25 – Ndalama

Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Ndalama.

Mavesi atatu ofunika kwambiri

“Musadziwunjikire chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga ndi pamene mbala zimathyola ndi kuba. Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba. Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko.

Koma kulemekeza Mulungu kuli ndi phindu lalikulu. Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi. Koma ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire. Anthu amene amafuna kulemera amagwa mʼmayesero ndi mu msampha ndi mʼzilakolako zambiri zopusa ndi zoopsa zimene zimagwetsera anthu mʼchitayiko ndi mʼchiwonongeko. Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri.

Yesu anayangʼanayangʼana ndipo anati kwa ophunzira ake, “Nʼkovutadi kuti achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!” Ophunzira anadabwa ndi mawu ake. Koma Yesu anatinso, “Ananu, nʼkovutadi kulowa mu ufumu wakumwamba! Ndi kwapafupi kwa ngamira kuti idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kuti alowe mu ufumu wa Mulungu.” Ophunzira anadabwa kwambiri, ndipo anati kwa wina ndi mnzake, “Nanga ndani amene angapulumuke?” Yesu anawayangʼana ndipo anati, “Kwa munthu zimenezi nʼzosatheka, koma osati ndi Mulungu; zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu.”

Mavesi onse motsatira dongosolo lolondola – 384 ndime

Patapita nthawi, Kaini anatenga zipatso za ku munda nakazipereka kwa Yehova monga nsembe. Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake. Koma sanakondwere ndi Kaini ndi nsembe yake. Kotero Kaini anakwiya kwambiri ndipo nkhope yake inagwa.

Abramu anali wolemera kwambiri; anali ndi ziweto ndiponso siliva ndi golide.

Motero dziko linayamba kuwachepera kuti onse nʼkukhala pamodzi, popeza katundu wawo anali wochuluka kwambiri moti sakanatha kukhala pamodzi.

Ndipo adalitsike Mulungu Wammwambamwamba amene anapereka adani ako mʼdzanja lako.” Ndipo Abramu anamupatsa iye chakhumi cha zonse anali nazo.

Yehova wadalitsa mbuye wanga kwambiri, ndiponso walemera. Wamupatsa nkhosa ndi ngʼombe, siliva ndi golide, antchito aamuna ndi antchito aakazi, komanso ngamira ndi abulu.

Kenaka wantchitoyo anatulutsa ziwiya zagolide ndi zasiliva ndi zovala nazipereka kwa Rebeka. Anaperekanso mphatso zina za mtengowapatali kwa mlongo wake ndi amayi ake a Rebeka.

Isake anadzala mbewu mʼmunda, ndipo chaka chomwecho anakolola zinthu zambiri chifukwa Yehova anamudalitsa. Isake analemera. Chuma chake chinkachulukirachulukira mpaka anasanduka munthu wolemera kwambiri. Anali ndi nkhosa, ngʼombe ndi antchito ambiri mwakuti Afilisti anamuchitira nsanje.

ndipo mwala uwu ndawuyimikawu udzakhala Nyumba ya Mulungu. Ine ndidzakupatsani chakhumi cha zinthu zonse zimene mudzandipatse.”

Yosefe anasunga tirigu wochuluka kwambiri ngati mchenga wa ku nyanja. Kunali tirigu wochuluka kwambiri motero kuti analeka nʼkulembera komwe.

Pamene njala inafalikira dziko lonse, Yosefe anatsekula nkhokwe za zakudya namagulitsa tirigu kwa anthu a ku Igupto aja, pakuti njala inafika poyipa kwambiri mu Igupto monse. Anthu ankabwera ku Igupto kuchokera ku mayiko ena onse kudzagula tirigu kwa Yosefe, chifukwa njala inafika poyipa kwambiri pa dziko lonse lapansi.

Yosefe anaperekanso chakudya kwa abambo ake, kwa abale ake ndi kwa onse a mʼnyumba ya abambo ake monga mwa chiwerengero cha ana awo.

Njala inakula kwambiri motero kuti chakudya chinasowa mʼdziko lonse. Anthu a ku Igupto ndi ku Kanaani analefuka nayo njalayo. Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse zimene anthu a mu Igupto ndi Kanaani ankapereka pogula tirigu, ndipo anabwera nazo ku nyumba kwa Farao. Anthu a ku Igupto ndi Kanaani ndalama zitawathera, Aigupto onse anabwera kwa Yosefe nati, “Tipatseni chakudya. Nanga tiferenji pamaso panu? Ndalama zathu zatha.” Ndipo Yosefe anawayankha kuti, “Bwerani ndi ziweto zanu ndipo tidzasinthana ndi chakudya poti mukuti ndalama zanu zatha.” Choncho anthu anabwera ndi ziweto zawo monga akavalo, nkhosa, mbuzi, ngʼombe ndi abulu ndipo Yosefe anawapatsa zakudya. Chitatha chaka chimenecho, anthu anapitanso kwa Yosefe chaka chinacho nati, “Ife sitingakubisireni mbuye wathu kuti ndalama zathu zatithera ndipo ziweto zathu zili ndi inu, palibenso choti nʼkukupatsani mbuye wathu kupatula matupi athu ndi dziko lathu. Tiferenji ife ndi dziko lathu inu mukuona? Mutipatse chakudya ndipo tidzigulitsa ife ndi minda yathu yomwe. Ife tidzakhala akapolo a Farao. Tipatseni mbewuzo kuti tikhale ndi moyo tisafe ndipo dziko lisachite bwinja.” Choncho Yosefe anamugulira Farao dziko lonse la Igupto. Aliyense mu Igupto anagulitsa munda wake chifukwa njala inakula kwambiri. Dziko lonse linasanduka la Farao, ndipo Yosefe anawasandutsa anthu onse kukhala akapolo a Farao, kuchokera ku malire a mbali ina ya Igupto kukafika ku malire a mbali ina ya dzikolo.

Mkazi aliyense adzapemphe Mwigupto woyandikana naye ndiponso mkazi amene akukhala mʼnyumba yake, kuti amupatse ziwiya za siliva ndi golide ndiponso zovala zimene mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi. Ndipo potero mudzawalanda zonse Aiguptowo.”

Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzakupatsani buledi wogwa kuchokera kumwamba ngati mvula. Anthu azituluka tsiku lililonse kukatola buledi wokwanira tsiku limenelo. Ine ndidzawayesa mʼnjira imeneyi kuti ndione ngati adzatsatira malangizo anga. Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, pamene azidzakonza buledi amene abwera naye, adzapeza kuti ndi wokwanira masiku awiri.”

Ndipo Mose anawawuza kuti, “Wina aliyense asasunge mpaka mmawa.” Komabe ena sanamvere Mose, anasungako mpaka mmawa. Koma mmawa mwake tonse tinali mphutsi zokhazokha. Kotero Mose anawapsera mtima.

“Usabe.

“Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako kapena wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”

Choncho musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide kuti muziyipembedza pamodzi ndi Ine.’ ”

“Munthu aliyense amene aba munthu mnzake, ndi kukamugulitsa, kapena kumangomusunga, ayenera kuphedwa.

“Ngati munthu asungitsidwa ndi mnzake ndalama kapena katundu, ndipo zinthu zija nʼkubedwa mʼnyumba mwake, wakubayo ngati agwidwa, ayenera kubwezera kawiri chobedwacho. Koma ngati mbalayo sipezeka, mwini nyumbayo ayenera kukaonekera ku bwalo lamilandu kuti akamve ngati anaba katundu wa mnzakeyo.

“Ngati mukongoza ndalama kwa mʼbale wanu amene ndi mʼmphawi pakati panu, musadzamuchite monga zimene amachita wokongoza ndalama. Musadzamuyikire chiwongoladzanja.

“Uza Aisraeli kuti abweretse chopereka kwa Ine. Iwe ulandire choperekacho mʼmalo mwanga kuchokera kwa munthu amene akupereka mwakufuna kwake.

Kuchokera pa zomwe muli nazo, mutenge chopereka cha Yehova. Aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka abweretse kwa Yehova zopereka izi: Golide, siliva ndi mkuwa;

Onse amene anali ndi mtima wofuna, amuna ndi amayi omwe anabwera kudzapereka zodzikometsera zagolide za mtundu uliwonse: zomangira zovala, ndolo, mphete ndi zokometsera. Onse anapereka golide wawo monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

ndipo anati kwa Mose, “Anthu akubweretsa kuposa zimene zikufunika kugwirira ntchito imene Yehova analamulira kuti ichitike.” Choncho Mose analamulira ndipo analengeza mu msasa onse, “Mwamuna kapena mayi aliyense asaperekenso chopereka chilichonse cha ku malo wopatulika.” Choncho anthu analetsedwa kubweretsa zambiri, chifukwa zimene anali nazo zinali zoposera zimene zimafunika kugwirira ntchito yonse.

“Ngati munthu wina aliyense achimwa, nachita zinthu mosakhulupirika kwa Yehova chifukwa cha kunyenga mnzake pokana kumubwezera zimene anamusungitsa, kapena kumubera kapenanso kumulanda, kapena ndi kunama kuti sanatole chinthu chimene chinatayika, kapena kulumbira mwachinyengo pa chinthu chilichonse chimene munthu akachita amachimwa nacho,

“ ‘Pamene mukolola zinthu mʼmunda mwanu musakolole mpaka mʼmphepete mwa munda, ndipo musatole khunkha lake. Musakolole mphesa zonse mʼmunda wanu wa mpesa kapena kutola mphesa zakugwa mʼmundamo. Zimenezi muzisiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wako. “ ‘Musabe. “ ‘Musamanamizane. “ ‘Musachitirane zinthu mwachinyengo.

“ ‘Musapsinje mnzanu kapena kumulanda zinthu zake. “ ‘Musasunge malipiro a munthu wantchito usiku wonse mpaka mmawa.

“ ‘Musamachite za chinyengo poweruza mlandu, kapena poyeza utali, kulemera ngakhalenso kuchuluka kwa zinthu. Miyeso ya sikelo, miyeso yoyezera kulemera kwa zinthu, miyeso yotchedwa efa ndi miyeso yotchedwa hini zikhale zolungama. Ine ndine Yehova, Mulungu wanu amene ndinakutulutsani ku dziko la Igupto.

“ ‘Pamene mukukolola zinthu mʼmunda mwanu, musakolole munda wanu mpaka mʼmalire mwenimweni, ndipo musatole khunkha lake. Zimenezo musiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”

Pa zaka zisanu ndi chimodzi muzikalima minda yanu, ndipo kwa zaka zisanu ndi chimodzi muzikasadza mitengo yanu ya mpesa ndi kuthyola zipatso zake. Koma chaka chachisanu ndi chiwiri ndi chaka choti nthaka ipume, chaka cha Sabata la Yehova. Musalime mʼminda yanu kapena kusadza mitengo yanu ya mpesa. Musakolole zimene zinamera zokha mʼmunda mwanu. Musakakolole kapena kuthyola mphesa za mʼmitengo imene simunasadze. Chaka chimenechi nʼchoti nthaka ipumule.

“ ‘Muzichotsera Masabata asanu ndi awiri a zaka, ndi kuchulukitsa zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawirinso kuti Masabata asanu ndi awiri a zakawo akwane zaka 49. Ndipo pa tsiku la khumi la mwezi wachisanu ndi chiwiri mulize lipenga mofuwula. Tsiku lochita mwambo wopepesera machimo muziliza lipenga mʼdziko lanu lonse. Mupatule chaka cha makumi asanu, ndipo mulengeze kuti pakhale ufulu mʼdziko lonse kwa onse amene ali mʼmenemo. Kwa inu chakachi chidzakhala choyimba lipenga la chikondwerero. Aliyense wa inu adzayenera kubwerera pa munda wake, ndipo aliyense wa inu adzabwerera ku fuko lake. Kwa inu chakachi chidzakhaladi chaka choyimba lipenga kukondwerera zaka makumi asanu. Pa chaka chimenechi musadzale kanthu ndipo musakolole mbewu zomera zokha kapenanso kuthyola mphesa pa mitengo yosasadzira. Chimenechi ndi chaka chokondwerera zaka makumi asanu. Choncho chikhale chaka chopatulika kwa inu. Muzidya zokhazo zimene zakololedwa mʼminda.

“ ‘Ngati mʼbale wako akhala wosauka kuti sangathe kudzisamalira yekha, umuthandize. Ukhale naye ngati mlendo kapena ngati munthu amene ukhala naye kwa kanthawi.

Usalandire chiwongoladzanja chilichonse kuchokera kwa iye kapena kuwonjezerapo kanthu kena, koma uziopa Mulungu kuti mʼbale wakoyo akhale nawe. Musakongoze mnzanu ndalama kuti mulandire chiwongoladzanja, kapena kumugulitsa chakudya kuti mupeze phindu.

“ ‘Chakhumi chilichonse chochokera mʼdziko, kaya ndi tirigu wochokera mʼnthaka kapena chipatso cha mʼmitengo ndi za Yehova. Chimenecho ndi chopatulika kwa Yehova.

Ndipo Yehova anati kwa Aaroni, “Iweyo sudzakhala ndi cholowa mʼdziko lawo, ndiponso sudzalandira gawo lililonse pakati pawo. Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisraeli. “Taonani, ndawapatsa Alevi chakhumi chonse mu Israeli ngati cholowa chawo chifukwa cha ntchito ya ku tenti ya msonkhano.

Yehova anati kwa Mose, “Yankhula ndi Alevi ndi kunena nawo kuti, ‘Pamene mulandira chakhumi kuchoka kwa Aisraeli chimene ndimakupatsani ngati cholowa chanu, muyenera kupereka chakhumi cha choperekacho kwa Yehova. Chopereka chanucho chidzawerengedwa kwa inu ngati tirigu wochokera kopunthira kapena ngati mphesa zopsinya kuchokera kopsinyira mphesa. Mwa njira imeneyi inunso muzipereka chopereka kwa Yehova kuchokera ku chakhumi chanu chilichonse chimene mumalandira kuchokera kwa Aisraeli. Kuchokera ku chakhumicho muziperekako gawo la Yehova kwa Aaroni, wansembe. Muyenera kupereka monga gawo la Yehova magawo abwino kwambiri ndi opatulika a chilichonse chimene chapatsidwa kwa inu.’

Nʼchifukwa chiyani dzina la abambo athu lasowa pakati pa fuko lawo, kodi popeza analibe mwana wamwamuna? Tipatseni cholowa chathu pakati pa abale a abambo athu.” Tsono Mose anabweretsa nkhani yawo pamaso pa Yehova ndipo Yehova anati kwa iye, “Zimene ana aakazi a Zelofehadi akunena ndi zoona. Uyenera kuwapatsadi cholowa chawo pakati pa abale a abambo awo ndipo uwapatse cholowa cha abambo awowo. “Uza Aisraeli kuti, ‘Ngati munthu afa wosasiya mwana wamwamuna, muzipereka cholowa chake kwa mwana wake wamkazi. Ngati alibe mwana wamkazi, muzipereka cholowa chakecho kwa abale ake. Ngati alibe abale muzipereka cholowa chake kwa abale a abambo ake. Ngati abambo ake analibe mʼbale, muzipereka cholowa chakecho kwa mnansi wake wa mʼbanja lake kuti chikhale chake. Ili likhale lamulo kwa Aisraeli, monga momwe Yehova analamulira Mose.’ ”

Ndipo tabweretsa zopereka kwa Yehova zimene munthu aliyense anapeza: ziwiya zagolide, zibangiri, zigwinjiri, mphete zosindikizira, ndolo ndi mikanda kuti tichitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova.”

Cholowa chilichonse mu Israeli sichiyenera kupita ku fuko lina, popeza fuko lililonse la Israeli liyenera kusunga cholowa chimene linalandira.”

“Usabe.

“Usasirire mkazi wa mnzako. Usasirire nyumba ya mnzako kapena munda wake, wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”

dziko limene buledi sadzasowa ndipo simudzasowa chilichonse; dziko limene miyala yake ndi chitsulo ndipo ku mapiri ake mukhoza kukumbako mkuwa.

kuopa kuti mukadya ndi kukhuta, mukamanga nyumba zabwino ndi kukhalamo, ndi pamene ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu zaswana, ndi siliva ndi golide wanu wachuluka ndiponso kuti zonse zimene muli nazo zachuluka, mtima wanu udzayamba kunyada ndi kuyiwala Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani ku dziko la ukapolo. Iye anakutsogolerani kudutsa mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha, dziko lija la ludzu ndi lopanda madzi, lokhala ndi njoka zaululu ndi zinkhanira. Iye anatulutsa madzi kuchokera mʼthanthwe lowuma. Iye anakupatsani mana kuti mudye mʼchipululu, zinthu zoti ngakhale makolo anu sanazidziwe, kuti akuchepetseni ndi kukuyesani ndipo kuti pa mapeto pake zikuyendereni bwino. Mu mtima mwanu mukhoza kuganiza kuti, “Mphamvu zanga ndi kulimbika kwa dzanja langa ndi zimene zandilemeretsa chonchi.” Koma kumbukirani Yehova Mulungu chifukwa ndi amene amakupatsani mphamvu zopezera chuma chimenechi kuti atsimikize pangano limene analumbira kwa makolo anu, monga liliri lero lino.

Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu, Ambuye wa ambuye, Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, amene sakondera ndipo salandira ziphuphu. Iye amatchinjiriza ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo amakonda mlendo namupatsa chakudya ndi chovala.

Kumeneko muzipititsako zopereka zanu ndi nsembe zanu zopsereza, ndi chakhumi chanu ndi mphatso zapadera zimene munalonjeza kupereka ndi zopereka zanu zaufulu ndi ana oyamba a ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu.

Tsono kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuti azikhalako muzikabweretsako chilichonse chimene ndikulamulirani inu: zopereka ndi nsembe zanu zopsereza, chakhumi chanu ndi mphatso zapadera, ndi chuma chanu chonse chosankhika chimene munalonjeza kwa Yehova.

Musamadyere mʼmizinda yanu chakhumi cha tirigu wanu ndi vinyo watsopano ndi mafuta, kapena za ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu, kapena chilichonse chimene mwalonjeza kuchipereka, nsembe zanu zaufulu, kapena mphatso zapadera,

Muzionetsetsa kuti mukupatula chakhumi pa zokolola zanu chaka chilichonse. Muzidyera chakhumi cha tirigu wanu, vinyo wanu watsopano ndi mafuta, ndi ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa malo amene adzasankhe ngati kokhalako dzina lake, kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu.

Kumapeto kwa zaka zisanu ndi ziwiri zilizonse, muzikhululukirana ngongole. Zimenezi muzichita motere: wobwereketsa aliyense adzakhululukira ngongole imene anabwereketsa kwa Mwisraeli mnzake. Iye asadzafunenso kuti Mwisraeli mnzakeyo kapena mʼbale wake amubwezere chifukwa nthawi ya Ambuye yokhululukirana ngongole yalengezedwa. Mukhoza kulonjerera ngongole kwa mlendo, koma mukhululukire ngongole ina iliyonse imene mʼbale wanu ali nayo.

Pakuti Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani monga analonjeza, ndipo inu mudzabwereketsa chuma kwa mitundu yambiri ya anthu koma inu simudzabwereka kwa aliyense. Mudzalamulira mitundu yambiri ya anthu koma inuyo palibe amene adzakulamulireni.

Ngati pali mʼbale wanu wina wosauka mu mzinda wanu wina uliwonse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musawumitse mitima yanu kapena kuchita kaligwiritsa kwa mʼbale wanu wosaukayo. Koma mukhale ofewa manja ndipo mumukongoze mʼbale wanu momasuka pa chilichonse chimene akufuna.

Musayesere ndi pangʼono pomwe kusunga maganizo oyipa awa mu mtima mwanu: “Chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka chokhululukirana ngongole, chayandikira,” kuti musaonetse mtima woyipa kwa mʼbale wanu wosauka nʼkusamupatsa chilichonse. Iye angadzakunenereni inu mlandu kwa Ambuye, ndipo mudzapezeka wochimwa. Mumupatse iye mowolowamanja ndipo muchite zimenezi mosasungira kanthu kumtima. Tsono chifukwa cha zimenezi, Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse ndi pa chilichonse chimene mukhudza. Anthu osauka sadzatha mʼdziko lanu. Chomwecho ndikukulamulani kuti mukhale ofewa manja kwa abale anu ndi kwa osauka, osowa mʼdziko mwanu.

Pamenepo muzichita Chikondwerero cha Masabata pamaso pa Yehova Mulungu wanu popereka chopereka chaufulu mofanana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wakupatsani

Aliyense wa inu adzabweretse mphatso molingana ndi momwe Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani.

Asadziwunjikire akazi kuopa kuti mtima wake ungamusocheretse. Asadziwunjikirenso golide ndi siliva wambiri.

Iwowa sadzakhala ndi cholowa pakati pa abale awo pakuti Yehova ndiye cholowa chawo monga anawalonjezera.

Musamasunthe mwala wa malire anu ndi mnzanu amene anayikidwa ndi makolo anu pa cholowa chimene mulandire mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.

Musamalipitse mʼbale wanu chiwongoladzanja, kaya pa ndalama, kapena pa chakudya, kapena pa china chilichonse choti nʼkupereketsa chiwongoladzanja. Mlendo mukhoza kumulipitsa chiwongoladzanja koma osati mʼbale wanu Mwisraeli, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochitika zanu zonse mʼdziko mukulowamoli.

Ngati munthu agwidwa akuba mʼbale wake wa Chiisraeli namamuzunza ngati kapolo kapena kumugulitsa, wogulitsa mnzakeyo ayenera kuphedwa. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.

Mukakolola mphesa mʼmunda mwanu musamabwereremonso kachiwiri. Zotsalazo muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye.

Iye anatibweretsa ku malo ano natipatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi lino. Ndipo tsopano ndikubweretsa zipatso zoyamba zimene inu Yehova mwandipatsa.” Ikani dengulo pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kuwerama mopereka ulemu pamaso pake. Ndipo inu ndi Alevi pamodzi ndi alendo okhala pakati panu mudzakondwera mʼzinthu zonse zabwino zimene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, inu ndi a pa banja panu.

Mukatha kupatula chakhumi pa zonse zimene mwakolola mʼchaka chachitatu chimene ndi chaka chakhumi, muzichipereka kwa wansembe, mlendo, ana ndi akazi amasiye, kuti pamenepo adye mʼmizinda yanu nakhuta. Kenaka munene kwa Yehova Mulungu wanu kuti “Ndatulutsamo mʼnyumba mwanga gawo lopatulika ndipo ndalipereka kwa Mlevi, mlendo, ana ndi akazi amasiye, monga mwa zonse zimene munalamula. Sindinapatuke pa zimene munalamula kapena kuyiwala ndi chimodzi chomwe.

Yehova adzakupambanitsani kwambiri ndipo adzakupatsani ana ambiri, ziweto zambiri, ndi zokolola zochuluka, mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzakupatsani. Yehova adzatsekula kumwamba kumene amasungirako chuma chake, kutumiza mvula mʼdziko lanu pa nthawi yake ndi kudalitsa ntchito yonse ya manja anu. Mudzakongoza mitundu yambiri koma inu simudzakongola kwa aliyense.

Zonse za siliva ndi golide, ziwiya zamkuwa ndi zachitsulo, ndi zake za Yehova ndipo ziyenera kukasungidwa mosungiramo chuma chake.”

Komatu Mose sanapereke malo kwa fuko la Levi. Mose anawawuza kuti zopereka zimene anthu ankapereka kwa Yehova ndizo cholowa chawo.

Yehova amasaukitsa ndipo amalemeretsa, amatsitsa ndipo amakweza. Iye amakweza osauka kuwachotsa pa fumbi, ndipo amachotsa anthu osowa pa dzala. Iye amawakhazika pamodzi ndi ana a mafumu, amawapatsa mpando waulemu. “Pakuti nsanamira za dziko lapansi ndi za Yehova, anakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.

Tsono Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Atafika kwa Davide anati, “Panali anthu awiri mʼmizinda ina, wina wolemera ndi wina wosauka. Munthu wolemerayo anali ndi nkhosa ndi ngʼombe zambiri, koma wosaukayo analibe chilichonse kupatula kankhosa kamodzi kakakazi kamene anakagula. Iye anakasunga ndipo kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kamadya chakudya chake, kamamwera chikho chake ndipo kamagona mʼmanja mwake. Kanali ngati mwana wamkazi kwa iyeyo. “Ndipo mlendo anafika kwa munthu wolemera uja, koma munthu wolemerayo sanafune kutenga imodzi mwa nkhosa kapena ngʼombe zake kuti akonzere chakudya mlendo amene anafika kwa iye. Mʼmalo mwake anatenga mwana wankhosa wamkazi wa munthu wosauka uja nakonzera chakudya mlendo uja amene anabwera kwa iye.” Davide anapsa mtima kwambiri chifukwa cha munthuyo ndipo anati kwa Natani, “Pali Yehova, munthu amene anachita zimenezi ayenera kufa basi! Iye ayenera kulipira mwana wankhosa wamkaziyo kanayi, chifukwa anachita chinthu chimenechi ndipo analibe chifundo.”

Koma mfumu inayankha Arauna kuti, “Ayi, Ine ndikunenetsa kuti ndikulipira. Sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe yopsereza imene sindinavutikire.” Kotero Davide anagula malo wopunthira tiriguwo ndi ngʼombe ndipo anapereka kwa Araunayo masekeli asiliva makumi asanu. Davide anamanga guwa lansembe la Yehova pamenepo ndipo anaperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Ndipo Yehova anayankha pempherolo mʼmalo mwa dziko lonse, ndipo mliri unatha pa Aisraeli.

Solomoni anakutira golide weniweni mʼkati mwake mwa Nyumbayi, ndipo anayalika maunyolo a golide mopingasa kutsogolo kwa malo wopatulika amene anakutidwa ndi golide. Motero anakuta mʼkati monse ndi golide. Anakutanso ndi golide guwa lansembe la mʼkati mwa chipinda chopatulika.

Anayala golide pansi mu Nyumbamo mʼzipinda zamʼkati ndi zakunja zomwe.

Solomoni anapanganso ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Yehova: guwa lansembe lagolide; tebulo lagolide pamene ankayikapo buledi woperekedwa kwa Mulungu; zoyikapo nyale zagolide weniweni (dzanja lamanja zisanu ndipo zisanu zina ku dzanja lamanzere, mʼkati mwenimweni mwa malo opatulika); maluwa agolide, nyale ndi mbaniro; mbale zagolide weniweni, zozimitsira nyale, mbale zowazira magazi, mbale ndi zofukizira; ndiponso zomangira zitseko zagolide za chipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndiponso za zitseko za chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu.

Golide amene Solomoni ankalandira pa chaka ankalemera makilogalamu 23,000,

Zomwera zonse za Mfumu Solomoni zinali zagolide, ziwiya zonse za Nyumba Yaufumu ya Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide weniweni. Panalibe chimene chinapangidwa ndi siliva chifukwa siliva sankayesedwa kanthu pa nthawi ya Solomoni. Mfumu inali ndi sitima zapamadzi zomwe zinali pa nyanja pamodzi ndi sitima za Hiramu. Kamodzi pakapita zaka zitatu zinkabwera zitanyamula golide, siliva ndi minyanga ya njovu, anyani ndi apusi. Mfumu Solomoni inali yopambana pa chuma ndi pa nzeru kuposa mafumu ena onse pa dziko lapansi.

Mayi wamasiye uja ankapita kukatunga madzi, Eliya anamuyitananso namuwuza kuti, “Chonde munditengerekonso buledi.” Iye anayankha kuti “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, ine ndilibe chakudya china chilichonse, koma kaufa pangʼono mʼmbiya ndi mafuta pangʼono mʼbotolo. Ine ndikutola tinkhuni tochepa kuti ndipite nato ku nyumba ndi kukaphika chakudya changa ndi cha mwana wanga, kuti tikadye kenaka tife.” Eliya anati kwa iye, “Musachite mantha. Pitani mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mundipangire kachakudya pangʼono kuchokera pa ufa umene muli nawo ndi kubwera nako kwa ine, ndipo kenaka mukaphike choti mudye inuyo ndi mwana wanuyo. Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ufa umene uli mʼmbiyamo sudzatha ndipo mafuta amene ali mʼbotolomo sadzathanso mpaka tsiku limene Yehova adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ” Mayi wamasiyeyo anapita nakachita zimene Eliya anamuwuza. Choncho panali chakudya cha Eliya, mayiyo pamodzi ndi banja lake lonse chimene anadya masiku ambiri. Pakuti ufa umene unali mʼmbiya sunathe ndiponso mafuta amene anali mʼbotolo sanathe, monga momwe ananenera Yehova kudzera mwa Eliya.

Elisa anayankha mayiyo kuti, “Kodi ufuna ndikuchitire chiyani? Tandiwuza uli ndi chiyani mʼnyumba mwako?” Mayiyo anayankha kuti, “Mdzakazi wanu alibe kanthu kalikonse koma timafuta pangʼono chabe.” Elisa anati, “Pita kabwereke mitsuko yonse yopanda kanthu kwa anzako. Usakabwereke mitsuko yochepa. Kenaka ukalowe mʼnyumba mwako ndi kudzitsekera iwe ndi ana ako. Mukakatero mukakhuthulire mafuta mʼmitsuko yonseyo, ndipo mtsuko uliwonse ukadzaza muzikawuyika pambali.” Mayi uja anachoka kwa Elisa nakadzitsekera ndi ana ake. Anthu anabweretsa mitsuko kwa iye ndipo ankathiramo mafuta. Mitsuko yonse itadzaza, mayiyo anawuza mwana wake kuti, “Bweretsa mtsuko wina.” Koma iye anayankha kuti, “Mitsuko yonse yatha.” Pamenepo mafuta analeka kutuluka. Mayiyo anapita nakamuwuza munthu wa Mulungu amene anamuyankha kuti, “Pita, kagulitse mafutawo ndipo ukabweze ngongole ija. Ndalama zotsalazo zikakhale zako ndi ana ako.”

Mfumu Hezekiya inapereka siliva yense amene anapezeka mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba zosungiramo chuma cha mfumu. Nthawi imeneyi Hezekiya mfumu ya Yuda anakanganula golide amene anakuta zitseko ndi mphuthu za chipata cha Nyumba ya Yehova namupereka kwa mfumu ya ku Asiriya.

Monga ananenera Yehova, Nebukadinezara anachotsa chuma chonse cha mʼNyumba ya Yehova ndiponso cha mʼnyumba ya mfumu ndipo anatenga ziwiya zonse zagolide za ku Nyumba ya Yehova zimene Solomoni mfumu ya Israeli anapanga. Anatenga anthu onse a mu Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo. Akuluakulu onse pamodzi ndi anthu ankhondo, anthu onse aluso ndi amisiri osula onse pamodzi analipo 10,000. Osauka okha ndiye anatsala mʼdzikomo.

Yabesi analira kwa Mulungu wa Israeli kuti, “Mundidalitse ndipo mukulitse dziko langa! Dzanja lanu likhale pa ine ndipo mundisunge kuti choyipa chisandigwere ndi kundisautsa.” Ndipo Mulungu anamupatsa chopempha chakecho.

Komanso anthu oyandikana nawo ochokera ku Isakara, Zebuloni ndi Nafutali anabweretsa zakudya pa abulu, ngamira, nyulu ndi ngʼombe. Panali ufa wambiri, makeke ankhuyu, ntchintchi za mphesa, vinyo, mafuta, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi, popeza munali chimwemwe mu Israeli.

“Ine movutikira kwambiri ndapereka ku Nyumba ya Mulungu matani 3,400 agolide, matani 34,000 asiliva, ndiponso mkuwa ndi chitsulo, matabwa ndi miyala. Ndipo iwe utha kuwonjezerapo pa zimenezi.

Ine ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu zinthu zanga zonse, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva ndi zitsulo zopangira zinthu zazitsulo, mkuwa wopangira zinthu zamkuwa ndi matabwa opangira zinthu zamatabwa komanso miyala yokongola ya onikisi yokongoletsera, miyala ya maonekedwe osiyanasiyana, ndi miyala yonse yosalala ndi miyala ya marabulo, zonsezi ndapereka zochuluka. Kupatulapo izi, ine modzipereka ku Nyumba ya Mulungu wanga, tsopano ndikupereka chuma changachanga cha golide ndi siliva ku Nyumba ya Mulungu wanga, kuwonjezera pa zimene ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu woyerayu:

Iwo anapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu matani 170 a golide, matani 340 a siliva, matani 620 a mkuwa ndi matani 3,400 a chitsulo. Aliyense amene anali ndi miyala yokongola anayipereka ku nyumba yosungiramo chuma cha Nyumba ya Yehova ndipo amene ankayangʼanira anali Yehieli Mgeresoni. Anthu anakondwa chifukwa cha kupereka mwaufulu kwa atsogoleri awo, pakuti anapereka kwa Yehova mwaufulu ndiponso ndi mtima wonse. Nayenso mfumu Davide anakondwera kwambiri.

Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu; Inu ndinu wolamulira zinthu zonse. Mʼdzanja lanu muli nyonga ndi mphamvu, kukweza ndi kupereka nyonga kwa onse.

“Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndani, kuti tikupatsani mowolowamanja motere? Zinthu zonse zimachokera kwa Inu, ndipo ife takupatsani zomwe zimachokera mʼdzanja lanu.

Inu Yehova Mulungu wathu, zinthu zonse zimene tapereka kumangira Nyumba yanu zachokera mʼdzanja lanu ndipo zonsezi ndi zanu.

Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza izi ndi zokhumba za mtima wako ndipo sunapemphe katundu, chuma kapena ulemu, kapena imfa ya adani ako, ndiponso poti sunapemphe moyo wautali koma nzeru ndi luntha kuti ulamulire anthu anga amene Ine ndakuyika kukhala mfumu yawo, Ine ndidzakupatsa nzeru ndi chidziwitso. Ndipo ndidzakupatsanso katundu, chuma ndi ulemu, zinthu zoti palibe mfumu imene inali nazo iwe usanakhalepo ndipo palibe wina amene adzakhale nazo iweyo ukadzafa.”

Mfumu inasandutsa siliva ndi golide kukhala ngati miyala wamba mu Yerusalemu. Inasandutsanso mkungudza kukhala wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya ku zigwa.

Iyo inalamula anthu amene amakhala mu Yerusalemu kupereka gawo lawo kwa ansembe ndi Alevi kuti iwowo adzipereke ku malamulo a Yehova. Lamuloli atangolilengeza, Aisraeli anapereka mowolowamanja zipatso zoyamba kucha za tirigu, vinyo watsopano, mafuta ndi uchi ndi zonse zomwe nthaka yawo inabereka. Anabweretsa zochuluka kwambiri, chakhumi cha chilichonse.

Tsono anthu ena ndi akazi awo anayamba kudandaula kwambiri chifukwa cha Ayuda anzawo. Ena ankanena kuti, “Ife ndi ana athu aamuna ndi aakazi, tilipo ochuluka kwambiri. Choncho tikufuna tirigu kuti tidye ndi kukhala ndi moyo.” Panali ena amene ankanena kuti, “Ife tikuchita kupereka minda yathu, mitengo yathu ya mphesa ndi nyumba zathu ngati chikole kuti tipeze tirigu chifukwa njala yakula.” Panalinso ena amene ankanena kuti, “ife tinachita kukongola ndalama zoti tipereke msonkho wa minda ndi mitengo yathu ya mphesa kwa mfumu. Ngakhale kuti ndife amodzi ndi abale athuwa, ndipo ngakhalenso ana athu ndi ofanana ndi ana awo, ife tikukakamiza ana athu kuti akhale akapolo. Ena mwa ana athu aakazi atengedwa kale ukapolo. Ife tilibe mphamvu yochitapo kanthu popeza anthu ena anatenga kale minda yathu ndi mitengo yathu ya mphesa.” Nditamva madandawulo awo ndi zimene amanenazi ndinapsa mtima kwambiri. Nditalingalira bwino ndinatsimikiza zoti ndichitepo kanthu ndipo kenaka ndinawadzudzula anthu olemekezeka ndi akuluakuluwo. Ndinawawuza kuti, “Zoona ndithu inu nʼkumalipiritsana chiwongoladzanja chachikulu anthu apachibale nokhanokha!” Choncho ndinayitanitsa msonkhano waukulu kuti ndiwazenge mlandu ndipo ndinati, “Monga zakhaliramu ife tikutha kuwombola abale anthu amene anagulitsidwa ukapolo kwa anthu ena. Kodi tsopano inu mukugulitsanso abale anu kwa anzawo kuti ife tiwumirizidwe kuwawombola?” Iwo anakhala chete, chifukwa sanapeze mawu oti anene. Kotero ndinapitiriza kunena kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino. Kodi inu simungakhale ndi moyo woopa Mulungu wathu kuti tipewe kunyoza kwa adani athu, anthu a mitunda inayi? Ine ndi abale anga ndiponso antchito anga tikuwakongozanso anthuwa ndalama ndi tirigu. Ndipo tiyeni tilekeretu zolandira chiwongoladzanja! Abwezereni lero lomwe minda yawo, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndiponso nyumba zawo. Muwabwezerenso chiwongoladzanja cha ndalama, tirigu, vinyo ndi mafuta zimene munatenga.” Iwo anayankha kuti, “Ife tidzawabwezera zimenezi popanda kupemphapo kanthu kalikonse kwa iwo. Tidzachita monga mwanena.” Pambuyo pake ndinayitanitsa ansembe ndipo pamaso pawo ndinawalumbiritsa atsogoleriwo ndi akuluakuluwo kuti adzachitadi zomwe analonjezazo. Ndipo inenso ndinakutumula chovala changa ndi kuti, “Chimodzimodzinso Mulungu akutumule munthu wosasunga malonjezano ake. Amulande nyumba yake ndi katundu wake ndi kumusandutsa mʼmphawi!” Apo msonkhano wonse unati, “Ameni” natamanda Yehova. Ndipo anthu aja anachita monga analonjezera.

“Ife ansembe, Alevi ndi anthu onse, tachita maere kuti tidziwe pamene banja lathu lililonse lidzabweretsa ku nyumba ya Mulungu wathu pa nthawi yoyikika ya chaka zopereka za nkhuni zoyaka pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo.” “Tilonjezanso kuti tidzabwera ndi zipatso zoyamba kucha za mʼminda yathu ndi zipatso zoyamba kucha za mtengo uliwonse wa zipatso chaka ndi chaka kuti tidzapereke ku Nyumba ya Mulungu wathu.” “Tidzabweranso nawo ku Nyumba ya Mulungu, kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa ndi ana angʼombe oyamba kubadwa monga zalembedwera mu Malamulo. Tidzaperekanso ana oyamba kubadwa a ziweto zathu ndi ana ankhosa oyamba kubadwa.” “Ndiponso ku zipinda za Nyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe tidzaperekanso mtanda wathu wa buledi wa ufa ndi mphatso zina monga zipatso za mtengo uliwonse, vinyo ndi mafuta. Tidzaperekanso kwa alevi chakhumi cha mbewu zathu pakuti alevi ndiwo amasonkhanitsa chakhumi mʼmidzi yathu yonse. Wansembe, mdzukulu wa Aaroni azikhala pamodzi ndi Alevi pamene akulandira chakhumi. Ndipo Alevi azibwera ndi chakhumicho ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda zosungiramo chuma.” Choncho Israeli, kuphatikiza zidzukulu za Alevi, azipititsa zopereka za tirigu, vinyo ndi mafuta ku zipinda zosungiramo katundu wopatulika, komanso kokhala ansembe amene akutumikira pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu ndi anthu oyimba nyimbo. “Kwambiri ife sitidzaleka kusamala Nyumba ya Mulungu.”

Choncho anamupatsa chipinda chachikulu chimene kale ankasungamo zopereka zakudya, lubani, ziwiya, zopereka za chakhumi za tirigu, vinyo ndi mafuta zoyenera kuperekedwa kwa Alevi, oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, komanso mphatso zoyenera kupereka kwa ansembe.

Pambuyo pake Ayuda anayambanso kubwera ndi zopereka zawo za chakhumi cha tirigu, vinyo ndi mafuta kuti ziperekedwe ku nyumba yosungiramo chuma.

ndipo anali ndi nkhosa 7,000, ngamira 3,000, ngʼombe zantchito 1,000 ndi abulu aakazi 500, ndiponso anali ndi antchito ambiri. Iye anali munthu wotchuka kwambiri pakati pa anthu onse a mʼmayiko a kummawa. Ana ake aamuna ankachita phwando mosinthanasinthana mʼnyumba zawo, ndipo ankayitana alongo awo atatu aja kudzadya ndi kumwa nawo.

nati, “Ndinatuluka maliseche mʼmimba mwa amayi anga, namonso mʼmanda ndidzalowa wamaliseche. Yehova ndiye anapereka ndipo Yehova watenga; litamandike dzina la Yehova.”

Adzachisanza chuma chimene anachimeza; Mulungu adzachitulutsa mʼmimba mwa munthuyo.

Pakuti iye anapondereza anthu osauka ndipo anawasiya wopanda thandizo; iyeyo analanda nyumba zimene sanamange.

Zaka zawo zimatha ali mu ulemerero ndipo amatsikira ku manda mwamtendere.

Iwe unkawumiriza abale ako kuti akupatse chikole popanda chifukwa; umalanda anthu zovala zawo ndi kuwasiya amaliseche. Sunawapatse madzi anthu otopa, ndipo unawamana chakudya anthu anjala,

Pamenepo Wamphamvuzonseyo adzakhala golide wako, siliva wako wamtengowapatali.

Anthu amasuntha miyala ya mʼmalire, kuti akuze dziko lawo; amadyetsa ziweto zimene aba. Amalanda abulu a ana amasiye ndipo amatenganso ngʼombe ya mkazi wamasiye ngati chikole. Amachotsa mʼmisewu anthu osauka, ndipo amathamangitsa amphawi onse mʼdziko. Amphawiwo amakhala ngati mbidzi mʼchipululu, amayendayenda kufuna chakudya; dziko lowuma limapereka chakudya cha ana awo. Iwo amakolola za mʼminda ya eni ake, ndipo amakunkha mphesa mʼminda ya anthu oyipa. Amagona maliseche usiku wonse kusowa zovala; pa nthawi yozizira amasowa chofunda. Amavumbwa ndi mvula ya mʼmapiri ndipo amakangamira ku matanthwe kusowa pobisalapo. Amatsomphola mwana wamasiye wa ku bere; ndipo amagwira mwana wakhanda wa mʼmphawi kuti akhale chikole. Amphawi amangoyenda maliseche kusowa zovala; amasenza mitolo ya tirigu, koma nʼkumagonabe ndi njala.

Popeza ine ndinaopa kwambiri chiwonongeko chochokera kwa Mulungu, ndinachitanso mantha ndi ulemerero wake, sindikanatha kuchita zinthu zimenezi. “Ngati ndinayika mtima wanga pa chuma kapena kunena kwa golide wabwino kwambiri kuti, ‘Iwe ndiye chitetezo changa,’ ngati ndinakondwera chifukwa choti chuma changa chinali chambiri, zinthu zimene manja anga anazipeza,

Iye sakondera akalonga ndipo salemekeza anthu olemera kupambana osauka, pakuti onsewa ndi ntchito ya manja ake?

Yobu atawapempherera abwenzi ake aja, Yehova anamubwezera chuma chake ndipo anamupatsa mowirikiza kuposa zomwe anali nazo kale.

Mʼdziko monsemo munalibe akazi okongola ngati ana a Yobu, ndipo abambo awo anawapatsa cholowa pamodzi ndi alongo awo.

Tandipempha, ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako; malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.

Koma osowa sadzayiwalika nthawi zonse, kapena chiyembekezo cha ozunzika kutayika nthawi zonse.

Iye amatamandira zokhumba za mu mtima wake; amadalitsa aumbombo ndi kuchitira chipongwe Yehova.

amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanja ndipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa. Iye amene amachita zinthu zimenezi sadzagwedezeka konse.

Yehova, Inu mwandipatsa cholowa changa ndi chikho changa; mwateteza kolimba gawo langa. Malire a malo anga akhala pabwino; ndithudi, ine ndili cholowa chokondweretsa kwambiri.

Salimo la Davide. Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.

Wopani Yehova inu oyera mtima ake, pakuti iwo amene amaopa Iye sasowa kanthu.

Thupi langa lidzafuwula mokondwera, “Ndani angafanane nanu Yehova? Mumalanditsa osauka kwa amene ali ndi mphamvu zambiri, osauka ndi osowa kwa iwo amene amawalanda.”

Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino; khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika. Udzikondweretse wekha mwa Yehova ndipo Iye adzakupatsa zokhumba za mtima wako.

Ine ndinali wamngʼono ndipo tsopano ndakalamba koma sindinaonepo olungama akusiyidwa kapena ana awo akupempha chakudya. Iwo ndi owolowamanja nthawi zonse ndipo amabwereketsa mwaufulu; ana awo adzadalitsika.

olungama adzalandira dziko ndipo adzakhazikikamo kwamuyaya.

Komabe Ine ndine wosauka ndi wosowa; Ambuye andiganizire. Inu ndinu thandizo langa ndi wondiwombola wanga; Inu Mulungu wanga, musachedwe.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso. Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake; Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake.

Iwo amene adalira kulemera kwawo ndi kutamandira kuchuluka kwa chuma chawo? Palibe munthu amene angawombole moyo wa mnzake kapena kuperekera mnzake dipo kwa Mulungu. Dipo la moyo ndi la mtengowapatali, palibe malipiro amene angakwanire,

“Pano tsopano pali munthu amene sanayese Mulungu linga lake, koma anakhulupirira chuma chake chambiri nalimbika kuchita zoyipa!”

Musadalire kulanda mwachinyengo kapena katundu wobedwa; ngakhale chuma chanu chichuluke, musayike mtima wanu pa icho.

Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira, wozunzika amene alibe wina womuthandiza. Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa ndi kupulumutsa osowa ku imfa.

Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye; mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika. Landitsani anthu ofowoka ndi osowa; apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.

Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango; Yehova amapereka chisomo ndi ulemu; Iye sawamana zinthu zabwino iwo amene amayenda mwangwiro.

Iye adzayankha pemphero la anthu otayika; sadzanyoza kupempha kwawo.

Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake, ndipo chilungamo chake ndi chosatha.

Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu, amene amachita ntchito yake mwachilungamo.

Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbi ndi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala; amawakhazika pamodzi ndi mafumu, pamodzi ndi mafumu a anthu ake.

Koma mafano awo ndi siliva ndi golide, opangidwa ndi manja a anthu.

Yehova akuwonjezereni madalitso; inuyo pamodzi ndi ana anu. Mudalitsidwe ndi Yehova, Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Ndingamubwezere chiyani Yehova, chifukwa cha zokoma zake zonse zimene wandichitira?

Maso a onse amayangʼana kwa Inu, ndipo Inu mumawapatsa chakudya chawo pa nthawi yoyenera. Mumatsekula dzanja lanu ndi kukwaniritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.

Awa ndiwo mathero a anthu opeza chuma mwankhanza; chumacho chimapha mwiniwake.

ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika, ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova; ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova.

Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse; zokolola zonse zoyamba kucha uzilemekeza nazonso Yehova. Ukatero nkhokwe zako zidzadzaza ndi zinthu zambiri, ndiponso mitsuko yako idzadzaza ndi vinyo.

Wodala munthu amene wapeza nzeru, munthu amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru ndi labwino kuposa la siliva, phindu lakelo ndi labwino kuposanso golide. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali; ndipo zonse zimene umazikhumba sizingafanane ndi nzeru.

Usaleke kuchitira zabwino amene ayenera kulandira zabwino, pamene uli nazo mphamvu zochitira zimenezi. Usanene kwa mnansi wako kuti, “Pita, uchite kubweranso. Ndidzakupatsa mawa” pamene uli nazo tsopano.

Mwana wanga, ngati wamuperekera mnansi wako chikole, ngati walonjeza kumulipirira mlendo, ngati wagwidwa ndi zimene iwe unanena, wakodwa ndi mawu a mʼkamwa mwako. Tsono popeza iwe mwana wanga wadziponya mʼmanja mwa mnansi wako, chita izi kuti udzipulumutse: pita msanga ukamupemphe mnansi wako; kuti akumasule! Usagone tulo, usawodzere. Dzipulumutse monga imachitira mphoyo mʼdzanja la mlenje, ndi monga imachitira mbalame mu msampha wa munthu wosaka.

Paja anthu sayinyoza mbala ikaba chifukwa chakuti ili ndi njala. Komabe ngati mbalayo igwidwa iyenera kulipira kasanu nʼkawiri, ngakhale kulandidwa katundu wa mʼnyumba mwake.

Ine ndili ndi chuma ndi ulemu, chuma ndi kupindula pa ntchito kokhazikika. Chipatso changa ndi chabwino kuposa golide, ngakhale golide wosalala; zimene ine ndimabereka zimaposa siliva wabwino kwambiri. Ndimachita zinthu zolungama. Ine sindipatuka mʼnjira za chilungamo. Ndimapereka chuma kwa amene amandikonda ndi kudzaza nyumba zawo zosungiramo chuma.

Chuma chochipeza mwachinyengo sichipindulitsa, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa. Yehova salola kuti munthu wolungama azikhala ndi njala; koma amalepheretsa zokhumba za anthu oyipa. Wochita zinthu mwaulesi amasauka, koma wogwira ntchito mwakhama amalemera. Amene amakolola nthawi yachilimwe ndi mwana wanzeru, koma amene amangogona nthawi yokolola ndi mwana wochititsa manyazi.

Chuma cha munthu wolemera ndiye chitetezo chake; koma umphawi ndiye chiwonongeko cha osauka.

Mawu a munthu wolungama ali ngati siliva wabwino kwambiri, koma mtima wa munthu woyipa ndi wopanda phindu. Milomo ya anthu olungama imalimbikitsa ambiri; koma chitsiru chimafa chifukwa chosowa nzeru. Mdalitso wa Yehova ndiwo umabweretsa chuma, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.

Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa, koma amakondwera ndi muyeso woyenera.

Woperekera mlendo chikole adzapeza mavuto, koma wodana ndi za chikole amakhala pa mtendere. Mkazi wodekha amalandira ulemu, koma amuna ankhanza amangopata chuma.

Munthu wina amapatsako anzake zinthu mwaufulu nʼkumangolemererabe; wina amamana chomwe akanatha kupereka, koma kumanka nasawukabe. Munthu wopereka mowolowamanja adzalemera; iye amene amathandiza ena iyenso adzathandizidwa. Anthu amatemberera womana anzake chakudya, koma madalitso amakhala pamutu pa munthu amene amagulitsa chakudyacho. Iye amene amafunafuna zabwino mwakhama amapeza zabwinozo, koma wofunafuna zoyipa zidzamupeza. Aliyense amene amadalira chuma chake adzafota, koma wolungama adzaphukira ngati tsamba lobiriwira.

Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu, koma munthu wakhama adzalemera.

Wina amadziyesa kuti ndi wolemera chonsecho alibe kanthu kalikonse; munthu wina amaoneka ngati wosauka chonsecho ali ndi chuma chambiri. Chuma cha munthu wolemera chitha kuwombola moyo wake, koma munthu wosauka amamva chidzudzulo.

Chuma chochipeza mofulumira chidzatha pangʼonopangʼono koma chuma chosonkhanitsidwa pangʼonopangʼono chidzachulukirachulukira.

Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake cholowa, koma chuma cha munthu wochimwa amachilandira ndi olungama.

Munthu wosauka ngakhale anansi ake omwe amamuda, koma munthu wolemera ali ndi abwenzi ambiri. Wonyoza mnansi wake ndi wochimwa koma ndi wodala amene amachitira chifundo anthu osowa. Kodi amene amakonzekera zoyipa sasochera? Koma amene amakonzekera zabwino anthu amawaonetsa chikondi ndi kukhulupirika. Ntchito iliyonse imakhala ndi phindu, koma kuyankhulayankhula kumabweretsa umphawi.

Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake, koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu.

Munthu wolungama amakhala ndi chuma chambiri, zimene woyipa amapindula nazo zimamugwetsa mʼmavuto.

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono nʼkumaopa Yehova, kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri uli pamavuto. Kuli bwino kudyera ndiwo zamasamba pamene pali chikondi, kusiyana ndi kudyera nyama yangʼombe yonenepa pamene pali udani.

Munthu wofuna phindu mwachinyengo amavutitsa banja lake, koma wodana ndi ziphuphu adzakhala ndi moyo.

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono zozipeza mwachilungamo, kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri zozipeza popanda chilungamo.

Nʼkwabwino kwambiri kupeza nzeru kupambana golide. Kukhala womvetsa bwino zinthu nʼkwabwino kupambana ndi kukhala ndi siliva.

Nʼkwabwino kudya mkute koma pali mtendere, kuposa kuchita madyerero mʼnyumba mʼmene muli mikangano. Kapolo wanzeru adzalamulira mwana wochititsa manyazi, ndipo kapoloyo adzagawana nawo cholowa ngati mmodzi mwa abale. Siliva amamuyesa mʼngʼanjo ndipo golide amamuyesa mʼngʼanjo, koma Yehova amayesa mitima.

Munthu wopanda nzeru amavomereza zopereka chikole ndipo iyeyo amasanduka chikole cha mnansi wake.

Munthu wosauka amapempha koma munthu wolemera amayankha mwaukali.

Amene amakomera mtima osauka amachita ngati wakongoletsa Yehova, ndipo Yehovayo ndiye adzamubwezere.

Munthu waulesi satipula mʼmunda pa nthawi yoyenera; kotero pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzapeza kanthu kalikonse.

Masikelo ndi miyeso ya zinthu imene ili yachinyengo zonsezi Yehova zimamunyansa.

Chakudya chochipeza mwachinyengo chimukomera munthu, koma pa mapeto pake chimasanduka ngati mchenga mʼkamwa mwake.

Cholowa chochipeza mofulumira poyamba, sichidzakhala dalitso pa mapeto pake.

Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa zinthu zake; koma aliyense wochita zinthu mofulumira amadzakhala wosauka. Chuma chochipeza ndi mawu onyenga ndi chosakhalitsa ndipo chimakola anthu mu msampha wa imfa.

Amene atsekera mʼkhutu mwake wosauka akamalira, nayenso adzalira koma palibe adzamuyankhe.

Aliyense wokonda zisangalalo adzasanduka mʼmphawi, ndipo wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera. Anthu oyipa adzakhala chowombolera cha anthu olungama ndipo osakhulupirika chowombolera anthu olungama mtima. Nʼkwabwino kukhala mʼchipululu kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wopsa mtima msanga. Munthu wanzeru samwaza chuma chake, koma wopusa amachiwononga.

Chilakolako cha munthu waulesi chidzamupha yekha chifukwa manja ake amangokhala goba osagwira ntchito. Tsiku lonse anthu oyipa amasirira zambiri, koma anthu olungama amapereka mowolowamanja.

Mbiri yabwino ndi yofunika kuposa chuma chambiri; kupeza kuyanja nʼkwabwino kuposa siliva kapena golide. Wolemera ndi wosauka ndi ofanana; onsewa anawalenga ndi Yehova.

Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womukongozayo. Amene amafesa zoyipa amakolola mavuto, ndipo ndodo yaukali wake idzathyoka. Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsika, pakuti iye amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.

Amene amapondereza anthu osauka kuti awonjezere chuma chake, ndiponso amene amapereka mphatso kwa anthu olemera onsewa adzasauka.

Mʼmphawi usamubere chifukwa ndi osauka, ndipo usawapondereze anthu osowa mʼbwalo la milandu, pakuti Yehova adzawateteza pa mlandu wawo ndipo adzalanda moyo onse amene amawalanda iwo.

Usakhale munthu wopereka chikole kapena kukhala mboni pa ngongole; ngati ulephera kupeza njira yolipirira adzakulanda ngakhale bedi lako lomwe.

Usadzitopetse wekha ndi kufuna chuma, ukhale ndi nzeru ya kudziretsa. Ukangoti wachipeza chumacho uwona posachedwa kuti palibepo. Chumacho chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi ndi kuwuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.

Paja anthu oledzera ndi adyera amadzakhala amphawi ndipo aulesi adzavala sanza.

Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu odziwa zinthu; Munthu wodziwa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chamtengowapatali ndiponso chabwino.

Ukati, “Bwanji ndigone pangʼono,” kapena “Ndiwodzereko pangʼono,” kapenanso “Ndipinde manja pangʼono kuti ndipumule,” umphawi udzafika pa iwe ngati mbala ndipo usiwa udzakupeza ngati munthu wachifwamba.

Mawu amodzi woyankhulidwa moyenera ali ngati zokongoletsera zagolide mʼzotengera zasiliva.

Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya kuti adye; ngati ali ndi ludzu mupatse madzi kuti amwe. Pochita izi, udzamusenzetsa makala a moto pa mutu pake, ndipo Yehova adzakupatsa mphotho.

Paja chuma sichikhala mpaka muyaya, ndipo ufumu sukhala mpaka mibado yonse.

Munthu wosauka wa makhalidwe abwino aposa munthu wolemera wa makhalidwe okhotakhota. Amene amasunga malamulo ndi mwana wozindikira zinthu, koma amene amayenda ndi anthu adyera amachititsa manyazi abambo ake. Amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja chochuluka amakundikira chumacho anthu ena, amene adzachitira chifundo anthu osauka.

Munthu wolemera amadziyesa kuti ndi wanzeru, koma munthu wosauka amene ali ndi nzeru zodziwa zinthu amamutulukira.

Amene amalima mʼmunda mwake adzakhala ndi chakudya chochuluka, koma amene amangosewera adzakhala mʼmphawi. Munthu wokhulupirika adzadalitsika kwambiri, koma wofuna kulemera mofulumira adzalangidwa. Kukondera si kwabwino, ena amachita zolakwazo chifukwa cha kachidutswa ka buledi. Munthu wowumira amafunitsitsa kulemera koma sazindikira kuti umphawi udzamugwera. Amene amadzudzula mnzake potsiriza pake mnzakeyo adzamukonda kwambiri, kupambana amene amanena mawu oshashalika. Amene amabera abambo ake kapena amayi ake namanena kuti “kumeneko sikulakwa,” ndi mnzake wa munthu amene amasakaza.

Amene amapereka kwa osauka sadzasowa kanthu, koma amene amatsinzina maso ake adzatembereredwa kwambiri.

Munthu wolungama amasamalira anthu osauka, koma woyipa salabadira zimenezi.

Woyenda ndi munthu wakuba ndi mdani wa moyo wake womwe; amalumbira koma osawulula kanthu.

Choyamba, mundichotsere kutali nane mabodza ndi chinyengo. Chachiwiri, ndisakhale mʼmphawi kapena munthu wachuma. Koma muzindidyetsa chakudya chondikwanira tsiku ndi tsiku kuopa kuti ndikakhuta kwambiri ndingayambe kukukanani, nʼkumanena kuti, ‘Yehova ndiye yaninso?’ Kuopanso kuti ndikakhala wosauka ndingayambe kuba, potero nʼkuyipitsa dzina la Mulungu wanga.”

Yankhula ndi kuweruza mwachilungamo. Uwateteze amphawi ndi osauka. Kodi mkazi wangwiro angathe kumupeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala yamtengowapatali.

Iye amachitira chifundo anthu osauka ndipo amapereka chithandizo kwa anthu osowa.

Ndinagwira ntchito zikuluzikulu: Ndinadzimangira nyumba ndi kuwoka mipesa. Ndinalima madimba ndi minda yamitengo; ndipo ndinadzalamo mitengo ya zipatso za mitundu yonse. Ndinakumba mayiwe osungiramo madzi woti ndizithirira minda ya mitengo yodzalidwa ija. Ndinagula akapolo aamuna ndi akapolo aakazi, ndiponso ndinali ndi akapolo ena omwe anabadwira mʼnyumba mwanga. Ndinalinso ndi ngʼombe ndi nkhosa zambiri kupambana aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. Ndinadzikundikira siliva ndi golide, ndiponso chuma chochokera kwa mafumu ndi madera awo. Ndinali ndi amuna ndi akazi oyimba ndiponso azikazi; zinthu zokondweretsa mtima wa munthu. Ndinali munthu wotchuka kupambana wina aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. Mu zonsezi nzeru zanga zinali nane. Sindinadzimane chilichonse chimene maso anga anachifuna; mtima wanga sindinawumane zokondweretsa. Mtima wanga unakondwera ndi ntchito yanga yonse, ndipo iyi ndiyo inali mphotho ya ntchito zanga zonse zolemetsa. Koma pamene ndinayamba kuyangʼanayangʼana zonse zimene ndinachita ndi manja anga, ndi zimene ndinazivutikira kuti ndizipeze, zonsezi zinali zopandapake; kungodzivuta chabe, palibe chomwe ndinapindula pansi pano.

Aliyense amene amakonda ndalama sakhutitsidwa ndi ndalamazo; aliyense amene amakonda chuma sakhutitsidwa ndi zimene amapeza. Izinso ndi zopandapake.

Munthu anabadwa wamaliseche kuchokera mʼmimba mwa amayi ake, ndipo monga iye anabadwira, adzapitanso choncho. Pa zonse zimene iye anakhetsera thukuta palibe nʼchimodzi chomwe chimene adzatenge mʼmanja mwake.

Komatu pamene Mulungu apereka chuma kwa munthu aliyense ndi zinthu zina, ndi kulola kuti akondwere ndi chumacho, munthuyo alandire chumacho ndi kusangalala ndi ntchito yake, imene ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.

Mulungu amapereka chuma, zinthu ndi ulemu kwa munthu, kotero kuti munthuyo sasowa kanthu kalikonse kamene akukalakalaka, koma Mulungu samulola kuti adyerere zinthuzo, ndipo mʼmalo mwake amadyerera ndi mlendo. Izi ndi zopandapake, ndi zoyipa kwambiri.

Phwando ndi lokondweretsa anthu, ndipo vinyo ndi wosangalatsa moyo, koma ndalama ndi yankho la chilichonse.

Dzala mbewu zako mmawa ndipo madzulo usamangoti manja lobodo, pakuti sudziwa chimene chidzapindula, mwina ichi kapena icho, kapena mwina zonse ziwiri zidzachita bwino.

Dziko lawo ndi lodzaza ndi siliva ndi golide; ndipo chuma chawo ndi chosatha. Dziko lawo ndi lodzaza ndi akavalo; ndipo magaleta awo ankhondo ngosawerengeka. Dziko lawo ndi lodzaza ndi mafano; iwo amapembedza ntchito ya manja awo, amagwadira zomwe anapanga ndi zala zawo.

kuwalanda anthu osauka ufulu wawo ndi kumana chilungamo osautsidwa pakati pa anthu anga, amalanda zinthu za akazi amasiye ndi kubera ana amasiye.

Koma munthu wolemekezeka amalingaliranso kuchita zinthu zabwino, Iye amakhazikika pa zinthu zabwinozo.

“Bwerani, inu nonse amene muli ndi ludzu, bwerani madzi alipo; ndipo inu amene mulibe ndalama bwerani, mudzagule chakudya kuti mudye! Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka osalipira ndalama, osalipira chilichonse. Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene samadya, ndipo mukuwononga malipiro anu pa zinthu zimene sizikhutitsa? Tamverani, mvetsetsani zimene ndikunena kuti mudye zimene zili zabwino; ndipo mudzisangalatse.

Anthu anjala kodi mwawagawira chakudya chanu? Osowa ndi ongoyendayenda, kodi mwawapatsa malo ogona? Munthu wausiwa kodi mwamupatsa chovala?

Ndipo ngati mudyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu oponderezedwa, pamenepo kuwala kwanu kudzaonekera mu mdima, ndipo usiku wanu udzakhala ngati usana.

Ukadzaona zimenezi udzasangalala kwambiri, mtima wako udzalumpha ndi kudzaza ndi chimwemwe; chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe chuma cha mitundu ya anthu chidzabwera kwa iwe. Gulu la ngamira lidzaphimba dziko lako, ngamira zingʼonozingʼono zidzachokera ku Midiyani ndi ku Efai. Ndipo onse a ku Seba adzabwera atanyamula golide ndi lubani uku akutamanda Yehova.

Ndidzakupatsa golide mʼmalo mwa mkuwa, ndi siliva mʼmalo mwa chitsulo. Ndidzakupatsa mkuwa mʼmalo mwa thabwa ndi chitsulo mʼmalo mwa miyala. Olamulira ako adzakhala a mtendere. Ndidzasandutsa okulamulira kuti akhale achilungamo.

Iwe Yerusalemu, ndiwe bwinja! Ukutanthauza chiyani kuvala zovala zofiira ndi kuvalanso zokometsera zagolide? Ngakhale udzikonze maso ako powapaka zokometsera, ukungodzivuta chabe. Zibwenzi zako zikukunyoza; zikufuna kuchotsa moyo wako.

Anthu ako ndi chuma chako ndidzazipereka kwa ofunkha popanda malipiro, chifukwa cha machimo anu onse a mʼdziko lanu lonse.

Inu muli ndi mitsinje yambiri ndi chuma chambiri. Koma chimaliziro chanu chafika, moyo wanu watha.

Anthu ake onse akubuwula pamene akufunafuna chakudya; asinthanitsa chuma chawo ndi chakudya kuti akhale ndi moyo. “Inu Yehova, taonani ndipo ganizirani, chifukwa ine ndanyozeka.”

“Iwo adzataya siliva wawo mʼmisewu ndipo golide wawo adzakhala chinthu chonyansa. Siliva ndi golide wawo sizidzatha kuwapulumutsa pa tsiku la ukali wa Yehova. Chuma chawochi sichidzawathandiza kuthetsa njala, kapena kukhala okhuta, pakuti ndicho chinawagwetsa mʼmachimo.

“ ‘Tsono tchimo la mʼbale wako Sodomu linali ili: Iye ndi ana ake aakazi ankanyadira kuchuluka kwa chakudya ndi chuma chawo. Koma sanalabadireko kuthandiza osauka ndi aumphawi. Anali odzitukumula ndipo ankachita zonyansa pamaso panga. Nʼchifukwa chake ndinawachotsa monga mmene waoneramu.

Iye sapondereza munthu wina aliyense, koma amabwezera wangongole nʼchigwiriro chake. Iye salanda zinthu za osauka, koma amapereka chakudya kwa anthu anjala, ndipo amapereka zovala kwa anthu ausiwa. Iye sakongoletsa ndalama mwa katapira, kapena kulandira chiwongoladzanja chachikulu. Amadziletsa kuchita zoyipa ndipo sakondera poweruza milandu. Iye amatsatira malangizo anga, ndipo amasunga malamulo anga mokhulupirika. Munthu ameneyo ndi wolungama; iye adzakhala ndithu ndi moyo, akutero Ambuye Yehova.

Iye amapondereza munthu wosauka ndi wosowa. Amalanda zinthu za osauka. Sabweza chikole cha munthu wa ngongole. Iye amatembenukira ku mafano nachita zonyansa. Iye amakongoletsa mwa katapira ndipo amalandira chiwongoladzanja chachikulu. Kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu! Chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi, adzaphedwa ndipo adzalandira chilango chomuyenera.

Mwa iwe muli anthu amene amalandira ziphuphu kuti aphe anzawo; ena amachita katapira ndi kupeza phindu loposera muyeso; enanso amapeza phindu mwachinyengo poopseza anzawo. Ndipo mwandiyiwala Ine, akutero Ambuye Yehova.

Anthu a mʼdzikomo amasautsa anzawo ndi kulanda anthu osowa. Amazunza anthu osauka ndi amphawi. Amavutitsa alendo posawachitira zinthu mwachilungamo. “Ndinafunafuna munthu pakati pawo woti amange linga, woti ayimirire dziko pamaso panga kundipepesa kuti ndisaliwononge, koma sindinamupeze.

Mwa nzeru zako ndi kumvetsa kwako unadzipezera chuma ndipo unasonkhanitsa golide ndi siliva mʼnyumba zosungira chuma chako. Ndi nzeru zako zochitira malonda unachulukitsa chuma chako ndipo wayamba kunyada chifukwa cha chuma chakocho. “ ‘Choncho Ine Ambuye Yehova ndikuti, “ ‘Popeza umadziganizira kuti ndiwe mulungu, Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo, anthu ankhanza, kuti adzalimbane nawe. Adzakuthira nkhondo kuti awononge zonse zimene unazipeza ndi nzeru zako, ndipo adzawononga kunyada kwakoko.

Iwe udzanena kuti, ‘Ndikukathira nkhondo dziko la midzi yopanda mipanda; ndikathira nkhondo anthu okhala mwamtendere, anthu amene satchinjirizidwa ndi mipanda, zipata kapena mipiringidzo. Ndipita kukalanda chuma chawo ndi kukafunkha zinthu zawo. Ndidzalimbana ndi midzi imene kale inali mabwinja. Ndikathira nkhondo anthu amene anasonkhanitsidwa kuchokera kwa anthu a mitundu ina. Iwowa ali ndi ziweto zambiri, katundu wochuluka ndiponso amakhala pakatikati pa dziko lapansi.’ Anthu a ku Seba, a ku Dedani ndiponso amalonda a ku Tarisisi pamodzi ndi midzi yake yonse adzakufunsa kuti, ‘Kodi wabwera kudzafunkha? Kodi wasonkhanitsa gulu lako la nkhondo kudzalanda chuma, kudzatenga siliva ndi golide, ziweto ndi katundu kuti zikhale zofunkha zochuluka?’ ”

Pamene Belisazara ankamwa vinyo, analamula kuti ziwiya zagolide ndi zasiliva zimene Nebukadinezara abambo ake anakatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu zikatengedwe kuti mfumu ndi akalonga ake, akazi ake ndi azikazi amweremo. Choncho anabweretsa ziwiya zagolide zimene anazitenga mʼNyumba ya Mulungu; ndipo mfumu ndi akalonga ake, akazi ake ndi azikazi ake anamweramo. Akumwa vinyo, anatamanda milungu yagolide ndi siliva, yamkuwa, chitsulo, yamtengo ndi mwala.

Ansembe ankati akachuluka iwo ankandichimwiranso kwambiri; iwo anasinthanitsa ulemerero wawo ndi chinthu china chonyansa.

Munthu wamalonda amagwiritsa ntchito masikelo achinyengo; iyeyo amakonda kubera anthu. Efereimu amadzitama ponena kuti, “Ndine wolemera kwambiri; ndili ndi chuma chambiri. Palibe amene angandiloze chala chifukwa cha kulemera kwanga.”

“Ine ndidzakubwezerani zonse zimene zinawonongedwa ndi dzombe, dzombe lalikulu ndi dzombe lalingʼono, dzombe lopanda mapiko ndi dzombe lowuluka; gulu langa lalikulu la nkhondo limene ndinalitumiza pakati panu. Mudzakhala ndi chakudya chambiri, mpaka mudzakhuta, ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu, amene wakuchitirani zodabwitsa; ndipo anthu anga sadzachitanso manyazi.

Mumapondereza munthu wosauka ndi kumukakamiza kuti akupatseni tirigu. Nʼchifukwa chake, ngakhale mwamanga nyumba zamiyala yosema, inuyo simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, inu simudzamwa vinyo wake. Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu.

Imvani izi, inu amene mumapondereza anthu osowa ndipo simulabadira anthu osauka a mʼdzikomu. Mumanena kuti, “Kodi chikondwerero cha mwezi watsopano chidzatha liti kuti tigulitse zinthu? Ndipo tsiku la Sabata litha liti kuti tigulitse tirigu, kuti tichepetse miyeso, kukweza mitengo kuti tibere anthu ndi miyeso ya chinyengo, tigule osauka ndi ndalama zasiliva ndi osowa powapatsa nsapato, tigulitse ngakhale mungu wa tirigu?”

Amasirira minda ndi kuyilanda, amasirira nyumba ndi kuzilanda. Amatenga nyumba ya munthu mwachinyengo, munthu mnzawo kumulanda cholowa chake.

“Kodi onse ogwidwawo sadzamunyoza ndi kumunyogodola ponena kuti, “Tsoka kwa amene amadzikundikira katundu amene si wake ndipo amadzilemeretsa ndi chuma cholanda! Kodi izi zidzachitika mpaka liti? Kodi angongole ako sadzakuwukira mwadzidzidzi? Kodi sadzadzuka ndi kukuchititsa mantha? Pamenepo iwe udzalandidwa kalikonse.

Chuma chawo chidzafunkhidwa, nyumba zawo zidzagwetsedwa. Adzamanga nyumba, koma osakhalamo; adzadzala minda ya mpesa koma sadzamwako vinyo wake.”

Ngakhale siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa pa tsiku la ukali wa Yehova. Dziko lonse lapansi lidzanyeka mʼmoto wa nsanje yake chifukwa adzakantha modzidzimutsa onse okhala pa dziko lapansi.

‘Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanganso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Ndinawawuza kuti, “Ngati mukuganiza kuti zili bwino, patseni malipiro anga; koma ngati si choncho, sungani malipirowo.” Kotero anandipatsa ndalama zasiliva makumi atatu. Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ziponye kwa wowumba mbiya,” mtengo woyenera umene anapereka pondigula Ine! Choncho ndinatenga ndalama zasiliva makumi atatu ndi kuziponya mʼnyumba ya Yehova kwa wowumba mbiya.

“Kodi munthu angathe kuba za Mulungu? Komatu inu mumandibera. “Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi timakuberani motani?’ “Pa zakhumi ndi pa zopereka. Mtundu wanu wonse ndinu otembereredwa, chifukwa mukundibera. Bweretsani chakhumi chathunthu ku nyumba yosungira, kuti mukhale chakudya mʼnyumba mwanga.” Akutero Yehova Wamphamvuzonse, “Tandiyesani, ndipo muone ngati sindidzatsekula zipata zakumwamba, ndi kukugwetserani madalitso ochuluka amene mudzasowe malo owayikamo.

Pofika ku nyumbayo, anaona mwanayo pamodzi ndi amayi ake Mariya, ndipo anagwada namulambira Iye. Pomwepo anamasula chuma chawo ndi kupereka mphatso zawo za ndalama zagolide, lubani ndi mure.

“Odala ndi amene ali osauka mu mzimu, chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.

Odala ndi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo, chifukwa adzakhutitsidwa.

Ndipo ngati wina afuna kukuzenga mlandu kuti akulande malaya ako, umupatsenso mkanjo wako. Ngati wina akukakamiza kuti uyende naye mtunda umodzi, iwe uyende naye mitunda iwiri. Wina akakupempha kanthu umupatse, ndipo wofuna kubwereka usamukanize.

“Samalani kuti musachite ntchito zanu zolungama pamaso pa anthu kuti akuoneni. Popeza ngati mutero simudzalandira mphotho yochokera kwa Atate anu akumwamba. “Pamene mupereka zachifundo, musachite modzionetsera monga amachita achiphamaso mʼmasunagoge ndi pa misewu kuti atamidwe ndi anthu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti iwowo alandiriratu mphotho yawo yonse. Koma pamene mupereka zachifundo, dzanja lanu lamanzere lisadziwe chimene dzanja lanu lamanja likuchita, kotero kuti kupereka kwanu kukhale mwachinsinsi. Ndipo Atate anu amene amaona zochitika mwachinsinsi, adzakupatsani mphotho.

Mutipatse chakudya chathu chalero. Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso tawakhululukira amangawa athu.

“Musadziwunjikire chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga ndi pamene mbala zimathyola ndi kuba. Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba. Pakuti kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhala komweko.

“Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri. Pakuti pena adzamuda mmodzi ndi kukonda winayo kapena adzagwira ntchito mokhulupirika kwa mmodzi, nadzanyoza winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma pa nthawi imodzi.

“Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena mudzamwa chiyani; kapenanso za thupi lanu kuti mudzavala chiyani. Kodi moyo suposa chakudya? Kodi thupi siliposa zovala? Onani mbalame zamlengalenga sizifesa kapena kukolola kapena kusunga mʼnkhokwe komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Kodi inu simuziposa kwambiri? Kodi ndani wa inu podandaula angathe kuwonjeza ora limodzi pa moyo wake? “Ndipo bwanji inu mudera nkhawa za zovala? Onani makulidwe a maluwa akutchire. Sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu. Ndikukuwuzani kuti angakhale Solomoni mu ulemerero wake sanavale mofanana ndi limodzi la maluwa amenewa. Ngati umu ndi mmene Mulungu avekera udzu wa kutchire umene ulipo lero ndipo mawa uponyedwa ku moto, kodi sadzakuvekani koposa? Aa! Inu a chikhulupiriro chochepa! Chifukwa chake musadere nkhawa ndi kuti, ‘Tidzadya chiyani?’ kapena ‘Tidzamwa chiyani?’ kapena ‘Tidzavala chiyani?’ Pakuti anthu akunja amazifuna zinthu zonsezi ndipo Atate anu akumwamba adziwa kuti musowa zimenezi. Koma muyambe mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake ndipo zinthu zonsezi zidzapatsidwa kwa inu. Chifukwa chake musadere nkhawa ndi za mawa, popeza tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.

“Pemphani ndipo mudzapatsidwa; funafunani ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsekulirani. Pakuti wopempha aliyense amalandira; ndi wofuna amapeza; ndipo iye amene agogoda, adzamutsekulira.

Tsono ngati inu woyipitsitsa mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanga Atate anu akumwamba sadzapereka mphatso zabwino kwa iwo amene amupempha?

Yesu anayankha kuti, “Nkhandwe zili ndi mapanga ndi mbalame zamlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa Munthu alibe malo ogona ngakhale potsamira mutu wake.”

“Musatenge ndalama zagolide kapena zasiliva kapena zakopala mʼzikwama mwanu; musatenge thumba la paulendo, kapena malaya awiri kapena nsapato kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira chakudya chake.

Ngati aliyense apereka madzi ozizira a mʼchikho kwa mmodzi wa angʼonoangʼono awa chifukwa cha kuti ndi ophunzira anga, ndikuwuzani zoona, ndithudi sadzataya mphotho yake.”

Koma mbewu zina zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinabala zipatso 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa.

Zimene zinafesedwa pakati pa minga, ndi munthu amene amamva mawu koma nkhawa za moyo uno ndi chinyengo cha chuma zimalepheretsa mawuwo kuti abale chipatso. Koma zimene zinafesedwa pa nthaka yabwino, ndi munthu amene amamva mawu ndipo amawazindikira. Iye amabala zipatso zokwanira 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa.”

“Ufumu wakumwamba ufanana ndi chuma chobisika mʼmunda. Munthu atachipeza anachibisanso ndipo ndi chimwemwe anapita nakagulitsa zonse anali nazo, nakagula mundawo. “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi wogulitsa malonda amene amafuna ngale zabwino. Atapeza imodzi ya mtengowapatali, iye anapita nakagulitsa chilichonse anali nacho ndi kukayigula.”

Kodi munthu adzapindula chiyani ngati atapeza zonse za dziko lapansi nataya moyo wake? Kapena munthu angapereke chiyani chosinthana ndi moyo wake?

Yesu ndi ophunzira ake atafika ku Kaperenawo, wolandira msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu anabwera kwa Petro namufunsa kuti, “Kodi aphunzitsi anu sapereka msonkho wa Nyumba ya Mulungu?” Iye anayankha kuti, “Inde amapereka.” Petro atalowa mʼnyumba, Yesu ndiye anayamba kuyankhula. Ndipo anamufunsa kuti, “Ukuganiza bwanji Simoni, kodi mafumu a dziko lapansi amalandira msonkho kuchokera kwa ana awo kapena kwa ena?” Petro anayankha kuti, “Kuchokera kwa ena.” Yesu ananena kwa iye kuti, “Ndiye kuti ana sapereka.” Koma kuti ife tisawakhumudwitse pita ku nyanja kaponye mbedza yako. Katenge nsomba imene ukayambe kuyikola; kayitsekule kukamwa ndipo ukapezamo ndalama. Katenge ndalamayo ndi kukapereka msonkho wanga ndi wanu.

“Nʼchifukwa chake, ufumu wakumwamba ukufanana ndi mfumu imene inafuna kuti antchito ake abweze ngongole. Atangoyamba kulandira, anamubweretsa munthu kwa iye amene anakongola ndalama 10,000. Popeza sakanatha kubweza, bwanayo analamula kuti iye, mkazi wake, ana ake ndi zonse anali nazo zigulitsidwe kuti zibweze ngongoleyo. “Wantchitoyo anagwada pamaso pake namupempha iye kuti, ‘Lezereni mtima ndipo ndidzabweza zonse.’ Bwana wakeyo anamuchitira chifundo, namukhululukira ngongoleyo ndipo anamulola apite. “Koma wantchito uja atatuluka, anakumana ndi wantchito mnzake amene anakongola kwa iye madinari 100. Anamugwira, nayamba kumukanyanga pa khosi, namuwumiriza nati, ‘Bwezere zimene unakongola kwa ine!’ “Wantchito mnzakeyo anagwada namupempha iye kuti, ‘Lezere mtima ine, ndipo ndidzakubwezera.’ “Koma iye anakana. Mʼmalo mwake, anachoka nakamumangitsa kufikira atabweza ngongoleyo. Pamene antchito ena anaona zomwe zinachitikazo, anamva chisoni kwambiri ndipo anapita nakawuza bwana wawo zonse zimene zinachitika. “Pamenepo bwanayo anayitana wantchitoyo nati, ‘Iwe wantchito woyipa mtima, ndinakukhululukira ngongole yako yonse chifukwa unandipempha. Kodi iwe sukanamuchitira chifundo wantchito mnzako monga momwe ine ndinakuchitira iwe?’ Ndi mkwiyo, bwana wakeyo anamupereka kwa oyangʼanira ndende kuti amuzuze mpaka atabweza zonse zimene anakongola. “Umu ndi mmene Atate anga akumwamba adzachitira ndi aliyense wa inu ngati simukhululukira mʼbale wanu ndi mtima wonse.”

Yesu anayankha kuti, “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndi kupereka kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ukakachita zimenezi, ukabwere udzanditsate Ine.” Mnyamatayo atamva zimenezi, anachoka mokhumudwa, chifukwa anali ndi chuma chambiri.

Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti nʼkovuta kuti olemera akalowe mu ufumu wakumwamba. Komanso ndikuwuzani kuti, nʼkwapafupi kuti ngamira idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi kuti wolemera akalowe mu ufumu wa Mulungu.” Ophunzira atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa kuti, “Nanga angapulumuke ndani?” Yesu anawayangʼana iwo nati, “Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka.”

Petro anamuyankha Iye kuti, “Ife tinasiya zonse ndi kukutsatirani Inu! Nanga tsono ife tidzalandira chiyani?” Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti pa nthawi yokonzanso zinthu zonse, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake waufumu mu ulemerero wake kumwamba, inu amene mwanditsata Ine mudzakhalanso pa mipando khumi ndi iwiri yaufumu, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli. Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena bambo kapena mayi kapena mkazi, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine adzalandira madalitso ochuluka ndi kulandiranso moyo wosatha.

“Ufumu wakumwamba uli ngati mwini munda amene anapita mmawa kukalemba anthu aganyu kuti akagwire ntchito mʼmunda wake wa mpesa. Anagwirizana kuwalipira dinari monga malipiro a tsiku limodzi ndipo anawatumiza mʼmunda wake wamphesa. “Nthawi 9 koloko mmawa, anatulukanso naona ena atayimirira pa msika akungokhala. Anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa, ndipo ndidzakulipirani malipiro oyenera.’ Ndipo anapita. “Anatulukanso nthawi ya 12 koloko masana, ndi nthawi ya 3 koloko masananso nachita chimodzimodzi. Nthawi ya 5 koloko madzulo anatulukanso ndipo anapeza enanso atangoyimirira. Anawafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukungoyimirira pano tsiku lonse osagwira ntchito?’ “Iwo anayankha kuti, ‘Chifukwa palibe munthu amene watilemba ganyu.’ “Iye anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa.’ “Ndipo pofika madzulo, mwini munda wamphesa anayitana kapitawo wake nati, ‘Itana antchito ndipo uwapatse malipiro awo, kuyambira omalizira aja mpaka oyamba.’ “Antchito amene anawalemba ganyu pa 5 koloko masana anafika ndipo aliyense analandira dinari. Ndipo atabwera kwa amene analembedwa poyamba anayembekezera kuti alandira zambiri. Koma aliyense wa iwo analandira dinari. Atalandira, anayamba kuderera kwa mwini mundayo. Iwo anati, ‘Anthu amene munawalemba pomalizira agwira ntchito ora limodzi, ndipo mwawafananitsa ndi ife amene tathyoka nayo ntchito ndi kutentha kwa dzuwa tsiku lonse.’ “Koma iye anamuyankha mmodzi wa iwo nati, ‘Bwenzi, ine sikuti sindinachite chilungamo. Kodi sunavomereze kuti ugwira ntchito ndi kulandira dinari? Tenga malipiro ako pita. Ndikufuna kumupatsa munthu amene ndinamulemba pomaliza mofanana ndi mmene ndakupatsira iwe. Kodi ndilibe ufulu wochita zimene ndikufuna ndi ndalama zanga? Kapena ukuyipidwa chifukwa ndine wopereka mowolowamanja?’ “Momwemo omalizira adzakhala oyamba ndipo oyamba adzakhala omalizira.”

Yesu analowa mʼdera lina la Nyumba ya Mulungu ndipo anatulutsa kunja anthu onse amene ankachita malonda. Anagubuduza matebulo a osinthira ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda. Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero koma inu mwayisandutsa phanga la anthu achifwamba.”

Tiwuzeni tsono maganizo anu ndi otani, kodi nʼkololedwa kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?” Koma Yesu podziwa maganizo awo oyipa anati, “Inu achiphamaso, bwanji mufuna kundipezera chifukwa? Onetseni ndalama imene mumapereka msonkho.” Iwo anabweretsa dinari, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi chithunzi ichi ndi malemba awa ndi za ndani?” Iwo anayankha kuti, “Ndi za Kaisara.” Pamenepo anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”

“Tsoka kwa inu, aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi, achiphamaso! Mumapereka chakhumi cha timbewu tonunkhira ndi cha timbewu tokometsera chakudya. Koma mwasiya zofunikira kwambiri za mʼmalamulo monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika. Muyenera kuchita zomalizirazi komanso osasiya zoyambazo.

“Komanso udzafanizidwa ndi munthu amene ankapita pa ulendo, ndipo anayitana antchito ake nawasiyira chuma chake. Wina anamupatsa ndalama 5,000, kwa wina 2,000 ndi kwa wina 1,000. Aliyense monga mwa nzeru zake. Pamenepo anapita pa ulendo wake. Munthu amene analandira ndalama 5,000 uja, anapita nthawi yomweyo nachita nazo malonda napindula 5,000 zina. Chimodzimodzinso amene analandira 2,000 uja anapindula 2,000 zina. Koma munthu amene analandira 1,000 uja, anapita nakumba dzenje nabisapo ndalama ya mbuye wake. “Patapita nthawi yayitali, mbuye wa antchitowo anabwera nawayitana kuti afotokoze chimene anachita ndi ndalama zija. Munthu amene analandira ndalama 5,000 uja anabweretsa 5,000 zina nati, ‘Ambuye munandisungitsa 5,000, taonani ndapindula 5,000 zinanso.’ “Ambuye ake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika iwe! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika iwe kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’ “Munthu amene anali ndi ndalama 2,000 uja anabweranso nati, ‘Ambuye munandisungitsa 2,000, onani, ndapindula 2,000 zinanso.’ “Mbuye wake anayankha nati, ‘Wachita bwino, wantchito wabwino ndi wokhulupirika! Wakhala wokhulupirika pa zinthu zochepa; ndidzakuyika kukhala woyangʼanira zinthu zambiri. Bwera, udzakondwere pamodzi ndi mbuye wako!’ “Kenaka munthu amene analandira ndalama 1,000 uja anabwera nati, ‘Ambuye ndinadziwa kuti ndinu munthu wowuma mtima, amene mumakolola pamene simunadzale ndi kututa kumene simunafese. Choncho ndinachita mantha ndipo ndinapita ndi kukabisa ndalama yanuyo pa dzenje. Onani, si iyi ndalama yanu ija.’ “Mbuye wake anayankha nati, ‘Iwe wantchito woyipa ndi waulesi! Iwe umadziwa kuti ndimakolola pamene sindinadzale, ndi kututa kumene sindinafese. Bwanji sunayike ndalama yanga kwa osunga ndalama kuti ine pobwera ndidzalandire ndalama yangayo pamodzi ndi chiwongoladzanja? “ ‘Mulandeni ndalamayo, ndipo patsani iye amene ali ndi ndalama 10,000. Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zambiri, ndipo adzakhala nazo zochuluka. Aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho. Ndipo muponyeni wantchito wopanda phinduyu kunja, ku mdima kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.’ ”

“Pamenepo mfumu idzati kwa a ku dzanja lamanja, ‘Bwerani inu odalitsika ndi Atate anga; landirani ufumu umene unakonzedwa chifukwa cha inu kuyambira pachiyambi cha dziko. Pakuti ndinali ndi njala ndipo munandipatsa chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo munandipatsa madzi akumwa, ndinali mlendo ndipo munandilandira, ndinali wausiwa ndipo munandiveka, ndinali wodwala ndipo munandisamalira, ndinali ku ndende ndipo inu munandiyendera.’ “Ndipo olungamawo adzamuyankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala ndipo tinakudyetsani, kapena ludzu ndipo tinakupatsani madzi akumwa? Ndi liti tinakuonani muli mlendo ndipo tinakulandirani, kapena wa usiwa ndipo tinakuvekani? Ndi liti tinakuonani mutadwala kapena ku ndende ndipo tinakuyenderani?’ “Mfumu idzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene munachitira mmodzi wa abale anga onyozekawa munandichitira Ine.’

“Pamenepo adzanena kwa akumanzere kwake kuti, ‘Chokani kwa Ine, inu otembereredwa, pitani ku moto wosatha wokonzedwera mdierekezi ndi angelo ake. Pakuti ndinali ndi njala ndipo simunandipatse chakudya, ndinali ndi ludzu ndipo simunandipatse madzi akumwa, ndinali mlendo koma inu simunandilandire, ndinali wa usiwa koma simunandiveke, ndinali wodwala komanso ku ndende simunandisamalire.’ “Iwo adzayankha kuti, ‘Ambuye ndi liti tinakuonani muli ndi njala kapena ludzu kapena mlendo kapena wausiwa kapena wodwala kapena mʼndende, ndipo kuti sitinakuthandizeni?’ “Iye adzayankha kuti, ‘Zoonadi, ndikuwuzani kuti chilichonse chimene simunachitire mmodzi wa abale anga onyozekawa simunandichitire Ine.’

mayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo. Ophunzira ataona izi anayipidwa nafunsa kuti, “Chifukwa chiyani akuwononga chotere? Mafuta amenewa akanatha kugulitsidwa pa mtengo waukulu, ndipo ndalama zake zikanaperekedwa kwa osauka.” Yesu podziwa izi anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Wandichitira Ine chinthu chabwino. Osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse.

nafunsa kuti, “Kodi mundipatsa chiyani ngati nditamupereka Iye kwa inu?” Pamenepo anamuwerengera ndalama zokwanira masiliva makumi atatu. Kuyambira pamenepo Yudasi anafunafuna nthawi yabwino yoti amupereke Yesu.

Yudasi, amene anamupereka Iye, ataona kuti Yesu waweruzidwa kuti akaphedwe, anatsutsika mu mtima mwake nakabweza ndalama zamasiliva makumi atatu zija kwa akulu a ansembe ndi kwa akuluakulu. Iye anati, “Ndachimwa pakuti ndapereka munthu wosalakwa.” Iwo anayankha nati, “Ife tilibe nazo kanthu izo ndi zako.” Pamenepo Yudasi anaponya ndalamazo mʼNyumba ya Mulungu nachoka. Kenaka anapita nakadzimangirira. Akulu a ansembe anatola ndalamazo nati, “Sikololedwa ndi lamulo kuti ndalamazi tiziyike mosungira chuma cha Mulungu, popeza ndi ndalama za magazi.” Choncho anagwirizana kuti ndalamazo azigwiritse ntchito pogulira munda wa wowumba mbiya kuti ukhale manda alendo. Ndi chifukwa chake umatchedwa munda wamagazi mpaka lero lino. Pamenepo zimene anayankhula mneneri Yeremiya zinakwaniritsidwa kuti, “Anatenga ndalama zamasiliva makumi atatu mtengo umene anamuyikira Iye anthu a Israeli. Ndipo anazigwiritsa ntchito kugula munda wa wowumba mbiya monga mmene Ambuye anandilamulira ine.”

Mbewu zinanso zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinamera, zinakula ndi kubereka zipatso, zina zochuluka makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi ndi zina 100.”

Komabe ena, monga mbewu zofesedwa pakati pa minga, amamva mawu; koma nkhawa zamoyo uno, chinyengo cha chuma ndi zokhumba za zinthu zina zimabwera ndi kutchinga mawu, ndipo amawachititsa kukhala osabala chipatso. Ena, ngati mbewu zofesedwa pa nthaka yabwino, amamva mawu, nawalandira, ndi kubereka zipatso zokwanira makumi atatu, makumi asanu ndi limodzi, kapena ngakhale 100 kuwonjezera pa zomwe zinafesedwa.”

Koma Iye anayankha kuti, “Apatseni kanthu koti adye.” Iwo anati kwa Iye, “Apa pafunika ndalama za miyezi isanu ndi itatu zomwe munthu amalandira! Kodi tipite kukagwiritsa ntchito ndalama zotere kugulira buledi kuti tiwapatse adye?” Iye anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati? Pitani mukaone.” Ataona anati kwa Iye, “Asanu ndi nsomba ziwiri.” Pamenepo Yesu anawalamulira kuti awakhazike anthu pansi mʼmagulu pa msipu obiriwira. Ndipo anakhala pansi mʼmagulu a anthu 100 ndi gulu la anthu makumi asanu. Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri, nayangʼana kumwamba, Iye anayamika nagawa malofu a bulediwo. Kenaka anawapatsa ophunzira ake kuti awapatse anthu. Ndipo anagawanso nsomba ziwirizo kwa onse. Onse anadya ndipo anakhuta, ndipo ophunzira ake anatola buledi ndi nsomba zotsalira zokwanira madengu khumi ndi awiri. Chiwerengero cha amuna amene anadya chinali 5,000.

dyera, nkhwidzi, chinyengo, machitidwe onyansa, kaduka, chipongwe, kudzikuza ndi kupusa. Zoyipa zonsezi zimatuluka mʼkati ndipo zimadetsa munthu.”

Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa. Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake?

Yesu anamuyangʼana ndi kumukonda nati, “Ukusowa chinthu chimodzi. Pita, kagulitse zonse zimene uli nazo ndipo kapereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ndipo ukabwere ndi kunditsata Ine.” Pa chifukwa ichi nkhope yake inagwa. Anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi chuma chambiri.

Yesu anayangʼanayangʼana ndipo anati kwa ophunzira ake, “Nʼkovutadi kuti achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!” Ophunzira anadabwa ndi mawu ake. Koma Yesu anatinso, “Ananu, nʼkovutadi kulowa mu ufumu wakumwamba! Ndi kwapafupi kwa ngamira kuti idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kuti alowe mu ufumu wa Mulungu.” Ophunzira anadabwa kwambiri, ndipo anati kwa wina ndi mnzake, “Nanga ndani amene angapulumuke?” Yesu anawayangʼana ndipo anati, “Kwa munthu zimenezi nʼzosatheka, koma osati ndi Mulungu; zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu.”

Petro anati kwa Iye, “Ife tasiya zonse ndi kukutsatani!” Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe aliyense amene wasiya nyumba kapena abale kapena alongo kapena amayi kapena abambo kapena ana kapena minda chifukwa cha Ine ndi Uthenga Wabwino adzalephera kulandira 100 (nyumba, abale, alongo, amayi, ana ndi minda, pamodzi ndi mazunzo) mʼbado uno ndi moyo wosatha nthawi ya mʼtsogolo.

Atafika ku Yerusalemu, Yesu analowa mʼbwalo lakunja la Nyumba ya Mulungu ndipo anayamba kupirikitsa anthu amene amagula ndi kugulitsa mʼmenemo. Anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda, ndipo Iye sanalole aliyense kugulitsa malonda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu. Ndipo pamene ankawaphunzitsa, Iye anati, “Kodi sikunalembedwe kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero kwa anthu a mitundu yonse?’ Koma inu mwayisandutsa ‘phanga la achifwamba.’ ”

Iwo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ife tikudziwa kuti Inu ndi munthu amene mumanena zoona. Inu simutengeka ndi anthu, chifukwa simusamala kuti ndi ndani; koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu molingana ndi choonadi. Kodi ndi koyenera kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? Kodi ife tipereke msonkho kapena ayi?” Koma Yesu anadziwa chinyengo chawo. Iye anafunsa kuti, “Bwanji mukufuna kundipeza chifukwa? Bweretsani ndalama kuti ndiyione.” Iwo anamubweretsera ndalama, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi nkhope iyi ndi ya ndani? Nanga malembawa ndi a ndani?” Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.” Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.” Ndipo anazizwa naye.

Yesu anakhala pansi moyangʼanana ndi pamene amaperekera zopereka ndipo amaona anthu akupereka ndalama zawo mʼthumba la Nyumba ya Mulungu. Anthu ambiri olemera anaponya ndalama zambiri. Koma mkazi wamasiye, wosauka anabwera ndi kuyikamo tindalama tiwiri ta kopala, tongokwanira theka la ndalama. Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mayi wosauka wamasiyeyu waponya zambiri mʼthumbali kuposa ena onsewa. Iwo apereka molingana ndi chuma chawo; koma iye, mwaumphawi wake, wapereka zonse anali nazo ngakhale zoti akanagulira chakudya.”

Pamene Iye anali mʼBetaniya, atakhala pa tebulo akudya mʼnyumba ya munthu wodziwika kuti Simoni wakhate, anabwera mayi ndi botolo la mafuta onunkhira amtengo wapamwamba opangidwa ndi nadi. Anaphwanya botololo nakhuthula mafutawo pa mutu wa Yesu. Ena mwa iwo amene analipo, anakwiya nati kwa wina ndi mnzake, “Chifukwa chiyani akuwononga mafuta onunkhirawa? Akanatheka kugulitsidwa ndi ndalama zambiri zoposa malipiro a pa chaka ndipo ndalamazo ndi kupatsa osauka.” Ndipo anamudzudzula iye mwaukali. Yesu anati, “Musiyeni, chifukwa chiyani mukumuvutitsa? Wandichitira Ine chinthu chabwino. Anthu osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, ndipo mukhoza kuwathandiza nthawi iliyonse mungafune. Koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse.

Iwo anakondwa pakumva zimenezi ndipo analonjeza kumupatsa iye ndalama. Ndipo ankadikira mpata wabwino woti amupereke.

Yohane anayankha kuti, “Munthu amene ali ndi malaya awiri apatseko amene alibe, ndi amene ali ndi chakudya achitenso chimodzimodzi.”

Amisonkho nawonso anabwera kudzabatizidwa. Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, ife tichite chiyani?” Iye anawawuza kuti, “Musalandire moposa zimene muyenera.” Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?” Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.”

Akuyangʼana ophunzira ake, Iye anati, “Odala ndinu amene ndi osauka, chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu. Inu amene mukumva njala tsopano, ndinu odala chifukwa mudzakhutitsidwa. Inu amene mukulira tsopano, ndinu odala chifukwa mudzasekerera.

“Ndinu atsoka, anthu olemera, popeza mwalandiriratu zokusangalatsani. Tsoka inu amene mukudya bwino tsopano, chifukwa mudzakhala ndi njala. Ndinu atsoka, amene mukusekerera tsopano, chifukwa mudzabuma ndi kulira.

Ngati wina akumenyani patsaya limodzi mupatseninso tsaya linalo. Ngati wina akulanda mwinjiro wako, umulole atenge ndi mkanjo omwe. Mupatseni aliyense amene akupemphani kanthu ndipo ngati wina atenga chinthu chanu, musamulamule kuti akubwezereni.

“Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amakonda amene amawakondanso. Ndipo ngati muchita zabwino kwa amene ndi abwino kwa inu, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amachita izi.

Ndipo ngati mukongoza amene mukuyembekeza kuti abweza, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amabwereketsa kwa ochimwa anzawo, ndipo amayembekezera kubwezeredwa zonse. Koma kondani adani anu, achitireni zabwino, akongozeni koma osayembekezera kulandira kanthu. Pamenepo mphotho yanu idzakhala yayikulu ndipo inu mudzakhala ana a Wammwambamwamba, chifukwa ndi wokoma mtima kwa anthu osayamika ndi oyipa.

Perekani ndipo mudzapatsidwa. Adzakupatsani mʼthumba mwanu muyeso wabwino, wotsenderezeka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyeso umene mumagwiritsa ntchito, ndi omwewo adzakuyeserani.”

Yesu pomuyankha anati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa.

Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, ‘Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.’

Mutipatse chakudya chathu chalero,

Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!”

Koma popereka kwa osauka, perekani chimene chili mʼkati ndipo chilichonse chidzakhala choyera. “Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumapereka kwa Mulungu chakhumi cha timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsera chakudya ndi mbewu zina zonse za mʼmunda, koma mumakana chilungamo ndi chikondi cha Mulungu. Mumayenera kuchita zomalizirazi osalekanso kuchita zoyambazi.

Munthu wina mʼgulu la anthu anati kwa Iye, “Aphunzitsi, muwuzeni mʼbale wanga andigawireko chuma chamasiye.” Yesu anayankha kuti, “Munthu iwe, ndani anandiyika Ine kukhala woweruza kapena wogawa chuma pakati panu?” Kenaka Iye anawawuza kuti, “Chenjerani! Khalani tcheru ndi makhalidwe onse adyera; moyo wa munthu sukhala chifukwa cha kuchuluka kwa zimene ali nazo.”

Ndipo Iye anawawuza fanizo ili, “Munda wa munthu wina wachuma unabereka kwambiri. Iye anaganiza kuti, ‘Ndichite chiyani? Ndilibe malo osungiramo mbewu zanga.’ “Ndipo Iye anati, ichi ndi chimene ndidzachite: Ndidzaphwasula nkhokwe zanga zonse ndi kumanga zokulirapo, ndipo ndidzasungira mʼmenemo mbewu ndi katundu. Ndipo ndidzawuza moyo wanga kuti, ‘Uli nazo zinthu zabwino zambiri zimene zikhalepo zaka zambiri, usapupulume; idya, imwa ndi kukondwera.’ ” “Koma Mulungu anati kwa iye, ‘Iwe wopusa! Usiku womwe uno moyo wako udzachotsedwa kwa iwe, ndipo ndi ndani amene adzatenge zimene iwe wadzikonzera?’ “Umu ndi mmene zidzakhalire ndi aliyense amene amadziwunjikira chuma, koma si wachuma pamaso pa Mulungu.”

Kenaka Yesu anati kwa ophunzira ake, “Choncho Ine ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu, zimene mudzadya; kapena za thupi lanu, zimene mudzavala. Moyo uposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. Taonani makwangwala: iwo safesa kapena kukolola, alibe nyumba zosungamo zinthu kapena nkhokwe; komabe, Mulungu amawadyetsa. Koposa kotani inu amene ndi ofunikira kuposa mbalame. Ndi ndani wa inu akhoza kuwonjeza ora pa moyo wake chifukwa cha kudandaula? Popeza simungathe kuchita kanthu kakangʼono aka, nʼchifukwa chiyani mumadandaula ndi zinazi? “Taonani mmene maluwa amakulira. Iwo sagwira ntchito kapena kusoka zovala. Koma Ine ndikuwuzani kuti, ngakhale Solomoni muulemelero wake wonse sanavalepo ngati limodzi la awa. Ngati umu ndi mmene Mulungu amavekera udzu wakuthengo, umene lero ulipo ndipo mawa uponyedwa pa moto, nanga Iye adzakuvekani inu motani. Haa! Inu achikhulupiriro chochepa! Ndipo musayike mtima wanu pa zimene mudzadye kapena kumwa; musade nazo nkhawa. Pakuti anthu akunja amathamanga kufunafuna zinthu zotere, ndipo Atate amadziwa kuti mumazifuna zimenezi. Koma funafunani ufumu wake, ndipo mudzapatsidwa zonsezi.

Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupereke kwa osauka. Dzipezereni zikwama zandalama zimene sizidzatha, ndi kudzikundikira chuma chomwe sichidzatha kumwamba, kumene mbala sizingafikeko, ndipo dzimbiri silingawononge.

Popeza kumene kuli chuma chanu, mtima wanunso udzakhala komweko.”

Kenaka Yesu anati kwa mwini malo uja, “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamayitane abwenzi ako, abale ako, anthu afuko lako kapena anzako achuma; ngati iwe utero, iwo adzakuyitananso, choncho udzalandiriratu mphotho yako. Koma ukakonza phwando, itana anthu osauka, ofa ziwalo, olumala ndi osaona. Pamenepo udzakhala wodala, chifukwa iwo sangakubwezere kanthu, koma Mulungu ndiye adzakubwezera pa chiukitso cha olungama.”

Mʼnjira yomweyo, wina aliyense wa inu amene sasiya zonse ali nazo sangakhale ophunzira wanga.

“Kapena tiyeni tifanizire mayi amene anali ndi ndalama zasiliva khumi ndipo imodzi nʼkutayika, kodi sayatsa nyale ndi kusesa mʼnyumba ndi kufuna mosamalitsa mpaka atayipeza? Ndipo pamene wayipeza, amayitana anzake, ndi anansi pamodzi nati, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza ndalama yanga yotayika ija.’ Momwemonso, Ine ndikukuwuzani kuti angelo a Mulungu amakondwera kwambiri chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima.”

Yesu anapitiriza kunena kuti, “Panali munthu amene anali ndi ana aamuna awiri. Wamngʼonoyo anati kwa abambo ake, ‘Abambo, patseni gawo langa la chuma chanu.’ Ndipo iye anawagawira awiriwo chuma chawo. “Pasanapite nthawi, wamngʼonoyo anasonkhanitsa chuma chake chonse, napita ku dziko lakutali ndipo kumeneko anayamba kumwaza chuma chake mʼnjira zachitayiko. Iye atawononga zonse, kunagwa njala yoopsa mʼdziko lonselo ndipo anayamba kusauka. Iye anapita kwa nzika ina ya dzikolo nakakhala naye ndi kumagwira ntchito, amene anamutumiza ku munda kukadyetsa nkhumba. Iye analakalaka atakhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumbazo zinkadya, koma panalibe wina amene anamupatsa kanthu. “Maganizo ake atabweramo, iye anati, ‘Ndi antchito angati a abambo anga amene ali ndi chakudya chimene amadya nʼkutsalako ndipo ine ndili pano kufa ndi njala! Ine ndinyamuka ndi kubwerera kwa abambo anga ndipo ndikati kwa iwo: abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi kwa inu. Ndine wosayeneranso kutchedwa mwana wanu; munditenge ngati mmodzi wa antchito anu.’ Ndipo iye ananyamuka ndi kupita kwa abambo ake. “Koma iye akanali patali, abambo ake anamuona ndipo anamvera chisoni; anathamangira mwanayo, namukumbatira ndi kupsompsona. “Mwanayo anati, ‘Abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi inunso. Ine sindiyenera konse kutchedwa mwana wanu.’ “Koma abambowo anati kwa antchito ake, ‘Fulumirani! Bweretsani mkanjo wabwino kwambiri ndipo mumuveke. Muvekeni mphete ndi nsapato. Bweretsani mwana wangʼombe wonenepa ndipo iphani. Tiyeni tikhale ndi phwando ndi kukondwerera. Pakuti mwana wangayu anali wakufa, ndipo ali ndi moyonso; iye anatayika ndipo wapezeka.’ Chomwecho anayamba kukondwerera.

Yesu anawuza ophunzira ake kuti, “Panali munthu wina wachuma amene kapitawo wake anzake anamuneneza kuti amawononga chuma chakecho. Choncho anamuyitana ndi kumufunsa kuti, ‘Kodi nʼchiyani chimene ndikumva za iwe? Pereka tsatanetsatane wa ntchito yako, pakuti supitirizanso kukhala kapitawo wanga.’ “Kapitawoyo analingalira kuti, ‘Kodi tsopano ndidzachita chiyani? Bwana wanga andichotsa ntchito. Ine ndilibe mphamvu zokwanira zolimira, komanso ine ndimachita manyazi kupempha. Ine ndikudziwa chimene ndidzachita kotero kuti, pamene ntchito yanga yatha pano, anthu adzandilandire mʼnyumba zawo.’ “Choncho iye anayitana aliyense amene anali ndi ngongole kwa bwana wake. Iye anafunsa woyamba, ‘Kodi uli ndi ngongole yotani kwa bwana wanga?’ “Iye anayankha kuti, ‘Migolo yamafuta a olivi 800.’ “Kapitawo uja anamuwuza iye, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo, khala pansi msanga ndipo lemba kuti ndi migolo 400.’ “Kenaka iye anafunsa wachiwiri kuti, ‘Nanga iwe uli ndi ngongole yotani?’ “Iye ayankha kuti madengu a tirigu 1,000. “Iye anati, ‘Tenga pamene unalemba ngongole yakoyo ndipo ulembepo 800.’ “Bwana anayamikira kapitawo wosakhulupirikayo popeza anachita mochenjera. Pakuti anthu a dziko lino lapansi ndi ochenjera kwambiri akamachita zinthu ndi anthu ofanana nawo kuposa anthu a kuwunika. Ine ndikukuwuzani inu, gwiritsani ntchito chuma cha dziko lapansi kuti mudzipezere nokha abwenzi, kuti pamene chatha mudzalandiridwe mʼmalo okhala amuyaya.

“Amene akhulupirika pa zinthu zochepa akhoza kukhulupirikanso pa zinthu zambiri, ndipo amene sakhulupirika pa zinthu zochepa adzakhala wosakhulupirika pa zinthu zambiri. Ndipo ngati simunakhale okhulupirika pogwiritsa ntchito chuma cha dziko lapansi, ndani amene adzakusungitsani chuma chenicheni? Ndipo ngati simunakhale okhulupirika ndi chuma cha mwini wake, ndani amene adzakupatsani katundu wanuwanu?

“Palibe wantchito amene angatumikire mabwana awiri. Mwina iye adzadana ndi wina ndi kukonda winayo, kapena adzakhala wodzipereka kwa wina ndi kumunyoza winayo. Inu simungathe kutumikira Mulungu komanso ndalama nthawi imodzi.” Afarisi amene ankakonda ndalama atamva zimenezi anamuseka Yesu.

“Panali munthu wachuma amene ankavala zovala zofiirira za mtengowapatali ndipo ankakhala moyo wachisangalalo tsiku lililonse. Pa khomo la mpanda wake ankagonekapo munthu wopempha wotchedwa Lazaro, wazilonda thupi lonse ndipo ankafunitsitsa atadya zomwe zinkagwa pansi kuchokera pamene munthu wolemerayo amadyerapo. Agalu ankabweranso ndi kumanyambita zilonda zake. “Nthawi inafika imene wopemphayo anamwalira ndipo angelo anamunyamula nakamuyika mʼmanja mwa Abrahamu. Munthu wolemerayo anamwaliranso ndipo anayikidwa mʼmanda. Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake. Ndipo anafuwula kwa iye kuti, ‘Abambo Abrahamu, mundimvere chisoni ine ndipo mutumeni Lazaroyo kuti aviyike msonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikumva ululu mʼmoto muno.’ “Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo. Ndipo kuwonjezera pa zonsezi, pakati pa inu ndi ife pali chiphompho chachikulu chimene chinayikidwa, kotero kuti amene akufuna kubwera kumeneko sangathe, kapena palibe amene angawoloke kuchokera kumeneko kudzafika kuno.’ “Iye anayankha kuti, ‘Ndipo ndikupemphani inu, abambo, mutumeni Lazaro ku nyumba ya abambo anga, pakuti ine ndili ndi abale asanu. Lolani iye akawachenjeze kotero kuti asadzabwere kumalo ano amazunzo.’ “Abrahamu anayankha kuti, ‘Ali ndi Mose ndi Aneneri; aleke amvere iwo.’ “Iye anati, ‘Ayi, bambo Abrahamu, koma ngati wina ochokera kwa akufa adzapita kwa iwo, adzatembenuka mtima.’ “Anati kwa iye, ‘Ngati iwo samvera Mose ndi Aneneri, sadzakhulupirira ngakhale wina atauka kwa akufa.’ ”

Aliyense amene ayesetsa kusunga moyo wake adzawutaya, ndipo aliyense amene ataya moyo wake adzawusunga.

Ine ndimasala kudya kawiri pa Sabata ndipo ndimapereka chakhumi pa zonse ndimapeza.’

Yesu atamva izi, anati kwa iye, “Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine.” Atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri chifukwa anali munthu wachuma chambiri.

Yesu anamuyangʼana nati, “Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu! Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.” Amene anamva izi anafunsa kuti, “Nanga ndani amene angapulumuke?” Yesu anayankha kuti, “Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”

Petro anati kwa Iye, “Ife tinasiya zonse tinali nazo kutsatira Inu!” Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.”

Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.”

Iye anati, “Munthu wa banja laufumu anapita ku dziko lakutali kukadzozedwa ufumu ndipo kenaka abwerenso kwawo. Tsono iye anayitana antchito ake khumi ndi kuwapatsa ndalama khumi. Iye anati, ‘Gwiritsani ntchito ndalama izi mpaka nditabwerera.’ “Koma anthu ake anamuda ndipo anatuma nthumwi pambuyo pake kukanena kuti, ‘Sitikufuna munthuyu kuti akhale mfumu yathu.’ “Iye analandira ufumuwo ngakhale zinali zotero, ndipo anabwerera kwawo. Kenaka iye anatumiza uthenga kwa antchito ake amene anawapatsa ndalama aja, ndi cholinga chakuti adziwe chimene anapindula nazo. “Woyamba anabwera ndipo anati, ‘Bwana ndalama zanu zapindula khumi zina.’ “Bwana wakeyo anayankha kuti, Wachita bwino wantchito wabwino. ‘Chifukwa wakhulupirika pa zinthu zazingʼono, lamulira mizinda khumi.’ “Wachiwiri anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama zanu zapindula zisanu zina.’ “Bwana anayankha kuti, ‘Iwe lamulira mizinda isanu.’ “Kenaka wantchito wina anabwera ndipo anati, ‘Bwana, ndalama yanu nayi; ine ndinayibisa ndi kuyisunga mʼkansalu. Ine ndimakuopani, chifukwa ndinu munthu wowuma mtima. Inu mumatenga chimene simunachiyike ndi kukolola chimene simunadzale.’ “Bwana wake anayankha kuti, ‘Ine ndikukuweruza iwe ndi mawu ako omwewo. Ndiwe wantchito woyipa. Kani umadziwa kuti ndine munthu wowuma mtima ndi wotenga chimene sindinasungitse, ndi kukolola chimene sindinadzale? Nanga nʼchifukwa chiyani sunasungitse ndalama yanga, kuti ine pobwera, ndidzayitenge ndi chiwongoladzanja?’ “Ndipo iye anawuza amene anayimirira pafupi kuti, ‘Tengani ndalama yake ndi kumupatsa amene ali ndi ndalama khumiyo!’ ” Iwo anati, “Bwana iyeyu ali nazo kale khumi!” Iye anayankha kuti, “Ndikukuwuzani kuti, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zambiri, koma amene alibe, adzalandidwa ngakhale chimene ali nacho.

Kenaka Iye analowa mʼdera la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kutulutsa kunja amene amachita malonda. Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzakhala nyumba ya mapemphero, koma inu mwayisadutsa phanga la achifwamba.”

Kodi ndi bwino kwa ife kumapereka msonkho kwa Kaisara kapena kusapereka?” Iye anaona chinyengo chawo ndipo anawawuza kuti, “Onetseni ndalama. Chithunzi ndi malembawa ndi zayani?” Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.” Iye anawawuza kuti, “Ndiye perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zimene ndi za Mulungu.”

Yesu atayangʼana, anaona olemera akuyika mphatso zawo mu chosungira ndalama za mʼNyumba ya Mulungu. Iye anaonanso mkazi wamasiye wosauka akuyikamo timakopala tiwiri. Iye anati, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mkazi wamasiye wosaukayu wapereka zambiri kuposa ena onsewa. Anthu onsewa atapa mphatso zawo kuchokera pa zochuluka zimene ali nazo; koma uyu, mwa umphawi wake, wapereka zonse zimene ali nazo.”

Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo. Chifukwa cha zimenezi Iye anapanga chikwapu cha zingwe ndipo anatulutsa onse mʼbwalo la Nyumbayo, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe; Iye anamwaza ndalama zawo ndi kugudubuza matebulo. Kwa amene amagulitsa nkhunda, Iye anati, “Tulutsani izi muno! Osasandutsa Nyumba ya Atate anga msika!” Ophunzira ake anakumbukira kuti zinalembedwa kuti, “Kudzipereka kwanga ku nyumba yanu kudzandiphetsa.”

Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.”

Kenaka Yesu ananenetsa kuti, “Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu.

Mbala sibwera chabe koma kuti idzabe, kupha ndi kuwononga. Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka. “Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.

Koma mmodzi wa ophunzira ake, Yudasi Isikarioti, amene pambuyo pake adzamupereka anati, “Nʼchifukwa chiyani mafuta awa sanagulitsidwe ndipo ndalama zake nʼkuzipereka kwa osauka?” Mafutawo anali a mtengo wa malipiro a chaka chimodzi. Iye sananene izi chifukwa cha kuganizira osauka koma chifukwa anali mbava; ngati wosunga thumba la ndalama, amabamo zomwe ankayikamo. Yesu anayankha kuti, “Mulekeni. Mafutawa anayenera kusungidwa mpaka tsiku loyika maliro anga. Inu mudzakhala ndi osauka nthawi zonse, koma simudzakhala nane nthawi zonse.”

Tsiku limenelo inu simudzandipemphanso kalikonse. Ine ndikukuwuzani zoona kuti Atate anga adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. Mpaka tsopano simunapemphe kalikonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.

Okhulupirira onse anali pamodzi ndipo aliyense ankapereka zinthu zake kuti zikhale za onse. Ankagulitsa minda yawo ndi katundu wawo, ndi kugawira kwa aliyense molingana ndi zosowa zake. Tsiku ndi tsiku ankasonkhana pamodzi pa bwalo la pa Nyumba ya Mulungu. Ankadya pamodzi mʼnyumba zawo mwasangala ndi mtima woona.

Petro anati kwa iye, “Ine ndilibe siliva kapena golide, koma chimene ndili nacho ndikupatsa. Mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda.”

Okhulupirira onse anali a mtima umodzi, ndi maganizo amodzi. Palibe munthu amene amati zomwe anali nazo zinali zake zokha, koma amagawana chilichonse chimene anali nacho. Atumwi anapitirira kuchitira umboni mwa mphamvu zakuuka kwa Ambuye Yesu, ndipo pa iwo panali chisomo chochuluka. Panalibe anthu osowa kanthu pakati pawo. Pakuti amene anali ndi malo, kapena nyumba amagulitsa ndi kubweretsa ndalamazo ndi kuzipereka kwa atumwi, ndipo zimagawidwa kwa aliyense amene anali ndi chosowa.

Yosefe, wa fuko la Levi, wochokera ku Kupro amene atumwi anamutcha Barnaba, kutanthauza kuti mwana wachilimbikitso, anagulitsa munda wake ndipo anadzapereka ndalamazo kwa atumwi.

Koma munthu wina dzina lake Hananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, anagulitsanso munda wawo. Mogwirizana ndi mkazi wakeyo anapatulapo pa ndalamazo nazisunga, ndipo anatenga zotsalazo ndi kukapereka kwa atumwi. Koma Petro anamufunsa kuti, “Hananiya, chifukwa chiyani Satana anadzaza chotere mu mtima wako kuti unamize Mzimu Woyera ndipo wapatula ndi kusunga ndalama? Kodi sunali wako usanagulitse? Ndipo utagulitsa ndalamazo sizinali mʼmanja mwako kodi? Nʼchiyani chinakuchititsa zimenezi? Iwe sunanamize anthu koma Mulungu.”

Simoni ataona kuti Mzimu anaperekedwa kwa iwo atumwi atawasanjika manja, iye anafuna kuwapatsa ndalama ndipo anati, “Inenso ndipatseni mphamvu imeneyi kuti aliyense amene ndimusanjika manja anga azilandira Mzimu Woyera.” Petro anayankha kuti, “Ndalama zako utayike nazo pamodzi, chifukwa unaganiza kuti ungathe kugula mphatso ya Mulungu ndi ndalama!

Ophunzirawo, aliyense monga mwakupata kwake, anatsimikiza kuthandiza abale okhala ku Yudeya.

Ine sindinasirire siliva kapena golide kapena zovala za munthu aliyense. Inu nomwe mukudziwa kuti manja angawa ananditumikira kuti tipeze zimene ine ndi anzanga tinkazifuna. Pa zonse zimene ndinachita, ndinakuonetsani kuti pogwira ntchito molimbika motere tiyenera kuthandiza ofowoka, pokumbukira mawu a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupereka kumadalitsa kuposa kulandira.’ ”

tsono, iwe amene umaphunzitsa ena, sudziphunzitsa wekha kodi? Kodi iwe amene umalalikira kuti anthu asabe, umabanso?

Koma, “Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, mupatse kanthu kakumwa. Pochita ichi, udzamuwunjikira makala amoto pamutu pake.”

Ichi nʼchifukwa chakenso inu mumapereka msonkho. Pakuti olamulira ndi atumiki a Mulungu amene amapereka nthawi yawo yonse kulamulira. Mubwezereni aliyense amene munamukongola. Ngati inu muli ndi ngongole yamsonkho, perekani msonkho kwa oyenera kuwalipira. Ngati ndi kuopa perekeni kwa oyenera kuwaopa ndipo ngati ndi ulemu kwa oyenera ulemu. Musakhale ndi ngongole ndi wina aliyense kupatula ngongole ya kukondana wina ndi mnzake. Pakuti amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa lamulo. Malamulo awa: “Usachite chigololo,” “Usaphe,” “Usabe,” “Usasirire,” ndi malamulo ena onse amene alipo, akhazikika pa lamulo limodzi ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.”

Kodi simukudziwa kuti munthu woyipa sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musanyengedwe: achigololo, kapena opembedza mafano, kapena achiwerewere, kapena amuna adama, kapena ogonana ndi amuna okhaokha; kapena akuba, kapena aumbombo, kapena oledzera, kapena achipongwe, kapena opeza ndalama mwachinyengo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.

Ngati ndipereka zanga zonse kwa osauka ndi kupereka thupi langa kuti alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ine sindipindula kanthu.

Tsopano za zopereka zothandiza anthu a Ambuye a ku Yerusalemu. Muchite zomwe ndinawuza mipingo ya ku Galatiya kuti ichite. Pa tsiku loyamba la sabata lililonse, aliyense wa inu azipatula ndalama molingana ndi zomwe wapezera. Asunge, kuti ndikabwera pasadzakhalenso msonkhamsonkha.

Koma tili ndi chuma ichi mʼmbiya zadothi, kusonyeza kuti mphamvu yoposayi, imachokera kwa Mulungu osati kwa ife.

Motero sitiyangʼana zinthu zimene ndi zooneka ndi maso, koma zinthu zimene ndi zosaoneka. Pakuti zimene zimaoneka ndi zosakhalitsa, koma zimene sizioneka ndi zamuyaya.

Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu.

Motero ndikuchitira umboni kuti anapereka mmene akanathera, ndipo mwinanso kuposera mmene akathera kupereka. Anapereka mosakakamizidwa, ndipo anatipempha motiwumiriza kuti tiwapatse mwayi woti nawonso athandize anthu oyera mtima a ku Yudeya. Iwo anachita moposera mmene ife timayembekezera. Choyamba anadzipereka kwa Ambuye ndipo kenaka kwa ife monga mwa chifuniro cha Mulungu.

Pakuti mukudziwa chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, kuti ngakhale anali wolemera, koma chifukwa cha inuyo anasanduka wosauka, kuti umphawi wakewo, inuyo mulemere.

Ndipo ngati mtima ofunitsitsa ulipo, mphatsoyo imalandiridwa molingana ndi zimene munthuyo ali nazo, osati zimene alibe. Cholinga chathu sikuti tipeputse ena pamene inuyo mukuvutika, koma kuti pakhale kufanana. Zambiri zimene muli nazo pakati panu muthandize nazo osowa, kuti nawonso akadzakhala nazo zambiri adzakuthandizeni pa zosowa zanu. Cholinga nʼkuchita mofanana, monga kwalembedwa kuti, “Iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere.”

Choncho ndinaganiza kuti nʼkofunika kupempha abale kuti adzakuchezereni ineyo ndisanafike, ndikuti adzatsirize kukonzekera mphatso zomwe munalonjeza kupereka mowolowamanja. Motero mphatsoyo idzakhala yokonzeratu, ndipo idzakhala mphatso yoperekedwa mowolowamanja, osati mokakamizidwa.

Takumbukirani mawu awa: Amene adzala pangʼono, adzakololanso pangʼono, ndipo amene adzala zochuluka, adzakololanso zochuluka. Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera. Ndipo Mulungu akhoza kukudalitsani kwambiri, kuti inuyo nthawi zonse mukhale ndi zinthu zokukwanirani, ndiponso ndi zina zochuluka kuti muthandize pa ntchito zonse zabwino. Paja analemba kuti, “Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya.”

Tsono Mulungu amene amapereka mbewu kwa wofesa, ndiponso chakudya kuti adye, adzaperekanso mbewu mʼnkhokwe zanu ndi kuzichulukitsa. Iye adzachulukitsanso zipatso za chilungamo chanu. Adzakulemeretsani pa zonse kuti mukhale owolowamanja pa nthawi zonse. Ndipo kuwolowamanja kwanu kudzera mwa ife, kudzakhala kuthokoza kwa Mulungu. Ntchito imene mukugwirayi siyongothandiza kokha anthu a Mulungu kupeza zosowa, komanso ikuthandiza kuti anthu ambiri ayamike Mulungu. Chifukwa cha ntchito imene mwawatsimikizira nokha, anthu ena onse adzayamika Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu kumene kumaonekera pamene mukuvomereza Uthenga Wabwino wa Khristu, ndiponso chifukwa chowagawira mowolowamanja iwowo pamodzi ndi wina aliyense.

Chimene iwo anapempha ndi chakuti ife tipitirize kukumbukira osauka, chinthu chimene ine ndinali okonzeka kuchichita.

Pakuti malamulo onse akuphatikizidwa mu lamulo ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.”

Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa. Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha. Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa. Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira.

Ngakhale ndili wamngʼono kwambiri pakati pa anthu onse a Mulungu, anandipatsa chisomo chimenechi cholalikira kwa anthu a mitundu ina chuma chopanda malire cha Khristu.

Iye amene wakhala akuba asabenso, koma agwire ntchito ndi kuchita kenakake kaphindu ndi manja ake, kuti akhale ndi kenakake kogawana ndi amene akusowa.

Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena.

Koma zonse zimene ndinkaziyesa zaphindu, tsopano ndikuziona kuti nʼzosapindulitsa chifukwa cha Khristu. Kuwonjeza pamenepo, ndikuziona zonse kuti nʼzopanda phindu poyerekeza ndi phindu lopambana la kudziwa Khristu Yesu Ambuye anga. Nʼchifukwa cha Yesuyo ndataya zinthu zonse ndipo ndikuziyesa zinyalala kuti ndipindule Khristu

Sindikunena izi chifukwa choti ndikusowa thandizo, poti ine ndaphunzira kukhala wokwaniritsidwa ndi zimene ndili nazo. Ndimadziwa kusauka nʼkutani, ndipo ndimadziwa kulemera nʼkutani. Ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhutitsidwa mwa njira ina iliyonse, kaya nʼkudya bwino kapena kukhala ndi njala, kaya kukhala ndi chuma kapena umphawi. Ndikhoza kuchita zonse kudzera mwa Iye amene amandipatsa mphamvu. Komatu munachita bwino kundithandiza mʼmavuto anga. Ndipo inu Afilipi mukudziwa kuti masiku oyambirira olalikira Uthenga Wabwino, nditachoka ku Makedoniya, panalibe mpingo ndi umodzi omwe umene unagwirizana nane pa nkhani yopereka ndi kulandira, kupatula inu. Pakuti ngakhale pamene ndinali ku Tesalonika, munanditumizira kangapo zondithandiza pa zosowa zanga. Osati ndikufuna mphatso zanu, koma ndikufuna kuti pa zimene muli nazo pawonjezerekepo phindu. Ndalandira zonse ndipo ndili nazo zokwanira zoposa zosowa zanga popeza ndalandira kwa Epafrodito mphatso zochuluka zimene munatumiza. Ndizo zopereka za fungo labwino, nsembe zolandiridwa zokondweretsa Mulungu. Ndipo Mulungu wanga adzakwaniritsa zosowa zanu monga mwa chuma chake chaulemerero mwa Khristu Yesu.

Muzifunafuna zinthu za kumwamba, osati zinthu za pa dziko lapansi.

Kondwerani nthawi zonse. Pempherani kosalekeza. Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.

Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, “Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye.”

Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali.

Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.

Koma kulemekeza Mulungu kuli ndi phindu lalikulu. Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi. Koma ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire. Anthu amene amafuna kulemera amagwa mʼmayesero ndi mu msampha ndi mʼzilakolako zambiri zopusa ndi zoopsa zimene zimagwetsera anthu mʼchitayiko ndi mʼchiwonongeko. Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri.

Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa.

Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero.

Popeza mkulu wa mpingo amayendetsa ntchito za banja la Mulungu, ayenera kukhala wopanda cholakwa, asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena womwa zoledzeretsa, kapena wandewu, kapena wopeza phindu mwachinyengo.

Melikizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba. Anakumana ndi Abrahamu pamene ankabwerera kuchokera ku nkhondo atagonjetsa mafumu aja, Melikizedeki anakumana naye namudalitsa. Ndipo Abrahamu anamupatsa chakhumi cha zonse anafunkha. Choyamba dzina la Melikizedeki likutanthauza, “Mfumu ya chilungamo,” kenakanso, “Mfumu ya Salemu,” kutanthauza, “Mfumu ya mtendere.” Alibe abambo kapena mayi, alibe chiyambi kapena chitsiriziro cha moyo wake. Iye ali ngati Mwana wa Mulungu ndipo akupitirira kukhala wansembe wamuyaya. Mukuona tsono kuti munthuyo anali wamkulu ndithu, pakuti Abrahamu kholo lathu anamupatsa chakhumi cha zimene anafunkha. Tsono lamulo likuti, ana a Levi amene amakhala ansembe azilandira chakhumi kuchokera kwa Aisraeli, abale awo ngakhale kuti abale awowo ndi ochokera kwa Abrahamu. Melikizedeki sanali wochokera kwa Levi, komabe analandira chakhumi kuchokera kwa Abrahamu nadalitsa Abrahamuyo amene analandira malonjezo a Mulungu. Mosakayika konse, munthu amene amadalitsa ndi wamkulu kuposa amene akudalitsidwayo. Ansembe amene amalandira chakhumi amafa, choncho Melikizedeki ndi wamkulu kuwaposa iwo chifukwa Malemba amamuchitira umboni kuti ndi wamoyo. Wina angathe kunena kuti Levi, amene amalandira chakhumi, anapereka chakhumicho kudzera mwa Abrahamu, chifukwa pamene Melikizedeki anakumana ndi Abrahamu nʼkuti Levi ali mʼthupi la kholo lake.

Ndi chikhulupiriro Mose atakula, anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao. Iye anasankha kuzunzika nawo limodzi anthu a Mulungu kuposa kusangalala ndi zokondweretsa za uchimo kwa nthawi yochepa. Anaona kuti kuzunzika chifukwa cha Khristu kunali kwa mtengowapatali kuposa chuma cha ku Igupto, chifukwa amaona mphotho ya mʼtsogolo.

Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati, “Sadzakusiyani, kapena kukutayani konse.”

Ndipo musayiwale kumachita zabwino ndi kuthandiza ena, pakuti Mulungu amakondwera ndi nsembe zotere.

Abale omwe ndi anthu wamba anyadire pamene akwezedwa. Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo. Pakuti dzuwa limatuluka nʼkutentha kwake, ndipo limafotetsa zomera. Duwa lake limathothoka ndipo kukongola kwake kumatheratu. Momwemonso munthu wachuma adzazimirira ngakhale atamachitabe malonda ake.

Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda.

Tangoganizirani, pakati panu patabwera munthu atavala mphete yagolide ndi zovala zapamwamba, ndipo winanso wosauka nʼkulowa atavala sanza. Ngati musamala kwambiri munthu wovala bwinoyu uja, nʼkumuwuza kuti, “Khalani pa mpando wabwinowu,” koma wosauka uja nʼkumuwuza kuti, “Ima apo,” kapena “Khala pansi pafupi ndi chopondapo mapazi angawa,” kodi simunachite tsankho pakati panu ndi kukhala oweruza a maganizo oyipa? Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda? Koma mwakhala mukunyoza amphawi. Kodi si anthu olemerawa amene akukudyerani masuku pamutu? Si anthu amenewa amene amakukokerani ku bwalo la milandu? Kodi si omwewa amene amachita chipongwe dzina la wolemekezeka, limene inu mumatchulidwa?

Ngati musungadi lamulo laufumu lija lopezeka mʼMalemba lakuti, “Konda mnansi wako monga iwe mwini,” ndiye kuti mukuchita bwino.

Abale anga, phindu lake nʼchiyani ngati munthu anena kuti ali ndi chikhulupiriro koma chopanda ntchito zabwino? Kodi chikhulupiriro choterechi chingamupulumutse? Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku. Ngati mmodzi wa inu amuwuza kuti, “Pita ndi mtendere, ukafundidwe ndipo ukakhute,” koma osamupatsa zimene akuzisowa, phindu lake nʼchiyani pamenepa? Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

Koma ngakhale mumapempha simulandira, chifukwa mumapempha ndi zolinga zoyipa. Mumapempha kuti muzigwiritse ntchito pa zokusangalatsani nokha.

Tsono tamverani, inu amene mumati, “Lero kapena mawa tipita ku mzinda wakutiwakuti, tikatha chaka chimodzi tikuchita malonda ndi kupanga ndalama.” Chifukwa chiyani mukutero? Inu simukudziwa zimene ziti zichitike mawa. Kodi moyo wanu ndi wotani? Inu muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa ndipo kenaka ndikuzimirira. Koma inuyo muyenera kunena kuti, “Ambuye akalola, tikadzakhala ndi moyo, tidzachita zakutizakuti.”

Tsono tamverani, inu anthu achuma, lirani ndi kufuwula chifukwa cha zovuta zimene zidzakugwereni. Chuma chanu chawola ndipo njenjete zadya zovala zanu. Golide ndi siliva wanu zachita dzimbiri. Dzimbirilo lidzakhala umboni wokutsutsani ndi kuwononga mnofu wanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano otsiriza.

Taonani, ndalama za malipiro zimene munakanika kulipira aganyu aja ankasenga mʼmunda mwanu zikulira mokutsutsani. Kulira kwa okololawo kwamveka mʼmakutu mwa Ambuye Wamphamvuzonse. Mwakhala pa dziko lapansi pano moyo ofewa ndipo mwalidyera dziko lapansi. Mwadzinenepetsa pa tsiku lokaphedwa.

Mayeserowa abwera nʼcholinga chakuti chikhulupiriro chanu, chimene ndi chamtengo woposa wa golide, amene amawonongeka ngakhale amayengedwa ndi moto, chitsimikizike kuti ndi chenicheni. Pamenepo ndiye mudzalandire mayamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka.

Pakuti mukudziwa kuti simunawomboledwe ndi zinthu zimene zimawonongeka monga siliva kapena golide, kuchoka ku khalidwe lanu lachabe limene munalandira kwa makolo anu.

Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa maonekedwe akunja, monga kuluka tsitsi ndi kuvala zokometsera zagolide ndi zovala zamberewere. Mʼmalo mwake kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa munthu wa mʼkatimo, kukongola kosatha kwa mtima ofatsa ndi mzimu wachete, zimene ndi za mtengowapatali pamaso pa Mulungu.

Musamakonde dziko lapansi kapena chilichonse cha dziko lapansi. Ngati munthu wina aliyense akonda dziko lapansi, mwa iyeyo mulibe chikondi chokonda Atate. Pakuti zonse za mʼdziko lapansi, zilakolako za thupi, zinthu zimene maso amakhumbira ndiponso kuyandikira zinthu za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya.

Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu? Ana okondedwa, chikondi chathu chisakhale cha pakamwa pokha koma cha ntchito zathu ndi mʼchoonadi.

Tsono popeza ndiwe wofunda chabe, sindiwe wotentha kapena wozizira, ndatsala pangʼono kuti ndikulavule mʼkamwa mwanga. Iwe umati: ‘Ndine wolemera, ndine wachuma ndipo sindisowa kanthu.’ Koma sudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, waumphawi, wosaona ndi wamaliseche. Ndikukulangiza kuti ugule kwa Ine golide woyengedwa ndi moto kuti ukhale wolemera. Ugule zovala zoyera kuti uvale ndi kuphimba umaliseche wako wochititsa manyaziwo. Ndiponso ugule kwa Ine mankhwala a mʼmaso kuti uwone.

Ndinamva ngati liwu kuchokera pakati pa zamoyo zinayi zija likuti, “Kilogalamu imodzi ya tirigu mtengo ndi malipiro a tsiku limodzi ndipo makilogalamu atatu a barele mtengo wake ndi malipiro a tsiku limodzi koma usawononge mafuta ndi vinyo!”

Kenaka, mafumu a pa dziko lapansi, ana a mafumu, atsogoleri a ankhondo, olemera, amphamvu, kapolo aliyense, ndi mfulu aliyense anakabisala kumapanga ndi pakati pa matanthwe a ku mapiri. Iwo anafuwulira mapiri ndi matanthwe kuti, “Tigwereni ndi kutivundikira kuti asatione wokhala pa mpando waufumuyo ndi kupulumuka ku mkwiyo wa Mwana Wankhosa!

Chinakakamiza aliyense, wamngʼono, wamkulu, wolemera, wosauka, mfulu ndi kapolo kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi. Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, chimene ndi dzina la chirombocho kapena nambala yotanthauza dzina lake.

“Amalonda a dziko lapansi adzalira nakhuza maliro ake chifukwa palibenso amene akugula katundu wawo, katundu wagolide, siliva, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale; nsalu zoyera kwambiri zapamwamba ndi zofiira; nsalu zasilika ndi zapepo; mitengo iliyonse yonunkhira ndi zinthu zilizonse zopangidwa ndi mnyanga, kapena matabwa ogulidwa ndi ndalama zambiri kapena mkuwa kapena chitsulo ndi mwala wonyezimira; zokometsera zakudya, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta a olivi, ufa wosalala ndi tirigu; ngʼombe ndi nkhosa; akavalo ndi ngolo; ndi anthu adzagulitsidwa ukapolo. “Iwo adzanena kuti, ‘Chipatso chimene unachilakalaka chakuchokera. Chuma chako chonse ndi ulemerero zatha, sizidzapezekanso.’

Amalonda amene anagulitsa zinthu izi napeza chuma kuchokera kwa iye adzayima patali potero ataopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kukhuza maliro ndipo adzalira mokuwa kuti, “ ‘Tsoka! Tsoka! Mzinda waukulu, iwe wovala nsalu zoyera kwambiri, zapepo ndi zofiira, ndi wonyezimira ndi golide, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale! Chuma chambiri choterechi chafika powonongeka mu ora limodzi!’ “Oyendetsa sitima ndi onse oyenda pa sitima ya pamadzi, ogwira ntchito mʼsitima ndi onse amene amadalira nyanja pamoyo wa tsiku ndi tsiku adzayima patali potero.

Iye anandiwuza kuti, “Kwatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa onse akumva ludzu, ndidzawapatsa zakumwa zaulere zochokera ku kasupe wamadzi amoyo.

Mzimu Woyera ndi mkwatibwi akuti, “Bwerani!” Ndipo amene akumva anena kuti Bwerani! Iye amene ali ndi ludzu abwere, ndipo aliyense amene afuna alandire mphatso yaulere ya madzi amoyo.

Chichewa - Chichewa - NY

NYCCL - Mawu A Mulungu Mu Chichewa Chalero - 2016

This Bible text is from Biblica Open God's Word In Contemporary Chichewa
https://open.bible/bibles/chichewa-biblica-text-bible/
provided by: Biblica Inc, available by Creative Commons CC-BY-SA-4.0,
and this new compilation is shared as www.creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0.
Languages are made available to you by www.ipedge.net