01 – Baibulo Lopatulika

Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Baibulo Lopatulika.

Mavesi atatu ofunika kwambiri

Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo

Ine ndikukuwuzani zoonadi kuti, kufikira kutha kwa thambo ndi dziko lapansi, chilichonse chimene chinalembedwa mʼmalamulo, ngakhale kalemba kakangʼonongʼono, chidzakwaniritsidwa.

Iye amene akana Ine ndipo salandira mawu anga ali ndi womuweruza. Tsiku lomaliza mawu amene ndiyankhulawa adzamutsutsa.

Mavesi onse motsatira dongosolo lolondola – 343 ndime

Mulungu anaona kuti kuwalako kunali bwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima.

Ndipo njoka inali yochenjera kuposa nyama yakuthengo iliyonse imene Yehova Mulungu anapanga. Njokayo inati kwa mkaziyo, “Kodi Mulungu ananenadi kuti, ‘Inu musadye zipatso za mtengo uliwonse mʼmundamu?’ ”

Pamene Yehova anaona kuti kuyipa kwa munthu pa dziko lapansi kunali kwakukulu ndi kuti nthawi zonse amalingalira ndi kukhumbira kuchita zoyipa zokhazokha,

Yehova ndi wankhondo; Yehova ndilo dzina lake.

Tsono Mose anapita kukawuza anthu mawu onse a Yehova ndi malamulo onse, ndipo anthu onse anayankha mogwirizana kuti, “Tidzachita zonse zimene Yehova wanena.” Ndipo Mose analemba zonse zimene Yehova ananena. Mmawa mwake Mose anadzuka nayamba kumanga guwa lansembe mʼmunsi mwa phirilo ndipo anayimika miyala khumi ndi iwiri ngati zipilala kuyimira mafuko khumi ndi awiri a Israeli.

Mulungu si munthu kuti aname, kapena mwana wa munthu kuti asinthe maganizo ake. Kodi amayankhula koma osachita? Kodi amalonjeza koma osakwaniritsa?

Musawonjezere pa zimene ndikukulamulirani ndipo musachotserepo, koma muwasunge malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani.

Taonani, ndakuphunzitsani malangizo ndi malamulo monga Yehova Mulungu wanga anandilamulira kuti inuyo muwatsatire mʼdziko limene mukulowa ndi kulitengali. Muwasunge mosamalitsa pakuti zimenezi zidzaonetsa nzeru zanu ndi kuzindikira kwanu kwa anthu a mitundu ina, amene adzamva za malangizo onsewa nati, “Ndithudi, mtundu waukulu uwu ndi wa anthu anzeru ndi ozindikira.”

Kumbukirani tsiku limene munayimirira pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku Horebu, pamene anati kwa ine, “Sonkhanitsa anthu pamaso panga kuti amve mawu anga ndi kuti aphunzire kundilemekeza mʼmoyo wawo onse mʼdzikomo ndi kuti ana awo aziwaphunzitsa zimenezi.”

Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi moto wonyeketsa ndipo ndi Mulungu wansanje.

Choncho samalirani kuchita zimene Yehova Mulungu wanu akukulamulirani inu, musapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere.

Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse. Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka. Muwamange ngati zizindikiro pa manja anu ndi kuwamangirira pa zipumi zanu. Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.

Iye anakutsitsani nakumvetsani njala kenaka nʼkukudyetsani mana amene anali osadziwika kwa inu kapena makolo anu, kuti akuphunzitseni kuti munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.

Samalirani malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda mʼnjira yake ndi kumuopa Iye.

Ndipo Yehova anati kwa ine, “Anthu awa ndawaona ndipo ndi anthu okanikadi!

Tsopano inu Aisraeli, nʼchiyani chimene Yehova afuna kwa inu? Iye akufuna kuti muzimuopa poyenda mʼnjira zake zonse ndi kumamukonda Iye, kumutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi kusunga malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero kuti zizikuyenderani bwino.

Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndipo nthawi zonse muzitsata zimene Iyeyo anakulamulani, malangizo, zikhazikitso ndi malamulo ake.

Sungani mawu amenewa mu mtima mwanu ndi mʼmaganizo mwanu, muwamangirire pa mikono yanu ndipo muwayike pamphumi panu. Mawuwa muziphunzitsa ana anu, muzikamba za iwo pamene mukhala pansi mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mugona ndi pamene mukudzuka. Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu,

Taonani, lero ndikuyika dalitso ndi temberero pakati panu, dalitso ngati mumvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero. Temberero ngati simumvera malamulo a Yehova Mulungu wanu ndi kupatuka pa njira imene ndikulamulirani lero potsata milungu ina imene simunayidziwe.

Onetsetsani kuti mukuchita zimene ndikukulamulirani. Musawonjezerepo kapena kuchotserapo.

Ngati mneneri kapena wina aliyense amene amanena zamʼtsogolo mwa maloto atuluka pakati panu, nalengeza za chizindikiro chozizwitsa kapena chodabwitsa, chinthu nʼkuchitikadi, tsono iyeyo nʼkunena kuti, “Tiyeni titsatire milungu ina, tiyeni tiyipembedze,” (kunena milungu imene simunayidziwe), musamumvere mneneriyo kapena wolotayo. Yehova Mulungu wanu afuna akuyeseni kuti aone ngati mumamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Muyenera kutsatira Yehova Mulungu wanu, ndipo ndi Iyeyo amene muyenera kumuopa. Muzisunga malamulo ake ndi kumamumvera, muzimutumikira ndipo kumukangamira Iyeyo.

Asunge zimene walembazo ndipo ayenera kumaziwerenga masiku onse a moyo wake, kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake posunga mosamalitsa malamulo ndi malangizowa.

Yehova Mulungu wanu akukulamulani lero lino kuti mutsate malangizo ndi malamulo ake ndipo muwasunge mosamalitsa ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

“Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita kapena sasunga mawu a malamulo awa.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”

Ngati mumvera Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamalitsa malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, Yehova Mulungu wanu adzakukwezani pamwamba pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.

Koma ngati simumvera Yehova Mulungu wanu ndi kusatsata mosamalitsa malamulo ake ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, matemberero awa adzabwera pa inu ndikukugonjetsani:

Zinsinsi ndi za Yehova Mulungu wathu koma zinthu zimene zaululidwa ndi zathu ndi ana athu kwamuyaya, kuti titsatire mawu onse a mʼmalamulowa.

ngati mudzamvera Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo ake ndi mawu ake amene alembedwa Mʼbuku ili la Malamulo ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.

Lero kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni zodzakutsutsani pakuti ndayika pamaso panu moyo ndi imfa, madalitso ndi matemberero. Tsopano sankhani moyo kuti inu ndi ana anu mukhale ndi moyo.

Mudzasonkhanitse anthu onse pamodzi, amuna, akazi ndi ana pamodzi ndi alendo amene akukhala mʼmizinda yanu, kuti adzawamve ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamala mawu onse a mʼmalamulowa.

“Tengani Buku ili la Malamulo ndi kuliyika pambali pa Bokosi la Chipangano la Yehova Mulungu wanu. Likhale kumeneko ngati mboni yokutsutsani. Pakuti Ine ndikudziwa kuwukira kwanu ndi kuwuma mtima kwanu. Ngati inu mwakhala mukuwukira Yehova ine ndili moyo ndiponso ndili nanu pamodzi, nanga mudzawukira motani ine ndikamwalira!

Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana.

Koma onetsetsani kuti mukuopa Yehova ndi kumutumikira mokhulupirika ndi mtima wanu wonse. Nthawi zonse muziganizira zinthu zazikulu wakhala akukuchitirani.

Koma Samueli anayankha kuti, “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina kapena kumvera mawu a ake? Taona, kumvera ndi kwabwino kuposa nsembe, ndipo kutchera khutu ndi kwabwino kuposa kupereka mafuta a nkhosa. Pakuti kuwukira kuli ngati tchimo lowombeza, ndipo kukhala nkhutukumve kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Chifukwa mwakana mawu a Yehova. Iyenso wakukana kuti iweyo ukhale mfumu.” Tsono Sauli anati kwa Samueli, “Ine ndachimwa. Ndaphwanya malamulo a Yehova ndiponso malangizo anu. Ndinkaopa anthu ndipo ndinawamvera.

Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova; ndilibe mlandu wochoka pamaso pa Mulungu wanga. Malamulo ake onse ali pamaso panga, sindinasiye malangizo ake.

Koma anthuwa sanamvere ndipo anawumitsa khosi ngati momwe analili makolo awo, amene sanadalire Yehova Mulungu wawo.

“Pitani ndipo mukafunse Yehova mʼmalo mwanga ndi mʼmalo mwa otsala a Israeli ndi Yuda za zimene zalembedwa mʼbuku limene lapezekali. Mkwiyo wa Yehova ndi waukulu umene watsanulidwa pa ife chifukwa makolo athu sanasunge mawu a Yehova. Iwo sanachite motsatira zonse zimene zalembedwa mʼbuku ili.”

Koma iwo ananyoza amithenga a Mulungu, anapeputsa mawu awo ndipo ankaseka aneneri ake mpaka anawutsa mkwiyo wa Yehova pa anthu ake ndipo panalibenso mankhwala owachiritsa.

Popeza Ezara anadzipereka kuwerenga ndi kusunga malamulo a Yehova, iye anafunitsitsa kuphunzitsa Aisraeli malamulo ndi malangizo a Mulungu.

Ndinakhala pansi chomwecho wokhumudwa mpaka nthawi ya nsembe ya madzulo. Ndipo onse amene ankaopa mawu a Mulungu wa Israeli chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo anayamba kubwera kwa ine kudzasonkhana.

Koma anthuwo amawuza Mulungu kuti, ‘Tichokereni!’ Ife tilibe chikhumbokhumbo chofuna kudziwa njira zanu.

Sindinapatuke kusiya malamulo ochokera pakamwa pake; ndasunga mawu a pakamwa pake kupambana chakudya changa cha tsiku ndi tsiku.

Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati: “Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga poyankhula mawu opanda nzeru? Onetsa chamuna; ndikufunsa ndipo undiyankhe. “Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi? Ndiwuze ngati ukudziwa.

Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.

Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi, oyengedwa kasanu nʼkawiri. Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.

Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova; ndilibe mlandu wochoka pamaso Mulungu wanga.

Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro; mawu a Yehova alibe cholakwika. Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa Iye.

Lamulo la Yehova ndi langwiro, kutsitsimutsa moyo. Maumboni a Yehova ndi odalirika, amapereka nzeru kwa wopanda nzeru. Malangizo a Yehova ndi olungama, amapereka chimwemwe mu mtima. Malamulo a Yehova ndi onyezimira, amapereka kuwala. Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro, chimakhala mpaka muyaya. Maweruzo a Yehova ndi owona ndipo onse ndi olungama; ndi a mtengowapatali kuposa golide, kuposa golide weniweni; ndi otsekemera kuposa uchi, kuposa uchi wochokera pa chisa chake. Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo; powasunga pali mphotho yayikulu.

pakuti chikondi chanu chili pamaso panga nthawi zonse, ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu nthawi zonse.

Liwu la Yehova ndi lamphamvu; liwu la Yehova ndi laulemerero.

Mʼmanja mwanu ndipereka mzimu wanga; womboleni Yehova Mulungu wachoonadi.

Ndidzakulangiza ndi kukuphunzitsa njira imene udzayendamo; ndidzakupatsa uphungu ndi kukuyangʼanira. Usakhale ngati kavalo kapena bulu, zimene zilibe nzeru, koma ziyenera kuwongoleredwa ndi zitsulo za mʼkamwa ndi pamutu, ukapanda kutero sizibwera kwa iwe.

Dziko lonse lapansi liope Yehova; anthu onse amulemekeze Iye.

Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya, zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.

Bwerani ana anga, mundimvere; ndidzakuphunzitsani kuopa Yehova.

Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera. Mʼbuku mwalembedwa za ine. Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga; lamulo lanu lili mu mtima mwanga.” Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu; sinditseka milomo yanga monga mukudziwa Inu Yehova. Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga; ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu. Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu pa msonkhano waukulu.

Koma kwa woyipa, Mulungu akuti, “Kodi uli ndi mphamvu yanji kuti uzinena malamulo anga kapena kutenga pangano langa pa milomo yako? Iwe umadana ndi malangizo anga ndipo umaponyera kumbuyo kwako mawu anga.

Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.

Ambuye analengeza mawu, ndipo gulu linali lalikulu la iwo amene anapita kukawafalitsa;

iwo sanasunge pangano la Mulungu ndipo anakana kukhala mʼmoyo wotsatira lamulo lake.

“Koma anthu anga sanandimvere; Israeli sanandigonjere. Kotero ndinawasiya ndi mitima yawo yosamverayo kuti atsate zimene ankafuna. “Anthu anga akanangondimvera, Israeli akanatsatira njira zanga, nʼkanafulumira motani kuti ndigonjetse adani awo ndi kutembenuza mkono wanga kulimbana ndi amaliwongo! Iwo amene amadana ndi Yehova akanakhwinyata pamaso pake, ndipo chilango chawo chinakakhala mpaka kalekale.

Ndiphunzitseni njira yanu Yehova, ndipo ndidzayenda mʼchoonadi chanu; patseni mtima wosagawikana kuti ndilemekeze dzina lanu.

Mu msonkhano wa oyera mtima Mulungu amaopedwa kwambiri; Iye ndiye wochititsa mantha kupambana onse amene amuzungulira.

Yehova anatumiza mdima nasandutsa dziko kuti likhale la mdima. Koma anthuwo anakaniratu mawu a Yehova.

pakuti iwowo anawukira mawu a Mulungu ndi kunyoza uphungu wa Wammwambamwamba. Kotero Iye anawapereka kuti agwire ntchito yakalavulagaga; anagwa pansi ndipo panalibe woti awathandize.

Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa; anawalanditsa ku manda.

Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama; malangizo ake onse ndi odalirika. Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi, ochitidwa mokhulupirika ndi molungama.

Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru; onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu. Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.

Tamandani Yehova. Wodala munthu amene amaopa Yehova, amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake.

Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova kusiyana ndi kudalira munthu. Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova kusiyana ndi kudalira mafumu.

Odala ndi amene moyo wawo ulibe cholakwa, amene amayenda monga mwa malamulo a Yehova.

Pamenepo ine sindikanachititsidwa manyazi, poganizira malamulo anu onse.

Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake? Akawasamala potsata mawu anu.

Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse; musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.

Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga kuti ndisakuchimwireni.

Ndi milomo yanga ndimafotokoza malamulo anu onse amene amachokera pakamwa panu.

Tsekulani maso anga kuti ndithe kuona zinthu zodabwitsa mʼmalamulo anu.

Moyo wanga wafowoka polakalaka malamulo anu nthawi zonse.

Inu mumadzudzula onyada, otembereredwa, amene achoka pa malamulo anu.

Mundichotse mʼnjira zachinyengo; mundikomere mtima pondiphunzitsa malamulo anu.

Ndasankha njira ya choonadi; ndayika malamulo anu pa mtima panga.

Mundipatse mtima womvetsa zinthu ndipo ndidzasunga malamulo anu ndi kuwamvera ndi mtima wanga wonse.

Ndidzasunga malamulo anu nthawi zonse, ku nthawi za nthawi.

popeza ndimakondwera ndi malamulo anu chifukwa ndimawakonda.

Ndayipidwa kwambiri chifukwa cha oyipa amene ataya malamulo anu.

Ndidzafulumira ndipo sindidzazengereza kumvera malamulo anu.

Ndi bwino kuti ndinasautsidwa kuti ndithe kuphunzira malamulo anu.

Lamulo lochokera mʼkamwa mwanu limandikomera kwambiri kuposa ndalama zambirimbiri za siliva ndi golide.

Mawu anu Yehova ndi amuyaya; akhazikika kumwambako.

Ndithu, ine ndimakonda malamulo anu! Ndimalingaliramo tsiku lonse.

Mawu anu ndi otsekemera ndikawalawa, otsekemera kuposa uchi mʼkamwa mwanga!

Ndimapeza nzeru zodziwira zinthu kuchokera mʼmalangizo anu; kotero ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.

Mawu anu ndi nyale ya kumapazi kwanga ndi kuwunika kwa pa njira yanga.

Mtima wanga wakhazikika pa kusunga zophunzitsa zanu mpaka kumapeto kwenikweni.

Chokani kwa ine, inu anthu ochita zoyipa, kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga!

Inu mumakana onse amene amasochera kuchoka pa zophunzitsa zanu, pakuti chinyengo chawo ndi chopanda phindu.

Yehova, ndi nthawi yoti muchitepo kanthu; malamulo anu akuswedwa.

Mitsinje ya misozi ikuyenda kuchoka mʼmaso mwanga, chifukwa anthu sakumvera malamulo anu.

Ndikusautsidwa kwambiri mʼkati mwanga chifukwa adani anu amanyalanyaza mawu anu.

Ngakhale ndili wamngʼono ndi wonyozeka, sindiyiwala malangizo anu.

Chilungamo chanu nʼchamuyaya, ndipo malamulo anu nʼchoona.

Maso anga amakhala chipenyere nthawi yonse ya usiku, kuti ndithe kulingalira malonjezo anu.

Mawu anu onse ndi owona; malamulo anu onse olungama ndi amuyaya.

Olamulira amandizunza popanda chifukwa, koma mtima wanga umanjenjemera ndi mawu anu.

Ine ndimakondwa ndi lonjezo lanu, ngati munthu amene wapeza chuma chambiri.

Ndikufunitsitsa chipulumutso chanu Yehova, ndipo ndimakondwera ndi malamulo anu.

Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera ndipo ndidzayamika dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu, pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu kupambana zinthu zonse.

Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.

“Kodi inu anthu osachangamukanu, mudzakondwera ndi kusachangamuka mpaka liti? Nanga anthu onyogodola adzakondabe kunyogodola mpaka liti? Kapena opusa adzadana ndi nzeru mpaka liti?

Popeza iwo anadana ndi chidziwitso ndipo sanasankhe kuopa Yehova, popeza iwo sanasamale malangizo anga ndipo ananyoza chidzudzulo changa. Tsono adzadya zipatso zoyenera mayendedwe awo ndi kukhuta ndi ntchito zimene anachita kwa ena.

ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu; ngati upempha kuti uzindikire zinthu inde kupempha ndi mtima wonse kuti ukhale womvetsa zinthu, ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika, ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova; ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova.

Makhalidwe ochitira ena chifundo ndi owonetsa kukhulupirika asakuchokere. Uwamangirire mʼkhosi mwako ngati mkanda ndi kuwalemba pa mtima pako.

Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse ndipo usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

Upeze nzeru, upeze nzeru zomvetsa zinthu; usayiwale mawu anga kapena kutayana nawo. Usasiye nzeru ndipo idzakusunga. Uziyikonda ndipo idzakuteteza.

Mwana wanga, mvetsetsa zimene ndikunena; tchera khutu ku mawu anga. Usayiwale malangizo angawa, koma uwasunge mu mtima mwako.

Maso ako ayangʼane patsogolo; uziyangʼana kutsogolo molunjika. Uzilingalira bwino kumene kupita mapazi ako ndipo njira zako zonse zidzakhala zosakayikitsa. Usapatukire kumanja kapena kumanzere; usapite kumene kuli zoyipa.

Paja malamulo awa ali ngati nyale, malangizowa ali ngati kuwunika, ndipo chidzudzulo cha mwambo ndiwo moyo weniweni,

Kuopa Yehova ndiko kudana ndi zoyipa. Ine ndimadana ndi kunyada, kudzitama, kuchita zoyipa, ndiponso kuyankhula zonyenga.

Usadzudzule munthu wonyoza kuti angadzadane nawe; dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.

Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru; kudziwa Woyerayo ndiko kukhala womvetsa bwino zinthu.

Kuopa Yehova ndiye kasupe wamoyo, kumathandiza munthu kuti apewe msampha wa imfa.

Nʼkwabwino kwambiri kupeza nzeru kupambana golide. Kukhala womvetsa bwino zinthu nʼkwabwino kupambana ndi kukhala ndi siliva.

Usayankhule munthu wopusa akumva, pakuti adzanyoza mawu ako anzeru.

Wokana kumvera malamulo ngakhale pemphero lake lomwe limamunyansa Yehova.

“Mawu ali wonse a Mulungu ndi opanda cholakwika; Iye ndi chishango kwa amene amathawira kwa Iye. Usawonjezepo kanthu pa mawu ake, kuopa kuti Iye angadzakudzudzule ndi kukupeza kuti ndiwe wabodza.”

Basi zonse zamveka; mathero a nkhaniyi ndi awa: uziopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wa anthu onse.

Nʼchifukwa chake monga momwe moto umawonongera chiputu ndipo monga momwe udzu wowuma umapsera mʼmalawi a moto, momwemonso mizu yawo idzawola ndipo maluwa awo adzafota ndi kuwuluka ngati fumbi; chifukwa akana malamulo a Yehova Wamphamvuzonse, ndipo anyoza mawu a Woyerayo wa Israeli.

Yehova anati, “Pita ndipo ukawawuze anthu awa: “ ‘Kumva muzimva, koma osamvetsetsa; kupenya muzipenya koma osaona kanthu.’

kuti akalandireko mawu enieni ndi malangizo? Ngati anthuwo sayankhula monga mwa mawu awa, mwa iwo mulibe kuwala.

Yehova anandiwuza kuti, “Tsopano pita, ukalembe zimenezi mʼbuku iwo akuona ndipo lidzakhala ngati umboni wosatha masiku a mʼtsogolo. Amenewa ndi anthu owukira, onama ndi osafuna kumvera malangizo a Yehova. Iwo amawuza alosi kuti, ‘Musationerenso masomphenya!’ Ndipo amanena kwa mneneri kuti, ‘Musatinenerenso zoona,’ mutiwuze zotikomera, munenere za mʼmutu mwanu. Patukani pa njira ya Yehova, lekani kutsata njira ya Yehova; ndipo tisamvenso mawu a Woyerayo uja wa Israeli!” Nʼchifukwa chake Woyerayo wa Israeli akunena kuti, “Popeza inu mwakana uthenga uwu, mumakhulupirira zopondereza anzanu ndipo mumadalira kuchita zoyipa, choncho tchimo linalo lidzakhala ngati mingʼalu pa khoma lalitali ndi lopendama limene linagwa mwadzidzidzi ndi mwamsangamsanga.

Udzu umanyala ndipo maluwa amafota, koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”

Ndani wakhulupirira zimene tanenazi; kapena ndani amene Yehova wamuzindikiritsa mphamvu zake?

“Pakuti maganizo anga siwofanana ndi maganizo anu, ngakhale njira zanu si njira zanga,” akutero Yehova. “Monga momwe mlengalenga muli kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nʼzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.

Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.

Pamene mufuwula kupempha thandizo, mafano anu amene munasonkhanitsawo ndiyetu akupulumutseni! Mphepo idzanyamula mafano anu onsewo, mpweya chabe udzawulutsa mafanowo. Koma munthu amene amadalira ine adzalandira dziko lokhalamo. Phiri langa lopatulika lidzakhala lakelake.”

Yehova akuti, “Kunena za pangano lake ndi iwo, Mzimu wanga umene uli pa inu, ndiponso mawu anga amene ndayika mʼkamwa mwanu sadzachoka mʼkamwa mwanu, kapena kuchoka mʼkamwa mwa ana anu, kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zawo kuyambira tsopano mpaka kalekale,” akutero Yehova.

Kodi si manja anga amene anapanga zinthu zonsezi, motero zonsezi ndi zanga?” Akutero Yehova. “Koma munthu amene ndimakondwera naye ndi uyu: amene ali wodzichepetsa ndi wosweka mtima, ndipo amamvera mawu anga.

Inenso ndawasankhira chilango chowawa ndipo ndidzabweretsa pa iwo zimene amaziopa zija. Pakuti pamene ndinawayitana palibe amene anayankha, pamene ndinayankhula palibe amene anatchera khutu. Anachita zoyipa pamaso panga ndi kusankha kuchita zimene zimandinyansa zija.” Imvani mawu a Yehova, inu amene mumanjenjemera ndi mawu ake: “Abale anu amene amakudani, ndi kukuchotsani pakati pawo chifukwa cha dzina langa, amanena kuti, ‘Yehova alemekezeke kuti ife tione chimwemwe chanu!’ Koma ndi iwowo amene adzachite manyazi.

Inu Yehova, kodi suja mumafuna anthu onena zoona? Inu munawakantha anthuwo, koma sanamve kupweteka; munawaphwanya anthuwo, koma sanatengepo phunziro. Anawumitsa mitima yawo ngati mwala ndipo anakaniratu kulapa. Ndiye ndinati, “Awa ndi amphawi chabe; anthu ochita zopusa. Sadziwa njira ya Yehova, sazindikira zimene Mulungu wawo amafuna.

Imvani, inu anthu okhala pa dziko lapansi, ndikubweretsa masautso pa anthu awa. Zimenezi ndi mphotho ya ntchito zawo. Iwowa sanamvere mawu anga ndipo anakana lamulo langa.

koma ndinawalamula kuti: Mverani Ine, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata zonse zimene ndakulamulirani, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino. Koma anthuwo sanamvere kapena kulabadira; mʼmalo mwake anapitirira kusamvera ndi mitima yawo yoyipa. Iwo anabwerera mʼmbuyo mʼmalo mopita patsogolo.

Anthu anzeru achita manyazi; athedwa nzeru ndipo agwidwa. Iwo anakana mawu a Yehova. Nanga tsono nzeru zawo ziwapinduliranji?

Koma ngati simumvera, ndidzalira kwambiri chifukwa cha kunyada kwanu. Mʼmaso mwanga mwadzaza ndi misozi yowawa chifukwa nkhosa za Yehova zatengedwa ukapolo.

Munandiyankhula ndipo mawu anu ndinawalandira bwino. Mawu anu anandipatsa chimwemwe ndipo mtima wanga unasangalala. Paja ine, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndimadziwika ndi dzina lanu.

Yehova akuti, “Ndi wotembereredwa munthu amene amadalira munthu mnzake, amene amatsamira pa munthu mnzake kuti amuthandize pamene mtima wake wafulatira Yehova.

Komatu iwo sanandimvere kapena kulabadira. Ndi mitima yawo yowumayo sanamvere kapena kulandira malangizo anga.

“Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Tamverani! Ine ndidzabweretsa masautso amene ndinanena aja pa mzinda uno ndi pa mizinda yozungulira, chifukwa anthu ake ndi nkhutukumve ndipo sanamvere mawu anga.’ ”

Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Musamvere zimene aneneri amenewa akulosera kwa inu; zomwe aloserazo nʼzachabechabe. Iwo akungoyankhula za masomphenya a mʼmitima mwawo basi, osati zochokera kwa Yehova.

Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova.

Ndipo ngakhale Yehova kawirikawiri wakhala akukutumizirani atumiki ake onse, aneneri, inuyo simunamvere kapena kutchera khutu.

Ukawawuze kuti, ‘Yehova akuti: Ngati simundimvera Ine ndi kuleka kutsatira malamulo anga, amene ndakupatsani, ndipo ngati simumvera mawu a atumiki anga, aneneri amene ndakhala ndikukutumizirani, ngakhale kuti simunawamvere, ndiye kuti Ine ndidzasandutsa Nyumba ino kukhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.’ ”

Tsopano konzani njira zanu ndi zochita zanu ndipo mverani Yehova Mulungu wanu. Mukatero ndiye kuti Yehova adzaleka osakupatsani chilango chimene ankati akupatseni.

Inde, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, “Musalole kuti aneneri ndi owombeza amene ali pakati panu akunyengeni. Musamvere maloto awo. Iwo akunenera zabodza kwa inu mʼdzina langa ngakhale Ine sindinawatume,” akutero Yehova.

“Masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzachita pangano latsopano ndi Aisraeli ndiponso nyumba ya Yuda. Silidzakhala ngati pangano limene ndinachita ndi makolo awo pamene ndinawagwira padzanja nʼkuwatulutsa ku Igupto; chifukwa anaphwanya pangano langa, ngakhale ndinali mwamuna wawo,” akutero Yehova. “Ili ndi pangano limene ndidzachita ndi Aisraeli atapita masiku amenewo,” akutero Yehova. “Ndidzayika lamulo langa mʼmitima mwawo ndi kulilemba mʼmaganizo mwawo. Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga. Sipadzafunikanso kuti wina aphunzitse mnzake, kapena munthu wina kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, ‘Mudziwe Yehova,’ chifukwa onse adzandidziwa Ine, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,” akutero Yehova. “Ndidzawakhululukira zoyipa zawo ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”

“Komabe inu mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Tamvani tsono inu Aisraeli: Kodi zochita zanga ndizo zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene ndi zosalungama?

Ansembe aziphunzitsa anthu anga kusiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba, ndiponso pakati pa zinthu zoyenera ndi zosayenera kuperekedwa nsembe.

Anthu anga akuwonongeka chifukwa chosadziwa. “Pakuti mwakana kudziwa, Inenso ndidzakukanani monga ansembe anga; chifukwa mwayiwala lamulo la Mulungu wanu, Inenso ndidzayiwala ana anu.

Tsoka kwa iwo, chifukwa andisiya Ine! Chiwonongeko kwa iwo, chifukwa andiwukira! Ndimafunitsitsa kuwapulumutsa koma amayankhula za Ine monama.

“Nthawi ikubwera,” Ambuye Yehova akunena kuti, “Ndidzagwetsa njala mʼdziko lonse; osati njala ya chakudya kapena ludzu la madzi, koma njala yofuna kumva mawu a Yehova.

“Koma makolo anu anakana kumvera uthenga umenewu; anawumitsa mtima nandifulatira, natseka makutu awo kuti asamve. Anawumitsa mitima yawo ngati mwala wa sangalabwi ndipo sanamvere lamulo kapena mawu amene Yehova Wamphamvuzonse anawatumiza mwa Mzimu wake kudzera mwa aneneri oyamba aja. Kotero Yehova Wamphamvuzonse anakwiya kwambiri. “ ‘Pamene ndinawayitana, iwo sanamvere; choncho pamene iwo anandiyitana, Ine sindinamverenso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.

Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ ”

“Musaganize kuti ndinadza kudzathetsa malamulo kapena zonena za aneneri; sindinabwere kudzathetsa koma kukwaniritsa. Ine ndikukuwuzani zoonadi kuti, kufikira kutha kwa thambo ndi dziko lapansi, chilichonse chimene chinalembedwa mʼmalamulo, ngakhale kalemba kakangʼonongʼono, chidzakwaniritsidwa. Chifukwa chake aliyense amene aphwanya limodzi la malamulowa ngakhale lalingʼonongʼono ndi kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, adzakhala wotsirizira mu ufumu wakumwamba, koma aliyense amene achita ndi kuphunzitsa malamulo awa adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba.

“Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri. Pakuti pena adzamuda mmodzi ndi kukonda winayo kapena adzagwira ntchito mokhulupirika kwa mmodzi, nadzanyoza winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma pa nthawi imodzi.

“Lowani pa chipata chopapatiza. Pakuti chipata cholowera kuchiwonongeko nʼchachikulu ndipo msewu wake ndi waukulunso. Ndipo anthu ambiri amalowera pamenepo. Koma chipata ndi chopapatiza ndi msewu ndi waungʼono umene utsogolera anthu ku moyo wosatha ndipo ndi owerengeka okha amene ayipeza njirayo.

“Si munthu aliyense amene amanena kwa Ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowe mu ufumu wakumwamba, koma ndi yekhayo amene amachita chifuniro cha Atate anga amene ali kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine pa tsikulo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinkanenera mʼdzina lanu ndi mʼdzina lanunso tinkatulutsa ziwanda ndi kuchita zodabwitsa zambiri?’ Pamenepo ndidzawawuza momveka bwino kuti, ‘Sindinakudziweni inu. Chokani kwa Ine, inu ochita zoyipa!’

“Nʼchifukwa chake aliyense amene amva mawu anga ndi kuwachita akufanana ndi munthu wanzeru amene anamanga nyumba yake pa thanthwe. Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo; koma sinagwe, chifukwa maziko ake anali pa thanthwe. Koma aliyense amene amva mawu angawa ndi kusawachita ali ngati munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pa mchenga. Mvula inagwa, mitsinje inadzaza, ndi mphepo zinawomba pa nyumbayo, ndipo inagwa ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.”

Ngati wina aliyense sakakulandirani kapena sakamvera mawu anu, musase fumbi la kumapazi anu pamene mutuluka mʼnyumbayo kapena mu mzindawo. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku lachiweruziro, mlandu wa Sodomu ndi Gomora udzachepa kusiyana ndi wa mzindawo.

“Aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzavomereza pamaso pa Atate anga akumwamba. Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamukana pamaso pa Atate anga akumwamba.

“Aliyense amene akonda abambo kapena amayi ake koposa Ine sayenera kukhala wanga; aliyense amene akonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine sayenera kukhala wanga. Aliyense amene satenga mtanda wake ndi kunditsata Ine sayenera kukhala wanga. Aliyense amene asunga moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo chifukwa cha Ine adzawupeza. “Iye amene alandira inu alandira Ine, ndipo amene alandira Ine alandiranso amene anandituma Ine.

Iye anayankha kuti, “Nzeru zakudziwa zinsinsi za ufumu wakumwamba zapatsidwa kwa inu koma osati kwa iwo.

Ichi ndi chifukwa chake ndimayankhula kwa iwo mʼmafanizo: “Ngakhale akupenya koma saona, ngakhale akumva koma samvetsetsa kapena kuzindikira. Mwa iwo zimene ananenera Yesaya zikwaniritsidwa: “ ‘Kumva mudzamva koma osamvetsetsa. Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu. Pakuti mtima wa anthu awa ndi wokanika, mʼmakutu mwawo ndi mogontha, ndipo atsinzina kuti asaone kanthu. Mwina angapenye ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka, Ineyo nʼkuwachiritsa.’ Koma maso anu ndi odala chifukwa amapenya ndi makutu anu chifukwa amamva. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama anafuna kuona zimene inu mukupenya koma sanazione ndi kumva zimene inu mukumva koma sanazimve. “Tamverani tsono zimene fanizo la wofesa litanthauza: Pamene aliyense akumva uthenga wa ufumu koma sawuzindikira, woyipayo amabwera ndi kuchotsa zimene zafesedwa mu mtima mwake. Iyi ndi mbewu yofesedwa mʼmbali mwa njira. Zimene zinafesedwa pa malo amiyala ndi munthu amene amamva mawu ndi kuwalandira msanga ndi chimwemwe. Koma popeza alibe muzu, iwo amakhala nthawi yochepa. Pamene vuto kapena zunzo libwera chifukwa cha mawu, iye amagwa mofulumira. Zimene zinafesedwa pakati pa minga, ndi munthu amene amamva mawu koma nkhawa za moyo uno ndi chinyengo cha chuma zimalepheretsa mawuwo kuti abale chipatso. Koma zimene zinafesedwa pa nthaka yabwino, ndi munthu amene amamva mawu ndipo amawazindikira. Iye amabala zipatso zokwanira 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa.”

Iye anayankha kuti, “Mbewu iliyonse imene Atate anga akumwamba sanadzale idzazulidwa ndi mizu yomwe.

Yesu anayankha kuti, “Inu mukulakwitsa chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu ya Mulungu.

Yesu anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse. Ili ndi lamulo loyamba ndi loposa onse. Ndipo lachiwiri ndi lofanana nalo: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’ Malamulo onse ndi aneneri zakhazikika pa malamulo awiriwa.”

Ndipo uthenga wa ufumu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi ngati umboni kwa mitundu yonse, ndipo pomwepo chimaliziro chidzafika.”

Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”

Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine.

Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati, “Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”

Iye anawawuza kuti, “Chinsinsi cha ufumu wa Mulungu chapatsidwa kwa inu. Koma kwa amene ali kunja zinthu zonse zinenedwa mʼmafanizo: kotero kuti, “ ‘Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu, kumva mudzamva koma osamvetsetsa, kuti mwina angatembenuke ndi kukhululukidwa!’ ” Pamenepo Yesu anawawuza kuti, “Kodi simukulimvetsa fanizoli? Kodi nanga mudzazindikira bwanji fanizo lina lililonse? Wofesa amafesa mawu. Anthu ena ali ngati mbewu za mʼmbali mwa njira, mʼmene mawu amafesedwamo. Akangowamva, Satana amabwera ndi kuchotsa mawu amene anafesedwa mwa iwo. Ena, monga mbewu zofesedwa pa miyala, amamva mawu ndipo nthawi yomweyo amawalandira ndi chimwemwe. Koma popeza alibe mizu, amakhala kwa kanthawi kochepa. Mavuto kapena masautso akafika chifukwa cha mawu, amagwa mofulumira. Komabe ena, monga mbewu zofesedwa pakati pa minga, amamva mawu; koma nkhawa zamoyo uno, chinyengo cha chuma ndi zokhumba za zinthu zina zimabwera ndi kutchinga mawu, ndipo amawachititsa kukhala osabala chipatso. Ena, ngati mbewu zofesedwa pa nthaka yabwino, amamva mawu, nawalandira, ndi kubereka zipatso zokwanira makumi atatu, makumi asanu ndi limodzi, kapena ngakhale 100 kuwonjezera pa zomwe zinafesedwa.”

Posasamala zomwe ananena, Yesu anamuwuza mkulu wa sunagoge uja kuti, “Usachite mantha; ingokhulupirira.”

Potero mumachepetsa mawu a Mulungu kukhala wopanda mphamvu ndi miyambo yanu imene mumapatsirana. Ndipo mumachita zinthu zina zambiri monga zimenezi.”

Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata. Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa. Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake? Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”

Yesu anawafunsa kuti, “Kodi si pamenepa nanga pomwe mumalakwira chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu za Mulungu?

Ndipo Uthenga Wabwino uyenera kuyamba walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.

Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”

Anati kwa iwo, “Pitani mʼdziko lonse lapansi ndipo mukalalikire Uthenga Wabwino kwa zolengedwa zonse. Aliyense amene akakhulupirire nabatizidwa adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira adzalangidwa.

Pamenepo ophunzira aja anapita ndi kukalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo anatsimikizira mawuwo ndi zizindikiro zimene ankachita.

kotero kuti malingaliro a mitima ya ambiri adzawululidwa. Ndipo lupanga lidzabaya moyo wakonso.”

Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa: ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha.’ ”

Iwo anadabwa ndi chiphunzitso chake chifukwa uthenga wake unali ndi ulamuliro.

“Kodi nʼchifukwa chiyani munditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye’ koma simuchita zimene Ine ndinena? Ine ndidzakuonetsani mmene alili munthu amene amabwera kwa Ine ndi kumva mawu anga ndi kuwachita. Iye ali ngati munthu womanga nyumba, amene anakumba mozama nayika maziko ake pa mwala. Madzi osefukira atabwera ndi mphamvu, nawomba nyumbayo koma sinagwedezeka, chifukwa anayimanga bwino. Koma amene amamva mawu anga koma osawachita, akufanana ndi munthu amene anamanga nyumba yake koma yopanda maziko. Nthawi yomwe madziwo anawomba nyumbayo, inagwa ndipo inawonongekeratu.”

Iye anati, “Kudziwa zinsinsi za ufumu wa Mulungu kwapatsidwa kwa inu, koma kwa ena ndimawayankhula mʼmafanizo kuti, “ngakhale akuona, asapenye; ngakhale akumva, asazindikire.” “Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbewu ndi mawu a Mulungu. Mbewu za mʼmbali mwa njira ndi anthu amene amamva mawu, ndipo kenaka mdierekezi amabwera ndi kuchotsa mawuwo mʼmitima mwawo kuti asakhulupirire ndi kupulumutsidwa. Mbewu za pa thanthwe ndi anthu amene amalandira mawu mwachimwemwe pamene akumva, koma mawuwo sazika mizu. Iwo amakhulupirira kwa kanthawi, koma pa nthawi ya mayesero, amagwa. Mbewu zimene zinagwa pakati pa minga zikuyimira anthu amene amamva mawu, koma akamayenda mʼnjira zawo amatsamwitsidwa ndi zodandaulitsa za moyo uno, chuma ndi zosangalatsa, ndipo iwo samakhwima. Koma mbewu za pa nthaka yabwino zikuyimira anthu amene ali ndi mtima woona ndi wabwino, amene amamva mawu nawasunga, ndipo amalimbikira mpaka amabala zipatso.

Yesu anayankha kuti, “Amayi ndi abale anga ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kumachita zimene mawuwo akunena.”

Ndipo Iye anawuza onse kuti, “Ngati wina aliyense akufuna kutsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kusenza mtanda wake tsiku ndi tsiku nʼkumanditsata Ine. Popeza aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene adzataya moyo wake chifukwa cha Ine adzawupulumutsa. Kodi chabwino ndi chiti kwa munthu, kupata zonse zapansi pano, koma ndi kutaya moyo wake kapena kudziwononga iye mwini? Ngati wina aliyense achita nane manyazi ndi ndiponso mawu anga, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wake ndi mu ulemerero wa Atate ndi angelo oyera.

Iye anati kwa wina, “Nditsate Ine.” Koma munthuyo anayankha kuti, “Ambuye, choyamba loleni ndipite kuti ndikayike maliro a abambo anga.” Yesu anati kwa iye, “Aleke akufa ayikane akufa okhaokha, koma iwe pita ukalalikire ufumu wa Mulungu.” Koma winanso anati, “Ine ndidzakutsatani Ambuye; koma choyamba ndiloleni ndibwerere kuti ndikatsanzikane nalo banja langa.” Yesu anayankha kuti, “Munthu amene akulima ndi khasu lokokedwa nʼkumayangʼana mʼmbuyo, si woyenera kugwira ntchito mu ufumu wa Mulungu.”

Koma Yesu anayankha kuti, “Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.”

Wina anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndi anthu ochepa okha amene adzapulumutsidwe?” Iye anawawuza kuti, “Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza, chifukwa ndikukuwuzani kuti ambiri adzafuna kulowa koma sadzatha kutero.

“Ngati wina aliyense abwera kwa Ine ndipo sadana ndi abambo ndi amayi ake, mkazi wake ndi ana, abale ake ndi alongo ake, inde ngakhale moyo wake omwe, iye sangakhale ophunzira wanga. Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake ndi kunditsata Ine sangakhale ophunzira wanga.

“Malamulo ndi Aneneri zinagwira ntchito mpaka nthawi ya Yohane. Kuyambira nthawi imeneyo, Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ukulalikidwa, ndipo aliyense akuyesetsa mwamphamvu kuti alowemo. Nʼkwapafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke kulekana ndi kuti kalemba kakangʼono kachoke mʼMalamulo.

“Abrahamu anayankha kuti, ‘Ali ndi Mose ndi Aneneri; aleke amvere iwo.’ “Iye anati, ‘Ayi, bambo Abrahamu, koma ngati wina ochokera kwa akufa adzapita kwa iwo, adzatembenuka mtima.’ “Anati kwa iye, ‘Ngati iwo samvera Mose ndi Aneneri, sadzakhulupirira ngakhale wina atauka kwa akufa.’ ”

Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”

Iye anawawuza kuti, “Inu ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zimene aneneri ananena!

Ndipo kuyambira ndi Mose ndi aneneri onse Iye anawafotokozera zimene zinalembedwa mʼmalemba wonse zokhudzana ndi Iye mwini.

Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene ndinakuwuzani pamene ndinali nanu: chilichonse chiyenera kukwaniritsidwa chimene chinalembedwa cha Ine mʼbuku la Malamulo a Mose, Aneneri ndi Masalimo.” Kenaka anawatsekula maganizo kuti azindikire Malemba.

Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu.

Pakuti lamulo linapatsidwa kudzera mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinabwera kudzera mwa Yesu Khristu.

Iye ataukitsidwa kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira zimene Iye ananena ndipo anakhulupirira Malemba ndi mawu amene Yesu anayankhula.

Ine ndikuyankhula kwa iwe zinthu za dziko lapansi ndipo sukukhulupirira. Nanga kodi udzakhulupirira bwanji ngati nditayankhula zinthu zakumwamba?

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi. Aliyense wokhulupirira Iye saweruzidwa, koma aliyense wosakhulupirira waweruzidwa kale chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.

Pakuti amene Mulungu wamutuma amayankhula mawu a Mulungu; Mulungu wamupatsa Mzimu Woyera mopanda malire.

Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.”

Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi.”

“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo.

kapena mawu ake kukhala mwa inu, pakuti simukhulupirira Iye amene anamutuma. Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni.

Mzimu Woyera apereka moyo, thupi silipindula kanthu. Mawu amene ndayankhula kwa inu ndiwo mzimu ndipo ndi moyo.

Ine ndinakuwuzani kuti mudzafera mʼmachimo anu ngati simukhulupirira kuti Ine Ndine. Ndithu inu mudzafera mʼmachimo anu.”

Kwa Ayuda amene anamukhulupirira, Yesu anati, “Ngati inu mutsatira chiphunzitso changa, ndithu ndinu ophunzira anga. Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”

Nʼchifukwa chiyani simukumvetsetsa mawu anga? Chifukwa chake nʼchakuti simungathe kumva zoyankhula zanga. Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza. Koma chifukwa ndikuwuzani choonadi, inu simukundikhulupirira Ine! Ndani mwa inu angatsimikize kuti ndine wochimwa? Ngati Ine ndikunena choonadi, nʼchifukwa chiyani simukundikhulupirira? Munthu wochokera kwa Mulungu amamva zimene Mulungu amanena. Chifukwa chimene simumvera nʼchakuti, inuyo sindinu ochokera kwa Mulungu.”

Ine ndikukuwuzani choonadi, munthu akasunga mawu anga, sadzafa konse.”

koma inu simukhulupirira chifukwa simuli a gulu lankhosa zanga. Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine.

Ngati anawatcha milungu anthu amene analandira mawu a Mulungu, pajatu Malemba sangasweke,

Munthu amene amakonda moyo wake adzawutaya, pamene munthu amene amadana ndi moyo wake mʼdziko lino lapansi adzawusungira ku moyo wosatha. Aliyense amene atumikira Ine ayenera kunditsata; ndipo kumene Ine ndili, wotumikira wanga adzakhalanso komweko. Atate anga adzalemekeza amene atumikira Ine.

Ngakhale Yesu anachita zizindikiro zodabwitsa zonsezi pamaso pawo, sanamukhulupirirebe. Izi zinakwaniritsa mawu a mneneri Yesaya kuti: “Ambuye, wakhulupirira uthenga wathu ndani, ndipo ndi kwa yani komwe mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa?” Pa chifukwa cha ichi iwo sanakhulupirire, chifukwa Yesaya ananenanso kuti: “Iye wachititsa khungu maso awo ndi kuwumitsa mitima yawo, kotero kuti iwo sangathe kuona ndi maso awo, kapena kuzindikira ndi mitima yawo, kapena kutembenuka kuti Ine ndikanawachiza.” Yesaya ananena izi chifukwa anaona ulemerero wa Yesu ndi kuyankhula za Iye. Komabe pa nthawi yomweyi ambiri ngakhale atsogoleri anakhulupirira Iye. Koma chifukwa cha Afarisi iwo sanavomereze chikhulupiriro chawo chifukwa amaopa kuti angawatulutse mʼsunagoge; pakuti iwo amakonda kuyamikiridwa ndi anthu kuposa kuyamikiridwa ndi Mulungu.

Iye amene akana Ine ndipo salandira mawu anga ali ndi womuweruza. Tsiku lomaliza mawu amene ndiyankhulawa adzamutsutsa.

Pakuti Ine sindiyankhula mwa Ine ndekha, koma Atate amene anandituma amandilamulira choti ndinene ndi momwe ndinenere. Ine ndikudziwa kuti lamulo lake ndi moyo wosatha. Choncho chilichonse chimene Ine ndinena ndi chimene Atate andiwuza.”

Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine.

“Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga.

Iye amene amadziwa malamulo anga ndi kuwasunga ndiye amene amandikonda. Wokonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga ndipo Inenso ndidzamukonda ndikudzionetsa ndekha kwa iye.”

Yesu anamuyankha kuti, “Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye. Iye amene sandikonda Ine sasunga mawu anga. Mawu awa amene mukumva si anga ndi a Atate amene anandituma Ine.

Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa.

Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera.

Ine ndawapatsa mawu anu ndipo dziko lapansi likudana nawo, pakuti sali a dziko lapansi monga Ine sindilinso wa dziko lapansi.

Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi.

Pilato anati, “Kani ndiwe mfumu!” Yesu anayankha kuti, “Inu mwalondola ponena kuti, Ine ndine mfumu. Kunena zoona, Ine ndinabadwa chifukwa cha chimenechi, ndipo nʼchifukwa chake ndinabwera mʼdziko lapansi, kudzachitira umboni choonadi. Aliyense amene ali mbali yachoonadi amamvera mawu anga.”

Petro ndi atumwi enawo anayankha kuti, “Ife tiyenera kumvera Mulungu osati anthu!

Ndipo Paulo ndi Barnaba anawayankha molimba mtima kuti, “Ife tinayenera kuyankhula Mawu a Mulungu kwa inu poyamba. Popeza inu mwawakana ndi kudziyesa nokha osayenera moyo wosatha, ife tsopano tikupita kwa anthu a mitundu ina.

Tsopano anthu a ku Bereya anali akhalidwe labwino kusiyana ndi Atesalonika, pakuti iwo analandira mawu ndi chidwi chachikulu ndipo ankasanthula Malemba tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zimene ankanena Paulozo zinali zoona.

Koma ena anawumitsa mitima; anakana kukhulupirira ndipo ananyoza Njirayo pa gulu la anthu. Kotero Paulo anawasiya. Iye anatenga ophunzirawo ndipo amakambirana tsiku ndi tsiku mʼsukulu ya Turano.

Ndikudziwa kuti ndikachoka ine, padzafika mimbulu yolusa pakati panu imene sidzalekerera gulu lankhosalo. Ngakhale pakati pa inu nokha padzapezeka anthu oyankhula zonama ndi cholinga chofuna kukhala ndi ophunzira kuti awatsate. Tsono inu, samalani! Kumbukirani kuti kwa zaka zitatu, usana ndi usiku ndiponso ndi misozi sindinaleke kuchenjeza aliyense wa inu.

“Pita kwa anthu awa ndi kuwawuza kuti, ‘Kumva mudzamva, koma osamvetsetsa; kupenya mudzapenya, koma osaona kanthu.’ Pakuti mtima wa anthu ndi wokanika; mʼmakutu mwawo ndi mogontha, ndipo atsinzina kuti asaone kanthu. Mwina angapenye ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka, Ineyo nʼkuwachiritsa.

Ndine Paulo, mtumiki wa Khristu Yesu, woyitanidwa ndi Mulungu kukhala mtumwi. Ndinapatulidwa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Mulungu umene analonjeza kale mʼMalemba Oyera kudzera mwa aneneri ake.

Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino chifukwa ndiwo mphamvu za Mulungu zopulumutsa aliyense amene akhulupirira, poyamba Myuda, kenaka Mhelene. Pakuti mu Uthenga Wabwino anawulula kuti chilungamo chimachokera kwa Mulungu. Kuyambira pachiyambi mpaka potsiriza ndi chilungamo chobwera mwachikhulupiriro, monga kwalembedwera kuti, “Wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.” Mkwiyo wa Mulungu ukuonekera kuchokera kumwamba. Ukutsutsana ndi kusapembedza konse ndi kuyipa kwa anthu amene amapondereza choonadi mwa chikhalidwe chawo choyipa. Za Mulungu zimene zingathe kudziwika, ndi zomveka bwino kwa iwo pakuti Mulungu anazionetsera kwa iwo. Pakuti kuyambira pamene dziko lapansi linalengedwa, zinthu zosaoneka za Mulungu, mphamvu zake zosatha ndi chikhalidwe cha umulungu, zakhala zikuoneka bwinobwino. Akhala akuzindikira poona zimene Mulungu analenga, kotero kuti anthu sangathe kuwiringula. Ngakhale iwo anadziwa Mulungu, sanamulemekeze ngati Mulungu kapena kumuthokoza, koma maganizo awo anasanduka wopanda pake ndipo mʼmitima yawo yopusa munadzaza mdima. Ngakhale ankadzitama kuti ndi anzeru, anasanduka opusa.

Nanga kodi pali ubwino wotani pokhala Myuda, kapena muli ubwino wanjinso mu mdulidwe? Ubwino wake ndi wambiri mʼnjira zonse! Choyambirira iwo anapatsidwa Mawu a Mulungu kuti awasunge. Nanga zili bwanji ngati ena analibe chikhulupiriro? Kodi kupanda chikhulupiriro kwawo kukanalepheretsa kukhulupirika kwa Mulungu? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Mulungu akhale woona, ndi munthu aliyense akhale wonama. Monga kwalembedwa kuti, “Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama pamene muyankhula ndi kupambana pamene muweruza.”

Monga kwalembedwa kuti, “Palibe munthu wolungama, inde palibe ndi mmodzi yemwe. Palibe ndi mmodzi yemwe amene amazindikira, palibe amene amafunafuna Mulungu.

Kodi tsono ife, tikutaya Malamulo pamene tikunena kuti pafunika chikhulupiriro? Ayi. Mʼnjira iliyonse ayi! Komatu ife tikukwaniritsadi Malamulo.

Koma tsopano tamasulidwa ku Malamulowo pakuti tinafa ku zimene zinkatimanga, ndipo Mzimu Woyera akutithandiza kutumikira Mulungu mʼnjira yatsopano ndipo osati mʼnjira yakale yolembedwa.

Choncho lamulo ndi loyera, lolungama ndi labwino.

Atamandike Mulungu, amene amandipulumutsa kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye athu! Kotero tsono, ineyo ndi mtima wanga ndimatumikira lamulo la Mulungu, koma ndi thupi langa ndimatumikira lamulo la uchimo.

Pakuti mtima umene wakhazikika pa zathupi ndi wodana ndi Mulungu. Sunagonjere lamulo la Mulungu ndipo sungathe kutero.

Ndipo iwo adzalalikira bwanji osatumidwa? Kwalembedwa kuti, “Akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga Wabwino!” Koma si onse amene anavomereza Uthenga Wabwino. Pakuti Yesaya akuti, “Ambuye, ndani amene wakhulupirira uthenga wathu?” Motero, chikhulupiriro chimabwera pamene timva uthenga ndipo uthenga umamveka kuchokera ku mawu a Khristu.

monga kwalembedwa kuti, “Mulungu anawapatsa mzimu wosatha kumvetsa zinthu, maso osatha kupenya; makutu osatha kumva mpaka lero lino.”

Pakuti zilizonse zimene zinalembedwa kale zinalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembawo amatilimbikitsa kupirira kuti tikhale ndi chiyembekezo.

Abale, ine ndikukupemphani kuti musamale chifukwa cha amene ayambitsa mipatuko ndi kuyika zokhumudwitsa panjira yanu, motsutsana ndi chiphunzitso chimene mwachiphunzira. Muwapewe iwo. Pakuti otero sakutumikira Ambuye athu Khristu koma zilakolako zawo. Ndi mawu okoma ndi oshashalika iwo amanamiza anthu osalakwa.

Pakuti uthenga wa mtanda ndi chopusa kwa iwo amene akuwonongeka, koma kwa ife amene tikupulumutsidwa uthengawu ndi mphamvu ya Mulungu.

Komabe ife timayankhula uthenga wa nzeru kwa okhwima, koma osati ndi nzeru ya mʼbado uno kapena ya olamula a mʼbado uno, amene mphamvu yawo ikutha. Ayi, ife timayankhula za nzeru yobisika ya Mulungu, nzeru imene inabisidwa ndipo imene Mulungu anatikonzera mu ulemerero wathu isanayambe nthawi.

Izi ndi zimene timayankhula osati mʼmawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma mʼmawu wophunzitsidwa ndi Mzimu, kufotokozera zoonadi zauzimu mʼmawu auzimu. Munthu wopanda Mzimu savomereza zinthu zimene zichokera kwa Mzimu wa Mulungu, popeza ndi zopusa kwa iyeyo, ndipo sangazimvetsetse chifukwa zimazindikirika mwa Mzimu. Munthu wauzimu amaweruza pa zinthu zonse, koma iye mwini saweruzidwa ndi munthu aliyense.

Mdulidwe si kanthu, kusachita mdulidwe si kanthunso. Chofunika nʼkusunga malamulo a Mulungu.

Tsono abale, ndikufuna ndikukumbutseni za Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani. Munawulandira ndipo munawukhulupirira kolimba. Inu munapulumutsidwa ndi Uthenga Wabwinowu, ngati mwasunga mawu amene ndinakulalikirani. Kupanda kutero, mwangokhulupirira pachabe.

Ngati wina sakonda Ambuye akhale wotembereredwa. Maranatha! (Ambuye athu bwerani)!

Pakuti kwa Mulungu ndife fungo labwino la Khristu pakati pa iwo amene akupulumutsidwa ndi amene akuwonongeka. Kwa amene akuwonongeka ndife fungo la imfa, limawapha. Ndipo kwa amene akupulumuka ndife fungo lamoyo, limawapatsa moyo. Ndani angayithe ntchito yotereyi?

Iye watipatsa kulimba mtima kuti tikhale atumiki a pangano latsopano, osati malamulo olembedwa koma a Mzimu; pakuti malamulo olembedwa amapha koma Mzimu amapereka moyo. Koma ngati utumiki umene unabweretsa imfa uja, wolembedwa ndi malemba pa mwalawu, unabwera ndi ulemerero mwakuti Aisraeli sanathe kuyangʼanitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha ulemerero wa pa nkhopeyo, ngakhale kuti unali kunka nuzilala, kodi nanga utumiki wa Mzimu sudzaposa apa? Ngati utumiki umene umatsutsa anthu unali ndi ulemerero, nanga koposa kotani ulemerero wa utumiki wobweretsa chilungamo!

Koma ife takaniratu njira zonse zachinsinsi ndi zochititsa manyazi. Sitichita kanthu mwachinyengo kapena mopotoza Mawu a Mulungu. Mʼmalo mwake, timayankhula choonadi poyera pamaso pa Mulungu, kufuna kuti aliyense ativomereze mu mtima mwake. Koma ngakhale uthenga wathu wabwino utakhala wophimbika, ndi wophimbika kwa okhawo amene akutayika. Mulungu wa dziko lapansi anachititsa khungu anthu osakhulupirira, kuti asathe kuona kuwala kwa Uthenga Wabwino umene umaonetsa ulemerero wa Khristu, amene ndi chifaniziro cha Mulungu.

Koma ndikuopa kuti monga Hava ananyengedwa ndi kuchenjera kwa njoka, mitima yanunso ingasocheretsedwe kuleka nʼkudzipereka moona mtima ndi modzipereka kwenikweni kwa Khristu.

Pakuti anthu oterewa ndi atumwi onama, antchito achinyengo, odzizimbayitsa ngati atumwi a Khristu. Sizododometsa zimenezi, pakuti Satana mwini amadzizimbayitsa kuoneka ngati mngelo wowunikira anthu.

Pakuti sitingachite chilichonse chotsutsana ndi choonadi, koma chokhacho chovomerezana ndi choonadi.

Ine ndikudabwa kuti mukusiya mwamsangamsanga chotere Mulungu amene anakuyitanani mwachisomo cha Khristu ndipo mwatembenuka ndi kutsatira uthenga wina wosiyana, umene si Uthenga Wabwino konse. Pali anthu ena amene akukusokonezani komanso akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wa Khristu. Ngakhale ife kapena mngelo wochokera kumwamba, akalalikira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene tinakulalikirani uja, iyeyo akhale wotembereredwa! Monga tanena kale, tsopano ndikubwereza kunenanso kuti, “Ngati wina aliyense akulalikirani Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene munawulandira, iyeyo akhale wotembereredwa.”

Ife sitinawagonjere ndi pangʼono pomwe, nʼcholinga chakuti choonadi cha Uthenga Wabwino chikhalebe ndi ife.

Onse amene amadalira ntchito za lamulo ndi otembereredwa, pakuti zalembedwa mʼBuku la Malamulo kuti, “Ndi wotembereredwa aliyense amene sachita zonse zimene zalembedwa mʼBuku la Malamulo.”

Khristu anatiwombola ku temberero la lamulo pokhala temberero mʼmalo mwathu, pakuti analemba kuti, “Aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa.” Iye anatiwombola ife ndi cholinga chakuti madalitso woperekedwa kwa Abrahamu abwere kwa anthu a mitundu ina kudzera mwa Khristu Yesu, kuti ndi chikhulupiriro tilandire lonjezo la Mzimu.

Malonjezo awa anaperekedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Malemba sakunena kuti, “kwa mbewu zake,” kutanthauza anthu ambiri, koma, “kwa mbewu yako,” kutanthauza munthu mmodzi, amene ndi Khristu.

Choncho lamulo linayikidwa kukhala lotiyangʼanira kuti lititsogolere kwa Khristu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro.

Kodi tsopano ine ndasanduka mdani wanu chifukwa ndakuwuzani choonadi?

Ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate a ulemerero akupatseni mzimu wa nzeru ndi wa vumbulutso, kuti mumudziwe kwenikweni. Ndimapempheranso kuti maso a mitima yanu atsekuke ndi cholinga choti mudziwe chiyembekezo chimene Iye anakuyitanirani, chuma cha ulemerero chomwe chili mwa anthu oyera mtima.

Motero sitidzakhalanso makanda, ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso ndi kuchenjera kwa anthu achinyengo amene amasocheretsa anthu ndi kuchenjera kwawo.

kuti awupatule ukhale oyera, atawuyeretsa powusambitsa ndi madzi omwe ndi mawu ake.

Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu.

Ndipo pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chipitirire kukulirakulira pa chidziwitso ndi kuzama mʼmaganizo, kuti mukhoza kuzindikira chabwino koposa zonse ndi chiti kuti muthe kukhala wopanda chodetsa ndi wopanda chilema kufikira tsiku la Khristu.

powawuza mawu amoyo. Ndipo ine ndidzatha kunyadira pa tsiku la Khristu kuti sindinathamange kapena kugwira ntchito pachabe.

ngati mupitirirabe kukhala mʼchikhulupiriro chanu, okhazikika ndi olimba, osasunthidwa kuchoka pa chiyembekezo chimene munachigwira mu Uthenga Wabwino. Uwu ndi Uthenga Wabwino umene munawumva, umene wakhala ukulalikidwa kwa olengedwa onse a pansi pa thambo, ndi umenenso, ine Paulo ndinakhala mtumiki wake.

Musalole kuti wina aliyense akutengeni ukapolo ndi mʼnzeru zachinyengo zolongosola zinthu zozama, zomwe zimachokera ku miyambo ya anthu ndi ku maganizo awo okhudza za dziko lapansi osati kwa Khristu.

Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende.

Inu mwakhala otitsatira athu ndi a Ambuye; ngakhale kuti panali masautso akulu, munalandira uthenga mwachimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera.

Monga mukudziwa, ife nʼkuti titazunzika ndi kunyozedwa ku Filipi. Koma mothandizidwa ndi Mulungu wathu, tinalimba mtima mpaka kukulalikirani uthenga wake wabwino ngakhale ambiri ankatsutsana nafe.

Ndipo ifenso tikuyamika Mulungu kosalekeza chifukwa mutalandira Mawu a Mulungu, amene munawamva kuchokera kwa ife, munawalandira osati ngati mawu a anthu, koma monga momwe alili, Mawu a Mulungu, amene akugwira ntchito mwa inu amene mukhulupirira.

ndikukupatsani mpumulo amene mukusautsidwa, pamodzi ndi ifenso. Izi zidzachitika Ambuye Yesu akadzaoneka mʼmalawi amoto kuchokera kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu. Iye adzalanga amene sadziwa Mulungu ndi amene samvera Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu. Adzalangidwa ndi chiwonongeko chamuyaya ndipo sadzaonanso nkhope ya Ambuye ndi ulemerero wamphamvu zake

Ndipo kenaka woyipitsitsayo adzaonekera, amene Ambuye Yesu adzamugonjetsa ndi mpweya otuluka mʼkamwa mwake ndi kumuwononga ndi ulemerero wa kubwera kwake. Woyipitsitsayo adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzaonetsa mphamvu zake pochita zizindikiro ndi zodabwitsa zachinyengo. Iye adzagwiritsa ntchito mtundu uliwonse wachinyengo kupusitsa amene akuwonongeka. Iwo akuwonongeka chifukwa akukana kukonda choonadi ndi kuti apulumutsidwe. Chifukwa cha chimenechi, Mulungu akuwatumizira chinyengo chachikulu kuti akhulupirire bodza. Choncho adzalangidwa onse amene sanakhulupirire choonadi, koma anakondwera mu zoyipa.

Tikudziwa kuti Malamulo ndi abwino ngati munthu awagwiritsa ntchito bwino. Tikudziwanso kuti Malamulo sakhazikitsidwa chifukwa cha anthu olungama, koma ophwanya lamulo ndi owukira, osaopa Mulungu ndi ochimwa, wopanda chiyero ndi osapembedza; amene amapha abambo awo ndi amayi awo, kapena anthu ena. Malamulo amayikidwa chifukwa cha anthu achigololo ndi ochita zadama ndi amuna anzawo, anthu ogulitsa akapolo, abodza ndi olumbira zabodza, ndi ochita chilichonse chotsutsana ndi chiphunzitso choona. Chiphunzitso chimene chimagwirizana ndi Uthenga Wabwino wonena za ulemerero wa Mulungu wodala, umene Iye mwini anandisungitsa.

Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amafuna kuti anthu onse apulumutsidwe ndipo kuti adziwe choonadi.

Ine zina zikandichedwetsa kubwera, mudziwe za mmene anthu ayenera kukhalira mʼNyumba ya Mulungu, imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi maziko achoonadi.

Mzimu akunena momveka bwino kuti mʼmasiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chawo ndi kutsatira mizimu yonyenga ndi zinthu zophunzitsidwa ndi ziwanda.

Ngati abale uwalangiza zimenezi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa mʼchoonadi cha chikhulupiriro ndi mʼchiphunzitso chabwino chimene wakhala ukutsata.

Mpaka nditabwera, udzipereke powerenga mawu a Mulungu kwa anthu, kulalikira ndi kuphunzitsa.

Samala kwambiri moyo wako ndi ziphunzitso zako. Uzichitabe zimenezi chifukwa ukatero, udzadzipulumutsa ndiponso udzapulumutsa okumvetsera.

Choncho usachite manyazi kuchitira umboni Ambuye athu, kapena kuchita manyazi chifukwa cha ine wamʼndende. Koma umve nane zowawa chifukwa cha Uthenga Wabwino, mothandizidwa ndi mphamvu za Mulungu.

Ngati tinapirira, tidzalamuliranso naye pamodzi. Ngati ife timukana, Iye adzatikananso.

Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola.

Ndiponso mtumiki wa Ambuye asamakangane ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa aliyense, wodziwa kuphunzitsa, osati wokalipakalipa. Otsutsana naye awalangize mofatsa, mwina Mulungu adzawapatsa mwayi woti asinthike ndi kuzindikira choonadi.

amaphunzira nthawi zonse koma samatha kuzindikira choonadi.

Kuyambira uli wamngʼono wakhala ukudziwa Malemba Oyera, amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa kudzera mʼchikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu. Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.

Lalikira Mawu; khala wokonzeka pa nthawi yake, ngakhale pamene si pa nthawi yake. Konza zolakwa zawo, dzudzula ndipo limbikitsa moleza mtima kwambiri ndi malangizo osamalitsa. Pakuti idzafika nthawi imene anthu adzakana chiphunzitso choona. Mʼmalo mwake, chifukwa chokhumba kumva zowakomera zokha, adzasonkhanitsa aphunzitsi ambiri omawawuza zimene iwo akufuna kumva. Sadzafuna kumva choona koma adzafuna kumva nthano chabe.

Iye ayenera kugwiritsa mawu okhulupirika monga tinaphunzitsira, kuti athe kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona ndiponso kugonjetsa amene atsutsana nacho.

Mawu amenewa ndi woona. Nʼchifukwa chake, uwadzudzule mwamphamvu, kuti akhale ndi chikhulupiriro choona,

Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona.

Nʼchifukwa chake, ife tiyenera kusamalira kwambiri zimene tinamva, kuopa kuti pangʼono ndi pangʼono tingazitaye. Popeza uthenga umene unayankhulidwa kudzera mwa angelo unali okhazikika ndithu, choncho aliyense amene ananyozera ndi kusamvera analandira chilango choyenera. Nanga ife tidzapulumuka bwanji tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotere? Ambuye ndiye anayamba kuyankhula za chipulumutsochi, kenaka amenenso anamvawo anatitsimikizira.

Tsono monga Mzimu Woyera akuti, “Lero mukamva mawu ake, musawumitse mitima yanu ngati munachitira pamene munawukira, pa nthawi yoyesedwa mʼchipululu. Pamene makolo anu anandiputa ndi kundiyesa, ndipo kwa zaka makumi anayi anaona zimene Ine ndinachita. Nʼchifukwa chake ndinawukwiyira mʼbadowo, ndipo Ine ndinati, ‘Nthawi zonse mitima yawo imasochera, ndipo iwo sadziwa njira zanga.’ Kotero Ine ndinalumbira nditakwiya kuti, ‘Iwo sadzalowa mu mpumulo wanga.’ ” Abale samalani, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woyipa ndi wosakhulupirira, womulekanitsa ndi Mulungu wamoyo.

Pakuti Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa ife, monganso iwo aja; koma iwo sanapindule nawo uthengawo chifukwa anangomva koma osakhulupirira. Tsono ife amene takhulupirira talowa mu mpumulo, monga momwe Mulungu akunenera kuti, “Ndili wokwiya ndinalumbira kuti, ‘Iwo sadzalowa konse mu mpumulo wanga.’ ” Ananena zimenezi ngakhale anali atatsiriza kale ntchito yolenga dziko lapansi.

Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima. Palibe kanthu kobisika pamaso pa Mulungu. Zinthu zonse zili poyera ndi zovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.

Nʼkosatheka kuwabwezanso anthu amene nthawi ina anawunikiridwa. Iwowa analawapo mphatso yochokera kumwamba, nʼkulandira nawo Mzimu Woyera. Analawa kukoma kwa mawu a Mulungu ndi mphamvu za nthawi ikubwera. Popeza anabwerera mʼmbuyo, nʼkosatheka kuti atembenukenso mtima chifukwa akupachikanso Mwana wa Mulungu ndi kumunyozetsa poyera.

Tsono ili ndi pangano ndidzapangane ndi nyumba ya Israeli: Atapita masiku amenewa, akutero Ambuye, Ine ndidzayika malamulo anga mʼmaganizo mwawo, ndi kulemba mʼmitima mwawo. Ine ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.

“Ili ndi pangano limene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo,” akutero Yehova. “Ndidzayika malamulo anga mʼmitima mwawo, ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo mwawo.”

Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu Aliyense amene amakana malamulo a Mose amaphedwa popanda nʼchifundo chomwe, malingana pali mboni ziwiri kapena zitatu. Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo?

Ndipo popanda chikhulupiriro nʼkosatheka kukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene amabwera kwa Iye ayenera kukhulupirira kuti Mulungu alipodi ndi kuti Iye amapereka mphotho kwa amene akumufunitsitsa.

Chenjerani kuti musakane kumvera amene akuyankhula nanu. Anthu amene anakana kumvera iye amene anawachenjeza uja pa dziko lapansi pano, sanapulumuke ku chilango ayi, nanga tsono ife tidzapulumuka bwanji ngati tikufulatira wotichenjeza wochokera kumwamba?

Pakuti Mulungu wathu ndi moto wonyeketsa.

Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa.

Choncho chotsani chizolowezi choyipa ndi khalidwe loyipa pakati panu, ndipo modzichepetsa landirani mawu amene anadzalidwa mwa inu, amene akhoza kukupulumutsani. Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena. Munthu aliyense amene amangomva mawu koma osachita zimene mawuwo amanena, ali ngati munthu amene amayangʼana nkhope yake pa galasi. Akadziyangʼana amachoka, nthawi yomweyo nʼkuyiwala mmene akuonekera.

Inu anthu achigololo, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko lapansi ndi kudana ndi Mulungu? Choncho, aliyense wosankha kukhala bwenzi la dziko lapansi amasanduka mdani wa Mulungu. Kapena mukuganiza kuti Malemba amanena popanda chifukwa kuti Mulungu amafunitsitsa mwansanje mzimu umene Iye anayika kuti uzikhala mwa ife? Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati, “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma apereka chisomo kwa odzichepetsa.” Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani. Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira. Chitani chisoni chifukwa cha zimene mwachita, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni. Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.

Tsopano mwayeretsa mitima yanu pomvera choonadi, kuti muzikondana ndi abale anu, kukondana kwenikweni kochokera pansi pa mtima. Popeza mwabadwanso, osati ndi mbewu imene imawonongeka, koma imene siwonongeka, ndiye kuti ndi Mawu a Mulungu amoyo ndi okhalitsa. Pakuti, “Anthu onse ali ngati udzu, ndipo ulemerero wawo uli ngati duwa la kuthengo. Udzu umafota ndipo duwa limathothoka, koma mawu a Ambuye adzakhala mpaka muyaya.” Ndipo awa ndi mawu amene tinalalikira kwa inu.

Monga makanda obadwa kumene amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wauzimu, kuti mukule ndi kukufikitsani ku chipulumutso chanu,

Tsono kwa inu okhulupirira, mwalawo ndi wamtengowapatali. Koma kwa amene sakhulupirira, “Mwala umene amisiri anawukana wasanduka mwala wa maziko, ndi “Mwala wopunthwitsa anthu ndiponso thanthwe limene limagwetsa anthu.” Iwo amapunthwa chifukwa samvera uthenga, pakuti ichi ndiye chinali chifuniro cha Mulungu pa iwo.

Pakuti nthawi yafika kuti chiweruzo chiyambe mʼnyumba ya Mulungu, ndipo ngati chiyamba ndi ife nanga podzafika kwa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, chidzakhala chotani?

Ifeyo tinamva mawuwa akuchokera kumwamba pamene tinali naye pamodzi pa phiri lopatulika lija. Tsono ifenso tili ndi mawu a uneneri amene ndi odalirika kwambiri ndipo inu mudzachita bwino mukawasamalira mawuwa, monga kuwunika kumene kukuwala mu mdima, mpaka tsiku lidzayambe kucha, pamene nthanda idzayambe kuwala mʼmitima mwanu. Kuposa zonse, inu muyenera kuzindikira kuti palibe mawu a uneneri amene amatanthauzidwa pa okha. Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.

Koma panalinso aneneri onama pakati pa Aisraeli, monga padzakhalanso aphunzitsi onyenga pakati panu. Iwo adzalowetsa mwamseri ziphunzitso zonama ndi zowononga, nadzakana Ambuye amene anawawombola, ndipo motero adzadziyitanira okha chiwonongeko mwadzidzidzi. Ambiri adzatsata njira zawo zochititsa manyazi ndipo chifukwa cha iwowa, anthu adzanyoza njira ya choonadi. Pofuna kupeza chuma, aphunzitsiwa adzakudyerani chuma chanu pokuwuzani nkhani zopeka. Chiweruzo chawo chinakonzedwa kale, ndipo chikuwadikira.

Iye walemba chimodzimodzi makalata ake onse, kuyankhula za zinthu izi. Mʼmakalata ake mumakhala zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osadziwa ndi osakhazikika amazipotoza, monga amachita ndi malemba ena onse, potero akudziwononga okha. Nʼchifukwa chake, abale okondedwa, popeza mukuzidziwa kale zimenezi, chenjerani kuti musatengeke ndi zolakwa za anthu osaweruzika, mungagwe ndi kuchoka pamalo otetezedwa.

Ife timatsimikiza kuti tikumudziwa ngati tikusunga malamulo ake. Munthu akamanena kuti, “Ine ndimadziwa Mulungu,” koma samvera malamulo a Mulunguyo, ndi wabodza ameneyo ndipo mwa iye mulibe choonadi. Koma munthu aliyense akamvera mawu ake, ndiye kuti chikondi cha Mulungu chafikadi penipeni mwa iyeyo. Pamenepo timatsimikizadi kuti tili mwa Iye. Aliyense amene amati amakhala mwa Mulungu, ayenera kukhala moyo umene Yesu ankakhala.

Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi.

Ife ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo aliyense amene amadziwa Mulungu amamvera zimene timayankhula. Koma aliyense amene sachokera kwa Mulungu samvera zimene timayankhula. Mmenemu ndiye mmene timasiyanitsira pakati pa mzimu wachoonadi ndi Mzimu wachinyengo.

Chodziwira kuti timakonda ana a Mulungu nʼchakuti timakonda Mulungu ndi kusunga malamulo ake.

Aliyense amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu ali nawo umboniwu mu mtima mwake, koma aliyense amene sanakhulupirire Mulungu amayesa kuti Mulunguyo ndi wonama, chifukwa sanakhulupirire umboni umene Mulungu anachitira wa Mwana wake.

Ndipo chikondi ndiye kuyenda momvera malamulo ake. Lamulo lake ndi lakuti mukhale moyo wachikondi monga munamva kuyambira pachiyambi.

Aliyense amene sasunga chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu. Koma amene amasunga chiphunzitsochi, ameneyo alinso ndi Atate ndi Mwana. Ngati wina aliyense abwera kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamulandire mʼnyumba mwanu kapena kumupatsa moni. Aliyense wolandira munthu wotere ndiye kuti akuvomerezana nazo ntchito zake zoyipa.

Ngakhale munazidziwa kale zonsezi, ndafuna kuti ndikukumbutseni kuti Ambuye anapulumutsa anthu ake ndi kuwatulutsa mʼdziko la Igupto, koma pambuyo pake anawononga amene sanakhulupirire.

Mʼdzanja lake lamanja ananyamula nyenyezi zisanu ndi ziwiri, ndipo mʼkamwa mwake munali lupanga lakuthwa konsekonse. Nkhope yake imawala ngati dzuwa lowala kwambiri.

Ine ndimadziwa zochita zako, ntchito yako yowawa ndi kupirira kwako. Ine ndimadziwa kuti sungalekerere anthu oyipa amene amadzitcha atumwi pamene sichoncho, unawayesa, ndipo unawapeza kuti ndi abodza.

Tsono tembenukani mtima. Mukapanda kutero, ndidzabwera kwanuko posachedwa ndipo ndidzachita nanu nkhondo ndi lupanga lotuluka mʼkamwa mwanga lija.

Tsono popeza ndiwe wofunda chabe, sindiwe wotentha kapena wozizira, ndatsala pangʼono kuti ndikulavule mʼkamwa mwanga. Iwe umati: ‘Ndine wolemera, ndine wachuma ndipo sindisowa kanthu.’ Koma sudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, waumphawi, wosaona ndi wamaliseche.

Pamenepo chinjokacho chinamupsera mtima mayiyo ndipo chinachoka kupita kukachita nkhondo ndi ana ena onse a mayiyo, ndiye kuti anthu amene anasunga malamulo a Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu. Kenaka ndinaona chinjokacho chitayima mʼmbali mwa nyanja.

Kenaka ndinaona mngelo wina akuwuluka mu mlengalenga ndipo anali ndi Uthenga Wabwino wamuyaya woti akalalikire kwa anthu okhala pa dziko lapansi, kwa a mtundu uliwonse, a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse ndi kwa anthu onse. Mngeloyo anayankhula mokweza mawu kuti, “Wopani Mulungu ndi kumutamanda, chifukwa nthawi yoweruza anthu yafika. Mumupembedze Iye amene analenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi akasupe amadzi.”

Inu Ambuye, ndani angapande kukuopani, ndi kulemekeza dzina lanu? Pakuti Inu nokha ndiye woyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzapembedza pamaso panu, pakuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”

Maso ake anali ngati malawi amoto, ndipo pamutu pake panali zipewa zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lodziwika ndi Iye yekha, osati wina aliyense. Iye anavala mkanjo woviyika mʼmagazi, ndipo dzina lake ndi Mawu a Mulungu.

Mʼkamwa mwake munatuluka lupanga lakuthwa limene anati akaphe nalo mitundu ya anthu. Iye adzalamulira ndi ndodo yachitsulo. Iye anaponda choponderamo mphesa cha ukali wa Mulungu Wamphamvuzonse.

Ena onse anaphedwa ndi lupanga lija linatuluka mʼkamwa mwa wokwera pa kavalo uja, ndipo mbalame zonse zinadya mokwanira mnofu wa anthu akufawo.

Ndikuchenjeza aliyense amene akumva mawu onena zamʼtsogolo a mʼbukuli kuti, “Ngati wina awonjezerapo kalikonse, Mulungu adzamuwonjezera miliri imene yalembedwa mʼbuku ili. Ndipo wina akachotsapo mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili, Mulungu adzachotsa gawo lake pa mtengo wamoyo ndi la mu mzinda woyera zimene zanenedwa mʼbuku ili.”

Chichewa - Chichewa - NY

NYCCL - Mawu A Mulungu Mu Chichewa Chalero - 2016

This Bible text is from Biblica Open God's Word In Contemporary Chichewa
https://open.bible/bibles/chichewa-biblica-text-bible/
provided by: Biblica Inc, available by Creative Commons CC-BY-SA-4.0,
and this new compilation is shared as www.creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0.
Languages are made available to you by www.ipedge.net