32 – Kufa chifukwa cha chikhulupiriro

Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Kufa chifukwa cha chikhulupiriro.

Mavesi atatu ofunika kwambiri

Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti, ‘Mbewu ya tirigu imakhala imodzi yokha ngati sikugwa mʼnthaka ndi kufa. Koma ngati imfa, imabereka mbewu zambiri.’ Munthu amene amakonda moyo wake adzawutaya, pamene munthu amene amadana ndi moyo wake mʼdziko lino lapansi adzawusungira ku moyo wosatha. Aliyense amene atumikira Ine ayenera kunditsata; ndipo kumene Ine ndili, wotumikira wanga adzakhalanso komweko. Atate anga adzalemekeza amene atumikira Ine.

Iwo adzakuchotsani mʼsunagoge mwawo. Kunena zoona, nthawi ikubwera imene aliyense amene adzakuphani adzaganiza kuti akutumikira Mulungu. Iwo adzachita zoterozo chifukwa sanadziwe Atate kapena Inenso. Ine ndakuwuzani izi kuti nthawi ikadzafika mudzakumbukire kuti Ine ndinakuchenjezani kale. Ine sindinakuwuzeni izi poyamba paja chifukwa ndinali nanu.”

Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachisanu, ndinaona kunsi kwa guwa lansembe kunali mizimu ya anthu amene anaphedwa chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi chifukwa chochitira umboni. Iwo anafuwula kuti, “Mudzawaleka mpaka liti, Inu Ambuye wamkulu, woyera ndi woona, osawaweruza anthu okhala mʼdziko lapansi ndi kulipsira magazi athu?” Pamenepo aliyense wa anthuwo anapatsidwa mwinjiro woyera ndipo anawuzidwa kuti adikire pangʼono kufikira chiwerengero cha anzawo ndi abale awo amene anayeneranso kuphedwa ngati iwo, chitakwanira.

Mavesi onse motsatira dongosolo lolondola – 322 ndime

Patapita nthawi, Kaini anatenga zipatso za ku munda nakazipereka kwa Yehova monga nsembe. Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake. Koma sanakondwere ndi Kaini ndi nsembe yake. Kotero Kaini anakwiya kwambiri ndipo nkhope yake inagwa. Choncho Yehova anati kwa Kaini, “Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa? Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.” Tsiku lina Kaini anati kwa mʼbale wake Abele, “Tiye tipite ku munda.” Ndipo ali ku mundako, Kaini anawukira mʼbale wake namupha. Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?” Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?” Yehova anati, “Kodi wachita chiyani? Tamvera! Magazi a mʼbale wako akulirira kwa Ine kuchokera mʼnthaka.

Nthawi ina zitatha izi, Mulungu anamuyesa Abrahamu. Iye anati, “Abrahamu!” Ndipo iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.” Ndipo Mulungu anati, “Tenga Isake, mwana wako yekhayo amene umamukonda ndi kupita naye ku dziko la Moriya. Ukamupereke iye ngati nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri a kumeneko limene ndidzakuwuza.” Abrahamu anadzuka mmamawa wake namangirira chokhalira pa bulu. Atadula nkhuni zokwanira zowotchera nsembe yopsereza, Abrahamu, antchito ake awiri pamodzi ndi Isake ananyamuka kupita kumalo kumene Mulungu anamuwuza Abrahamu. Pa tsiku lachitatu, Abrahamu anakweza maso ake ndipo anaona malowo chapatali. Ndipo Abrahamu anati kwa antchito ake aja, “Bakhalani pano ndi buluyu. Ine ndi mnyamatayu tipita uko kukapemphera, koma tibweranso.” Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza zija namusenzetsa mwana wake Isake, ndipo iye mwini anatenga moto ndi mpeni. Pamene awiriwo amayendera pamodzi, Isake anati kwa abambo ake Abrahamu, “Abambo?” Abrahamu anayankha, “Ee mwana wanga.” Isake anafunsa, “Moto ndi nkhuni zilipo, koma nanga mwana wankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?” Abrahamu anayankha, “Mwana wanga, Mulungu adzipezera yekha mwana wankhosa wa nsembe yopsereza.” Ndipo awiriwo anapitiriza ulendo. Atafika pamalo pamene Mulungu anamuwuza paja, Abrahamu anamangapo guwa lansembe nayika nkhuni pamwamba pa guwapo. Kenaka anamumanga mwana wake Isake namugoneka paguwapo, pamwamba pa nkhuni paja. Kenaka Abrahamu anatambasula dzanja lake natenga mpeni kuti aphe mwana wake. Koma mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba nati, “Abrahamu! Abrahamu!” Iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.” Mngeloyo anati, “Usatambasulire mwanayo dzanja lako kuti umuphe, pakuti tsopano ndadziwa kuti iwe umaopa Mulungu. Iwe sunandimane mwana wako mmodzi yekhayo.” Abrahamu anatukula maso ake ndipo anaona nkhosa yamphongo itakoledwa ndi nyanga zake mu ziyangoyango. Iye anapita nakatenga nkhosa ija ndikuyipha ngati nsembe yopsereza mʼmalo mwa mwana wake.

Ziweto zimene musankhe ziyenera kukhala zazimuna za chaka chimodzi, zopanda chilema, ndipo zikhale nkhosa kapena mbuzi.

“Usaphe.

Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”

Kenaka mfumu inalamulira alonda amene anali naye kuti, “Iphani ansembe a Yehovawa chifukwa iwo akugwirizana ndi Davide. Iwo amadziwa kuti Davide ankathawa koma sanandiwuze.” Koma antchito a mfumu aja sanasamule dzanja kuti aphe ansembe a Yehova. Kotero mfumu inalamula Doegi kuti, “Uwaphe ndiwe ansembewa.” Choncho Doegi Mwedomu anapita ndi kuwapha. Tsiku limenelo iye anapha amuna 85 amene amavala efodi wa nsalu yofewa. Kunena za Nobi, mzinda wa ansembe, Sauli anapha amuna ndi amayi, ana ndi makanda pamodzi ndi ngʼombe, abulu ndi nkhosa.

Pamene Yezebeli ankapha aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri 100 ndi kuwabisa mʼmapanga awiri, phanga lililonse aneneri makumi asanu, ndipo ankawapatsa chakudya ndi madzi).

Iye anayankha kuti, “Ndakhala wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Aisraeli asiya pangano lanu, agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga. Ndatsala ine ndekha ndipo tsopano akufuna kundipha.”

Dalirani Yehova ndi mphamvu zake; funafunani nkhope yake nthawi zonse.

Kenaka Mzimu wa Mulungu unabwera pa Zekariya mwana wa wansembe Yehoyada. Iye anayimirira pamaso pa anthu ndipo anati, “Zimene Mulungu akunena ndi Izi: ‘Chifukwa chiyani simukumvera Malamulo a Yehova? Simudzapindula. Chifukwa mwasiya Yehova, Iyenso wakusiyani.’ ” Koma anthuwo anamuchitira chiwembu molamulidwa ndi mfumu ndipo anamugenda miyala ndi kumupha mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu.

“Komabe iwo anakhala osamvera ndipo anakuwukirani nafulatira malamulo anu. Anapha aneneri anu, amene anakawadandaulira kuti abwerere kwa Inu. Anachita chipongwe choopsa.

Atamva zimenezi, Yobu anayimirira nangʼamba mkanjo wake, ndi kumeta tsitsi lake. Kenaka anadzigwetsa pansi napembedza Mulungu, nati, “Ndinatuluka maliseche mʼmimba mwa amayi anga, namonso mʼmanda ndidzalowa wamaliseche. Yehova ndiye anapereka ndipo Yehova watenga; litamandike dzina la Yehova.”

Ngakhale Iye andiphe, komabe ndidzamukhulupirira; ndithu, ndidzafotokoza mlandu wanga pamaso pake.

Koma ndikudziwa kuti mpulumutsi wanga ali ndi moyo, ndipo pa nthawi yomaliza adzabwera kudzanditeteza. Ndipo khungu langa litatha nʼkuwonongeka, mʼthupi langa lomweli ndidzamuona Mulungu. Ine ndemwe ndidzamuona Iye ndi maso angawa, ineyo, osati wina ayi. Ndithu mtima wanga ukufunitsitsadi!

Koma Iye amadziwa mmene ndimayendera; Iyeyo akandiyesa adzandipeza kuti ndili ngati golide. Mapazi anga akhala akuponda mʼmapazi ake; ndasunga njira yake ndipo sindinayitaye.

Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu? Akonzekeranji zopanda pake anthu? Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo; ndipo olamulira asonkhana pamodzi kulimbana ndi Ambuye ndi wodzozedwa wakeyo. Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo ndipo titaye zingwe zawo.” Wokhala mmwamba akuseka; Ambuye akuwanyoza iwowo.

Koma lolani kuti onse amene apeza chitetezo mwa Inu akondwere; lolani kuti aziyimba nthawi zonse chifukwa cha chimwemwe. Aphimbeni ndi chitetezo chanu, iwo amene amakonda dzina lanu akondwere mwa Inu.

Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. Choncho mtima wanga ndi wosangalala ndipo pakamwa panga pakukondwera; thupi langanso lidzakhala pabwino, chifukwa Inu simudzandisiya ku manda, simudzalola kuti woyera wanu avunde. Inu mwandidziwitsa njira ya moyo; mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu, ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja.

Ndipo ine mʼchilungamo ndidzaona nkhope yanu; pamene ndidzadzuka, ndidzakondwera kwambiri poonana nanu.

amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo chifukwa cha dzina lake. Ngakhale ndiyende mʼchigwa cha mdima wakuda bii, sindidzaopa choyipa, pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditonthoza.

Salimo la Davide. Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndi linga la moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani? Pamene anthu oyipa abwera kudzalimbana nane kudzadya mnofu wanga, pamene adani anga ndi achiwembu andithira nkhondo, iwo adzapunthwa ndi kugwa. Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzaopa. Ngakhale nkhondo itayambika kulimbana nane, ngakhale nthawi imeneyo, ine ndidzalimbika mtima. Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova, ichi ndi chimene ndidzachifunafuna: kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova, ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake. Pakuti pa tsiku la msautso Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo; adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.

Kondwerani mwa Yehova inu olungama; imbani, inu nonse amene muli owongoka mtima!

Oyipa amakonza chiwembu kutsutsana ndi olungama ndipo amawakukutira mano; koma Ambuye amaseka oyipa pakuti Iye amadziwa kuti tsiku lawo likubwera. Oyipa amasolola lupanga ndi kupinda uta kugwetsa osauka ndi osowa, kupha iwo amene njira zawo ndi zolungama. Koma malupanga awo analasa mitima yawo yomwe, ndipo mauta awo anathyoka.

Komabe chifukwa cha Inu timakumana ndi imfa tsiku lonse, tili ngati nkhosa zoyenera kuti ziphedwe.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali. Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto. Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,

Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha; Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.

Tulani nkhawa zanu kwa Yehova ndipo Iye adzakulimbitsani; Iye sadzalola kuti wolungama agwe.

Koma Inu Yehova, mumawaseka, mumayinyoza mitundu yonseyo. Inu mphamvu yanga, ine ndiyangʼana kwa inu; Inu Mulungu, ndinu linga langa. Mulungu wanga wachikondi. Mulungu adzapita patsogolo panga ndipo adzandilola kunyada pa iwo amene amandinyoza.

Pa bedi panga ndimakumbukira inu; ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku. Chifukwa ndinu thandizo langa, ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu. Moyo wanga umakangamira Inu; dzanja lanu lamanja limandigwiriziza. Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa; adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi.

Koma olungama asangalale ndi kukondwera pamaso pa Mulungu; iwo akondwere ndi kusangalala. Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando, mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo; dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.

Komabe ineyo ndili ndi Inu nthawi zonse; mumandigwira dzanja langa lamanja. Inu mumanditsogolera ndi malangizo anu ndipo pambuyo pake mudzanditenga ku ulemerero. Kodi kumwamba ndili ndi yani kupatula Inu? Ndipo dziko lapansi lilibe chilichonse chimene ndimachilakalaka koposa Inuyo. Thupi ndi mtima wanga zitha kufowoka, koma Mulungu ndiye mphamvu ya mtima wanga ndi cholandira changa kwamuyaya.

Ndi odala amene aphunzira kuyamika Inu, amene amayenda mʼkuwunika kwa nkhope yanu Yehova. Amakondwera mʼdzina lanu tsiku lonse lathunthu; amasangalala koposa mʼchilungamo chanu.

Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.

Kwezekani Inu Mulungu, kuposa mayiko akumwamba, ndipo ulemerero wanu uphimbe dziko lonse lapansi.

Yehova amateteza munthu wodzichepetsa mtima; pamene ndinali ndi chosowa chachikulu, Iye anandipulumutsa. Pumula iwe moyo wanga, pakuti Yehova wakuchitira zokoma. Pakuti Inu Yehova mwapulumutsa moyo wanga ku imfa, maso anga ku misozi, mapazi anga kuti angapunthwe, kuti ine ndiyende pamaso pa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.

Imfa ya anthu oyera mtima ndi yamtengowapatali pamaso pa Yehova.

Oyera mtima asangalale mu ulemu wake ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo.

Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino, ndipo tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa.

Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya, Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmaso mwa munthu aliyense; adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi, Yehova wayankhula.

Koma anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo; matupi awo adzadzuka. Iwo amene ali ku fumbi tsopano adzadzuka ndi kuyimba mosangalala. Monga mame amafewetsa pansi kutsitsimutsa zomera, momwenso Yehova adzaukitsa anthu amene anafa kale.

Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera. Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba; kumeneko adzakondwa mpaka muyaya. Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe, ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.

Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga; kondwera, iwe dziko lapansi; imbani nyimbo inu mapiri! Pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake, ndipo wachitira chifundo anthu ake ovutika.

Ndinapereka msana wanga kwa ondimenya masaya anga ndinawapereka kwa anthu ondizula ndevu; sindinawabisire nkhope yanga anthu ondinyoza ndi ondilavulira. Popeza Ambuye Yehova amandithandiza, sindidzachita manyazi. Tsono ndalimba mtima ngati msangalabwi, chifukwa ndikudziwa kuti sindidzachita manyazi.

Anthu amene Yehova anawawombola adzabwerera nakafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa; chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pa nkhope zawo. Adzakhala ndi chikondwerero ndi chimwemwe, chisoni ndi kubuwula zidzathawa.

Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu, munthu amene moyo wake unali wamasautso, wozolowera zowawa, ndipo anali ngati munthu amene anzake amaphimba nkhope zawo akamuona. Iye ananyozedwa, ndipo ife sitinamuyese kanthu. Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife; ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga, kumukantha ndi kumusautsa. Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu; iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere, ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa. Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera, aliyense mwa ife akungodziyendera; ndipo Yehova wamusenzetsa zoyipa zathu zonse. Anthu anamuzunza ndi kumusautsa, koma sanayankhule kanthu. Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira, kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta, momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake. Atatha kumugwira mwankhanza ndikumuyimba mlandu, kenaka anapita naye kukamupha. Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake, poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo? Ndani anaganizirapo poona kuti iye anakanthidwa chifukwa cha zolakwa za anthu anga? Anamukonzera manda ake pamodzi ndi anthu oyipa ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi anthu achuma, ngakhale kuti iye sanachite za chiwawa, kapena kuyankhula za chinyengo. Komatu ndi Yehova amene anafuna kuti amuzunze ndi kumusautsa. Yehova anapereka moyo wa mtumiki wake kuti ukhale nsembe yoperekedwa chifukwa cha zolakwa. Tsono iye adzaona zidzukulu zake ndipo adzakhala ndi moyo wautali, ndipo chifuniro cha Yehova chidzachitika mwa iye. Atatha mazunzo a moyo wake, adzaona kuwala, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzalungamitsa anthu ambiri, popeza adzasenza zolakwa zawo. Motero Ine ndidzamupatsa ulemu pamodzi ndi akuluakulu, adzagawana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza anapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo anamuyika mʼgulu la anthu olakwa kuti akhululukidwe. Pakuti iye anasenza machimo a anthu ambiri, ndipo anawapempherera anthu olakwa.

Inu mudzatuluka mu mzindawo mwachimwemwe ndipo adzakutsogolerani mwamtendere; mapiri ndi zitunda zidzakuyimbirani nyimbo, ndipo mitengo yonse yamʼthengo idzakuwombereni mʼmanja.

Anthu olungama amafa, ndipo palibe amene amalingalira mu mtima mwake; anthu odzipereka amatengedwa, ndipo palibe amene amamvetsa chifukwa chake. Anthu olungama amatengedwa kuti tsoka lisawagwere. Iwo amene amakhala moyo wolungama amafa mwamtendere; amapeza mpumulo pamene agona mu imfa.

Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni, nkhata ya maluwa yokongola mʼmalo mwa phulusa, ndiwapatse mafuta achikondwerero mʼmalo mwa kulira. Ndiwapatse chovala cha matamando mʼmalo mwa mtima wopsinjika. Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo, yoyidzala Yehova kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.

Ine ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Yehova; moyo wanga ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso, ndipo wandiveka mkanjo wachilungamo. Zili ngati mkwati wovala nkhata ya maluwa mʼkhosi mwake, ndiponso ngati mkwatibwi wovala mikanda yamtengowapatali.

Iyenso anasautsidwa mʼmasautso awo onse, ndipo mngelo wochokera kwa Iye anawapulumutsa. Mwa chikondi ndi chifundo chake iye anawapulumutsa, anawanyamula ndikuwatenga kuyambira kale lomwe.

Koma alipo Ayuda ena Sadirake, Mesaki ndi Abedinego amene munawayika kuti ayangʼanire ntchito ya dera la ku Babuloni. Anthu amenewa sakumvera inu mfumu. Iwo sakutumikira milungu yanu kapena kulambira fano la golide limene munaliyimikalo.” Tsono Nebukadinezara anakwiya ndi kupsa mtima kwambiri, ndipo anayitanitsa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego. Choncho amuna awa anabwera pamaso pa mfumu, ndipo Nebukadinezara anawafunsa kuti, “Kodi ndi zoona, Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, kuti simukutumikira milungu yanga kapena kupembedza fano la golide ndinaliyikalo? Tsopano ngati muli okonzeka kulambira ndi kupembedza fano ndinalipanga, mukangomva kulira kwa lipenga chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muchita bwino. Koma ngati simulipembedza, mudzaponyedwa mʼnganjo ya moto. Nanga ndi mulungu uti amene adzatha kukupulumutsani mʼmanja anga?”

Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anayankha mfumu Nebukadinezara kuti, “Sikoyenera kuti tikuyankheni pa nkhani imeneyi. Ngati tiponyedwa mʼngʼanjo ya moto, Mulungu amene timamutumikira akhoza kutipulumutsa ku ngʼanjo yamotoyo, ndipo adzatilanditsa mʼdzanja lanu mfumu. Koma ngakhale Mulungu wathu atapanda kutipulumutsa, tikufuna mudziwe inu mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu kapena kupembedza fano la golide limene munaliyimika.”

Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima ndi Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, ndipo anayipidwa nawo. Iye analamulira kuti ngʼanjo ayitenthetse kasanu ndi kawiri kuposa nthawi zonse, ndipo analamula ena mwa asilikali amphamvu kwambiri mʼgulu lake lankhondo kuti amange Sadirake, Mesaki ndi Abedenego ndi kuwaponya mʼngʼanjo ya moto. Choncho amuna awa, atavala mikanjo yawo, mabuluku, nduwira ndi zovala zina zonse, anamangidwa ndi kuponyedwa mʼngʼanjo ya moto. Tsono popeza lamulo la mfumu linali lofulumiza, ngʼanjo inatenthetsedwa kowirikiza mwakuti malawi ake anapha asilikali amene ananyamula Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, ndipo anyamata atatuwa, ali chimangidwire, anagwera mʼngʼanjo ya moto.

Kenaka mfumu Nebukadinezara anadabwa ndipo anafunsa nduna zake kuti, “Kodi sanali amuna atatu amene anamangidwa ndi kuponyedwa mʼmoto?” Iwo anayankha kuti, “Ndi zoonadi, mfumu.” Iye anati, “Taonani! Ndikuona amuna anayi akuyendayenda mʼmoto, osamangidwa ndi osapwetekedwa ndipo wachinayi akuoneka ngati mwana wa milungu.” Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo langʼanjo ya moto ndi kufuwula kuti, “Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, tulukani! Bwerani kuno!” Ndipo Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anatuluka mʼmoto, ndipo akalonga, akazembe, abwanamkubwa ndi nduna zamfumu anasonkhana mowazungulira. Anaona kuti moto sunatenthe matupi awo ngakhale tsitsi kumutu kwawo silinapse; zovala zawo sizinapse, ndipo sankamveka fungo la moto. Kenaka Nebukadinezara anati, “Atamandike Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, amene anatumiza mngelo wake ndi kupulumutsa atumiki ake! Iwo anakhulupirira Iye ndi kunyozera lamulo la mfumu ndipo anali okonzeka kutaya moyo wawo koposa kutumikira kapena kupembedza mulungu wina aliyense wosakhala Mulungu wawo.

Danieli atamva kuti lamulo lasindikizidwa, anapita ku nyumba kwake nalowa mʼchipinda chapamwamba chimene mazenera ake anali otsekula kuloza ku Yerusalemu. Katatu pa tsiku iye ankagwada pansi pa mawondo ndipo amapemphera, kuyamika Mulungu wake, monga momwe ankachitira kale. Ndipo anthu awa anapita pamodzi ndi kukapeza Danieli akupemphera ndi kupempha Mulungu wake kuti amuthandize. Kotero iwo anapita kwa mfumu ndipo anayankhula naye za lamulo lake kuti, “Kodi simunasindikize lamulo lakuti pa masiku makumi atatu otsatirawa aliyense amene apemphera kwa mulungu wina aliyense kapena kwa munthu kupatula kwa inu mfumu, adzaponyedwa mʼdzenje la mikango?” Mfumu inayankha kuti, “Lamulo lilipobe monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperezi, amene sangathe kusinthika.” Kenaka iwo anati kwa mfumu, “Danieli, amene ndi mmodzi mwa akapolo ochokera ku Yuda, sakulabadira inu mfumu, kapena lamulo limene munasindikizapo dzina lanu lija. Iye akupempherabe katatu pa tsiku.” Mfumu itamva izi, inavutika kwambiri mu mtima mwake. Iyo inayesa kupeza njira yopulumutsira Danieli. Iyo inachita chotheka chilichonse kufikira kulowa kwa dzuwa kuti imupulumutse. Ndipo anthuwo anapita pamodzi kwa mfumu ndipo anati kwa iye, “Kumbukirani, inu mfumu kuti monga mwa lamulo la Amedi ndi Aperezi, palibe chimene mfumu inalamulira kapena kukhazikitsa chimasinthidwa.”

Choncho mfumu inalamula, ndipo anabwera naye Danieli ndi kukamuponya mʼdzenje la mikango. Mfumu inati kwa Danieli, “Mulungu wako amene umutumikira nthawi zonse, akupulumutse!” Anatenga mwala natseka pa khoma pa dzenje la mikango, ndipo mfumu inadindapo chizindikiro chake ndi cha nduna zake kuti wina asasinthepo kanthu pa za Danieli. Kenaka mfumu inabwerera ku nyumba yake ndipo inakhala usiku wonse osadya kanthu, osalola chosangalatsa chilichonse. Ndipo sinagone tulo. Mʼbandakucha, mfumu inanyamuka ndi kufulumira kupita ku dzenje la mikango lija. Itayandikira pa dzenjelo, inayitana Danieli moonetsa nkhawa, “Danieli, mtumiki wa Mulungu wa moyo! Kodi Mulungu wako, amene umutumikira nthawi zonse, wakulanditsa ku mikango?” Danieli anayankha kuti, “Inu mfumu mukhale ndi moyo wautali! Mulungu wanga anatumiza mngelo wake, ndipo anatseka pakamwa pa mikango. Iyo sinandivulaze chifukwa Mulungu anaona kuti ndine wosalakwa ndi kutinso sindinakulakwireni inu mfumu.” Mfumu inali ndi chimwemwe chopambana ndipo inalamulira kuti amutulutse Danieli mʼdzenjemo. Ndipo atamutulutsa Danieli mʼdzenjemo, sanapezeke ndi chilonda chilichonse pa thupi lake, chifukwa iye anadalira Mulungu wake.

Idzayankhula motsutsana ndi Wammwambamwamba ndipo adzazunza oyera mtima ndi kusintha masiku azikondwerero ndi malamulo. Oyera mtimawo adzalamulidwa ndi mfumuyi kwa zaka zitatu ndi theka.

“Pa nthawi imeneyo Mikayeli, mngelo wamkulu amene amateteza anthu a mtundu wako, adzabwera. Imeneyi idzakhala nthawi ya mavuto aakulu omwe sanaonekepo kuyambira pachiyambi cha mitundu ya anthu mpaka nthawi ikudzayo. Komatu pa nthawiyi anthu a mtundu wako, aliyense amene dzina lake lidzapezeke lolembedwa mʼbuku adzapulumutsidwa. Ambiri mwa amene akugona mʼnthaka adzadzuka: ena adzapita ku moyo wosatha, ena ku malo amanyazi ndi chilango chosatha. Amene ali anzeru mʼnjira ya chilungamo adzawala ngati kuwala kwa mlengalenga, ndipo amene alondolera ambiri ku njira yolungama, adzawala ngati nyenyezi ku nthawi zosatha.

Yehova ndi wabwino, ndiye kothawirako nthawi ya masautso. Amasamalira amene amamudalira,

komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga.

Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.” “Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine. Sangalalani, kondwerani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba, chifukwa moterenso ndi mmene anazunzira aneneri inu musanabadwe.

Koma Ine ndikuwuzani kuti, ‘Kondani adani anu ndi kuwapempherera okuzunzani

“Musadziwunjikire chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri zimawononga ndi pamene mbala zimathyola ndi kuba. Koma mudziwunjikire chuma kumwamba kumene njenjete ndi dzimbiri siziwononga ndipo mbala sizithyola ndi kuba.

Chenjerani ndi anthu pakuti adzakuperekani ku mabwalo amilandu nadzakukwapulani mʼmasunagoge mwawo. Chifukwa cha Ine, mudzaperekedwa kwa olamulira ndi kwa mafumu kuti mukhale mboni kwa iwo ndi kwa a mitundu ina. Koma pamene akumangani, inu musadandaule kuti mukanena bwanji kapena mukanena chiyani. Mudzapatsidwa pa nthawi imeneyo zoti munene, pakuti sindinu mudzanena, koma Mzimu Woyera wa Atate anu, adzayankhula mwa inu.

“Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe ndi abambo mwana wawo: ndipo ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. Anthu onse adzada inu chifukwa cha Ine, koma iye amene apirira mpaka kumapeto, adzapulumuka. Pamene akuzunzani pamalo ena thawirani kwina. Pakuti ndikuwuzani zoonadi kuti simudzamaliza mizinda yonse ya Israeli Mwana wa Munthu asanabwere.

Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena.

Aliyense amene satenga mtanda wake ndi kunditsata Ine sayenera kukhala wanga. Aliyense amene asunga moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo chifukwa cha Ine adzawupeza.

“Idzani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa. Ndipo inu mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa ndi losavuta ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”

Koma Afarisi anatuluka kunja ndi kukonza njira yoti amuphere.

Zimene zinafesedwa pa malo amiyala ndi munthu amene amamva mawu ndi kuwalandira msanga ndi chimwemwe. Koma popeza alibe muzu, iwo amakhala nthawi yochepa. Pamene vuto kapena zunzo libwera chifukwa cha mawu, iye amagwa mofulumira.

“Ufumu wakumwamba ufanana ndi chuma chobisika mʼmunda. Munthu atachipeza anachibisanso ndipo ndi chimwemwe anapita nakagulitsa zonse anali nazo, nakagula mundawo. “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi wogulitsa malonda amene amafuna ngale zabwino. Atapeza imodzi ya mtengowapatali, iye anapita nakagulitsa chilichonse anali nacho ndi kukayigula.”

Ndipo iye anati kwa antchito ake, “Uyu ndi Yohane Mʼbatizi; iye wauka kwa akufa! Ichi ndi chifukwa chake mphamvu zodabwitsa zikugwira ntchito mwa iye.” Pakuti Herode anamugwira Yohane ndi kumumanga ndipo anamuyika mʼndende chifukwa cha Herodia mkazi wa mʼbale wake Filipo. Chifukwa Yohane anakhala akunena kwa iye kuti, “Sichololedwa kwa inu kutenga mkaziyo.” Herode anafuna kupha Yohane koma iye anaopa anthu chifukwa anamuyesa iye mneneri. Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodia anavina pamaso pa anthu ndipo anasangalatsa kwambiri. Kotero Herode analonjeza ndi lumbiro kumupatsa chilichonse chimene mwanayo angamupemphe. Ndipo atamupangira amayi ake anati, “Mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.” Mfumuyo inamva chisoni koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo amene anali pa phwando lake analamulira kuti chofuna chake chipatsidwe; ndipo anakadula mutu wa Yohane mʼndende. Mutu wake anawubweretsa mʼmbale ndi kumupatsa mtsikanayo amene anawutengera kwa amayi ake. Ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo wake ndi kukawuyika mʼmanda. Pomwepo iwo anapita kukamuwuza Yesu.

Kuyambira nthawi imeneyo Yesu anayamba kuwafotokozera ophunzira ake kuti Iye ayenera kupita ku Yerusalemu ndi kukazunzidwa kwambiri mʼmanja mwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo kuti ayenera kuphedwa, ndi kuti tsiku lachitatu adzaukitsidwa.

Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Ngati wina aliyense abwera pambuyo panga ayenera kudzikana ndi kutenga mtanda wake ndi kunditsata Ine. Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupeza.

Petro anamuyankha Iye kuti, “Ife tinasiya zonse ndi kukutsatirani Inu! Nanga tsono ife tidzalandira chiyani?”

“Tikupita ku Yerusalemu, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo adzamuweruza kuti aphedwe, ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amunyoze ndi kumukwapula ndi kumupachika. Pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa!”

“Tamverani fanizo lina: Panali mwini munda amene anadzala mphesa. Anamanga mpanda kuzungulira mundawo, nakumba moponderamo mphesa ndipo anamanga nsanja. Kenaka anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita pa ulendo. Pamene nthawi yokolola inakwana, anatumiza antchito ake kwa matenanti aja kuti akatenge zipatso zake. “Alimi aja anagwira antchito ake; namenya mmodzi, napha wina, ndi kumuponya miyala wachitatuyo. Kenaka anatumiza antchito ena oposa oyambawo ndipo matenantiwo anawachitira chimodzimodzi. Pomalizira anatumiza mwana wake. Anati adzamuchitira ulemu mwana wanga. “Koma alimiwo ataona mwanayo anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndiye olowa mʼmalo mwa abambo ake. Tiyeni timuphe ndipo titenge cholowa chake.’ Pamenepo anamutenga namuponyera kunja kwa munda wamphesa namupha.

Choncho ndi kutumizirani aneneri ndi anthu anzeru ndi aphunzitsi. Ena a iwo mudzawapha ndi kuwapachika; ena mudzawakwapula mʼmasunagoge anu ndi kuwafunafuna kuchokera mudzi wina kufikira wina. Ndipo magazi onse a olungama amene anakhetsedwa pansi pano, kuyambira magazi a Abele, olungama kufikira Zakariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, adzakhala pa inu.

“Pamenepo adzakuperekani kuti mukazunzidwe ndi kuphedwa, ndipo mitundu yonse idzakudani chifukwa cha Ine. Pa nthawi imeneyo ambiri adzasiya chikhulupiriro ndipo adzadana ndi kuperekana wina ndi mnzake,

koma wopirira kufikira chimaliziro adzapulumuka.

Popeza kudzakhala masautso aakulu, omwe safanana ndi ena ali onse chiyambireni cha dziko lapansi mpaka lero lino ndipo sadzafanananso ndi ena. Ngati masiku amenewo sakanafupikitsidwa, palibe mmodzi akanapulumuka, koma chifukwa cha osankhidwawo masiku amenewo adzafupikitsidwa.

ndipo anapangana kuti amugwire Yesu mobisa ndi kumupha.

Koma Petro ananenetsa nati, “Ngakhale kutakhala kufa nanu pamodzi, sindidzakukanani.” Ndipo ophunzira onse ananena chimodzimodzi.

Akulu a ansembe ndi akulu olamulira Ayuda amafunafuna umboni wonama wofuna kuphera Yesu.

Kenaka anamulavulira kumaso namumenya ndi zibakera. Ena anamumenya makofi.

Mmamawa, akulu a ansembe onse ndi akuluakulu anavomerezana kuti aphe Yesu. Anamumanga, napita naye kukamupereka kwa bwanamkubwa Pilato.

Pamenepo anawamasulira Baraba koma analamula kuti Yesu akakwapulidwe, ndipo anamupereka kuti akapachikidwe.

Anamuthira malovu ndipo anatenga ndodo namumenya nayo pa mutu mobwerezabwereza. Atamaliza kumuchitira chipongwe, anamuvula malaya aja namuveka malaya ake aja napita naye kokamupachika.

Atamupachika Iye, anagawana zovala zake pochita maere.

Ena, monga mbewu zofesedwa pa miyala, amamva mawu ndipo nthawi yomweyo amawalandira ndi chimwemwe. Koma popeza alibe mizu, amakhala kwa kanthawi kochepa. Mavuto kapena masautso akafika chifukwa cha mawu, amagwa mofulumira.

Mfumu Herode anamva zimenezi, pakuti dzina la Yesu linali litadziwika kwambiri. Ena amati, “Yohane Mʼbatizi waukitsidwa kwa akufa, ndipo nʼchifukwa chake mphamvu zochita zodabwitsa zinkagwira ntchito mwa Iye.” Ena anati, “Iye ndi Eliya.” Enanso anati, “Ndi mneneri, ofanana ndi mmodzi wa aneneri akale.” Koma Herode atamva zimenezi anati, “Yohane, munthu amene ndinamudula mutu, waukitsidwa kuchokera kwa akufa.” Pakuti Herode iye mwini analamula kuti amumange Yohane ndi kumuyika mʼndende. Anachita izi chifukwa cha Herodia, mkazi wa mʼbale wake Filipo, amene iye anamukwatira. Pakuti Yohane ankanena kwa Herode kuti, “Sikololedwa kwa inu kuti mukwatire mkazi wa mʼbale wanu.” Ndipo Herodia anamusungira Yohane chidani ndipo anafuna kumupha, koma sanathe kutero, chifukwa Herode anaopa Yohane ndipo anamuteteza, podziwa kuti iye anali munthu wolungama ndi woyera mtima. Herode akamamva Yohane, ankathedwa nzeru; komabe amakonda kumumvetsera. Pomaliza mpata unapezeka. Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwake, Herode anakonzera phwando akuluakulu ake, akulu a ankhondo ndi anthu odziwika a mu Galileya. Mwana wamkazi wa Herodia atabwera ndi kudzavina, anakondweretsa Herode ndi alendo ake a pa mphwandopo. Mfumu inati kwa mtsikanayo, “Undipemphe chilichonse chimene ukuchifuna, ndipo ndidzakupatsa.” Ndipo analonjeza ndi lumbiriro kuti, “Chilichonse chimene upempha ndidzakupatsa, ngakhale theka la ufumu wanga.” Iye anatuluka nati kwa amayi ake, “Kodi ndikapemphe chiyani?” Iye anamuyankha kuti, “Mutu wa Yohane Mʼbatizi.” Nthawi yomweyo mtsikana uja anafulumira kupita komwe kunali mfumu ndi pempho lake: “Ndikufuna kuti mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.” Mfumu inamva chisoni chachikulu, koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo ake a pa mphwandolo, sanafune kumukaniza. Nthawi yomweyo iye anatumiza yemwe anali ndi ulamuliro wonyonga anthu kuti abweretse mutu wa Yohane. Munthuyo anapita, nakadula mutu wa Yohane mʼndende, nabweretsa mutuwo mʼmbale. Anawupereka kwa mtsikanayo, ndipo iye anakapereka kwa amayi ake. Atamva izi, ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo ndi kukawuyika mʼmanda.

Iye anayamba kuwaphunzitsa kuti, “Mwana wa Munthu ayenera kumva zowawa zambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe, ndi aphunzitsi a malamulo, ndi kuti ayenera kuphedwa ndipo patatha masiku atatu adzaukanso.”

Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata. Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa.

chifukwa amaphunzitsa ophunzira ake. Anati kwa iwo, “Mwana wa Munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu. Adzamupha, ndipo patatha masiku atatu adzauka.”

Iye anati, “Ife tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Adzamuweruza kuti aphedwe ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina, amene adzamuchita chipongwe ndi kumuthira malovu, kumukwapula ndi kumupha. Patatha masiku atatu adzauka.”

Kenaka Iye anayamba kuyankhula nawo mʼmafanizo: “Munthu wina analima munda wamphesa. Anamanga mpanda mozungulira, nakumba dzenje lofinyiramo mphesa ndipo anamanga nsanja. Anawubwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita ku dziko lina. Pa nthawi yokolola anatumiza wantchito kwa alimiwo kuti akatenge kuchokera kwa iwo zina mwa zipatso za munda wamphesa. Koma iwo anamugwira, namumenya ndi kumupirikitsa wopanda kanthu. Kenaka anatumizanso wantchito wina kwa iwo. Iwo anamumenya munthuyo pamutu ndipo anamuzunza mochititsa manyazi. Anatumizanso wina, ndipo iwo anamupha. Anatumizanso ena ambiri; ena a iwo anawamenya, ena anawapha. “Munthu uja anatsala ndi mwana mmodzi, wamwamuna amene amamukonda. Pomaliza anamutumiza mwanayo nati, ‘Adzamuchitira ulemu mwana wanga.’ “Koma alimi aja anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndi mlowamʼmalo. Tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’ Ndipo anamutenga ndi kumupha, ndipo anamuponya kunja kwa munda wamphesa.

“Muyenera kukhala tcheru. Mudzaperekedwa ku mabwalo oweruza ndi kukwapulidwa mwankhanza mʼmasunagoge. Mudzayima pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu monga mboni kwa iwo chifukwa cha Ine. Ndipo Uthenga Wabwino uyenera kuyamba walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. Nthawi iliyonse pamene mwamangidwa ndi kuyimbidwa mlandu, musadandaule za zimene mudzanena. Zimene mudzapatsidwe pa nthawiyo yankhulani; pakuti sindinu amene mudzayankhula, koma Mzimu Woyera. “Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe, ndipo abambo adzapereka mwana wawo. Ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine, koma amene adzalimbika mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.

Tsopano panali patatsala masiku awiri okha kuti tsiku la Paska ndi Phwando la Buledi wopanda yisiti lifike, ndipo akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ankafunafuna mpata woti amugwire Yesu ndi kumupha.

Koma Petro ananenetsa kuti, “Ngakhale kutakhala kufa nanu, ine sindidzakukanani.” Ndipo ena onse ananena chimodzimodzi.

Akulu a ansembe ndi onse olamulira a Ayuda ankafunafuna umboni womutsutsa Yesu kuti amuphe, koma sanapeze wina uliwonse.

Mwamva mwanowo. Muganiza chiyani?” Onse anavomereza kuti ndi woyenera imfa. Kenaka ena anayamba kumulavulira malovu; anamumanga mʼmaso, namumenya ndi zibakera ndipo anati, “Nenera!” Ndipo asilikali anamutenga namumenya.

Anafuwula kuti, “Mpachikeni!” Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wapalamula mlandu wotani?” Koma anafuwula kwambiri, “Mpachikeni!” Pilato pofuna kuwakondweretsa anthuwo, anawamasulira Baraba. Analamula kuti Yesu akwapulidwe mwankhanza, ndipo anamupereka kuti akapachikidwe.

Ndipo anamuchita chipongwe, anamuvula mwinjiro wofiira uja ndi kumuveka zovala zake. Kenaka anamutenga kuti akamupachike.

Ndipo anamupachika Iye. Anachita maere ogawana zovala zake kuti aone chimene aliyense angatenge. Linali ora lachitatu mmawa pamene anamupachika Yesu.

Ndi mawu ofuwula, Yesu anapuma komaliza.

Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,

Ndinu odala, anthu akamakudani, kukusalani ndi kukunyozani ndi kumayipitsa dzina lanu chifukwa cha Mwana wa Munthu. “Nthawi imeneyo sangalalani ndipo lumphani ndi chimwemwe chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba. Pakuti ndi zomwezonso zimene makolo awo anachitira aneneri.

“Koma Ine ndikuwuza inu amene mukundimva: Kondani adani anu, chitirani zabwino amene amakudani. Dalitsani amene amakutembererani, apempherereni amene amakusautsani.

Koma kondani adani anu, achitireni zabwino, akongozeni koma osayembekezera kulandira kanthu. Pamenepo mphotho yanu idzakhala yayikulu ndipo inu mudzakhala ana a Wammwambamwamba, chifukwa ndi wokoma mtima kwa anthu osayamika ndi oyipa.

Tsopano Herode olamulirayo anamva zonse zimachitikazi. Ndipo iye anavutika kwambiri chifukwa ena amati Yohane waukitsidwa kwa akufa, ena amati Eliya waonekera, ndipo ena anatinso mmodzi wa aneneri akalekale waukanso. Koma Herode anati, “Ine ndinamudula mutu Yohane. Nanga uyu ndani amene ndikumva zinthu zotere za Iye?” Ndipo iye anayesetsa kuti amuone Iye.

Ndipo Iye anati, “Mwana wa Munthu ayenera kuzunzika kwambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo, Iye ayenera kuphedwa ndipo tsiku lachitatu adzauka kwa akufa.”

Ndipo Iye anawuza onse kuti, “Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku nʼkumanditsata Ine. Popeza aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupulumutsa.

“Tsoka kwa inu, chifukwa mumawaka manda a aneneri, komatu ndi makolo anu amene anawapha. Tsono potero mumachitira umboni za zimene makolo anu anachita. Anapha aneneri, ndipo inu mumawaka manda awo. Chifukwa cha ichi, Mulungu mu nzeru zake anati, ‘Ine ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, ena mwa iwo adzawapha ndipo ena adzawazunza.’ Choncho mʼbado uwu udzasenza magazi a aneneri onse amene anakhetsedwa kuyambira pachiyambi cha dziko, kuyambira magazi a Abele kufikira magazi a Zakariya amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi malo opatulika. Inde, Ine ndikuwuzani inu, mʼbado uno udzasenza zonsezi.

“Ine ndikuwuzani, abwenzi anga, musachite mantha ndi amene amapha thupi chifukwa akatero sangachitenso kanthu. Koma Ine ndidzakuonetsani amene muyenera kumuopa: Wopani Iye, amene pambuyo pakupha thupi, ali ndi mphamvu yakukuponyani ku gehena. Inde, Ine ndikuwuzani, muopeni Iye.

“Musachite mantha, inu kagulu kankhosa, pakuti zinakondweretsa Atate anu kuti akupatseni ufumu. Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupereke kwa osauka. Dzipezereni zikwama zandalama zimene sizidzatha, ndi kudzikundikira chuma chomwe sichidzatha kumwamba, kumene mbala sizingafikeko, ndipo dzimbiri silingawononge.

“Ngati wina aliyense abwera kwa Ine ndipo sadana ndi abambo ndi amayi ake, mkazi wake ndi ana, abale ake ndi alongo ake, inde ngakhale moyo wake omwe, iye sangakhale ophunzira wanga. Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sangakhale ophunzira wanga.

Mʼnjira yomweyo, wina aliyense wa inu amene sasiya zonse ali nazo sangakhale ophunzira wanga.

Aliyense amene ayesetsa kusunga moyo wake adzawutaya, ndipo aliyense amene ataya moyo wake adzawusunga.

Iye adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina. Ndipo adzamuchita chipongwe, adzamunyoza, adzamulavulira, adzamukwapula ndi kumupha. Tsiku lachitatu Iye adzaukanso.”

Iye anapitirira kuwawuza anthu fanizo ili: “Munthu wina analima munda wamphesa, nabwereketsa kwa alimi ena ndipo anachoka kwa nthawi yayitali. Pa nthawi yokolola, iye anatumiza wantchito wake kwa alimi aja kuti amupatseko zina mwa zipatso za munda wamphesawo. Koma alimi aja anamumenya namubweza wopanda kanthu. Iye anatumiza wantchito wina, koma uyunso anamumenya namuchita zachipongwe ndi kumubweza wopanda kanthu. Iye anatumizanso wina wachitatu ndipo iwo anamuvulaza namuponya kunja. “Kenaka mwini mundawo anati, ‘Kodi ndichite chiyani? Ndidzatumiza mwana wanga wamwamuna, amene ndimukonda; mwina iwo adzamuchitira ulemu.’ “Koma alimiwo ataona mwanayo, anakambirananso. Iwo anati, ‘Uyu ndiye wodzamusiyira chumachi. Tiyeni timuphe ndipo chumachi chikhala chathu.’ Ndipo anamuponya kunja kwa mundawo ndi kumupha. “Nanga tsono mwini munda wamphesayo adzawatani anthuwa?

Koma mʼmoyo umene ukubwerawo, anthu amene adzaukitsidwe kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa. Ndipo sadzafanso, pakuti adzakhala ngati angelo. Iwo ndi ana a Mulungu, chifukwa adzakhala ataukitsidwa kwa akufa.

“Koma zonsezi zisanachitike, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzakuperekani ku masunagoge ndi ku ndende, ndipo adzakutengerani pamaso pa mafumu ndi olamulira, ndipo zonsezi zidzachitika chifukwa cha dzina langa. Umenewu udzakhala mwayi wanu ochitira umboni. Koma tsimikizani mtima kuti musadzade nkhawa za momwe mudzadzitchinjirizire. Pakuti Ine ndidzakupatsani mawu ndi nzeru kotero kuti palibe mmodzi wa adani anu adzathe kuwakana kapena kuwatsutsa. Inu mudzaperekedwa ndi makolo anu, abale, anansi ndi abwenzi anu ndipo ena mwa inu adzakuphani. Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine.

Mukadzalimbikira ndiye mudzapeze moyo.

akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo amafunafuna mpata woti amuphere Yesu, pakuti ankachita mantha ndi anthu.

Inu ndinu amene mwayima nane mʼmayesero.

Koma iye anayankha kuti, “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu ku ndende ndi kufa komwe.”

Anthu amene ankalonda Yesu anayamba kumuchita chipongwe ndi kumumenya. Anamumanga mʼmaso ndi kumufunsa kuti, “Tanenera! Wakumenya iwe ndi ndani?”

Koma iwo anapitirirabe kufuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!” Kachitatu anawafunsanso iwo kuti, “Chifukwa chiyani? Kodi munthu uyu wachita choyipa chanji? Ine sindinapeze cholakwa mwa Iye chakuti aphedwe choncho ndingomukwapula ndi kumumasula.” Koma ndi mawu ofuwulitsa, analimbikirabe kuti Iye apachikidwe, ndipo kufuwulako kunapitirira.

Pamene anafika pamalo otchedwa Bade, anamupachika Iye pamodzi ndi achifwambawo, mmodzi kudzanja lake lamanja ndi winayo la ku lamazere. Yesu anati, “Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita.” Ndipo anagawana malaya ake mochita maere.

Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti lero lino udzakhala ndi Ine mʼparadaiso.”

Yesu anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Atate, ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu.” Atanena zimenezi, anamwalira.

Akulu a ansembe ndi oweruza anamupereka Iye kuti aphedwe, ndipo anamupachika Iye;

“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo.

“Musadabwe ndi zimenezi. Pakuti nthawi ikubwera pamene onse amene ali mʼmanda adzamva mawu ake ndi kutuluka. Iwo amene anachita zabwino adzauka ndi kupita ku moyo wosatha ndipo amene anachita zoyipa adzauka ndi kupita ku chilango chamuyaya.

Koma pano pali chakudya chochokera kumwamba, chimene munthu akadya sangafe. Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo.”

Kodi Mose sanakupatseni lamulo? Komatu palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene akusunga lamulo. Nʼchifukwa chiyani mukufuna kundipha Ine?”

Ine ndikukuwuzani choonadi, munthu akasunga mawu anga, sadzafa konse.”

“Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.

monga momwe Atate amandidziwa Ine, ndiponso Ine kudziwira Atatewo. Ndimapereka moyo wanga chifukwa cha nkhosa. Ine ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za gulu ili. Ine ndiyenera kuzibweretsanso. Izonso zidzamvera mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi mʼbusa mmodzi. Nʼchifukwa chake Atate anga amandikonda, popeza Ine ndikupereka moyo wanga kuti ndiwutengenso. Palibe amene angawuchotse mwa Ine, koma ndikuwupereka mwakufuna kwanga. Ine ndili ndi ulamuliro wa kuwupereka ndi ulamuliro wakuwutenganso. Lamulo ili ndinalandira kwa Atate anga.”

Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo. Aliyense amene ali ndi moyo ndi kukhulupirira Ine sadzamwalira. Kodi iwe ukukhulupirira izi?”

Choncho kuyambira tsiku limeneli iwo anakonzekera za kuti amuphe.

Choncho akulu a ansembe anakonza njira yoti aphenso Lazaro,

Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti, ‘Mbewu ya tirigu imakhala imodzi yokha ngati sikugwa mʼnthaka ndi kufa. Koma ngati imfa, imabereka mbewu zambiri.’ Munthu amene amakonda moyo wake adzawutaya, pamene munthu amene amadana ndi moyo wake mʼdziko lino lapansi adzawusungira ku moyo wosatha. Aliyense amene atumikira Ine ayenera kunditsata; ndipo kumene Ine ndili, wotumikira wanga adzakhalanso komweko. Atate anga adzalemekeza amene atumikira Ine.

Petro anafunsa kuti, “Ambuye, nʼchifukwa chiyani ine sindingakutsatireni tsopano? Ine ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha Inu.”

Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.

“Ngati dziko lapansi lidana nanu, dziwani kuti linayamba kudana ndi Ine. Inu mukanakhala anthu a dziko lapansi, dziko lapansi likanakukondani ngati anthu ake omwe. Koma mmene zilili, inu si anthu a dziko lapansi. Ine ndakusankhani kuchokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake dziko lapansi limakudani. Kumbukirani mawu amene ndinayankhula nanu akuti, ‘Palibe wantchito amene amaposa bwana wake.’ Ngati anandizunza Ine, iwo adzakuzunzaninso inu. Ngati anamvera chiphunzitso changa, iwo adzamvera chanunso. Iwo adzakuchitani zimenezi chifukwa cha dzina langa, popeza sakudziwa amene anandituma Ine.

Iwo adzakuchotsani mʼsunagoge mwawo. Kunena zoona, nthawi ikubwera imene aliyense amene adzakuphani adzaganiza kuti akutumikira Mulungu. Iwo adzachita zoterozo chifukwa sanadziwe Atate kapena Inenso. Ine ndakuwuzani izi kuti nthawi ikadzafika mudzakumbukire kuti Ine ndinakuchenjezani kale. Ine sindinakuwuzeni izi poyamba paja chifukwa ndinali nanu.”

Chimodzimodzinso ndi inu. Tsopano ino ndi nthawi yanu yomva chisoni, koma Ine ndidzakuonaninso ndipo inu mudzasangalala, ndipo palibe amene adzachotsa chimwemwe chanu.

“Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”

Ine ndawapatsa mawu anu ndipo dziko lapansi likudana nawo, pakuti sali a dziko lapansi monga Ine sindilinso wa dziko lapansi.

Kenaka Pilato anatenga Yesu namukwapula mwankhanza. Asilikali analuka nkhata yaminga ndi kumuveka pamutu pake. Kenaka anamuveka mkanjo wapepo ndipo ankapita kwa Iye mobwerezabwereza ndi kumanena kuti, “Moni mfumu ya Ayuda?” Ndipo amamumenya makofi.

Atangomuona Iye akulu a ansembe ndi akuluakulu ena anafuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!” Koma Pilato anayankha kuti, “Inu mutengeni ndi kumupachika. Koma ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu.”

Yesu anayankha kuti, “Inu simukanakhala ndi mphamvu pa Ine akanapanda kukupatsani kumwamba. Nʼchifukwa chake amene wandipereka Ine kwa inu ndiye wochimwa kwambiri.”

Koma iwo anafuwula kuti, “Choka nayeni! Choka nayeni! Mpachikeni!” Pilato anafunsa kuti, “Kodi ine ndipachike mfumu yanuyi?” Akulu a ansembe anayankha kuti, “Ife tilibe mfumu ina koma Kaisara.” Pomaliza Pilato anamupereka kwa iwo kuti akapachikidwe. Choncho asilikali anamutenga Yesu. Atanyamula mtanda wake, anapita kumalo otchedwa “Malo a Bade” (mʼChiaramaiki amatchedwa Gologota). Pamenepo iwo anamupachika Iye pamodzi ndi anthu ena awiri, mmodzi mbali ina ndi wina mbali inanso ndipo Yesu pakati.

Yesu atalandira chakumwachi anati, “Kwatha.” Ndipo Iye anaweramitsa mutu wake napereka mzimu wake.

Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti uli wamngʼono unkadziveka wekha lamba ndi kupita kumene unkafuna; koma ukadzakalamba udzatambasula manja ako ndipo wina wake adzakuveka ndikukutsogolera kupita kumene sukufuna kupita.” Yesu ananena izi kumuzindikiritsa mtundu wa imfa imene Petro adzalemekezera nayo Mulungu. Kenaka Iye anati kwa Petro, “Nditsate Ine!”

Yesu anayankha kuti, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo? Iwe uyenera kunditsata Ine.” Chifukwa cha ichi mbiri inafala pakati pa abale kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananene kuti iye sadzafa. Iye anati, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo?”

Yesu ameneyu anaperekedwa kwa inu mwa kufuna ndi kudziwiratu kwa Mulungu; ndipo inu mothandizidwa ndi anthu oyipa, munamupha Iye pomupachika pa mtanda. Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kumumasula Iye ku zowawa za imfa, chifukwa kunali kosatheka kuti agwiridwe ndi imfa.

Iwo anagwira atumwi ndi kuwatsekera mʼndende ya anthu wamba.

Akuluakuluwo atamva zimenezi anakwiya kwambiri nafuna kuwapha.

Akuluakulu enawo anavomerezana naye. Iwo anayitana atumwi aja ndipo anawakwapula kwambiri. Ndipo anawalamula kuti asayankhulenso mʼdzina la Yesu ndipo anawamasula. Iwo anachoka ku Bwalo Lalikulu akukondwa chifukwa anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzina la Yesu.

“Anthu wokanika inu, osachita mdulidwe wa mu mtima ndi a makutu ogontha! Inu ofanana ndi makolo anu. Nthawi zonse mumakana kumvera Mzimu Woyera: Kodi analipo mneneri amene makolo anu sanamuzunze? Iwo anapha ngakhale amene ananeneratu za kubwera kwa Wolungamayo. Ndipo tsopano inu munamupereka ndi kumupha Iye. Inu amene munalandira Malamulo amene anaperekedwa ndi angelo ndipo simunawamvere.” Atamva zimenezi, iwo anakwiya kwambiri ndipo anamukukutira mano. Koma Stefano, wodzaza ndi Mzimu Woyera, anayangʼana kumwamba ndipo anaona ulemerero wa Mulungu ndiponso Yesu atayimirira ku dzanja lamanja la Mulungu. Stefano anati, “Taonani, ndikuona kumwamba kotsekuka ndiponso Mwana wa Munthu atayimirira ku dzanja la manja la Mulungu.”

Koma iwo anatseka mʼmakutu mwawo, ndipo anafuwula kolimba, onse anathamangira kwa iye, anamukokera kunja kwa mzinda ndipo anayamba kumugenda miyala. Mboni zinasungitsa zovala zawo kwa mnyamata otchedwa Saulo. Akumugenda miyala, Stefano anapemphera kuti, “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” Ndipo anagwada pansi nafuwula mwamphamvu kuti, “Ambuye musawawerengere tchimoli.” Atanena mawu amenewa anamwalira.

Ndipo Saulo anavomerezana nawo pa imfa ya Stefano. Tsiku lomwelo, mpingo wa mu Yerusalemu unayamba kuzunzidwa, ndipo onse, kupatulapo atumwi, anabalalikira ku madera onse a Yudeya ndi Samariya. Anthu okonda Mulungu anayika maliro a Stefano ndipo anamulira kwambiri. Koma Saulo anayamba kuwononga mpingo. Amapita nyumba ndi nyumba, ndipo amagwira amuna ndi amayi ndi kukawatsekera ku ndende.

Mawu amene ndunayo imawerenga anali awa: “Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira, kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta, momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake. Iye ananyozedwa ndipo panalibe chilungamo pa mlandu wake. Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo?”

Pa nthawi imeneyi, Saulo ankaopsezabe okhulupirira Ambuye nafuna kuwapha. Iye anapita kwa mkulu wa ansembe, ndi kukapempha makalata a chilolezo kuti apite nawo ku masunagoge a ku Damasiko, kuti ngati atakapezeka ena kumeneko otsata Njirayo, kaya ndi amuna kapena amayi, akawamange ndi kuwatenga kubwera nawo ku Yerusalemu. Akuyandikira ku Damasikoku paulendo wake, mwadzidzidzi kuwala kochokera kumwamba kunamuzungulira iye. Iye anagwa pansi ndipo anamva mawu akuti, “Saulo, Saulo ukundizunziranji Ine?” Saulo anafunsa kuti, “Ndinu yani Ambuye?” Ambuye anayankha kuti, “Ndine Yesu amene iwe ukumuzunza.”

Patapita masiku ambiri, Ayuda anapangana zoti aphe Saulo, koma iye anadziwa za chiwembucho. Anthu ankadikirira usana ndi usiku pa zipata za mzindawo kuti amuphe.

Anayankhula ndi kutsutsana ndi Ayuda a Chihelene, koma iwo ankafuna kumupha.

Inali nthawi yomweyi imene mfumu Herode anamanga ena a mu mpingo ndi cholinga chakuti awazunze. Iye analamula kuti Yakobo mʼbale wa Yohane, aphedwe ndi lupanga. Ataona kuti zimenezi zinakondweretsa Ayuda, anawonjeza ndi kugwiranso Petro. Izi zinachitika pa nthawi ya Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. Atamugwira Petro, namutsekera mʼndende, anamupereka kwa magulu anayi a asilikali kuti amuyangʼanire, gulu lililonse linali ndi asilikali anayi. Herode anafuna kumuzenga mlandu pamaso pa anthu onse chikondwerero cha Paska chitapita.

Pamenepo anthu a mitundu ina ndi Ayuda, pamodzi ndi atsogoleri awo anakonza chiwembu choti azunze atumwiwo ndi kuwagenda ndi miyala. Koma atazindikira zimenezi, anathawira ku Lusitra ndi Derbe, mizinda ya ku Lukaoniya, ndiponso ku dziko lozungulira mizindayo,

Kumeneko analimbikitsa mitima ya ophunzira ndi kuwapatsa mphamvu kuti akhalebe woona mʼchikhulupiriro. Iwo anati, “Ife tiyenera kudutsa mʼmasautso ambiri kuti tikalowe mu ufumu wa Mulungu.”

anthu amene anapereka moyo wawo chifukwa cha dzina la Ambuye athu Yesu Khristu.

Gulu la anthu linatsutsana ndi Paulo ndi Sila, ndipo woweruza milandu analamula kuti avulidwe ndi kumenyedwa. Atawakwapula kwambiri anawaponya mʼndende, nalamula woyangʼanira kuti awasunge mosamalitsa. Chifukwa cha mawu amenewa woyangʼanira ndende anakawayika mʼchipinda chamʼkati mwa ndende, nawamangirira miyendo yawo mʼzigologolo.

Kuchoka kwa munthu mmodzi Iye analenga mtundu uliwonse wa anthu, kuti akakhale pa dziko lonse lapansi; ndipo Iye anakonzeratu nthawi yawo ndiponso malo enieni kumene adzakhale. Mulungu anachita izi kuti anthu amufunefune, ndikuti pomufunafunapo amupeze ngakhale kuti Iye sali kutali ndi aliyense wa ife. ‘Pakuti timakhala mwa Iye, kuyenda mwa Iye ndi kukhala moyo mwa Iye.’ Monga olemba ndakatulo anu ena akuti, ‘Ife ndi zidzukulu zake.’

“Ndipo tsopano, mokakamizidwa ndi Mzimu, ndikupita ku Yerusalemu, sindikudziwa zimene zikandichitikire kumeneko.” Chimene ndikudziwa ndi chakuti Mzimu Woyera wandichenjeza mu mzinda uliwonse kuti ndende ndi mavuto zikundidikira. Koma sindilabadira konse za moyo wanga ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malingana ndikatsirize ntchito yanga ndi utumiki umene Ambuye Yesu anandipatsa, ntchito yochitira umboni Uthenga Wabwino wachisomo cha Mulungu.

Koma Paulo anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukulira ndi kunditayitsa mtima? Ndine wokonzeka osati kumangidwa kokha ayi, komanso kufa ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.” Titalephera kumuletsa tinamuleka ndipo tinati, “Chifuniro cha Ambuye chichitike.”

Pamene anthuwo ankafuna kupha Paulo, nkhaniyi inamveka kwa mkulu wa magulu a asilikali a Aroma kuti mzinda wonse wa Yerusalemu wasokonezeka.

Ine ndinkazunza anthu otsatira Njirayi mpaka kuwapha. Ndinkagwira amuna ndi amayi ndi kuwayika mʼndende. Mkulu wa ansembe ndiponso akuluakulu a Ayuda angathe kundichitira umboni. Iwowa anandipatsa makalata opita nawo kwa abale awo ku Damasiko. Ndipo ndinapita kumeneko kuti ndikawagwire anthu amenewa ndi kubwera nawo ku Yerusalemu kuti adzalangidwe.

Ine ndinayankha Ambuye kuti, “Anthu awa akudziwa kuti ine ndinkapita ku sunagoge iliyonse ndipo ndinkawaponya mʼndende ndi kuwakwapula amene ankakhulupirira inu. Ndipo pamene ankapha Stefano, ine ndinali pomwepo kuvomereza ndi kusunga zovala za amene amamupha.”

Kutacha Ayuda ena anakonza chiwembu ndipo analumbira kuti sadya kapena kumwa mpaka atapha Paulo. Anthu amene anakonza chiwembuchi analipo makumi anayi. Iwo anapita kwa akulu a ansembe ndi akuluakulu a Ayuda nakawawuza kuti, “Ife talumbira kolimba kuti sitidya kalikonse mpaka titapha Paulo. Tsopano inu pamodzi ndi akuluakulu a Bwalo Lalikulu mupemphe mkulu wa asilikali kuti akubweretsereni Paulo ngati kuti mukufuna kudziwa bwino za mlandu wake. Ife takonzeka kudzamupha asanafike kumeneko.”

“Inenso ndimaganiza kuti ndimayenera kuchita zinthu zambiri pofuna kuthana ndi dzina la Yesu wa ku Nazareti. Ndipo izi ndi zimene ndinazichita ku Yerusalemu. Ndi ulamuliro wa akulu a ansembe, ine ndinayika mʼndende oyera mtima ambiri, ndipo pamene amaphedwa, ine ndimavomereza. Nthawi zambiri ndinkapita mʼsunagoge iliyonse kuti alangidwe, ndipo ndinayesera kuwakakamiza kuti achitire chipongwe Mulungu. Mu mkwiyo wangawo, ndimapita ngakhale ku mizinda yachilendo kuti ndikawazunze.

Ichi nʼchifukwa chake Ayuda anandigwira mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu nafuna kundipha.

Iye adzapereka moyo wosatha kwa amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pochita ntchito zabwino mopirira.

Koma si pokhapo ayi, koma ife tikukondweranso mʼmasautso athu chifukwa tikudziwa kuti masautso amatiphunzitsa kupirira.

Pakuti pa nthawi yake, tikanali ochimwa, Khristu anatifera anthu osapembedzafe. Sizichitika kawirikawiri kuti munthu wina afere munthu wolungama, ngakhale kuti chifukwa cha munthu wabwino wina atha kulimba mtima kumufera. Koma Mulungu anaonetsa chikondi chake kwa ife chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera. Popeza chifukwa cha magazi ake ife tapezeka olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa kotani ku mkwiyo wa Mulungu. Pakuti pamene tinali adani a Mulungu, tinayanjanitsidwa ndi Iye kudzera mu imfa ya Mwana wake. Nanga tidzapulumutsidwa bwanji kudzera mʼmoyo wake, titayanjanitsidwa naye?

Kodi simukudziwa kuti tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu tinabatizidwa mu imfa yake? Chifukwa chake ife tinayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo. Tinalowa mu imfa ndi cholinga choti monga momwe Khristu anaukitsidwa kwa akufa ndi ulemerero wa Atate, ifenso tikakhale mʼmoyo watsopano. Pakuti ngati ife tinakhala amodzi ndi Iye mu imfa yake, tidzakhalanso ndithu amodzi ndi Iye mu kuuka kwake. Ife tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye kuti thupi la uchimo likhale lopanda mphamvu ndi kuti tisakakhalenso akapolo a tchimo chifukwa aliyense amene anafa anamasuka ku tchimo.

Koma ngati tinafa pamodzi ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo pamodzi ndi Iye. Pakuti tikudziwa kuti popeza Khristu anaukitsidwa kwa akufa, Iye sangafenso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye. Imfa imene Iye anafa, anafa ku tchimo kamodzi kokha, koma moyo umene akhala ndi wa kwa Mulungu. Kotero inunso, mudzione nokha ngati akufa ku tchimo koma a moyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.

Pakuti ngati inu mukhala monga mwa khalidwe lauchimo, mudzafa. Koma ngati mwa Mzimu mupha ntchito zoyipa zathupi, mudzakhala ndi moyo. Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu.

Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa mʼmalo a Mulungu ndi olowa mʼmalo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye. Ine ndiganiza kuti masautso amene tikuwamva nthawi ino, sakufanana ndi ulemerero umene udzaonetsedwa mwa ife.

Ife tikudziwa kuti chilengedwe chonse chakhala chikubuwula ndi ululu ngati ululu wa nthawi yobereka mwana mpaka tsopano lino. Si zokhazo ayi, ngakhale ife tomwe, amene tili ndi zipatso zoyamba za Mzimu, tikubuwulira mʼkati mwathu pomwe tikudikira mwachidwi kusankhidwa kwathu ngati ana, kuwomboledwa kwa matupi athu.

Ndipo ife tikudziwa kuti zinthu zonse zimathandizana kuwachitira ubwino amene amakonda Mulungu, amene anayitanidwa monga mwa cholinga chake. Pakuti amene Mulungu anawadziwiratu, anawasankhiratunso kuti akonzedwe mʼchifanizo cha Mwana wake, kuti Iye akhale Mwana woyamba kubadwa mwa abale ambiri. Iwo amene anawasankhiratu, anawayitananso. Amene Iye anawayitana anawalungamitsanso ndipo amene anawalungamitsa anawapatsanso ulemerero.

Nanga tsono tidzanena chiyani pa izi? Ngati Mulungu ali mbali yathu, adzatitsutsa ife ndani? Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anamupereka chifukwa cha ife tonse. Iye adzalekeranjinso pamodzi naye kutipatsa ife zinthu zonse mwaulere?

Ndani amene adzatilekanitsa ife ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zowawa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena umaliseche, kapena choopsa, kapena lupanga? Monga kwalembedwa: “Chifukwa cha inu, ife tikuphedwa tsiku lonse: ife tikutengedwa ngati nkhosa zoti zikaphedwe.” Ayi, mu zonsezi ife ndife oposa agonjetsi mwa Iye amene anatikonda. Pakuti ine ndatsimikiza ndi mtima wonse kuti ngakhale imfa, kapena moyo, ngakhale angelo, kapena ziwanda, ngakhale zinthu zilipo, kapena zili mʼtsogolo, kapena mphamvu zina, ngakhale kutalika, kapena kuya, kapena chilichonse mʼchilengedwe chonse, sizingathe kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

“Ambuye, anthuwa apha aneneri anu ndi kugwetsa maguwa anu ansembe. Ndatsala ine ndekha wamoyo ndipo akufuna kundipha?” Ndipo yankho la Mulungu linali lotani? “Ine ndadzisungira ndekha anthu 7,000 amene sanapembedzepo Baala.” Chimodzimodzinso lero lino, alipo Aisraeli pangʼono osankhidwa mwachisomo.

Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu. Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.

Kondwerani mʼchiyembekezo, pirirani mʼmasautso ndiponso khulupirikani mʼpemphero. Gawanani ndi anthu a Mulungu amene ali ndi chosowa. Cherezani alendo. Adalitseni amene akuzunzani. Adalitseni ndipo musawatemberere.

Ngati nʼkotheka, khalani mwamtendere ndi aliyense monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choyipa, koma lekerani Mulungu. Pakuti kwalembedwa, “Kubwezera chilango nʼkwanga. Ndidzawalanga ndine,” akutero Ambuye. Koma, “Ngati mdani wako ali ndi njala, mupatse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, mupatse kanthu kakumwa. Pochita ichi, udzamuwunjikira makala amoto pamutu pake.”

Aliyense ayenera kumvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sunachokere kwa Mulungu. Olamulira amene alipo anayikidwa ndi Mulungu. Kotero kuti, iwo amene awukira ulamuliro atsutsana ndi chimene Mulungu anakhazikitsa. Ndipo amene atero adzibweretsera okha chilango. Pakuti olamulira saopseza amene amachita zabwino koma amene amachita zoyipa. Kodi mukufuna kukhala osaopa olamulira? Tsono chitani zoyenera ndipo adzakuyamikirani. Pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokuchitirani zabwino. Koma ngati muchita zoyipa muchite mantha, pakuti iye ali ndi mphamvu zolangira. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wobweretsa mkwiyo ndi kulanga onse ochita zoyipa.

Ngati ife tikhala ndi moyo, ife tikhala ndi moyo kwa Ambuye. Ndipo ngati ife tifa, tifa kwa Ambuye. Choncho, ngati tikhala ndi moyo kapena kufa, ndife ake a Ambuye. Pa chifukwa ichi, Khristu anafa ndi kuukanso kotero kuti Iye akhale ndi Ambuye wa akufa ndi amoyo.

Ayi, ife timayankhula za nzeru yobisika ya Mulungu, nzeru imene inabisidwa ndipo imene Mulungu anatikonzera mu ulemerero wathu isanayambe nthawi. Palibe olamulira aliyense wa mʼbado uno amene anamumvetsetsa popeza anakamumvetsetsa sakanamupachika Ambuye wa ulemerero. Komabe monga zalembedwa kuti, “Palibe diso linaona, palibe khutu linamva, palibe amene anaganizira, zimene Mulungu anakonzera amene amukonda”

Kodi inu simukudziwa kuti ndinu Nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?

Pakuti kwa ine zikuoneka ngati kuti Mulungu watiyika ife atumwi pachionetsero, kumapeto kwa mndandanda, monga anthu oweruzidwa kuti akaphedwe mʼmabwalo. Ife tayikidwa kuti tionekere ku dziko lonse, kwa angelo ndi anthu.

Mpaka pano tili ndi njala ndi ludzu, tili ndi sanza, tikuzunzidwa, tilibe nyumba. Timagwira ntchito molimbika ndi manja athu. Akamatitemberera, ife timadalitsa; tikasautsidwa, ife timapirira. Pamene atilalatira timayankha mwachifundo. Mpaka pano takhala ngati zinyalala za dziko, monga zakudzala za dziko lapansi.

Kodi simukudziwa kuti thupi lanu ndi Nyumba ya Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene mwalandira kuchokera kwa Mulungu? Inu simuli panokha ayi. Ndinu ochita kugulidwa. Nʼchifukwa chake lemekezani Mulungu mʼthupi lanu.

Pakuti nthawi zonse pamene mudya bulediyu ndikumwa chikhochi, mukulalikira imfa ya Ambuye mpaka Iye adzabweranso.

Ngati ndipereka zanga zonse kwa osauka ndi kupereka thupi langa kuti alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ine sindipindula kanthu. Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa. Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.

Koma nʼzoonadi kuti Khristu anaukitsidwa kwa kufa, chipatso choyamba cha onse ogona tulo.

Mdani wotsiriza kuwonongedwa ndi imfa.

Abale, ndimafa tsiku ndi tsiku, ndikunenetsa zimenezi, mongotsimikizira monga ndimakunyadirani mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Wopusa iwe! Chimene mudzala sichikhala ndi moyo pokhapokha chitayamba chafa.

Zidzaterenso pamene akufa adzauka. Thupi loyikidwa mʼnthaka ngati mbewu limavunda, koma likadzauka lidzakhala losavunda. Limayikidwa mʼmanda mopanda ulemu, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi ulemerero. Limayikidwa mʼmanda lili lofowoka, koma likadzaukitsidwa lidzakhala ndi mphamvu. Limayikidwa mʼmanda thupi la mnofu chabe, koma likadzaukitsidwa lidzakhala lauzimu. Ngati pali thupi la mnofu, palinso thupi lauzimu.

Pakuti chovunda chiyenera kuvala chosavunda, ndi thupi ili lakufa liyenera kuvala losafa. Pamene thupi lovundali likadzasanduka losavunda, ndipo thupi lotha kufali likadzasanduka losatha kufa, pamenepo zidzakwaniritsidwa zimene zinalembedwa zakuti, “Imfa yogonjetsedwa kwathunthu.” “Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?”

Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse. Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu. Pakuti monga momwe tili mʼmasautso pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatitonthoza kwambiri. Ngati ife tikusautsidwa, nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe ndi kupulumutsidwa. Ngati ife tikutonthozedwa nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe, ndi chitonthozo chimene chimabweretsa mwa inu kupirira kosawiringula pa zosautsa zomwe timasauka nazo ife. Ndipo chiyembekezo chathu pa inu nʼcholimba chifukwa tikudziwa kuti monga momwe mumamva zowawa pamodzi nafe, momwemonso mumatonthozedwa nafe pamodzi.

Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za masautso amene tinakumana nawo mʼchigawo cha Asiya. Tinapanikizidwa koopsa kuposa muyeso woti nʼkutha kupirira, mwakuti sitinkadziwa kuti nʼkukhalabe ndi moyo. Zoonadi, tinamva mʼmitima mwathu chilango cha imfa. Koma izi zimachitika kuti tisangodzidalira mwa ife tokha koma Mulungu yemwe amaukitsa akufa. Mulungu watilanditsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatilanditsanso. Ife tayika chiyembekezo chathu pa Iyeyo kuti adzapitiriza kutilanditsabe.

Koma tili ndi chuma ichi mʼmbiya zadothi, kusonyeza kuti mphamvu yoposayi, imachokera kwa Mulungu osati kwa ife. Tapanikizika kwambiri mbali zonse koma osaphwanyika; tathedwa nzeru koma osataya mtima; tazunzidwa, koma osasiyidwa; takanthidwa, koma osawonongeka. Nthawi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu mʼthupi mwathu, kuti moyo wake Yesu uwonekenso mʼthupi mwathu. Pakuti nthawi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake wa Yesu uwonekenso mʼmatupi mwathu amene amafa. Choncho imfa ikugwira ntchito mwa ife, koma moyo ukugwira ntchito mwa inu.

Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku. Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri. Motero sitiyangʼana zinthu zimene ndi zooneka ndi maso, koma zinthu zimene ndi zosaoneka. Pakuti zimene zimaoneka ndi zosakhalitsa, koma zimene sizioneka ndi zamuyaya.

Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu. Pakali pano tibuwula, ndi kulakalaka kuvala nyumba yathu ya kumwambayo, chifukwa tikavala, sitidzapezekanso amaliseche. Pamene tili mu msasa uno, timalemedwa ndipo timabuwula, chifukwa sitifuna kukhala amaliseche koma ovala nyumba yathu ya kumwamba, kuti chimene chili chakufa chimezedwe ndi moyo. Tsono ndi Mulungu amene anatikonzeratu ife kuti tilandire zimenezi. Iye anatipatsa Mzimu ngati chikole, kutsimikizira zimene zikubwera.

Nʼchifukwa chake nthawi zonse timalimba mtima, ndipo timadziwa kuti pamene tikukhala mʼthupi, ndiye kuti tili kutali ndi Ambuye. Ife timakhala mwachikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso. Inde, ife tikulimba mtima, ndipo tikanakonda kulekana nalo thupi lathu ndi kukhala ndi Ambuye. Choncho timayesetsa kukondweretsa Ambuye, ngakhale tikhale mʼthupi, kapena tichokemo.

Pakuti chikondi cha Khristu ndicho chimatikakamiza, chifukwa tikutsimikiza kuti mmodzi anafera anthu onse, kotero kuti anthu onse anafanso. Ndipo Iye anafera anthu onse kuti amene ali ndi moyo, asakhale ndi moyo wofuna kudzikondweretsa okha, koma azikondweretsa amene anawafera naukitsidwa chifukwa cha iwowo.

Choncho, kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ife sitiganizirapo za munthu aliyense monga mwanzeru za umunthu, ngakhale kuti poyamba tinkaganiza za Khristu mʼnjira imeneyi, koma tsopano sititeronso. Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano.

Ife sitikuyika chokhumudwitsa pa njira ya wina aliyense, kuti utumiki wathu usanyozeke. Mʼmalo mwake, mwanjira iliyonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu popirira kwambiri mʼmasautso, mʼzowawa ndi mʼzodetsa nkhawa. Pomenyedwa, kuponyedwa mʼndende ndi mʼzipolowe. Pogwira ntchito mwamphamvu, posagona usiku onse, posowa chakudya; pokhala moyo woyera mtima, pomvetsa zinthu, wokoma mtima ndi wachifundo mwa Mzimu Woyera ndi mwachikondi choonadi ndi poyankhula choonadi mwamphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili mʼdzanja lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo. Timatumikira Mulungu ngakhale ena amatinyoza ndi ena amatilemekeza, ena amatinenera chipongwe, enanso amatiyamikira. Ena amatitenga kukhala ngati onena zoona, ndipo enanso amatitenga kukhala ngati onena zabodza. Amatiyesa osadziwika komatu ndife odziwika kwambiri. Amatiyesa wooneka ngati tikufa, koma tikupitirirabe ndi moyo, okanthidwa, koma osaphedwa. Amatiyesa achisoni, koma ndife achimwemwe nthawi zonse, aumphawi, koma olemeretsa ambiri; wopanda kanthu, koma tili ndi zonse.

Sindikunena izi kuti mupezeke olakwa. Ndinanena kale kuti ife timakuganizirani kwambiri kotero kuti tili pamodzi, ngakhale tikhale moyo kapena timwalire. Ndimakukhulupirirani kwambiri ndipo ndimakunyadirani kwambiri. Ndikulimbikitsidwa kwambiri; mʼmasautso athu onse, chimwemwe changa chilibe malire.

Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri.

Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankhula ngati wamisala. Ine ndine woposa iwowo. Ndagwira ntchito kwambiri kupambana iwo, ndakhala ndikuyikidwa mʼndende kawirikawiri, ndakwapulidwapo kwambiri, kawirikawiri ndinali pafupi kufa. Andikwapulapo kasanu zikoti zija za Ayuda, makumi anayi kuchotsapo chimodzi. Katatu anandimenya ndi ndodo. Kamodzi anandigendapo miyala. Katatu sitima yathu ya panyanja inasweka, ndipo ndinakhala usiku ndi usana ndi kuyandama pa nyanja. Ndakhala ndikuyenda maulendo ataliatali. Moyo wanga wakhala ukukumana ndi zoopsa pa mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa abale anga Ayuda, zoopsa zochokera kwa anthu akunja. Ndinakumana ndi zoopsa mʼmizinda, mʼmidzi, pa nyanja, ndi pakati pa abale onyenga. Ndakhala ndikugwira ntchito molimbika ndipo kawirikawiri ndakhala ndikuchezera usiku wonse osagona. Ndakhala ndikumva njala ndi ludzu ndipo kawirikawiri ndakhala wopanda chakudya. Ndakhala ndi kuzizidwa ndi wosowa zovala. Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa chipsinjo cha nkhawa ya mipingo yonse.

kapena chifukwa cha mavumbulutso aakulu kuposa awa. Choncho, kuti ndisadzitukumule, ndinayikidwa minga mʼthupi langa, wamthenga wa Satana, kuti adzindizunza. Katatu konse ndinapempha Ambuye kuti andichotsere. Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine. Tsono, chifukwa cha Khristu, ndimakondwera pamene ndili wofowoka, pamene akundinyoza, pamene ndikumva zowawa, ndi pamene akundizunza ndi kundisautsa. Pakuti pamene ndili wofowoka ndiye kuti ndili wamphamvu.

Pakuti inu munamva za moyo wanga wakale mʼChiyuda, mmene ndinkazunzira mpingo wa Mulungu koopsa ndi kuyesetsa kuwuwononga.

Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Nthawi imeneyo mwana wobadwa mwathupi anazunza mwana wobadwa mwamphamvu za Mzimu. Zili chimodzimodzinso lero.

Amene ali ake a Khristu Yesu anapachika pa mtanda thupi lawo la uchimo pamodzi ndi zokhumba zawo ndi zolakalaka zawo.

Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha.

Ine sindingathe kunyadira kanthu kena koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu, kudzera mwa mtandawo dziko lapansi linapachikidwa kwa ine ndi ine ku dziko lapansi.

Nʼchifukwa chake ine Paulo, ndili wamʼndende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu anthu a mitundu ina.

Choncho, ine ndikukupemphani kuti musakhumudwe popeza ndikusautsidwa chifukwa cha inu pakuti masautso angawa ndi ulemerero wanu. Nʼchifukwa chake ine ndikugwada pamaso pa Atate,

Ine monga wamʼndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukulimbikitsani kuti mukhale moyo woyenera mayitanidwe amene munalandira. Mukhale odzichepetsa kwathunthu ndi ofatsa; mukhale oleza mtima, ololerana wina ndi mnzake mwachikondi.

Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu.

Tsopano abale, ndikufuna mudziwe kuti chimene chandichitikira ine chathandiza kwambiri kupititsa patsogolo Uthenga Wabwino. Chotsatira chake nʼchakuti zadziwika bwino lomwe kwa onse amene ali ku nyumba yaufumu kuti ine ndili mʼmaunyolo chifukwa cha Khristu. Moti chifukwa cha maunyolo angawa, abale ambiri alimbikitsidwa kuyankhula Mawu a Mulungu molimbika ndi mopanda mantha.

Ndili ndi chiyembekezo chonse kuti sindidzachita manyazi ndi pangʼono pomwe, koma ndidzakhala ndi chilimbikitso chokwanira kuti monga mwa nthawi zonse, tsopano Khristu adzakwezedwa mʼthupi langa kaya ndi mʼmoyo kapena mu imfa.

Pakuti kwa ine kukhala moyo ndi Khristu ndipo kufa ndi phindu. Ngati nditi ndipitirire kukhala ndi moyo mʼthupi ndiye kuti kwa ine ndi kugwira ntchito yopindulitsa. Kodi ndisankhe chiyani? Sindikudziwa. Ndathinidwa ndi zinthu ziwirizi: Ndikulakalaka kunyamuka kuti ndikakhale ndi Khristu, chimene ndi chinthu chabwino kwambiri.

osachita mantha ndi pangʼono pomwe ndi amene akutsutsana nanu. Ichi ndi chizindikiro kwa iwo kuti adzawonongedwa, koma inu mudzapulumutsidwa ndi Mulungu. Pakuti inu mwapatsidwa mwayi osati ongokhulupirira Khristu kokha, koma wakumva zowawa mʼmalo mwa Khristu.

Ndipo pokhala munthu choncho anadzichepetsa yekha ndipo anamvera mpaka imfa yake, imfa yake ya pamtanda!

Koma ngakhale ndikuthiridwa ngati nsembe ya chakumwa yoperekedwa pa nsembe ndi pa utumiki wochokera mʼchikhulupiriro chanu, ndine wokondwa ndi wosangalala pamodzi ndi inu nonse.

Iyeyu anatsala pangʼono kufa chifukwa cha ntchito ya Khristu, anayika moyo pa chiswe kuti akwaniritse thandizo limene inu simukanatha.

Pakuti ochita mdulidwe weniweni ndife. Ife amene timatumikira Mulungu motsogozedwa ndi Mzimu. Ife amene timanyadira Khristu, ndipo sitidalira zinthu za thupi

Koma zonse zimene ndinkaziyesa zaphindu, tsopano ndikuziona kuti nʼzosapindulitsa chifukwa cha Khristu. Kuwonjeza pamenepo, ndikuziona zonse kuti nʼzopanda phindu poyerekeza ndi phindu lopambana la kudziwa Khristu Yesu Ambuye anga. Nʼchifukwa cha Yesuyo ndataya zinthu zonse ndipo ndikuziyesa zinyalala kuti ndipindule Khristu ndi kuti ndipezeke mwa Iyeyo, osati ndi chilungamo changa chobwera chifukwa chotsata malamulo, koma chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Khristu. Chilungamochi nʼchochokera kwa Mulungu, timachilandira mwachikhulupiriro. Ine ndikufuna kudziwa Khristu, ndithu, kudziwa mphamvu zake za kuuka kwa akufa. Ndikufuna kuyanjana naye mʼmasautso ake, kufanana naye pa imfa yake kuti nanenso ndidzaukitsidwe kwa akufa.

Koma ife ndife nzika za kumwamba ndipo tikudikirira mwachidwi Mpulumutsi wochokera kumeneko, Ambuye Yesu Khristu. Iyeyo, ndi mphamvu imene imamuthandiza kukhazikitsa zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, adzasintha matupi athu achabewa kuti akhale ofanana ndi thupi lake la ulemerero.

Nthawi zonse muzikondwa mwa Ambuye. Ndikubwerezanso; muzikondwa!

Musade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa china chilichonse, mwa pemphero ndi chidandaulo pamodzi ndi chiyamiko, perekani zopempha zanu kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu, umene upambana nzeru zonse udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Tsopano ine ndikukondwa kuti ndinavutika chifukwa cha inu, ndipo ndikukwaniritsa mʼthupi langa zimene zikuperewera pa masautso a Khristu, chifukwa cha thupi lake, limene ndi Mpingo.

Tsono popeza munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mitima yanu pa zinthu za kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Muzifunafuna zinthu za kumwamba, osati zinthu za pa dziko lapansi. Pakuti munafa, ndipo moyo wanu tsopano wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. Khristu, amene ndiye moyo wanu, akadzaonekanso, pamenepo inunso mudzaoneka naye pamodzi mu ulemerero. Choncho, iphani zilakolako za dziko lapansi mwa inu, monga: dama, zodetsa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoyipa ndi umbombo, pakuti umbombo ndiko kupembedza mafano.

Inu mukudziwa kuti mudzalandira mphotho monga cholowa kuchokera kwa Ambuye. Ndi Ambuye Khristu amene mukumutumikira.

Inu mwakhala otitsatira athu ndi a Ambuye; ngakhale kuti panali masautso akulu, munalandira uthenga mwachimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera.

amene anapha Ambuye Yesu ndi aneneri ndipo anatithamangitsanso ife. Iwo sakondweretsa Mulungu ndipo amadana ndi anthu onse

ndi cholinga chakuti wina asasunthike ndi mavutowa. Inu mukudziwa bwino lomwe kuti ndife oyenera kukumana ndi zimenezi. Kunena zoona, pamene tinali nanu, tinkakuwuzani kuti tidzayenera kuzunzidwa. Ndipo monga mukudziwa bwino, zimenezi zinachitikadi.

Abale, ife sitikufuna mukhale osadziwa za amene akugona, kapena kumva chisoni ngati anthu ena opanda chiyembekezo. Ife timakhulupirira kuti Yesu anamwalira naukanso. Moteronso timakhulupirira kuti amene anamwalira ali mwa Yesu, Mulungu adzawaukitsa nʼkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo. Molingana ndi mawu a Ambuye mwini, tikukuwuzani kuti, ife amene tikanali ndi moyo, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sitidzawasiya kumbuyo amene anagona kale.

Iye anatifera ndi cholinga chakuti, kaya tili ndi moyo kapena tagona, tikhale naye pamodzi.

Kondwerani nthawi zonse. Pempherani kosalekeza. Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.

Nʼchifukwa chake, timayankhula monyadira mʼmipingo yonse ya Mulungu za kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso onse ndi mayesero amene mukudutsamo. Zonsezi zikutsimikiza kuti Mulungu amaweruza molungama. Zotsatira zake ndi zakuti mudzatengedwa kukhala oyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu umene mukuwuvutikira. Mulungu ndi wolungama ndipo adzalanga amene amakusautsaniwo ndikukupatsani mpumulo amene mukusautsidwa, pamodzi ndi ifenso. Izi zidzachitika Ambuye Yesu akadzaoneka mʼmalawi amoto kuchokera kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu. Iye adzalanga amene sadziwa Mulungu ndi amene samvera Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu. Adzalangidwa ndi chiwonongeko chamuyaya ndipo sadzaonanso nkhope ya Ambuye ndi ulemerero wamphamvu zake pa tsiku limene iye adzabwera kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ndi kuyamikidwa ndi onse amene anakhulupirira. Inu mudzakhala nawo mʼgulumo chifukwa munakhulupirira umboni wathu.

Potero adzadziwunjikira chuma chokhalitsa ngati maziko okhazikika a nthawi zakutsogolo, kuti akalandire moyo, umene ndi moyo weniweni.

Pakuti Mzimu amene Mulungu anatipatsa, si Mzimu wotipatsa manyazi, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzisunga. Choncho usachite manyazi kuchitira umboni Ambuye athu, kapena kuchita manyazi chifukwa cha ine wamʼndende. Koma umve nane zowawa chifukwa cha Uthenga Wabwino, mothandizidwa ndi mphamvu za Mulungu. Iye anatipulumutsa ndipo anatiyitanira ku moyo oyera mtima, osati chifukwa cha chilichonse chimene tinachita, koma chifukwa cha chikonzero ndi chisomo chake. Chisomo chimenechi anatipatsa ife mwa Khristu Yesu nthawi isanayambe. Koma tsopano Mulungu watiwululira kudzera mʼkuoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu, amene anathetsa mphamvu za imfa ndipo mwa Uthenga Wabwino anaonetsa poyera moyo umene sungafe.

Nʼchifukwa chake ndikuvutika monga ndililimu. Komabe zimenezi sizikundichititsa manyazi, popeza ndikumudziwa amene ndamukhulupirira ndipo ndikutsimikiza mtima kuti akhoza kusamalira chimene ndinamusungitsa mpaka tsiku lijalo.

Umve nane zowawa, monga msilikali wa Khristu Yesu. Palibe msilikali amene ali pa ntchito amagwiranso ntchito za anthu wamba, iye amafuna kukondweretsa bwana wolamulira.

Kumbukira Yesu Khristu wochokera ku mtundu wa Davide kuti anauka kwa akufa. Uwu ndiye uthenga wanga wabwino umene ndikuwuvutikira choterewu mpaka kumangidwa ndi maunyolo ngati wakuba. Koma mawu a Mulungu sanamangidwe ndi maunyolo. Choncho ndikupirira chilichonse chifukwa cha osankhidwa, kuti nawonso apulumutsidwe ndi Khristu Yesu ndi kulandira ulemerero wosatha. Mawu oyenera kuwadalira ndi awa: Ngati ife tinafa naye pamodzi, tidzakhalanso moyo pamodzi naye. Ngati tinapirira, tidzalamuliranso naye pamodzi. Ngati ife timukana, Iye adzatikananso.

Tsono iwe, umadziwa zonse zimene ndimaphunzitsa, makhalidwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga, mazunzo anga, masautso anga, monga zinandichitikira ku Antiokeya, ku Ikoniya ndi ku Lusitra. Ndinazunzika kwambiri. Koma Ambuye anandipulumutsa pa zonsezi. Kunena zoona, munthu aliyense amene akufuna kukhala moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi,

Koma iwe, khala tcheru nthawi zonse, pirira mʼzovuta, gwira ntchito ya mlaliki, gwira ntchito zonse za utumiki wako. Pakuti moyo wanga wayamba kale kuthiridwa ngati nsembe, ndipo nthawi yakwana yoti ndinyamuke ulendo wanga. Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liwiro ndipo ndasunga chikhulupiriro. Tsopano mphotho yanga ikundidikira imene ndi chipewa cha chilungamo, imene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa pa tsiku lijalo, osati ine ndekha komanso onse amene akufunitsitsa kubwera kwake.

Kuchokera kwa Paulo, amene ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu ndi Timoteyo mʼbale wathu. Kulembera Filemoni, bwenzi lathu lokondedwa ndi mtumiki mnzathu.

komabe ndikupempha mwachikondi. Ine Paulo, munthu wokalamba, ndipo tsopano ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu,

Koma tikuona Yesu, amene kwa kanthawi kochepa anamuchepetsa pangʼono kwa angelo, koma tsopano wavala ulemerero ndi ulemu chifukwa anamva zowawa za imfa, kuti mwachisomo cha Mulungu, Iye afere anthu onse. Mulungu amene analenga zinthu zonse ndipo zinthu zonse zilipo chifukwa cha Iye ndi mwa Iye, anachiona choyenera kubweretsa ana ake ambiri mu ulemerero. Kunali koyenera kudzera mʼnjira ya zowawa, kumusandutsa Yesu mtsogoleri wangwiro, woyenera kubweretsa chipulumutso chawo.

Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi mnofu ndi magazi, Yesu nayenso anakhala munthu ngati iwowo kuti kudzera mu imfa yake awononge Satana amene ali ndi mphamvu yodzetsa imfa. Pakuti ndi njira yokhayi imene Iye angamasule amene pa moyo wawo wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa.

Kotero tsono kwatsala mpumulo wa Sabata kwa anthu a Mulungu; Pakuti aliyense amene analowa mu mpumulo wa Mulungu anapuma pa ntchito zake, monga momwe Mulungu anachitira. Tiyeni tsono tiyesetse kulowa mu mpumulo, kuti pasapezeke wina aliyense wolephera potsatira chitsanzo chawo cha kusamvera.

Yesu, pa nthawi imene anali munthu pa dziko lapansi pano, anapereka mapemphero ake ndi zopempha mofuwula ndi misozi kwa Iye amene akanamupulumutsa ku imfa, ndipo anamumvera chifukwa anagonjera modzipereka. Ngakhale Iye anali Mwana wa Mulungu anaphunzira kumvera pomva zowawa. Atasanduka wangwiro kotheratu, anakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye.

Kumbukirani masiku akale aja mutangowunikiridwa chatsopano, pa nthawi imeneyi munapirira zowawa zambiri. Nthawi zina ankakunyozani pagulu ndi kukuzunzani. Nthawi zina munkamva zowawa pamodzi ndi amene ankasautsidwa chotere. Munkawamvera chisoni amene anali mʼndende ndiponso munkalola mokondwera kuti akulandeni katundu wanu chifukwa munkadziwa kuti muli nacho chuma choposa ndi chosatha. Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu.

Onsewa anakhalabe mwachikhulupiriro mpaka anafa. Iwo sanalandire zimene Mulungu anawalonjeza; iwo anangozionera chapatali ndi kuzilandira. Ndipo iwo anavomereza kuti analidi alendo ndi osakhazikika pa dziko lapansi. Anthu amene amanena zinthu zotere amaonekeratu kuti akufuna dziko lawo lenileni. Akanakhala kuti akuganizira za dziko limene analisiya akanapeza mpata obwerera kwawo. Mʼmalo mwake, iwo amafunitsitsa dziko labwino, ndilo lakumwamba. Nʼchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wawo, pakuti Iye anawalonjeza mudzi.

Iye anasankha kuzunzika nawo limodzi anthu a Mulungu kuposa kusangalala ndi zokondweretsa za uchimo kwa nthawi yochepa. Anaona kuti kuzunzika chifukwa cha Khristu kunali kwa mtengowapatali kuposa chuma cha ku Igupto, chifukwa amaona mphotho ya mʼtsogolo. Ndi chikhulupiriro anachoka ku Igupto wosaopa ukali wa mfumu. Iye anapirira chifukwa anamuona Mulungu amene ndi wosaonekayo.

Kodi ndinenenso chiyani? Nthawi yandichepera yoti ndinene za Gideoni, Baraki, Samsoni, Yefita, Davide, Samueli ndi aneneri, amene ndi chikhulupiriro anagonjetsa mafumu, anakhazikitsa chilungamo ndi kulandira zimene zinalonjezedwa. Anatseka pakamwa pa mikango, anazimitsa moto waukali, ndipo anapulumuka osaphedwa ndi lupanga. Anali ofowoka koma analandira mphamvu; anasanduka amphamvu pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani awo. Amayi ena analandira anthu awo amene anafa, ataukitsidwanso. Enanso anazunzidwa ndipo anakana kumasulidwa, kuti adzaukenso ndi moyo wabwino. Ena anawaseka ndi kuwakwapula, pamenenso ena anamangidwa ndi kupita ku ndende. Anagendedwa miyala; anachekedwa pakati; ena anaphedwa ndi lupanga. Iwo anayendayenda atavala zikopa zankhosa ndi zikopa zambuzi, umphawi okhaokha, ozunzidwa ndi kuvutitsidwa. Dziko lapansi silinawayenere. Anayendayenda mʼzipululu ndi mapiri, ndiponso mʼmapanga ndi mʼmaenje.

Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.

Tiyeni tiyangʼanitsitse Yesu, amene ndi woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu. Chifukwa cha chimwemwe chimene chimamudikira anapirira zowawa zapamtanda. Iye ananyoza manyazi a imfa yotere ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu. Muzilingalira za Iye amene anapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafowoke ndi kutaya mtima. Polimbana ndi uchimo, simunafike mpaka pokhetsa magazi.

Nʼchifukwa chakenso Yesu anafera kunja kwa mzinda kuti ayeretse anthu ake kudzera mʼmagazi ake. Tiyeni tsono, tipite kwa iye kunja kwa msasa, titasenza chitonzo chake. Pakuti ife tilibe mzinda wokhazikika koma tikudikira mzinda umene ukubwera.

Abale, muchiyese ngati chimwemwe chenicheni nthawi zonse pamene mukukumana ndi mayesero amitundumitundu. Inu mukudziwa kuti kuyesedwa kwa chikhulupiriro chanu kumabweretsa chipiriro. Chipiriro chiyenera kugwira ntchito yake kuti mukhale okhwima ndi angwiro, osasowa kanthu kalikonse.

Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.

Abale, tengerani chitsanzo cha aneneri amene anayankhula mʼdzina la Ambuye. Iwowo anakumana ndi zovuta koma anapirira. Monga mukudziwa, tinawatenga ngati odalitsika anthu amene anapirira. Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mwaona zimene Ambuye anamuchitira potsiriza pake. Ambuye ndi wodzaza ndi chisoni ndi chifundo.

kuti tidzalandire chuma chomwe sichingawonongeke, kuyipitsidwa kapena kufota. Chuma chimenechi akukusungirani kumwamba. Mwachikhulupiriro, mukusungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mpaka chipulumutso chitafika chimene chinakonzedwa kuti adzachionetse nthawi yotsiriza.

Pamene mukubwera kwa Iye, amene ndi Mwala wa moyo, umene anthu anawukana, koma Mulungu anawusankha kuti ndi wa mtengowapatali, inunso, mukhale ngati miyala ya moyo yoti Mulungu amangire nyumba yake yauzimu kuti mukhale ansembe opatulika, opereka nsembe zauzimu zovomerezeka ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.

Munayitanidwa kudzachita zimenezi, chifukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire mʼmapazi ake. “Iye sanachite tchimo kapena kunena bodza.” Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sanabwezere chipongwe, pamene Iye ankamva zowawa, sanaopseze. Mʼmalo mwake, anadzipereka kwa Mulungu amene amaweruza molungama.

Koma ngakhale mumve zowawa chifukwa cha chilungamo, ndinu odala. “Musaope anthu, musachite mantha.”

Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu.

Abale okondedwa musadabwe ndi mayesero owawa amene mukukumana nawo ngati kuti china chake chachilendo chakuchitikirani. Koma kondwerani popeza mukumva zowawa pamodzi ndi Khristu, kuti mudzakondwere kwakukulu pamene ulemerero wake udzaonekera. Ngati akuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, ndiye kuti Mzimu waulemerero wa Mulungu uli pa inu.

koma ngati mumva zowawa chifukwa ndinu Mkhristu, musachite manyazi, koma muyamike Mulungu chifukwa cha dzinalo.

Nʼchifukwa chake, iwo amene akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu, adzipereke okha mʼmanja mwa Mlengi wawo wokhulupirika ndi kumapitiriza kuchita zabwino.

Ndipo Mʼbusa wamkulu akadzaonekera, mudzalandira chipewa cha ulemerero chosafota.

Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni. Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani. Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze. Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi. Ndipo Mulungu wachisomo chonse, amene anakuyitanani ku ulemerero wake wamuyaya mwa Khristu, mutamva zowawa pa kanthawi, adzakukonzaninso ndi kukulimbitsani pa maziko olimba.

Musakhale ngati Kaini, amene anali wa woyipayo ndipo anapha mʼbale wake. Nanga anamupha chifukwa chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoyipa ndipo zochita za mʼbale wake zinali zolungama.

Abale anga, musadabwe ngati dziko lapansi lidana nanu. Ife tikudziwa kuti tinatuluka mu imfa ndi kulowa mʼmoyo, chifukwa timakonda abale athu. Aliyense amene sakonda mʼbale wake akanali mu imfa. Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha. Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu.

Inu ana okondedwa, ndinu ochokera kwa Mulungu ndipo mwawagonjetsa aneneri onyengawa, chifukwa Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali mʼdziko lapansi.

chifukwa aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko lapansi. Chikhulupiriro chathu ndicho timagonjetsera dziko lapansi. Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Yekhayo amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.

“Onani akubwera ndi mitambo,” ndipo “Aliyense adzamuona, ndi amene anamubaya omwe.” Ndipo anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi “adzalira chingʼangʼadza chifukwa cha Iye.” Zidzakhaladi momwemo, Ameni. “Ine ndine Alefa ndi Omega,” akutero Ambuye Mulungu Wamphamvuzonseyo “amene muli, amene munalipo, ndi amene mudzakhalapo.”

Ine ndine Wamoyo; ndinali wakufa ndipo taona ndine wamoyo mpaka muyaya! Ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi Hade.

Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wakudya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku paradizo wa Mulungu.

“Lembera mngelo wa mpingo wa ku Simurna kuti: Awa ndi mawu ochokera kwa amene ndi Woyamba ndi Wotsiriza, amene anafa nʼkukhalanso ndi moyo. Ine ndimadziwa masautso ako ndi umphawi wako, chonsecho ndiwe wolemera! Ndikudziwa zimene amakusinjirira anthu amene amati ndi Ayuda pamene sizili choncho, koma ndi a mpingo wa Satana. Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, Satana adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani chipewa cha ulemerero wamoyo.

Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana sadzapwetekedwa ndi pangʼono pomwe ndi imfa yachiwiri.

Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa kumene mumakhala, kumene kuli mpando waufumu wa Satana. Komabe inu ndinu okhulupirika kwa Ine. Simunataye chikhulupiriro chanu pa Ine, ngakhale mʼmasiku a Antipa, mboni yanga yokhulupirika, amene anaphedwa mu mzinda wanu, kumene amakhala Satana.

Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Kwa amene adzapambane ndidzamupatsa chakudya chobisika cha mana. Ndidzamupatsanso mwala woyera wolembedwapo dzina latsopano, lodziwa iye yekha amene walandirayo.’ ”

Amene adzapambana ndi kuchita chifuniro changa mpaka kumapeto, ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu yonse ya anthu. Adzayilamulira ndi ndodo yachitsulo ndipo nadzayiphwanyaphwanya ngati mbiya. Ulamuliro umenewu ndi omwe ndinalandira kwa Atate anga. Ine ndidzamupatsanso nthanda, nyenyezi yowala mʼmamawa ija. Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.

Amene adzapambane adzavala zoyera ngati ena aja. Sindidzafafaniza dzina lake mʼbuku lamoyo, koma ndidzamuchitira umboni pamaso pa Atate anga ndi angelo ake. Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”

Iye amene adzapambane ndidzamusandutsa mzati wa mʼNyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso. Pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, Yerusalemu watsopano, umene ukubwera pansi kuchokera kumwamba kwa Mulungu wanga; ndipo pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano. Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.’ ”

Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambana ndi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu. Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”

Mwana Wankhosa atatsekula chomatira chachisanu, ndinaona kunsi kwa guwa lansembe kunali mizimu ya anthu amene anaphedwa chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi chifukwa chochitira umboni. Iwo anafuwula kuti, “Mudzawaleka mpaka liti, Inu Ambuye wamkulu, woyera ndi woona, osawaweruza anthu okhala mʼdziko lapansi ndi kulipsira magazi athu?” Pamenepo aliyense wa anthuwo anapatsidwa mwinjiro woyera ndipo anawuzidwa kuti adikire pangʼono kufikira chiwerengero cha anzawo ndi abale awo amene anayeneranso kuphedwa ngati iwo, chitakwanira.

Zitatha izi ndinayangʼana patsogolo panga ndipo ndinaona gulu lalikulu la anthu loti munthu sangathe kuliwerenga lochokera dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu wa anthu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse, atayima patsogolo pa mpando waufumu, pamaso pa Mwana Wankhosa. Iwo anali atavala mikanjo yoyera ndi kunyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo.

Pamenepo mmodzi wa akuluakulu aja anandifunsa kuti, “Kodi avala mikanjo yoyerawa ndani ndipo akuchokera kuti?” Ine ndinayankha kuti, “Mbuye wanga mukudziwa ndinu.” Tsono iye anandiwuza kuti, “Amenewa ndi amene anatuluka mʼmazunzo aakulu aja. Anachapa mikanjo yawo naziyeretsa mʼmagazi a Mwana Wankhosa. Nʼchifukwa chake, “iwowa ali patsogolo pa mpando waufumu wa Mulungu ndipo akutumikira usana ndi usiku mʼNyumba ya Mulungu; ndipo Iye wokhala pa mpando waufumu adzawaphimba ndi tenti yake. ‘Iwowa sadzamvanso njala, sadzamvanso ludzu, dzuwa kapena kutentha kulikonse sikudzawawotcha.’ Pakuti Mwana Wankhosa amene ali pakati pa mpando waufumu adzakhala mʼbusa wawo. ‘Iye adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.’ ‘Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.’ ”

A mitundu ina anapsa mtima; koma yafika nthawi yoonetsa mkwiyo. Nthawi yakwana yoweruza anthu akufa, yopereka mphotho kwa atumiki anu, aneneri, anthu oyera mtima anu ndi amene amaopa dzina lanu, wamngʼono pamodzi ndi wamkulu yemwe. Yafika nthawi yowononga amene awononga dziko lapansi.”

Abale athuwo anamugonjetsa ndi magazi a Mwana Wankhosa ndiponso mawu a umboni wawo. Iwo anadzipereka kwathunthu, moti sanakonde miyoyo yawo.

Pamenepo chinjokacho chinamupsera mtima mayiyo ndipo chinachoka kupita kukachita nkhondo ndi ana ena onse a mayiyo, ndiye kuti anthu amene anasunga malamulo a Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu. Kenaka ndinaona chinjokacho chitayima mʼmbali mwa nyanja.

Chinaloledwa kuchita nkhondo ndi oyera mtima ndi kuwagonjetsa. Ndipo chinapatsidwanso mphamvu zolamulira anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse.

Chirombo cha chiwirichi chinapatsidwa mphamvu zakupereka mpweya kwa fano la chirombo choyamba chija kuti liyankhule ndi kuphetsa aliyense wokana kupembedza fanolo. Chinakakamiza aliyense, wamngʼono, wamkulu, wolemera, wosauka, mfulu ndi kapolo kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi. Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, chimene ndi dzina la chirombocho kapena nambala yotanthauza dzina lake. Pano pafunika nzeru. Munthu amene ali ndi nzeru atanthauze nambala ya chirombocho, pakuti nambalayo ikutanthauza munthu. Nambala yake ndi 666.

Pamenepa ndi pofunika kupirira kwa anthu oyera mtima amene amasunga malamulo a Mulungu ndi kukhalabe okhulupirika kwa Yesu. Kenaka ndinamva mawu kuchokera kumwamba akuti, “Lemba kuti, Odala anthu amene akufa ali mwa Ambuye kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo.” “Inde,” akutero Mzimu, “akapumule ntchito zawo zotopetsa pakuti ntchito zawo zidzawatsata.”

Ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera mtima, magazi a amene anachitira umboni Yesu. Nditamuona mkaziyo ndinadabwa kwambiri.

Kuwala kwa nyale sikudzawunikanso mwa inu. Mawu a mkwati ndi mkwatibwi sadzamvekanso mwa iwe. Amalonda anu anali akuluakulu a dziko lapansi. Mitundu yonse inasokonezedwa ndi zamatsenga zako. Mwa iye munapezeka magazi a aneneri ndi a oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa pa dziko lapansi.”

Iye anavala mkanjo woviyika mʼmagazi, ndipo dzina lake ndi Mawu a Mulungu. Magulu ankhondo akumwamba ankamutsatira atakwera pa akavalo oyera, ndipo iwowo atavala nsalu zoyera kwambiri ndi zosada.

Ndinaona mipando yaufumu pamene anakhalapo anthu amene anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndipo ndinaona mizimu ya amene anadulidwa makosi chifukwa cha umboni wa Yesu ndi chifukwa cha Mawu a Mulungu. Iwo sanapembedze nawo chirombo kapena fano lake ndipo sanalembedwe chizindikiro chake pa mphumi zawo kapena pa manja awo. Iwo anakhalanso ndi moyo nalamulira pamodzi ndi Khristu zaka 1,000. (Akufa ena onse sanaukenso mpaka zitatha zaka 1,000). Uku ndiko kuuka kwa akufa koyamba. Odala ndi oyera mtima amene adzaukitsidwa nawo pa kuukitsidwa koyamba. Imfa yachiwiri ilibe mphamvu pa iwo koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu ndipo adzalamulira naye pamodzi zaka 1,000.

‘Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ ” Amene anakhala pa mpando waufumuyo anati, “Ndikulenga zinthu zonse zikhale zatsopano!” Ndipo anati, “Lemba izi, pakuti mawu awa ndi okhulupirika ndi woona.” Iye anandiwuza kuti, “Kwatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa onse akumva ludzu, ndidzawapatsa zakumwa zaulere zochokera ku kasupe wamadzi amoyo.

Iye amene adzapambane adzalandira zonsezi, ndipo ndidzakhala Mulungu wake ndi Iye adzakhala mwana wanga.

“Taonani, ndikubwera posachedwa! Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense malinga ndi zimene anachita. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chimaliziro ndine.

Chichewa - Chichewa - NY

NYCCL - Mawu A Mulungu Mu Chichewa Chalero - 2016

This Bible text is from Biblica Open God's Word In Contemporary Chichewa
https://open.bible/bibles/chichewa-biblica-text-bible/
provided by: Biblica Inc, available by Creative Commons CC-BY-SA-4.0,
and this new compilation is shared as www.creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0.
Languages are made available to you by www.ipedge.net