamanso aziveke ziguduli. Munthu aliyense azifuwula kwa Mulungu ndi mphamvu zake zonse. Anthuwo asiye makhalidwe awo oyipa ndi machitidwe achiwawa. Angadziwe ndani? Mwina Mulungu nʼkutikhululukira ndipo mwa chifundo chake nʼkuleka kutikwiyira, ifeyo osawonongedwa.” Mulungu ataona zimene anthuwo anachita, ndi mmene anasiyira makhalidwe awo oyipa, anawachitira chifundo ndipo sanabweretse chiwonongeko chimene anawaopseza nacho.

Taonani, pa phiripo, mapazi a munthu amene akubweretsa nkhani yabwino, amene akulengeza za mtendere! Inu anthu a ku Yuda, chitani madyerero anu ndipo kwaniritsani malumbiro anu. Anthu oyipa sadzakuthiraninso nkhondo; iwo adzawonongedwa kotheratu.

Mʼmasiku amenewo, Yohane Mʼbatizi anadza nalalikira mʼchipululu cha Yudeya kuti, “Tembenukani mtima chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.”

Koma iye ataona Afarisi ndi Asaduki ambiri akubwera kumene ankabatiza, anawawuza kuti, “Ana a njoka inu! Ndani anakuchenjezani kuthawa mkwiyo umene ukubwera? Onetsani chipatso cha kutembenuka mtima.

Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ ”

Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, “Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira.”

Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye. Atapita patsogolo, anaona abale ena awiri, Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo. Iwowa anali mʼbwato ndi abambo awo, Zebedayo, akukonza makoka awo ndipo Yesu anawayitana. Nthawi yomweyo anasiya bwato ndi abambo awo namutsata Iye.

Yesu anayendayenda mu Galileya kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda onse pakati pa anthu.

“Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine. Sangalalani, kondwerani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba, chifukwa moterenso ndi mmene anazunzira aneneri inu musanabadwe. “Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo usukuluka, adzawukometsanso ndi chiyani? Ulibenso ntchito koma kungowutaya kunja, anthu nawuponda.

“Inu ndinu kuwunika kwa dziko lapansi. Mzinda wa pa phiri sungathe kubisika. Anthu sayatsa nyale ndikuyivundikira ndi mbiya, mʼmalo mwake amayika poonekera ndipo imawunikira onse mʼnyumbamo. Momwemonso kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kulemekeza Atate anu akumwamba.

“Musadziwunjikire chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga ndi pamene mbala zimathyola ndi kuba. Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba. Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko.

Wophunzira wina anati kwa Iye, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakayika maliro a abambo anga.” Koma Yesu anamuwuza kuti, “Nditsate Ine ndipo uwaleke akufa ayikane akufa okhaokha.”

Ndipo Yesu atachoka kumeneko, anaona munthu wina dzina lake Mateyu, atakhala mʼnyumba ya msonkho. Anati kwa iye, “Nditsate Ine.” Ndipo iye ananyamuka namutsata.

Yesu anayendayenda mʼmizinda yonse ndi mʼmidzi, kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa nthenda zawo zonse ndi zofowoka za mʼmatupi mwawo.

Pamenepo anati kwa ophunzira ake, “Zokolola ndi zambiri koma antchito ndi ochepa. Nʼchifukwa chake, pemphani Ambuye mwini zokolola kuti atumize antchito ku munda wake.”

Pamene mukupita, muzikalalikira uthenga uwu: ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’ Chiritsani odwala, ukitsani akufa, chiritsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, perekani kwaulere.

“Musatenge ndalama zagolide kapena zasiliva kapena zakopala mʼzikwama mwanu; musatenge thumba la paulendo, kapena malaya awiri kapena nsapato kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira chakudya chake. Mukalowa mu mzinda ndi mʼmudzi uliwonse, funafunani munthu woyenera ndipo mukhale mʼnyumba mwake kufikira mutachoka. Pamene mulowa mʼnyumba mupereke moni. Mtendere wanu ukhale pa a mʼnyumbayo ngati ndi oyenera. Koma ngati siwoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu.

Ngati wina aliyense sakakulandirani kapena sakamvera mawu anu, musase fumbi la kumapazi anu pamene mutuluka mʼnyumbayo kapena mu mzindawo. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku lachiweruziro, mlandu wa Sodomu ndi Gomora udzachepa kusiyana ndi wa mzindawo.

“Taonani ndikukutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu. Chifukwa chake khalani ochenjera ngati njoka ndi woona mtima ngati nkhunda. Chenjerani ndi anthu pakuti adzakuperekani ku mabwalo amilandu nadzakukwapulani mʼmasunagoge mwawo. Chifukwa cha Ine, mudzaperekedwa kwa olamulira ndi kwa mafumu kuti mukhale mboni kwa iwo ndi kwa a mitundu ina.

Koma pamene akumangani, inu musadandaule kuti mukanena bwanji kapena mukanena chiyani. Mudzapatsidwa pa nthawi imeneyo zoti munene, pakuti sindinu mudzanena, koma Mzimu Woyera wa Atate anu, adzayankhula mwa inu.

“Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe ndi abambo mwana wawo: ndipo ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. Anthu onse adzada inu chifukwa cha Ine, koma iye amene apirira mpaka kumapeto, adzapulumuka. Pamene akuzunzani pamalo ena thawirani kwina. Pakuti ndikuwuzani zoonadi kuti simudzamaliza mizinda yonse ya Israeli Mwana wa Munthu asanabwere.

“Aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzavomereza pamaso pa Atate anga akumwamba. Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamukana pamaso pa Atate anga akumwamba.

“Musaganize kuti Ine ndabweretsa mtendere pa dziko lapansi. Sindinabwere kudzapereka mtendere koma lupanga. Pakuti Ine ndabwera kudzalekanitsa “ ‘Munthu ndi abambo ake, mwana wamkazi ndi amayi ake, mtengwa kulekanitsidwa ndi apongozi ake, adani a munthu adzakhala a mʼbanja mwake momwe.’ “Aliyense amene akonda abambo kapena amayi ake koposa Ine sayenera kukhala wanga; aliyense amene akonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine sayenera kukhala wanga. Aliyense amene satenga mtanda wake ndi kunditsata Ine sayenera kukhala wanga. Aliyense amene asunga moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo chifukwa cha Ine adzawupeza. “Iye amene alandira inu alandira Ine, ndipo amene alandira Ine alandiranso amene anandituma Ine.

Ndipo Yesu atamaliza kulangiza ophunzira ake khumi ndi awiri aja, anachoka kumeneko kupita kukaphunzitsa ndi kukalalikira ku mizinda ya ku Galileya.

Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka. Odala ndi munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”

Kuyambira masiku a Yohane Mʼbatizi mpaka tsopano, ufumu wakumwamba ndi wolimbirana ndipo anthu amphamvu okha ndi amene akuwulanda.

Anthu a ku Ninive adzayimirira pachiweruzo ndi mʼbado uwu ndi kuwutsutsa pakuti iwo analapa Yona atalalikira ndipo tsopano wamkulu kuposa Yona ali pano.

Pamenepo Iye anawawuza zinthu zambiri mʼmafanizo ndi kuti, “Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa, zina zinagwera mʼmbali mwa njira ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. Zina zinagwa pamalo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. Koma dzuwa litakwera, mbewu zinapserera ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu. Mbewu zina zinagwa pa minga ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. Koma mbewu zina zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinabala zipatso 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa.

“Tamverani tsono zimene fanizo la wofesa litanthauza: Pamene aliyense akumva uthenga wa ufumu koma sawuzindikira, woyipayo amabwera ndi kuchotsa zimene zafesedwa mu mtima mwake. Iyi ndi mbewu yofesedwa mʼmbali mwa njira. Zimene zinafesedwa pa malo amiyala ndi munthu amene amamva mawu ndi kuwalandira msanga ndi chimwemwe. Koma popeza alibe muzu, iwo amakhala nthawi yochepa. Pamene vuto kapena zunzo libwera chifukwa cha mawu, iye amagwa mofulumira. Zimene zinafesedwa pakati pa minga, ndi munthu amene amamva mawu koma nkhawa za moyo uno ndi chinyengo cha chuma zimalepheretsa mawuwo kuti abale chipatso. Koma zimene zinafesedwa pa nthaka yabwino, ndi munthu amene amamva mawu ndipo amawazindikira. Iye amabala zipatso zokwanira 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa.”

Iye anawawuza fanizo lina kuti, “Ufumu wakumwamba uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. Ngakhale mbewuyi ndi yayingʼono mwa mbewu zanu zonse za mʼmunda, imakula ndi kukhala mtengo kotero kuti mbalame zamlengalenga zimabwera ndi kupumula mʼnthambi zake.”

Iye anayankha kuti, “Mbewu iliyonse imene Atate anga akumwamba sanadzale idzazulidwa ndi mizu yomwe.

Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine. Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupeza. Kodi munthu adzapindula chiyani ngati atapeza zonse za dziko lapansi nataya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthana ndi moyo wake? Pakuti Mwana wa Munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate ake ndi angelo ake ndipo pamenepo Iye adzapereka mphotho kwa munthu mofanana ndi zimene anachita.

Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena bambo kapena mayi kapena mkazi, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine adzalandira madalitso ochuluka ndi kulandiranso moyo wosatha.

“Ufumu wakumwamba uli ngati mwini munda amene anapita mmawa kukalemba anthu aganyu kuti akagwire ntchito mʼmunda wake wa mpesa. Anagwirizana kuwalipira dinari monga malipiro a tsiku limodzi ndipo anawatumiza mʼmunda wake wamphesa. “Nthawi 9 koloko mmawa, anatulukanso naona ena atayimirira pa msika akungokhala. Anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa, ndipo ndidzakulipirani malipiro oyenera.’ Ndipo anapita. “Anatulukanso nthawi ya 12 koloko masana, ndi nthawi ya 3 koloko masananso nachita chimodzimodzi. Nthawi ya 5 koloko madzulo anatulukanso ndipo anapeza enanso atangoyimirira. Anawafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukungoyimirira pano tsiku lonse osagwira ntchito?’ “Iwo anayankha kuti, ‘Chifukwa palibe munthu amene watilemba ganyu.’ “Iye anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa.’ “Ndipo pofika madzulo, mwini munda wamphesa anayitana kapitawo wake nati, ‘Itana antchito ndipo uwapatse malipiro awo, kuyambira omalizira aja mpaka oyamba.’ “Antchito amene anawalemba ganyu pa 5 koloko masana anafika ndipo aliyense analandira dinari. Ndipo atabwera kwa amene analembedwa poyamba anayembekezera kuti alandira zambiri. Koma aliyense wa iwo analandira dinari. Atalandira, anayamba kuderera kwa mwini mundayo. Iwo anati, ‘Anthu amene munawalemba pomalizira agwira ntchito ora limodzi, ndipo mwawafananitsa ndi ife amene tathyoka nayo ntchito ndi kutentha kwa dzuwa tsiku lonse.’ “Koma iye anamuyankha mmodzi wa iwo nati, ‘Bwenzi, ine sikuti sindinachite chilungamo. Kodi sunavomereze kuti ugwira ntchito ndi kulandira dinari? Tenga malipiro ako pita. Ndikufuna kumupatsa munthu amene ndinamulemba pomaliza mofanana ndi mmene ndakupatsira iwe. Kodi ndilibe ufulu wochita zimene ndikufuna ndi ndalama zanga? Kapena ukuyipidwa chifukwa ndine wopereka mowolowamanja?’

“Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonzera phwando mwana wake wamwamuna. Anatumiza antchito ake kwa amene anayitanidwa kuphwando koma anakana kubwera. “Kenaka anatumiza antchito ena nati, ‘Awuzeni oyitanidwa kuti phwando lakonzedwa: ndapha ngʼombe yayimuna ndi nyama zina zonenepa ndipo zonse zakonzedwa. Bwerani ku phwando laukwati.’ “Koma iwo sanalabadire ndipo anachoka; wina anapita ku munda wake ndi wina ku malonda ake. Ndipo otsalawo anagwira antchito ake, nawazunza ndi kuwapha. Mfumu inakwiya. Inatumiza asilikali ake ndipo anawononga opha anzawowo ndi kutentha mzinda wawo.

“Pamenepo anati kwa antchito ake, ‘Phwando laukwati lakonzedwa, koma amene ndinawayitana sanali oyenera. Pitani ku mphambano za misewu ndipo kayitaneni aliyense amene mukamupeze kuti abwere ku phwando.’ Pamenepo antchitowo anapita ku misewu nakasonkhanitsa anthu onse amene anakawapeza, abwino ndi oyipa omwe, ndipo nyumba ya madyerero inadzaza ndi oyitanidwa.

“Pamenepo adzakuperekani kuti mukazunzidwe ndi kuphedwa, ndipo mitundu yonse idzakudani chifukwa cha Ine. Pa nthawi imeneyo ambiri adzasiya chikhulupiriro ndipo adzadana ndi kuperekana wina ndi mnzake, ndipo aneneri onama ambiri adzaoneka ndi kunyenga anthu ambiri.

Ndipo uthenga wa ufumu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi ngati umboni kwa mitundu yonse, ndipo pomwepo chimaliziro chidzafika.”

Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine. Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera, ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”

Ndipo Yohane anabwera mʼmadera a mʼchipululu nabatiza, ndi kulalikira za ubatizo wa kutembenuka mtima ndi wa chikhululukiro cha machimo.

Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati, “Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”

Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja, popeza anali asodzi. Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.

Yesu anayakha kuti, “Tiyeni tipite kwina ku midzi ya pafupi kuti ndikalalikirenso kumeneko. Ichi ndi chifukwa chimene ndinabwerera.”

Pamene ankayendabe, anaona Levi mwana wa Alufeyo atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anamuwuza kuti, “Tsate Ine.” Ndipo Levi anayimirira namutsata Iye.

Iye anasankha khumi ndi awiri, nawayika akhale atumwi; pokhala ndi Iye aziwatuma kukalalikira ndi kuti akhale ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda.

“Tamverani! Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa, mbewu zina zinagwera mʼmbali mwa njira, ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. Zina zinagwa pa malo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. Koma dzuwa litakwera, mbewuzo zinapserera, ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu. Mbewu zina zinagwa pa minga, ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. Mbewu zinanso zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinamera, zinakula ndi kubereka zipatso, zina zochuluka makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi ndi zina 100.” Pamenepo Yesu anati, “Amene ali ndi makutu akumva, amve.” Ali yekha, ophunzira ndi ena omuzungulira, anamufunsa za mafanizo. Iye anawawuza kuti, “Chinsinsi cha ufumu wa Mulungu chapatsidwa kwa inu. Koma kwa amene ali kunja zinthu zonse zinenedwa mʼmafanizo: kotero kuti, “ ‘Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu, kumva mudzamva koma osamvetsetsa, kuti mwina angatembenuke ndi kukhululukidwa!’ ”

Pamenepo Yesu anawawuza kuti, “Kodi simukulimvetsa fanizoli? Kodi nanga mudzazindikira bwanji fanizo lina lililonse? Wofesa amafesa mawu. Anthu ena ali ngati mbewu za mʼmbali mwa njira, mʼmene mawu amafesedwamo. Akangowamva, Satana amabwera ndi kuchotsa mawu amene anafesedwa mwa iwo. Ena, monga mbewu zofesedwa pa miyala, amamva mawu ndipo nthawi yomweyo amawalandira ndi chimwemwe. Koma popeza alibe mizu, amakhala kwa kanthawi kochepa. Mavuto kapena masautso akafika chifukwa cha mawu, amagwa mofulumira. Komabe ena, monga mbewu zofesedwa pakati pa minga, amamva mawu; koma nkhawa zamoyo uno, chinyengo cha chuma ndi zokhumba za zinthu zina zimabwera ndi kutchinga mawu, ndipo amawachititsa kukhala osabala chipatso. Ena, ngati mbewu zofesedwa pa nthaka yabwino, amamva mawu, nawalandira, ndi kubereka zipatso zokwanira makumi atatu, makumi asanu ndi limodzi, kapena ngakhale 100 kuwonjezera pa zomwe zinafesedwa.”

Iye anatinso, “Umu ndi mmene ulili ufumu wa Mulungu. Munthu amafesa mbewu mʼnthaka. Usiku ndi usana, kaya agona kapena adzuka, mbewu imamera ndi kukula, ngakhale sadziwa mmene zimachitikira. Nthaka pa yokha imatulutsa mbewu, umayamba mʼmera, kenaka ngala, kenaka mbewu yokhwima mʼngalayo. Mbewuyo ikangokhwima, amayimweta chifukwa nthawi yokolola yakwana.”

Ndipo anatinso, “Kodi tinene kuti ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani, kapena ndi fanizo lotani limene tidzagwiritsa ntchito pakuwufotokozera? Uli ngati mbewu ya mpiru imene ndi mbewu yayingʼono kwambiri yomwe mumadzala mʼnthaka. Koma ikadzalidwa, imakula ndi kukhala yayikulu koposa mbewu zina zonse za mʼmunda ndipo mʼnthambi zake zazikulu mbalame zamlengalenga zimadzapuma pa mthunzi wake.”

Yesu sanamulole, koma anati, “Pita kwanu ku banja lako ndipo ukawawuze zimene Ambuye wakuchitira, ndi chifundo chimene wakuchitira.” Pomwepo munthuyo anapita nayamba kuwuza anthu a ku Dekapoli zinthu zimene Yesu anamuchitira. Ndipo anthu onse anadabwa.

Atayitana khumi ndi awiriwo, Iye anawatuma awiriawiri ndipo anawapatsa ulamuliro pa mizimu yoyipa. Zomwe anawalangiza ndi izi: “Musatenge kanthu ka paulendo koma ndodo yokha; osatenga buledi, thumba, kapena ndalama. Muvale nsapato koma osatenga malaya apadera. Pamene mulowa mʼnyumba mukakhale momwemo kufikira mutachoka mʼmudzimo.

Ndipo ngati pa malo ena sakakulandirani kapena kukumverani, sasani fumbi la kumapazi anu pamene mukuchoka, kuti ukhale umboni wowatsutsa.” Anatuluka kupita kukalalikira kuti anthu atembenuke mtima.

Ndipo anawawuzanso kuti, “Inu muli ndi njira yabwino yokankhira kumbali malamulo a Mulungu kuti mukatsatire miyambo yanuyo!

Analinso ndi tinsomba tochepa; Iye anayamikanso chifukwa cha nsombazo. Ndipo anawuza ophunzira kuti awagawire. Anthu anadya ndipo anakhuta. Atamaliza, ophunzira anatola buledi ndi nsomba zotsalira ndi kudzaza madengu asanu ndi awiri. Panali amuna pafupifupi 4,000. Ndipo atawawuza kuti apite kwawo,

Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata. Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa. Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake?

Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”

Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe aliyense amene wasiya nyumba kapena abale kapena alongo kapena amayi kapena abambo kapena ana kapena minda chifukwa cha Ine ndi Uthenga Wabwino adzalephera kulandira 100 (nyumba, abale, alongo, amayi, ana ndi minda, pamodzi ndi mazunzo) mʼbado uno ndi moyo wosatha nthawi ya mʼtsogolo.

“Muyenera kukhala tcheru. Mudzaperekedwa ku mabwalo oweruza ndi kukwapulidwa mwankhanza mʼmasunagoge. Mudzayima pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu monga mboni kwa iwo chifukwa cha Ine. Ndipo Uthenga Wabwino uyenera kuyamba walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.

Nthawi iliyonse pamene mwamangidwa ndi kuyimbidwa mlandu, musadandaule za zimene mudzanena. Zimene mudzapatsidwe pa nthawiyo yankhulani; pakuti sindinu amene mudzayankhula, koma Mzimu Woyera.

“Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe, ndipo abambo adzapereka mwana wawo. Ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine, koma amene adzalimbika mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.

Anati kwa iwo, “Pitani mʼdziko lonse lapansi ndipo mukalalikire Uthenga Wabwino kwa zolengedwa zonse. Aliyense amene akakhulupirire nabatizidwa adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira adzalangidwa.

Pamenepo ophunzira aja anapita ndi kukalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo anatsimikizira mawuwo ndi zizindikiro zimene ankachita.

monga mmene zinaperekedwera kwa ife ndi iwo amene anaona poyambirira ndi atumiki a mawu.

kupatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso kudzera mwa chikhululukiro cha machimo awo,

Koma mngeloyo anawawuza kuti, “Musachite mantha. Ine ndakubweretserani Uthenga Wabwino wachimwemwe chachikulu umene udzakhala wa anthu onse.

Iye anapita ku dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yorodani, nalalikira ubatizo wa kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo. Monga analembera mʼbuku la Yesaya mneneri kuti: “Mawu a wofuwula mʼchipululu, konzani njira ya Ambuye, wongolani njira zake. Chigwa chilichonse chidzadzazidwa ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzasalazidwa, misewu yokhotakhota idzawongoledwa, ndi njira zosasalala zidzasalazidwa. Ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.”

Ndipo ndi mawu ena ambiri, Yohane anawachenjeza anthu ndi kuwalalikira Uthenga Wabwino.

“Mzimu wa Ambuye ali pa Ine; chifukwa wandidzoza kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka. Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe ndi kwa osaona kuti apenyenso, kumasulidwa kwa osautsidwa,

Koma Iye anati, “Ine ndikuyenera kulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso chifukwa ichi ndi chimene ananditumira.”

Atatha kuyankhula anati kwa Simoni, “Kankhirani kwa kuya ndipo muponye makhoka kuti mugwire nsomba.” Simoni anayankha kuti, “Ambuye, tagwira ntchito molimbika usiku wonse, koma sitinagwire kanthu. Koma pakuti mwatero, ndiponya makhoka.” Atachita izi, anagwira nsomba zambiri kotero kuti makhoka awo anayamba kungʼambika. Choncho anakodola anzawo a bwato linalo kuti abwere ndi kuwathandiza, ndipo anabwera nadzaza mabwato onse awiri mpaka kuyamba kumira. Simoni Petro ataona izi, anagwa pa mawondo a Yesu nati, “Chokani kwa ine Ambuye: Ine ndine munthu wochimwa!” Iye ndi anzake onse anadabwa ndi nsomba zimene anagwira, chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anzake a Simoniyo. Kenaka Yesu anati kwa Simoni, “Musachite mantha; kuyambira tsopano ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” Kenaka anakokera mabwato awo ku mtunda, nasiya zonse namutsata Iye.

Zitatha izi, Yesu anachoka ndipo anaona wolandira msonkho dzina lake Levi atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anati kwa iye, “Nditsate Ine.” Ndipo Levi anayimirira, nasiya zonse ndi kumutsata Iye.

“Nthawi imeneyo sangalalani ndipo lumphani ndi chimwemwe chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba. Pakuti ndi zomwezonso zimene makolo awo anachitira aneneri.

Ndipo Iye anawayankha otumidwawo kuti, “Bwererani ndi kukamuwuza Yohane zimene mwaona ndi kumva: Osaona akuona, olumala akuyenda, akhate akuchiritsidwa, osamva akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo Uthenga Wabwino ukulalikidwa kwa osauka. Odala munthu amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.”

Zitatha izi, Yesu anayendayenda kuchoka mzinda wina kupita wina ndiponso mudzi wina kupita wina, akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ophunzira ake khumi ndi awiri aja anali naye,

“Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa mbewuzo, zina zinagwa mʼmbali mwa njira; zinapondedwa, ndipo mbalame zamlengalenga zinadya. Zina zinagwa pa thanthwe, ndipo pamene zinamera, zinafota chifukwa panalibe chinyezi. Mbewu zina zinagwera pakati pa minga, zinakulira pamodzi ndi mingazo ndipo zinalepheretsa mmerawo kukula. Mbewu zina zinagwera pa nthaka yabwino. Zinamera ndipo zinabala mowirikiza 100 kuposa zimene zinafesedwa zija.” Atanena izi, anafuwula kuti, “Amene ali ndi makutu, amve.” Ophunzira ake anamufunsa tanthauzo lake la fanizolo. Iye anati, “Kudziwa zinsinsi za ufumu wa Mulungu kwapatsidwa kwa inu, koma kwa ena ndimawayankhula mʼmafanizo kuti, “ngakhale akuona, asapenye; ngakhale akumva, asazindikire.”

“Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbewu ndi mawu a Mulungu. Mbewu za mʼmbali mwa njira ndi anthu amene amamva mawu, ndipo kenaka mdierekezi amabwera ndi kuchotsa mawuwo mʼmitima mwawo kuti asakhulupirire ndi kupulumutsidwa. Mbewu za pa thanthwe ndi anthu amene amalandira mawu mwachimwemwe pamene akumva, koma mawuwo sazika mizu. Iwo amakhulupirira kwa kanthawi, koma pa nthawi ya mayesero, amagwa. Mbewu zimene zinagwa pakati pa minga zikuyimira anthu amene amamva mawu, koma akamayenda mʼnjira zawo amatsamwitsidwa ndi zodandaulitsa za moyo uno, chuma ndi zosangalatsa, ndipo iwo samakhwima. Koma mbewu za pa nthaka yabwino zikuyimira anthu amene ali ndi mtima woona ndi wabwino, amene amamva mawu nawasunga, ndipo amalimbikira mpaka amabala zipatso.

“Bwerera kwanu kafotokoze zimene Mulungu wakuchitira.” Ndipo munthuyo anachoka ndi kukanena ku mzinda wonsewo zimene Yesu anamuchitira iye.

Yesu atawayitana khumi ndi awiriwo pamodzi, Iye anawapatsa mphamvu ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda zonse ndi kuchiritsa matenda. Ndipo Iye anawatumiza kukalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kukachiritsa odwala. Iye anawawuza kuti, “Musatenge kanthu paulendo. Musatenge ndodo, thumba, buledi, ndalama, ndi malaya apadera. Nyumba iliyonse imene mulowa, mukhale momwemo kufikira mutachoka mu mzindawo.

Ngati anthu sakulandirani, sasani fumbi la kumapazi anu pomwe mukuchoka mu mzinda wawo ngati umboni owatsutsa.” Ndipo iwo ananyamuka napita, mudzi ndi mudzi, kulalikira Uthenga Wabwino ndi kuchiritsa anthu paliponse.

Ndipo Iye anawuza onse kuti, “Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku nʼkumanditsata Ine. Popeza aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupulumutsa. Kodi chabwino ndi chiti kwa munthu, kupata zonse zapansi pano, koma ndi kutaya moyo wake kapena kudziwononga iye mwini?

Ngati wina aliyense achita nane manyazi ndi ndiponso mawu anga, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wake ndi mu ulemerero wa Atate ndi angelo oyera.

Iye anati kwa wina, “Nditsate Ine.” Koma munthuyo anayankha kuti, “Ambuye, choyamba loleni ndipite kuti ndikayike maliro a abambo anga.” Yesu anati kwa iye, “Aleke akufa ayikane akufa okhaokha, koma iwe pita ukalalikire ufumu wa Mulungu.”

Koma winanso anati, “Ine ndidzakutsatani Ambuye; koma choyamba ndiloleni ndibwerere kuti ndikatsanzikane nalo banja langa.” Yesu anayankha kuti, “Munthu amene akulima ndi khasu lokokedwa nʼkumayangʼana mʼmbuyo, si woyenera kugwira ntchito mu ufumu wa Mulungu.”

Zitatha izi Ambuye anasankha enanso 72 ndi kuwatumiza awiriawiri patsogolo pake ku mzinda uliwonse ndi kumalo kumene Iye anatsala pangʼono kupitako.

Iye anawawuza kuti, “Zokolola ndi zambiri, koma ogwira ntchito ndi ochepa. Pemphani Ambuye wa zokolola, kuti atumize antchito ku munda wake wa zokolola.

Pitani! Ine ndikukutumizani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Musatenge chikwama kapena thumba kapena nsapato; ndipo musalonjere wina aliyense pa njira.

Koma mukalowa mʼmudzi ndipo osalandiridwa bwino, kapiteni ku misewu mʼmudzimo nʼkukanena kuti, ‘Tikukusansirani ngakhale fumbi la mʼmudzi wanuwu limene lamamatira ku mapazi athuwa. Komabe dziwani izi: Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ Ine ndikuwuzani kuti adzachita chifundo polanga Sodomu pa tsikulo kusiyana ndi mudziwo.

“Womvera inu, akumvera Ine; wokana inu, akukana Ine. Ndipo wokana Ine; akukana Iye amene anandituma Ine.”

Anthu a ku Ninive adzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi mʼbado uno ndipo adzawutsutsa, pakuti anatembenuka mtima ndi ulaliki wa Yona. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Yona.

“Ine ndikukuwuza kuti, aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Mwana wa Munthu adzamuvomerezanso pamaso pa angelo a Mulungu. Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu adzakanidwanso pamaso pa angelo a Mulungu.

“Akadzakutengerani ku masunagoge pamaso pa oweruza ndi a maulamuliro, musadere nkhawa mmene mudzadzitchinjirizire nokha kapena chimene mudzayankhule, pakuti Mzimu Woyera nthawi imeneyo adzakuphunzitsani zoyenera kunena.”

Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupereke kwa osauka. Dzipezereni zikwama zandalama zimene sizidzatha, ndi kudzikundikira chuma chomwe sichidzatha kumwamba, kumene mbala sizingafikeko, ndipo dzimbiri silingawononge. Popeza kumene kuli chuma chanu, mtima wanunso udzakhala komweko.”

Kodi mukuganiza kuti Ine ndinabwera kudzabweretsa mtendere pa dziko lapansi? Ayi, Ine ndikukuwuzani kuti, ndinabweretsa kugawikana. Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo mʼbanja limodzi mudzakhala anthu asanu ndipo adzawukirana wina ndi mnzake, atatu kuwukira awiri, ndipo awiri kuwukira atatu. Anthu adzawukirana. Abambo kudzawukira mwana wawo wamwamuna, mwana wawoyo adzawukira abambo ake. Amayi adzawukira mwana wawo wamkazi, mwana wawoyo adzawukira amayi ake. Amayi adzawukira mpongozi wawo wamkazi, mpongoziyo adzawukira amayiwo.”

Ine ndikuti, ayi! Koma ngati inu simutembenuka mtima, inunso mudzawonongeka nonse.”

Yesu anayankha kuti, “Munthu wina ankakonza phwando lalikulu ndipo anayitana alendo ambiri. Nthawi yaphwando itakwana anatuma wantchito wake kuti akawuze onse amene anayitanidwa kuti, ‘Bwerani, pakuti zonse zakonzeka.’ “Koma onse anayamba kupereka zifukwa mofanana. Woyamba anati, ‘Ine ndangogula kumene munda, ndipo ndikuyenera kupita kuti ndikawuone. Pepani mundikhululukire.’ “Wina anati, ‘Ndangogula kumene ngʼombe khumi zokoka ngolo ndipo kupita kukaziyesa. Pepani mundikhululukire.’ “Wina anatinso, ‘Ine ndangokwatira kumene, choncho sinditha kubwera.’ “Wantchitoyo anabwera ndikudzamuwuza bwana wakeyo zimenezi. Pamenepo mphwandoyo anapsa mtima ndipo analamula wantchito wakeyo kuti, ‘Pita msangamsanga kunja mʼmisewu ndi mʼmakwalala a mu mzinda ndipo ukabweretse osauka, ofa ziwalo, osaona ndi olumala.’ “Wantchitoyo anati, ‘Bwana, zimene munanena zachitika koma malo akanalipobe.’ “Ndipo mbuye uja anawuza wantchito wake kuti, ‘Pita kunja ku misewu ikuluikulu ndi kunja kwa mpanda ndipo ukawawuze kuti alowe, kuti nyumba yanga idzaze. Ine ndikukuwuzani inu kuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anayitanidwa adzalawa phwandolo.’ ”

“Ngati wina aliyense abwera kwa Ine ndipo sadana ndi abambo ndi amayi ake, mkazi wake ndi ana, abale ake ndi alongo ake, inde ngakhale moyo wake omwe, iye sangakhale ophunzira wanga. Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sangakhale ophunzira wanga.

Mʼnjira yomweyo, wina aliyense wa inu amene sasiya zonse ali nazo sangakhale ophunzira wanga. “Mchere ndi wabwino, koma ngati usukuluka adzawukoleretsanso ndi chiyani?

Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale.”

Momwemonso, Ine ndikukuwuzani kuti angelo a Mulungu amakondwera kwambiri chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima.”

Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.”

Tsiku lina pamene Iye ankaphunzitsa anthu mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu ndi kuphunzitsa Uthenga Wabwino, akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, pamodzi ndi akuluakulu anabwera kwa Iye.

“Koma zonsezi zisanachitike, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzakuperekani ku masunagoge ndi ku ndende, ndipo adzakutengerani pamaso pa mafumu ndi olamulira, ndipo zonsezi zidzachitika chifukwa cha dzina langa. Umenewu udzakhala mwayi wanu ochitira umboni.

Koma tsimikizani mtima kuti musadzade nkhawa za momwe mudzadzitchinjirizire. Pakuti Ine ndidzakupatsani mawu ndi nzeru kotero kuti palibe mmodzi wa adani anu adzathe kuwakana kapena kuwatsutsa.

Inu mudzaperekedwa ndi makolo anu, abale, anansi ndi abwenzi anu ndipo ena mwa inu adzakuphani. Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine.

Kenaka Yesu anawafunsa iwo kuti, “Ine nditakutumizani wopanda chikwama cha ndalama, thumba kapena nsapato, kodi inu munasowa kanthu?” Iwo anayankha kuti, “Palibe chimene tinasowa.” Iye anawawuza kuti, “Koma tsopano ngati muli ndi chikwama cha ndalama, chitengeni, ndiponso thumba. Ndipo ngati mulibe lupanga, gulitsani mkanjo wanu ndi kugula.

Ndipo kutembenuka mtima ndi kukhululukidwa kwa machimo zidzalalikidwa mu dzina lake kwa anthu amitundu yonse kuyambira mu Yerusalemu. Inu ndinu mboni za zimenezi.

Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu; ana wobadwa osati monga mwachilengedwe, kapena chisankho cha munthu, kapena chifuniro cha mwamuna koma wobadwa mwa Mulungu.

Pa tsiku lotsatira Yesu anaganiza zopita ku Galileya. Atamupeza Filipo, anati kwa iye, “Nditsate.”

Poyankha Yesu ananena kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu.” Nekodimo anati, “Kodi munthu angabadwenso bwanji atakalamba? Kodi angalowe kachiwiri mʼmimba ya amayi ake kuti abadwenso?” Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu. Thupi limabereka thupi, koma Mzimu amabereka mzimu. Iwe usadabwe chifukwa ndakuwuza kuti, ‘Uyenera kubadwanso.’ Mphepo imawomba kulikonse kumene ikufuna. Ungathe kumva kuwomba kwake, koma sungathe kudziwa kumene ikuchokera kapena kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi amene abadwa ndi Mzimu Woyera.”

Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ife tiyankhula zimene tikuzidziwa ndi kuchitira umboni zimene taziona, komabe inu simuvomereza umboni wathu. Ine ndikuyankhula kwa iwe zinthu za dziko lapansi ndipo sukukhulupirira. Nanga kodi udzakhulupirira bwanji ngati nditayankhula zinthu zakumwamba?

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi. Aliyense wokhulupirira Iye saweruzidwa, koma aliyense wosakhulupirira waweruzidwa kale chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. Ndipo chiweruzo ndi ichi: kuwunika kunabwera mʼdziko lapansi, koma anthu anakonda mdima mʼmalo mwa kuwunikako, chifukwa ntchito zawo zinali zoyipa. Aliyense wochita zoyipa amadana ndi kuwunika, ndipo sabwera poyera chifukwa cha mantha kuti ntchito zake zingaonekere. Koma aliyense wokhala mu choonadi amabwera ku kuwunika, kuti zionekere poyera zimene iye wachita zachitika kudzera mwa Mulungu.”

Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.”

Kodi inu simunena kuti, ‘Kwatsala miyezi inayi ndipo kenaka kukolola?’ Ine ndikukuwuzani kuti, tsekulani maso anu ndipo muyangʼane mʼminda! Mbewu zacha kale kuti zikololedwe. Ngakhale tsopano amene akukolola akulandira malipiro ake, ndipo akututa mbewu ku moyo wosatha kuti wofesa ndi wokolola asangalale pamodzi. Nʼchifukwa chake mawu akuti, ‘Wina amafesa ndipo wina amakolola’ ndi woona. Ine ndinakutumani kukakolola zimene simunagwirire ntchito. Ena anagwira ntchito yolemetsa ndipo inu mwatuta phindu la ntchito yawo.”

“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo.

Ine ndinakuwuzani kuti mudzafera mʼmachimo anu ngati simukhulupirira kuti Ine Ndine. Ndithu inu mudzafera mʼmachimo anu.”

Kwa Ayuda amene anamukhulupirira, Yesu anati, “Ngati inu mutsatira chiphunzitso changa, ndithu ndinu ophunzira anga. Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”

Ife tiyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma kukanali masana. Usiku ukubwera, pamene wina aliyense sadzagwira ntchito.

“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani inu Afarisi, kuti munthu amene salowera pa khomo mʼkhola la nkhosa, koma amalowera pena pake ndi wakuba ndi wachifwamba.

Iye amene akana Ine ndipo salandira mawu anga ali ndi womuweruza. Tsiku lomaliza mawu amene ndiyankhulawa adzamutsutsa. Pakuti Ine sindiyankhula mwa Ine ndekha, koma Atate amene anandituma amandilamulira choti ndinene ndi momwe ndinenere.

Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.

Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi kuti mukakhulupirira mukhale nawo moyo mʼdzina lake.

Iye anati, “Ponyani khoka lanu kudzanja lamanja la bwato lanu ndipo mupha kanthu.” Atatero, iwo analephera kukoka ukonde chifukwa chakuchuluka kwa nsomba. Kenaka ophunzira amene Yesu amamukonda anati kwa Petro, “Ndi Ambuye!” Petro atangomva iye akunena kuti ndi Ambuye, iye anavala chovala chake (pakuti anali atavula) ndipo analumphira mʼnyanja. Ophunzira enawo analowa mʼbwato akukoka ukonde odzaza ndi nsomba, popeza iwo sanali kutali kuchokera ku mtunda, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi. Atafika pa mtunda, iwo anaona moto wamakala pamenepo ndi nsomba, ndi buledi. Yesu anawawuza kuti, “Tabweretsa nsomba zina mwagwirazo.” Simoni Petro anakwera mʼbwato ndi kukokera khoka ku gombe, lodzaza ndi nsomba zikuluzikulu 153, komabe ndi nsomba zochuluka chotero khoka silinangʼambike.

Koma mudzalandira mphamvu Mzimu Woyera akadzafika pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”

Ndipo aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.’

Petro anawayankha kuti, “Lapani ndipo mubatizidwe aliyense wa inu, mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe. Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti lonjezoli ndi lanu ndi ana anu ndiponso la onse amene ali kutali, ndi iwo onse amene Ambuye Mulungu wathu adzawayitane.” Petro anawachenjeza ndi mawu ena ambiri, ndipo anawadandaulira iwo kuti, “Mudzipulumutse ku mʼbado owonongeka uno.”

Iwo amene anawulandira uthenga wake anabatizidwa ndipo tsiku lomwelo miyoyo pafupifupi 3,000 inawonjezedwa ku gulu lawo.

Ankayamika Mulungu ndipo anthu onse ankawakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankawonjezera ena pa chiwerengero cha olandira chipulumutso.

Chifukwa chake, lapani, bwererani kwa Mulungu, kuti machimo anu afafanizidwe, kuti nthawi ya kutsitsimuka ibwere kuchokera kwa Ambuye, ndi kuti Iye atumize Yesu Khristu amene anasankhidwa chifukwa cha inu. Iye ayenera kukhalabe kumwamba mpaka nthawi ya kukonzanso zinthu zonse monga Mulungu analonjeza kale kudzera mwa aneneri ake oyera mtima.

Koma anthu ambiri amene anamva uthenga anakhulupirira, ndipo chiwerengero cha anthu chinakwana 5,000.

Chipulumutso sichipezeka mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo limene lapatsidwa kwa anthu limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”

Ataona kulimba mtima kwa Petro ndi Yohane ndi kuzindikira kuti anali osaphunzira, anthu wamba, anadabwa kwambiri ndipo anazindikira kuti anthuwa anakhala pamodzi ndi Yesu.

Pamenepo anawayitananso ndipo anawalamula kuti asayankhule kapena kuphunzitsa konse mʼdzina la Yesu. Koma Petro ndi Yohane anayankha kuti, “Weruzani nokha ngati nʼkwabwino pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu. Ife sitingaleke kuyankhula za zimene tinaziona ndi kuzimva.”

Tsopano, Ambuye taonani kuti atiopseza, tithandizeni ife atumiki anu, kuti tiyankhule mawu anu molimba mtima. Tambasulani dzanja lanu kuchiritsa anthu ndipo kuti, zizindikiro zodabwitsa zichitike mʼdzina la mtumiki wanu woyera Yesu.” Iwo atatha kupemphera, malo amene anasonkhanapo anagwedezeka. Ndipo iwo onse anadzazidwa ndi Mzimu Woyera ndipo anayankhula Mawu a Mulungu molimba mtima.

Atumwi anapitirira kuchitira umboni mwa mphamvu zakuuka kwa Ambuye Yesu, ndipo pa iwo panali chisomo chochuluka.

Atafika nawo atumwi aja, anawayimika pamaso pa Bwalo Lalikulu kuti afunsidwe mafunso ndi mkulu wa ansembe. Iye anati, “Ife tinakuletsani kuti musaphunzitsenso mʼdzina ili, koma inu mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mukufuna kutisenzetsa imfa ya munthu ameneyu.” Petro ndi atumwi enawo anayankha kuti, “Ife tiyenera kumvera Mulungu osati anthu!

Akuluakulu enawo anavomerezana naye. Iwo anayitana atumwi aja ndipo anawakwapula kwambiri. Ndipo anawalamula kuti asayankhulenso mʼdzina la Yesu ndipo anawamasula. Iwo anachoka ku Bwalo Lalikulu akukondwa chifukwa anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzina la Yesu. Ndipo tsiku ndi tsiku, sanaleke kuphunzitsa ndi kulalikira mʼNyumba ya Mulungu komanso nyumba ndi nyumba, Uthenga Wabwino wa kuti Yesu ndi Khristu.

Okhulupirira amene anabalalika amalalikira konse kumene amapita. Filipo anapita ku mzinda wa ku Samariya ndipo analalikira za Khristu kumeneko.

Koma atakhulupirira Filipo akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ndiponso dzina la Yesu Khristu, anthuwo anabatizidwa amuna ndi amayi.

Atatha kuchitira umboni ndi kulalikira mawu a Ambuye, Petro ndi Yohane anabwerera ku Yerusalemu, atalalikira Uthenga Wabwino mʼmidzi yambiri ya Asamariya.

Pamenepo Filipo anayambira pa malemba omwewo kumuwuza za Uthenga Wabwino wa Yesu. Akuyenda mu msewu anafika pamalo pamene panali madzi ndipo ndunayo inati, “Taonani madzi awa. Kodi pali chondiletsa kuti ndibatizidwe?” Filipo anati, “Ngati mukhulupirira ndi mtima wanu wonse mukhoza kubatizidwa.” Ndunayo inayankha kuti, “Ine ndikukhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu.” Ndipo analamulira galeta kuti liyime. Onse awiriwo, Filipo ndi Ndunayo anatsika ndi kulowa mʼmadzi ndipo Filipo anamubatiza.

Koma Filipo anapezeka kuti ali ku Azoto ndipo anazungulira konse, kulalikira Uthenga Wabwino mʼmizinda yonse mpaka anakafika ku Kaisareya.

Koma Barnaba anamutenga napita naye kwa atumwi. Iye anawafotokozera iwo za mmene Saulo anaonera Ambuye pa njira paja, ndi kuti Ambuye anamuyankhula, ndi momwe analalikira ku Damasiko mʼdzina la Yesu mosaopa. Kotero Saulo anakhala nawo nayendayenda mwaufulu mu Yerusalemu akulalikira molimba mtima mʼdzina la Ambuye. Anayankhula ndi kutsutsana ndi Ayuda a Chihelene, koma iwo ankafuna kumupha.

Uwu ndi uthenga umene Mulungu anatumiza kwa Aisraeli, kulalikira Uthenga Wabwino wamtendere mwa Yesu Khristu amene ndi Ambuye wa onse. Inu mukudziwa zimene zinachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa ubatizo umene Yohane analalikira,

Iye anatilamulira ife kuti tilalikire kwa anthu ndi kuchitira umboni kuti Iye ndiye amene Mulungu anamusankha kukhala woweruza wa amoyo ndi akufa. Aneneri onse achitira Iye umboni kuti aliyense amene akhulupirira Iye amakhululukidwa machimo chifukwa cha dzina lake.” Petro akuyankhulabe mawu amenewa, Mzimu Woyera unatsikira pa onse amene amamva uthengawo.

Atumwi ndi abale a ku Yudeya konse anamva kuti anthu a mitundu ina analandiranso Mawu a Mulungu.

Iye anatiwuza mmene anaonera mngelo atayimirira mʼnyumba mwake ndi kumuwuza kuti, ‘Tumiza anthu ku Yopa kuti akayitane Simoni wotchedwa Petro. Iye adzakuwuza uthenga umene udzapulumutsa iwe ndi a pa banja ako.’

Iwo atamva zimenezi analibenso chonena ndipo anayamika Mulungu nati, “Potero Mulungu wapatsa anthu a mitundu ina mwayi wotembenuka mtima ndi kulandira moyo.”

Komabe, ena pakati pawo ochokera ku Kupro ndi ku Kurene anapita ku Antiokeya ndipo iwo anayamba kuyankhulanso kwa Agriki, nawawuza za Uthenga Wabwino wa Ambuye Yesu. Mphamvu ya Ambuye inali nawo ndipo anthu ambiri anakhulupirira natembenukira kwa Ambuye.

Yesu asanabwere, Yohane analalikira kwa anthu onse Aisraeli za kutembenuka mtima ndi ubatizo.

“Ife tikukuwuzani Uthenga Wabwino; umene Mulungu analonjeza makolo athu.

Pa Sabata linalo pafupifupi anthu onse a mu mzindawo anasonkhana kudzamva Mawu a Ambuye.

Ndipo Paulo ndi Barnaba anawayankha molimba mtima kuti, “Ife tinayenera kuyankhula Mawu a Mulungu kwa inu poyamba. Popeza inu mwawakana ndi kudziyesa nokha osayenera moyo wosatha, ife tsopano tikupita kwa anthu a mitundu ina. Pakuti izi ndi zimene Ambuye anatilamula ife: “ ‘Ine ndakuyika iwe ukhale kuwunika kwa anthu a mitundu ina, kuti ukafikitse chipulumutso ku malekezero a dziko lapansi!’ ”

Anthu a mitundu ina atamva izi, anakondwa ndipo analemekeza Mawu Ambuye; ndipo onse amene anawasankha kuti alandire moyo osatha anakhulupirira. Mawu a Ambuye anafalikira mʼchigawo chonse.

Koma Ayuda anawutsa mitima ya akazi otchuka opembedza Mulungu ndi akulu a mu mzindamo. Iwo anabweretsa mazunzo kwa Paulo ndi Barnaba ndipo anawathamangitsa mʼchigawo chawo. Tsono iwo anasasa fumbi la ku mapazi awo powatsutsa, ndipo anapita ku Ikoniya.

Ku Ikoniya, Paulo ndi Barnaba analowanso mʼsunagoge ya Ayuda. Kumeneko iwo anaphunzitsa momveka bwino kotero kuti anthu ambiri Achiyuda ndi anthu a mitundu ina anakhulupirira. Koma Ayuda amene anakana kukhulupirira anawutsa anthu a mitundu ina nawononga maganizo awo kutsutsana ndi abale.

Ndipo Paulo ndi Barnaba anakhala kumeneko nthawi yayitali, nalalikira molimba mtima za Ambuye amene anawapatsa mphamvu yochitira zozizwitsa ndi zizindikiro zodabwitsa pochitira umboni mawu a chisomo.

“Anthu inu, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Ife takubweretserani Uthenga Wabwino, kuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo.

Iwo analalikira Uthenga Wabwino mu mzindawo ndipo anthu ambiri anatembenuka mtima ndi kukhala ophunzira. Kenaka anabwerera ku Lusitra, ku Ikoniya ndi ku Antiokeya. Kumeneko analimbikitsa mitima ya ophunzira ndi kuwapatsa mphamvu kuti akhalebe woona mʼchikhulupiriro. Iwo anati, “Ife tiyenera kudutsa mʼmasautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.”

Atakambirana kwambiri Petro anayimirira, ndipo anawayankhula nati: “Abale, mukudziwa kuti masiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu kuti anthu a mitundu ina amve kuchokera pakamwa panga mawu a Uthenga Wabwino ndi kukhulupirira.

Paulo ndi anzake anadutsa mayiko a Frugiya ndi Galatiya, Mzimu Woyera atawaletsa kulalikira Mawu a Mulungu ku Asiya. Atafika ku malire a Musiya, anayesa kulowa ku Bituniya, koma Mzimu wa Yesu sunawalole kutero. Ndipo iwo anadutsa Musiya ndipo anapita ku Trowa. Nthawi ya usiku Paulo anaona masomphenya, munthu wa ku Makedoniya atayimirira ndi kumupempha kuti, “Bwerani ku Makedoniya, mudzatithandize.” Paulo ataona masomphenyawa, tinakonzeka kupita ku Makedoniya, kutsimikiza kuti Mulungu anatiyitana kuti tikalalikire Uthenga Wabwino.

Woyangʼanira ndendeyo anayitanitsa nyale, nathamangira mʼkati ndipo anadzigwetsa pa mapazi a Paulo ndi Sila akunjenjemera. Iye anawatulutsa kunja ndipo anawafunsa kuti, “Amuna inu, ndichite chiyani kuti ndipulumuke?” Iwo anayankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka, iwe ndi a mʼbanja lako.”

Paulo, monga mwachizolowezi chake, analowa mʼsunagoge, ndipo anakambirana nawo Mawu a Mulungu kwa masabata atatu, kuwafotokozera ndi kuwatsimikizira kuti Khristu anayenera kufa ndi kuuka. Iye anati, “Yesu amene ndikukulalikirani ndiye Khristu.” Ena mwa Ayuda anakopeka mtima ndipo anatsatira Paulo ndi Sila, monganso linachitira gulu lalikulu la Agriki woopa Mulungu, pamodzi ndi amayi odziwika ambiri.

Tsopano anthu a ku Bereya anali akhalidwe labwino kusiyana ndi Atesalonika, pakuti iwo analandira mawu ndi chidwi chachikulu ndipo ankasanthula Malemba tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zimene ankanena Paulozo zinali zoona.

Paulo anayimirira mʼbwalo la Areopagi nati: “Inu anthu a ku Atene! Ine ndikuona kuti mʼnjira zonse ndinu opembedza kwambiri. Pakuti pamene ndimayenda ndi kuona zinthu zimene mumazipembedza, ndapezanso guwa lansembe lolembedwapo kuti, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Tsopano chimene mumachipembedza osachidziwa ndi chimene ndikuchilalikira. “Mulungu amene analenga dziko lapansi ndiponso zonse zili mʼmenemo ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndipo sakhala mʼnyumba zachipembedzo zomangidwa ndi manja. Ndipo satumikiridwa ndi manja a anthu ngati kuti Iye amasowa kanthu, chifukwa Iye ndiye amapereka moyo ndi mpweya kwa anthu onse ndi zina zonse. Kuchoka kwa munthu mmodzi Iye analenga mtundu uliwonse wa anthu, kuti akakhale pa dziko lonse lapansi; ndipo Iye anakonzeratu nthawi yawo ndiponso malo enieni kumene adzakhale. Mulungu anachita izi kuti anthu amufunefune, ndikuti pomufunafunapo amupeze ngakhale kuti Iye sali kutali ndi aliyense wa ife. ‘Pakuti timakhala mwa Iye, kuyenda mwa Iye ndi kukhala moyo mwa Iye.’ Monga olemba ndakatulo anu ena akuti, ‘Ife ndi zidzukulu zake.’ “Tsono popeza ndife ana a Mulungu, tisaganize kuti umulungu wake ndi wofanana ndi ndalama zagolide, zasiliva, mwala, kapenanso fanizo lopangidwa mwaluso la nzeru za anthu. Nthawi imene anthu sankadziwa, Mulungu anawalekerera koma tsopano akulamulira kuti anthu onse, kulikonse atembenuke mtima. Pakuti Iye wayika tsiku limene adzaweruze dziko lapansi mwa chilungamo kudzera mwa Munthu amene anamusankha. Iye watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.”

Pa nthawi yomweyi Myuda wina dzina lake Apolo, mbadwa ya ku Alekisandriya anafika ku Efeso. Anali munthu wophunzira ndi wodziwa bwino Malemba. Apoloyu anaphunzitsidwa njira ya Ambuye, ndipo anayankhula ndi changu chachikulu naphunzitsa za Yesu molondola, ngakhale amadziwa ubatizo wa Yohane wokha. Iye anayamba kuyankhula mʼsunagoge molimba mtima. Pamene Prisila ndi Akula anamva, iwo anamuyitanira ku nyumba yawo ndipo anamufotokozera njira ya Mulungu molongosoka bwino.

Paulo analowa mʼsunagoge ndipo anayankhula molimba mtima kwa miyezi itatu, kuwatsutsa mowakopa za ufumu wa Mulungu. Koma ena anawumitsa mitima; anakana kukhulupirira ndipo ananyoza Njirayo pa gulu la anthu. Kotero Paulo anawasiya. Iye anatenga ophunzirawo ndipo amakambirana tsiku ndi tsiku mʼsukulu ya Turano. Izi zinachitika kwa zaka ziwiri, kotero kuti Ayuda onse ndi Agriki amene amakhala ku Asiya anamva Mawu a Ambuye.

Inu mukudziwa kuti, sindinakubisireni kanthu kalikonse kopindulitsa koma ndinakuphunzitsani poyera komanso nyumba ndi nyumba. Ine ndinawuza Ayuda komanso Agriki kuti ayenera kutembenukira kwa Mulungu polapa ndikuti akhulupirire Ambuye athu Yesu. “Ndipo tsopano, mokakamizidwa ndi Mzimu, ndikupita ku Yerusalemu, sindikudziwa zimene zikandichitikire kumeneko.” Chimene ndikudziwa ndi chakuti Mzimu Woyera wandichenjeza mu mzinda uliwonse kuti ndende ndi mavuto zikundidikira. Koma sindilabadira konse za moyo wanga ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malingana ndikatsirize ntchito yanga ndi utumiki umene Ambuye Yesu anandipatsa, ntchito yochitira umboni Uthenga Wabwino wachisomo cha Mulungu.

Iwe udzakhala mboni yake kwa anthu onse pa zimene waziona ndi kuzimva.

Usiku omwewo Ambuye anayimirira pambali pa Paulo nati, “Limba mtima! Monga wandichitira Ine umboni mu Yerusalemu, moteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.”

Tsopano dzuka ndipo imirira. Ine ndaonekera kwa iwe kuti ndikusankhe kuti ukhale mtumiki ndiponso mboni ya zimene waziona za Ine ndiponso zimene ndidzakuonetsa.

kuti ukatsekule maso awo kuti atembenuke mtima kuchoka ku mdima ndi kulowa mʼkuwala, kuchoka ku mphamvu za Satana ndi kupita kwa Mulungu, kuti alandire chikhululukiro cha machimo awo ndi kukhala mʼgulu la amene akuyeretsedwa chifukwa chokhulupirira Ine.

Koma Mulungu wakhala akundithandiza mpaka lero lino. Ine ndayima pano kuti ndichitire umboni kwa anthu onse otchuka ndi anthu wamba. Ine sindikunena zina zowonjezera koma zimene Aneneri ndi Mose ananena kuti zidzachitika. Iwo ananena kuti Khristu adzamva zowawa ndipo popeza Iye adzakhala woyamba kuuka kwa akufa, adzalalikira za kuwunika kwa anthu a mtundu wake ndiponso kwa anthu a mitundu ina.”

Paulo anakhala kumeneko zaka ziwiri zathunthu mʼnyumba yobwereka yomwe amalipira ndipo ankalandira aliyense amene amabwera kudzamuona. Molimba mtima ndi popanda womuletsa, Paulo analalikira za ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu.

Poyamba, ndikuthokoza Mulungu wanga kudzera mwa Yesu Khristu chifukwa cha nonsenu, pakuti pa dziko lonse lapansi anthu akukamba za chikhulupiriro chanu.

Ine ndi wokakamizidwa ndi udindo wotumikira Agriki pamodzi ndi omwe si Agriki, kwa anzeru ndi kwa opusa omwe. Pa chifukwa chimenechi, ine ndikufunitsitsa kulalikira Uthenga Wabwino kwa inunso amene muli ku Roma. Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino chifukwa ndiwo mphamvu za Mulungu zopulumutsa aliyense amene akhulupirira, poyamba Myuda, kenaka Mhelene.

Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera.

Pakuti malipiro a tchimo ndi imfa, koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

kuti ngati udzavomereza ndi pakamwa pako kuti, “Yesu ndiye Ambuye,” ndi kukhulupirira mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Pakuti ndi mtima wanu mukhulupirira ndi kulungamitsidwa, ndipo ndi pakamwa panu muvomereza ndi kupulumutsidwa. Pakuti Malemba akuti, “Aliyense amene akhulupirira Iye, sadzachititsidwa manyazi.” Pakuti palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi a mitundu ina, pakuti Ambuye mmodzi yemweyo ndi Ambuye wa onse ndipo amadalitsa mochuluka onse amene ayitana pa Iye pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”

Kodi adzayitana bwanji amene sanamukhulupirire? Ndipo adzakhulupirira bwanji asanamve za Iye? Ndipo adzamva bwanji popanda wina kulalikira kwa iwo? Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, “Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!”

Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, “Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?”

Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu. Koma ndikufunsa kuti kodi iwo anamva? Inde, iwo anamva kuti, “Liwu lawo linamveka ponseponse pa dziko lapansi. Mawu awo anafika ku malekezero a dziko lonse.”

mwamphamvu ya zizindikiro ndi zodabwitsa kudzera mwamphamvu ya Mzimu Woyera. Choncho kuchokera ku Yerusalemu ndi kuzungulira ku Iluriko, ine ndalalikira kwathunthu Uthenga Wabwino wa Khristu.

Tsopano kwa Iye amene ali ndi mphamvu yokhazikitsa monga mwa uthenga wanga wabwino ndikulalikidwa kwa Yesu Khristu, monga mwa vumbulutso lachinsinsi chobisika kwa nthawi yayitali, koma tsopano chavumbulutsidwa ndi kudziwika kudzera mʼMalemba a uneneri mwa lamulo la Mulungu wosatha, kuti mitundu yonse ikhulupirire ndi kumvera Iye,

Pakuti Khristu sananditume ine kudzabatiza, koma kudzalalikira Uthenga Wabwino, osati ndi mawu anzeru za umunthu, kuopa kuti mtanda wa Khristu ungakhale wopanda mphamvu. Pakuti uthenga wa mtanda ndi chopusa kwa iwo amene akuwonongeka, koma kwa ife amene tikupulumutsidwa uthengawu ndi mphamvu ya Mulungu. Pakuti kwalembedwa kuti, “Ine ndidzawononga nzeru za anthu anzeru; luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”

Tsono poti mwa nzeru za Mulungu dziko lapansi mu nzeru zake silinamudziwe Iye, Mulungu amakondweretsedwa kuti kudzera mu chopusa cha zomwe zinalalikidwa apulumutse iwo amene akhulupirira. Ayuda amafuna zizindikiro zodabwitsa ndipo Agriki amafunafuna nzeru, koma ife timalalikira Khristu wopachikidwa. Chitsa chokhumudwitsa kwa Ayuda ndi chopusa kwa a mitundu ina. Koma kwa iwo amene Mulungu anawayitana, Ayuda ndi Agriki omwe, Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndi nzeru za Mulungu. Pakuti za Mulungu zooneka ngati zopusa, ndi za nzeru kuposa nzeru za munthu, ndipo za Mulungu zooneka ngati zofowoka, zili ndi mphamvu kuposa mphamvu za munthu.

Pamene ndinabwera kwa inu, abale, sindinabwere ndi luntha lodziwa kuyankhula kapena nzeru zapamwamba pamene ndinachitira umboni chinsinsi cha Mulungu. Pakuti ndinatsimikiza pamene ndinali ndi inu kuti ndisadziwe kanthu kena kupatula Yesu Khristu wopachikidwayo. Ndinabwera kwa inu wofowoka ndi wamantha, ndiponso wonjenjemera kwambiri. Uthenga ndi ulaliki wanga sunali wa mawu anzeru ndi onyengerera koma woonetsa mphamvu za Mzimu, kuti chikhulupiriro chanu chisatsamire pa nzeru ya anthu koma pa mphamvu za Mulungu.

Komabe ife timayankhula uthenga wa nzeru kwa okhwima, koma osati ndi nzeru ya mʼbado uno kapena ya olamula a mʼbado uno, amene mphamvu yawo ikutha. Ayi, ife timayankhula za nzeru yobisika ya Mulungu, nzeru imene inabisidwa ndipo imene Mulungu anatikonzera mu ulemerero wathu isanayambe nthawi. Palibe olamulira aliyense wa mʼbado uno amene anamumvetsetsa popeza anakamumvetsetsa sakanamupachika Ambuye wa ulemerero. Komabe monga zalembedwa kuti, “Palibe diso linaona, palibe khutu linamva, palibe amene anaganizira, zimene Mulungu anakonzera amene amukonda”

koma Mulungu waululira ife mwa Mzimu wake. Mzimu amafufuza zinthu zonse, ndi zozama za Mulungu zomwe. Kodi ndani mwa anthu angadziwe maganizo a munthu wina, kupatula mzimu wa munthuyo wokhala mʼkati mwake? Chimodzimodzinso palibe amene adziwa maganizo a Mulungu kupatula Mzimu wa Mulunguyo. Mzimu amene tinalandira ife si wa dziko lapansi koma Mzimu wochokera kwa Mulungu wotipatsa ife mwaulere. Izi ndi zimene timayankhula osati mʼmawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma mʼmawu wophunzitsidwa ndi Mzimu, kufotokozera zoonadi zauzimu mʼmawu auzimu.

Munthu wopanda Mzimu savomereza zinthu zimene zichokera kwa Mzimu wa Mulungu, popeza ndi zopusa kwa iyeyo, ndipo sangazimvetsetse chifukwa zimazindikirika mwa Mzimu. Munthu wauzimu amaweruza pa zinthu zonse, koma iye mwini saweruzidwa ndi munthu aliyense. Pakuti “Ndani anadziwa malingaliro a Ambuye, kuti akhoza kumulangiza Iye.” Koma tili nawo mtima wa Khristu.

Ndipo abale sindikanakuyankhulani ngati auzimu koma adziko lapansi, makanda chabe mwa Khristu. Ndinakupatsani mkaka osati chakudya cholimba pakuti munali musanakonzeke kuchilandira. Zoonadi, simunakonzekebe.

Ine ndinadzala mbewu, Apolo anayithirira, koma Mulungu ndiye anayikulitsa. Choncho kuphatikiza iye wodzala ndi iye wothirira, onse sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amakulitsa zinthu. Munthu wodzala ndi munthu wothirira ali ndi cholinga chimodzi, ndipo aliyense adzapatsidwa mphotho molingana ndi ntchito yake. Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; inu ndinu munda wa Mulungu, Nyumba ya Mulungu.

Mwachisomo chimene Mulungu wandipatsa, ine ndinayika maziko monga mmisiri waluntha, ndipo ena akumangapo. Koma aliyense ayenera kuchenjera mmene akumangira. Pakuti wina sangayikenso maziko ena oposera amene anakhazikitsidwa kale, amene ndi Yesu Khristu. Ngati munthu aliyense amanga pa maziko awa pogwiritsa ntchito golide, siliva, miyala yamtengowapatali, milimo yamitengo, tsekera kapena udzu, ntchito yake idzaonekera pamene Tsiku la chiweruzo lidzazionetsa poyera. Tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito ya munthu aliyense. Ngati zimene zamangidwazo sizidzagwa, adzalandira mphotho yake. Ndipo ngati zidzanyeke ndi moto, sadzalandira mphotho koma iye mwini adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wapulumuka mʼmoto.

Komatu ndikamalalikira Uthenga Wabwino, sindingadzitamandire popeza ndimawumirizidwa kulalikira. Tsoka kwa ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino!

Ngati ndikugwira ntchitoyi mwakufuna kwanga, ndili ndi mphotho; koma ngati si mwakufuna kwanga, ndiye kuti ntchitoyi ndi Ambuye anandipatsa. Tsono mphotho yanga ndi chiyani? Ndi iyi: kuti polalikira Uthenga Wabwino ndiwupereke kwaulere komanso kuti ndisagwiritse ntchito ufulu wanga polalikira uthengawo.

Ngakhale ndine mfulu ndipo sindine kapolo wa munthu, ndimadzisandutsa kapolo wa aliyense kuti ndikope ambiri mmene ndingathere. Kwa Ayuda ndimakhala ngati Myuda kuti ndikope Ayuda. Kwa olamulidwa ndi Malamulo ndimakhala ngati wolamulidwa nawo (ngakhale kuti sindine wolamulidwa ndi Malamulowo) kuti ndikope amene amalamulidwa ndi Malamulo. Kwa amene alibe Malamulo ndimakhala wopanda Malamulo (ngakhale kuti sindine wopanda Malamulo a Mulungu koma ndili pansi pa ulamuliro wa Khristu) kuti ndikope wopanda Malamulo. Kwa ofowoka ndimakhala wofowoka, kuti ndikope ofowoka. Ndimachita zinthu zilizonse kwa anthu onse kuti mwanjira ina iliyonse ndipulumutse ena.

Ngati ndili ndi mphatso ya uneneri, nʼkumazindikira zinsinsi ndi kudziwa zonse, ndipo ngati ndili ndi chikhulupiriro chosuntha mapiri, koma wopanda chikondi, ine sindili kanthu. Ngati ndipereka zanga zonse kwa osauka ndi kupereka thupi langa kuti alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ine sindipindula kanthu.

Tsono abale, ndikufuna ndikukumbutseni za Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani. Munawulandira ndipo munawukhulupirira kolimba. Inu munapulumutsidwa ndi Uthenga Wabwinowu, ngati mwasunga mawu amene ndinakulalikirani. Kupanda kutero, mwangokhulupirira pachabe.

Koma mwachisomo cha Mulungu, ndili mmene ndililimu, ndipo chisomo chake kwa ine sichinali chopanda ntchito. Ndinagwira ntchito kuposa ena onse a iwo. Choncho sindine koma chisomo cha Mulungu chimene chinali ndi ine. Tsono kaya ndi ineyo kapena iwowo, izi ndi zomwe timalalikira, ndipo izi ndi zimene munakhulupirira.

Wopusa iwe! Chimene mudzala sichikhala ndi moyo pokhapokha chitayamba chafa. Mukadzala, simudzala thupi limene lidzamere, koma mbewu chabe, mwina ya tirigu kapena ya china chake.

Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino. Pakuti kwa Mulungu ndife fungo labwino la Khristu pakati pa iwo amene akupulumutsidwa ndi amene akuwonongeka. Kwa amene akuwonongeka ndife fungo la imfa, limawapha. Ndipo kwa amene akupulumuka ndife fungo lamoyo, limawapatsa moyo. Ndani angayithe ntchito yotereyi?

Kusiyana ndi ena ambiri, ife sitilalikira Mawu a Mulungu kuti tipeza phindu. Mʼmalo mwake, ife mwa Khristu timayankhula pamaso pa Mulungu moona mtima, monga anthu otumidwa ndi Mulungu.

Koma ngati utumiki umene unabweretsa imfa uja, wolembedwa ndi malemba pa mwalawu, unabwera ndi ulemerero mwakuti Aisraeli sanathe kuyangʼanitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha ulemerero wa pa nkhopeyo, ngakhale kuti unali kunka nuzilala, kodi nanga utumiki wa Mzimu sudzaposa apa? Ngati utumiki umene umatsutsa anthu unali ndi ulemerero, nanga koposa kotani ulemerero wa utumiki wobweretsa chilungamo! Pakuti zimene zinali ndi ulemerero, tsopano zilibenso ulemerero pofananitsa ndi ulemerero wopambanawo. Ndipo ngati zosakhalitsa zinabwera ndi ulemerero, koposa kotani ulemerero wamuyayawo!

Choncho, popeza tili ndi chiyembekezo chotere, ndife olimba mtima kwambiri.

Zonsezi zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa ndi Iye mwini kudzera mwa Khristu ndipo anatipatsa ife utumiki wa chiyanjanitso. Mulungu ankayanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthu monga mwa zochimwa zawo. Ndipo watisungitsa ife uthenga uwu wa chiyanjanitso.

Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu.

Pakuti akunena kuti, “Pa nthawi yanga yabwino yokomera anthu mtima ndinakumvera, ndipo pa nthawi yopulumutsa ndinakuthandiza. Taonani, ndikukuwuzani kuti, ino ndiyo nthawi yabwino ya Ambuye, lero ndiye tsiku la chipulumutso.”

Ife sitikuyika chokhumudwitsa pa njira ya wina aliyense, kuti utumiki wathu usanyozeke.

Chisoni chimene Mulungu amafuna chimabweretsa kutembenuka mtima komwe kumabweretsa chipulumutso, ndipo sichikhumudwitsa. Koma chisoni cha dziko lapansi chimabweretsa imfa.

Takumbukirani mawu awa: Amene adzala pangʼono, adzakololanso pangʼono, ndipo amene adzala zochuluka, adzakololanso zochuluka.

Tsono Mulungu amene amapereka mbewu kwa wofesa, ndiponso chakudya kuti adye, adzaperekanso mbewu mʼnkhokwe zanu ndi kuzichulukitsa. Iye adzachulukitsanso zipatso za chilungamo chanu.

kuti tikalalikire Uthenga Wabwino mu zigawo zina kupitirira kwanuko. Pakuti sitikufuna kudzitama pa ntchito yogwira ena kale mʼdera la munthu wina.

Kodi linali tchimo kwa ine kudzichepetsa nʼcholinga chakuti ndikukwezeni pamene ndinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu mwaulere?

Ngakhale ife kapena mngelo wochokera kumwamba, akalalikira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene tinakulalikirani uja, iyeyo akhale wotembereredwa! Monga tanena kale, tsopano ndikubwereza kunenanso kuti, “Ngati wina aliyense akulalikirani Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene munawulandira, iyeyo akhale wotembereredwa.”

Kodi tsopano ndikufuna kukopa anthu kuti andivomereze, kapena Mulungu? Kapena ndikufuna kukondweretsa anthu? Ngati ine ndikanakhala kuti ndikufunabe kukondweretsa anthu, sindikanakhala mtumiki wa Khristu. Abale, ine ndikufuna kuti mudziwe, kuti Uthenga Wabwino umene ndinalalikira si ochokera kwa munthu ayi.

Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa. Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha.

Iye anabwera ndipo analalikira mtendere kwa inu amene munali kutali ndi mtendere ndiponso kwa iwonso amene anali pafupi.

Iye ndiye amene anapereka mphatso kwa ena kuti akhale atumwi ndi ena aneneri, ena alaliki, ndi ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yawo ndi kukonza oyera mtima kuti agwire ntchito ya utumiki kuti thupi la Khristu lilimbikitsidwe. Izi zidzatifikitsa tonse ku umodzi wachikhulupiriro, kumudziwa Mwana wa Mulungu, kukhwima msinkhu ndi kufika pa muyeso wangwiro weniweni wopezeka mwa Khristu. Motero sitidzakhalanso makanda, ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso ndi kuchenjera kwa anthu achinyengo amene amasocheretsa anthu ndi kuchenjera kwawo.

Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu.

Mundipempherere inenso, kuti nthawi iliyonse pamene nditsekula pakamwa panga, andipatse mawu kuti ndiwulule zinsinsi za Uthenga Wabwino mopanda mantha. Ndine kazembe wa Uthenga Wabwinowu ngakhale ndili womangidwa mʼndende. Pempherani kuti ndilalikire mopanda mantha, monga ndiyenera.

Moti chifukwa cha maunyolo angawa, abale ambiri alimbikitsidwa kuyankhula Mawu a Mulungu molimbika ndi mopanda mantha. Nʼzoonadi kuti ena amalalikira Khristu chifukwa cha kaduka ndi mikangano, koma ena chifukwa cha zolinga zabwino. Olalikira ndi zolinga zabwinowa amachita izi mwachikondi, podziwa kuti ine ndili muno chifukwa cha kuteteza Uthenga Wabwino. Ena aja amalalikira Khristu modzikonda osati moona mtima namaganiza kuti kutero kubweretsa mavuto pamene ndili mʼmaunyolo. Nanga kodi zimenezo zili ndi ntchito? Chofunika ndi chakuti Khristu alalikidwe, kaya ndi mwachinyengo kapena moona. Ndipo ndikukondwera chifukwa cha chimenechi. Ndithu, ndidzapitirira kukondwera,

ngati mupitirirabe kukhala mʼchikhulupiriro chanu, okhazikika ndi olimba, osasunthidwa kuchoka pa chiyembekezo chimene munachigwira mu Uthenga Wabwino. Uwu ndi Uthenga Wabwino umene munawumva, umene wakhala ukulalikidwa kwa olengedwa onse a pansi pa thambo, ndi umenenso, ine Paulo ndinakhala mtumiki wake. Tsopano ine ndikukondwa kuti ndinavutika chifukwa cha inu, ndipo ndikukwaniritsa mʼthupi langa zimene zikuperewera pa masautso a Khristu, chifukwa cha thupi lake, limene ndi Mpingo. Ine ndakhala mtumiki wake mwa lamulo limene Mulungu anandipatsa kuti ndipereke Mawu a Mulungu athunthu, chinsinsi chimene chakhala chikubisika kwa nthawi ndi mibado, koma tsopano chawululidwa kwa oyera mtima. Kwa iwo amene Mulungu anawasankha kuti awadziwitse pakati pa a mitundu ina, ulemerero wa chuma cha chinsinsi ichi, amene ndi Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero. Ife tikulalikira Khristu, kulangiza ndi kuphunzitsa aliyense mwa nzeru zonse kuti timupereke aliyense wangwiro mwa Khristu.

Inu mukudziwa kuti mudzalandira mphotho monga cholowa kuchokera kwa Ambuye. Ndi Ambuye Khristu amene mukumutumikira.

Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende. Pempherani kuti ndilalikire momveka bwino, monga ndikuyenera. Mayendedwe anu pakati pa akunja, akhale anzeru ndipo mugwiritse ntchito mpata uliwonse umene muli nawo. Mayankhulidwe anu nthawi zonse akhale odzaza ndi chisomo ndi okoma, kuti mudziwe kuyankha aliyense.

chifukwa uthenga wathu wabwino sunafike kwa inu ndi mawu okha, koma ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndi chitsimikizo chachikulu. Mukudziwa mmene tinkakhalira pakati panu kuti tikuthandizeni. Inu mwakhala otitsatira athu ndi a Ambuye; ngakhale kuti panali masautso akulu, munalandira uthenga mwachimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera.

Monga mukudziwa, ife nʼkuti titazunzika ndi kunyozedwa ku Filipi. Koma mothandizidwa ndi Mulungu wathu, tinalimba mtima mpaka kukulalikirani uthenga wake wabwino ngakhale ambiri ankatsutsana nafe. Pakuti kulalikira kumene tikuchita, sitikuchita ndi maganizo olakwika kapena zolinga zoyipa, kapenanso kufuna kukunamizani. Koma timayankhula monga anthu ovomerezeka ndi Mulungu ndi osungitsidwa Uthenga Wabwino. Ife sitikufuna kukondweretsa anthu koma Mulungu, amene amasanthula mitima yathu. Monga mukudziwa kuti sitinagwiritse ntchito mawu oshashalika kapena mtima wofuna phindu, Mulungu ndiye mboni yathu. Ife sitinafune kutamidwa ndi anthu, kapena ndi inu, kapena wina aliyense mwa inu. Ngati atumwi a Khristu tikanatha kukhala cholemetsa kwa inu, mʼmalo mwake tinali ngati ana aangʼono pakati panu. Monga mmene amayi amasamalira ana awo angʼono, moteronso tinakusamalirani. Chifukwa tinakukondani kwambiri, tinali okondwa kugawana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso miyoyo yathu. Abale, pakuti mukumbukira kugwira ntchito kwathu kwambiri ndi kuvutika; ife tinagwira ntchito usana ndi usiku ndi cholinga chakuti tisakhale cholemetsa, kwa aliyense pamene ife tinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu.

pa tsiku limene iye adzabwera kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ndi kuyamikidwa ndi onse amene anakhulupirira. Inu mudzakhala nawo mʼgulumo chifukwa munakhulupirira umboni wathu.

Iye anakuyitanirani zimenezi kudzera mwa uthenga wathu wabwino, kuti mulandire nawo ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu. Kotero tsono, abale, imani mwamphamvu ndi kugwiritsa ziphunzitso zimene tinakupatsani kudzera mʼmawu apakamwa kapena kudzera mʼkalata.

Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuyitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa mboni zambiri.

Choncho usachite manyazi kuchitira umboni Ambuye athu, kapena kuchita manyazi chifukwa cha ine wamʼndende. Koma umve nane zowawa chifukwa cha Uthenga Wabwino, mothandizidwa ndi mphamvu za Mulungu. Iye anatipulumutsa ndipo anatiyitanira ku moyo oyera mtima, osati chifukwa cha chilichonse chimene tinachita, koma chifukwa cha chikonzero ndi chisomo chake. Chisomo chimenechi anatipatsa ife mwa Khristu Yesu nthawi isanayambe. Koma tsopano Mulungu watiwululira kudzera mʼkuoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu, amene anathetsa mphamvu za imfa ndipo mwa Uthenga Wabwino anaonetsa poyera moyo umene sungafe. Ine ndinasankhidwa kukhala wamthenga, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wa Uthenga Wabwinowu. Nʼchifukwa chake ndikuvutika monga ndililimu. Komabe zimenezi sizikundichititsa manyazi, popeza ndikumudziwa amene ndamukhulupirira ndipo ndikutsimikiza mtima kuti akhoza kusamalira chimene ndinamusungitsa mpaka tsiku lijalo.

Ndipo zinthu zimene unamva ine ndikuziyankhula pamaso pa mboni zambiri, uziphunzitse kwa anthu odalirika amene akaphunzitsenso ena.

Choncho ndikupirira chilichonse chifukwa cha osankhidwa, kuti nawonso apulumutsidwe ndi Khristu Yesu ndi kulandira ulemerero wosatha. Mawu oyenera kuwadalira ndi awa: Ngati ife tinafa naye pamodzi, tidzakhalanso moyo pamodzi naye. Ngati tinapirira, tidzalamuliranso naye pamodzi. Ngati ife timukana, Iye adzatikananso.

Uziwakumbutsa anthu a Mulungu zinthu izi. Uwachenjeze pamaso pa Mulungu kuti asamakangane pa za mawu. Zimenezi nʼzopanda phindu ndipo zimangowononga amene akumvawo. Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola. Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, chifukwa anthu oyankhula zotere amanka napotokerapotokera.

Lalikira Mawu; khala wokonzeka pa nthawi yake, ngakhale pamene si pa nthawi yake. Konza zolakwa zawo, dzudzula ndipo limbikitsa moleza mtima kwambiri ndi malangizo osamalitsa. Pakuti idzafika nthawi imene anthu adzakana chiphunzitso choona. Mʼmalo mwake, chifukwa chokhumba kumva zowakomera zokha, adzasonkhanitsa aphunzitsi ambiri omawawuza zimene iwo akufuna kumva. Sadzafuna kumva choona koma adzafuna kumva nthano chabe. Koma iwe, khala tcheru nthawi zonse, pirira mʼzovuta, gwira ntchito ya mlaliki, gwira ntchito zonse za utumiki wako.

Koma Ambuye anayima nane limodzi, ndipo anandipatsa mphamvu, kuti kudzera mwa ine, uthenga ulalikidwe kwambiri, ndikuti anthu a mitundu ina amve. Ndipo ndinalanditsidwa mʼkamwa mwa mkango.

Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chimapulumutsa chaonekera kwa anthu onse.

Ine ndikupemphera kuti mgwirizano wako ndi ife mʼchikhulupiriro ukhale opindulitsa pozamitsa nzeru zako zozindikira zinthu zilizonse zabwino zimene timagawana chifukwa cha Khristu. Mʼbale, chikondi chako chandipatsa chimwemwe chachikulu ndi chilimbikitso, chifukwa umatsitsimutsa mitima ya anthu a Ambuye. Tsopano ngakhale kuti mwa Khristu nditha kulimba mtima ndi kulamulira kuti uchite zimene uyenera kuchita,

Popeza lonjezo lakuti tidzalowe mu mpumulo umene anatilonjeza lilipobe, tiyeni tisamale kuti pasakhale wina aliyense mwa inu wodzalephera kulowamo. Pakuti Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa ife, monganso iwo aja; koma iwo sanapindule nawo uthengawo chifukwa anangomva koma osakhulupirira. Tsono ife amene takhulupirira talowa mu mpumulo, monga momwe Mulungu akunenera kuti, “Ndili wokwiya ndinalumbira kuti, ‘Iwo sadzalowa konse mu mpumulo wanga.’ ” Ananena zimenezi ngakhale anali atatsiriza kale ntchito yolenga dziko lapansi.

Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima. Palibe kanthu kobisika pamaso pa Mulungu. Zinthu zonse zili poyera ndi zovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.

Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu.

Ndipo popanda chikhulupiriro nʼkosatheka kukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene amabwera kwa Iye ayenera kukhulupirira kuti Mulungu alipodi ndi kuti Iye amapereka mphotho kwa amene akumufunitsitsa.

Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa.

Ngati wina amadziyesa ngati ndi wachipembedzo, koma chonsecho saletsa lilime lake, amadzinyenga yekha ndipo chipembedzo chakecho ndi cha chabechabe.

Abale anga, ngati mmodzi wa inu apatuka pa choonadi ndipo wina wake ndi kumubweza, kumbukirani izi: Aliyense wobweza wochimwa kuchoka ku cholakwa chake, adzamupulumutsa ku imfa ndi kukwirira machimo ambiri.

Mulungu anawawululira kuti ntchito yawoyo sankayigwira chifukwa cha iwo eni, koma chifukwa inu, pamene iwo ankayankhula zinthu zimene mwamva tsopano kuchokera kwa amene amalalikira Uthenga Wabwino mwamphamvu ya Mzimu Woyera wotumidwa kuchokera kumwamba. Ngakhale angelo amalakalaka kuona nawo zinthuzi.

Popeza mwabadwanso, osati ndi mbewu imene imawonongeka, koma imene siwonongeka, ndiye kuti ndi Mawu a Mulungu amoyo ndi okhalitsa. Pakuti, “Anthu onse ali ngati udzu, ndipo ulemerero wawo uli ngati duwa la kuthengo. Udzu umafota ndipo duwa limathothoka, koma mawu a Ambuye adzakhala mpaka muyaya.” Ndipo awa ndi mawu amene tinalalikira kwa inu.

Monga makanda obadwa kumene amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wauzimu, kuti mukule ndi kukufikitsani ku chipulumutso chanu, pakuti tsopano mwalawadi kuti Ambuye ndi wabwino.

Tsono kwa inu okhulupirira, mwalawo ndi wamtengowapatali. Koma kwa amene sakhulupirira, “Mwala umene amisiri anawukana wasanduka mwala wa maziko, ndi “Mwala wopunthwitsa anthu ndiponso thanthwe limene limagwetsa anthu.” Iwo amapunthwa chifukwa samvera uthenga, pakuti ichi ndiye chinali chifuniro cha Mulungu pa iwo.

Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.

Koma lemekezani Khristu mʼmitima mwanu ngati Ambuye wanu. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene akufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho. Koma chitani zimenezi mofatsa ndi mwaulemu, mukhale ndi chikumbumtima chosakutsutsani, kuti anthu ena akanena zoyipa za makhalidwe anu abwino mwa Khristu, achite okha manyazi ndi chipongwe chawocho.

Ife sitinatsate nkhani zongopeka titakuwuzani za mphamvu zake ndi zakubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu, koma tinaona ndi maso athu za ukulu wake.

Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape.

Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse.

Aliyense amene ndi mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza mbewu ya Mulungu ili mwa iye, sangathe kuchimwa, chifukwa ndi mwana wa Mulungu. Mmenemu ndi mmene timadziwira ana a Mulungu ndi amene ali ana a mdierekezi. Aliyense amene sachita chilungamo si mwana wa Mulungu; ngakhalenso amene sakonda mʼbale wake.

Ife ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo aliyense amene amadziwa Mulungu amamvera zimene timayankhula. Koma aliyense amene sachokera kwa Mulungu samvera zimene timayankhula. Mmenemu ndiye mmene timasiyanitsira pakati pa mzimu wachoonadi ndi Mzimu wachinyengo.

Timalandira umboni wa anthu, koma umboni wa Mulungu ndi wopambana. Umboniwo ndi umene anachitira Mwana wake. Aliyense amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu ali nawo umboniwu mu mtima mwake, koma aliyense amene sanakhulupirire Mulungu amayesa kuti Mulunguyo ndi wonama, chifukwa sanakhulupirire umboni umene Mulungu anachitira wa Mwana wake. Ndipo umboniwo ndi uwu: Mulungu anatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowu uli mwa Mwana wake.

amene akuchitira umboni chilichonse chimene anachiona. Awa ndi Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu Khristu.

Taonani ndayima pa khomo ndikugogoda. Ngati wina amva mawu anga natsekula chitseko, Ine ndidzalowamo ndi kudya naye, Ine ndi iyeyo.

Ndipo ankafuwula mokweza kuti: “Chipulumutso chimachokera kwa Mulungu wathu, wokhala pa mpando waufumu ndi kwa Mwana Wankhosa.”

Ndipo ndidzapereka mphamvu kwa mboni zanga ziwiri, zitavala ziguduli, ndipo kwa masiku 1,260 zidzakhala zikulalikira.” Mboni ziwirizo ndi mitengo iwiri ya olivi ndi zoyikapo nyale ziwiri zija zimene zili pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi. Ngati wina atafuna kuzipweteka mbonizo, moto umatuluka mʼkamwa mwawo ndikuwononga adani awo. Mbonizo zili ndi mphamvu yomanga mvula kuti isagwe pa nthawi imene akulalikirayo; ndipo zili ndi mphamvu yosanduliza madzi kukhala magazi ndi yokantha dziko lapansi ndi miliri ya mitundumitundu nthawi iliyonse imene zingafune.

Tsono zikadzatsiriza umboni wawowo, chirombo chotuluka mʼChidzenje chakuya chija chidzachita nawo nkhondo nʼkuzigonjetsa mpaka kuzipha. Mitembo yawo idzakhala ili gone pabwalo la mu mzinda waukulu umene mozimbayitsa umatchedwa Sodomu ndi Igupto, kumenenso Ambuye wawo anapachikidwako. Kwa masiku atatu ndi theka, anthu ochokera ku mtundu uliwonse, fuko lililonse, chiyankhulo chilichonse ndi dziko lililonse, azidzayangʼanitsitsa mitembo yawoyo koma adzakana kuyikwirira. Anthu okhala pa dziko lapansi adzasangalala nazo zimenezi. Adzachita chikondwerero ndi kutumizirana mphatso, chifukwa aneneri awiri amenewa ankasautsa anthu okhala pa dziko lapansi. Koma patapita masiku atatu ndi theka aja, mpweya wopatsa moyo wochoka kwa Mulungu unalowa mwa aneneriwo, ndipo anayimirira, ndipo amene anawaona anachita mantha aakulu.

Abale athuwo anamugonjetsa ndi magazi a Mwana Wankhosa ndiponso mawu a umboni wawo. Iwo anadzipereka kwathunthu, moti sanakonde miyoyo yawo.

Pamenepo chinjokacho chinamupsera mtima mayiyo ndipo chinachoka kupita kukachita nkhondo ndi ana ena onse a mayiyo, ndiye kuti anthu amene anasunga malamulo a Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu. Kenaka ndinaona chinjokacho chitayima mʼmbali mwa nyanja.

Iwo sananenepo bodza ndipo alibe cholakwa.

Zitatha izi, ndinamva chimene chinamveka ngati phokoso la gulu lalikulu mmwamba likufuwula kuti, “Haleluya! Chipulumutso ndi ulemerero ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu,

Kenaka mngelo anandiwuza kuti, “Lemba kuti, Odala amene ayitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwana Wankhosa.” Ndipo anatinso, “Awa ndiwo mawu woona a Mulungu.” Pamenepo ndinadzigwetsa pa mapazi ake kumupembedza. Koma anandiwuza kuti, “Usatero ayi, ine ndine mtumiki mnzako ngati iwe yemwe, ndiponso ngati abale ako amene asunga umboni wa Yesu. Pembedza Mulungu. Pakuti umboni wa Yesu ndiye mzimu wa uneneri.”

Ndinaona mipando yaufumu pamene anakhalapo anthu amene anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndipo ndinaona mizimu ya amene anadulidwa makosi chifukwa cha umboni wa Yesu ndi chifukwa cha Mawu a Mulungu. Iwo sanapembedze nawo chirombo kapena fano lake ndipo sanalembedwe chizindikiro chake pa mphumi zawo kapena pa manja awo. Iwo anakhalanso ndi moyo nalamulira pamodzi ndi Khristu zaka 1,000.

“Taonani, ndikubwera posachedwa! Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense malinga ndi zimene anachita.

Chichewa - Chichewa - NY

NYCCL - Mawu A Mulungu Mu Chichewa Chalero - 2016

This Bible text is from Biblica Open God's Word In Contemporary Chichewa
https://open.bible/bibles/chichewa-biblica-text-bible/
provided by: Biblica Inc, available by Creative Commons CC-BY-SA-4.0,
and this new compilation is shared as www.creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0.
Languages are made available to you by www.ipedge.net