04 – Kulenga
Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Kulenga.
Awa ndi mawu oyera a Mulungu Wamphamvuzonse.
Sitimadalira mawu a anthu.
Kwa aliyense amene amakonda Mulungu… awa ndi zomwe Mulungu akunena za: Kulenga.
Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.
”Koma Mulungu amayipatsa thupi monga Iye wafunira, ku mbewu ya mtundu uliwonse amapereka thupi lakelake. Mnofu siwofanana. Anthu ali ndi mnofu wa mtundu wina, nyama zili ndi wina, mbalame zili ndi wina, nsomba zili ndi winanso.
”Pakuti kuyambira pamene dziko lapansi linalengedwa, zinthu zosaoneka za Mulungu, mphamvu zake zosatha ndi chikhalidwe cha umulungu, zakhala zikuoneka bwinobwino. Akhala akuzindikira poona zimene Mulungu analenga, kotero kuti anthu sangathe kuwiringula.
”Pachiyambi Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi. Dziko lapansi linali losakonzedwa ndi lopanda kanthu. Mdima wandiweyani unakuta nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo. Pamenepo Mulungu anati, “Kuwale” ndipo kunawaladi. Mulungu anaona kuti kuwalako kunali bwino ndipo Iye analekanitsa kuwala ndi mdima. Mulungu anatcha kuwalako “usana” ndipo mdima anawutcha “usiku.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku loyamba.
”Kenaka Mulungu anati, “Pakhale thambo pakati pa madzi kuti lilekanitse madzi a mʼmwamba ndi madzi a pansi.” Ndipo Mulungu anapanga thambo nalekanitsa madzi amene anali pansi ndi pamwamba pa thambo lija, ndipo zinachitikadi. Mulungu anatcha thambo lija “kumwamba.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachiwiri.
”Mulungu anati, “Madzi a pansi pa thambo asonkhane pa malo amodzi kuti mtunda uwoneke,” ndipo zinachitikadi. Mulungu anawutcha mtundawo “dziko,” madzi osonkhana pamodziwo anawatcha “nyanja.” Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. Kenaka Mulungu anati, “Dziko libereke zomera zobala mbewu, mitengo yobala zipatso za mbewu, molingana ndi mitundu yake.” Ndipo zinachitikadi. Dziko linabereka zomera zokhala ndi mbewu monga mwa mitundu yake ndi mitengo yokhala ndi zipatso za mbewu mʼkati mwake monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino. Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachitatu.
”Mulungu anati, “Pakhale zowunikira kuthambo kuti zilekanitse usana ndi usiku. Ndipo zimenezi zikhale zizindikiro zoonetsa nyengo, masiku ndi zaka; zikhale kuthambo kuti ziwunikire pa dziko lapansi. Ndipo zinachitikadi.” Mulungu anapanga zowunikira zazikulu ziwiri; chachikulu chilamulire usana ndi chachingʼono chilamulire usiku. Iye anapanganso nyenyezi. Mulungu anaziyika mlengalenga kuti ziziwunikira pa dziko lapansi, kuti zilamulire usana ndi usiku, ndi kuti zilekanitse kuwala ndi mdima. Mulungu anaona kuti zinali bwino. Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachinayi.
”Mulungu anati, “Mʼmadzi mukhale zamoyo zochuluka ndipo mbalame ziwuluke mlengalenga pamwamba pa dziko lapansi.” Choncho Mulungu analenga zamoyo zikuluzikulu za mʼnyanja ndi chamoyo chamtundu uliwonse chokhala mʼmadzi ndi mbalame iliyonse ya mapiko monga mwa mtundu wake. Mulungu anaona kuti zinali bwino. Mulungu anazidalitsa nati, “Muswane, ndi kudzaza mʼmadzi a mʼnyanja, ndipo mbalame zichuluke pa dziko lapansi.” Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa pa tsiku lachisanu.
”Kenaka Mulungu anati, “Dziko lapansi litulutse zolengedwa zamoyo monga mwa mitundu yawo: ziweto, zolengedwa zokwawa ndi nyama zakuthengo, iliyonse monga mwa mtundu wake.” Ndipo zinaterodi. Mulungu anapanga nyama zakuthengo monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo ndi nyama zokwawa monga mwa mitundu yawo. Ndipo Mulungu anaona kuti zinali bwino.
”Zitatha izi Mulungu anati, “Tipange munthu mʼchifanizo chathu, mofanana ndi ife kuti alamulire nsomba za mʼnyanja, mbalame zamlengalenga, nyama zonse zoweta ndi zonse zokwawa za pa dziko lapansi ndi zamoyo zonse zakutchire.” Ndipo Mulungu analenga munthu mʼchifanizo chake. Anawalengadi mʼchifanizo cha Mulungu; analenga iwo, mwamuna ndi mkazi. Mulungu anawadalitsa nati kwa iwo, “Muberekane, muchulukane, mudzaze dziko lapansi ndipo muligonjetse. Mulamulire nsomba zamʼnyanja, mbalame zamlengalenga ndi cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimayenda mokwawa pa dziko lapansi.” Kenaka Mulungu anati, “Ine ndakupatsani chomera chilichonse cha pa dziko lapansi chimene chili ndi mbewu komanso mtengo uliwonse wobala zipatso zokhala ndi mbewu mʼkati mwake kuti zikhale chakudya chanu. Ndaperekanso msipu kwa nyama zonse za pa dziko lapansi ndi kwa mbalame zamlengalenga ndi kwa cholengedwa chamoyo chilichonse chimene chimakwawa, chilichonse chimene chili ndi moyo.” Ndipo zinachitikadi. Mulungu anaona zonse zimene anazilenga kuti zinali zabwino kwambiri. Ndipo panali madzulo ndiponso mmawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
”Motero kumwamba, dziko lapansi ndi zonse za mʼmenemo zinatha kulengedwa monga mwa kuchuluka kwawo. Pofika tsiku lachisanu ndi chiwiri Mulungu anamaliza ntchito zonse zimene ankagwira ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri anapumula ku ntchito zake zonse. Ndipo Mulungu anadalitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri nalipatula, chifukwa pa tsiku limeneli Iye anapumula ku ntchito yonse yolenga imene anayigwira.
”Mbiri ya momwe kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwera pa tsiku lija Yehova Mulungu ankazilenga ndi iyi: Yehova Mulungu atapanga dziko lapansi ndi kumwamba, zitsamba zinali zisanamere ndipo chomera chilichonse chinali chisanamerenso popeza Yehova Mulungu anali asanagwetse mvula pa dziko lapansi. Panalibe munthu wolima nthaka, koma kasupe ankatuluka mʼnthaka ndi kuthirira pa dziko lonse. Tsono Yehova Mulungu anawumba munthu kuchokera ku dothi nawuziramo mpweya wamoyo mʼmphuno mwake ndipo munthuyo anakhala wamoyo. Kenaka Yehova Mulungu anatsekula munda wa Edeni chakummawa; kumeneko anayikako munthu amene anamupanga uja.
”Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi: Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu. Iye analenga mwamuna ndi mkazi. Anawadalitsa ndipo anawatcha “Munthu.” Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti.
”Pakuti Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo mʼmasiku asanu ndi limodzi. Iye anapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Kotero Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale loyera.
”Tsiku la Sabata lidzakhala chizindikiro chamuyaya pakati pa Ine ndi Aisraeli chosonyeza kuti Yehova analenga za kumwamba ndi dziko lapansi kwa masiku asanu ndi limodzi ndi kuti pa tsiku lachisanu ndi chiwiri analeka kugwira ntchito napumula.”
”Komabe, ndikunenetsa kuti pali Ine, ndiponso pamene dziko lapansi ladzaza ndi ulemerero wa Yehova,
”Tsopano tafunsani za masiku a mʼmbuyomu, zakale inu musanabadwe, kuyambira tsiku limene Mulungu analenga munthu pa dziko lapansi. Tafufuzani kuyambira kumapeto mpaka mapeto anzake a thambo. Kodi chinachitikako china chachikulu ngati ichi, kapena chinayamba chamvekako chokhala ngati ichi?
”Yehova Mulungu wanu ndiye mwini wake kumwamba ngakhale mmwambamwamba, dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo.
”Iye amakweza osauka kuwachotsa pa fumbi, ndipo amachotsa anthu osowa pa dzala. Iye amawakhazika pamodzi ndi ana a mafumu, amawapatsa mpando waulemu. “Pakuti nsanamira za dziko lapansi ndi za Yehova, anakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.
”Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera, ndipo maziko a dziko lapansi anakhala poyera, Yehova atabangula mwaukali, pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwake.
”Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, Inu amene mumakhala pa Akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
”Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu, ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola. Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu. Wanu, Inu Yehova ndi ufumu; Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse.
”Inu nokha ndiye Yehova. Munalenga kumwamba, ngakhale kumwambamwamba, zolengedwa zonse zimene zili mʼmenemo. Munalenga dziko ndi zonse zokhalamo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo. Zonse mumazisunga ndi moyo ndipo zonse za kumwamba zimakupembedzani.
”Iye amagwedeza dziko lapansi kulisuntha pamalo pake ndipo amanjenjemeretsa mizati yake. Iye amayankhula ndi dzuwa ndipo siliwala; Iyeyo amaphimba kuwala kwa nyenyezi. Ndi Mulungu yekha amene anayala mayiko akumwamba ndipo amayenda pa mafunde a pa nyanja. Iye ndiye mlengi wa nyenyezi zamlalangʼamba ndi akamwiniatsatana, nsangwe ndi kumpotosimpita. Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka, zodabwitsa zimene sizingawerengeke.
”“Koma funsa nyama zakuthengo ndipo zidzakuphunzitsa, kapena mbalame zamumlengalenga ndipo zidzakuwuza; kapena uyankhule ndi dziko lapansi ndipo lidzakuphunzitsa, kapena ulole nsomba zamʼnyanja kuti zikufotokozere. Kodi mwa zonsezi ndi chiti chimene sichidziwa kuti lachita zimenezi ndi dzanja la Yehova? Mʼmanja mwake ndi mʼmene muli moyo wa cholengedwa chilichonse, ndiponso moyo wa anthu a mitundu yonse.
”Mulungu anayala thambo la kumpoto pa phompho; Iye anakoloweka dziko lapansi mʼmalo mwake pamene panali popanda nʼkanthu komwe. Amasunga madzi ambiri mʼmitambo yake, koma mitamboyo siphulika chifukwa cha kulemera kwa madziwo. Iye amaphimba mwezi wowala, amawuphimba ndi mitambo yake. Mulungu anawalembera madzi malire wonga uta, kukhala malire pakati pa kuwunika ndi mdima. Mizati yochirikiza mitambo yakumwamba imanjenjemera, ndi kudabwa pa kudzudzula kwake.
”Mzimu wa Mulungu wandiwumba, mpweya wa Wamphamvuzonse umandipatsa moyo.
”Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati: “Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga poyankhula mawu opanda nzeru? Onetsa chamuna; ndikufunsa ndipo undiyankhe. “Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi? Ndiwuze ngati ukudziwa. Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa! Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli? Kodi maziko ake anawakumba potani, kapena ndani anayika mwala wake wapangodya, pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa? “Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa, pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko, pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake ndi kuyikulunga mu mdima wandiweyani, pamene ndinayilembera malire ake ndikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake. Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirire apa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’
”“Taganiza za mvuwu, imene ndinayipanga monga momwe ndinapangira iwe, ndipo imadya udzu ngati ngʼombe. Mphamvu zake ndi zazikulu kwambiri, thupi lake ndi lanyonga kwambiri! Mchira wake umayima tolotolo ngati mtengo wamkungudza; mitsempha ya ntchafu zake ndi yogwirana bwino.
”Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene mwaziyika pa malo ake,
”Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera; maziko a dziko lapansi anakhala poyera, Yehova atabangula mwaukali, pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwanu.
”Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu; thambo limalalikira ntchito za manja ake.
”Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi, mawuwo amafika mpaka kumalekezero a dziko lapansi.
”Salimo la Davide. Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo, dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo; pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanja ndi kulikhazika pamwamba pa madzi.
”Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa, zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.
”Mayiko akumwamba ndi anu ndiponso dziko lapansi ndi lanu; munapanga dziko lonse ndi zonse zili mʼmenemo. Munalenga Kumpoto ndi Kummwera; Tabori ndi Herimoni akuyimba ndi chimwemwe pa dzina lanu.
”Mapiri asanabadwe, musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse, kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.
”Nyanja ndi yake, pakuti anayilenga ndi Iye, ndipo manja ake anawumba mtunda wowuma. Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira, tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;
”Pachiyambi Inu munakhazikitsa maziko a dziko lapansi ndipo mayiko akumwamba ndi ntchito ya manja anu. Izi zidzatha, koma Inu mudzakhalapo; zidzatha ngati chovala. Mudzazisintha ngati chovala ndipo zidzatayidwa.
”Tamanda Yehova, iwe moyo wanga. Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri; mwavala ulemerero ndi ufumu. Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala; watambasula miyamba ngati tenti ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake. Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake, ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo. Amapanga mphepo kukhala amithenga ake, malawi amoto kukhala atumiki ake. Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake; silingasunthike.
”Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova! Munazipanga zonse mwanzeru, dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu. Kuli nyanja yayikulu ndi yotambalala, yodzaza ndi zolengedwa zosawerengeka, zamoyo zanu zazikulu ndi zazingʼono zomwe.
”Ntchito za Yehova nʼzazikulu; onse amene amakondwera nazo amazilingalira.
”Mudalitsidwe ndi Yehova, Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi. Kumwamba ndi kwa Yehova, koma dziko lapansi Iye walipereka kwa anthu.
”Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga; tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.
”Thandizo langa limachokera kwa Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
”Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
”Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera, kumwamba ndi dziko lapansi, ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.
”Amene mwachidziwitso chake anapanga mayiko akumwamba, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. Amene anapanga miyuni ikuluikulu, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. Dzuwa lilamulire usana, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya. Mwezi ndi nyenyezi zilamulire usiku, pakuti chikondi chake chosasinthika nʼchamuyaya.
”Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga; munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga. Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa; ntchito zanu ndi zodabwitsa, zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
”Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo; Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.
”Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi, ndipo iliyonse amayitchula dzina.
”Yehova anakhazikitsa dziko lapansi pogwiritsa ntchito nzeru. Anagwiritsanso ntchito nzeru zakudziwa bwino zinthu pamene ankakhazikitsa zakumwamba.
”“Yehova anandilenga ine nzeru monga ntchito yake yoyamba. Mwa ntchito zake zakalekale yoyamba ndinali ine. Ndinapangidwa kalekalelo, pachiyambi penipeni dziko lapansi lisanalengedwe. Nyanja, akasupe odzaza ndi madzi, zonsezi kulibe pamene ine ndinkabadwa. Mapiri asanakhazikitsidwe pa malo awo, mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinali nditabadwa kale, lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake; lisanalengedwe dothi loyamba la dziko lapansi. Ine ndinalipo pamene Yehova ankakhazikitsa mlengalenga, pamene ankalemba malire a nyanja yozama, pamene anakhazikitsa mitambo ya mlengalenga ndi kukhazikitsa akasupe a madzi ozama, pamene anayikira nyanja malire kuti madzi asadutse malirewo, ndiponso pamene ankayika malire a dziko lapansi. Tsono ine ndinali pambali pake ngati mmisiri; ndikumukondweretsa tsiku ndi tsiku, kusangalala nthawi zonse pamaso pake. Ndinkasangalala ndi dziko lake lonse ndiponso kumakondwera nawo anthu onse.”
”Makutu amene amamva ndi maso amene amaona, zonsezi anazilenga ndi Yehova.
”Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti “Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse. Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”
”Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena chowononga pa phiri lopatulika la Yehova, pakuti anthu a dziko lapansi adzadzaza ndi nzeru yotha kudziwa Yehova monga momwe nyanja imadzazira ndi madzi.
”Inu mumazondotsa zinthu ngati kuti dothi lasanduka wowumba mbiya. Kodi chinthu chopangidwa chingawuze wochipanga kuti “Sunandipange ndi iwe?” Kapena mʼphika kunena kwa amene anawuwumba kuti, “Iwe sudziwa chilichonse?”
”“Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pakati pa akerubi, Inu nokha ndiye Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
”Kodi ndani akhoza kuyeza kuchuluka kwa madzi a mʼnyanja ndi chikhatho chake, kapena kuyeza kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake? Ndani akhoza kuyeza dothi lonse la dziko lapansi mʼdengu, kapena kuyeza kulemera kwa mapiri ndi zitunda ndi pasikelo?
”Kodi simukudziwa? Kodi simunamve? Kodi sanakuwuzeni kuyambira pachiyambi pomwe? Kodi simunamvetsetse chiyambire cha dziko lapansi? Yehova amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba ndiye analenga dziko lapansi, Iye amaona anthu a dziko lapansi ngati ziwala. Ndipo anafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchinga, nayikunga ngati tenti yokhalamo.
”Tayangʼanani mlengalenga ndipo onani. Kodi ndani analenga zonsezi mukuzionazi? Yehova ndiye amene amazitsogolera ngati gulu la ankhondo, nayitana iliyonse ndi dzina lake. Ndipo popeza Iye ali ndi nyonga zambiri, palibe ndi imodzi yomwe imene inasowapo.
”Kodi simukudziwa? Kodi simunamve? Yehova ndiye Mulungu wamuyaya, ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi. Iye sadzatopa kapena kufowoka ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.
”Yehova Mulungu amene analenga zamlengalenga ndi kuziyalika, amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene zimabereka, amenenso amapereka mpweya kwa anthu ake okhala mʼdzikomo, ndi moyo kwa onse oyendamo, akuti,
”onsewo amadziwika ndi dzina langa; ndinawalenga chifukwa cha ulemerero wanga, ndinawawumba, inde ndinawapanga.”
”Yehova Mpulumutsi wanu, amene anakuwumbani mʼmimba ya amayi anu akuti: “Ine ndine Yehova, amene anapanga zinthu zonse, ndinatambasula ndekha zinthu zakuthambo, ndinayala ndekha dziko lapansi.
”“Yehova Woyerayo wa Israeli, ndiponso Mlengi wake akunena, zokhudza zinthu zimene zikubwera ndi izi: Kodi iwe ukundifunsa za ana anga, kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga? Ndine amene ndinapanga dziko lapansi ndikulenga munthu kuti akhalemo. Ine ndi manja anga ndinayalika thambo; ndimalamulira zolengedwa zonse za mlengalenga.
”Yehova analenga zinthu zakumwamba, Iye ndiye Mulungu; amene akulenga dziko lapansi, ndi kulikhazikitsa, sanalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma analipanga kuti anthu akhalemo. Iyeyu akunena kuti: Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina.
”“Tamvera Ine, iwe Yakobo, Israeli, amene ndinakuyitana: Mulungu uja Woyamba ndi Wotsiriza ndine. Inde dzanja langa linamanga maziko a dziko lapansi, dzanja langa lamanja linafunyulula mlengalenga. Ndi mawu anga ndinalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
”Koma inu mumayiwala Yehova Mlengi wanu, amene anayala za mlengalenga ndi kuyika maziko a dziko lapansi. Inu nthawi zonse mumaopsezedwa chifukwa cha ukali wa anthu okuponderezani amene angofuna kukuwonongani. Kodi uli kuti tsopano ukali wa anthu okuponderezaniwo?
”Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu. Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba; ife tonse ndi ntchito ya manja anu.
”Yehova akuti, “Kumwamba ndi mpando wanga waufumu ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga. Tsono nyumba ili kuti yomwe mundimangire, ndipo malo ali kuti amene inu mungandikonzere kuti ndizipumuliramo? Kodi si manja anga amene anapanga zinthu zonsezi, motero zonsezi ndi zanga?” Akutero Yehova. “Koma munthu amene ndimakondwera naye ndi uyu: amene ali wodzichepetsa ndi wosweka mtima, ndipo amamvera mawu anga.
”Koma Yehova ndiye Mulungu woona; Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo, Mfumu yamuyaya. Akakwiya, dziko limagwedezeka; anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo. “Awuze anthu awa kuti, ‘Milungu iyi, imene sinalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzawonongeka pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.’ ” Koma Mulungu analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake; Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake ndipo anayala thambo mwaluso lake.
”Ndi mphamvu zanga ndi dzanja langa lamphamvu ndinalenga dziko lapansi ndi anthu ake onse pamodzi ndi nyama zili mʼmenemo, ndipo ndimalipereka kwa aliyense amene ndikufuna.
”“Aa, inu Ambuye Yehova, munalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Munazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo palibe chokulakani.
”“Yehova analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake; Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake ndipo anayala thambo mwaluso lake.
”(Iye amene analenga nyenyezi za Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, amene amasandutsa mdima kuti ukhale mmawa ndi kudetsa usana kuti ukhale usiku, amene amayitana madzi a mʼnyanja ndi kuwathira pa dziko lapansi, Yehova ndiye dzina lake.
”Iye amene amamanga malo ake okhalamo kumwamba, ndi kuyika maziko ake pa dziko lapansi, Iye amene amayitana madzi a ku nyanja ndikuwakhuthulira pa dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova.
”Iye anayankha kuti, “Ndine Mhebri, ndipo ndimapembedza Yehova, Mulungu Wakumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda.”
”Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi chidziwitso cha ulemerero wa Yehova, monga momwe madzi amadzazira nyanja.
”Uthenga wa Yehova kwa Israeli. Yehova, amene amayala mlengalenga, amene amayika maziko a dziko lapansi, ndiponso amene amalenga mzimu wokhala mwa munthu, akunena kuti,
”Koma pachiyambi cha chilengedwe, Mulungu ‘analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.’
”mwana wa Enosi, mwana wa Seti, mwana wa Adamu, mwana wa Mulungu.
”Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu. Mawuwa anali ndi Mulungu pachiyambi. Zinthu zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo popanda Iye sikukanakhala kanthu kalikonse kolengedwa.
”Iye anali mʼdziko lapansi, ndipo ngakhale kuti dziko lapansi linalengedwa ndi Iye, dziko lapansilo silinamuzindikire Iye.
”Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali ndipo anati, “Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano.”
”“ ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu, ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Kodi mudzandimangira nyumba yotani? Akutero Ambuye. Kapena malo opumuliramo Ine ali kuti?
”“Anthu inu, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Ife takubweretserani Uthenga Wabwino, kuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo.
”“Mulungu amene analenga dziko lapansi ndiponso zonse zili mʼmenemo ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndipo sakhala mʼnyumba zachipembedzo zomangidwa ndi manja. Ndipo satumikiridwa ndi manja a anthu ngati kuti Iye amasowa kanthu, chifukwa Iye ndiye amapereka moyo ndi mpweya kwa anthu onse ndi zina zonse. Kuchoka kwa munthu mmodzi Iye analenga mtundu uliwonse wa anthu, kuti akakhale pa dziko lonse lapansi; ndipo Iye anakonzeratu nthawi yawo ndiponso malo enieni kumene adzakhale. Mulungu anachita izi kuti anthu amufunefune, ndikuti pomufunafunapo amupeze ngakhale kuti Iye sali kutali ndi aliyense wa ife. ‘Pakuti timakhala mwa Iye, kuyenda mwa Iye ndi kukhala moyo mwa Iye.’ Monga olemba ndakatulo anu ena akuti, ‘Ife ndi zidzukulu zake.’
”Pakuti kuyambira pamene dziko lapansi linalengedwa, zinthu zosaoneka za Mulungu, mphamvu zake zosatha ndi chikhalidwe cha umulungu, zakhala zikuoneka bwinobwino. Akhala akuzindikira poona zimene Mulungu analenga, kotero kuti anthu sangathe kuwiringula.
”Monga kwalembedwa kuti, “Ine ndakusandutsa kukhala kholo la mitundu yambiri.” Iye ndiye kholo lathu pamaso pa Mulungu, amene anamukhulupirira, Mulungu amene amapereka moyo kwa akufa ndipo amapereka moyo kwa zinthu zopanda moyo.
”Choncho monga momwe tchimo linalowa mʼdziko lapansi kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mu tchimo, mʼnjirayi imfa inafika kwa anthu onse pakuti onse anachimwa.
”Pakuti chilengedwe chikudikira ndi chiyembekezo kuonetsedwa poyera kwa ana a Mulungu. Pakuti chilengedwe sichinasankhe kugonjera zopanda pake, koma mwachifuniro cha Iye amene analola kuti chigonjere. Koma chili ndi chiyembekezo chakuti chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi ndi kulandiranso ufulu ndi ulemerero wa ana a Mulungu. Ife tikudziwa kuti chilengedwe chonse chakhala chikubuwula ndi ululu ngati ululu wa nthawi yobereka mwana mpaka tsopano lino.
”Pakuti zinthu zonse nʼzochokera kwa Iye, nʼzolengedwa ndi Iye ndipo zimabweretsa ulemerero kwa Iye. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya! Ameni.
”koma kwa ife pali Mulungu mmodzi yekha, Atate, zinthu zonse zinachokera mwa Iye ndipo ndife ake. Komanso pali Ambuye mmodzi Yesu Khristu kumene zinthu zonse zinachokera ndipo mwa Iye ife tili ndi moyo.
”Koma Mulungu amayipatsa thupi monga Iye wafunira, ku mbewu ya mtundu uliwonse amapereka thupi lakelake. Mnofu siwofanana. Anthu ali ndi mnofu wa mtundu wina, nyama zili ndi wina, mbalame zili ndi wina, nsomba zili ndi winanso.
”Kwalembedwa kuti, “Munthu woyamba Adamu anakhala wamoyo,” Adamu wotsiriza anakhala wopatsa moyo. Zauzimu sizinabwere koyambirira, koma zachilengedwe, pambuyo pake zauzimu. Munthu woyamba anali wa dziko lapansi, wochokera mʼnthaka koma munthu wachiwiri anali wochokera kumwamba. Monga analili munthu wa dziko lapansi, momwemonso anthu onse amene ndi a dziko lapansi. Ndipo monga alili munthu wakumwamba, momwemonso anthu onse amene ndi akumwamba.
”Pakuti Mulungu amene anati, “Kuwala kuwunike kuchokera mu mdima,” Iyeyo ndiye anawunikira mʼmitima mwathu kutipatsa kuwala kuti tidziwe ulemerero wa Mulungu umene ukuoneka pa nkhope ya Yesu Khristu.
”Ndinasankhidwa kuti ndifotokoze momveka bwino kwa munthu aliyense za chinsinsi chimenechi, chinsinsi chimene kuyambira kale chinali chobisika mwa Mulungu amene analenga zinthu zonse.
”Mwanayu ndiye chithunzi cha Mulungu wosaonekayo. Iye ndiye Mwana wake woyamba kubadwa ndi wolamulira zolengedwa zonse. Pakuti zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye. Zinthu zakumwamba ndi za pa dziko lapansi, zooneka ndi zosaoneka, maufumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu. Zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye ndipo anazilengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse zisanalengedwe ndipo zinthu zonse zimamangika pamodzi mwa Iye.
”Koma masiku otsiriza ano, Mulungu wayankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Mwanayu anamusankha kuti akhale mwini wa zinthu zonse, ndiponso Mulungu analenga dziko lonse kudzera mwa Iye. Mwanayo ndiye kuwala kwa ulemerero wa Mulungu, chithunzithunzi chenicheni cha khalidwe lake. Iyeyu amachirikiza zinthu zonse ndi mphamvu ya mawu ake. Iye atayeretsa anthu kuchoka ku machimo awo, anakhala pansi kumwamba kudzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
”Mulungu akutinso, “Ambuye, pachiyambi Inu munayika maziko a dziko lapansi; ndipo zakumwambako ndi ntchito za manja anu.
”Pakuti nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wina, koma amene anapanga zonse ndi Mulungu.
”Ndi chikhulupiriro timazindikira kuti dziko lapansi ndi la mmwamba zinapangidwa ndi Mawu a Mulungu, ndikuti zinthu zoonekazi zinachokera ku zinthu zosaoneka.
”Poyamba mudziwe kuti mʼmasiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, adzanyoza ndi kutsata zilakolako zawo zoyipa. Iwo adzati, “Kodi suja Ambuye analonjeza kuti adzabweranso? Nanga ali kuti? Lija nʼkale anamwalira makolo athu, koma zinthu zonse zili monga anazilengera poyamba paja.” Koma iwo akuyiwala dala kuti Mulungu atanena mawu, kumwamba kunakhalapo ndipo analenga dziko lapansi ndi madzi. Ndi madzinso achigumula, dziko lapansi la masiku amenewo linawonongedwa. Dziko la kumwamba ndi lapansi la masiku ano akulisunga ndi mawu omwewo kuti adzalitentha ndi moto. Akuzisunga mpaka tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osapembedza Mulungu. Koma abale okondedwa, musayiwale chinthu chimodzi ichi: Kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi!
”“Ndinu woyeneradi kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu, Ambuye ndi Mulungu wathu, pakuti munalenga zinthu zonse, ndipo mwakufuna kwanu zinalengedwa monga zilili.”
”Mngeloyo analumbira mʼdzina la Iye wokhala ndi moyo mpaka muyaya, amene analenga kumwamba ndi zonse zili kumeneko, dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo, nati, “Pasakhalenso zochedwa tsopano!
”Kenaka ndinaona mngelo wina akuwuluka mu mlengalenga ndipo anali ndi Uthenga Wabwino wamuyaya woti akalalikire kwa anthu okhala pa dziko lapansi, kwa a mtundu uliwonse, a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse ndi kwa anthu onse. Mngeloyo anayankhula mokweza mawu kuti, “Wopani Mulungu ndi kumutamanda, chifukwa nthawi yoweruza anthu yafika. Mumupembedze Iye amene analenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi akasupe amadzi.”
”