23 – Chikondi

Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Chikondi.

Mavesi atatu ofunika kwambiri

“Koma Ine ndikuwuza inu amene mukundimva: Kondani adani anu, chitirani zabwino amene amakudani. Dalitsani amene amakutembererani, apempherereni amene amakusautsani. Ngati wina akumenyani patsaya limodzi mupatseninso tsaya linalo. Ngati wina akulanda mwinjiro wako, umulole atenge ndi mkanjo omwe.

Anzanga okondedwa, tiyeni tikondane wina ndi mnzake, pakuti chikondi chimachokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi ndi mwana wa Mulungu ndipo amadziwa Mulungu. Aliyense amene alibe chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi. Mmene Mulungu anaonetsera chikondi chake pakati pathu ndi umu: Iye anatumiza Mwana wake mmodzi yekha ku dziko lapansi kuti mwa Iyeyo tikhale ndi moyo. Chikondi ndi ichi: osati kuti ife ndife amene tinamukonda Mulungu, koma kuti Iyeyo ndiye amene anatikonda ndipo anatumiza Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu. Anzanga okondedwa, popeza Mulungu anatikonda chotere, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.

“Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka, ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse.

Mavesi onse motsatira dongosolo lolondola – 326 ndime

Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi.

Choncho Yakobo anagwira ntchito zaka zisanu ndi ziwiri chifukwa cha Rakele. Koma kwa iye zaka zonsezi zinakhala ngati masiku wochepa chifukwa anamukonda Rakele.

“Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

“Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako kapena wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”

“Ngati ukumana ndi ngʼombe kapena bulu wa mdani wako zitasochera, uwonetsetse kuti wazitenga kupita nazo kwa mwini wakeyo. Ngati uwona bulu wa munthu wina amene amakuda atagwa ndi katundu, usamusiye pomwepo, uwonetsetse kuti wamuthandiza.

Ndipo Iye anadutsa kutsogolo kwa Mose akulengeza kuti, “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosapsa mtima msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika,

“ ‘Musamude mʼbale wanu mu mtima mwanu. Koma mudzudzuleni mnzanu moona mtima kuti musakhale wolakwa. “ ‘Musamubwezere mnzanu choyipa kapena kumusungira kanthu kunkhosi, koma konda mnansi wako monga iwe mwini. Ine ndine Yehova.

Mlendo amene akhala nanu akhale ngati mmodzi mwa mbadwa zanu. Mumukonde monga momwe mumadzikondera inu nomwe. Paja inu munali alendo mʼdziko la Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

“ ‘Ngati mʼbale wako akhala wosauka kuti sangathe kudzisamalira yekha, umuthandize. Ukhale naye ngati mlendo kapena ngati munthu amene ukhala naye kwa kanthawi. Usalandire chiwongoladzanja chilichonse kuchokera kwa iye kapena kuwonjezerapo kanthu kena, koma uziopa Mulungu kuti mʼbale wakoyo akhale nawe. Musakongoze mnzanu ndalama kuti mulandire chiwongoladzanja, kapena kumugulitsa chakudya kuti mupeze phindu.

(Koma Mose anali munthu wodzichepetsa kwambiri kuposa munthu aliyense pa dziko lapansi).

Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse.

Choncho dziwani kuti Yehova Mulungu wanu, ndi Mulungu. Iye ndi Mulungu wokhulupirika, wosunga pangano lake la chikondi chosasinthika ku mibadomibado, kwa iwo amene amamukonda nasunga malamulo ake. Koma iwo amene amamuda adzawabwezera powawononga pamaso pawo; sadzachedwa kuwabwezera iwo amene amadana naye.

Iye amatchinjiriza ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo amakonda mlendo namupatsa chakudya ndi chovala. Muzikonda alendo popeza inuyo munali alendo mʼdziko la Igupto.

Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndipo nthawi zonse muzitsata zimene Iyeyo anakulamulani, malangizo, zikhazikitso ndi malamulo ake.

Choncho mukasunga mokhulupirika malamulo amene ndikukupatsani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iyeyo ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,

musamumvere mneneriyo kapena wolotayo. Yehova Mulungu wanu afuna akuyeseni kuti aone ngati mumamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

Mumupatse iye mowolowamanja ndipo muchite zimenezi mosasungira kanthu kumtima. Tsono chifukwa cha zimenezi, Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse ndi pa chilichonse chimene mukhudza. Anthu osauka sadzatha mʼdziko lanu. Chomwecho ndikukulamulani kuti mukhale ofewa manja kwa abale anu ndi kwa osauka, osowa mʼdziko mwanu.

Aliyense wa inu adzabweretse mphatso molingana ndi momwe Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani.

Yehova Mulungu wanu adzasintha mitima yanu pamodzi ndi mitima ya zidzukulu zanu, kotero kuti mudzamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, ndipo mudzakhala ndi moyo.

Ndi kuti mukonde Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kukhulupirika kwa Iye. Pakuti Yehova ndiye moyo wanu, ndipo mudzakhala zaka zambiri mʼdziko limene analumbira kulipereka kwa makolo anu, Abrahamu, Isake ndi Yakobo.

Koma samalitsani kuti mumvere malamulo ndi malangizo amene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani: kukonda Yehova Mulungu wanu, kuchita zimene iye amafuna, kumvera malamulo ake, kukhala okhulupirika kwa Iye ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.”

“Musandiyankhulenso modzitama, pakamwa panu pasatuluke zonyada, pakuti Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo ndiye amene amayesa ntchito za anthu onse.

Davide atatha kuyankhula ndi Sauli, mtima wa Yonatani unagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo iye ankamukonda Davide monga momwe ankadzikondera yekha. Choncho Sauli anamusunga Davideyo kuyambira tsiku limenelo ndipo sanamulole kuti abwerere ku nyumba ya abambo ake. Ndipo Yonatani anapanga pangano ndi Davide chifukwa ankamukonda monga momwe ankadzikondera. Yonatani anavula mkanjo umene anavala ndipo anamupatsa Davide pamodzi ndi zovala za nkhondo, lupanga, uta ndi lamba.

Mnyamatayo anapita. Kenaka Davide anatuluka ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, nadzigwetsa pansi ndi kugunditsa nkhope yake pansi katatu. Anapsompsona nayamba kulira onse awiri, koma Davide analira kwambiri. Yonatani anawuza Davide kuti, “Pita mu mtendere pakuti ife awiri tinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, ‘Yehova ndiye akhale mboni pakati pa iwe ndi ine ndiponso pakati pa zidzukulu zako ndi zidzukulu zanga kwa nthawi yonse.’ ” Kenaka Davide anachoka, ndipo Yonatani anabwerera ku mzinda kuja.

“Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka, ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse.

Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu, pakuti ndi zakalekale. Musakumbukire machimo a ubwana wanga ndi makhalidwe anga owukira; molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine, pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.

Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama ndipo amawaphunzitsa njira zake.

Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake.

Kondani Yehova oyera mtima ake onse! Yehova amasunga wokhulupirika koma amalanga kwathunthu anthu odzikuza.

Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba, kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo. Chilungamo chanu Mulungu chili ngati mapiri aakulu, chiweruzo chanu chili ngati kuzama kwakukulu. Yehova mumasunga munthu pamodzi ndi chinyama. Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali! Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthu amapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu.

Musandichotsere chifundo chanu Yehova; chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso. Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake; Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake. Yehova adzamuthandiza pamene akudwala ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pamene Mneneri Natani anabwera kwa iye atachita chigololo ndi Batiseba. Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, molingana ndi chikondi chanu chosasinthika; molingana ndi chifundo chanu chachikulu mufafanize mphulupulu zanga.

Ndiyankheni Inu Yehova mwa ubwino wanu wa chikondi chanu; mwa chifundo chanu chachikulu tembenukirani kwa ine.

Inu Ambuye, ndinu wokhululuka ndi wabwino, wodzaza ndi chikondi kwa onse amene amayitana Inu.

Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.

Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri ameneyo ndidzamuletsa; aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza, ameneyo sindidzamulekerera.

Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka. Iye sadzatsutsa nthawi zonse, kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya; satichitira molingana ndi machimo athu, kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu. Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa; monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo, koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.

Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa, ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo;

Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake ndi chosatha.

Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha ndi chifukwa cha machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse, pakuti Iye wapha ludzu la munthu womva ludzu ndipo wakhutitsa wanjala ndi zinthu zabwino.

Pakuti chikondi chake pa ife ndi chachikulu, ndipo kukhulupirika kwa Yehova nʼkosatha. Tamandani Yehova.

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Onani, nʼkokoma ndi kokondweretsa ndithu pamene abale akhala pamodzi mwachiyanjano!

Yamikani Mulungu wakumwamba, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.

Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika. Yehova ndi wabwino kwa onse; amachitira chifundo zonse zimene anazipanga.

Yehova amagwiriziza anthu odzichepetsa, koma amagwetsa pansi anthu oyipa.

Makhalidwe ochitira ena chifundo ndi owonetsa kukhulupirika asakuchokere. Uwamangirire mʼkhosi mwako ngati mkanda ndi kuwalemba pa mtima pako.

Imwa madzi a mʼchitsime chakochako, madzi abwino ochokera mʼchitsime chako. Kodi akasupe ako azingosefukira mʼmisewu? Kodi mitsinje yako izingoyendayenda mʼzipata za mzinda? Mitsinjeyo ikhale ya iwe wekha, osati uyigawireko alendo. Yehova adalitse kasupe wako, ndipo usangalale ndi mkazi wa unyamata wako. Iye uja ali ngati mbalale yayikazi yokongola ndiponso ngati gwape wa maonekedwe abwino. Ukhutitsidwe ndi mawere ake nthawi zonse, ndipo utengeke ndi chikondi chake nthawi zonse. Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukukopeka ndi mkazi wachigololo? Bwanji ukukumbatira mkazi wachilendo?

Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo, zinthu zisanu ndi ziwiri zimene zimamunyansa: maso onyada, pakamwa pabodza, manja akupha munthu wosalakwa, mtima wokonzekera kuchita zoyipa, mapazi othamangira msanga ku zoyipa, mboni yonama yoyankhula mabodza komanso munthu amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.

Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa. Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama, kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.

Ndimakonda amene amandikonda, ndipo amene amandifunafuna amandipeza.

Udani umawutsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.

Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi, koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.

Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino koma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto.

Munthu wina amapatsako anzake zinthu mwaufulu nʼkumangolemererabe; wina amamana chomwe akanatha kupereka, koma kumanka nasawukabe. Munthu wopereka mowolowamanja adzalemera; iye amene amathandiza ena iyenso adzathandizidwa.

Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti amamuda, koma wokonda mwana wake sazengereza kumulanga.

Wonyoza mnansi wake ndi wochimwa koma ndi wodala amene amachitira chifundo anthu osowa.

Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake, koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu.

Kuyankha kofatsa kumathetsa mkwiyo, koma mawu ozaza amautsa ukali.

Yehova amapasula nyumba ya munthu wonyada koma amasamalira malo a mkazi wamasiye.

Munthu aliyense wodzikuza amamunyansa Yehova. Koma dziwani izi: Iwo sadzakhala osalangidwa. Chifukwa cha chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake; chifukwa cha kuopa Yehova munthu amapewa zoyipa.

Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wodzikuza adzagwa. Nʼkwabwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu oponderezedwa, kusiyana ndi kugawana zolanda ndi anthu onyada.

Mawu okometsera ali ngati chisa cha njuchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.

Iye amene amakhululukira zolakwa za wina, amafunitsitsa chikondi; wobwerezabwereza nkhani amapha chibwenzi.

Bwenzi lako limakukonda nthawi zonse, ndipo mʼbale wako anabadwa kuti azikuthandiza pamavuto.

Mawu ako angathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo. Wokonda kuyankhulayankhula adzadya zipatso zake.

Pali abwenzi amene chibwenzi chawo nʼchapamaso, koma pali bwenzi limene limakukangamira kuposa mʼbale wako.

Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.

Chimene munthu amafuna ndi chikondi chosatha; nʼkwabwino kukhala wosauka kusiyana ndi kukhala wabodza.

Za chilungamo ndi zolondola ndi zomwe zimakondweretsa Yehova kuposa kupereka nsembe. Maso odzikuza ndi mtima wonyada, zimatsogolera anthu oyipa ngati nyale nʼchifukwa chake amachimwa.

Amene atsekera mʼkhutu mwake wosauka akamalira, nayenso adzalira koma palibe adzamuyankhe.

Amene amatsata chilungamo ndi kukhulupirika, amapeza moyo ndi ulemerero.

Amene amagwira pakamwa pake ndi lilime lake sapeza mavuto. Munthu wonyada ndi wodzikuza amamutcha, “Mnyodoli,” iye amachita zinthu modzitama kwambiri.

Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsika, pakuti iye amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.

Chotsani munthu wonyoza, ndipo kukangana kudzatha; mapokoso ndi zonyoza zidzaleka. Amene amakonda kukhala woyera mtima ndi kumayankhula mawu abwino, adzakhala bwenzi la mfumu.

Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya kuti adye; ngati ali ndi ludzu mupatse madzi kuti amwe. Pochita izi, udzamusenzetsa makala a moto pa mutu pake, ndipo Yehova adzakupatsa mphotho.

Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu, koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri.

Munthu wamkwiyo amayambitsa mikangano, ndipo munthu waukali amachita zolakwa zambiri.

Kunyada kwa munthu kudzamutsitsa, koma munthu wodzichepetsa amalandira ulemu.

Pali zinthu zitatu zimene zimandidabwitsa, zinthu zinayi zimene ine sindizimvetsetsa. Ndipo ndi izi: mmene chiwulukira chiwombankhanga mlengalenga; mmene iyendera njoka pa thanthwe; mmene chiyendera chombo pa nyanja; ndiponso mmene mwamuna achitira akakhala ndi namwali.

Yankhula mʼmalo mwa amene sangathe kudziyankhulira okha. Uwayankhulire anthu onse osiyidwa pa zonse zowayenera. Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uwateteze amphawi ndi osauka.

Usamafulumire kukwiya mu mtima mwako, pakuti mkwiyo ndi bwenzi la zitsiru.

Nyimbo ya Solomoni, nyimbo yoposa nyimbo zonse. Undipsompsone ndi milomo yako chifukwa chikondi chako nʼchokoma kuposa vinyo. Mafuta ako odzola ndi onunkhira bwino; dzina lako lili ngati mafuta onunkhira otsanulidwa. Nʼchifukwa chake atsikana amakukonda! Nditenge ndipo ndizikutsata, tiye tifulumire! Mfumu indilowetse mʼchipinda chake. Ife timasangalala ndi kukondwera nawe, tidzatamanda chikondi chako kupambana vinyo. Amachita bwinotu potamanda iwe!

Iwe bwenzi langa, uli ngati kavalo wamkazi ku magaleta a Farao. Masaya ako ndi okongola ndi ndolo zamʼmakutuzo, khosi lako likukongola ndi mikanda yamiyala yamtengowapatali. Tidzakupangira ndolo zagolide zokongoletsedwa ndi mikanda yasiliva. Pamene mfumu inali pa malo ake odyera, mafuta anga onunkhira anamveka fungo lake. Wokondedwa wanga ali ngati kathumba ka mure kwa ine, kamene kamakhala pakati pa mawere angawa. Wokondedwa wanga ali ngati mpukutu wa maluwa ofiira, ochokera ku minda ya mpesa ya ku Eni-Gedi. Iwe wokondedwa wanga, ndiwe wokongoladi! Ndithu, ndiwe chiphadzuwa, maso ako ali ngati nkhunda. Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongoladi! Ndithu, ndiwe wokongoladi kwambiri! Ndipo malo athu ogonapo ndi msipu wobiriwira.

Ine ndine duwa la ku Saroni, duwa lokongola la ku zigwa. Monga duwa lokongola pakati pa minga ndi momwe alili wokondedwa wanga pakati pa atsikana. Monga mtengo wa apulosi pakati pa mitengo ya mʼnkhalango ndi momwe alili bwenzi langa pakati pa anyamata. Ndimakondwera kukhala pansi pa mthunzi wako, ndipo chipatso chake ndi chokoma mʼkamwa mwanga. Iye wanditengera ku nyumba yaphwando, ndipo mbendera yake yozika pa ine ndi chikondi. Undidyetse keke ya mphesa zowuma, unditsitsimutse ndi ma apulosi, pakuti chikondi chandifowoketsa. Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere, ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira. Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo: Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Tamverani bwenzi langa! Taonani! Uyu akubwera apayu, akulumphalumpha pa mapiri, akujowajowa pa zitunda. Bwenzi langa ali ngati gwape kapena mwana wa mbawala. Taonani! Uyo wayima kuseri kwa khoma lathulo, akusuzumira mʼmazenera, akuyangʼana pa mpata wa zenera.

Bwenzi langa anayankha ndipo anati kwa ine, “Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga, ndipo tiye tizipita. Ona, nyengo yozizira yatha; mvula yatha ndipo yapitiratu. Maluwa ayamba kuoneka pa dziko lapansi; nthawi yoyimba yafika, kulira kwa njiwa kukumveka mʼdziko lathu. Mtengo wankhuyu ukubereka zipatso zake zoyambirira; mitengo ya mpesa ya maluwa ikutulutsa fungo lake. Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga tiye tizipita.” Nkhunda yanga yokhala mʼmingʼalu ya thanthwe, mʼmalo obisala a mʼmbali mwa phiri, onetsa nkhope yako, nʼtamvako liwu lako; pakuti liwu lako ndi lokoma, ndipo nkhope yako ndi yokongola. Mutigwirire nkhandwe, nkhandwe zingʼonozingʼono zimene zikuwononga minda ya mpesa, minda yathu ya mpesa imene yayamba maluwa. Bwenzi langa ndi wangadi ndipo ine ndine wake; amadyetsa gulu lake la ziweto pakati pa maluwa okongola. Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira ndipo mithunzi ikayamba kuthawa, unyamuke bwenzi langa, ndipo ukhale ngati gwape kapena ngati mwana wa mbawala pakati pa mapiri azigwembezigwembe.

Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo: Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Kodi ndani amene akubwera kuchokera ku chipululu ngati utsi watolotolo, wonunkhira mure ndi lubani, zopangidwa kuchokera ku zonunkhira zonse za anthu amalonda?

Ndiwe wokongoladi wokondedwa wanga! Ndithudi, ndiwe wokongola! Maso ako ali ngati nkhunda kumbuyo kwa nsalu yophimba kumutu. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi. Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zomwe zangometedwa kumene, zochokera kozisambitsa kumene. Iliyonse ili ndi ana amapasa; palibe imene ili yokha. Milomo yako ili ngati mbota yofiira; pakamwa pako ndi pokongola kwambiri. Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba kumutuyo, masaya ako akuoneka ngati mabandu a makangadza. Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide, yomangidwa bwino ndi yosalala; pa nsanja imeneyo pali zishango 1,000, zishango zonsezo za anthu ankhondo. Mawere ako ali ngati tiana tiwiri ta nswala, ngati ana amapasa a nswala amene akudya pakati pa maluwa okongola. Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira ndipo mithunzi ikayamba kuthawa, ndidzapita ku phiri la mure ndi ku chitunda cha lubani. Ndiwe wokongola kwambiri wokondedwa wanga; palibe chilema pa iwe.

Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, wanditenga mtima, iwe wanditenga mtima ndi kapenyedwe ka maso ako, ndiponso ndi umodzi mwa mikanda ya mʼkhosi mwako. Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, chikondi chako nʼchosangalatsa! Chikondi chako nʼchosangalatsa kwambiri kupambana vinyo, ndiponso fungo la mafuta ako ndi lopambana zonunkhiritsa zonse! Iwe mkwatibwi wanga, milomo yako ikuchucha uchi ngati chisa cha njuchi; pansi pa lilime lako pali mkaka ndi uchi. Fungo lonunkhira la zovala zako likumveka ngati fungo la ku Lebanoni. Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, ndiwe munda wopiringidzidwa; ndiwe kasupe wotchingidwa, chitsime chotetezedwa. Zomera zako ndi munda wa zipatso za makangadza; muli zipatso zokoma kwambiri, muli hena ndi nadi, nadi ndi safiro, kalamusi ndi sinamoni, komanso mtengo uliwonse wonunkhira bwino. Mulinso mure ndi aloe ndi zonunkhiritsa zonse zabwino kwambiri. Iwe ndiwe kasupe wa mʼmunda, chitsime cha madzi oyenda, mtsinje wa madzi ochokera ku Lebanoni. Dzuka, iwe mphepo yakumpoto, ndipo bwera, iwe mphepo yakummwera! Uzira pa munda wanga, kuti fungo lake lonunkhira lifalikire ponseponse. Bwenzi langa alowe mʼmunda mwake ndi kudya zipatso zake zabwino kwambiri.

Ndalowa mʼmunda mwanga, iwe mlongo wanga, iwe mkwatibwi wanga; ndasonkhanitsa mure wanga ndi zokometsera zakudya zanga. Ndadya uchi wanga pamodzi ndi zisa zake zomwe; ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga. Idyani abwenzi anga, imwani; Inu okondana, imwani kwambiri. Ndinagona tulo koma mtima wanga unali maso. Tamverani, bwenzi langa akugogoda: “Nditsekulire, mlongo wanga, bwenzi langa, nkhunda yanga, wangwiro wanga. Mutu wanga wanyowa ndi mame, tsitsi langa lanyowa chifukwa cha nkhungu ya usiku.” Ndavula kale zovala zanga, kodi ndizivalenso? Ndasamba kale mapazi anga kodi ndiwadetsenso? Bwenzi langa anapisa dzanja lake pa chibowo cha pa chitseko; mtima wanga unagunda chifukwa cha iye.

Inu akazi a ku Yerusalemu ndithu ndikukupemphani, mukapeza wokondedwa wangayo, kodi mudzamuwuza chiyani? Muwuzeni kuti ine ndadwala nacho chikondi. Iwe wokongola kuposa akazi onsewa, kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana wina aliyense bwanji? Kodi wokondedwa wakoyo ndi wopambana ena onse chotani kuti uzichita kutipempha motere?

Wokondedwa wangayo ndi wowala kwambiri ndi wathanzi pakati pa anthu 1,000. Mutu wake ndi golide woyengeka bwino; tsitsi lake ndi lopotanapotana, ndiponso lakuda bwino ngati khwangwala. Maso ake ali ngati nkhunda mʼmbali mwa mitsinje ya madzi, ngati nkhunda zitasamba mu mkaka, zitayima ngati miyala yamtengowapatali. Masaya ake ali ngati timinda ta mbewu zokometsera zakudya zopatsa fungo lokoma. Milomo yake ili ngati maluwa okongola amene akuchucha mure. Manja ake ali ngati ndodo zagolide zokongoletsedwa ndi miyala yamtengowapatali. Thupi lake ndi losalala ngati mnyanga wanjovu woyikamo miyala ya safiro. Miyendo yake ili ngati mizati yamwala, yokhazikika pa maziko a golide. Maonekedwe ake ali ngati Lebanoni, abwino kwambiri ngati mkungudza. Milomo yake ndi yosangalatsa kwambiri; munthuyo ndi wokongola kwambiri! Uyu ndiye wachikondi wanga ndi bwenzi langa, inu akazi a ku Yerusalemu.

Wokondedwa wangayo ndine wake ndipo iyeyo ndi wangawanga; amadyetsa ziweto zake pakati pa maluwa okongola.

Usandipenyetsetse; pakuti maso ako amanditenga mtima. Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.

Iwe namwali waufumu, mapazi ako ngokongola mu nsapato wavalazo! Ntchafu zako nʼzowumbika bwino ngati miyala yamtengowapatali, ntchito ya manja ya mmisiri waluso. Mchombo wako uli ngati chikho chowumbika bwino chimene nthawi zonse ndi chodzaza ndi vinyo. Chiwuno chako ndi choningʼa ngati mtolo wa tirigu utazunguliridwa ndi maluwa okongola. Mawere ako akuoneka ngati ana awiri a mbawala, ngati mphoyo zamapasa. Khosi lako lili see! ngati nsanja ya mnyanga wa njovu. Maso ako ali ngati mayiwe a ku Hesiboni, amene ali pafupi ndi chipata cha Bati Rabimu. Mphuno yako ili ngati nsanja ya ku Lebanoni, yoyangʼana ku Damasiko. Mutu wako uli bwinobwino nengʼaa ngati phiri la Karimeli. Tsitsi lako lili ngati nsalu yakuda yaufumu; mfumu yakopeka ndi maonekedwe ake okongola. Ndiwe wokongola kwambiri ndiponso wosangalatsa, iwe wokondedwa, namwali wokondweretsawe! Msinkhu wako uli ngati mtengo wa mgwalangwa, ndipo mawere ako ali ngati phava la zipatso. Ndinati, “Ndikwera mtengo wa mgwalangwa; ndidzathyola zipatso zake.” Mawere ako ali ngati maphava a mphesa, fungo la mpweya wako lili ngati ma apulosi, ndipo pakamwa pako pali ngati vinyo wokoma kwambiri. Tsono vinyo ameneyu amuthirire wachikondi wanga, ayenderere bwino pa milomo yake ndi mano ake.

Wokondedwayo ine ndine wake, ndipo chilakolako chake chili pa ine. Bwera wachikondi wanga, tiye tipite ku madera a ku midzi, tikagone ku midzi. Tiye tilawirire mmamawa kupita ku minda ya mpesa, tikaone ngati mitengo ya mpesa yayamba kuphukira, ngati maluwa ake ayamba kuoneka, komanso ngati makangadza ayamba kuonetsa maluwa. Kumeneko ndidzakuonetsa chikondi changa. Mitengo ya mankhwala a chisulo ikupereka fungo lake labwino, ndipo pa khomo pathu pali zipatso zonse zokoma, zatsopano ndi zakale zomwe, zimene ndakusungira wokondedwa wanga.

Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.

Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani: musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho. Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo, atatsamira wokondedwa wakeyo? Ndinakudzutsa pa tsinde pa mtengo wa apulosi, pamenepo ndi pamene amayi anachirira, pamenepo ndi pamene wokubereka anamva ululu pokubala iweyo.

Undiyike pamtima pako ngati chidindo, ngati chidindo cha pa dzanja lako; pakuti chikondi nʼchamphamvu ngati imfa, nsanje ndiyaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti lawilawi ngati malawi a moto wamphamvu. Madzi ochuluka sangachizimitse chikondi, mitsinje singachikokolole chikondicho. Ngati wina apereka chuma chonse cha mʼnyumba mwake chifukwa cha chikondi, adzangonyozeka nazo kotheratu.

Kudzikuza kwa anthu kudzatha, ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa; Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu pa tsiku limenelo. Yehova Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku limene adzatsitse onse onyada ndi odzitama, ndipo adzagonjetsa onse amphamvu,

Koma munthu wolemekezeka amalingaliranso kuchita zinthu zabwino, Iye amakhazikika pa zinthu zabwinozo.

Ndinapereka msana wanga kwa ondimenya masaya anga ndinawapereka kwa anthu ondizula ndevu; sindinawabisire nkhope yanga anthu ondinyoza ndi ondilavulira.

Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu, munthu amene moyo wake unali wamasautso, wozolowera zowawa, ndipo anali ngati munthu amene anzake amaphimba nkhope zawo akamuona. Iye ananyozedwa, ndipo ife sitinamuyese kanthu. Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife; ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga, kumukantha ndi kumusautsa. Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu; iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere, ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa. Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera, aliyense mwa ife akungodziyendera; ndipo Yehova wamusenzetsa zoyipa zathu zonse. Anthu anamuzunza ndi kumusautsa, koma sanayankhule kanthu. Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira, kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta, momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.

Anthu anjala kodi mwawagawira chakudya chanu? Osowa ndi ongoyendayenda, kodi mwawapatsa malo ogona? Munthu wausiwa kodi mwamupatsa chovala?

Ndipo ngati mudyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu oponderezedwa, pamenepo kuwala kwanu kudzaonekera mu mdima, ndipo usiku wanu udzakhala ngati usana.

Ndidzafotokoza za kukoma mtima kwa Yehova, ntchito zimene Iye ayenera kutamandidwa. Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha zonse zimene watichitira. Inde, mwa chifundo ndi kukoma mtima kwake Yehova wachitira nyumba ya Israeli zinthu zabwino zambiri.

Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati, “Ine ndakukondani ndi chikondi chopanda malire. Nʼchifukwa chake ndipitiriza kukukondani.

Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu, ndi chifundo chake ndi chosatha. Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse; kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.

Ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga ndi kuvomereza kuti tinachimwa: Ndinati, “Inu Ambuye, Mulungu wamkulu ndi woopsa, amene mumasunga pangano lanu la chikondi kwa onse amene amakukondani ndi kumvera malamulo anu,

Ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya; ndidzakutomera mwachilungamo, mwaungwiro, mwachikondi ndi mwachifundo. Ndidzakutomera mokhulupirika ndipo udzadziwa Yehova.

Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino. Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe? Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.

Funafunani Yehova, inu nonse odzichepetsa a mʼdziko, inu amene mumachita zimene amakulamulani. Funafunani chilungamo, funafunani kudzichepetsa; mwina mudzatetezedwa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.

Yehova Mulungu wako ali pakati pako, ali ndi mphamvu yopulumutsa. Adzakondwera kwambiri mwa iwe, adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake, adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe.”

“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Muziweruza molungama; muzichitirana chifundo ndi kumverana chisoni. Musamazunze akazi amasiye kapena ana amasiye, alendo kapena osauka. Musamaganizirane zoyipa mʼmitima mwanu.’

“Odala ndi amene ali osauka mu mzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo. Odala ndi amene ali achisoni, chifukwa adzatonthozedwa. Odala ndi amene ali ofatsa, chifukwa adzalandira dziko lapansi. Odala ndi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo, chifukwa adzakhutitsidwa. Odala ndi amene ali ndi chifundo, chifukwa adzawachitira chifundo. Odala ndi amene ali oyera mtima, chifukwa adzaona Mulungu. Ndi odala amene amabweretsa mtendere, chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu. Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.” “Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine. Sangalalani, kondwerani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba, chifukwa moterenso ndi mmene anazunzira aneneri inu musanabadwe.

Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wokwiyira mʼbale wake adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene wonena mʼbale wake kuti, ‘Ndiwe wopanda phindu,’ adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu lalikulu. Ndipo aliyense amene anganene mnzake ‘wopandapake’ adzatengeredwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene angamunene mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe,’ adzaponyedwa ku gehena. “Nʼchifukwa chake, pamene ukupereka chopereka chako pa guwa lansembe ndipo nthawi yomweyo ukumbukira kuti mʼbale wako ali nawe chifukwa, usiye choperekacho pa guwa lansembepo, choyamba pita kayanjane ndi mʼbale wako; ukatero bwera kudzapereka chopereka chakocho.

“Munamva kuti, ‘Diso kulipira diso ndi dzino kulipira dzino.’ Koma ndikuwuzani kuti musamukanize munthu woyipa, akakumenya patsaya mupatseni tsaya linalo. Ndipo ngati wina afuna kukuzenga mlandu kuti akulande malaya ako, umupatsenso mkanjo wako. Ngati wina akukakamiza kuti uyende naye mtunda umodzi, iwe uyende naye mitunda iwiri. Wina akakupempha kanthu umupatse, ndipo wofuna kubwereka usamukanize.

“Munamva kuti, ‘Konda mnansi wako ndi kudana ndi mdani wako.’ Koma Ine ndikuwuzani kuti, ‘Kondani adani anu ndi kuwapempherera okuzunzani kuti mukhale ana a Atate anu akumwamba, amene awalitsa dzuwa lake pa oyipa ndi pa abwino, nagwetsa mvula pa olungama ndi pa osalungama.’ Ngati mukonda amene akukondani inu, mudzapeza mphotho yanji? Kodi ngakhale amisonkho sachita chimodzimodzi? Ndipo ngati inu mupatsa moni abale anu okhaokha mukuchita chiyani choposa ena? Kodi ngakhale akunja sachita chimodzimodzi? Nʼchifukwa chake, inu khalani angwiro monga Atate anu akumwamba ali wangwiro.”

“Samalani kuti musachite ntchito zanu zolungama pamaso pa anthu kuti akuoneni. Popeza ngati mutero simudzalandira mphotho yochokera kwa Atate anu akumwamba. “Pamene mupereka zachifundo, musachite modzionetsera monga amachita achiphamaso mʼmasunagoge ndi pa misewu kuti atamidwe ndi anthu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwowo alandiriratu mphotho yawo yonse. Koma pamene mupereka zachifundo, dzanja lanu lamanzere lisadziwe chimene dzanja lanu lamanja likuchita, kotero kuti kupereka kwanu kukhale mwachinsinsi. Ndipo Atate anu amene amaona zochitika mwachinsinsi, adzakupatsani mphotho.

Ngati inu mukhululukira anthu pamene akuchimwirani, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani. Koma ngati inu simukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.

“Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri. Pakuti pena adzamuda mmodzi ndi kukonda winayo kapena adzagwira ntchito mokhulupirika kwa mmodzi, nadzanyoza winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma pa nthawi imodzi.

“Musaweruze ena, kuti inunso mungadzaweruzidwe. Pakuti momwe inu muweruzira ena, inunso mudzaweruzidwa chimodzimodzi, muyeso umene muyesera ena inunso mudzayesedwa ndi womwewo. “Chifukwa chiyani iwe uyangʼana kachitsotso ka mʼdiso la mʼbale wako koma susamalira chimtengo chili mʼdiso mwako? Kodi unganene bwanji kwa mʼbale wako kuti, ‘Ndikuchotse kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene nthawi zonse chimtengo uli nacho mʼdiso mwako? Wachiphamaso iwe! Yamba wachotsa chimtengo chili mʼdiso mwako ndipo pamenepo udzatha kuona bwino ndi kuchotsa kachitsotso kali mʼdiso mwa mʼbale wako.

Nʼchifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu akuchitireni, yambani ndinu kuwachitira, pakuti izi ndi zimene malamulo ndi aneneri amaphunzitsa.

“Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”

Ndipo Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati simusintha ndi kukhala ngati tiana tatingʼono, simudzalowa konse mu ufumu wakumwamba. Chifukwa chake, aliyense amene adzichepetsa yekha ngati kamwana aka, ameneyo ndiye wamkulu koposa onse mu ufumu wakumwamba.

“Kodi mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi nʼkusowa, kodi sasiya 99 zija mʼmapiri ndi kupita kukafuna imodzi yosocherayo? Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti akayipeza amasangalala kwambiri chifukwa cha nkhosa imodziyo kuposa nkhosa 99 zimene sizinasochere. Chimodzimodzinso Atate anu akumwamba safuna kuti mmodzi wa anawa atayike.

“Ngati mʼbale wako akuchimwira, pita kamuwuze cholakwa chake pa awiri. Ngati akumvera, wamubweza mʼbale wakoyo.

Kenaka Petro anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, “Ambuye, kodi mʼbale wanga akandichimwira ndimukhululukire kokwanira kangati? Mpaka kasanu nʼkawiri?” Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuza iwe kuti osati kasanu nʼkawiri, koma ka 70 kuchulukitsa ndi kasanu nʼkawiri.

lemekeza abambo ako ndi amayi ako ndipo konda mnansi wako monga iwe mwini.”

Yesu anayankha kuti, “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndi kupereka kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ukakachita zimenezi, ukabwere udzanditsate Ine.”

“Momwemo omalizira adzakhala oyamba ndipo oyamba adzakhala omalizira.”

Siziyenera kutero ndi inu. Mʼmalo mwake, aliyense amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu akhale wotumikira wanu. Ndipo aliyense amene akufuna kukhala woyamba akhale kapolo wanu. Momwenso Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kukhala dipo la anthu ambiri.”

Yesu anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse. Ili ndi lamulo loyamba ndi loposa onse. Ndipo lachiwiri ndi lofanana nalo: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’

Wamkulu pakati panu adzakhala wokutumikirani. Pakuti aliyense amene adzikuza adzachepetsedwa, ndipo aliyense amene adzichepetsa adzakuzidwa.

“Pamenepo mfumu idzati kwa a ku dzanja lamanja, ‘Bwerani inu odalitsika ndi Atate anga; landirani ufumu umene unakonzedwa chifukwa cha inu kuyambira pachiyambi cha dziko. Pakuti ndinali ndi njala ndipo munandipatsa chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo munandipatsa madzi akumwa, ndinali mlendo ndipo munandilandira, ndinali wausiwa ndipo munandiveka, ndinali wodwala ndipo munandisamalira, ndinali ku ndende ndipo inu munandiyendera.’ “Ndipo olungamawo adzamuyankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala ndipo tinakudyetsani, kapena ludzu ndipo tinakupatsani madzi akumwa? Ndi liti tinakuonani muli mlendo ndipo tinakulandirani, kapena wa usiwa ndipo tinakuvekani? Ndi liti tinakuonani mutadwala kapena ku ndende ndipo tinakuyenderani?’ “Mfumu idzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene munachitira mmodzi wa abale anga onyozekawa munandichitira Ine.’

“Pamenepo adzanena kwa akumanzere kwake kuti, ‘Chokani kwa Ine, inu otembereredwa, pitani ku moto wosatha wokonzedwera mdierekezi ndi angelo ake. Pakuti ndinali ndi njala ndipo simunandipatse chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo simunandipatse madzi akumwa, ndinali mlendo koma inu simunandilandire, ndinali wa usiwa koma simunandiveke, ndinali wodwala komanso ku ndende simunandisamalire.’ “Iwo adzayankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala kapena ludzu kapena mlendo kapena wausiwa kapena wodwala kapena mʼndende, ndipo kuti sitinakuthandizeni?’ “Iye adzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene simunachitire mmodzi wa abale anga onyozekawa simunandichitire Ine.’

mayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo.

Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi chafufumimba napemphera kuti, “Atate anga, ngati ndikotheka, chikho ichi chichotsedwe kwa Ine. Koma osati monga mmene ndifunira, koma monga mufunira Inu.”

Atakhala pansi, Yesu anayitana khumi ndi awiriwo nati, “Ngati wina aliyense afuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza ndi wotumikira onse.”

Sizili choncho ndi inu. Mʼmalo mwake, amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala wotumikira, ndipo aliyense amene akufuna kukhala wamkulu akhale kapolo wa onse. Pakuti ngakhale Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kuti ukhale dipo la anthu ambiri.”

Pamene muyimirira kupemphera, ngati muli ndi chifukwa ndi wina, mukhululukireni, kuti Atate anu akumwamba akukhululukireni machimo anu.” (Koma ngati simukhululukirana, ngakhale Atate anu akumwamba sadzakhululukira machimo anu).

Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse ndi mphamvu zako zonse.’ Lachiwiri ndi ili: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’ Palibe lamulo lina loposa amenewa.” Munthuyo anayankha kuti, “Mwanena bwino Aphunzitsi. Mwalondola ponena kuti Mulungu ndi mmodzi ndipo palibe wina wofanana naye koma Iye yekha. Kumukonda Iye; ndi mtima wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini, ndi zopambana kuposa zopereka ndi nsembe zopsereza.”

Pamene Iye anali mʼBetaniya, atakhala pa tebulo akudya mʼnyumba ya munthu wodziwika kuti Simoni wakhate, anabwera mayi ndi botolo la mafuta onunkhira amtengo wapamwamba opangidwa ndi nadi. Anaphwanya botololo nakhuthula mafutawo pa mutu wa Yesu.

Yohane anayankha kuti, “Munthu amene ali ndi malaya awiri apatseko amene alibe, ndi amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi.”

“Koma Ine ndikuwuza inu amene mukundimva: Kondani adani anu, chitirani zabwino amene amakudani. Dalitsani amene amakutembererani, apempherereni amene amakusautsani. Ngati wina akumenyani patsaya limodzi mupatseninso tsaya linalo. Ngati wina akulanda mwinjiro wako, umulole atenge ndi mkanjo omwe. Mupatseni aliyense amene akupemphani kanthu ndipo ngati wina atenga chinthu chanu, musamulamule kuti akubwezereni. Inu muwachitire anthu ena, zomwe mukanafuna kuti iwo akuchitireni.

“Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amakonda amene amawakondanso. Ndipo ngati muchita zabwino kwa amene ndi abwino kwa inu, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amachita izi. Ndipo ngati mukongoza amene mukuyembekeza kuti abweza, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amabwereketsa kwa ochimwa anzawo, ndipo amayembekezera kubwezeredwa zonse.

Koma kondani adani anu, achitireni zabwino, akongozeni koma osayembekezera kulandira kanthu. Pamenepo mphotho yanu idzakhala yayikulu ndipo inu mudzakhala ana a Wammwambamwamba, chifukwa ndi wokoma mtima kwa anthu osayamika ndi oyipa. Khalani achifundo, monga momwe Atate anu ali achifundo.” “Musaweruze, ndipo inu simudzaweruzidwa. Musatsutse ndipo inu simudzatsutsidwa. Khululukirani ena ndipo mudzakhululukidwa. Perekani ndipo mudzapatsidwa. Adzakupatsani mʼthumba mwanu muyeso wabwino, wotsenderezeka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyeso umene mumagwiritsa ntchito, ndi omwewo adzakuyeserani.”

Mayi amene amakhala moyo wauchimo mu mzindawo atadziwa kuti Yesu akudya ku nyumba ya Mfarisiyo, anabweretsa botolo la mafuta onunkhira a alabasta. Iye anayimirira kumbuyo kwa Yesu pa mapazi ake akulira, nayamba kumadontheza misozi pa mapazi ake. Ndipo iye anapukuta mapaziwo ndi tsitsi lake, nawapsompsona ndi kuwathira mafuta onunkhirawo.

“Anthu awiri anakongola ndalama kwa munthu wina wokongoletsa ndalama: mmodzi ndalama zokwana 500 ndi winayo ndalama makumi asanu. Panalibe mmodzi mwa iwo anali ndi ndalama zobwezera, ndipo iye anawakhululukira ngongole zawo. Tsopano ndi ndani mwa awiriwa adzamukonde koposa?” Simoni anayankha kuti, “Ndikuganiza kuti ndi amene anamukhululukira ngongole yayikulu.” Yesu anati, “Wayankha molondola.” Kenaka anatembenukira kwa mayiyo nati kwa Simoni, “Ukumuona mayiyu? Ine ndabwera mʼnyumba yako. Iwe sunandipatse madzi otsukira mapazi anga, koma iyeyu wanyowetsa mapazi anga ndi misozi yake ndi kuwapukuta ndi tsitsi lake. Iwe sunandipsompsone, koma mayiyu, kuyambira pamene Ine ndalowa, sanaleke kupsompsona mapazi anga. Iwe sunadzoze mutu wanga mafuta, koma iye wadzoza mapazi anga mafuta onunkhira. Tsono, ndikukuwuza iwe, machimo ake amene ndi ambiri akhululukidwa, monga chaonetsera chikondi chake chachikulu. Koma iye amene wakhululukidwa zochepa amakonda pangʼono.”

Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.”

Yesu pomuyankha anati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa. Wansembe ankapita pa njira yomweyo, ndipo ataona munthuyo, analambalala. Chimodzimodzinso, Mlevi wina pamene anafika pa malopo ndi kumuona, analambalalanso. Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, anafika pamene panali munthuyo; ndipo atamuona, anamva naye chisoni. Anapita panali munthu wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa zilonda zake, nʼkuzimanga. Kenaka anamukweza pa bulu wake, napita naye ku nyumba ya alendo, namusamalira. Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, ‘Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.’ “Kodi ukuganiza ndi ndani mwa atatuwa, amene anali mnansi wa munthu amene anavulazidwa ndi achifwambawo?” Katswiri wa Malamulo uja anayankha kuti, “Amene anamuchitira chifundo.” Yesu anamuwuza kuti, “Pita, uzikachita chimodzimodzi.”

“Pamene wina wakuyitanani ku phwando la ukwati, musakhale pa malo aulemu ayi, chifukwa mwina anayitananso munthu wina wolemekezeka kuposa inu. Ngati zitatero, ndiye kuti munthu uja amene anakuyitani inu nonse awiri adzakuwuzani kuti, ‘Mupatseni munthu uyu malo anu.’ Pamenepo inu mudzachita manyazi, pokakhala malo wotsika. Koma akakuyitanani, khalani pa malo otsika, kuti amene anakuyitanani uja adzakuwuzeni kuti, ‘Bwenzi, bwera udzakhale pa malo aulemu pano.’ Pamenepo inu mudzalandira ulemu pamaso pa alendo anzanu onse. Pakuti aliyense wodzikuza adzamuchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamukweza.”

Kenaka Yesu anati kwa mwini malo uja, “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamayitane abwenzi ako, abale ako, anthu afuko lako kapena anzako achuma; ngati iwe utero, iwo adzakuyitananso, choncho udzalandiriratu mphotho yako. Koma ukakonza phwando, itana anthu osauka, ofa ziwalo, olumala ndi osaona. Pamenepo udzakhala wodala, chifukwa iwo sangakubwezere kanthu, koma Mulungu ndiye adzakubwezera pa chiukitso cha olungama.”

Ndipo iye ananyamuka ndi kupita kwa abambo ake. “Koma iye akanali patali, abambo ake anamuona ndipo anamvera chisoni; anathamangira mwanayo, namukumbatira ndi kupsompsona. “Mwanayo anati, ‘Abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi inunso. Ine sindiyenera konse kutchedwa mwana wanu.’ “Koma abambowo anati kwa antchito ake, ‘Fulumirani! Bweretsani mkanjo wabwino kwambiri ndipo mumuveke. Muvekeni mphete ndi nsapato. Bweretsani mwana wangʼombe wonenepa ndipo iphani. Tiyeni tikhale ndi phwando ndi kukondwerera. Pakuti mwana wangayu anali wakufa, ndipo ali ndi moyonso; iye anatayika ndipo wapezeka.’ Chomwecho anayamba kukondwerera.

“Palibe wantchito amene angatumikire mabwana awiri. Mwina iye adzadana ndi wina ndi kukonda winayo, kapena adzakhala wodzipereka kwa wina ndi kumunyoza winayo. Inu simungathe kutumikira Mulungu komanso ndalama nthawi imodzi.”

Ngati iye akulakwira kasanu ndi kawiri pa tsiku, ndipo ngati nʼkubweranso kwa iwe kasanu ndi kawiri nati, ‘Ndalapa,’ umukhululukire.”

“Ine ndikukuwuzani kuti munthu wolandira msonkhoyu, osati Mfarisiyu, anapita kwawo atalungamitsidwa pamaso pa Mulungu. Chifukwa chake, aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”

Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.”

Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu wapereka zambiri kuposa ena onsewa. Anthu onsewa atapa mphatso zawo kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo; koma uyu, mwa umphawi wake, wapereka zonse zimene ali nazo.”

Koma inu simuyenera kukhala choncho. Mʼmalo mwake, wamkulu pakati panu akhale ngati wamngʼono pa onse, ndipo iye amene alamulira akhale ngati wotumikira. Pakuti wamkulu ndani, iye amene ali pa tebulo kapena iye amene akutumikira? Kodi si iye amene ali pa tebulo? Koma ndili pakati panu ngati mmodzi wokutumikirani.

Koma iye anayankha kuti, “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu ku ndende ndi kufa komwe.”

Yesu anati, “Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita.” Ndipo anagawana malaya ake mochita maere.

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi.

Nʼkoyenera kuti Iyeyo akule, ine ndichepe.

Nʼchifukwa chake Atate anga amandikonda, popeza Ine ndikupereka moyo wanga kuti ndiwutengenso.

Yesu analira. Pamenepo Ayuda anati, “Taonani mmene Iye anamukondera Lazaro!”

Kenaka Mariya anatenga botolo la mafuta a nadi, onunkhira bwino kwambiri, amtengowapatali; Iye anadzoza mapazi a Yesu napukuta ndi tsitsi lake. Ndipo nyumba yonse inadzaza ndi fungo lonunkhira bwino la mafutawo.

Inali pafupifupi nthawi ya phwando la Paska. Yesu anadziwa kuti nthawi yafika yoti achoke mʼdziko lapansi ndi kupita kwa Atate. Atawakonda ake amene anali mʼdziko lapansi, Iye anawaonetsa chikondi chake chonse.

Atachita izi, anathira madzi mʼbeseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira chimene anachimanga mʼchiwuno mwake.

Tsono ngati Ine, Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi anu. Ine ndakupatsani chitsanzo kuti muzichita monga Ine ndachitira. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti wantchito saposa mbuye wake, kapena wotumidwa kuposa amene wamutuma. Ngati inu mudziwa zinthu zimenezi, mudzakhala odala mukamazichita.

Mmodzi wa ophunzira ake amene Yesu anamukonda, anali atatsamira pachifuwa chake.

“Lamulo latsopano limene ndikukupatsani ndi lakuti: Kondanani wina ndi mnzake, monga momwe Ine ndinakonda inu. Nanunso mukondane wina ndi mnzake. Mukamakondana aliyense adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga.”

“Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga.

Iye amene amadziwa malamulo anga ndi kuwasunga ndiye amene amandikonda. Wokonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga ndipo Inenso ndidzamukonda ndikudzionetsa ndekha kwa iye.”

Yesu anamuyankha kuti, “Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye. Iye amene sandikonda Ine sasunga mawu anga. Mawu awa amene mukumva si anga ndi a Atate amene anandituma Ine.

“Monga momwe Atate amandikondera Ine, Inenso ndakukondani. Tsopano khalani mʼchikondi changa. Ngati mumvera malamulo anga, mudzakhala mʼchikondi changa, monga Ine ndimamvera malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala mʼchikondi chawo. Ine ndakuwuzani izi kuti chimwemwe changa chikhale mwa Inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chokwanira. Lamulo langa ndi ili: ‘Kondanani wina ndi mnzake monga Ine ndakonda inu.’ Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani. Ine sindikutchulaninso antchito, chifukwa wantchito sadziwa zimene bwana wake akuchita. Mʼmalo mwake Ine ndakutchani abwenzi pakuti zilizonse zimene ndinaphunzira kwa Atate, Ine ndakudziwitsani.

Lamulo langa ndi ili: ‘Muzikondana.’

Atate mwini anakukondani chifukwa inu mwandikonda Ine ndipo mwakhulupirira kuti Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate.

Ine ndikhale mwa iwo ndipo Inu mwa Ine kuti umodzi wawo ukhale wangwiro. Choncho dziko lapansi lidzadziwa kuti Inu munandituma Ine ndipo Inu mwawakonda iwowa monga momwe Inu munandikondera Ine.

Ine ndawadziwitsa dzina lanu, ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzina lanulo, kuti chikondi chomwe munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”

Iwo atamaliza kudya chakudya chammawa, Yesu anati kwa Simoni Petro, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda Ine kuposa mmene amandikondera awa?” Iye anati, “Inde Ambuye, Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.” Yesu anati, “Samala ana ankhosa anga.” Yesu anatinso, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?” Iye anayankha kuti, “Inde, Ambuye, Inu mukudziwa kuti ine ndimakukondani.” Yesu anati, “Weta nkhosa zanga.” Yesu anati kwa iye kachitatu, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?” Petro anadzimvera chisoni chifukwa Yesu anamufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda Ine?” Iye anati, “Ambuye, Inu mudziwa zinthu zonse. Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.” Yesu anati, “Dyetsa nkhosa zanga.

Okhulupirira onse anali pamodzi ndipo aliyense ankapereka zinthu zake kuti zikhale za onse. Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake. Tsiku ndi tsiku ankasonkhana pamodzi pa bwalo la pa Nyumba ya Mulungu. Ankadya pamodzi mʼnyumba zawo mwasangala ndi mtima woona.

Panalibe anthu osowa kanthu pakati pawo. Pakuti amene anali ndi malo, kapena nyumba amagulitsa ndi kubweretsa ndalamazo ndi kuzipereka kwa atumwi, ndipo zimagawidwa kwa aliyense amene anali ndi chosowa.

Akumugenda miyala, Stefano anapemphera kuti, “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” Ndipo anagwada pansi nafuwula mwamphamvu kuti, “Ambuye musawawerengere tchimoli.” Atanena mawu amenewa anamwalira.

Mawu amene ndunayo imawerenga anali awa: “Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira, kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta, momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake. Iye ananyozedwa ndipo panalibe chilungamo pa mlandu wake. Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo?”

Pa zonse zimene ndinachita, ndinakuonetsani kuti pogwira ntchito molimbika motere tiyenera kuthandiza ofowoka, pokumbukira mawu a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupereka kumadalitsa kuposa kulandira.’ ”

Ndipo chiyembekezo chimenechi sichitikhumudwitsa chifukwa Mulungu mwa Mzimu Woyera, amene Iye anatipatsa, wadzaza mʼmitima mwathu ndi chikondi chake. Pakuti pa nthawi yake, tikanali ochimwa, Khristu anatifera anthu osapembedzafe. Sizichitika kawirikawiri kuti munthu wina afere munthu wolungama, ngakhale kuti chifukwa cha munthu wabwino wina atha kulimba mtima kumufera. Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera. Popeza chifukwa cha magazi ake ife tapezeka olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa kotani ku mkwiyo wa Mulungu. Pakuti pamene tinali adani a Mulungu, tinayanjanitsidwa ndi Iye kudzera mu imfa ya Mwana wake. Nanga tidzapulumutsidwa bwanji kudzera mʼmoyo wake, titayanjanitsidwa naye?

Ndani amene adzatilekanitsa ife ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zowawa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena umaliseche, kapena choopsa, kapena lupanga? Monga kwalembedwa: “Chifukwa cha inu, ife tikuphedwa tsiku lonse: ife tikutengedwa ngati nkhosa zoti zikaphedwe.” Ayi, mu zonsezi ife ndife oposa agonjetsi mwa Iye amene anatikonda.

Pakuti ine ndatsimikiza ndi mtima wonse kuti ngakhale imfa, kapena moyo, ngakhale angelo, kapena ziwanda, ngakhale zinthu zilipo, kapena zili mʼtsogolo, kapena mphamvu zina, ngakhale kutalika, kapena kuya, kapena chilichonse mʼchilengedwe chonse, sizingathe kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani.

Chikondi chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choyipa; gwiritsitsa chabwino. Mukondane kwathunthu monga abale. Lemekezanani wina ndi mnzake kuposa inu eni. Musakhale aulesi mʼmachitidwe anu. Khalani achangu mu mzimu ndipo tumikirani Ambuye. Kondwerani mʼchiyembekezo, pirirani mʼmasautso ndiponso khulupirikani mʼpemphero. Gawanani ndi anthu a Mulungu amene ali ndi chosowa. Cherezani alendo.

Adalitseni amene akuzunzani. Adalitseni ndipo musawatemberere. Kondwani pamodzi ndi amene akukondwa ndipo lirani ndi amene akulira. Muyanjane wina ndi mnzake. Musakhale onyada, koma lolani kuyanjana ndi anthu wamba. Musaganize kuti mumadziwa zonse. Musabwezere choyipa ndi choyipa kwa aliyense. Samalitsani kuchita chabwino pamaso pa aliyense. Ngati nʼkotheka, khalani mwamtendere ndi aliyense monga momwe mungathere.

Okondedwa anga, musabwezere choyipa, koma lekerani Mulungu. Pakuti kwalembedwa, “Kubwezera chilango nʼkwanga. Ndidzawalanga ndine,” akutero Ambuye. Koma, “Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, mupatse kanthu kakumwa. Pochita ichi, udzamuwunjikira makala amoto pamutu pake.” Musagonjetsedwe ndi choyipa, koma gonjetsani choyipa pochita chabwino.

Musakhale ndi ngongole ndi wina aliyense kupatula ngongole ya kukondana wina ndi mnzake. Pakuti amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa lamulo. Malamulo awa: “Usachite chigololo,” “Usaphe,” “Usabe,” “Usasirire,” ndi malamulo ena onse amene alipo, akhazikika pa lamulo limodzi ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.” Chikondi sichichitira mnzake zoyipa. Chifukwa chake chikondi ndicho chokwaniritsa lamulo.

Mulandire amene ndi ofowoka mʼchikhulupiriro, osatsutsana naye pa maganizo ake.

Tsono nʼchifukwa chiyani iwe ukuweruza mʼbale wako? Kapena nʼchifukwa chiyani ukumunyoza mʼbale wako? Pakuti ife tonse tidzayima pa mpando wakuweruza wa Mulungu. Kwalembedwa, akutero Ambuye, “Pamene Ine ndili ndi moyo, aliyense adzandigwadira ndipo lilime lililonse lidzavomereza Mulungu.” Choncho tsopano, aliyense wa ife adzafotokoza yekha kwa Mulungu.

Motero, tiyeni tisiye kuweruzana wina ndi mnzake. Mʼmalo mwake, tsimikizani mʼmaganizo anu kuti musayike chokhumudwitsa kapena chotchinga mʼnjira ya mʼbale wanu. Monga mmodzi amene ndili mwa Ambuye Yesu, ndine wotsimikiza mtima kuti palibe chakudya chimene pachokha ndi chodetsedwa. Koma ngati wina atenga china chake kukhala chodetsedwa, kwa iyeyo ndi chodetsedwa. Ngati mʼbale wako akuvutika chifukwa cha chimene umadya, iwe sukuchitanso mwachikondi. Usamuwononge mʼbale wako amene Khristu anamufera chifukwa cha chakudya chakocho.

Tsono tiyeni tiyesetse kuchita zimene zidzabweretsa mtendere ndi kulimbikitsana mwachikondi.

Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu tiziwalezera mtima anthu ofowoka, ndipo tisamadzikondweretse tokha. Aliyense wa ife akondweretse mnzake pomuchitira zabwino zomulimbikitsa. Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretsa yekha koma, monga kwalembedwa kuti, “Chipongwe cha anthu okunyozani chinagwera Ine.” Pakuti zilizonse zimene zinalembedwa kale zinalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembawo amatilimbikitsa kupirira kuti tikhale ndi chiyembekezo. Mulungu amene amapereka kupirira ndi chilimbikitso akupatseni maganizo amodzi pakati panu monga inu mukutsatira Khristu Yesu, kotero kuti ndi mtima umodzi ndi movomerezana mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Tsopano landiranani wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, ndi cholinga choti Mulungu alemekezeke.

Mupatsane moni wina ndi mnzake mwachikondi choona. Mipingo yonse ya Khristu ikupereka moni.

Abale, ine ndikukupemphani kuti musamale chifukwa cha amene ayambitsa mipatuko ndi kuyika zokhumudwitsa panjira yanu, motsutsana ndi chiphunzitso chimene mwachiphunzira. Muwapewe iwo. Pakuti otero sakutumikira Ambuye athu Khristu koma zilakolako zawo. Ndi mawu okoma ndi oshashalika iwo amanamiza anthu osalakwa.

Komabe monga zalembedwa kuti, “Palibe diso linaona, palibe khutu linamva, palibe amene anaganizira, zimene Mulungu anakonzera amene amukonda”

Chokha choti mwakasumirana chikuonetseratu kuti mwagonjetsedwa kale. Bwanji osangolola kuti ena akulakwireni? Bwanji osangolola kuti ena akubereni?

Tsopano pa zinthu zomwe munandilembera nʼkwabwino kuti munthu asakwatire. Koma chifukwa choti chigololo chawanda, mwamuna aliyense akhale naye mkazi wakewake ndipo mkazi aliyense akhale naye mwamuna wakewake. Mwamuna akwaniritse udindo wake wa pa banja kwa mkazi wake, ndipo chimodzimodzi mkazi kwa mwamuna wake. Thupi la mkazi wokwatiwa si la iye mwini yekha koma ndi la mwamuna wakenso. Momwemonso, thupi la mwamuna si la iye mwini yekha koma ndi la mkazi wakenso. Musamakanizane, pokhapokha mutagwirizana awiri kuti mwakanthawi mudzipereke kumapemphero. Kenaka mukhalirenso pamodzi kuopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cholephera kudziretsa.

Ngakhale ndine mfulu ndipo sindine kapolo wa munthu, ndimadzisandutsa kapolo wa aliyense kuti ndikope ambiri mmene ndingathere.

Munthu aliyense asafunefune zokomera iye yekha, koma zokomeranso ena.

Musakhumudwitse aliyense, kaya ndi Myuda, Mgriki, kapena mpingo wa Mulungu. Mu zonse ndikuyesetsa kukondweretsa aliyense mʼnjira iliyonse. Popeza sindikufunafuna zokondweretsa ine ndekha koma zokomera ambiri kuti apulumutsidwe.

kuti pasakhale kugawikana mʼthupi koma kuti ziwalo zonse zisamalirane. Ngati chiwalo chimodzi chikumva kuwawa, ziwalo zonse zimamvanso kuwawa. Ngati chiwalo chimodzi chilandira ulemu, ziwalo zonse zimakondwera nawo.

Ngakhale nditamayankhula mʼmalilime a anthu ndi a angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chinganga chaphokoso kapena ngati chitsulo chosokosera. Ngati ndili ndi mphatso ya uneneri, nʼkumazindikira zinsinsi ndi kudziwa zonse, ndipo ngati ndili ndi chikhulupiriro chosuntha mapiri, koma wopanda chikondi, ine sindili kanthu. Ngati ndipereka zanga zonse kwa osauka ndi kupereka thupi langa kuti alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ine sindipindula kanthu. Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa. Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse. Chikondi ndi chosatha. Koma mphatso ya uneneri idzatha, pamene pali kuyankhula malilime adzatha, pamene pali chidziwitso chidzatha.

Ndipo tsopano zatsala zinthu zitatu: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.

Funafunani chikondi, ndikufunitsitsa mphatso zauzimu, makamaka mphatso ya uneneri.

Chitani zonse mwachikondi.

Pakuti chikondi cha Khristu ndicho chimatikakamiza, chifukwa tikutsimikiza kuti mmodzi anafera anthu onse, kotero kuti anthu onse anafanso. Ndipo Iye anafera anthu onse kuti amene ali ndi moyo, asakhale ndi moyo wofuna kudzikondweretsa okha, koma azikondweretsa amene anawafera naukitsidwa chifukwa cha iwowo.

Mʼmalo mwake, mwanjira iliyonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu popirira kwambiri mʼmasautso, mʼzowawa ndi mʼzodetsa nkhawa. Pomenyedwa, kuponyedwa mʼndende ndi mʼzipolowe. Pogwira ntchito mwamphamvu, posagona usiku onse, posowa chakudya; pokhala moyo woyera mtima, pomvetsa zinthu, wokoma mtima ndi wachifundo mwa Mzimu Woyera ndi mwachikondi choonadi ndi poyankhula choonadi mwamphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili mʼdzanja lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo. Timatumikira Mulungu ngakhale ena amatinyoza ndi ena amatilemekeza, ena amatinenera chipongwe, enanso amatiyamikira. Ena amatitenga kukhala ngati onena zoona, ndipo enanso amatitenga kukhala ngati onena zabodza. Amatiyesa osadziwika komatu ndife odziwika kwambiri. Amatiyesa wooneka ngati tikufa, koma tikupitirirabe ndi moyo, okanthidwa, koma osaphedwa. Amatiyesa achisoni, koma ndife achimwemwe nthawi zonse, aumphawi, koma olemeretsa ambiri; wopanda kanthu, koma tili ndi zonse.

Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri. Motero ndikuchitira umboni kuti anapereka mmene akanathera, ndipo mwinanso kuposera mmene akathera kupereka. Anapereka mosakakamizidwa, ndipo anatipempha motiwumiriza kuti tiwapatse mwayi woti nawonso athandize anthu oyera mtima a ku Yudeya. Iwo anachita moposera mmene ife timayembekezera. Choyamba anadzipereka kwa Ambuye ndipo kenaka kwa ife monga mwa chifuniro cha Mulungu.

Popeza pa zinthu zonse munachita bwino, monga pachikhulupiriro, poyankhula, pachidziwitso, pakhama lambiri ndi pachikondi chanu pa ife, onetsetsani kuti muchitenso bwino pachisomo ichi chopereka. Sindikukulamulirani, koma ndikufuna kuona ngati chikondi chanu nʼchoona pofananitsa ndi changu cha anthu ena. Pakuti mukudziwa chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, kuti ngakhale anali wolemera, koma chifukwa cha inuyo anasanduka wosauka, kuti umphawi wakewo, inuyo mulemere.

Ndipo ngati mtima ofunitsitsa ulipo, mphatsoyo imalandiridwa molingana ndi zimene munthuyo ali nazo, osati zimene alibe.

Choncho anthu amenewa atsimikizireni za chikondi chanu ndipo adziwe chifukwa chimene ife timakunyadirani, kuti mipingo yonse iwone chimenechi.

Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.

Mwa kufatsa ndi kuleza mtima kwa Khristu, ndikukupemphani, ine Paulo amene anthu ena amati ndimachita manyazi tikaonana maso ndi maso ndi inu, koma wosaopa pamene ndili kutali nanu!

Tsono, chifukwa cha Khristu, ndimakondwera pamene ndili wofowoka, pamene akundinyoza, pamene ndikumva zowawa, ndi pamene akundizunza ndi kundisautsa. Pakuti pamene ndili wofowoka ndiye kuti ndili wamphamvu.

Potsiriza abale, ndikuti tsalani bwino. Yesetsani kukhala angwiro, mvetsetsani pempho langa, khalani a mtima umodzi, khalani mwamtendere. Ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere adzakhala nanu. Lonjeranani ndi mpsopsono wachiyero.

Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.

Palibe Myuda kapena Mgriki, kapolo kapena mfulu, mwamuna kapena mkazi, pakuti nonse ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.

Pakuti mwa Khristu Yesu mdulidwe kapena kusachita mdulidwe zilibe phindu. Chinthu chokhacho chimene chimafunika ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi.

Inu abale, Mulungu anakuyitanani kuti mukhale mfulu. Koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo kuchita zoyipa zachikhalidwe cha uchimo cha thupi lanu, koma mutumikirane wina ndi mnzake mwachikondi. Pakuti malamulo onse akuphatikizidwa mu lamulo ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.” Ngati mupitiriza kulumana ndi kukhadzulana, samalani kuti mungawonongane.

Ntchito za thupi lanu la uchimo zimaonekera poyera ndi izi: dama, zodetsa ndi kuchita zonyansa; kupembedza mafano ndi ufiti; kudana, kukangana, kupsa mtima, kudzikonda, kugawikana, mipatuko ndi nsanje, kuledzera, mchezo ndi zina zotere. Ine ndikukuchenjezani monga ndinachita poyamba paja kuti amene amachita zimenezi sadzalandira ufumu wa Mulungu.

Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi.

Abale, ngati munthu agwa mʼtchimo lililonse, inu amene Mzimu amakutsogolerani, mumuthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe. Thandizanani kusenza zolemetsa zanu, ndipo mʼnjira imeneyi mudzakwanitsa lamulo la Khristu.

Ngati wina adziyesa kanthu pamene iyeyo sali kanthu konse, akudzinamiza yekha. Munthu aliyense aziyesa yekha ntchito zake mmene zilili. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, iyeyo asadzifanizire ndi munthu wina wake,

Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa. Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira.

Dziko lapansi lisanalengedwe, Mulungu anatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi wopanda cholakwa pamaso pake. Mwa chikondi chake,

Choncho, kuyambira pamene ndinamva za chikhulupiriro chanu mwa Ambuye Yesu ndi za chikondi chanu pa oyera mtima onse, ine sindilekeza kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani mʼmapemphero anga.

Koma chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ndi olemera mʼchifundo, anatipanga kukhala amoyo ndi Khristu ngakhale pamene ife tinali akufa mu zolakwa zathu. Koma tinapulumutsidwa mwachisomo.

Pakuti ndife ntchito ya Mulungu, olengedwa mwa Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anazikonzeratu kale kuti tizichite.

kuti Khristu akhazikike mʼmitima mwanu mwachikhulupiriro. Ndipo ndikukupemphererani kuti muzikike ndi kukhazikika mʼchikondi kuti mukhale ndi mphamvu, kuti pamodzi ndi anthu oyera mtima onse muthe kuzindikira kupingasa, kutalika ndi kukwera komanso kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. Ndikukupemphererani kuti mudziwe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kwathunthu ndi moyo wa Mulungu mwini.

Ine monga wamʼndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukulimbikitsani kuti mukhale moyo woyenera mayitanidwe amene munalandira. Mukhale odzichepetsa kwathunthu ndi ofatsa; mukhale oleza mtima, ololerana wina ndi mnzake mwachikondi. Muyesetse kusunga umodzi wa Mzimu; umodzi umene umatimangirira pamodzi mu mtendere.

Iye amene wakhala akuba asabenso, koma agwire ntchito ndi kuchita kenakake kaphindu ndi manja ake, kuti akhale ndi kenakake kogawana ndi amene akusowa. Mʼkamwa mwanu musatuluke mawu aliwonse onyansa, koma okhawo amene ndi othandiza kulimbikitsa ena molingana ndi zosowa zawo, kuti athandize amene akawamve. Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa. Chotsani kuzondana, ukali ndi kupsa mtima, chiwawa ndi kuyankhula zachipongwe, pamodzi ndi choyipa chilichonse. Mukomerane mtima ndi kuchitirana chifundo wina ndi mnzake. Khululukiranani wina ndi mnzake, monga momwe Mulungu anakukhululukirani mwa Khristu.

Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu. Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu.

Gonjeranani wina ndi mnzake, kuonetsa kuopa Khristu.

Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo

Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha. Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake pakuti ndife ziwalo za thupi lake.

“Pa chifukwa ichi, mwamuna adzasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.” Ichi ndi chinsinsi chozama, koma ine ndikunena za Khristu ndi mpingo. Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake.

Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. “Lemekeza abambo ndi amayi ako.” Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, “zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi.” Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye. Inu antchito, mverani mabwana anu mwaulemu ndi mwamantha ndi moona mtima, monga momwe mungamvere Khristu.

Mtendere, chikondi pamodzi ndi chikhulupiriro kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi abale onse. Chisomo kwa onse amene amakonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosatha.

Mulungu angandichitire umboni kuti ndimakulakalakani ndi chikondi cha Khristu Yesu. Ndipo pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chipitirire kukulirakulira pa chidziwitso ndi kuzama mʼmaganizo, kuti mukhoza kuzindikira chabwino koposa zonse ndi chiti kuti muthe kukhala wopanda chodetsa ndi wopanda chilema kufikira tsiku la Khristu.

Ngati muli ndi chilimbikitso chilichonse chifukwa cholumikizana ndi Khristu, ngati muli ndi chitonthozo chifukwa cha chikondi chake, ngati muli ndi mtima umodzi mwa Mzimu, ndipo ngati mumakomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, tsono tsirizani chimwemwe changa pokhala amaganizo ofanana, achikondi chimodzimodzi, amodzi mu mzimu ndi acholinga chimodzinso. Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo. Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena.

Pa ubale wanu wina ndi mnzake, mukhale ndi mtima wofanana ndi wa Khristu Yesu: Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu, sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa. Koma anadzichepetsa kotheratu nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse. Ndipo pokhala munthu choncho anadzichepetsa yekha ndipo anamvera mpaka imfa yake, imfa yake ya pamtanda!

Tsono abale anga, ndimakukondani ndipo ndikukulakalakani. Ndinu chimwemwe changa ndi chipewa cha ulemerero wanga. Abwenzi okondedwa, chilimikani choncho mwa Ambuye.

Timayamika Mulungu Atate wa Ambuye athu Yesu Khristu, nthawi zonse pamene tikukupemphererani. Timayamika chifukwa tinamva za chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu ndi za chikondi chanu pa oyera mtima onse.

Tsopano ine ndikukondwa kuti ndinavutika chifukwa cha inu, ndipo ndikukwaniritsa mʼthupi langa zimene zikuperewera pa masautso a Khristu, chifukwa cha thupi lake, limene ndi Mpingo.

Cholinga changa nʼchakuti alimbikitsidwe ndi kuyanjana pamodzi mʼchikondi, akhale odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndi kuti azindikire chinsinsi cha Mulungu, chimene ndi Khristu.

Koma tsopano mukuyenera kuzichotsa zinthu zonsezi monga: mkwiyo, ukali, dumbo, chipongwe ndi mawu onyansa. Musanamizane wina ndi mnzake, popeza munavula munthu wakale pamodzi ndi zochita zake ndipo mwavala munthu watsopano, amene nzeru zake zikukonzedwanso kuti afanane ndi Mlengi wake. Pano palibe kusiyana pakati pa Mgriki ndi Myuda, wochita mdulidwe ndi wosachita, wosaphunzira kapena wosachangamuka, kapolo kapena mfulu, koma Khristu yekha basi ndipo amakhala mwa onse.

Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira. Mulezerane mtima ndipo muzikhululukirana ngati wina ali ndi chifukwa ndi mnzake. Muzikhululukirana monga Ambuye anakhululukira inu. Ndipo kuwonjezera pa zonsezi valani chikondi, chimene chimangirira zonsezi pamodzi mu mgwirizano wangwiro. Mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima mwanu, popeza monga ziwalo za thupi limodzi, munayitanidwa kuti mukhale ndi mtendere. Ndipo muziyamika. Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika. Ndipo chilichonse chimene mungachite, kaya nʼkuyankhula, kaya nʼkugwira ntchito, muchite zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, kuyamika kwa Mulungu Atate kudzera mwa Iye.

Inu akazi, gonjerani amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye. Inu amuna, kondani akazi anu ndipo musawapsere mtima. Inu ana, mverani makolo anu mu zonse pakuti izi zimakondweretsa Ambuye. Inu abambo, musakwiyitse ana anu, kuti angataye mtima.

Inu antchito, mverani mabwana anu mu zonse, ndipo muzichita zimenezi osati nthawi yokhayo imene akukuonani kuti akukondeni, koma muzichite moona mtima ndi mopereka ulemu kwa Ambuye. Chilichonse mungachite, muchite ndi mtima wanu onse, monga mmene mungagwirire ntchito ya Ambuye osati ya anthu.

Mayendedwe anu pakati pa akunja, akhale anzeru ndipo mugwiritse ntchito mpata uliwonse umene muli nawo. Mayankhulidwe anu nthawi zonse akhale odzaza ndi chisomo ndi okoma, kuti mudziwe kuyankha aliyense.

Ambuye achulukitse chikondi chanu ndi kuti chisefukire kwa wina ndi mnzake ndiponso kwa wina aliyense, monga momwe chikondi chathu chichitira kwa inu. Iye alimbikitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera mtima pamaso pa Mulungu ndi Atate athu pamene Ambuye athu Yesu akubwera ndi oyera ake onse.

Tsono kunena za kukondana wina ndi mnzake, nʼkosafunikira kuti tikulembereni, popeza ndi Mulungu amene anakuphunzitsani za kukondana wina ndi mnzake. Ndipo kunena zoona, mumakonda abale onse a mʼbanja la Mulungu a ku Makedoniya. Komabe, abale tikukulimbikitsani kuti muzichita zimenezi koposa kale.

Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira. Tsopano tikukupemphani abale kuti muziwalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene amakuyangʼanirani mwa Ambuye ndi amene amakulimbikitsani. Muziwachitira ulemu kwambiri mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo. Mukhale pa mtendere wina ndi mnzake. Ndipo tikukupemphani abale, muwachenjeze amene akungokhala osagwira ntchito, alimbikitseni amanyazi, thandizani ofowoka ndipo muzilezera mtima aliyense. Onetsetsani kuti wina asabwezere choyipa kwa omuchitira choyipa koma nthawi zonse yesetsani kukhala okoma mtima kwa wina ndi mnzake; ndiponso ndi kwa anthu ena onse.

Ife tiyenera kuyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale. Ndipo tiyenera kutero chifukwa chikhulupiriro chanu chikukulirakulirabe, ndiponso chikondi chimene aliyense wa inu ali nacho pa mnzake chikuchulukirachulukirabe. Nʼchifukwa chake, timayankhula monyadira mʼmipingo yonse ya Mulungu za kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso onse ndi mayesero amene mukudutsamo. Zonsezi zikutsimikiza kuti Mulungu amaweruza molungama. Zotsatira zake ndi zakuti mudzatengedwa kukhala oyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu umene mukuwuvutikira.

Ambuye atsogolere mitima yanu kuti mudziwe chikondi cha Mulungu ndiponso kupirira kumene Khristu amapereka.

Cholinga cha lamuloli ndi chikondi, chomwe chimachokera mu mtima woyera, chikumbumtima chabwino ndi chikhulupiriro choona.

Chisomo cha Ambuye athu chinatsanulidwa pa ine mochuluka, pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi zimene zili mwa Khristu Yesu.

Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata, koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe, pa makhalidwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.

Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.

Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa.

Ndikuyamika Mulungu amene ndimamutumikira ndi chikumbumtima chosatsutsika, monga momwe ankachitira makolo anga. Usiku ndi usana ndimakukumbukira mosalekeza mʼmapemphero anga. Ndikamakumbukira misozi yako, ndimalakalaka nditakuona kuti ndidzazidwe ndi chimwemwe.

Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga. Choncho usachite manyazi kuchitira umboni Ambuye athu, kapena kuchita manyazi chifukwa cha ine wamʼndende. Koma umve nane zowawa chifukwa cha Uthenga Wabwino, mothandizidwa ndi mphamvu za Mulungu.

Ndiponso mtumiki wa Ambuye asamakangane ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa aliyense, wodziwa kuphunzitsa, osati wokalipakalipa. Otsutsana naye awalangize mofatsa, mwina Mulungu adzawapatsa mwayi woti asinthike ndi kuzindikira choonadi.

Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero. Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino, opereka anzawo kwa adani awo, osaopa zoyipa, odzitukumula, okonda zowasangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu. Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa.

Tsono iwe, umadziwa zonse zimene ndimaphunzitsa, makhalidwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga,

Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona. Phunzitsa amuna achikulire kuti akhale osaledzera, aulemu wawo, odziletsa, okhwima mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkupirira. Chimodzimodzinso, phunzitsa amayi achikulire kuti akhale aulemu mʼmakhalidwe awo, asakhale osinjirira anzawo kapena zidakwa, koma akhale alangizi abwino. Tsono atha kulangiza amayi achichepere kukonda amuna awo ndi ana awo. Kuwaphunzitsa kukhala odziletsa ndi oyera mtima, osamala bwino mabanja awo, okoma mtima, ndi ogonjera amuna awo. Choncho palibe amene adzanyoze mawu a Mulungu. Momwemonso, uwalimbikitse amuna achichepere kuti akhale odziletsa. Pa zonse iwe mwini ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino. Pa chiphunzitso chako uwonetsa kuona mtima ndi kutsimikiza mtima kwako. Phunzitsa choonadi kuti anthu asapeze chokutsutsa, motero wotsutsana nawe adzachita manyazi chifukwa adzasowa kanthu koyipa kuti atinenere.

Uwakumbutse anthu kuti azigonjera oweruza ndi olamulira, aziwamvera ndi kukhala okonzeka kuchita chilichonse chabwino. Asamachitire chipongwe aliyense, asamakangane, akhale ofatsa ndipo oganizira ena, ndipo nthawi zonse akhale aulemu kwa anthu onse. Nthawi ina tinali opusa, osamvera, onamizidwa ndi omangidwa ndi zilakolako ndi zokondweretsa zamitundumitundu. Tinkakhala moyo wadumbo ndi wakaduka, odedwa ndiponso odana wina ndi mnzake. Koma kukoma mtima ndi chikondi cha Mulungu Mpulumutsi wathu chitaonekera, Iye anatipulumutsa, osati chifukwa cha ntchito zathu zolungama zimene tinachita koma chifukwa cha chifundo chake. Anatipulumutsa potisambitsa, kutibadwitsa kwatsopano ndi kutikonzanso mwa Mzimu Woyera

Ine ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakukumbukira iwe mʼmapemphero anga. Pakuti ndamva za chikondi chako, za chikhulupiriro chako mwa Ambuye Yesu ndiponso za chikondi chako pa oyera mtima onse.

Mʼbale, chikondi chako chandipatsa chimwemwe chachikulu ndi chilimbikitso, chifukwa umatsitsimutsa mitima ya anthu a Ambuye. Tsopano ngakhale kuti mwa Khristu nditha kulimba mtima ndi kulamulira kuti uchite zimene uyenera kuchita, komabe ndikupempha mwachikondi. Ine Paulo, munthu wokalamba, ndipo tsopano ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu,

Mulungu ndi wolungama, sangayiwale ntchito zanu ndi chikondi chanu chimene munamuonetsa pothandiza anthu ake monga mmene mukuchitirabe tsopano.

Pakuti Ine ndidzawakhululukira zoyipa zawo, ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”

Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.

Chifukwa Ambuye amadzudzula amene amawakonda ndipo amalanga aliyense amene amamulandira.” Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga? Ngati inu simulangidwa, komatu aliyense amalangidwa, ndiye kuti sindinu ana enieni koma amʼchigololo. Komanso, tonsefe tinali ndi abambo athu otibala amene amatilanga ndipo timawapatsa ulemu. Nanga kodi sitidzagonjera Atate a mizimu yathu kuti tikhale ndi moyo?

Pitirizani kukondana monga abale. Musayiwale kusamalira alendo, pakuti pochita zimenezi anthu ena anasamalira angelo amene samawadziwa. Muzikumbukira amene ali mʼndende ngati kuti inunso ndi omangidwa, ndiponso amene akusautsidwa ngati inunso mukuvutika.

Ndipo musayiwale kumachita zabwino ndi kuthandiza ena, pakuti Mulungu amakondwera ndi nsembe zotere.

Abale omwe ndi anthu wamba anyadire pamene akwezedwa.

Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima. Pakuti mkwiyo wa munthu subweretsa chilungamo chimene amafuna Mulungu. Choncho chotsani chizolowezi choyipa ndi khalidwe loyipa pakati panu, ndipo modzichepetsa landirani mawu amene anadzalidwa mwa inu, amene akhoza kukupulumutsani.

Ngati wina amadziyesa ngati ndi wachipembedzo, koma chonsecho saletsa lilime lake, amadzinyenga yekha ndipo chipembedzo chakecho ndi cha chabechabe.

Tangoganizirani, pakati panu patabwera munthu atavala mphete yagolide ndi zovala zapamwamba, ndipo winanso wosauka nʼkulowa atavala sanza. Ngati musamala kwambiri munthu wovala bwinoyu uja, nʼkumuwuza kuti, “Khalani pa mpando wabwinowu,” koma wosauka uja nʼkumuwuza kuti, “Ima apo,” kapena “Khala pansi pafupi ndi chopondapo mapazi angawa,” kodi simunachite tsankho pakati panu ndi kukhala oweruza a maganizo oyipa? Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda? Koma mwakhala mukunyoza amphawi. Kodi si anthu olemerawa amene akukudyerani masuku pamutu? Si anthu amenewa amene amakukokerani ku bwalo la milandu?

Ngati musungadi lamulo laufumu lija lopezeka mʼMalemba lakuti, “Konda mnansi wako monga iwe mwini,” ndiye kuti mukuchita bwino. Koma mukamaonetsa tsankho mukuchimwa, ndipo ndinu wochimwa monga wophwanya lamulo.

chifukwa munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso adzaweruzidwa mopanda chifundo. Chifundo chimapambana pa chiweruzo.

Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku. Ngati mmodzi wa inu amuwuza kuti, “Pita ndi mtendere, ukafundidwe ndipo ukakhute,” koma osamupatsa zimene akuzisowa, phindu lake nʼchiyani pamenepa? Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

Momwemonso, lilime ndi kachiwalo kakangʼono ka thupi koma limadzitama kuti nʼkuchita zikuluzikulu. Tangoganizirani za nkhalango yayikulu imene ingapse ndi kalawi kamoto koyamba mochepa. Lilime nalonso ndi moto, dziko la zoyipa pakati pa ziwalo za thupi. Limawononga munthu yense wathunthu. Limayika zonse za moyo wake pa moto, ndipo moto wake ndi wochokera ku gehena.

Ndani mwa inu amene ndi wanzeru ndi womvetsa zinthu? Mulekeni aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru ndiye zikutsogolera kudzichepetsa kwake ndi zochita zake Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi odzikonda, musadzitamandire kapena kukana choonadi.

Pakuti pamene pali kaduka ndi kudzikonda pomweponso pamakhala chisokonezo ndi zochitika zoyipa zonse. Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima. Anthu amtendere amene amadzala mtendere amakolola chilungamo.

Nʼchiyani chimene chimayambitsa ndewu ndi mapokoso pakati panu? Kodi sizichokera ku zilakolako zimene zimalimbana mʼkati mwanu? Mumalakalaka zinthu koma simuzipeza, choncho mumapha. Mumasirira zinthu koma simutha kuzipeza zimene mukufuna, choncho mumakangana ndi kumenyana. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu. Koma ngakhale mumapempha simulandira, chifukwa mumapempha ndi zolinga zoyipa. Mumapempha kuti muzigwiritse ntchito pa zokusangalatsani nokha.

Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma apereka chisomo kwa odzichepetsa.” Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani. Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira. Chitani chisoni chifukwa cha zimene mwachita, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni. Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani. Abale musamanenane. Aliyense wonenera zoyipa mʼbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo. Pamene muweruza malamulo, ndiye kuti simukusunga malamulowo, koma mukuwaweruza.

Aliyense amene amadziwa zabwino zimene amayenera kuchita koma osazichita, ndiye kuti wachimwa.

Inunso mukhale owugwira mtima ndi osasinthika chifukwa Ambuye ali pafupi kubwera. Abale, musamanenezane zoyipa kuopa kuti mungadzaweruzidwe. Woweruza ali pa khomo! Abale, tengerani chitsanzo cha aneneri amene anayankhula mʼdzina la Ambuye. Iwowo anakumana ndi zovuta koma anapirira.

Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.

Tsopano mwayeretsa mitima yanu pomvera choonadi, kuti muzikondana ndi abale anu, kukondana kwenikweni kochokera pansi pa mtima.

Choncho, lekani zoyipa zonse, chinyengo chilichonse, chiphamaso, nsanje ndi kusinjirira kulikonse. Monga makanda obadwa kumene amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wauzimu, kuti mukule ndi kukufikitsani ku chipulumutso chanu,

Chitirani ulemu aliyense, kondani abale okhulupirira, wopani Mulungu, ndipo chitirani mfumu ulemu. Inu akapolo, gonjerani ambuye anu ndi kuwachitira ulemu, osati kwa iwo okha amene ndi abwino ndi omvetsa zinthu, komanso kwa amene ndi ankhanza.

Munayitanidwa kudzachita zimenezi, chifukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire mʼmapazi ake. “Iye sanachite tchimo kapena kunena bodza.” Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sanabwezere chipongwe, pamene Iye ankamva zowawa, sanaopseze. Mʼmalo mwake, anadzipereka kwa Mulungu amene amaweruza molungama.

Potsiriza, nonse khalani a mtima umodzi, omverana chisoni. Kondanani monga abale, muchitirane chifundo ndi kudzichepetsa. Wina akakuchitirani choyipa musabwezere pochitanso choyipa, kapena kubwezera chipongwe akakuchitirani chipongwe, koma muwadalitse. Munayitanidwa kuti mulandire mdalitso.

Koposa zonse muzikondana wina ndi mnzake kwambiri, chifukwa chikondi chimaphimba machimo ambiri. Muzisamalirana wina ndi mnzake osamanyinyirika. Aliyense agwiritse ntchito mokhulupirika mphatso iliyonse imene anayilandira potumikira ena ngati adindo ogwiritsa bwino ntchito mphatso za Mulungu za mitundumitundu.

Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa, “Mulungu amatsutsana nawo odzikuza, koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.” Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni. Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.

Mupatsane moni ndi mpsopsono wachikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli mwa Khristu.

Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa chikhulupiriro chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru. Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu. Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi.

Koma munthu aliyense akamvera mawu ake, ndiye kuti chikondi cha Mulungu chafikadi penipeni mwa iyeyo. Pamenepo timatsimikizadi kuti tili mwa Iye.

Aliyense amene amati ali mʼkuwunika, koma nʼkumadana ndi mʼbale wake ali mu mdima. Aliyense amene amakonda mʼbale wake amakhalanso mʼkuwunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa. Koma aliyense wodana ndi mʼbale wake ali mu mdima ndipo akuyenda mu mdima. Iyeyo sakudziwa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa mʼmaso mwake.

Musamakonde dziko lapansi kapena chilichonse cha dziko lapansi. Ngati munthu wina aliyense akonda dziko lapansi, mwa iyeyo mulibe chikondi chokonda Atate.

Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.

Uthenga umene munawumva kuyambira pachiyambi ndi uwu: Tizikondana wina ndi mnzake.

Ife tikudziwa kuti tinatuluka mu imfa ndi kulowa mʼmoyo, chifukwa timakonda abale athu. Aliyense amene sakonda mʼbale wake akanali mu imfa. Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha. Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu. Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu? Ana okondedwa, chikondi chathu chisakhale cha pakamwa pokha koma cha ntchito zathu ndi mʼchoonadi.

Ndipo lamulo lake ndi ili: kukhulupirira dzina la Mwana wake, Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga Iye anatilamulira.

Anzanga okondedwa, tiyeni tikondane wina ndi mnzake, pakuti chikondi chimachokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi ndi mwana wa Mulungu ndipo amadziwa Mulungu. Aliyense amene alibe chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi. Mmene Mulungu anaonetsera chikondi chake pakati pathu ndi umu: Iye anatumiza Mwana wake mmodzi yekha ku dziko lapansi kuti mwa Iyeyo tikhale ndi moyo. Chikondi ndi ichi: osati kuti ife ndife amene tinamukonda Mulungu, koma kuti Iyeyo ndiye amene anatikonda ndipo anatumiza Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu. Anzanga okondedwa, popeza Mulungu anatikonda chotere, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake. Palibe amene anaonapo Mulungu, koma tikakondana wina ndi mnzake, ndiye kuti Mulungu amakhala mwa ife ndipo chikondi chake chafika pachimake penipeni mwa ife.

Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chikondi chafika pachimake penipeni pakati pathu, kotero kuti pa tsiku lachiweruzo tidzakhala olimba mtima chifukwa mʼdziko lapansi moyo wathu uli ngati wa Khristu. Mulibe mantha mʼchikondi. Koma chikondi ndi changwiro chimachotsa mantha, chifukwa mantha amabwera chifukwa choopa chilango. Munthu amene ali ndi mantha, chikondi chake sichangwiro. Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye anayamba kutikonda. Ngati wina anena kuti, “Ine ndimakonda Mulungu,” koma namadana ndi mʼbale wake ndi wabodza ameneyo. Pakuti aliyense amene sakonda mʼbale wake, amene akumuona, sangathenso kukonda Mulungu amene sanamuone. Ndipo Iye anatipatsa lamulo lakuti: Aliyense amene amakonda Mulungu ayenera kukondanso mʼbale wake.

Aliyense amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, iyeyo ndi mwana wa Mulungu, ndipo aliyense amene amakonda Atate amakondanso Mwana wake. Chodziwira kuti timakonda ana a Mulungu nʼchakuti timakonda Mulungu ndi kusunga malamulo ake. Pakuti kukonda Mulungu ndiye kusunga malamulo ake. Ndipo malamulo ake siwolemetsa,

Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi kwa Yesu Khristu, Mwana wa Atate, zikhale ndi ife mʼchoonadi ndi mʼchikondi.

Ndipo tsopano, amayi wokondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lomwe lija takhala nalo kuyambira pachiyambi. Ine ndikukupemphani kuti tidzikondana wina ndi mnzake. Ndipo chikondi ndiye kuyenda momvera malamulo ake. Lamulo lake ndi lakuti mukhale moyo wachikondi monga munamva kuyambira pachiyambi.

Khalani mʼchikondi cha Mulungu pamene mukudikira chifundo cha Ambuye athu Yesu Khristu kuti akubweretsereni moyo wosatha. Muwachitire chifundo amene akukayika. Ena muwapulumutse powalanditsa ku moto. Enanso muwachitire chifundo, koma mwa mantha, ndipo muzidana ngakhale ndi mwinjiro yomwe yayipitsidwa ndi machimo.

ndiponso kuchokera kwa Yesu Khristu mboni yokhulupirika, woyamba kuukitsidwa, ndi wolamulira mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene amatikonda ndipo watimasula ku machimo athu ndi magazi ake,

Komabe ndili ndi chotsutsana nawe: Wataya chikondi chako chapoyamba.

Iye akuti: Ndimadziwa ntchito zanu, chikondi chanu ndi chikhulupiriro chanu, kutumikira kwanu ndi kupirira kwanu. Ndikudziwa tsopano kuti ntchito zanu ndi zabwino kuposa zoyamba zija.

Amene ndimawakonda ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Choncho chita changu ndipo lapa.

‘Iwowa sadzamvanso njala, sadzamvanso ludzu, dzuwa kapena kutentha kulikonse sikudzawawotcha.’ Pakuti Mwana Wankhosa amene ali pakati pa mpando waufumu adzakhala mʼbusa wawo. ‘Iye adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.’ ‘Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.’ ”

Ndinaona mzinda wopatulika, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wovala zokongola kukonzekera mwamuna wake.

‘Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ ” Amene anakhala pa mpando waufumuyo anati, “Ndikulenga zinthu zonse zikhale zatsopano!” Ndipo anati, “Lemba izi, pakuti mawu awa ndi okhulupirika ndi woona.” Iye anandiwuza kuti, “Kwatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa onse akumva ludzu, ndidzawapatsa zakumwa zaulere zochokera ku kasupe wamadzi amoyo. Iye amene adzapambane adzalandira zonsezi, ndipo ndidzakhala Mulungu wake ndi Iye adzakhala mwana wanga.

Chichewa - Chichewa - NY

NYCCL - Mawu A Mulungu Mu Chichewa Chalero - 2016

This Bible text is from Biblica Open God's Word In Contemporary Chichewa
https://open.bible/bibles/chichewa-biblica-text-bible/
provided by: Biblica Inc, available by Creative Commons CC-BY-SA-4.0,
and this new compilation is shared as www.creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0.
Languages are made available to you by www.ipedge.net