12 – Tchimo la kugonana

Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Tchimo la kugonana.

Mavesi atatu ofunika kwambiri

Koma Ine ndikuwuzani kuti aliyense woyangʼana mkazi momusirira wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.

Amene ali ake a Khristu Yesu anapachika pa mtanda thupi lawo la uchimo pamodzi ndi zokhumba zawo ndi zolakalaka zawo.

Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chiwerewere nakakwatira mkazi wina, achita chigololo.”

Mavesi onse motsatira dongosolo lolondola – 177 ndime

Nʼchifukwa chake, mwamuna amasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake ndipo awiriwo amakhala thupi limodzi.

Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, “Kulirira Gomora kwakula ndipo tchimo lawo lafika poyipa kwambiri choncho ndikuti ndipiteko ndikaone ngati zimene achita zilidi zoyipa monga mmene madandawulo andipezera Ine. Ngati sizili choncho, ndikadziwa.” Anthu aja anatembenuka nʼkumapita, kulowera ku Sodomu, koma Abrahamu anali chiyimirire pamaso pa Yehova. Kenaka Abrahamu anasendera kufupi ndi Iye nati, “Kodi mudzawonongera kumodzi wolungama ndi woyipa? Nanga bwanji patakhala anthu makumi asanu olungama mu mzindamo? Kodi mudzawonongadi onse osausiyako mzindawo chifukwa cha anthu makumi asanu olungama omwe ali mʼmenemo? Ndithu simungachite zimenezi, kupha anthu olungama pamodzi ndi oyipa. Nʼzosatheka kuti inu nʼkufananitsa olungama ndi oyipa. Kodi woweruza wa dziko lapansi nʼkulephera kuchita chilungamo?” Yehova anati, “Nditapeza anthu makumi asanu olungama mu mzinda wa Sodomu, ndidzasiya malo onsewo osawawononga chifukwa cha iwo.” Ndipo Abrahamu anayankhulanso nati, “Tsono poti ndalimba mtima kuyankhula ndi Ambuye, ngakhale kuti ndine fumbi ndi phulusa chabe, bwanji anthu olungama atacheperapo ndi asanu pa anthu makumi asanu? Kodi mudzawononga mzinda wonse chifukwa cha asanuwo?” Iye anati, “Nditapezamo anthu 45, sindidzawuwononga.” Kenakanso anayankhula kwa Iye nati, “Bwanji atangopezekamo anthu 40 okha?” Iye anayankha, “Chifukwa cha anthu 40 amenewa, sindidzatero.” Ndipo Abrahamu anati, “Pepanitu musandipsere mtima Ambuye, koma mundilole kuti ndiyankhule. Nanga mutapezekamo anthu makumi atatu okha?” Iye anayankha, “Sindidzatero ngati atapezekamo anthu makumi atatu.” Abrahamu anati, “Tsono poti ndalimba mtima chonchi kumayankhula ndi Ambuye, bwanji atangopezeka anthu makumi awiri okha?” Iye anati, “Chifukwa cha anthu makumi awiriwo, sindidzawuwononga.” Kenaka Abrahamu anati, “Pepani Ambuye musandipsere mtima, ndingoyankhula kamodzi kokhaka basi. Bwanji atangopezeka khumi okha mʼmenemo?” Iye anayankha nati, “Chifukwa cha khumiwo, sindidzawuwononga.”

Angelo awiri aja anafika ku Sodomu madzulo ndipo Loti anali atakhala pansi pa chipata cha mzindawo. Loti atawaona, anayimirira ndi kukakumana nawo ndipo anaweramitsa mutu wake pansi mwaulemu. Iye anati, “Ambuye wanga, chonde patukirani ku nyumba kwa mtumiki wanu. Mukhoza kusambitsa mapazi anu ndi kugona usiku uno kenaka nʼkumapitirira ndi ulendo wanu mmamawa.” Iwo anati, “Ayi, tigona panja.” Koma iye anawawumiriza kwambiri kotero kuti anapita naye pamodzi ku nyumba kwake. Anawakonzera chakudya buledi wopanda yisiti ndipo anadya. Alendo aja asanapite kogona, amuna onse achinyamata ndi achikulire ochokera mbali zonse za mzinda wa Sodomu anazinga nyumba ya Loti. Iwo anayitana Loti namufunsa kuti, “Ali kuti amuna aja amene afika kuno usiku womwe uno? Atulutse, utipatse kuti tigone nawo malo amodzi.” Loti anatuluka panja kukakumana nawo natseka chitseko ndipo anati, “Ayi anzanga, musachite zinthu zoyipa zotere. Taonani, ine ndili ndi ana anga akazi awiri amene sanagonepo ndi mwamuna. Mundilole ndikutulutsireni amenewo ndipo muchite nawo zimene mungafune. Koma musachite chilichonse ndi anthuwa, pakuti iwowa ndi alendo anga ndipo ndiyenera kuwatchinjiriza.” Iwo anayankha kuti, “Tachoka apa tidutse.” Ndipo anati, “Munthu uyu anabwera kuno ngati mlendo chabe, tsono lero akufuna kuti akhale wotiweruza! Tikukhawulitsa kuposa iwowa.” Anapitiriza kumuwumiriza Loti uja nʼkumasunthira kutsogolo kuti athyole chitseko. Koma anthu aja anali mʼkatiwa anasuzumira namukokera Loti uja mʼkati mwa nyumba nʼkutseka chitseko. Kenaka anawachititsa khungu anthu amene anali panja pa nyumba aja, aangʼono ndi aakulu omwe, kuti asaone pa khomo.

Anthu awiri aja anati kwa Loti, “Kodi uli ndi wina aliyense pano, kaya ndi akamwini ako, kaya ndi ana ako aamuna kapena aakazi, kapena aliyense mu mzindamu amene ndi anzako? Atulutse onse muno, chifukwa tiwononga malo ano. Yehova waona kuti kuyipa kwa anthu a mu mzindawu kwakulitsa. Choncho watituma kuti tiwuwononge.” Choncho Loti anatuluka nayankhula ndi akamwini ake amene anali kuyembekezera kukwatira ana ake akazi nati, “Fulumirani, tiyeni tichoke pa malo ano chifukwa Yehova watsala pangʼono kuwononga mzindawu.” Koma akamwini akewo ankayesa kuti akungoselewula. Mmene kumacha, angelo aja anamufulumizitsa Loti nati, “Nyamuka, tenga mkazi wako ndi ana ako aakazi awiriwo, ndipo mutuluke mu mzindawo kuopa kuti mungaphedwe pamodzi nawo.” Koma Loti ankakayikabe. Koma Yehova anawachitira chifundo motero kuti anthu aja anagwira mkazi wake ndi ana ake aakazi aja nawatsogolera bwinobwino kuwatulutsa mu mzindawo. Atangowatulutsa, mmodzi wa angelowo anati, “Thawani kuti mudzipulumutse, musachewuke, musayime pena paliponse mʼchigwamo! Thawirani ku mapiri kuopa kuti mungawonongeke!”

Ndiye Yehova anathira sulufule wamoto wochokera kumwamba kwa Yehova pa Sodomu ndi Gomora.

Koma mkazi wa Loti anachewuka ndipo anasanduka mwala wa mchere.

Koma usiku, Mulungu anafika kwa Abimeleki kutulo nati, “Ufatu iwe chifukwa cha mkazi amene watengayu popeza ndi wokwatiwa.”

Pamene Sekemu mwana wa Hamori Mhivi, mfumu ya deralo, anamuona, anamugwirira.

Pa nthawi iyi nʼkuti ana a Yakobo atabwererako ku busa kuja. Iwo atangomva zimene zinachitika, anawawidwa mtima. Iwo anapsa mtima kwambiri kuti Sekemu nʼkuchita chonyansa choterechi mu dziko la Israeli, kumugwirira Dina, mwana wa Yakobo.

Anapha Hamori ndi Sekemu. Anakatenga Dina ku nyumba kwa Sekemu nanyamuka. Ana a Yakobo anafika kwa anthu ophedwawo ndi kututa katundu mu mzindawo chifukwa anagwiririra mlongo wawo.

Koma iwo anayankha kuti, “Pepani, nanga achite kumusandutsa mlongo wathu ngati mkazi wachiwerewere?”

Yuda atamuona anangomuyesa mkazi wadama chabe, chifukwa anadziphimba nkhope. Tsono anapita kwa mkaziyo pamphepete pa msewu paja nati, “Tabwera ndigone nawe.” Apa Yuda sankadziwa kuti mkazi uja anali mpongozi wake. Ndiye mkazi uja anamufunsa Yuda nati, “Mudzandipatsa chiyani kuti ndigone nanu?” Iye anati, “Ndidzakutumizira kamwana kambuzi ka mʼkhola mwanga.” Mkaziyo anayankha kuti, “Chabwino, ndavomera, koma mungandipatse chikole mpaka mutanditumizira mbuziyo?” Iye anati, “Ndikupatse chikole chanji?” Mkaziyo anayankha, “Mundipatse mphete yanuyo, chingwe chanucho pamodzi ndi ndodo imene ili mʼdzanja lanulo.” Choncho anazipereka kwa iye nagona naye ndipo anatenga pathupi. Kenaka Tamara anachoka, navula nsalu anadziphimba nayo ija, navalanso zovala zake za umasiye zija. Tsono Yuda anatuma bwenzi lake Mwadulamu uja ndi kamwana kambuzi kaja kuti akapereke kwa mkazi wadama uja, ndi kuti akatero amubwezere chikole chake chija. Koma atafika sanamupezepo. Anawafunsa anthu a komweko, “Kodi mkazi wadama uja amene ankakhala pambali pa msewu wa ku Enaimu, ali kuti?” Iwo anayankha, “Sipanakhalepo mkazi wa dama aliyense pano.” Choncho anabwerera kwa Yuda nati, “Sindinamupeze mkazi uja. Kuwonjeza apo, anthu a kumeneko amati, ‘Sipanakhalepo mkazi wadama pano.’ ” Pamenepo Yuda anati, “Mulekeni atenge zinthuzo zikhale zake, kuopa kuti anthu angatiseke. Ine sindinalakwe, ndinamutumizira kamwana kambuzika, koma simunamupeze.” Patapita miyezi itatu, Yuda anawuzidwa kuti, “Mpongozi wanu Tamara anachita zadama, ndipo zotsatira zake nʼzakuti ali ndi pathupi.” Yuda anati, “Kamutulutseni ndipo mukamutenthe kuti afe!” Akumutulutsa, iye anatuma mawu kwa apongozi ake. Anati, “Ndili ndi pathupi pa munthu amene ndi mwini wake wa zinthu izi. Taziyangʼanitsitsani, kodi mwini wa khoza, chingwe ndi ndodo yoyenderayi ndi yani?” Yuda anazizindikira zinthuzo ndipo anati, “Uyu ndi wolungama kuposa ine, chifukwa sindinamupereke kwa mwana wanga Sela.” Ndipo Yuda sanagone nayenso.

Patapita kanthawi, mkazi wa mbuye wake anayamba kusirira Yosefe nati, “Bwanji ugone nane!” Koma iye anakana namuwuza kuti, “Inu mukuona kuti mbuye wanga sadandaula ndi kena kalikonse mʼnyumba muno, ndipo chawo chilichonse anachiyika mʼmanja mwanga. Motero kuti palibe wina wamkulu kuposa ine mʼnyumba muno. Ndipo palibe chilichonse chimene mbuye wanga sanachipereke kwa ine kupatula inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Tsono ndingachite bwanji choyipa choterechi ndi kuchimwira Mulungu?” Ndipo ngakhale kuti iye anayankhula mawu omwewa ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, Yosefe sanalole kugona naye ngakhale kukhala naye pafupi. Tsiku lina Yosefe analowa mʼnyumbamo kukagwira ntchito zake, ndipo munalibe wina aliyense wantchito mʼnyumbamo. Mkazi uja anamugwira mkanjo Yosefe nati, “Tiye ugone nane!” Koma Yosefe anasiya mkanjo wake mʼmanja mwa mkaziyo nathawira kunja kwa nyumba.

Pamene mkazi uja anaona kuti Yosefe wamusiyira mkanjo wake mʼmanja mwake nathawira kunja kwa nyumba, iye anayitana antchito ake a mʼnyumba nati, “Taonani mwamuna wanga anabwera ndi Mhebri uyu mʼnyumba muno kuti adzagone nane. Iyeyu analowa ku chipinda kwanga kuti adzagone nane ndipo ine ndinakuwa kwambiri. Atandimva ndikukuwa, anandisiyira mkanjo wakewu nʼkuthawira kunja.” Tsono mkazi wa Potifara uja anasunga mkanjowo mpaka mbuye wake wa Yosefe atabwera ku nyumba. Tsono anamuwuza nkhaniyi nati: “Wantchito Wachihebri amene munatibweretsera uja anabwera kuti adzagone nane. Koma pamene ndinakuwa, iye anandisiyira mkanjo wake nathawira kunja.” Mbuye wake wa Yosefe atamva nkhani imene mkazi wake anamuwuza kuti, “Ndi zimene anandichitira wantchito wanu,” anapsa mtima kwambiri. Tsono iye anatenga Yosefe namuyika mʼndende mmene ankasungiramo amʼndende a mfumu. Ndipo Yosefe anakhala mʼndendemo

“Usachite chigololo.

“Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako kapena wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”

“Aliyense wogonana ndi chiweto ayenera kuphedwa.

“ ‘Munthu aliyense asagonane ndi wachibale wake. Ine ndine Yehova. “ ‘Usachititse manyazi abambo ako pogonana ndi amayi ako. Iwo ndi amayi ako. Usagonane nawo. “ ‘Usagonane ndi mkazi wa abambo ako (osakhala amayi okubala). Ukatero ukuchititsa manyazi abambo ako. “ ‘Usagonane ndi mlongo wako, mwana wamkazi wa abambo ako, kapena mwana wamkazi wa amayi ako, kaya anabadwira mʼnyumba mwanu kapena kwina. “ ‘Usagonane ndi mdzukulu wako: mwana wa mwana wako wamwamuna kapena mwana wa mwana wako wamkazi. Kutero nʼkudzichotsa ulemu. “ ‘Usagonane ndi mwana wamkazi wa mkazi wa abambo ako, amene abambo akowo anabereka; popeza ameneyo ndi mlongo wako. “ ‘Usagonane ndi mlongo wa abambo ako; popeza ameneyo ndi thupi limodzi ndi abambo ako. “ ‘Usagonane ndi mchemwali wa amayi ako chifukwa ameneyo ndi thupi limodzi ndi amayi ako. “ ‘Usachititse manyazi mchimwene wa abambo ako pogonana ndi mkazi wake popeza amenewo ndi azakhali ako. “ ‘Usagonane ndi mpongozi wako popeza ameneyo ndi mkazi wa mwana wako. Choncho usamuchititse manyazi. “ ‘Usagonane ndi mkazi wa mchimwene wako popeza potero ukuchititsa manyazi mʼbale wakoyo. “ ‘Usagonane ndi mkazi ndiponso mwana wake wamkazi. Usagonane ndi mwana wamkazi wa mwana wake wamwamuna, kapena mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi. Amenewo ndi thupi limodzi ndi mkaziyo. Kutero ndikuchita chinthu choyipa kwambiri. “ ‘Usakwatire mchemwali wa mkazi wako ndi kumagonana naye mkazi wakoyo ali moyo ngati wopikisana naye.

“ ‘Usamuyandikire mkazi kuti ugonane naye pa nthawi yake yosamba. “ ‘Usagonane ndi mkazi wa mnzako ndi kudziyipitsa naye. “ ‘Usapereke mwana wako aliyense kuti akhale nsembe yamoto kwa Moleki ndi kuyipitsa dzina la Yehova. Ine ndine Yehova. “ ‘Usagonane ndi mwamuna ngati mkazi; chimenecho ndi chinthu chonyansa. “ ‘Usagonane ndi nyama ndi kudziyipitsa nayo. Mkazi asadzipereke kwa nyama kuti agonane nayo. Chimenecho ndi chisokonezo.

“ ‘Musamuyipitse mwana wanu wamkazi pomusandutsa mkazi wachiwerewere. Mukatero dziko lidzasanduka la anthu achiwerewere ndi lodzaza ndi zoyipa.

“ ‘Ngati munthu wachita chigololo ndi mkazi wa mnzake, mwamunayo pamodzi ndi mkaziyo ayenera kuphedwa. “ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi wa abambo ake, wachititsa manyazi abambo ake. Munthuyo pamodzi ndi mkaziyo ayenera kuphedwa. Magazi awo adzakhala pa mitu pake. “ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi wa mwana wake, awiriwo ayenera kuphedwa. Iwo achita chinthu chonyansa kwambiri. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo. “ ‘Ngati munthu agonana ndi mwamuna mnzake ngati akugonana ndi mkazi, ndiye kuti onsewo achita chinthu cha manyazi. Choncho aphedwe. Magazi awo adzakhala pa mitu pawo. “ ‘Ngati munthu akwatira mkazi, nakwatiranso amayi ake, chimenecho ndi chinthu choyipa kwambiri. Mwamunayo pamodzi ndi akaziwo ayenera kutenthedwa pa moto kuti chinthu choyipa chotere chisapezekenso pakati panu. “ ‘Ngati mwamuna agonana ndi nyama, iye ayenera kuphedwa, ndipo muyeneranso kupha nyamayo. “ ‘Ngati mkazi agonana ndi nyama, aphedwe pamodzi ndi nyamayo. Mkaziyo ndi nyamayo ayenera kuphedwa, ndipo magazi awo adzakhala pa mitu pawo.

“ ‘Ngati munthu akakwatira mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake, kapena mwana wamkazi wa amayi ake, ndipo iwo nʼkugonana, ndiye kuti achita chinthu chochititsa manyazi. Onse awiri ayenera kuchotsedwa pa gulu la abale awo. Tsono popeza munthuyo wachititsa manyazi mlongo wake, adzayenera kulandira chilango. “ ‘Ngati munthu agonana ndi mkazi pa nthawi yake yosamba, ndiye kuti wavula msambo wake, ndipo mkaziyo wadzivulanso. Onse awiri achotsedwe pakati pa anthu anzawo. “ ‘Musagonane ndi mchemwali wa amayi anu kapena abambo anu, pakuti kutero ndi kuchititsa manyazi mʼbale wanu. Nonse mudzalipira mlandu wanu. “ ‘Ngati munthu agonana ndi azakhali ake, munthuyo wachititsa manyazi a malume ake. Onse adzalipira mlandu wawo. Onsewo adzafa wopanda mwana. “ ‘Munthu akakwatira mkazi wa mchimwene wake ndiye kuti wachita chinthu chonyansa. Wachititsa manyazi mʼbale wakeyo. Onse awiriwo adzakhala wopanda mwana.

“ ‘Asakwatire akazi amene adzidetsa ndi chiwerewere kapena akazi amene amuna awo awasudzula, chifukwa ansembe ndi oyera pamaso pa Mulungu wawo. Iwo akhale oyera chifukwa amapereka nsembe kwa Mulungu wanu. Muziwaona kuti ndi oyera, popeza Ine Yehova amene ndimawayeretsa ndine woyera, nawonso akhale oyera. “ ‘Ngati mwana wamkazi wa wansembe adziyipitsa pochita zachiwerewere, ndiye kuti iye akuchititsa manyazi abambo ake; mwanayo atenthedwe pa moto.

Asakwatire mkazi wamasiye, mkazi wosudzulidwa, kapena mkazi wachiwerewere, koma akwatire namwali wosadziwa mwamuna pakati pa anthu a mtundu wake,

“Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati mkazi wa munthu wina ayenda njira yosayenera nakhala wosakhulupirika kwa mwamuna wake, nakagonana ndi mwamuna wina koma mwamuna wake wosadziwa, ndipo palibe wina aliyense wadziwa za kudzidetsa kwake (pakuti palibe mboni yomuneneza chifukwa sanagwidwe akuchita),

“ ‘Limeneli ndiye lamulo la nsanje pamene mkazi wayenda njira yoyipa ndi kudzidetsa ali pa ukwati ndi mwamuna wake,

Kenaka mwamuna wina wa ku Israeli anabweretsa ku banja lake mkazi wa Chimidiyani pamaso pa Mose ndi anthu onse a Israeli pamene ankalira pa khomo la tenti ya msonkhano.

“Usachite chigololo.

“Usasirire mkazi wa mnzako. Usasirire nyumba ya mnzako kapena munda wake, wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”

Akazi asavale zovala za amuna, kapena mwamuna kuvala zovala za akazi, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa ndi aliyense wochita izi.

Koma ngati zomunenerazo ndi zoona, ndipo kuti chitsimikizo cha unamwali wa mtsikanayo sichinapezeke, iyeyu ayenera kumutengera pa khomo pa abambo ake pamene anthu a mu mzinda wake akamuphere ndi miyala. Iyeyo wachita chinthu chochititsa manyazi mu Israeli pochita chiwerewere akanali pa khomo pa abambo ake. Muyenera kuchotsa zoyipa pakati panu.

Ngati munthu apezeka akugona ndi mkazi wa mwini wake, ayenera kuphedwa munthuyo pamodzi ndi mkazi yemwe wagona nayeyo. Muyenera kuchotsa zoyipa mu Israeli.

Ngati munthu mu mzinda akumana ndi mkazi yemwe anachita kale chinkhoswe nagona naye, muwatengere awiriwo ku chipata cha mzinda ndi kuwapha ndi miyala. Aphedwe chifukwa mtsikanayo anali pafupi ndi anthu ndipo sanakuwe kuti ena amuthandize ndipo mwamunayo chifukwa anayipitsa mkazi wa mwini. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.

Koma ngati munthu akumana ndi mkazi kutchire yemwe anachita kale chinkhoswe namugwiririra, mwamuna yekhayo ndiye woyenera kuphedwa. Mtsikanayo musamuchite chilichonse, palibe tchimo limene wachita loti ayenera kuphedwa. Mlandu uwu ufanana ndi wa munthu amene alimbana ndi kupha mnzake woyandikana naye, pakuti mwamunayo anamupeza mtsikanayo kutchire, ndipo ngakhale mtsikana wachinkhosweyo anakuwa, panalibe anamulanditsa.

Ngati munthu apezana ndi namwali woti sanachite chinkhoswe, namugwiririra, munthuyo nʼkupezeka, ayenera kuwalipira abambo ake a namwaliyo ndalama za siliva makumi asanu. Iye ayenera kumukwatira mkaziyo chifukwa wamuyipitsa, ndipo sadzamulekanso moyo wake wonse.

Munthu asakwatire mkazi wa abambo ake pakuti ayenera kuchitira ulemu pogona pa abambo ake.

Aliyense wobadwa mʼbanja losavomerezeka, kapena mdzukulu wake wina aliyense, ngakhale mibado khumi pambuyo pake, asalowe mu msonkhano wa Yehova.

Pasapezeke Mwisraeli wamwamuna kapena wamkazi wochita chiwerewere ku Nyumba ya Mulungu. Musabweretse malipiro a wachiwerewere wamkazi kapena wamwamuna Mʼnyumba ya Yehova Mulungu wanu kudzapereka za malumbiro aliwonse, chifukwa Yehova Mulungu wanu amadana ndi zimenezi.

“Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mkazi wa abambo ake pakuti iye sachitira ulemu pogona pa abambo ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

“Ndi wotembereredwa munthu amene achita chigololo ndi nyama ya mtundu uli wonse.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

“Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa abambo ake kapena mwana wamkazi wa amayi ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

“Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi apongozi ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

Tsiku lina Samsoni anapita ku Gaza. Kumeneko anaonako mkazi wachiwerewere, ndipo analowa mu nyumba yake.

Pa nthawi imeneyo ku Israeli kunalibe mfumu. Mlevi wina ankakhala kutali ku dziko lamapiri la Efereimu. Iyeyu anatenga mzikazi wa ku Betelehemu, mʼdziko la Yuda. Tsiku lina mzikazi uja anakwiyira mwamuna wake ndipo anamuchokera kupita kwa abambo ake ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Anakakhala kumeneko miyezi inayi.

Pamene ankadya mosangalala, anangoona anthu ena achabechabe a mu mzindawo azungulira nyumba ija nʼkumamenya chitseko. Tsono anawuza mwini nyumbayo, munthu wokalamba uja kuti, “Mutulutse munthu amene wabwera mʼnyumba yakoyu kuti tigone naye.” Koma mwini nyumba uja anatuluka ku bwalo nawawuza kuti, “Ayi, abale anga musachite zoyipa zotere. Popeza munthu uyu walowa mʼnyumba mwanga muno, musachite chinthu chonyansa chotere. Onani, pano pali mwana wanga wamkazi wosadziwa mwamuna pamodzi ndi mzikazi wa mlendoyu. Ndikutulutsirani amenewa tsopano ndipo atengeni ndi kuchita nawo chomwe chikukomerani. Koma musachite chinthu chonyansa ndi munthuyu.” Koma anthuwo sanafune kumumvera. Choncho mlendo uja anagwira mzikazi wake namutulutsa kuja kumene kunali iwo. Tsono iwowo anagona naye ndi kuchita naye zonyansa usiku wonse mpaka mmawa. Mʼbandakucha anamulola kuti apite. Ndipo mmawa kukucha mzikazi uja anabwerera nakagwa pansi pa khomo pa nyumba imene mwamuna wake anali, ndipo anakhala pomwepo mpaka kunayera. Mwamuna wake anadzuka mʼmamawa, natsekula chitseko cha nyumba kuti atuluke ndi kumapita. Koma anangoona mzikazi wake uja ali thapsa pa khomo la nyumbayo, manja ake ali pa khonde. Iye anati kwa mkaziyo, “Dzuka tizipita.” Koma sanayankhe kanthu. Kenaka anamukweza pa bulu wake ndipo ananyamuka kumapita kwawo. Atafika ku nyumba yake, anatenga mpeni, nagwira mzikazi wake uja ndi kuduladula thupi lake nthuli khumi ndi ziwiri. Kenaka anazitumiza ku zigawo zonse za Israeli. Aliyense amene anaona zimenezi ankanena kuti, “Zoterezi sizinaonekepo kuyambira pamene Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ganizirani bwino chinthu chimenechi ndipo tiwuzeni zoyenera kuchita!”

Mʼmafuko onse a Aisraeli tidzasankha anthu khumi pa anthu 100 aliwonse: ndiye kuti anthu 100 pa anthu 1,000 aliwonse kapena anthu 1,000 pa anthu 10,000 aliwonse. Anthu amenewa adzasonkhanitsa zakudya za ankhondo, ndipo ankhondowo adzapita kukalipsira anthu a ku Geba mʼdziko la Benjamini chifukwa chochita chinthu chonyansa chotere mʼdziko la Israeli.” Choncho anthu a ku Israeli anasonkhana pamodzi nagwirizana chimodzi, kukalimbana ndi mzindawo.

Tsono Eli anakalamba kwambiri. Iye ankamva zonse zimene ana ake aamuna ankachitira Aisraeli onse, ndiponso kuti ankagona ndi akazi pa chipata cha tenti ya msonkhano.

Tsiku lina cha kumadzulo Davide anadzuka pa bedi lake ndipo ankayenda pamwamba pa nyumba yake. Ali pa dengapo anaona mkazi akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwambiri. Ndipo Davide anatuma munthu wina kuti akafufuze za iye. Munthuyo anati, “Kodi uyu si Batiseba, mwana wa Eliamu, mkazi wa Uriya Mhiti?” Ndipo Davide anatumiza amithenga kwa iye kukamuyitana. Batiseba anabwera kwa Davide ndipo anagona naye. (Nʼkuti mkaziyu atayeretsedwa ku masiku ake osamba). Kenaka anabwerera ku nyumba yake. Mkaziyo anakhala woyembekezera ndipo anatumiza mawu kwa Davide kunena kuti, “Ine ndine woyembekezera.”

Nʼchifukwa chiyani unanyoza mawu a Yehova pochita chimene chili choyipa pamaso pake? Iwe unakantha Uriya Mhiti ndi lupanga ndipo unatenga mkazi wake kukhala wako. Uriyayo unamupha ndi lupanga la Aamoni. Ndipo tsopano lupanga silidzachoka pa nyumba yako, chifukwa unandinyoza ine ndi kutenga mkazi wa Uriya Mhiti kukhala wako.’ “Yehova akuti, ‘Ine ndidzabweretsa tsoka pa iwe lochokera mʼbanja lako. Ndidzatenga akazi ako iwe ukuona ndi kuwapereka kwa wina amene ali pafupi nawe, ndipo iye adzagona ndi akazi ako masanasana Aisraeli onse akuona. Iwe unachita zimenezi mwamseri koma Ine ndidzachita izi masanasana Aisraeli onse akuona.’ ”

Koma atabweretsa kwa iye kuti adye, anamugwira ndipo anati, “Bwera ugone nane, iwe mlongo wanga.” Tamara anati kwa iye, “Ayi mlongo wanga! Usandikakamize. Zotere siziyenera kuchitika mu Israeli! Usachite chinthu choyipa chotere. Kodi ukuganiza bwanji za ine? Kodi manyazi anga ndidzawachotsa bwanji? Ndipo nanga iweyo? Udzakhalatu monga mmodzi mwa zitsiru zoyipitsitsa muno mu Israeli. Chonde kapemphe kwa mfumu. Sadzakuletsa kuti undikwatire.” Koma sanamvere zimene amanena Tamara ndipo popeza anali wamphamvu kuposa Tamarayo, iye anamugwirira.

Komatu Mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo ndipo kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, analinso ndi akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni, ndi Ahiti. Akazi amenewa anali ochokera ku mitundu ija imene Yehova anawuza Aisraeli kuti, “Simuyenera kudzakwatirana nawo amenewa, chifukwa ndithu, amenewa adzatembenuza mitima yanu kuti mutsatire milungu yawo.” Komabe Solomoni anawakonda kwambiri akazi amenewa. Iye anali ndi akazi 700 ochokera ku mabanja achifumu ndi azikazi 300 ndipo akaziwo anamusocheretsa. Solomoni atakalamba, akazi akewo anakopa mtima wake kuti atsatire milungu ina, ndipo sanatsatire Yehova Mulungu wake ndi mtima wodzipereka, monga unalili mtima wa Davide abambo ake. Pakuti iye ankapembedza Asitoreti, mulungu wamkazi wa Asidoni, ndiponso Moleki mulungu wonyansa wa Aamoni. Kotero Solomoni anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Sanatsatire Yehova kwathunthu monga anachitira Davide abambo ake.

Mʼdzikomo munalinso amuna ochita zachiwerewere mwa chipembedzo. Anthu ankachita zonyansa zonse za anthu a mitundu ina imene Yehova anayipirikitsa asanafike Aisraeli.

Iye anachotsa mʼdzikomo amuna onse ochita zadama pochita chipembedzo chawo ndiponso anachotsa mafano onse amene makolo ake anawapanga.

Iye anachotsa mʼdzikomo amuna onse ochita zachiwerewere mwa chipembedzo amene anatsalira pa nthawi ya ulamuliro wa Asa, abambo ake.

Iye anagwetsanso tinyumba ta ochita zachiwerewere, timene tinali mʼNyumba ya Yehova, kumene akazi ankalukirako mikanjo yovala popembedza Asera.

“Ndinachita pangano ndi maso anga kuti sindidzapenya namwali momusirira.

Nzeruyo idzakupulumutsanso kwa mkazi wachigololo; kwa mkazi wachilendo woyankhula moshashalika, amene wasiya mwamuna wa chitsikana wake ndi kuyiwala pangano limene anachita pamaso pa Mulungu wake.

Pakuti mkazi wachigololo ali ndi mawu okoma ngati uchi. Zoyankhula zake ndi zosalala ngati mafuta, koma kotsirizira kwake ngowawa ngati ndulu; ngakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.

Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukukopeka ndi mkazi wachigololo? Bwanji ukukumbatira mkazi wachilendo?

kukupulumutsa kwa mkazi wadama, zimenezi zidzakutchinjiriza kwa mkazi wadama, ndi kukuthandiza kuti usamvere mawu oshashalika a mkazi wachiwerewere. Mu mtima wako usakhumbire kukongola kwake, asakukope ndi zikope zake, paja mkazi wadama amakusandutsa kukhala ngati nyenyeswa za buledi ndipo mkazi wa mwini wake amasokonezeratu moyo wako wonse. Kodi munthu angathe kutenga moto zovala zake osapsa? Kodi munthu angathe kuyenda pa makala amoto mapazi ake osapserera? Ndizo zimachitikira munthu amene amagonana ndi mkazi wa munthu wina. Aliyense wokhudza mkazi wotere adzalangidwa.

Munthu wochita chigololo ndi wopanda nzeru. Wochita zimenezi amangodziwononga yekha.

Zidzakuteteza kwa mkazi wachigololo ndiponso zidzakuthandiza kusamvera mawu oshashalika a mkazi wachilendo. Tsiku lina pa zenera la nyumba yanga ndinasuzumira pa zenera. Ndinaona pakati pa anthu opusa, pakati pa anyamata, mnyamata wina wopanda nzeru. Iye ankayenda njira yodutsa pafupi ndi nyumba ya mkaziyo, kuyenda molunjika nyumba ya mkaziyo. Inali nthawi yachisisira madzulo, nthawi ya usiku, kuli mdima. Ndipo mkaziyo anadzakumana naye, atavala ngati munthu wachiwerewere wa mtima wonyenga.

Ndi mawu ake onyengerera amamukakamiza mnyamatayo; amukopa ndi mawu ake oshashalika. Nthawi yomweyo chitsiru chimamutsatira mkaziyo ngati ngʼombe yopita kukaphedwa, monga momwe mbawala ikodwera mu msampha, mpaka muvi utalasa chiwindi chake, chimakhala ngati mbalame yothamangira mʼkhwekhwe, osadziwa kuti moyo wake uwonongeka. Tsono ana inu, ndimvereni; mvetsetsani zimene ndikunena. Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyu; musasochere potsata njira zake. Paja iye anagwetsa anthu ambiri; wapha gulu lalikulu la anthu. Nyumba yake ndi njira yopita ku manda, yotsikira ku malo a anthu akufa.

Chilungamo cha anthu oyera mtima chimawapulumutsa, koma anthu onyenga adzagwidwa ndi zilakolako zawo zomwe.

Pakamwa pa mkazi wachigololo pali ngati dzenje lozama; amene Yehova wamukwiyira adzagwamo.

Paja mkazi wachiwerewere ali ngati dzenje lozama; ndipo mkazi woyendayenda ali ngati chitsime chopapatiza. Amabisala ngati mbala yachifwamba, ndipo amuna amakhala osakhulupirika chifukwa cha iyeyu.

Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa abambo ake, koma woyenda ndi akazi achiwerewere amasakaza chuma chake.

Umu ndi mʼmene mkazi amachitira atachita chigololo: Atatha kudya ndi kupukuta pakamwa pake iye amanena kuti “Sindinachite kalikonse kolakwa.”

Ndinapeza kanthu kowawa kupambana imfa, mkazi amene ali ngati khoka, amene mtima wake uli ngati khwekhwe, ndipo manja ake ali ngati maunyolo. Munthu amene amakondweretsa Mulungu adzathawa mkaziyo, koma mkaziyo adzakola munthu wochimwa.

Taonani momwe mzinda wokhulupirika wasandukira wadama! Mzinda umene kale unali wodzaza ndi chiweruzo cholungama; mu mzindamo munali chilungamo, koma tsopano muli anthu opha anzawo!

“Bwerani kuno, anthu ochita zoyipa, inu muli ngati zidzukulu za mkazi wachigololo ndi wadama!

“Ngati munthu asudzula mkazi wake ndipo mkaziyo nʼkuchoka nakakwatiwa ndi mwamuna wina, kodi mwamuna woyambayo angathe kumutenganso mkaziyo? Kodi atatero sindiye kuti dzikolo layipitsidwa kwambiri? Koma iwe Israeli wachita zadama ndi zibwenzi zambiri. Komabe bwerera kwa ine,” akutero Yehova. “Tayangʼana ku zitunda zowuma. Kodi aliponso malo ena amene iwe sunachitepo zadama? Iwe unkakhala mʼmbali mwa njira kumadikira zibwenzi zako, ngati Mluya wobisalira anthu mʼchipululu. Inu mwayipitsa dziko ndi zadama zanu ndi ntchito zanu zoyipa. Nʼchifukwa chake Yehova wayimitsa mvula, ndipo mvula ya nthawi ya masika sinagwe. Komabe uli ndi maonekedwe a mkazi wachiwerewere; ndipo sukuchita manyazi ndi pangʼono pomwe.

Pa nthawi ya Mfumu Yosiya Yehova anandiwuza kuti, “Kodi waona zomwe Israeli wosakhulupirika uja wachita? Anakwera pa phiri lililonse lalitali ndi kupita pa tsinde pa mtengo uliwonse wogudira kukapembedza. Choncho anachita za chiwerewere kumeneko. Ndinaganiza kuti atachita zonsezi, adzabwerera kwa Ine, koma sanabwerere, ndipo mlongo wake wosakhulupirika uja, Yuda, anaziona zimenezi. Anaona kuti ndinasudzula Israeli wosakhulupirikayo ndi kumupirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanaope, nayenso anapita kukachita chigololo.

Koma monga mkazi wosakhulupirika amasiya mwamuna wake, momwemonso inu mwakhala osakhulupirika kwa Ine, inu fuko la Israeli,” akutero Yehova.

Yehova akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji ndi zimene mwachita? Ana anu andisiya Ine ndipo amapembedza milungu imene si milungu konse. Ine ndinawapatsa zonse zimene ankasowa, komabe iwo anachita chigololo namasonkhana ku nyumba za akazi achiwerewere. Monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa, aliyense wa iwo ankathamangira mkazi wa mnzake.

“Kodi inu muziba ndi kupha, kuchita chigololo ndi kulumbira monama, kufukiza lubani kwa Baala ndi kutsatira milungu ina imene simunayidziwe,

Ndaona zonyansa zanu: zigololo zanu, kutchetcherera kwanu ndi ziwerewere zanu, zochitika pa mapiri ndi mʼminda. Tsoka iwe Yerusalemu! Udzakhala wosayeretsedwa pa zachipembedzo mpaka liti?”

Ndipo pakati pa aneneri a ku Yerusalemu ndaonapo chinthu choopsa kwambiri: amachita chigololo, amanena bodza ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoyipa. Choncho palibe amene amasiya zoyipa zake. Kwa Ine anthu onsewa ali ngati a ku Sodomu ndi Gomora.”

Pakuti anthu amenewa achita zoyipa kwambiri mu Israeli; achita chigololo ndi akazi a eni ake ndipo mʼdzina langa ankayankhula zabodza zimene sindinawawuze kuti atero. Ine ndikuzidziwa ndipo ndine mboni ya zimenezi,” akutero Yehova.

Amayi agwiriridwa mu Ziyoni, ndi anamwali mʼmizinda ya Yuda.

“ ‘Koma iwe unatama kukongola kwako ndipo unayamba kuchita zadama chifukwa cha kutchuka kwako. Unkachita chigololo ndi kumangodzipereka kwa aliyense wodutsa ndipo kukongola kwako kunakhala kwake. Unatenga zovala zako zina nukakongoletsera malo opembedzerako mafano, ndipo kumeneko umachitirako zigololo. Zinthu izi sizinachitikepo nʼkale lomwe ndipo sizidzachitikanso. Unatenga zokongoletsera zopangidwa ndi golide ndi siliva zimene ndinakupatsa ndipo unadzipangira wekha mafano aamuna amene unkachita nawo za dama.

“ ‘Ndipo unatenga ana ako aamuna ndi ana aakazi amene unandibalira ine, ndipo unakawapereka ngati nsembe kwa mafanowo. Kodi zigololo zakozo sizinakukwanire kuti uziphanso ana anga ndi kuwapereka ngati nsembe kwa mafano akowo? Chifukwa cha zadama zako zonyansazi unayiwala masiku a ubwana wako pamene unali wamaliseche, wausiwa ndiponso womangovivinizika mʼmagazi.

Pa msewu uliwonse wamanga nsanjazo. Motero wanyazitsa kukongola kwako podzipereka kwa aliyense amene adutsapo. Umachita chigololo ndi Aigupto, anthu adama oyandikana nawe. Choncho unandikwiyitsa chifukwa unachulukitsa za dama zako. Nʼchifukwa chake ndinatambasula dzanja langa kukukantha ndi kuchepetsa dziko lako. Ndinakupereka kwa adani ako, Afilisti amene amayipidwa ndi makhalidwe ako onyansa. Chifukwa cha chilakolako chako unachitanso zadama ndi Aasiriya. Ngakhale unachita nawo chigololo koma sunakhutitsidwebe. Choncho unapitirirabe kuchita chigololo ndi Ababuloni, anthu a mʼdziko lokonda zamalonda. Ngakhale unachita izi, komabe sunakhutitsidwe.

“ ‘Ambuye Yehova akuti: Mtima wako ndi wofowoka kwambiri chifukwa unachita zonsezo monga ngati mkazi wopanga manyazi. Unamanga nsanja pa msewu uliwonse. Unamanganso kachisi pabwalo lililonse. Komabe sunachite ngati mkazi wadama chifukwa unakana malipiro. “ ‘Iwe mkazi wachigololo! Umakonda amuna achilendo kupambana mwamuna wakowako! Amuna ndiwo amapereka malipiro kwa mkazi wadama. Koma iwe ndi amene ukupereka mphatso kwa zibwenzi zako zonse. Choncho umazinyengerera kuti zizibwera kwa iwe kuchokera mbali zonse kudzagona nawe. Chotero iwe ukusiyana ndi akazi ena achigololo, pakuti palibe amene ankakunyengerera kuti uchite naye chigololo. Iweyo ndiye unkapereka ndalama osati ena kukupatsa ndalama ayi. Motero unalidi wosiyana kwambiri ndi akazi ena.

“ ‘Tsono mkazi wachigololo iwe, imva mawu a Yehova! Ambuye Yehova akuti, popeza unavula ndi kuonetsa umaliseche wako mopanda manyazi, unachita chigololo ndi zibwenzi zako pamodzi ndi mafano ako onyansa, komanso popeza unapereka ana ako kuti aphedwe ngati nsembe zoperekedwa kwa mafano, nʼchifukwa chake Ine ndidzasonkhanitsa zibwenzi zako zonse, zimene unkasangalala nazo, amene unkawakonda ndi amene unkawada. Ndidzawasonkhanitsa motsutsana nawe kuchokera ku madera onse okuzungulira ndipo Ine ndidzakuvula pamaso pawo, ndipo iwo adzaona umaliseche wako wonse. Ine ndidzakulanga monga mmene amalangira akazi amene amachita chigololo ndiponso opha anthu. Chifukwa cha ukali wanga ndi nsanje yanga, ndidzakhetsa magazi ako mokwiya kwambiri.

Adzatentha nyumba zako ndi kukulanga iwe pamaso pa akazi ambiri. Ndidzathetsa chigololo chako, ndipo sudzalipiranso zibwenzi zako. Ukali wanga udzalekera pamenepo ndipo sindidzakuchitiranso nsanje. Ndidzakhala chete osakwiyanso. “ ‘Popeza sunakumbukire masiku a ubwana wako koma unandikwiyitsa ndi zinthu zonsezi, Ine ndidzakubwezera ndithu chilango pamutu pako chifukwa cha zimene wachita, akutero Ambuye Yehova. Paja unawonjezera chigololo pa machitidwe ako onyansa.

Mwa iwe muli anthu onenera anzawo zabodza kuti aphedwe. Mwa iwe mulinso amene amadyera zansembe pa mapiri a chipembedzo. Enanso amachita zonyansa. Mwa iwe muli ena ogonana ndi akazi a abambo awo, muli enanso amene amavuta akazi pamene ali woyipitsidwa ndi msambo. Ena amachita chigololo ndi akazi a anzawo, ndipo ena, mopanda manyazi, amayipitsa mkazi wa mwana wawo. Palinso ena amene amayipitsa alongo awo, ana aakazi a abambo awo.

Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, panali atsikana awiri ana a mayi mmodzi. Iwo ankachita za chiwerewere ku Igupto. Za chiwerewerezo anayamba ali achichepere. Kumeneko anthu ankangowasisita pa chifuwa ndi kuwagwiragwira mawere awo aja. Wamkulu dzina lake anali Ohola, ndipo mngʼono wakeyo anali Oholiba. Ine ndinawakwatira ndipo anabereka ana aamuna ndi ana aakazi. Ohola ndiye Samariya, ndipo Yerusalemu ndiye Oholiba. “Ohola anachita zachiwerewere ngakhale anali mkazi wanga; ndipo iye anakangamira abwenzi ake a ku Asiriya. Amenewo anali asilikali ovala zibakuwa zamlangali, abwanamkubwa ndiponso atsogoleri a nkhondo. Onsewo anali anyamata osiririka ndipo ankakwera pa akavalo. Ohola anachita zachiwerewere ndi onsewa, anthu otchuka a ku Asiriya. Iye anadziyipitsa ndi mafano a munthu aliyense amene anagona naye. Iye sanaleke za chiwerewere zimene anaziphunzira ku Igupto. Paja akanali mtsikana anyamata ankagona naye. Iwo ankamusisita mawere akanali anthete nachita naye zachiwerewere. “Nʼchifukwa chake Ine ndinamupereka kwa achikondi ake, Asiriya, amene iye ankawalakalaka. Iwowa anamuvula, namulanda ana ake aamuna ndi aakazi ndipo anamupha ndi lupanga. Ndipo atalangidwa choncho, iye anasanduka chinthu chonyozeka pakati pa akazi. “Mphwake Oholiba anaona zimenezi natengerako. Koma iye anachita zachiwerewere kuposa mkulu wake. Iyenso anakangamira Asiriya, abwanamkubwa, olamulira asilikali, ankhondo ovala zovala zonse za nkhondo ndi okwera pa akavalo. Onsewa anali anyamata osiririka. Ndinaona kuti iyenso anadziyipitsa; ndipo onse awiriwo anatsata njira imodzi. “Koma Oholiba uja anachita chigololo kopitirira mkulu wake. Iye anaona zithunzi za amuna pa khoma, zithunzi za Ababuloni zolembedwa ndi inki yofiira, atamanga malamba mʼchiwuno mwawo ndi kuvala nduwira pa mitu yawo. Onse amaoneka ngati atsogoleri a magaleta a Ababuloni, mbadwa za ku Kaldeya. Oholiba atangowaona, anawalakalaka ndipo anatuma amithenga ku Kaldeya kukawayitana. Ndipo Ababuloni anabwera nʼkudzagona naye. Choncho mwa chilakolako chawo anamuyipitsa. Koma atamuyipitsa choncho, iye ananyansidwa nawo. Iye atachita chiwerewere chake poyera ndi kuonetsa umaliseche wake, Ine ndinamuchokera monyansidwa monga mmene ndinachitira ndi mʼbale wake. Koma anachitabe zachiwerewere osalekeza. Ankakumbukira masiku a ubwana wake pamene ankachita za chiwerewere mʼdziko la Igupto. Kumeneko iye ankalakalaka zibwenzi zake, amene ziwalo zawo zinali ngati za abulu ndipo kutentha kwawo kunali ngati kwa akavalo. Motero, iwe Oholiba unafuna kuchitanso zadama monga unkachitira ku Igupto pamene unali mtsikana. Nthawi imene ija ankakusisita pa chifuwa ndi kugwiragwira mawere ako osagwa aja.

Motero ndidzathetsa zonyansa zako ndi zachigololo zomwe unaziyamba ku Igupto. Choncho sudzalakalaka za ku Igupto kapena kuzikumbukiranso. “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndikukupereka mʼmanja mwa amene amadana nawe, kwa iwo amene unawafulatira moyipidwa nawo. Adzachita nawe mwachidani. Adzakulanda zonse zimene unagwirira ntchito. Adzakusiya wamaliseche ndiponso wausiwa. Kuyipa kwa makhalidwe ako achiwerewere kudzakhala pammbalambanda. Zonyansa zako ndi chiwerewere chako, zabweretsa izi pa iwe chifukwa unachita zonyansa ndi anthu a mitundu ndi kudziyipitsa ndi mafano awo.

“Chifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza wandiyiwala Ine ndi kundifulatira, chomwecho uyenera kulangidwa chifukwa cha zonyansa zako ndi chiwerewere chako.” Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? Tsono uwayimbe mlandu chifukwa cha machitidwe awo onyansa. Iwo achita chigololo ndipo anapha anthu. Anachita chigololo popembedza mafano awo. Ngakhale ana amene anandiberekera Ine anawapereka kwa mafanowo ngati chakudya chawo. Anachitanso izi: Iwo anayipitsa malo anga opatulika ndi kudetsa masabata anga. Atapereka ana awo kwa mafano, tsiku lomwelo anakalowanso mʼNyumba yanga yopatulika ndi kuyipitsamo. Izi ndi zimene anachita mʼNyumba mwanga.

“Iwo anatuma amithenga kukayitana amuna a ku mayiko akutali. Anthuwo atabwera, abale awiri aja anasambasamba, kudzola utoto wodzikometsera kumaso, kenaka ndi kuvala zovala zamakaka. Anakhala pa bedi lokongola ndipo patsogolo pawo panali tebulo pamene munayikapo lubani ndi mafuta. Zonse zowapatsa Ine. “Mfuwu wa chigulu cha anthu unamveka. Anthu oledzera ochokera ku chipululu anabwera pamodzi ndi anthu wamba ndipo anaveka akaziwo zibangiri kumanja ndi zipewa zaufumu zokongola ku mutu. Ndipo ine ndinati za mkazi wotheratu ndi chigololoyo, ‘Tsono asiyeni kuti achite naye monga wachiwerewere, pakuti ichi ndi chimene iye ali basi.’ Tsono anapita kwa iwo monga mmene anthu amapitira kwa mkazi wadama. Momwemo anapita kwa Ohola ndi kwa Oholiba kukachita nawo zadama. Koma anthu olungama adzawazenga anthuwa mlandu wa chigololo ndi wa kupha anthu. Ndi iwodi anthu achigololo ndiponso mʼmanja mwawo muli magazi.

“Motero Ine ndidzathetsa zachigololo mʼdzikomo, ndipo akazi onse adzatengapo phunziro kuti asadzachite zachigololo monga za iwowo. Ndidzawalanga chifukwa cha ntchito zawo za dama ndipo adzazunzika chifukwa cha tchimo lawo lopembedza mafano. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.”

Yehova atayamba kuyankhula kudzera mwa Hoseya, Yehova anati kwa Hoseyayo, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubereke naye ana mʼchiwerewere chake pakuti anthu a mʼdziko muno achimwa pochita chigololo choyipitsitsa, posiya Yehova.”

“Dzudzulani amayi anu, adzudzuleni iwo, pakuti si mkazi wanga, ndipo ine sindine mwamuna wake. Iyeyo achotse maonekedwe adama pa nkhope yake, ndi kusakhulupirika pa mawere ake. Akapanda kutero ndidzamuvula, ndipo adzakhala wamaliseche monga tsiku limene anabadwa; ndidzamuwumitsa ngati chipululu, adzakhala ngati dziko lopanda madzi, ndi kumupha ndi ludzu. Sindidzaonetsa chikondi changa pa ana ake, chifukwa ndi ana a mʼchiwerewere. Amayi awo akhala akuchita zachiwerewere ndipo anawabereka anawo akuchita zinthu zochititsa manyazi. Iwo anati, ‘Ine ndidzatsatira zibwenzi zanga, zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi, ubweya ndi thonje, mafuta ndi chakumwa.’

Muli kutemberera kokha, kunama ndi kupha. Kuba ndi kuchita chigololo; machimo achita kunyanya ndipo akungokhalira kuphana.

za anthu anga. Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo ndipo ndodo yawo yamtengo imawayankha. Mzimu wachiwerewere umawasocheretsa; iwo sakukhulupirika kwa Mulungu wawo. Amapereka nsembe pamwamba pa mapiri ndi kufukiza lubani pa zitunda, pa tsinde pa mtengo wa thundu, mnjale ndi mkundi, pamene pali mthunzi wabwino. Nʼchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere ndipo akazi a ana anu akuchita zigololo. “Ine sindidzalanga ana anu aakazi pamene iwo adzachita zachiwerewere, kapena akazi a ana anu pamene adzachita zigololo. Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere, ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi achiwerewere a ku malo opembedzerako. Anthu amene alibe nzeru adzawonongeka ndithu!

Ndimadziwa zonse za Efereimu; Aisraeli ndi osabisika kwa Ine. Efereimu wayamba tsopano kuchita zachiwerewere; Israeli wadziyipitsa. “Ntchito zawo siziwalola kubwerera kwa Mulungu wawo. Mʼmitima mwawo muli mzimu wachiwerewere; Iwo sadziwa Yehova.

Iwe Israeli, usakondwere; monga imachitira mitundu ina. Pakuti wakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wako; umakonda malipiro a chiwerewere pa malo aliwonse opunthira tirigu.

Anagawana anthu anga pochita maere ndipo anyamata anawasinthanitsa ndi akazi achiwerewere; anagulitsa atsikana chifukwa cha vinyo kuti iwo amwe.

Zonsezi ndi chifukwa cha zilakolako za mkazi wachiwerewere, wokopa anthu uja, mkazi wochita zamatsenga, amene anakopa mitundu ya anthu ndi zachiwerewere zake, ndiponso anthu a mitundu ina ndi zaufiti zake.

Inu mukufunsa kuti, “Chifukwa chake nʼchiyani?” Chifukwa chake nʼchakuti Yehova ndi mboni ya pangano limene unachita ndi mkazi wa unyamata wako, chifukwa sunakhulupirike kwa iye, ngakhale kuti iyeyo ndiye mnzako, ndi mkazi wako mwapangano. Kodi Yehova sanawalenge iwo ngati munthu mmodzi? Ndi ake mʼthupi ndi mu mzimu. Nʼchifukwa chiyani ali mmodzi? Chifukwa Iye amafuna ana opembedza Mulungu. Motero samala moyo wako wauzimu, ndipo usakhale wosakhulupirika kwa mkazi wa unyamata wako. Yehova Mulungu wa Israeli akuti, “Ndimadana ndi kulekana ukwati. Ndimadana ndi munthu wochita zankhanza zotere kwa mkazi wake,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. Choncho tetezani mzimu wanu, ndipo musakhale osakhulupirika.

Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Tsono ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni. Mosataya nthawi ndidzanena mawu otsutsa mfiti, achigololo, a umboni wonama, amene salipira bwino antchito awo, amene amazunza akazi ndi ana amasiye, amene saweruza alendo mwachilungamo, komanso amene sandiopa Ine.”

“Munamva kuti kunanenedwa kuti, ‘Usachite chigololo.’ Koma Ine ndikuwuzani kuti aliyense woyangʼana mkazi momusirira wachita naye kale chigololo mu mtima mwake.

Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake pa chifukwa china chilichonse osati chifukwa cha chiwerewere, akumuchititsa mkaziyo chigololo ndipo aliyense wokwatira mkaziyo, akuchitanso chigololo.

Pakuti mu mtima mumatuluka maganizo oyipa, zakupha, zachigololo, zadama, zakuba, zaumboni wonama ndi zachipongwe.

Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chiwerewere nakakwatira mkazi wina, achita chigololo.”

Khalani maso ndi kupemphera kuti musagwe mʼmayesero. Mzimu ukufuna koma thupi ndi lofowoka.”

Pakuti kuchokera mʼkati mwa mitima ya anthu, mumatuluka maganizo oyipa, chiwerewere, kuba, kupha, chigololo, dyera, nkhwidzi, chinyengo, machitidwe onyansa, kaduka, chipongwe, kudzikuza ndi kupusa. Zoyipa zonsezi zimatuluka mʼkati ndipo zimadetsa munthu.”

Iye anayankha kuti, “Aliyense amene aleka mkazi wake ndi kukakwatira wina achita chigololo kulakwira mkaziyo. Ndipo akasiya mwamuna wake ndi kukakwatiwa ndi wina, achita chigololo.”

Iwe umadziwa malamulo: ‘Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni wonama, usachite chinyengo, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”

“Aliyense amene asiya mkazi wake ndi kukakwatira mkazi wina akuchita chigololo, ndipo mwamuna amene akwatira mkazi wosiyidwayo akuchitanso chigololo.”

Iwe umadziwa malamulo: ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usapereke umboni wonama, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”

Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi anabweretsa mkazi amene anagwidwa akuchita chigololo. Iwo anamuyimiritsa patsogolo pa anthu ndipo anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, mkazi uyu tinamugwira akuchita chigololo. Mʼmalamulo a Mose anatilamulira kuti akazi otere tiwagende ndi miyala. Tsopano Inu mukuti chiyani?” Iwo anagwiritsa ntchito funsoli ngati msampha, ndi cholinga choti apeze chifukwa cha kumuneneza Iye. Koma Yesu anawerama pansi ndi kuyamba kulemba pa dothi ndi chala chake. Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu.” Iye anaweramanso pansi ndi kulemba pa dothi. Iwo atamva izi anayamba kuchoka mmodzimmodzi, akuluakulu poyamba, mpaka Yesu anatsala yekha ndi mkaziyo atayimirira pomwepo. Yesu anaweramuka ndipo anamufunsa iye kuti, “Akuluakulu aja ali kuti? Kodi palibe amene wakutsutsa?” Iye anati, “Ambuye, palibe ndi mmodzi yemwe.” “Inenso sindikukutsutsa iwe. Pita kuyambira tsopano usakachimwenso.”

Koma tiwalembere iwo, kuwawuza kuti asadye chakudya choperekedwa kwa mafano, apewenso dama, asadyenso nyama zochita kupotola kapena kudya magazi.

Mupewe kudya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano, musadye magazi, kapena nyama yopha mopotola ndiponso musachite dama. Mudzachita bwino mukapewa zimenezi. Tsalani bwino.

Koma kunena za anthu a mitundu ina amene asandulika okhulupirira, ife tinawalembera zimene tinavomerezana zakuti asadye chakudya choperekedwa ku mafano, asadye magazi, asadye nyama yopotola ndiponso asachite zadama.”

Nʼchifukwa chake Mulungu anawasiya kuti azingochita zilakolako zochititsa manyazi zauchimo zomwe mitima yawo inkafuna. Zotsatira zake anachita za chiwerewere wina ndi mnzake kunyazitsa matupi awo. Iwo anasinthanitsa choonadi cha Mulungu ndi bodza ndipo anapembedza ndi kutumikira zinthu zolengedwa mʼmalo mwa Mlengi amene ali woyenera kutamandidwa mpaka muyaya. Ameni. Chifukwa cha ichi, Mulungu anawasiya kuti azitsata zilakolako zochititsa manyazi. Ngakhale akazi omwe anasiya machitidwe achibadwidwe pa za ukwati, namachita machitidwe ena otsutsana ndi chibadwa chawo. Chimodzimodzinso amuna analeka machitidwe a ukwati ndi akazi nʼkumakhumbana amuna okhaokha. Amuna ankachita zochitisa manyazizi ndi amuna anzawo, ndipo analandira chilango choyenera molingana ndi zochita zawo zachitayikozo.

Ndipo popeza anaona kuti nʼchopanda nzeru kumvera Mulungu, Iye anawasiya kuti atsatire maganizo achitayiko kuti achite zosayenera kuchitazo. Iwo ndi odzazidwa ndi mtundu uliwonse wa makhalidwe oyipa, zonyansa, umbombo ndi dumbo. Iwo ndi odzazidwa ndi kaduka, kupha, mikangano, chinyengo ndi udani. Iwowo ndi amiseche,

Ngakhale kuti amadziwa chiweruzo cholungama cha Mulungu chakuti amene amachita zinthu zotere amayenera imfa, iwo sangopitiriza chabe zimenezi, koma amavomerezanso amene amazichita zimenezi.

Nʼchifukwa chake, musalole tchimo lilamulire matupi anu amene anafa kuti mumvere zilakolako zonyansa. Musapereke ziwalo zathupi lanu ku tchimo, ngati zipangizo zamakhalidwe oyipa. Mʼmalo mwake, mudzipereke kwa Mulungu, ngati amene achoka ku imfa kupita ku moyo. Ndipo mupereke ziwalo zathupi lanu ngati zipangizo zachilungamo.

Ine ndikufanizira zinthu za tsiku ndi tsiku chifukwa chikhalidwe chanu nʼchofowoka. Monga momwe munkapereka ziwalo za matupi kukhala akapolo a zonyansa ndi makhalidwe oyipa, zimene zimanka zichulukirabe, choncho tsopano dziperekeni ziwalozo kuti zikhale akapolo achilungamo ndi a kuyera mtima.

Koma ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina pamene mwamuna wake ali moyo, amatchedwa wachigololo. Koma ngati mwamuna wakeyo amwalira, mkaziyo amasuka ku lamulo ndipo si wachigololo, ngakhale kuti wakwatiwa ndi mwamuna wina. Chimodzimodzi inunso, abale anga, munafa ku Malamulo kudzera mʼthupi la Khristu, kuti mukwatiwe ndi wina, ndi Iye amene anauka kwa akufa kuti tibalire Mulungu chipatso. Pakuti pamene tinkalamulidwa ndi khalidwe lathu lauchimo, zilakolako zauchimo zimene Malamulo anaziwutsa zinkagwira ntchito mʼmatupi mwathu kotero kuti zinabala imfa.

Koma mʼkati mwanga ndimaona lamulo lina likugwira ntchito kulimbana ndi zomwe mtima wanga umavomereza. Lamulo limenelo landisandutsa wamʼndende walamulo la uchimo lomwe likugwira ntchito mʼkati mwa ziwalo zanga.

Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa chifukwa mwa Khristu Yesu, lamulo la Mzimu Woyera amene amapereka moyo, lawamasula ku lamulo la tchimo ndi la imfa. Pakuti zimene Malamulo sanathe kuzichita, popeza anali ofowoka chifukwa cha khalidwe lathu la uchimo, Mulungu anazichita potumiza Mwana wake mʼchifanizo cha munthu ochimwa kuti akhale nsembe yauchimo. Ndipo Iye anagonjetsa tchimo mʼthupi la munthu, ndi cholinga chakuti chilungamo chofunikira cha lamulo chikwaniritsidwe kwathunthu mwa ife amene sitikhala monga mwachikhalidwe chathu cha uchimo koma mwa Mzimu. Pakuti anthu amene amakhala monga mwa makhalidwe oyipa a thupi amayika malingaliro awo pa zinthu zathupi. Koma amene amakhala monga mwa Mzimu amayika malingaliro awo pa zinthu za Mzimu. Kuyika mtima pa zathupi ndi imfa koma kuyika mtima pa za Mzimu ndi moyo ndi mtendere. Pakuti mtima umene wakhazikika pa zathupi ndi wodana ndi Mulungu. Sunagonjere lamulo la Mulungu ndipo sungathe kutero. Ndipo anthu amene amalamulidwa ndi khalidwe lauchimo sangathe kukondweretsa Mulungu.

Kotero abale, ife tili ndi zoti tikwaniritse, koma osati za khalidwe lathu lauchimo, kumachita zofuna zake. Pakuti ngati inu mukhala monga mwa khalidwe lauchimo, mudzafa. Koma ngati mwa Mzimu mupha ntchito zoyipa zathupi, mudzakhala ndi moyo.

Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu.

Malamulo awa: “Usachite chigololo,” “Usaphe,” “Usabe,” “Usasirire,” ndi malamulo ena onse amene alipo, akhazikika pa lamulo limodzi ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.”

Tiyeni tikhale moyenera monga nthawi ya masana, osati mʼmagulu amadyerero, achiwerewere ndi kuledzera, mʼmadama ndi zonyansa komanso osati mʼmagawano ndi nsanje. Koma valani Ambuye Yesu Khristu ndipo musaganizire za momwe mungakwaniritsire zokhumba zachikhalidwe cha uchimo.

Mbiri yamveka kuti pakati panu pakuchitika chigololo. Ndipo chigololo cha mtunduwu ngakhale pakati pa akunja sichingapezeke; munthu akumagonana ndi mkazi wa abambo ake.

Ndakulemberani mʼkalata yanga kuti musayanjane nawo anthu achigololo. Pamenepatu sindikutanthauzatu anthu a dziko lapansi lino amene ndi achigololo, kapena aumbombo, kapena opeza ndalama mwachinyengo, kapena opembedza mafano. Kukanatero mukanangochoka mʼdziko lapansi lino. Koma tsopano ndikukulemberani kuti musayanjane ndi aliyense amene adzitcha mʼbale koma ndi wachigololo, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, kapena wonamizira anzake, woledzera kapena wopeza ndalama mwachinyengo. Munthu wotere ngakhale kudya, osadya naye pamodzi. Kodi ndipindulanji kuti ndiweruze anthu amene si a mu mpingo? Kodi simuyenera kuweruza iwo amene ali mu mpingo? Mulungu adzaweruza akunja. “Chotsani woyipayo pakati panu.”

Kodi simukudziwa kuti munthu woyipa sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musanyengedwe: achigololo, kapena opembedza mafano, kapena achiwerewere, kapena amuna adama, kapena ogonana ndi amuna okhaokha; kapena akuba, kapena aumbombo, kapena oledzera, kapena achipongwe, kapena opeza ndalama mwachinyengo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu. Ndipo umu ndi mmene ena mwa inu munalili. Koma munatsukidwa, munayeretsedwa, munalungamitsidwa mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu ndi Mzimu wa Mulungu wathu.

Inu mumati, “Chakudya, kwake nʼkulowa mʼmimba ndipo mimba ntchito yake nʼkulandira chakudyacho.” Koma Mulungu adzawononga zonsezi. Thupi silochitira chigololo, koma la Ambuye, ndipo Ambuye ndiye mwini thupilo.

Kodi simukudziwa kuti matupi anuwo ndi ziwalo za Khristu mwini? Kodi tsono ndingatenge ziwalo za Khristu nʼkuzisandutsa ziwalo za mkazi wadama? Zosatheka! Kodi simukudziwa kuti amene amadzipereka kwa mkazi wadama, iyeyo ndi mkaziyo amasanduka thupi limodzi? Paja kunalembedwa kuti, “Awiriwo adzakhala thupi limodzi.” Koma amene amadzipereka kwa Ambuye, iyeyo ndi Ambuye amakhala mzimu umodzi. Thawani dama. Machimo onse amene munthu amachita amakhala kunja kwa thupi lake, koma amene amachita machimo okhudza chigololo, amachimwira thupi lake lomwe.

Tsopano pa zinthu zomwe munandilembera nʼkwabwino kuti munthu asakwatire. Koma chifukwa choti chigololo chawanda, mwamuna aliyense akhale naye mkazi wakewake ndipo mkazi aliyense akhale naye mwamuna wakewake. Mwamuna akwaniritse udindo wake wa pa banja kwa mkazi wake, ndipo chimodzimodzi mkazi kwa mwamuna wake. Thupi la mkazi wokwatiwa si la iye mwini yekha koma ndi la mwamuna wakenso. Momwemonso, thupi la mwamuna si la iye mwini yekha koma ndi la mkazi wakenso. Musamakanizane, pokhapokha mutagwirizana awiri kuti mwakanthawi mudzipereke kumapemphero. Kenaka mukhalirenso pamodzi kuopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cholephera kudziretsa.

Koma ngati sangathe kudziretsa, akwatire, popeza ndi bwino kukwatira kusiyana ndi kudzizunza ndi chilakolako.

Ngati wina akuganiza kuti akumulakwira namwali yemwe anapalana naye ubwenzi, ndipo ngati chilakolako chake chikunka chikulirakulirabe, ndipo akuona kuti nʼkofunika kumukwatira, ayenera kuchita monga wafunira, kutero si kuchimwa ayi.

Tisachite chigololo monga ena mwa iwo anachitira ndipo tsiku limodzi anafapo anthu 23,000.

Choncho, ngati mukuganiza kuti mwayima mwamphamvu, samalani mungagwe! Palibe mayesero amene mwakumana nawo oposa amene anthu ena onse anakumana nawo. Mulungu ngokhulupirika; sadzalola kuti inu muyesedwe koposa muyeso umene mutha kupirira. Koma pamene mwayesedwa, Iyenso adzakupatsani njira yopambanira mayeserowo.

Pakuti tonsefe tiyenera kukaonekera pa mpando woweruza wa Khristu, kuti aliyense wa ife akalandire zomuyenera molingana ndi zimene anachita ali mʼthupi; zabwino kapena zoyipa.

Abwenzi okondedwa, popeza tili ndi malonjezo amenewa, tiyeni tidziyeretse, kusiyana nazo zilizonse zimene zikhoza kudetsa thupi ndi mzimu, ndipo tiyesetse kukhala oyera mtima poopa Mulungu.

Ndikuopa kuti pamene ndidzabwerenso, Mulungu adzandichepetsa pamaso panu, ndipo ndidzamva chisoni ndi ambiri amene anachimwa kale ndipo sanalape zonyansa, zachigololo ndi zilakolako zoyipa zimene anachita.

Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo. Pakuti thupi lanu la uchimo limalakalaka zimene ndi zotsutsana ndi Mzimu, ndi Mzimu zimene ndi zotsutsana ndi thupi lanu la uchimo. Ziwirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mukufuna. Koma ngati Mzimu akutsogolerani, ndiye kuti simuli pansi pa lamulo. Ntchito za thupi lanu la uchimo zimaonekera poyera ndi izi: dama, zodetsa ndi kuchita zonyansa; kupembedza mafano ndi ufiti; kudana, kukangana, kupsa mtima, kudzikonda, kugawikana, mipatuko ndi nsanje, kuledzera, mchezo ndi zina zotere. Ine ndikukuchenjezani monga ndinachita poyamba paja kuti amene amachita zimenezi sadzalandira ufumu wa Mulungu.

Amene ali ake a Khristu Yesu anapachika pa mtanda thupi lawo la uchimo pamodzi ndi zokhumba zawo ndi zolakalaka zawo.

Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa. Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha.

Nthawi ina tonsefe tinalinso ndi moyo wonga wawo, tinkachitanso zilizonse zimene matupi ndi maganizo athu ankafuna. Mwachibadwa chathu, tinali oyenera chilango monga anthu ena onse.

Popeza sazindikiranso kanthu kalikonse, adzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite mtundu uliwonse wa zoyipa ndi zilakolako zosatha.

Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu. Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika. Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.

Choncho, iphani zilakolako za dziko lapansi mwa inu, monga: dama, zodetsa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoyipa ndi umbombo, pakuti umbombo ndiko kupembedza mafano.

Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama; aliyense wa inu aphunzire kulamulira thupi lake mʼnjira yoyera ndi yaulemu, osati yotsata chilakolako chonyansa monga amachitira akunja, amene sadziwa Mulungu.

Pakuti Mulungu sanatiyitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima. Choncho, aliyense amene akukana malangizo awa sakukana munthu koma Mulungu, Mulungu weniweniyo amene amakupatsani Mzimu Woyera.

Tikudziwanso kuti Malamulo sakhazikitsidwa chifukwa cha anthu olungama, koma ophwanya lamulo ndi owukira, osaopa Mulungu ndi ochimwa, wopanda chiyero ndi osapembedza; amene amapha abambo awo ndi amayi awo, kapena anthu ena. Malamulo amayikidwa chifukwa cha anthu achigololo ndi ochita zadama ndi amuna anzawo, anthu ogulitsa akapolo, abodza ndi olumbira zabodza, ndi ochita chilichonse chotsutsana ndi chiphunzitso choona.

Thawa zilakolako zoyipa zachinyamata. Funafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere pamodzi ndi amene akuyitanira pa dzina la Ambuye ndi mtima osadetsedwa.

Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero. Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino, opereka anzawo kwa adani awo, osaopa zoyipa, odzitukumula, okonda zowasangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu. Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa. Iwowa ndi anthu aja amene amayendayenda mʼmakomo a anthu nʼkumanyenga akazi ofowoka mʼmaganizo, olemedwa ndi machimo ndiponso otengeka ndi zilakolako zoyipa zamitundumitundu,

Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino,

Yangʼanitsitsani kuti pasakhale wina wachigololo. Kapena wosapembedza ngati Esau, amene chifukwa cha chakudya cha kamodzi kokha anagulitsa ukulu wake.

Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo mwamuna ndi mkazi azikhala wokhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzawalanga.

Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda. Munthu akayesedwa asanene kuti, “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense. Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo. Pamenepo, chilakolako chikakula chimabala tchimo; ndipo tchimo likakhwima limabereka imfa.

Koma ngakhale mumapempha simulandira, chifukwa mumapempha ndi zolinga zoyipa. Mumapempha kuti muzigwiritse ntchito pa zokusangalatsani nokha. Inu anthu achigololo, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko lapansi ndi kudana ndi Mulungu? Choncho, aliyense wosankha kukhala bwenzi la dziko lapansi amasanduka mdani wa Mulungu.

Monga ana omvera, musatsatenso zilakolako zoyipa zomwe munali nazo pamene munali osadziwa.

Okondedwa, ndikukupemphani, ngati alendo pansi pano, pewani zilakolako za uchimo, zimene zimachita nkhondo ndi moyo wanu.

Popeza kuti Khristu anamva zowawa mʼthupi lake, mukhale nawonso mtima omwewo, chifukwa iye amene wamva zowawa mʼthupi lake walekana nawo uchimo. Chifukwa cha ichi, iwo sakhalanso moyo wawo akuchita zofuna za matupi awo, koma amachita chifuniro cha Mulungu. Pakuti mwataya kale nthawi yambiri mʼmbuyomu pochita zimene anthu osapembedza amachita, moyo wokhumba zonyansa, zilakolako zoyipa kuledzera, zochitika zoyipa za pa phwando, mapokoso ndi kupembedza mafano onyansa.

Pakuti Mulungu sanalekerere angelo atachimwa paja, koma anawaponya mʼndende, nawayika mʼmaenje amdima, kuwasunga kuti adzaweruzidwe. Iye sanalekerere dziko lapansi kalelo, koma anapulumutsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, ndi anthu ena asanu ndi awiri atadzetsa chigumula pa dziko lapansi kwa anthu akhalidwe losapembedza Mulunguyo. Mulungu anaweruza mizinda ya Sodomu ndi Gomora nayiwononga ndi moto, kuti ikhale chitsanzo cha zimene zidzachitikira anthu osapembedza Mulungu. Koma Iye anapulumutsa Loti, munthu wolungama, amene ankavutika ndi khalidwe lonyansa la anthu oyipa. (Pakuti munthu wolungamayo, pokhala pakati pawo tsiku ndi tsiku ankavutika mu mtima ndi makhalidwe awo oyipa amene ankawaona ndi kuwamva). Tsono mutha kuona kuti Ambuye amadziwa kuwapulumutsa kwake pa mayesero anthu opembedza. Amadziwanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo. Makamaka amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi nanyoza ulamuliro. Anthu amenewa ndi odzikuza, ndipo otsata chifuniro cha iwo eni, sasamala za munthu, saopa kuchitira chipongwe zolengedwa za mmwamba.

Ndi maso awo odzaza ndi chigololo, salekeza kuchimwa. Amanyengerera anthu osakhazikika. Iwo ndi akatswiri pa dyera ndi chuma, ndipo ndi ana otembereredwa!

Pakuti anayankhula mawu opanda pake ndi onyada, ndipo ndi zilakolako zoyipa za thupi amanyenga anthu amene angopulumuka kumene pakati pa anzawo oyipa.

Poyamba mudziwe kuti mʼmasiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, adzanyoza ndi kutsata zilakolako zawo zoyipa.

Pakuti zonse za mʼdziko lapansi, zilakolako za thupi, zinthu zimene maso amakhumbira ndiponso kuyandikira zinthu za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya.

Pakuti anthu ena amene za chilango chawo zinalembedwa kale, alowa mobisika pakati panu. Amenewa ndi anthu osapembedza Mulungu, amene amapotoza chisomo cha Mulungu wathu kuchisandutsa ufulu ochitira zonyansa ndiponso amakana Yesu Khristu amene Iye ndiye Mbuye ndi Mfumu yathu.

Ndipo mukumbukire angelo amene sanakhutire ndi maudindo awo, koma anasiya malo awo. Angelo amenewa Mulungu anawamanga ndi maunyolo osatha, ndipo akuwasunga mʼmalo a mdima mpaka tsiku lalikulu lachiweruzo. Musayiwale mizinda ya Sodomu ndi Gomora ija, ndi mizinda yoyandikana nayo. Anthu mʼmenemo anadziperekanso kuchita zadama ndi kuchita zonyansa zachilendo. Mizinda imeneyi yakhala ngati chitsanzo cha amene adzalangidwa ndi moto wosatha. Nʼchimodzimodzinso zimene akuchita anthu amenewa potsata maloto awo, amadetsa matupi awo, amakana ulamuliro wa Mulungu ndiponso amachitira chipongwe angelo akumwamba.

Komabe, ndili ndi zinthu zingapo zotsutsana nanu. Kumeneko muli ndi anthu ena amene amatsata ziphunzitso za Balaamu, uja amene anaphunzitsa Baraki kukopa Aisraeli kuti azidya nsembe zoperekedwa ku mafano ndi kumachita chigololo.

Komabe ndili ndi chinthu chokudzudzula nacho. Umamulekerera mkazi uja Yezebeli amene amadzitcha yekha kuti ndi mneneri. Iye amaphunzitsa atumiki anga kuti azichita zadama ndi kumadya zansembe zoperekedwa ku mafano. Ndamupatsa nthawi kuti aleke zachigololo zake koma sakufuna. Tsono ndidzamugwetsa mʼmasautso ndipo amene amachita naye zadama zakezo ndidzawasautsa kwambiri akapanda kulapa ndi kuleka njira za mkaziyo.

Sanalapenso kuleka zakupha, zamatsenga awo, zachigololo zawo kapena umbava wawo.

Mngelo wachiwiri anatsatana naye ndipo anati, “Wagwa! Wagwa Babuloni womveka uja, amene anachititsa anthu a mitundu yonse kumwa vinyo wa zilakolako zake zachigololo.”

Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri anadza nati kwa ine, “Bwera ndikuonetse chilango cha mkazi wadama wotchuka uja amene akukhala pambali pa madzi ambiri. Mafumu a dziko lapansi amachita naye chigololo ndipo okhala pa dziko lapansi analedzera ndi vinyo wa zigololo zake.”

Pakuti mayiko onse amwa vinyo ozunguza mutu wazigololo zake. Mafumu a dziko lapansi achita naye chigololo, ndipo amalonda a dziko lapansi analemera kuchokera pa zolakalaka zake zosefukira.”

“Mafumu a dziko lapansi, amene anachita naye chigololo nachita naye pamodzi zosangalatsa moyo uno, akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzalira nakhuza maliro ake.

pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake. Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake.”

Koma amantha, osakhulupirira, okonda zonyansa, opha anthu, achiwerewere, amatsenga, opembedza mafano ndi abodza, malo awo adzakhala nyanja yamoto ya sulufule wotentha. Iyi ndi imfa yachiwiri.”

Chichewa - Chichewa - NY

NYCCL - Mawu A Mulungu Mu Chichewa Chalero - 2016

This Bible text is from Biblica Open God's Word In Contemporary Chichewa
https://open.bible/bibles/chichewa-biblica-text-bible/
provided by: Biblica Inc, available by Creative Commons CC-BY-SA-4.0,
and this new compilation is shared as www.creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0.
Languages are made available to you by www.ipedge.net